Kodi ndalama zoyendetsela nchito yathu timazipeza bwanji?
Caka ciliconse timasindikiza ndi kutumiza mabaibulo ndi mabuku ofotokoza Baibulo mamiliyoni ambilimbili. Timamanga ndi kuyang’anila maofesi a nthambi ndi nyumba zosindikiza mabuku padziko lonse lapansi. Mipingo yambili imasonkhana m’malo olambilila okongola ndi ocititsa cidwi kwambili ochedwa Nyumba za Ufumu. Nanga ndalama zocitila zonsezi timazipeza bwanji?
Nchito yathu imacilikizidwa ndi ndalama zimene anthu amapeleka mwakufuna kwao. (2 Akorinto 9:7) Mu 1879, magazini ya Nsanja ya Mlonda, imene panthawiyo inali kuchedwa Zion’s Watch Tower, inati: “Sitikaikila kuti YEHOVA ndi amene akutsogolela nchito yofalitsa magazini ino, motelo sitidzapemphetsa kwa anthu kapena kuwacondelela kuti athandize pa nchito imeneyi.” Mpaka pano sitipemphetsa ndalama.
Ndalama zimenezi zimapelekedwa mwacindunji ku ofesi ya nthambi kapena kuikidwa m’kabokosi ka zopeleka kamene kali m’Nyumba ya Ufumu iliyonse. Koma sitisonkhetsa ndalama, kapena kulipilitsa anthu ndalama ndipo mabuku athu sitigulitsa. Sitilipilidwa kuti tilalikile, tiphunzitse ena mu mpingo kapena timange malo olambilila. Pakuti Yesu anati: “Munalandila kwaulele, patsani kwaulele.” (Mateyu 10:8) Atumiki onse amene amagwila nchito pa maofesi a nthambi ndi ku likulu lathu, komanso amene ali mu Bungwe Lolamulila la Mboni za Yehova, salandila ndalama.
Ndalama zimenezi zimathandizanso pakacitika ngozi zacilengedwe. Akristu oyambilila anali ofunitsitsa kuthandiza ena panthawi ya mavuto. (Romans 15:26) Mofananamo, timathandiza amene akhudzidwa ndi ngozi za cilengedwe mwa kuwamangilanso nyumba zao, Nyumba zolambilila ndi kuwapatsa zakudya, zovala, ndi thandizo la mankhwala.
“Ngakhale kuti Mboni za Yehova zimacita zinthu zonsezi, ndalama zoyendetsela nchito yao zimacokela m’zopeleka zimene aliyense amacita mwakufuna kwake ndi panthawi imene afuna.”—Khoti loona pa Ufulu wa Anthu la European Court of Human Rights, 2011