LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • ll gao 13 masa. 28-29
  • Kodi Tiyenela Kucita Ciani Kuti Tikondweletse Mulungu?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Tiyenela Kucita Ciani Kuti Tikondweletse Mulungu?
  • Mvetselani kwa Mulungu Kuti Mukhale ndi Moyo Wamuyaya
  • Nkhani Zofanana
  • Anzake a Mulungu Amakana Kucita Voipa
    Na Imwe Mungakhale Mnzake wa Mulungu!
  • Gao 13
    Mvetselani kwa Mulungu
  • Kulambila Kumene Mulungu Amavomeleza
    Zimene Baibulo Ingatiphunzitse
  • Cikondi Ca Mulungu N’camuyaya
    Mmene Tingakhalilebe mu Cikondi ca Mulungu
Onaninso Zina
Mvetselani kwa Mulungu Kuti Mukhale ndi Moyo Wamuyaya
ll gao 13 masa. 28-29

GAO 13

Kodi Tiyenela Kucita Ciani Kuti Tikondweletse Mulungu?

Pewani zoipa. 1 Akorinto 6:9, 10

Zinthu zimene Mulungu safuna—kuba, kukolewa, kuseŵenzetsa mankhwala osokoneza ubongo, ndeu, kupemphela kwa mafano, ndi kulambila mafano

Ngati timakonda Yehova, sitidzacita zinthu zimene iye safuna.

Yehova safuna kuti tiziba, tizikolewa, kapena kuseŵenzetsa mankhwala osokoneza ubongo.

Mulungu amadana ndi kupha, kucotsa mimba, kugonana amuna kapena akazi okha-okha. Safuna kuti tikhale adyela kapena andeu.

Sitiyenela kulambila mafano kapena kucita zamizimu.

M’Paladaiso imene idzakhalako padziko lapansi, simudzakhala anthu ocita zoipa.

  • Kodi Mulungu amaona bwanji zamatsenga?—Deuteronomo 18:10-12.

  • N’cifukwa ciani sitiyenela kulambila mafano?—Yesaya 44:15-20.

Citani zabwino. Mateyu 7:12

Zinthu zimene Mulungu amakondwela nazo—kuonetsa ena cikondi, kukhala oona mtima, na kukhala okhululuka

Kuti tikondweletse Mulungu, tiyenela kuyesa-yesa kukhala ngati iye.

Onetsani cikondi kwa ena mwa kukhala okoma mtima ndi opatsa.

Khalani oona mtima.

Mboni za Yehova ziŵili zilalikila mwamuna

Uzani ena za Yehova ndi njila zake.—Yesaya 43:10.

Khalani acifundo ndi okhululuka.

  • Tsanzilani Yehova.—1 Petulo 1:14-16.

  • Muzikondana.—1 Yohane 4:7, 8, 11.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani