UMOYO WATHU WACIKHRISTU
“Okonzeka Kupeleka Mphatso kwa Yehova”
Kodi ise lelo tingakhale bwanji “okonzeka kupeleka mphatso kwa Yehova?” (1 Mbiri 29:5, 9, 14) Pansipa pali njila zingapo zimene tingasankhepo popanga zopeleka zaufulu zothandizila nchito yathu, m’dziko lathu na padziko lonse.
ZOPELEKA ZOTUMIZA PA INTANETI KAPENA ZOPONYA M’TUMABOKOSI ZIMATHANDIZILA PA:
NCHITO YA PADZIKO LONSE
kumanga na kuyendetsa zinthu m’maofesi a nthambi na m’maofesi omasulila mabuku
masukulu a maphunzilo aumulungu
atumiki anthawi zonse apadela
kupulinta mabuku, kupanga mavidiyo, na kuika zinthu pa webusaiti yathu
MPINGO
ndalama zoseŵenzetsa pa mpingo na kukonzako zinthu pa Nyumba ya Ufumu
ndalama zimene mpingo wagamula kuti zitumiziwe ku ofesi ya nthambi kuti:
zikathandizile kumanga Nyumba za Ufumu na Mabwalo a Misonkhano padziko lonse
makonzedwe a Kupeleka Cithandizo Padziko Lonse
nchito zina padziko lonse
MISONKHANO YACIGAWO KOMANSO YADELA
Zopeleka zanu pa msonkhano wacigawo zimatumizidwa kuti zithandizile nchito ya padziko lonse. Ndipo, ndalama zimene zimafunikila pa misonkhano yacigawo, yapadela, ndiponso ya maiko zimacokela pa ndalama zimenezo.
Zopekela zanu pa msonkhano wadela zimathandiza pa kulipilla malowo, kuyendetsela na kukonzela zinthu pa malo ocitilapo misonkhano yadela, komanso pa zinthu zina zimene zimafuna ndalama. Abale a m’dela angasankhe kupeleka ndalama zotsala kuti zikathandizile nchito ya padziko lonse.