THANDIZO KWA OFEDWA
Zimene Mungayembekezele
Ngakhale kuti akatswili ena amati pali njila imodzi yolilila malilo, m’ceni-ceni anthu amalila mosiyana-siyana. Kodi izi zitanthauza kuti ena sakhudzidwa kwambili na imfa, kapena “amabisa” mmene amamvelela? Osati kweni-kweni. Ngakhale kuti kuivomeleza imfa komanso kulila n’kothandiza, palinso zina zothandiza zimene mungacite. Kweni-kweni zimadalila cikhalidwe ca munthu, umunthu wake, zom’citikila mu umoyo, komanso mmene wakhudzidwila na imfa imeneyo.
KODI CISONI CINGAKHALE CACIKULU BWANJI?
Ofedwa sangadziŵe zoyembekezela munthu amene amam’konda akamwalila. Komabe, mmene angamvelele komanso zovuta zina zimene zingakhalepo, nthawi zambili zimakhala zodziŵikilatu. Ganizilani zitsanzo izi:
Kuthedwa nzelu. Munthu wofedwa amalila cifundo cikamugwila, kuyewa wokondedwa wake, kapenanso kukhumudwa-khumudwa. Ndipo kulota zocitika zokhudza wokondedwa wake komanso kum’ganizila kwambili kungawonjezelenso cisoni cake. Koma cinthu coyamba cingakhale kudabwa na kusakhulupilila. Tiina akumbukila mmene zinalili pamene mwamuna wake Timo, anamwalila mwadzidzidzi. Iye anati: “N’nadabwa. Poyamba n’nalephela ngakhale kulila. N’navutika kwambili maganizo cakuti nthawi zina n’nali kulephela kufuza bwino-bwino. Sin’nakhulupilile zimene zinacitika.”
Nkhawa, ukali, na kudziimba mlandu. Ivani anati: “Kwa nthawi ndithu, mwana wathu wamwamuna Eric wa zaka 24 atamwalila, ine na mkazi wanga Yolanda, tinali kukhala okwiya kwambili! Izi zinatidabwitsa, cifukwa kumbuyo konseko sitinakhalepo okwiya conco. Tinalinso kudziimba mlandu, cifukwa tinali kukaikila ngati tinacita zonse zotheka kuti tithandize mwana wathu.” Nayenso Alejandro, amene mkazi wake anamwalila pambuyo podwala kwa nthawi yaitali, anali kudziimba mlandu. Iye anati: “Poyamba n’naganiza kuti ngati Mulungu walola kuti nivutike conco, ndiye kuti ndine munthu woipa m’maso mwake. N’nadziimbanso mlandu cifukwa coona monga nipatsa mlandu Mulungu pa zimene zinacitika.” Kostas amene tam’gwila mawu m’nkhani yapita, anati: “Nthawi zina n’nali kukwiila Sophia cifukwa comwalila. Ndiyeno n’nadziimbanso mlandu cifukwa cokhala na maganizo amenewo. Sanacite kufuna kuti amwalile.”
Maganizo ovutitsa. Nthawi zina maganizo a munthu wofedwa sakhadzikika, amangoyenda-yenda. Mwacitsanzo, wofedwa angayambe kuganiza kuti wokondedwa wake amene anamwalila ca posacedwa, angamvetsele, kukhudzika mtima, komanso kuona. Mwina wofedwayo angavutike kuika maganizo pa cinthu cimodzi kapena kukumbukila zinthu. Tiina anakamba kuti: “Nthawi zina, nili mkati mokambilana na munthu, maganizo anga anali kucoka pa nkhaniyo! N’nali kuyamba kuganizila zimene zinacitika pa kumwalila kwa a Timo. Zimenezi zinali kunisautsa kwambili.”
Kufuna kukhala kwa yekha. Munthu wofedwa angakhale wokhumudwa-khumudwa komanso angamaipidwe kukhala pakati pa anthu. Kostas anati: “Nikakhala pakati pa okwatilana, n’nali kudzimva kuti nili nekha. Ndipo nikakhala pakati pa osakwatila n’nali kudzimvanso wosayenelela.” Nayenso Yolanda mkazi wa Ivan, amakumbukila mmene zinalili. Iye anati: “Zinali zovuta kukhala pakati pa anthu amene anali kudandaula za mavuto awo amene anali kuoneka ocepa poyelekezela na athu! Ndiyeno panalinso ena amene anali kutiuza mmene ana awo acitila bwino. N’nali kukondwela nawo, koma panthawi imodzi-modzi, sin’nali kufuna kumvela zimenezo. Ine na mwamuna wanga tinali kumvetsa kuti umoyo ndiye mmene ulili, koma tinali kufuna kukhala patekha cifukwa ca makambilano otelo.”
Mavuto okhudza thanzi. Mavuto ena odziŵikilatu amakhala kusafuna kudya, kuyonda, komanso kusoŵa tulo. Aaron amakumbukila mmene zinthu zinalili caka cotsatila kucokela pamene atate ake anamwalila. Iye anati: “N’nali kuvutika kugona. Nthawi zonse usiku, n’nali kuuka panthawi imodzi-modzi kuganizila za imfa ya atate.”
Alejandro akumbukila kuti anayamba kudwala matenda osadziŵika bwino. Iye anati: “Kangapo konse adokota ananipima, koma ananiuza kuti nili bwino-bwino. N’nayamba kuona kuti cisoni ndiye cinali kupangitsa zimenezo.” M’kupita kwa nthawi n’nayamba kumvelako bwino. Koma Alejandro anacitabe bwino kukaonana na adokota. Cisoni cikakula kwambili cingacepetse mphamvu yacitetezo ca m’thupi, cingakulitse matenda, kapena kuyambitsanso matenda ena.
Kulephela kucita zinthu zofunika. Ivan anati: “Eric atamwalila tinadziŵitsa abululu athu, mabwenzi, abwana ake, komanso a landilodi ake. Panalinso mapepa ambili a ku boma amene tinafunika kusaina, komanso kuona zinthu zaumwini za Eric. Kuti zonsezo zitheke, tinafunika kuika maganizo pa zimene tinali kucitazo. Koma panthawi imodzi-modzi, tinali olefuka maganizo komanso thupi.”
Koma kwa ena, vuto imadzabwela pakapita nthawi, pofuna kucita zinthu zimene mnzawo anali kucita. Ni mmenenso zinalili kwa Tiina. Iye anafotokoza kuti: “Nthawi zonse a Timo ndiye anali kusamalila za kasungidwe ka ndalama kubanki, komanso kucita zinthu zina zokhudza bizinesi. Tsopano zonsezi zinakhala udindo wanga, ndipo zinangowonjezela kupanikizika kwanga maganizo. N’nadzifunsa kuti, kodi nidzakwanitsa kucita zonsezi popanda kusokoneza?”
Mavuto amene tafotokoza pamwambapa, aonetsa kuti kupilila cisoni cobwela na imfa, kumakhala kovuta kwambili. Ndipo kukamba zoona, cisoni cimene cimakhalapo tikatayikidwa munthu amene tinali kum’konda, cingakhale cacikulu kwambili. Kudziŵilatu zimenezi, kungathandize amene anafedwa caposacedwa kupilila cisoni. Komanso kumbukilani kuti si onse ofedwa amene amakhudzidwa na zovuta zonse zimene zimabwela cifukwa ca imfa. Kuwonjezela apo, ofedwa angatonthozedwe kudziŵa kuti kumva cisoni cifukwa ca imfa n’cibadwa.
KODI NIDZAKHALANSO WACIMWEMWE?
Zimene mungayembekezele: Munthu akafedwa cisoni cimakhala cacikulu poyamba. Koma m’kupita kwa nthawi cimayamba kucepako. Izi sizitanthauza kuti cisonico “cimasililatu,” kapena munthuyo amaiŵalilatu za wokondedwa wake ayi. Nthawi zina cisoni cingabwelenso mwadzidzidzi pokumbukila zocitika zina, monga pa tsiku limene anakwatilana kapena limene wokondedwa wawo anamwalila. Koma m’kupita kwa nthawi, ambili amafika pokhazikika maganizo na kuyambanso kuika maganizo pa zocitika za tsiku na tsiku za mu umoyo. Izi zimatheka maka-maka ngati wofedwayo athandizidwa na acibululu, mabwenzi, komanso ngati acita zinthu zom’thandiza kupilila.
Kodi cisoni cingakhale kwa nthawi yaitali bwanji? Kwa ena, cisoni cimeneci cimakhala kwa miyezi cabe. Koma kwa ambili, caka cimodzi kapena ziŵili zingapitepo asanayambe kumvelako bwino. Ndipo ena zingatenge nthawi yaitali.a Alejandro anati: “Ine cisoni canga cinakhala pafupi-fupi zaka zitatu.”
Dzilezeleni mtima. Muzicita zimene mungakwanitse patsiku osati modzikakamiza, ndipo dziŵani kuti kumvela cisoni cifukwa ca imfa si kwa muyaya. Koma ngakhale n’conco, kodi pali zimene mungacite kuti mucepetse cisoni palipano, na kuti cisakhale kwa nthawi yaitali?
a Anthu ena ocepa angakhale na cisoni cacikulu kwambili ndipo cingatenge nthawi yaitali. Cisoni cimeneci cimachedwa cisoni “cocolowana” kapena “cokhalitsa.” Anthu aconco angafunikile kukaonana na madokota opeleka cithandizo kwa anthu ovutika maganizo.
Kumva cisoni cifukwa ca imfa n’cibadwa