ZIMENE ZACHITIKA M’CHAKA CHAPITACHI
“Taona Zodabwitsa”
Munthu wosaona akubatizidwa
TSIKU lina Yesu atachiritsa munthu wolumala, ‘anthu onse anadabwa kwambiri, ndipo anayamba kutamanda Mulungu, mwakuti anagwidwa ndi mantha. Iwo anali kunena kuti: “Taona zodabwitsa lero!”’ (Luka 5:25, 26) Masiku ano Yehova akuchita zambiri kudzera mwa Mwana wake, kapolo wokhulupirika ndi wanzeru komanso atumiki ake padziko lonse. Tikaganizira zonsezi timanenanso kuti: “Taona zodabwitsa.”