Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • yb15 tsamba 166-tsamba 167 ndime 3
  • Munthu Woyamba wa Chinenero Chamanja Kuphunzira Baibulo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Munthu Woyamba wa Chinenero Chamanja Kuphunzira Baibulo
  • Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2015
  • Nkhani Yofanana
  • ‘Yehova Wawalitsa Nkhope Yake pa Iwo’
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Muziona Kuti Abale ndi Alongo Anu Osamva Ndi Ofunika Kwambiri
    Nsanja ya Olonda—2009
  • “Akumva” Uthenga wa Ufumu ku Brazil
    Nsanja ya Olonda—2003
  • Vuto Losamva Silinandilepheretse Kuphunzitsa Anthu Ena Baibulo
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
Onani Zambiri
Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2015
yb15 tsamba 166-tsamba 167 ndime 3

DOMINICAN REPUBLIC

Munthu Woyamba wa Chinenero Chamanja Kuphunzira Baibulo

José Pérez

  • KUBADWA 1960

  • KUBATIZIDWA 1982

  • MBIRI YAKE Ali mnyamata ankakonda kwambiri Mulungu chifukwa chakuti abale ankamusonyeza chikondi ngakhale kuti iwo sankadziwa Chinenero Chamanja.

Picture on page 166

Ndinagontha ndili mwana ndipo ndinkapita kusukulu yophunzitsa Chinenero Chamanja. Ndili ndi zaka 11, ndinakumana ndi wa Mboni za Yehova ndipo anandiitanira ku misonkhano. Nditapita, sindinamveko chilichonse koma ndinangoona kuti anthu ake andilandira bwino kwambiri ndipo ndinaganiza zoti ndizisonkhanabe. Anthu ambiri mumpingomo ankandiitana kuti tikadye komanso tikacheze.

Mu 1982, ndinakhala wofalitsa ndipo chakumapeto kwa chakachi ndinabatizidwa. Mu 1984 ndinakwatira Eva, ndipo nayenso amangomva Chinenero Chamanja basi. Kunena zoona sitinkamvetsa mfundo zambiri za m’Baibulo koma chikondi chimene abale ankatisonyeza chinatitsimikizira kuti tapeza gulu la Yehova.—Yoh. 13:35.

Mu 1992, panakonzedwa zoti abale ndi alongo aphunzitsidwe Chinenero Chamanja cha ku America. Abale ndi alongo amene anaphunzitsidwawo anayamba kufufuza anthu ndiponso kuwaphunzitsa uthenga wabwino. Ndiyeno mu 1994, banja lina la ku Puerto Rico linaitanidwa kunthambi kuti liphunzitse abale ndi alongo 25 Chinenero Chamanja. Apa tsopano zinthu zinayamba kuyenda bwino m’gawo la chinenerochi.

Chakumapeto kwa chakachi kagulu ka chinenerochi kanakhazikitsidwa ndipo ine ndi Eva tinkasonkhana kumeneko. Titayamba kusonkhana kumeneku m’pamene tinamvetsa nkhani zina monga zoti Satana anatsutsa ulamuliro wa Yehova komanso zoti Yehova adzagwiritsa ntchito Ufumu wa Mesiya pokwaniritsa cholinga chake.

Pa December 1, 1995, mipingo ya Chinenero Chamanja cha ku America inakhazikitsidwa ku Santo Domingo ndi ku Santiago. Pofika mu August 2014, m’dzikoli munali mipingo 26 ya chinenero chamanja ndiponso timagulu 18.

Ine ndi Eva tinkangolankhula ndi ana athu Chinenero Chamanja. Mwana wathu woyamba dzina lake Éber amathandiza kumasulira Chinenero Chamanja kunthambi ya ku United States. Ine ndine mtumiki wothandiza ndipo mkazi wanga ndi mpainiya wokhazikika.

Mmene zinthu zinayendera m’gawo la Chinenero Chamanja kuyambira mu 1995 kufika mu 2014

  • 1995

    mipingo iwiri

    Chithunzi patsamba 167
  • 2014

    mipingo 26 ndi timagulu 18

    Chithunzi patsamba 167
    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena