Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ijwyp nkhani 98
  • Ndingatani Ngati Ndimalephera ku Sukulu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ndingatani Ngati Ndimalephera ku Sukulu?
  • Zimene Achinyamata Amafunsa
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zimene mungachite
  • Mungathandize Bwanji Mwana Wanu Kuti Azikhoza Bwino Kusukulu?
    Mfundo Zothandiza Mabanja
  • Ndingatani Kuti Ndimalize Homuweki Yanga?
    Zimene Achinyamata Amafunsa
  • Kodi Nthaŵi Yochita Homuweki Ndingaipeze Kuti?
    Galamukani!—2004
  • ‘Zochita Zandichulukira’
    Galamukani!—2009
Onani Zambiri
Zimene Achinyamata Amafunsa
ijwyp nkhani 98
Achinyamata ambiri aweruka kusukulu. Mtsikana mmodzi akuoneka wokhumudwa chifukwa cholephera mayeso.

ZIMENE ACHINYAMATA AMAFUNSA

Ndingatani Ngati Ndimalephera ku Sukulu?

“Ndimaona anzanga ena akubwera m’kalasi popanda kunyamula makope, kenako amangomvetsera nyimbo uku aphunzitsi akuphunzitsa. Koma akalephera mayeso amadandaula. Ndiye pali anthu ena ngati ineyo, amene amawerenga mwawafawafa, koma mayeso akabwera amalephera. Sindikudziwa kuti zimenezi zimachitika chifukwa chiyani. Zimakhala zopweteka kwambiri kulephera mayeso pambuyo poti wakhala mawiki ambiri ukuchezera kuwerenga.”—Yolanda.

Kodi nanunso mumamva ngati Yolanda? Kunena zoona kulephera m’kalasi kumakhala kowawa kwambiri.

Achinyamata ena amene amalephera kusukulu, amafika potaya mtima ndipo amasiya kulimbikira m’kalasi. Pomwe ena amafika posiya sukulu. Mwina mungaone kuti njira yabwino ndi kusiya kulimbikira kapena kusiya sukulu, koma pali njira yabwino kwambiri yothetsera vuto limeneli. Tiyeni tikambirane mfundo 6 zimene zingakuthandizeni kuti muzikhoza bwino m’kalasi.

  • Zimene mungachite

  • Zimene anzanu amanena

Zimene mungachite

  • Muzipezeka m’kalasi. Mfundo imeneyi ingaoneke ngati yosathandiza, koma mukamathawa m’kalasi mukhoza kumangolephera.

    “Kusukulu kwathu, ana amene amathawa m’kalasi alibe nazo ntchito ngati atalephera ndipo siziwayendera bwino.”—Matthew.

    Mfundo ya m’Baibulo: “Chilichonse chimene munthu wafesa, adzakololanso chomwecho.”—Agalatiya 6:7.

  • Musamalole kuti zinthu zizikupitani m’kalasi. Kungopezeka m’kalasi ndi poyambira pabwino. Koma mukakhala m’kalasimo, muziyesetsa kuti zinthu zisamakupiteni. Ndi bwinonso kumalemba notsi. Ndipo muzimvetsetsa zimene aphunzitsi akunena. Ngati n’zololeka, muzifunsa mafunso m’kalasi.

    “Ndimakonda kufunsa mafunso ambiri m’kalasi chifukwa ndimaona kuti aphunzitsi amafotokoza bwino zinthu akazindikira kuti wophunzira wina sakumvetsa.”—Olivia.

    Mfundo ya m’Baibulo: “Muzimvetsera mwatcheru kwambiri.”—Luka 8:18.

  • Musamabere Mayeso. Kubera mayeso ndi chinyengo. Ndipo anthu kusukulu amabera mayeso m’njira zosiyanasiyana. Ena amangokopera zimene anzawo alemba. Kuchita zimenezi ndi chinyengo ndipo sikungakuthandizeni ngakhale pang’ono.

    “Ngati simukumvetsa zinthu zina, musamangokopera mayankho amene anzanu alemba. Kubera mayeso sikungakuthandizeni ngakhale pang’ono. Tikutero chifukwa chakuti m’malo moti muphunzire kuthana ndi mavuto panokha, mumazolowera kudalira anthu ena.”—Jonathan.

    Mfundo ya m’Baibulo: “Aliyense payekha ayese ntchito yake, kuti aone kuti ndi yotani. Akatero adzakhala ndi chifukwa chosangalalira ndi ntchito yake.”—Agalatiya 6:4.

  • Muzilemberatu homuweki mukangofika kunyumba. Ngati n’kotheka muzilemberatu homuweki musanayambe kupuma kapena kuchita zinthu zina.a Mukatero, mukhoza kupeza mpata wochita zinthu zina momasuka.

    “Ndinkalemberatu homuweki yanga, ndipo izi zinathandiza kuti ndizikhoza bwino kusukulu. Ndikafika kunyumba ndinkalakalaka kugona kapena kumvetsera nyimbo. Koma ndinkayesetsa kumaliza kaye homuweki yanga kenaka n’kumapuma.”—Calvin.

    Mfundo ya m’Baibulo: “Muzitsimikizira kuti zinthu zofunika kwambiri ndi ziti.”—Afilipi 1:10.

  • Muzipempha ena kuti akuthandizeni. Musamachite manyazi kupempha ena kuti akuthandizeni. Mwachitsanzo, mukhoza kupempha malangizo kwa makolo anu. Mungapemphenso aphunzitsi anu kuti akuthandizeni kudziwa zimene mungachite kuti muzikhoza m’kalasi. Nthawi zina mukhoza kupemphanso anthu amene amakuphunzitsani patitayimu kuti akuthandizeni.

    “Muzipita kukakumana ndi aphunzitsi anu. Muziwapempha kuti akuthandizeni kumvetsa zimene amaphunzitsa komanso kuti muzikhoza bwino m’kalasi. Aphunzitsiwo adzasangalala kwambiri kumva kuti mukuchita bwino m’kalasi ndipo adzakuthandizani.”—David.

    Mfundo ya m’Baibulo: “Aphungu akachuluka [zolingalira] zimakwaniritsidwa.”—Miyambo 15:22.

  • Muzigwiritsa ntchito mwayi uliwonse umene ulipo. M’mayiko ena, mayeso amakhala ndi mafunso owonjezera amene angathandize kuti mukhoze bwino. Mukhoza kudziperekanso kuti mupange ma pulojekiti ena amene angathandize kuti mukhoze bwino. Ngati mwalephera mayeso, mukhoza kupempha aphunzitsi anu kuti mulembenso.

    Mtsikana akuimba gitala kuchipinda kwake.

    Kuyesetsa kuti muzikhoza m’kalasi kuli ngati kuphunzira kuimba gitala. Munthu akachita khama, zimamuyendera bwino.

    “Ngati ndikufuna kukhoza bwino phunziro linalake, ndimapempha aphunzitsi ngati pali pulojekiti inayake yoti ndipange kapena ngati ndingalembenso mayesowo.”—Mackenzie.

    Mfundo ya m’Baibulo: “Kugwira ntchito iliyonse kumapindulitsa.”—Miyambo 14:23.

Zimene anzanu amanena

Alexandra.

“Muzikumbukira kuti mwayi wa sukulu umabwera kamodzi pamoyo. Ndipo munthu amakolola zimene anafesa.”—Alexandra.

Elijah.

“Muziuza aphunzitsi anu zolinga zimene muli nazo. Ndili kusukulu ndinkafunsa aphunzitsi anga kuti andiuze zimene ndingachite kuti ndizikhoza bwino. Pena ankandiuza kuti ndilembenso zomwe ndalephera kapena ndikapange homuweki ina kunyumba.”—Elijah.

Mackenzie.

“Muzichita zimene mungathe ndipo muzipempha ena kuti akuthandizeni. Nthawi zambiri aphunzitsi amakuthandizani akaona kuti inunso mukuyesetsa kuti muzikhoza bwino m’kalasi.”—Mackenzie.

Mfundo zobwereza: Ndingatani Ngati Ndimalephera ku Sukulu?

  1. Muzipezeka m’kalasi.

  2. Musamalole kuti zinthu zizikupitani m’kalasi.

  3. Musamabere Mayeso.

  4. Muzilemberatu homuweki mukangofika kunyumba.

  5. Muzipempha ena kuti akuthandizeni.

  6. Muzigwiritsa ntchito mwayi ulionse umene ulipo.

a Kuti mupeze mfundo zina zokuthandizani mukamawerenga, onani nkhani yakuti “Zimene Achinyamata Amafunsa . . . Ndingatani Kuti Ndimalize Homuweki yanga?”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena