LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w15 12/15 masa. 15-16
  • Muziyamikila Kuolowa Manja kwa Yehova

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Muziyamikila Kuolowa Manja kwa Yehova
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • CITSANZO CABWINO KWAMBILI CA KUOLOWA MANJA
  • “Nchitoyi Ndi Yaikulu”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2016
  • “Munthu Wopatsa Mowolowa Manja Adzalandila Mphoto”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2017
  • Yehova Amadalitsa Kwambili Anthu Ofunitsitsa Kupeleka
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
  • “Okonzeka Kupeleka Mphatso kwa Yehova”
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2018
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
w15 12/15 masa. 15-16
Mkazi akuloŵetsa khadi la ku banki mu cida camakono cotumizila ndalama

MUZIYAMIKILA KUOLOWA MANJA KWA YEHOVA

YEHOVA ndi Mulungu woolowa manja. (Yakobo 1:17) Zinthu zonse zimene analenga zimasonyeza kuti ndi woolowa manja. Iye analenga nyenyezi zambilimbili kumwamba ndi zomela zosiyanasiyana zokongola padziko lapansi.—Salimo 65:12, 13; 147:7, 8; 148:3, 4.

Amene analemba Salimo 104 anayamikila kwambili Yehova cifukwa ca zinthu zonse zimene analenga moti analemba nyimbo yomutamanda. Mukaŵelenga lemba limeneli, kodi nanunso mumayamikila Yehova ngati mmene wamasalimo anacitila? Iye anati: “Ndidzaimbila Yehova moyo wanga wonse. Ndidzaimba nyimbo zotamanda Mulungu wanga nthawi yonse ya moyo wanga.” (Salimo 104:33) Kodi inunso mumafuna kutamanda Mulungu?

CITSANZO CABWINO KWAMBILI CA KUOLOWA MANJA

Yehova amafuna kuti tikhale owolowa manja monga mmene iye alili. Ndipo watiuza zifukwa zimene tiyenela kucitila zimenezi. Yehova anauzila mtumwi Paulo kulemba kuti: “Lamula acuma a m’nthawi ino kuti asakhale odzikweza, ndiponso kuti asamadalile cuma cosadalilika, koma adalile Mulungu, amene amatipatsa mowolowa manja zinthu zonse kuti tisangalale. Uwalamule kuti azicita zabwino, akhale olemela pa nchito zabwino, owolowa manja, okonzeka kugawila ena, ndiponso asunge maziko abwino a tsogolo lao monga cuma, kuti agwile mwamphamvu moyo weniweniwo.”—1 Timoteyo 6:17-19.

M’kalata yake yaciŵili yopita ku Akorinto, Paulo anafotokoza mtima umene tiyenela kukhala nao popatsa zinthu anthu ena. Iye anati: “Aliyense acite mogwilizana ndi mmene watsimikizila mumtima mwake, osati monyinyilika kapena mokakamizika, cifukwa Mulungu amakonda munthu wopeleka mokondwela.” (2 Akorinto 9:7) Kodi tikakhala owolowa manja ndani amapindula? Paulo ananena kuti anthu ena amapindula tikawapatsa zosowa zao, koma ifenso timapindula cifukwa Yehova amatidalitsa.—2 Akorinto 9:11-14.

Ndiyeno, Paulo anafotokoza umboni waukulu wakuti Mulungu ndi woolowa manja. Iye anati: “Tikuyamika Mulungu cifukwa ca mphatso yake yaulele, imene sitingathe n’komwe kuifotokoza.” (2 Akorinto 9:15) ‘Mphatso yaulele’ yocokela kwa Yehova ndi zinthu zonse zimene iye amatipatsa kudzela mwa Yesu Kristu. Mphatso imeneyi ndi yapamwamba kwambili cakuti sitingathe kuifotokoza.

Kodi tingaonetse bwanji kuti timayamikila zinthu zonse zimene Yehova ndi Yesu aticitila ndiponso zimene adzaticitila mtsogolo? Njila imodzi imene tingacitile zimenezi ndi mwa kugwilitsila nchito nthawi yathu, mphamvu zathu, ndi cuma cathu polambila Yehova ndi pothandiza ena kudziŵa za iye. Tingathe kucita zimenezi kaya tili ndi zinthu zambili kapena zocepa.—1 Mbiri 22:14; 29:3-5; Luka 21:1-4.

Zimene Ena Amapeleka Pocilikiza Nchito Yapadziko Lonse

Mofanana ndi Akristu a m’nthawi ya atumwi, Akristu ambili masiku ano amaika ndalama pambali kuti akaponye m’bokosi la zopeleka zaufulu ku mpingo wao pocilikiza nchito yapadziko lonse. (1 Akorinto 16:2) Mwezi uliwonse mipingo imatumiza zopeleka zimenezi ku ofesi ya Mboni za Yehova m’dziko lao. N’zothekanso kutumiza nokha zopeleka zanu ku ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova m’dziko lanu. Mungafunse ofesi ya nthambi m’dziko lanu kuti mudziŵe mmene mungacitile zimenezi. Adilesi ya ofesi ya nthambi iliyonse imapezeka pa webusaiti ya www.jw.org. Mungapeleke zopeleka zanu m’njila izi:

ZOPELEKA MWACINDUNJI

  • Mungatumize copeleka canu kudzela ku banki kapena pogwilitsila nchito makadi a kubanki. M’maiko ena, mungatumize ndalama kupitila pa webusaiti ya jw.org kapena webusaiti ina.

  • Mukhoza kupeleka ndalama, zinthu ngati ndolo (masikiyo), mphete, zibangili ndiponso zinthu zina zamtengo wapatali. Muyenela kuzitumiza limodzi ndi kalata yonena kuti zinthuzo ndi mphatso.

ZONGOBWELEKETSA

  • Mungapeleke ndalama n’kufotokoza kuti mudzaziitanitsa mukadzazifuna.

  • Muyenela kutumiza ndalamazo limodzi ndi kalata yonena kuti mwangobweleketsa ndalamazo.

MPHATSO ZINA

Kuwonjezela pa kupeleka mphatso za ndalama kapena zinthu zina zamtengo wapatali, pali njila zinanso zopelekela zinthu zothandiza pa nchito yolalikila padziko lonse. Njila zimenezi zili m’munsimu. Musanasankhe njila iliyonse, muyenela kufunsa ku ofesi ya nthambi kuti mudziŵe njila zimene ndi zotheka m’dziko lanu. Popeza malamulo amasiyana malinga ndi dziko, muyenela kufunsanso anthu odziŵa bwino za malamulo ndi misonkho.

Inshuwalansi: Mungakonze zoti gulu la Yehova lidzalandile ndalama za inshuwalansi kapena za penshoni.

Maakaunti Akubanki: Ngati n’zovomekezeka kwanuko, mukhoza kupeleka zinthu monga maakaunti anu akubanki, zikalata zosungitsila ndalama, kapena maakaunti a ndalama zimene mukusunga kuti mudzagwilitse nchito mukadzapuma pa nchito. Mukhozanso kukonza zoti mukadzamwalila, gulu la Mulungu lidzatenge zinthuzo.

Masheya: Mungapeleke ku gulu la Yehova masheya amene muli nao m’kampani kapena kukonza zoti lidzalandile masheyawo mukadzamwalila.

Malo ndi Nyumba: Mungapeleke ku gulu la Yehova malo ndi nyumba zoti zingagulitsidwe. Ngati nyumbayo ndi imene mukukhalamo, mukhoza kuipeleka komabe n’kupitiliza kukhalamo pa nthawi yonse imene muli ndi moyo.

Cuma Camasiye: Mukhoza kulemba mu wilo yovomelezeka ndi boma kuti gulu la Yehova lidzapatsidwe katundu wanu kapena ndalama zanu, inuyo mukadzamwalila. Njila imeneyi imacepetsako msonkho umene mwiniwake cumaco amapeleka.

Ngati mufuna kudziŵa zambili, mungafunse ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ya m’dziko lanu.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani