LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • g20 na. 1 masa. 5-7
  • Kodi Nkhawa N’ciani?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Nkhawa N’ciani?
  • Galamuka!—2020
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • NKHAWA YABWINO KOMANSO YOIPA
  • Zamkati
    Galamuka!—2020
  • Kodi Muli na Nkhawa?
    Galamuka!—2020
  • Zimene Mungacite kuti Muthane na Nkhawa
    Galamuka!—2020
Galamuka!—2020
g20 na. 1 masa. 5-7
Wa zamalonda ali mu mzinda ndipo akwela masitepu mothamanga kuti afike ku ofesi yake.

PEZANI THANDIZO PA NKHAWA ZANU

Kodi Nkhawa N’ciani?

Nkhawa imatanthauza zimene thupi limacita munthu akapanizika maganizo. Ubongo umatumiza mahomoni kumbali zonse za thupi. Izi zimapangitsa kuti mtima wa munthu uzigunda mothamanga, BP kukwela kapena kutsika, kupuma mwabefu, komanso kumvela kupweteka kwa minofu. Mukalibe kuzindikila zimene zikucitika, thupi lanu limakhala lokonzeka pa zimene zidzacitika. Zinthu zodetsa nkhawa zikatha, thupi lanu limakhalanso m’malo.

NKHAWA YABWINO KOMANSO YOIPA

Nkhawa ni njila yacibadwa imene imapangitsa munthu kulimbana na zovuta, kapena zinthu zoyofya. Nkhawa imayambila mu ubongo. Nkhawa yopindulitsa ingakuthandizeni kucita zinthu mwamsanga. Kukhala na nkhawa pa mlingo woyenela kungakuthandizeni kukwanilitsa zolinga zanu, kucita bwino pa mayeso a ku sukulu, pa maintavyu, kapena pa zamaseŵela.

Komabe, kukhala na nkhawa kwa nthawi yaitali, kapena nkhawa yaikulu, kungakuvulazeni. Ngati mumakhala na nkhawa pafupi-pafupi kapena nthawi zonse, mungayambe kudwala komanso kuvutika maganizo. Khalidwe lanu na kacitidwe ka zinthu ndi anthu ena kangasinthe. Nkhawa yaikulu ingapangitse munthu kuyamba kuseŵenzetsa amkolabongo na njila zina zowononga thanzi pofuna kulimbana na nkhawa. Ingapangitsenso munthu kuvutika maganizo, kulema kwambili, kapena kukhala na maganizo ofuna kudzipha.

Ngakhale kuti nkhawa ingakhudze anthu m’njila zosiyana-siyana, ingabweletse matenda ambili. Ndipo ingakhudze pafupi-fupi mbali zonse zathupi.

MMENE NKHAWA IMAKHUDZILA THUPI LANU

Mitsempha.

Wagwila pa mphumi ndipo ali na nkhawa.

Mitsempha ya m’thupi imapangitsa kuti mahomoni monga adrenaline na cortisol, atulutsidwe. Izi zimapangitsa kuti mtima uyambe kugunda mothamanga, BP kukwela, komanso kuti shuga iculuke m’magazi. Zonsezi zimapangitsa munthu kucitapo kanthu mwamsanga pa ngozi imene ingacitike. Nkhawa yopitilila malile ingapangitse munthu

  • kukhala wamtima wapacala, kuvutika maganizo, kudwala mutu, komanso na kusoŵa tulo

Cimangidwe ca thupi.

Minofu ingakutetezeni ku ngozi. Nkhawa yaikulu ingapangitse

  • thupi kuphwanya, mutu kuŵaŵa, kapena minofu kucita dzanzi

Kupuma.

Munthu amapuma mofulumila kuti akoke mpweya woculuka wa oxygen. Nkhawa yaikulu ingapangitse munthu kuyamba

  • kupuma mwabefu, na kusoŵa mpweya wokwanila m’thupi, komanso kudwala matenda ovutika maganizo

Kaseŵenzedwe ka Mtima.

Munthu akakhala na nkhawa, mtima wake umagunda mofulumila komanso mwamphamvu kuti upeleke magazi ku mbali zonse za thupi. Mitsempha ya magazi imakula kapena kucepa kuti ipeleke magazi ku mbali zimene zifunikila kwambili magazi, monga ku minofu. Nkhawa yaikulu ingapangitse munthu kukhala na

  • BP, matenda okhudza mtima, na sitroko

Anabele.

Anabele m’thupi lathu amatulutsa mahomoni ochedwa adrenaline na cortisol, amene amathandiza thupi kulimbana na nkhawa. Ciŵindi cimapangitsa shuga wa m’thupi kuculuka na kupeleka mphamvu zoculuka kuthupi lathu. Nkhawa yaikulu ingabweletse

  • matenda a shuga, kucepetsa mphamvu ya citetezo ca thupi, kudwala-dwala, kusintha-sintha mmene munthuyo alili, komanso kuina

Kumeza na kugaya zakudya.

Kugaya zakudya m’thupi lathu kumasokonezeka. Nkhawa yaikulu ingapangitse

  • munthu kucita mselu-selu, kusanza, kuthulula, na kumangika m’mimba

Ziwalo zobelekela.

Nkhawa zingacepetsenso cilako-cilako ca kugonana, zimene zingalepheletse nkhani ya ku cipinda kuyenda bwino. Ndipo nkhawa ikakula kwambili ingalepheletse

  • mwamuna kubala. Ndipo mkazi angayambe kusamba molekeza-lekeza

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani