LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • g20 na. 1 tsa. 3
  • Kodi Muli na Nkhawa?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Muli na Nkhawa?
  • Galamuka!—2020
  • Nkhani Zofanana
  • Kodi Nkhawa N’ciani?
    Galamuka!—2020
  • Zamkati
    Galamuka!—2020
  • Zimene Mungacite kuti Muthane na Nkhawa
    Galamuka!—2020
  • Kodi N’zinthu Ziti Zimabweletsa Nkhawa?
    Galamuka!—2020
Galamuka!—2020
g20 na. 1 tsa. 3
Ali na nkhawa ku nchito ndipo wagwetsa nkhope yake pansi komanso aoneka wacisoni.

PEZANI THANDIZO PA NKHAWA ZANU

Kodi Muli na Nkhawa?

Jill.a anati: “N’zoona kuti aliyense amakhala na nkhawa, koma ine zanyanya. Si vuto limodzi cabe limene nakumanapo nalo. Nakumana na mavuto osiyana-siyana ambili. Kuwonjezela apo, kwa nthawi yaitali nakhala nikusamalila mwamuna wanga amene amadwala maganizo komanso matenda ena ake.”

Barry anati: “Mkazi wanga ananithaŵa, ndipo n’nali kulela nekha ana aŵili. Kulela nekha ana kunali kovuta. Kuwonjezela apo, nchito inasila, ndipo sin’nali kukwanitsa kupeza ndalama zokonzetsela motoka. N’nasoŵa cocita. Kukamba zoona, n’nali na nkhawa kwambili. N’nali kudziŵa kuti kudzipha n’kulakwa, conco n’napempha Mulungu kuti nife cabe.”

Mofanana ndi Jill na Barry, kodi nthawi zina nkhawa zimakuculukilani? Ngati n’conco, lekani kuti nkhani zokonkhapo zikutonthozeni na kukuthandizani. Nkhanizi zidzafotokoza zinthu zimene kaŵili-kaŵili zimabweletsa nkhawa, mmene nkhawa zingatikhudzile, komanso zimene tingacite kuti ticepetse nkhawa.

a Maina ena asinthidwa.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani