LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • g20 na. 1 tsa. 4
  • Kodi N’zinthu Ziti Zimabweletsa Nkhawa?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi N’zinthu Ziti Zimabweletsa Nkhawa?
  • Galamuka!—2020
  • Nkhani Zofanana
  • Kodi Nkhawa N’ciani?
    Galamuka!—2020
  • Kodi Muli na Nkhawa?
    Galamuka!—2020
  • Zamkati
    Galamuka!—2020
  • Zimene Mungacite kuti Muthane na Nkhawa
    Galamuka!—2020
Galamuka!—2020
g20 na. 1 tsa. 4

PEZANI THANDIZO PA NKHAWA ZANU

Kodi N’zinthu Ziti Zimabweletsa Nkhawa?

Acipatala cochuka cochedwa Mayo Clinic anati: “Nkhawa zikuwonjeka kwa anthu akulu-akulu ambili. Umoyo m’dzikoli ni wosadalilika, ndipo zinthu zingasinthe nthawi iliyonse.” Onani zina mwa zinthu zimene zimabweletsa nkhawa:

  • kusila kwa cikwati

  • imfa ya munthu wokondedwa

  • matenda aakulu

  • ngozi yaikulu

  • upandu

  • umoyo wokhala na zocita zambili

  • matsoka acilengedwe komanso ocititsidwa ndi anthu

  • kupanikizika na sukulu komanso nchito

  • nkhawa zokhudza nchito, na kusoŵa ndalama

Bungwe loona za maganizo a anthu lochedwa American Psychological Association, linati: “Kucotsedwa nchito kumavutitsa maganizo kwambili. Anthu ocotsedwa nchito amakhala pangozi yodwala matenda, vikwati kusokonezeka, nkhawa, kuvutika maganizo ngakhale kufuna kudzipha. Kusila kwa nchito kumakhudza mbali zonse za umoyo wa munthu.”

ANA AMAKHALANSO NA NKHAWA

Ana ambili nawonso amavutika na nkhawa. Ena amawopsezedwa ku sukulu kapena kusasamalidwa bwino pa nyumba. Anthu ena amaŵacitila nkhanza monga kuŵamenya, kuŵacitila zinthu zoŵavutitsa maganizo, kapena kucita nawo zaciwelewele. Ana ambili akalemba mayeso amakhala na nkhawa yakuti kaya adzaphasa kapena adzafeluka. Kuwonjezela apo, ana ena amaona makolo awo akusudzulana. Ana amene ali na nkhawa angayambe kulota zinthu zoyofya, kupanizika maganizo, komanso kusafuna kukhala pakati pa anthu ena. Ena amalephela kulamulila mkwiyo wawo. Mwana amene adwala matenda a nkhawa afunika cithandizo ca mwamsanga.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani