LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w16 November masa. 19-20
  • “Nchitoyi Ndi Yaikulu”

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • “Nchitoyi Ndi Yaikulu”
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2016
  • Nkhani Zofanana
  • Yehova Amadalitsa Kwambili Anthu Ofunitsitsa Kupeleka
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
  • “Munthu Wopatsa Mowolowa Manja Adzalandila Mphoto”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2017
  • Muziyamikila Kuolowa Manja kwa Yehova
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • “Okonzeka Kupeleka Mphatso kwa Yehova”
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2018
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2016
w16 November masa. 19-20
Mfumu Davide ionetsa munthu mapulani a kamangidwe ka kacisi; m’bale ayang’ana mapulani a kamangidwe

“Nchitoyi Ndi Yaikulu”

NI NTHAWI ya msonkhano wofunika kwambili m’Yerusalemu. Mfumu Davide waitana akalonga ake onse, nduna za mfumu, ndi amuna olemekezeka. Onse ni okondwa ngako kumvela cilengezo capadela. Yehova wapatsa Solomo, mwana wa Davide, nchito yapadela yomanga kacisi kuti azilambililamo Mulungu woona. Mfumu ya Isiraeli yacikalambile inalandila mwa mzimu woyela mapulani akamangidwe ka kacisiyo. Ndipo iye lomba akupatsa mwana wake Solomo mapulaniwo. Ndiyeno, Davide akuuza anthuwo kuti: “Nchitoyi ndi yaikulu cifukwa cinyumba cacikuluci, si ca munthu ayi, koma ndi ca Yehova Mulungu.”—1 Mbiri 28:1, 2, 6, 11, 12; 29:1.

Ndiyeno Davide afunsa kuti: “Ndani lelo ali wokonzeka kupeleka mphatso kwa Yehova?” (1 Mbiri 29:5) Mukanakhalapo, kodi mukanayankha bwanji? Kodi mukanacilikiza nchito yaikulu imeneyo? Aisiraeli anagwapo pa nchito imeneyo. Ndithudi, “anasangalala cifukwa ca nsembe zaufulu zimene anapeleka, pakuti anapeleka nsembezo kwa Yehova ndi mtima wathunthu.”—1 Mbiri 29:9.

Patapita zaka zambili, Yehova anakhazikitsa cinthu cina capamwamba kupambana kacisi wakuthupi ameneyo. Iye anakhazikitsa kacisi wamkulu wauzimu, amene ni makonzedwe othandiza anthu kulambila Mulungu mwa nsembe ya Yesu. (Aheb. 9:11, 12) Kodi Yehova amathandiza bwanji anthu kuyanjananso naye masiku ano? Amacita zimenezo kupitilila m’nchito yopanga ophunzila. (Mat. 28:19, 20) Cifukwa ca nchitoyi, caka ciliconse anthu mamiliyoni amaphunzila Baibo, enanso masauzande amabatizika, ndipo mipingo yatsopano mahandiledi imapangidwa.

Ciwonjezeko cimeneci cimafunanso kupulintha mabuku ambili ophunzilila Baibo, kumanga ndi kukonzanso Nyumba za Ufumu, ndi mabwalo a misonkhano ya dela ndi ya cigawo. Kodi simungavomeleze kuti nchito yathu yolalikila uthenga wabwino ni yaikulu komanso yopindulitsa?—Mat. 24:14.

Kukonda Mulungu ndi anthu, komanso pakuti nchito yolalikila Ufumu ifunika kucitika mwamsanga, anthu a Mulungu ‘akupeleka mphatso kwa Yehova’ mwa kucita zopeleka zaufulu. N’zokondweletsa cotani nanga, ‘kulemekeza Yehova ndi zinthu zathu zamtengo wapatali.’ N’coyamikilikanso kuona kuti zopelekazo amaziseŵenzetsa bwino pa nchito yaikulu imene siinacitikepo n’kale lonse.—Miy. 3:9.

Zimene Ena Amapeleka Pocilikiza Nchito Ya Padziko Lonse

Anthu ambili masiku ano amapanga bajeti kapena kuika kandalama “kenakake pambali” kuti akaponye m’mabokosi a zopeleka za “Nchito Yapadziko Lonse.” (1 Akor. 16:2) Mwezi uliwonse, mipingo imatumiza zopeleka zimenezi ku ofesi ya Mboni za Yehova m’dziko lawo. N’zothekanso kutumiza mwekha zopeleka zanu ku ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova m’dziko lanu. Mungafunse ku ofesi ya nthambi m’dziko lanu kuti mudziŵe mmene mungacitile zimenezi. Adresi ya ofesi ya nthambi iliyonse imapezeka pa webusaiti ya www.jw.org. Mungapeleke zopeleka zanu m’njila izi:

ZOPELEKA MWACINDUNJI

  • Mungapeleke ndalama, ndolo (masikiyo), mphete, zibangili, ndi zinthu zina zamtengo wapatali. Tumizani zinthuzo pamodzi na kalata yokamba kuti ni copeleka.

ZOBWELEKETSA

  • Mungapeleke ndalama n’kufotokoza kuti mudzaziitanitsa mukadzazifuna.

  • Tumizani ndalamazo pamodzi na kalata yokamba kuti n’zobweleketsa.

MPHATSO ZINA

Kuwonjezela pa kupeleka mphatso za ndalama kapena zinthu zina zamtengo wapatali, pali njila zinanso zopelekela zinthu zothandiza pa nchito ya Ufumu padziko lonse. Njila zimenezi zili munsimu. Mukalibe kusankha njila iliyonse, muyenela kufunsa ku ofesi ya nthambi kuti mudziŵe njila zimene ndi zotheka m’dziko lanu. Popeza malamulo amasiyana malinga ndi dziko, muyenela kufunsanso anthu odziŵa bwino za malamulo ndi misonkho.

Inshuwalansi: Mungakonze zoti gulu la Yehova lidzalandile ndalama za inshuwalansi kapena za penshoni.

Maakaunti Akubanki: Mukhoza kupeleka zinthu monga maakaunti anu akubanki, zikalata zosungitsila ndalama, kapena maakaunti a ndalama zimene mukusunga kuti mudzagwilitse nchito mukadzapuma pa nchito. Mungakonzenso zoti mukadzamwalila, gulu la Mulungu lidzatenge zinthuzo. Pocita zimenezi, muyenela kutsatila malamulo amene mabanki a m’dziko lanu amayendela.

Masheya: Mungapeleke ku gulu la Yehova masheya amene muli nawo m’kampani kapena kukonza zoti lidzalandile masheyawo mukadzamwalila.

Malo na Nyumba: Mungapeleke ku gulu la Yehova malo na nyumba zimene angagulitse. Ngati nyumbayo ndi imene mukukhalamo, mukhoza kuipeleka koma n’kupitiliza kukhalamo pa nthawi yonse imene muli na moyo.

Cuma Camasiye: Mukhoza kulemba mu wilo yovomelezeka ndi boma kuti gulu la Yehova lidzapatsidwe katundu wanu kapena ndalama zanu, inuyo mukadzamwalila.

Ngati mufuna kudziŵa zambili, dinizani pa linki yakuti “Citani Copeleka ku Nchito Yathu ya Padziko Lonse” pansi pa peji yoyamba pa jw.org, kapena mungalembe kalata ku ofesi ya nthambi ya Mboni za Yehova ya m’dziko lanu.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani