Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • wp17 No. 4 tsamba 16
  • Kodi Baibulo Limanena Zotani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Baibulo Limanena Zotani?
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2017
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Baibulo lingakuthandizeni mukakhala ndi nkhawa?
  • Kodi zidzatheka anthufe kukhala opanda nkhawa?
  • Tayani Nkhaŵa Yanu Yonse pa Yehova
    Nsanja ya Olonda—1994
  • Muzimutulira Yehova Nkhawa Zanu Zonse
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2016
  • Nkhawa
    Galamukani!—2016
  • Baibulo Lingathandize Amuna Amene Ali Ndi Nkhawa
    Nkhani Zina
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2017
wp17 No. 4 tsamba 16
Banja lili m’Paradaiso

Mu Ufumu wa Mulungu, anthu “adzasangalala ndi mtendere wochuluka.”​—Salimo 37:11

Kodi Baibulo Limanena Zotani?

Kodi Baibulo lingakuthandizeni mukakhala ndi nkhawa?

Kodi mungayankhe bwanji?

  • Inde

  • Ayi

  • Mwina

Zimene Baibulo limanena

‘Muzimutulira [Mulungu] nkhawa zanu zonse, pakuti amakuderani nkhawa.’ (1 Petulo 5:7) Baibulo limatitsimikizira kuti Mulungu angatithandize tikakhala ndi nkhawa.

Mfundo zinanso zomwe tikuphunzira m’Baibulo

  • Mukapemphera, mungapeze “mtendere wa Mulungu” womwe ungakuthandizeni kuchepetsa nkhawa.​—Afilipi 4:6, 7.

  • Kuwerenga Mawu a Mulungu kungakuthandizeni kuti mudziwe zoyenera kuchita mukakhala ndi nkhawa.​—Mateyu 11:28-30.

Kodi zidzatheka anthufe kukhala opanda nkhawa?

Anthu ena amakhulupirira kuti . . . nkhawa ndi mbali imodzi ya moyo wa munthu, pomwe ena amakhulupirira kuti nkhawa zidzatha akadzamwalira n’kupita kumwamba. Kodi inuyo mukuganiza bwanji?

Zimene Baibulo limanena

Mulungu analonjeza kuti adzachotsa zinthu zonse zomwe zimayambitsa nkhawa.​—Chivumbulutso 21:4.

Mfundo zinanso zomwe tikuphunzira m’Baibulo

  • Ufumu wa Mulungu ukadzayamba kulamulira padzikoli, anthu azidzakhala mwamtendere komanso mosangalala.​—Yesaya 32:18.

  • Nkhawa zidzakhala mbiri yakale.​—Yesaya 65:17.

Kuti mudziwe zambiri, werengani mutu 3 m’buku lakuti, Zimene Baibulo Limaphunzitsa, lofalitsidwa ndi a Mboni za Yehova

Bukuli likupezekanso pawebusaiti yathu ya www.jw.org/ny

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena