LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • fg phunzilo 10 Mafunso. 1-4
  • Kodi Kulambila Koona Mungakudziŵe Bwanji?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Kulambila Koona Mungakudziŵe Bwanji?
  • Uthenga Wabwino Wocokela kwa Mulungu
  • Nkhani Zofanana
  • Kulambila Kumene Mulungu Amavomeleza
    Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
  • Kulambila Kumene Mulungu Amavomeleza
    Zimene Baibulo Ingatiphunzitse
  • Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
  • Mmene Mungadziŵile Cipembedzo Coona
    Na Imwe Mungakhale Mnzake wa Mulungu!
Onaninso Zina
Uthenga Wabwino Wocokela kwa Mulungu
fg phunzilo 10 Mafunso. 1-4

PHUNZILO 10

Kodi Kulambila Koona Mungakudziŵe Bwanji?

1. Kodi pali cipembedzo coona cimodzi cabe?

Yesu aphunzitsa

“Cenjelani ndi aneneli onama.”​—MATEYU 7:15.

Yesu anaphunzitsa otsatila ake cipembedzo cimodzi cabe coona. Cili monga mseu wotsogolela ku moyo wosatha. Yesu anati: “Amene akuupeza [mseu umenewu] ndi oŵelengeka.” (Mateyu 7:14) Mulungu amavomeleza cabe kulambila kumene kumazikidwa pa Mau ake, Baibo. Olambila onse oona ndi ogwilizana pa cikhulupililo cimodzi.​—Ŵelengani Yohane 4:23, 24; 14:6; Aefeso 4:4, 5.

Tambani vidiyo Kodi Mulungu Amavomeleza Kulambila Konse?

2. Kodi Yesu anakamba ciani za Akristu onama?

Mtsogoleli wacipembedzo akamba ndi anthu m’chalichi. Pambuyo pake akudalitsa asilikali kunkhondo.

“Amanena poyela kuti amadziŵa Mulungu, koma amamukana ndi zocita zao.”​—TITUS 1:16.

Yesu anacenjeza kuti aneneli onama adzaipitsa Cikristu. Kunja, amaoneka ngati olambila oona. Anthu a m’machalichi ao amakamba kuti ndi Akristu. Koma mungawazindikile mmene io alili m’ceni-ceni. N’cifukwa ciani takamba conco? Cifukwa kulambila koona kokha n’kumene kumakhala ndi Akristu eni-eni amene makhalidwe ao ndi njila zao zimawadziŵikitsa bwino.​—Ŵelengani Mateyu 7:13-23.

3. Kodi olambila oona mungawadziŵe bwanji?

Onani zinthu zisanu zimene tingawadziŵile:

  • Olambila oona amalemekeza Baibo kuti ndi Mau a Mulungu. Amayesa-yesa kutsatila mfundo zake. Conco, cipembedzo coona cimasiyana ndi cipembedzo cimene cimatsatila maganizo a anthu. (Mateyu 15:7-9) Olambila oona amacita zinthu mogwilizana ndi zimene amalalikila.​—Ŵelengani Yohane 17:17; 2 Timoteyo 3:16, 17.

  • Mkritsu akamba nkhani ya Baibo. Pambuyo pake apita kukalalikila za Ufumu wa Mulungu, athandizila kumene kwagwa tsoka, athandizila okalamba.

    Otsatila oona a Yesu amalemekeza dzina la Mulungu lakuti Yehova. Yesu analemekeza dzina la Mulungu mwa kulidziŵikitsa. Iye anathandiza anthu kudziŵa Mulungu, ndipo anawaphunzitsa kupemphela kuti dzina la Mulungu liyeletsedwe. (Mateyu 6:9) Kodi ndani amene amadziŵikitsa dzina la Mulungu kudela limene mumakhala?​—Ŵelengani Yohane 17:26; Aroma 10:13, 14.

  • Akristu oona amalalikila za Ufumu wa Mulungu. Mulungu anatumiza Yesu kuti abwele kudzalalikila uthenga wabwino wa Ufumu. Ufumu wa Mulungu ndiwo ciyembekezo cokha ca mtundu wa anthu. Yesu anapitiliza kulalikila za Ufumu mpaka pamene anamwalila. (Luka 4:43; 8:1; 23:42, 43) Iye anakamba kuti otsatila ake naonso adzalalikila za Ufumu umenewu. Ngati munthu wina wakufikilani ndi kuyamba kukamba za Ufumu wa Mulungu, kodi mumaganiza kuti munthu ameneyo ali mcipembedzo?​—Ŵelengani Mateyu 24:14.

  • Otsatila a Yesu sali mbali ya dziko loipali. Mungawazindikile cifukwa cakuti satenga mbali pandale ndi pankhondo. (Yohane 17:16; 18:36) Iwo samatengelanso zocita zoipa ndi makhalidwe oipa a dzikoli.​—Ŵelengani Yakobo 4:4.

  • Akristu oona amakondana kwambili. Mwa kugwilitsila nchito Mau a Mulungu, amaphunzila kulemekeza anthu a mitundu yonse. Ngakhale kuti nthawi zambili zipembedzo zonama zacilikiza kwambili nkhondo za maiko, olambila oona amakana kucita zimenezo. (Mika 4:1-3) M’malo mwake, Akristu oona mopanda dyela amagwilitsila nchito nthawi ndi cuma cao kuthandiza anthu ena ndi kuwalimbikitsa.​—Ŵelengani Yohane 13:34, 35; 1 Yohane 4:20.

4. Kodi tsopano mungacizindikile cipembedzo coona?

Kodi ni cipembedzo citi cimene ziphunzitso zake zonse zimacokela m’Mau a Mulungu, cimene cimalemekeza dzina la Mulungu, ndipo cimalengeza Ufumu wa Mulungu monga ciyembekezo cokha ca mtundu wa anthu? Kodi ndi gulu liti limene limaonetsana cikondi ndipo limadana ndi nkhondo? Kodi mungayankhe bwanji?​—Ŵelengani 1 Yohane 3:10-12.

Kuti mudziŵe zambili, onani nkhani 15 m’buku lakuti Zimene Baibo Imaphunzitsa m’Ceni-ceni.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani