Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
Mafunso otsatirawa tidzawakambirana pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu ya mlungu woyambira October 31, 2011.
1. N’chifukwa chiyani tiyenera kumamatira zikumbutso za Yehova? (Sal. 119:60, 61) [w00 12/1 tsa. 14 ndime 3]
2. Kodi tingaphunzire chiyani pa lemba la Salimo 133:1-3? [w06 9/1 tsa. 16 ndime 3]
3. Kodi Yehova ‘anafufuza’ Davide ndiponso ‘kudziwa bwino pamene akuyenda komanso pogona’ pake m’njira yotani? (Sal. 139:1, 3) [w06 9/1 tsa. 16 ndime 6; w93 10/1 tsa. 11 ndime 6]
4. Kodi Yehova “amachirikiza” kapena kuti ‘kuweramutsa’ atumiki ake pa mavuto ngati ati? (Sal. 145:14) [w04 1/15 tsa. 17 ndime 11]
5. Kodi ndi khalidwe liti la munthu wotchulidwa pa lemba la Miyambo 6:12-14 limene limamuchititsa kukhala wopanda pake? [w00 9/15 tsa. 26 ndime 5-6]
6. N’chifukwa chiyani munthu wanzeru “amamvera malamulo”? (Miy. 10:8) [w01 7/15 tsa. 26 ndime 1]
7. Kodi munthu wanzeru amasiyana bwanji ndi munthu wopusa akanyozedwa kapena kunenedwa zachipongwe? (Miy. 12:16) [w03 3/15 tsa. 27 ndime 3-4]
8. Kodi kuona zinthu moyenera kumatithandiza bwanji kukhala osangalala ‘n’kumachita phwando nthawi zonse’? (Miy. 15:15) [w06 7/1 tsa. 16 ndime 6]
9. Kodi ‘kupeza mtima wanzeru’ kumafuna chiyani ndipo munthu wotero ‘amakonda bwanji moyo wake’? (Miy. 19:8) [w99 7/1 tsa. 18 ndime 4; it-1-E tsa. 1059 ndime 1]
10. Kodi kuzindikira kungapindulitse bwanji banja? (Miy. 24:3) [w06 9/15 tsa. 27 ndime 11; be tsa. 32 ndime 1]