MFUNDO ZOTHANDIZA POPHUNZIRA
Muzigwiritsa Ntchito Baibulo Ngati Galasi
Mtumwi Yakobo anayerekezera Baibulo ndi galasi. Baibulo limatithandiza kudziwa zimene zili mumtima wathu. (Yak. 1:22-25) Ndiye kodi tingatani kuti tizigwiritsa ntchito Baibulo ngati galasi?
Muziwerenga mosamala. Munthu akayang’ana pa galasi mongodutsa, sangaone zinthu zina zomwe sizili bwino. Kuti tidziwe zinthu zimene sizili bwino mumtima mwathu tiyenera kuyang’anitsitsa, kapena kuti kuwerenga mosamala, m’Mawu a Mulungu.
Muziganizira kwambiri za inuyo osati ena. Ngati munthu atapendeketsa galasi angathe kuona zinthu zimene sizili bwino kwa munthu wina. Ifenso tikhoza kumaona mavuto a anthu ena pamene tikuwerenga Baibulo, koma tikamatero sitingaone mavuto athu omwe tiyenera kuwakonza.
Muzikhala oganiza bwino. Munthu akamangoganizira zinthu zolakwika zomwe waona pagalasi, akhoza kukhumudwa. Choncho tiyenera kukhala oganiza bwino tikamawerenga Baibulo. Tisamayembekezere kuti tizichita zambiri kuposa zimene Yehova amafuna.—Yak. 3:17.