Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • yb16 tsamba 143
  • Amakondana Ngakhale pa Nthawi ya Mavuto

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Amakondana Ngakhale pa Nthawi ya Mavuto
  • Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2016
Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2016
yb16 tsamba 143
Nyumba zomwe zinagwa kutachitika chivomezi ku Indonesia

INDONESIA

Amakondana Ngakhale pa Nthawi ya Mavuto

M’DZIKO la Indonesia, zinthu monga zivomezi, kusefukira kwa madzi komanso kuphulika kwa mapiri zimachitika kawirikawiri. Zimenezi zikachitika, atumiki a Yehova amathandiza mwamsanga anzawo amene akumana ndi mavutowa, makamaka abale awo auzimu. Mwachitsanzo, m’chaka cha 2005, chivomezi champhamvu chinawononga nyumba zambiri m’tauni ya Gunungsitoli, yomwe ndi tauni yaikulu pachilumba cha Nias ku North Sumatra. Abale a m’mipingo ya pachilumba cha Sumatra chomwe chili pafupi ndi chilumba cha Nias komanso a ku ofesi ya nthambi, anatumiza mwamsanga katundu kwa abale amene anakumana ndi vutoli. Woyang’anira dera komanso m’bale woimira ofesi ya nthambi anapita kuchilumbachi kuti akalimbikitse abale ndi alongo. M’bale Yuniman Harefa, yemwe ndi mkulu pachilumba cha Nias ananena kuti: “Chivomezichi chitachitika, anthu anachita mantha kwambiri. Koma zimene gulu la Mulungu linachita zinatithandiza kudziwa kuti sitili tokha.”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena