Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • km 12/14 tsamba 6
  • Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu
  • Utumiki Wathu wa Ufumu—2014
Utumiki Wathu wa Ufumu—2014
km 12/14 tsamba 6

Kubwereza za M’Sukulu ya Utumiki wa Mulungu

Mafunso otsatirawa tidzawakambirana pa Sukulu ya Utumiki wa Mulungu, ya mlungu woyambira December 29, 2014.

  1. N’chifukwa chiyani tiyenera kumvera lamulo la pa Deuteronomo 14:1 limene limaletsa kudzichekacheka pa nthawi yolira maliro? [Nov. 3, w04 9/15 tsa. 27 ndime 5]

  2. N’chifukwa chiyani mafumu a ku Isiraeli ankayenera kukopera buku la Chilamulo cha Mulungu ‘n’kumaliwerenga masiku onse a moyo wawo’? (Deut. 17:18-20) [Nov. 3, w02 6/15 tsa. 12 ndime 4]

  3. N’chifukwa chiyani chilamulo chinkanena kuti “usamange ng’ombe ndi bulu kuti uzilimitse pamodzi”? Nanga lamulo limeneli limagwira ntchito bwanji kwa Akhristu? (Deut. 22:10) [Nov. 10, w03 10/15 tsa. 32]

  4. N’chifukwa chiyani Chilamulo chinkaletsa kulanda “mphero kapena mwala woperera monga chikole”? (Deut. 24:6) [Nov. 17, w04 9/15 tsa. 26 ndime 3]

  5. Kodi Aisiraeli ankafunika kumvera Mulungu chifukwa cha chiyani, nanga ifeyo n’chiyani chiyenera kutilimbikitsa kutumikira Yehova? (Deut. 28:47) [Nov. 24, w10 9/15 tsa. 8 ndime 4]

  6. Kodi ndi zinthu ziti zimene tiyenera kuchita kuti tikhale ndi moyo, zomwe zatchulidwa pa Deuteronomo 30:19, 20? [Nov. 24, w10 2/15 tsa. 28 ndime 17]

  7. Kodi tikamawerenga Baibulo tiyenera kumatchula mokweza mawu onse kuchokera Genesis mpaka Chivumbulutso? Fotokozani. (Yoswa 1:8) [Dec. 8, w13 4/15 tsa. 7 ndime 4]

  8. Kodi ‘kalonga wa gulu lankhondo la Yehova’ amene watchulidwa pa Yoswa 5:14, 15 ndi ndani, ndipo kodi zimene lembali likunena zingatilimbikitse bwanji? [Dec. 8, w04 12/1 tsa. 8 ndime 7]

  9. N’chiyani chinachititsa kuti Akani achimwe, nanga ifeyo tikuphunzirapo chiyani? (Yoswa 7:20, 21) [Dec. 15, w10 4/15 tsa. 20-21 ndime 2 ndi 5]

  10. Kodi chitsanzo cha Kalebe chimatilimbikitsa bwanji? (Yoswa 14:10-13) [Dec. 29, w04 12/1 tsa. 12 ndime 2]

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena