UMOYO WACIKHILISITU
Mphamvu ya ‘Tumakobili Tuŵili Twatung’ono’
Copeleka ca mkazi wamasiye cinali cosakwanila ngakhale kugulila cakudya cochipa kwambili. (Onani w08 3/1 peji 12 ndime 1-3.) Komabe, copeleka cake cinaonetsa kuti anali kum’konda kwambili Yehova ndiponso anali kuona kulambila Mulungu kukhala kofunika ngako. Pa cifukwa cimeneci, copelekaco cinali camtengo wapatali kwa Atate wake wakumwamba.—Maliko 12:43.
TAMBANI VIDIYO YAKUTI ‘KUPELEKA MPHATSO KWA YEHOVA,’ KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATILAWA:
Kodi zopeleka zathu zimathandiza pa nchito monga ziti?
N’cifukwa ciani zopeleka zathu n’zofunika kwambili olo zioneke monga zocepa?
Tingadziŵe bwanji njila zosiyana-siyana zocitila zopeleka, zimene zilipo m’dela lathu?—Onani bokosi yakuti “Phunzilani Zambili pa Intaneti”