LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • jl phunzilo 24
  • Kodi Ndalama za Nchito Yathu Zimacokela Kuti?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Ndalama za Nchito Yathu Zimacokela Kuti?
  • Ndani Amene Akucita Cifunilo Ca Yehova Masiku Ano?
  • Nkhani Zofanana
  • Mmene Timapezela Ndalama Zoyendetsela Nchito za Ufumu
    Ufumu wa Mulungu Ukulamulila
  • Kodi ndalama zoyendetsela nchito yathu timazipeza bwanji?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Kodi N’kumupatsilanji Amene Zonse N’zake?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2018
  • “Okonzeka Kupeleka Mphatso kwa Yehova”
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2018
Onaninso Zina
Ndani Amene Akucita Cifunilo Ca Yehova Masiku Ano?
jl phunzilo 24

PHUNZILO 24

Kodi Ndalama za Nchito Yathu Zimacokela Kuti?

Wina apanga copeleka caufulu
Mboni za Yehova zili mu ulaliki

Ku Nepal

Anchito odzipeleka kumanga Nyumba ya Ufumu ku Togo

Ku Togo

Anchito odzipeleka akusewenza pa ofesi ya nthambi ku Britain

Ku Britain

Caka ciliconse, gulu lathu limasindikiza Mabaibo ndi mabuku mamiliyoni ambili ndi kuwagaŵila popanda kulipilitsa. Timamanga Nyumba za Ufumu ndi maofesi a nthambi ndipo timazisamalila. Timacilikiza abale ndi alongo ambili a pa Beteli ndi amishonale, ndipo timapeleka thandizo pakagwa tsoka. Conco mungafunse kuti: ‘Kodi ndalama zake zimacokela kuti?’

Sitipeleka cakhumi, kulipilitsa mtulo, kapena kuyendetsa mbale ya zopeleka. Nchito yathu yolalikila imafuna ndalama zambili, koma sitipempha ndalama. Zaka zopitilila 100 m’mbuyomu, magazini yaciŵili ya Nsanja ya Olonda inakamba kuti timakhulupilila kuti Yehova ndiye amatithandiza ndi kuti “sitidzapempha thandizo kwa anthu”—ndipo sitinapemphepo!—Mateyu 10:8.

Nchito yathu imacilikizidwa ndi zopeleka zaufulu. Anthu ambili amayamikila nchito yathu yophunzitsa Baibo ndipo amapeleka ndalama kuthandiza pa nchito imeneyi. Ndipo Mboni za Yehova mocokela pansi pa mtima zimagwilitsila nchito nthawi yao, mphamvu zao, ndalama zao, ndi zinthu zina kucita cifunilo ca Mulungu padziko lonse. (1 Mbiri 29:9) Pa Nyumba ya Ufumu, pa misonkhano yadela ndi ya cigawo, pamakhala mabokosi a zopeleka, kuti amene afuna aponyemo. Kapena mungacite zopeleka kupitila pa webusaiti yathu ya jw.org. Nthawi zambili, zopeleka zimene timalandila zimacokela kwa anthu amene alibe zambili, monga mkazi wamasiye wosauka uja, amene Yesu anayamikila cifukwa coponya tumakobili tuŵili moponyamo zopeleka. (Luka 21:1-4) Conco, aliyense ‘angaziika kenakake pambali’ kuti apeleke “mogwilizana ndi mmene watsimikizila mumtima mwake.”—1 Akorinto 16:2; 2 Akorinto 9:7.

Tili ndi cikhulupililo cakuti Yehova adzapitiliza kusonkhezela mitima ya anthu amene amafuna ‘kumulemekeza ndi zinthu zao zamtengo wapatali,’ kuti acilikize nchito ya Ufumu, kotelo kuti cifunilo cake cicitike.—Miyambo 3:9.

  • Kodi gulu lathu limasiyana bwanji ndi zipembedzo zina?

  • Kodi zopeleka zaufulu zimagwila nchito yanji?

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani