PEZANI THANDIZO PA NKHAWA ZANU
Kodi N’zinthu Ziti Zimabweletsa Nkhawa?
Acipatala cochuka cochedwa Mayo Clinic anati: “Nkhawa zikuwonjeka kwa anthu akulu-akulu ambili. Umoyo m’dzikoli ni wosadalilika, ndipo zinthu zingasinthe nthawi iliyonse.” Onani zina mwa zinthu zimene zimabweletsa nkhawa:
kusila kwa cikwati
imfa ya munthu wokondedwa
matenda aakulu
ngozi yaikulu
upandu
umoyo wokhala na zocita zambili
matsoka acilengedwe komanso ocititsidwa ndi anthu
kupanikizika na sukulu komanso nchito
nkhawa zokhudza nchito, na kusoŵa ndalama