March
Sondo, March 1
Inu mumalamulila ciliconse.—1 Mbiri 29:12.
Pamene tiŵelenga macaputa aŵili oyambilila a Genesis, timaona kuti Adamu na Hava anali na ufulu weni-weni umene anthu masiku ano amaulakalaka. Panalibe cowayofya, sanali kusoŵa ciliconse, ndiponso panalibe amene anali kuwapondeleza. Komanso sanali kudela nkhawa za cakudya, matenda, na imfa. Analinso na nchito yabwino. (Gen. 1:27-29; 2:8, 9, 15) Pamene tikambilana za ufulu, ni bwino kukumbukila kuti Yehova Mulungu yekha ndiye ali na ufulu wocita ciliconse—ufulu wopanda malile. Cifukwa ciani? Cifukwa iye ni Mlengi wa zinthu zonse komanso ni Mfumu Yamphamvuzonse m’cilengedwe conse. (1 Tim. 1:17; Chiv. 4:11) Conco, ufulu umene anthu na angelo ali nawo uli na malile. Iwo amafunika kuzindikila kuti Yehova Mulungu ali na mphamvu yoika malamulo alionse amene waona kuti ni acilungamo, oyenelela, ndi osapondeleza. Izi n’zimene iye anacita kwa anthu oyambilila atangowalenga. w18.04 4 ¶4, 6
Mande, March 2
Mapazi a munthu yemwe akuyenda . . . pobweletsa uthenga wabwino, ndi okongola kwabasi!—Yes. 52:7.
M’dongosolo lino la zinthu, timakwanitsa kupilila cifukwa ca thandizo la Yehova. (2 Akor. 4:7, 8) Ganizilani za anthu amene sali paubwenzi wolimba na Yehova. Ziyenela kuti zimakhala zovuta kwambili kwa iwo kupilila mavuto popanda thandizo la Yehova. Mofanana na Yesu, timawamvelela cifundo anthu amenewo, ndipo timafunitsitsa kuwauzako “uthenga wabwino wa zinthu zabwino.” Conco, muzileza mtima na anthu amene mumaphunzila nawo. Kumbukilani kuti iwo akhoza kukhala kuti sanaganizilepo mfundo zina za coonadi ca m’Baibo zimene ife timadziŵa bwino. Ndipo ambili mwa iwo ali na zikhulupililo zozika mizu kwambili. Iwo angaone kuti zikhulupililo za cipembedzo cawo zimawagwilizanitsa na mabanja awo, cikhalidwe cawo, ndi anthu a m’dela lawo. Sitiyenela kungouza anthu kuti aleke zikhulupililo zawo “zakale” zimene amazikonda kwambili. Koma coyamba, tifunika kuwathandiza kumvetsetsa komanso kukonda mfundo za coonadi ca m’Baibo, zimene poyamba kuphunzila sanali kuzidziŵa. Akayamba kukonda mfundo za coonadi, m’pamene angakhale okonzeka kuleka zikhulupililo zawo zakale. Zingatenge nthawi yaitali kuti tithandize munthu kupanga masinthidwe amenewa.—Aroma 12:2. w19.03 22 ¶10; 23 ¶12, 13
Ciŵili, March 3
Ndimakondwela nawe. —Maliko 1:11.
Mawu amenewa a Yehova aonetsa kuti iye amakonda Mwana wake na kukondwela naye, amatikumbutsa kuti tifunika kusakila mipata yolimbikitsila ena. (Yoh. 5:20) Timalimbikitsidwa ngati munthu amene timakonda waonetsa kuti nayenso amatikonda, komanso watiyamikila pa zabwino zimene timacita. Conco, nafenso tifunika kumalimbikitsa abale na alongo athu na kuwaonetsa cikondi. Tifunika kucita cimodzi-modzi kwa anthu a m’banja lathu. Tikayamikila ena, timalimbitsa cikhulupililo cawo na kuwasonkhezela kupitiliza kutumikila Yehova mokhulupilika. Maka-maka makolo, ayenela kuyesetsa kulimbikitsa ana awo. Ana amapita patsogolo mwauzimu ngati makolo awo amawayamikila mocokela pansi pa mtima na kuwaonetsa cikondi. Mawu akuti “Ndimakondwela nawe,” aonetsa kuti Yehova anali na cidalilo cakuti Yesu adzacita cifunilo ca Atate wake mokhulupilika. Yehova amam’dalila kwambili mwana wake. Conco, nafenso sitiyenela kukayikila olo pang’ono kuti Yesu adzakwanilitsa zonse zimene Yehova anatilonjeza. (2 Akor. 1:20) Ngati tiganizila citsanzo ca Yesu, timakhala ofunitsitsa kuphunzila kwa iye na kutsatila citsanzo cake.—1 Pet. 2:21. w19.03 8 ¶3; 9 ¶5-6
Citatu, March 4
Cilamulo ca mzimu umene umapatsa moyo mwa Khristu Yesu cakumasulani ku cilamulo ca ucimo ndi ca imfa.—Aroma 8:2.
Kuganizila phindu la mphatso yamtengo wapatali imene munthu watipatsa kumatisonkhezela kumuyamikila wopelekayo. Aisiraeli sanayamikile ufulu umene Yehova anawapatsa mwa kuwatulutsa mu ukapolo ku Iguputo. Miyezi yoŵelengeka pambuyo potulutsidwa mu ukapolo, iwo anayamba kulakalaka zakudya na zakumwa za ku Iguputo. Anayambanso kudandaula za cakudya cimene Yehova anali kuwapatsa, mpaka anafuna kubwelela ku Iguputo. Ganizani cabe, iwo anaona mankhaka, mavwembe, adyo, na anyezi kukhala zofunika ngako kuposa ufulu umene anapeza wolambila Mulungu woona, Yehova. N’zosadabwitsa kuti Yehova anawakwiyila kwambili. (Num. 11:5, 6, 10; 14:3, 4) Pamenepa pali phunzilo lalikulu kwa ise. Mtumwi Paulo anatilangiza ise Akhristu kuti tiyenela kupewa mzimu wosayamikila ufulu umene Yehova anatipatsa mokoma mtima kupitila mwa Mwana wake, Yesu Khristu.—2 Akor. 6:1. w18.04 9 ¶6-7
Cinayi, March 5
Iye amakonda cilungamo ndi ciweluzo cosakondela. Dziko lapansi ladzaza ndi kukoma mtima kosatha kwa Yehova.—Sal. 33:5.
Tonse timafuna kuti anthu ena azitikonda. Timafunanso kuti azicita nafe zinthu mwacilungamo. Ngati nthawi zambili timacitilidwa zinthu mopanda cikondi, kapena mopanda cilungamo, tingadzimve kukhala opanda pake, komanso tingataye mtima. Yehova amadziŵa kuti timafuna kucitilidwa zinthu mwacikondi komanso mwacilungamo. (Sal. 33:5) Sitiyenela kukayikila kuti iye amatikonda kwambili, ndipo amafuna kuti tizicitilidwa zinthu mwacilungamo. Izi zimaonekela bwino, tikaganizila kwambili za Cilamulo cimene Yehova anapatsa mtundu wa Aisiraeli, kupitila mwa Mose. Pamene tiphunzila za Cilamulo ca Mose, timaona kuti Mulungu wathu Yehova ni wacikondi kwambili. (Aroma 13:8-10) Tingaone kuti Cilamulo ca Mose cinazikidwa pa cikondi cifukwa zilizonse zimene Yehova amacita, amazicita cifukwa ca cikondi. (1 Yoh. 4:8) Malamulo onse a m’cilamulo amene Yehova anapeleka, anazikidwa pa malamulo aŵili akulu-akulu—lakuti uzikonda Mulungu, ndi lakuti uzikonda mnzako. (Lev. 19:18; Deut. 6:5; Mat. 22:36-40) Lililonse mwa malamulo oposa 600 a m’Cilamulo ca Mose, limatiphunzitsa mbali inayake ya cikondi ca Yehova. w19.02 20-21 ¶1-4
Cisanu, March 6
Kumene kuli cuma cako, mtima wako umakhalanso komweko.—Mat. 6:21.
Yobu anali kusamala na mmene anali kucitila zinthu ndi akazi. (Yobu 31:1) Anali kudziŵa kuti n’kulakwa kuyang’ana mkazi amene si wake momukhumbila. M’dzikoli, muli zinthu zambili zosonkhezela cilakolako coipa ca kugonana. Conco, funso n’lakuti, kodi tidzatengela citsanzo ca Yobu mwa kupewa kuyang’anitsitsa aliyense amene si mwamuna wathu kapena mkazi wathu? Kodi tidzapewanso kuona zithunzi zamalisece kulikonse kumene zimapezeka? (Mat. 5:28) Ngati tsiku lililonse tiyesetsa kukhala odziletsa, tidzalimbikitsidwa kukhalabe na mtima wamphumphu. Yobu anali kumvelanso Yehova pa nkhani ya mmene anali kuonela zinthu zakuthupi. Iye anaona kuti kudalila cuma, kungakhale kulakwa kofunika cilango. (Yobu 31:24, 25, 28) Masiku ano, anthu ambili ni okonda cuma. Ngati tiyesetsa kuona ndalama na katundu moyenela, monga mmene Baibo imatilangizila, tidzakhalabe na mtima wamphumphu.—Miy. 30:8, 9; Mat. 6:19,20. w19.02 6 ¶13-14
Ciŵelu, March 7
Monga Atate wakondela ine, inenso kukonda inu.—Yoh. 15:9.
M’zocita zake zonse, Yesu anaonetsa bwino cikondi cacikulu cimene Yehova ali naco pa ife. (1 Yoh. 4:8-10) Koposa zonse, Yesu anapeleka moyo wake na mtima wonse monga nsembe yotiwombola ku ucimo na imfa. Kaya ndife odzozedwa kapena a “nkhosa zina,” timapindula na cikondi cimene Yehova na Mwana wake anationetsa, mwa kupeleka nsembe imeneyi. (Yoh. 10:16; 1 Yoh. 2:2) Komanso, ganizilani ziphiphilitso za pa Cikumbutso. Ziphiphilitso zimenezi zimaonetsa kuti Yesu ni wacikondi, komanso kuti anali kuganizila ophunzila ake. Motani? Yesu anaonetsa cikondi cake kwa otsatila ake odzozedwa, mwa kuyambitsa mwambo wa Mgonelo wosalila zambili, ndi wosacolowana. Otsatila akewo anafunika kupitiliza kucita mwambo wa Cikumbutso caka ciliconse. Ndipo anafunika kucita izi m’mikhalidwe yosiyana-siyana, ngakhale pamene ali m’ndende. (Chiv. 2:10) Kodi iwo anakwanitsa kumvela lamulo la Yesu limeneli? Inde, anatelo. Kuyambila m’nthawi ya atumwi, Akhristu oona akhala akuyesetsa kucita Cikumbutso ca Imfa ya Yesu. w19.01 24 ¶13-15
Sondo, March 8
Mudzadziŵa coonadi, ndipo coonadi cidzakumasulani.—Yoh. 8:32.
Ufulu umenewu umaphatikizapo kumasuka ku cipembedzo conama, umbuli, na zamizimu. Koma umaphatikizaponso zambili. Kutsogoloku tidzakhala na “ufulu waulemelelo wa ana a Mulungu.” (Aroma 8:21) Ulaŵeni ufulu umenewu lomba mwa ‘kusunga mawu a Khristu,’ kapena kuti ziphunzitso zake. (Yohane 8:31) Mukatelo, “mudzadziŵa coonadi” mwa kuciseŵenzetsa mu umoyo wanu, osati cabe kuciphunzila. M’dziko la Satanali, ngakhale umoyo umene anthu amaona kuti ni wabwino, umakhala waufupi komanso wosapanganika. Sitingadziŵe kuti umoyo wathu udzakhala bwanji maŵa. (Yak. 4:13, 14) Conco, canzelu ni kuyendabe pa njila yopita ku “moyo weniweniwo,” kapena kuti moyo wosatha. (1 Tim. 6:19) Koma Mulungu sacita kutikakamiza kuyenda pa njila imeneyi. Cosankha n’cathu. Cotelo, pangani Yehova kukhala “gawo” lanu, kapena kuti bwenzi lanu. (Sal. 16:5) Muziyamikila “zinthu zabwino” zambili zimene iye wakupatsani. (Sal. 103:5) Ndipo khalani na cikhulupililo cakuti iye adzakuthandizani ‘kukondwela mokwanila’ komanso kukhala na “cimwemwe mpaka muyaya.”—Sal. 16:11. w18.12 28 ¶19, 21
Mande, March 9
Mwamunanso asasiye mkazi wake.—1 Akor. 7:11.
Akhristu tonse tiyenela kulemekeza cikwati, monga mmene Yesu na Yehova amacitila. Komabe, cifukwa ca kupanda ungwilo, ena amalephela kucita zimenezi. (Aroma 7:18-23) Conco, n’zosadabwitsa kuti Akhristu ena m’nthawi ya atumwi, anali na mavuto aakulu m’vikwati vawo. Paulo analemba kuti “mkazi asasiye mwamuna wake.” Ngakhale n’telo, Akhristu ena anali kupatukana ndithu. (1 Akor. 7:10) Palembali, Paulo sanachule mavuto amene anacititsa anthu ena okwatilana kupatukana. Koma mwacionekele vuto silinali lakuti mwamuna anacita ciwelewele, cifukwa mkazi akanakhala na ufulu wom’sudzula n’kukakwatiwa na wina. Paulo analemba kuti mkazi amene wasiya mwamuna wake, ayenela kukhala “conco wosakwatiwa. Apo ayi, abwelelane ndi mwamuna wakeyo.” Conco, Mulungu amaonabe aŵiliwo monga thupi limodzi. Paulo anapeleka malangizo akuti mosasamala kanthu za mavuto amene okwatilana ali nawo, ngati vuto si cigololo, ayenela kukambilana kuti apitilize kukhala limodzi. Iwo angapemphe malangizo a m’Baibo kwa akulu mu mpingo. w18.12 13 ¶14-15
Ciŵili, March 10
Pitilizani kufunafuna ufumu coyamba ndi cilungamo cake.—Mat. 6:33.
Masiku anonso, Mulungu amafuna kuti anthu ake akhale naye pa ubwenzi wolimba, na kuti azigwila nchito yake modzipeleka. (Mat. 28:19, 20; Yak. 4:8) Anthu ena ooneka monga akutifunila zabwino angayese kutilepheletsa kuika cifunilo ca Mulungu patsogolo. Mwacitsanzo, bwanji ngati abwana anu alonjeza kuti adzakukwezani pa nchito na kuwonjezela malipilo anu, koma muona kuti izi zingasokoneze pulogilamu yanu yocita zinthu zauzimu? Kapena bwanji ngati ndimwe mwana wa sukulu, ndipo mwapatsiwa mwayi wokacita maphunzilo owonjezela ku sukulu inayake ya kutali na kwanu? Kodi iyi ndiyo nthawi yopemphela na kufufuza malangizo othandiza pa nkhanizi, kufunsa anthu ena, kenako n’kupanga cosankha? Zingakhale bwino kuphunzililatu pali pano mmene Yehova amaonela nkhani zimenezi na kuyamba kuziona monga mmene iye amazionela. Mukatelo, ndiye kuti ngati mutapatsiwa mwayi wa nchito kapena wa maphunzilo ngati umenewo, simudzavutika kupanga cosankha. Mumakhala kuti mwadziikila kale zolinga zauzimu, mwakonzekeletsa mtima wanu, ndipo cangotsala n’kucita zinthu mogwilizana ndi cosankha canu. w18.11 27 ¶18
Citatu, March 11
Uteteze mtima wako kuposa zonse zimene ziyenela kutetezedwa.—Miy. 4:23.
Solomo anakhala mfumu ya Isiraeli ali wacinyamata. Atangoyamba kumene kulamulila, Yehova anaonekela kwa iye m’maloto na kumuuza kuti: “Pempha cimene ukufuna kuti ndikupatse.” Solomo anayankha kuti: “Ndine mwana ndipo sindikudziŵa zinthu zambili. . . . Mupatse mtumiki wanune mtima womvela kuti ndiweluze anthu anu.” (1 Maf. 3:5-10) Solomo anapempha kuti apatsidwe “mtima womvela.” Uku kunali kudzicepetsa kwambili. Ndiye cifukwa cake Yehova anamukonda maningi. (2 Sam. 12:24) Mulungu anakondwela kwambili na pempho la Solomo, cakuti anam’patsa “mtima wanzelu ndi womvetsa zinthu.” (1 Maf. 3:12) Pa nthawi yonse imene Solomo anali wokhulupilika, anadalitsidwa m’njila zambili. Mwacitsanzo, anapatsiwa mwayi womanga kacisi, amene anabweletsa ulemelelo ku “dzina la Yehova Mulungu wa Isiraeli.” (1 Maf. 8:20) Komanso anapatsiwa nzelu na Mulungu, moti anakhala wochuka kwambili. Ndipo mawu amene iye anakamba mouzilidwa na Mulungu, analembewa m’mabuku atatu a m’Baibo. Limodzi mwa mabuku amenewo ni buku la Miyambo. w19.01 14 ¶1-2
Cinayi, March 12
Musamatengele nzelu za nthawi ino.—Aroma. 12:2.
Anthu ena amakamba kuti safuna kutengela maganizo a munthu wina aliyense. Iwo angakambe kuti, “Na ine nili na nzelu.” Pokamba mawu amenewa, mwina iwo amatanthauza kuti amafuna kusankha okha zocita, ndiponso kuti ali na ufulu wocita zimenezo. Iwo safuna kuti ena azingowauza zocita, kapena kuwaumiliza kutengela zocita za anthu ena. Koma n’zolimbikitsa kudziŵa kuti tikayamba kuyendela maganizo a Yehova, timakhalabe na ufulu wosankha. Monga mmene 2 Akorinto 3:17 imakambila, “pamene pali mzimu wa Yehova, pali ufulu.” Timakhala na ufulu wosankha kuti tidzakhala munthu wotani. Timakhalanso na ufulu wosankha zocita malinga n’zokonda zathu. Umu ni mmene Yehova anatilengela. Komabe, ufulu umenewu uli na malile. (1 Pet. 2:16) Pa nkhani ya cabwino na coipa, Yehova amafuna kuti tiziyendela maganizo ake olembedwa m’Baibo. w18.11 19 ¶5-6
Cisanu, March 13
Dema wandisiya cifukwa cokonda zinthu za m’nthawi ino. —2 Tim. 4:10.
Pamene tinaphunzila coonadi, tinayamba kuona zinthu zauzimu kukhala zofunika kwambili kuposa zinthu zakuthupi. Ndipo tinalolela kudzimana zinthu zina zakuthupi kuti tiyambe kuyenda m’coonadi. Komabe, m’kupita kwa nthawi, tingayambe kuona anzathu akugula zipangizo zamakono zodula, kapena kusangalala na zinthu zina zakuthupi. Tingayambe kuganiza kuti tikumanidwa zabwino. Posakhutila na zinthu zofunika kwambili zimene tili nazo, tingayambe kunyalanyaza zinthu zauzimu pofuna kudziunjikila cuma. Izi zitikumbutsa nkhani ya Dema. Iye analeka kutumikila pamodzi na mtumwi Paulo cifukwa cokonda “zinthu za m’nthawi ino.” Mwina Dema anakonda kwambili zinthu zakuthupi kuposa kutumikila Mulungu. N’kuthekanso kuti sanafunenso kupitiliza na umoyo wodzimana kuti azitumikila pamodzi na Paulo. Izi zitiphunzitsa kuti ngati kale tinali na mtima wokonda cuma, tiyenela kukhala wosamala kuti tisakhalenso na mtima umenewu, cifukwa ungatilepheletse kukonda coonadi. w18.11 10 ¶9
Ciŵelu, March 14
Kufa simudzafa ayi.—Gen. 3:4.
Satana anakamba bodza limeneli cifukwa ca mtima wake waciwembu. Iye anali kudziŵa bwino kuti Hava akakhulupilila bodza lake n’kudya cipatsoco, adzafa. Adamu na Hava anakhulupililadi bodzalo, ndipo anaphwanya lamulo la Yehova. Zotulukapo zake, m’kupita kwa nthawi, iwo anafa. (Gen. 3:6; 5:5) Coipa kwambili kuposa pamenepo, kudzela mwa ucimo umenewo, ‘imfa inafalikila kwa anthu onse.’ Ndipo “imfa inalamulila monga mfumu . . . , ngakhalenso kwa anthu amene sanacimwe monga mmene anacimwila Adamu.” (Aroma 5:12, 14) Conco, m’malo mosangalala na moyo wangwilo komanso wosatha, monga mmene Mulungu anafunila pa ciyambi, anthu amangokhala na moyo “zaka 70. Ndipo ngati tili ndi mphamvu yapadela. . . zaka 80.” Olo zili conco, umoyo ni ‘wodzala ndi mavuto ndi zopweteka.’ (Sal. 90:10) N’zomvetsa cisoni kwambili! Koma zonsezi zinacitika cifukwa ca bodza la Satana. Pofotokoza zocita za Mdyelekezi, Yesu anati: “Sanakhazikike m’coonadi, cifukwa mwa iye mulibe coonadi.” (Yoh. 8:44) Mpaka pano, kwa Satana kulibe coonadi, cifukwa iye akupitiliza ‘kusoceletsa dziko lonse lapansi kumene kuli anthu’ poseŵenzetsa mabodza ake. (Chiv. 12:9) Ise sitifuna kusoceletsedwa na Mdyelekezi. w18.10 6-7 ¶1-4
Sondo, March 15
Odala ndi anthu amene amabweletsa mtendele, cifukwa adzachedwa ‘ana a Mulungu.—Mat. 5:9.
Anthu amene amayesetsa kukhazikitsa mtendele, amakhala acimwemwe. Yakobo analemba kuti: “Cilungamo ndico cipatso ca mbewu zimene anthu odzetsa mtendele amafesa mu mtendele.” (Yak. 3:18) Ngati tasemphana maganizo na winawake mu mpingo kapena m’banja, tingapemphe Mulungu kuti atithandize kukhazikitsa mtendele. Tikatelo, Yehova adzatipatsa mzimu wake woyela, umene udzatithandiza kuonetsa khalidwe labwino. Ndipo zotulukapo zake, tidzakhala acimwemwe. Yesu anagogomeza kufunika kocitapo kanthu kuti tikhazikitse mtendele ngati tasemphana maganizo na munthu wina. Iye anati: “Conco ngati wabweletsa mphatso yako paguwa lansembe, ndipo uli pomwepo wakumbukila kuti m’bale wako ali nawe cifukwa, siya mphatso yako patsogolo pa guwa lansembe pomwepo. Pita ukayanjane ndi m’bale wako coyamba, ndipo ukabwelako, peleka mphatso yako.”—Mat. 5:23, 24. w18.09 21 ¶17
Mande, March 16
Ndikukupatsani lamulo latsopano, kuti muzikondana. Mmene ine ndakukondelani, inunso muzikondana.—Yoh. 13:34.
Pamene Yesu anali na ophunzila ake, pa usiku wakuti adzaphedwa maŵa, anakamba za khalidwe la cikondi pafupi-fupi ka 30. Iye analamula ophunzila ake kuti ‘azikondana.’ (Yoh. 15:12, 17) Iwo anafunika kukhala na cikondi cacikulu pakati pawo kuti cidzakhale cizindikilo cakuti ni otsatila ake oona. (Yoh. 13:35) Pamenepa, Yesu sanali kukamba za cikondi ca mumtima cabe. Koma anali kukamba za cikondi codzimana, cimene cimaonekela na nchito zake. Iye anati: “Palibe amene ali ndi cikondi cacikulu kuposa ca munthu amene wapeleka moyo wake cifukwa ca mabwenzi ake. Mupitiliza kukhala mabwenzi anga mukamacita zimene ndikukulamulani.” (Yoh. 15:13, 14) Cikondi codzimana cimene atumiki a Yehova ali naco pakati pawo, komanso mgwilizano wawo wolimba, ni umboni wakuti iwo ni anthu a Mulungu. (1 Yoh. 3:10, 11) N’zokondweletsa ngako kuona kuti pakati pa atumiki a Yehova masiku ano pali cikondi cacikulu, mosasamala kanthu kuti ni osiyana mitundu, maiko, zikhalidwe, na zitundu. w18.09 12 ¶1-2
Ciŵili, March 17
Ngati munthu sasamalila anthu amene ndi udindo wake kuwasamalila, makamaka a m’banja lake, wakana cikhulupililo ndipo ndi woipa kuposa munthu wosakhulupilila.—1 Tim. 5:8.
Yehova amafuna kuti atumiki ake azisamalila mabanja awo. Mwacitsanzo, mungafunike kumaseŵenza kuti muzipeza ndalama zogwilitsila nchito posamalila banja lanu. Azimayi ambili amakhala pa nyumba kuti azisamalila ana awo. Ndipo ana ena aakulu amafunika kusamalila makolo awo odwala. Onsewa ni maudindo ofunika kwambili. (1 Akor. 10:31) Ngati muli na udindo wosamalila banja, ndiye kuti mwacidziŵikile simukhala na nthawi yoculuka yocita zinthu zauzimu ngati mmene mufunila. Koma musataye mtima! Yehova amakondwela mukamayesetsa kusamalila banja lanu. Ngati mulibe udindo waukulu wosamalila banja, kodi mungathandizeko Akhristu amene amasamalila makolo kapena acibululu odwala kapena okalamba? Kapena kodi mungathandizeko Akhrsitu ena amene ni odwala, okalamba, kapenanso amene ali na zosoŵa zina? Bwanji osafufuza mu mpingo mwanu kuti muone abale na alongo amene afunika thandizo? Mwa kucita izi, mungakhale mukuseŵenza pamodzi na Yehova poyankha pemphelo la Mkhristu winawake.—1 Akor 10:24. w18.08 24 ¶3, 5.
Citatu, March 18
Mulungu anali naye, ndipo anamulanditsa m’masautso ake onse.—Mac. 7:9, 10.
Yosefe anali na zaka pafupi-fupi 17 pamene abululu ake anam’gulitsa ku ukapolo cifukwa ca nsanje. Anam’citila nsanje cifukwa atate awo anali kum’konda kwambili. (Gen. 37:2-4, 23-28) Kwa zaka pafupi-fupi 13, Yosefe anavutika monga kapolo ku Iguputo, komanso anaikidwa m’ndende. Iye anali kutali na kumene kunali Yakobo, atate wake wokondedwa. N’ciani cinam’thandiza kuti asataye mtima kapena kukhumudwa na mavutowa? Pamene anali kuvutika m’ndende, Yosefe ayenela kuti anali kusumika maganizo ake pa umboni woonetsa kuti Yehova anali kum’dalitsa. (Gen. 39:21; Sal. 105:17-19) Mwacionekele, maloto aulosi amene iye analota pamene anali wacicepele, nawonso anamuthandiza kukhulupilila kuti Yehova anali kum’konda. (Gen. 37:5-11) N’zoonekelatu kuti Yosefe anali kukhutulila Yehova nkhawa zake m’pemphelo. (Sal. 145:18) Poyankha mapemphelo ake, Yehova anam’thandiza kukhulupilila na mtima wonse kuti iye adzakhala naye m’mayeselo ake onse. w18.10 28 ¶3-4
Cinayi, March 19
Munthu wosauka amadedwa ngakhale ndi mnzake, koma munthu wolemela amakhala ndi anzake ambili.—Miy. 14:20.
Nthawi zina timaona anthu molakwika cifukwa cakuti ni osauka kapena ni olemela. Kodi cuma kapena umphawi zingakhudze bwanji mmene timaonela munthu? Mouzilidwa na mzimu woyela, Solomo anafotokoza vuto limene ise anthu opanda ungwilo tili nalo, monga mmene lemba la lelo lionetsela. Kodi tiphunzilapo ciani pa lembali? Ngati sitisamala, tingayambe kukonda abale olemela na kumanyalanyaza abale osauka. Tingayambe kuona Akhristu ena kukhala ofunika kwambili kuposa ena cifukwa cakuti ni acuma. N’cifukwa ciani kucita izi n’koopsa? Cifukwa ngati timakonda Akhristu ena cifukwa cakuti ni acuma kapena osauka, tingayambitse magaŵano mu mpingo. Mtumwi Yakobo anakamba kuti vuto laconco linayambitsa magaŵano m’mipingo ina ya m’nthawi ya atumwi. (Yak. 2:1-4) Pa cifukwa ici, tifunika kusamala kuti maganizo aconco asasokoneze mpingo wathu masiku ano. w18.08 10 ¶8-10
Cisanu, March 20
Khalani okondana kwambili.—1 Pet. 4:8.
Njila ina imene timaonetsela kuti timayamikila Yehova potipatsa mwayi wokhala naye pa ubwenzi wapadela, ni mmene timacitila zinthu na Akhristu anzathu. Nawonso ni anthu a Yehova. Ngati sitiiŵala mfundo imeneyi, ndiye kuti nthawi zonse tidzayamba kucita zinthu mokoma mtima ndi mwacikondi na abale na alongo athu. (1 Ates. 5:15) Yesu anauza otsatila ake kuti: “Mwakutelo, onse adzadziŵa kuti ndinu ophunzila anga, ngati mukukondana.” (Yoh. 13:35) N’zocititsa cidwi kuti Malaki anakamba kuti Yehova ‘amachela khutu ndi kumvetsela’ pamene anthu ake akukambilana wina na mnzake. (Mal. 3:16) Zoonadi, “Yehova amadziŵa anthu ake.” (2 Tim. 2:19) Iye amaona ciliconse cimene timacita na kukamba. (Aheb. 4:13) Ngati tacita zinthu mosakomela mtima Akhristu anzathu, Yehova ‘amachela khutu ndi kumvetsela.’ Ndipo ngati timacelezana, kupatsana zinthu mowoloŵa manja, kukhululukilana, ndi kukomelana mtima, Yehova amaonanso zimenezo.—Aheb. 13:16; w18.07 26 ¶15, 17
Ciŵelu, March 21
Yehova [muzim’mamatila]. —Deut. 10:20.
Kumamatila kwa Yehova n’cinthu canzelu. Palibe wina wamphamvu, wanzelu kapena wacikondi kuposa Mulungu wathu. N’ndani wa ise amene sangakonde kukhala ku mbali yake? (Sal. 96:4-6) Komabe, olambila ena a Mulungu alephela kukhala okhulupilika kwa iye ndipo acoka kumbali yake. Ganizilani za Kaini. Iye anali kulambila Yehova, osati mulungu wina aliyense. Komabe, Mulungu sanakondwele na kulambila kwake, cifukwa maganizo oipa anayamba kuzika mizu mu mtima mwake. (1 Yoh. 3:12) Yehova anayesa kum’thandiza Kaini mwa kumuuza kuti: “Ukasintha n’kucita cabwino, sindikuyanja kodi? Koma ngati susintha kuti ucite cabwino, ucimo wamyata pakhomo kukudikilila, ndipo ukulakalaka kukudya. Kodi iweyo suugonjetsa?” (Gen. 4:6, 7) Mwanjila ina, tingakambe kuti Yehova anali kuuza Kaini kuti: “Ukalapa na kukhalabe ku mbali yanga, na ine nidzakhala ku mbali yako.” Koma iye sanamvele uphungu wa Mulungu. w18.07 17¶1, 3; 18 ¶4
Sondo, March 22
Onetsani kuwala kwanu pamaso pa anthu.—Mat. 5:16.
Njila imodzi imene timaonetsela kuunika kwathu, ndi mwa kulalikila uthenga wabwino na kupanga ophunzila. (Mat. 28:19, 20) Kuwonjezela apo, timapeleka ulemelelo kwa Yehova mwa khalidwe lathu labwino. Anthu amene timawalalikila komanso amene timakumana nawo, amaona khalidwe lathu. Ngati timwetulila na kuwapatsa moni mwaubwenzi, angacite cidwi na khalidwe lathu komanso ndi Mulungu amene timalambila. Yesu anauza ophunzila ake kuti: “Pamene mukuloŵa m’nyumba, pelekani moni kwa a m’banja limenelo.” (Mat. 10:12) M’dela limene Yesu na ophunzila ake anali kulalikilamo kaŵili-kaŵili, anthu anali na cizoloŵezi coitanila alendo m’nyumba zawo. Masiku ano, cizoloŵezi cimeneci m’madela ambili mulibe. Komabe, kukhala aubwenzi pamene mukufotokoza cifukwa cimene mwafikila pa khomo la munthu, nthawi zambili kumathandiza kucepetsa nkhawa kapena ukali umene mwininyumba angakhale nawo. Kaŵili-kaŵili, kumwetulila mwaubwenzi kumakhala ciyambi cabwino ca makambilano. Kucita izi kumakhalanso kothandiza kwa abale na alongo amene amacita ulaliki wa pa kasitandi. Nthawi zambili anthu amakhala omasuka kudzatenga mabuku athu ngati mumwetulila na kuwapatsa moni mwaubwenzi. w18.06 22 ¶4-5
Mande, March 23
Mulungu alibe tsankho. —Mac. 10:34.
Mtumwi Petulo anali na cizoloŵezi cogwilizana ndi Ayuda okha-okha. Koma Mulungu atamveketsa mfundo yakuti Akhristu sayenela kukhala a tsankho, Petulo analalikila Koneliyo, msilikali waciroma. (Mac. 10:28, 35) Pambuyo pake, Petulo anayamba kugwilizana ndi Akhristu a mitundu ina komanso kudya nawo. Patapita zaka, nthawi ina Petulo analeka kudya cakudya na Akhristu a ku Antiokeya amene sanali Ayuda. (Agal. 2:11-14) Pa nthawiyo, Paulo anam’patsa uphungu Petulo, ndipo mwacionekele iye anaulandila. Conco, m’kalata yake yoyamba yopita kwa Akhristu aciyuda ndi a mitundu ina amene anali kukhala ku Asia Minor, Petulo anafotokoza za kufunika kokonda gulu lonse la abale. (1 Pet. 1:1; 2:17) Mwacidziŵikile, atumwi anaphunzilapo kanthu pa citsanzo ca Yesu ca kukonda “anthu a mtundu uliwonse.” (Yoh. 12:32; 1 Tim. 4:10) Iwo anasintha kaganizidwe kawo, olo kuti kucita zimenezi kunawatengela nthawi. Cifukwa cakuti anali atavala “umunthu watsopano,” Akhristu a m’nthawi ya atumwi anayamba kuona anthu onse kukhala ofanana pamaso pa Mulungu.—Akol. 3:10, 11. w18.06 11 ¶15-16
Ciŵili, March 24
Khalani olimba. . . mutavalanso codzitetezela pacifuwa cacilungamo.—Aef. 6:14.
Mtundu wina wa codzitetezela pa cifuwa cimene asilikali aciroma anali kuvala m’nthawi ya atumwi, cinali kukhala na tunsimbi topyapyala toikidwa mosanjikiza. Nthawi na nthawi anali kufunikila kumaona ngati tunsimbi twa covalaco tukali togwila bwino kuti ateteze mtima wake na ziwalo zina zofunika kwambili za thupi. Ndithudi! Ici n’cizindikilo coyenelela kwambili coonetsa mmene miyezo yolungama ya Yehova imatetezela mtima wathu wophiphilitsa. (Miy. 4:23) Msilikali sangasinthanitse codzitetezela pacifuwa copangiwa na citsulo colimba n’kutenga cina copangiwa na citsulo cosalimba. Na ise n’cimodzi-modzi. Sitifunika kusinthanitsa miyezo yolungama ya Yehova na miyezo yathu. Sitiyenela kudalila nzelu zathu cifukwa sizingatithandize kukhala otetezeka. (Miy. 3:5, 6) M’malomwake, mofanana ndi msilikali amene anali kuonetsetsa kuti tunsimbi twa codzitetezela pa cifuwa n’togwila bwino, tifunika kuonetsetsa kuti mfundo za Yehova ni zozikika mozama mu mtima mwathu. Kuwonjezela apo, kumvetsetsa bwino mfundo za coonadi ca Mawu a Mulungu, kudzatithandiza kukhala wokonzeka kuteteza molimba mtima coonadi kwa otsutsa.—Sal. 111:7, 8; 1 Yoh. 5:3. w18.05 28 ¶3-4, 6-7
Citatu, March 25
Pamenepo anthuwo anayamba kukangana ndi Mose.—Num. 20:3.
Ngakhale kuti Mose anawatsogolela bwino kwa zaka zambili, anthuwo anapitiliza kudandaula osati cabe za kusoŵa kwa madzi, koma anakwiyilanso Mose, monga kuti iye ndiye anacititsa kuti asoŵe madzi. (Num. 20:1-5, 9-11) Mose anakwiya kwambili, cakuti anacita zinthu mosadekha. M’malo mokamba na thanthwe, monga mmene Yehova anam’lamulila, iye anakamba mokwiya kwa anthu. Komanso, anakamba mawu oonetsa ngati kuti iye ndiye adzatulutsa madzi. Ndiyeno, anamenya thanthwelo kaŵili, ndipo munatuluka madzi ambili. Kunyada na mkwiyo zinam’pangitsa kucita colakwa cacikulu. (Sal. 106:32, 33) Olo kuti Mose analephela kuonetsa khalidwe la kufatsa kwa kanthawi kocepa cabe, Mulungu sanamulole kukaloŵa m’Dziko Lolonjezedwa.(Num. 20:12) Pa nkhani imeneyi, tiphunzilapo mfundo zofunika kwambili. Yoyamba, nthawi zonse tifunika kuyesetsa kukhala ofatsa. Tikalephela kukhala ofatsa, ngakhale kwa nthawi yocepa, mzimu wonyada ukhoza kutiloŵa na kutipangitsa kukamba, kapena kucita zinthu zolakwika. Yaciŵili, tifunika kuyesetsa kucita zinthu mofatsa, ngakhale pamene takwiya kapena kupanikizika maganizo. w19.02 12-13 ¶19-21
Cinayi, March 26
Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu.—Mat. 24:14.
Kodi kugwila nchito yolalikila imene Yesu anatilamula n’kolemetsa? Kutalitali! Pambuyo pofotokoza fanizo la mpesa, Yesu anakamba kuti tikamagwila nchito yolalikila za Ufumu, tidzakhala acimwemwe. (Yoh. 15:11) Ndipo iye anatitsimikizila kuti cimwemwe cake cidzakhala mwa ise. Motani? Yesu anadziyelekezela na mtengo wa mpesa, ndipo ophunzila ake anawayelekezela na nthambi. (Yoh. 15:5) Mtengo wa mpesa umacilikiza nthambi zake. Malinga ngati nthambi n’zolumikizika kumtengo wa mpesawo, zimalandila madzi na cakudya kucokela kumtengowo. Na ise n’cimodzi-modzi. Malinga ngati tikhalabe ogwilizana na Khristu mwa kutsatila mapazi ake mosamala, tidzakhala na cimwemwe monga cimene iye amakhala naco pocita cifunilo ca Atate ake. (Yoh. 4:34; 17:13; 1 Pet. 2:21) Hanne, mpainiya amene watumikila kwa zaka zoposa 40, anati: “Cimwemwe cimene nimakhala naco pambuyo pogwila nchito yolalikila cimanilimbikitsa kupitiliza kum’tumikila Yehova.” Inde, cimwemwe coculuka cimene timapeza, cimatipatsa mphamvu yopitiliza kulalikila ngakhale m’magawo ouma.—Mat. 5:10-12. w18.05 17¶2;20 ¶14
Cisanu, March 27
Ine ndinasankhidwa . . . kuti ndikhale mphunzitsi wophunzitsa anthu a mitundu ina za cikhulupililo ndi coonadi.—1 Tim. 2:7.
M’nthawi ya Akhristu oyambilila, cioneka kuti mtumwi Paulo ndi amene anacita zambili polimbikitsa Akhristu anzake. Iye anatumiziwa na mzimu woyela kuti akalalikile kwa anthu a mitundu ina, okhala m’madela olamulidwa na Aroma na Agiriki. Anthu a m’madela amenewo anali kulambila milungu yambili. (Agal. 2:7-9) Paulo anayenda m’madela ambili komanso akutali, monga ku dziko limene lomba limachedwa Turkey, ku Greece na ku Italy. Kumeneko, anakhazikitsa mipingo yacikhristu pakati pa anthu amene sanali Ayuda. Akhristu acatsopano amenewo anali ‘kuvutitsidwa ndi anthu akwawo,’ ndipo anafunika kulimbikitsiwa. (1 Ates. 2:14) Conco, ca m’ma 50 C.E., Paulo analembela kalata mpingo wacatsopano wa ku Tesalonika. Analemba kuti: “Nthawi zonse timayamika Mulungu tikamachula za inu nonse m’mapemphelo athu. Timatelo pakuti timakumbukila nthawi zonse nchito zanu zacikhulupililo, ndi nchito zanu zacikondi. Timatelonso pokumbukila mmene munapililila.” (1 Ates. 1:2, 3) Iye anawauzanso kuti azilimbikitsana wina na mnzake. Anati: “Pitilizani kutonthozana ndi kulimbikitsana.”—1 Ates. 5:11. w18.04 18-19 ¶16-17
Ciŵelu, March 28
Uthenga wabwino uyenela ulalikidwe coyamba.—Maliko 13:10.
Wacicepele amene amafunitsitsa kukondweletsa Yehova, amaona nchito yolalikila kukhala yofunika ngako. Popeza kuti nchito yolalikila ni yofunika kugwilidwa mwamsanga, tiyenela kuiona kukhala cimodzi mwa zinthu zofunika kwambili mu umoyo wathu. Kodi mungadziikile colinga cakuti muzilalikila kaŵili-kaŵili? Kodi mungaciteko upainiya? Nanga mungacite ciani ngati simupeza cimwemwe cokwanila pa nchito yolalikila? Komanso mungacite ciani kuti muzilalikila mogwila mtima? Pali zinthu ziŵili zofunika zimene mungacite: Muzikonzekela bwino, komanso musaleke kuuzako ena zimene munaphunzila. Mukamacita zimenezi, mudzapeza cimwemwe coculuka pa nchito yolalikila. Pokonzekela, mungayambe mwa kufufuza yankho ya funso imene anzanu amakonda kufunsa ku sukulu. Webusaiti yathu ya jw.org na zofalitsa zina, zili na nkhani zimene zinakonzedwa kuti zithandize acicepele kudziŵa mmene angayankhile mafunso ofunsidwa kaŵili-kaŵili, monga yakuti, “N’cifukwa Ciani Mumakhulupilila Kuti Kuli Mulungu?” Mungakonzekele yankho ya funso imeneyi mwa kuŵelenga nkhani yakuti, “Kodi Niyenela Kukhulupilila za Cisanduliko—Evolution?” m’kabuku kakuti Mayankho pa Mafunso 10 Amene Acicepele Amafunsa. Kabuku kameneka kangakuthandizeni kukonzekela mayankho pa mafunso enanso. w18.04 27 ¶10-11
Sondo, March 29
Mubelekane, muculuke.—Gen. 1:28.
Olo kuti poyamba Adamu na Hava anali na ufulu m’njila zambili, Mulungu anawaikila malile kapena kuti malamulo. Ena mwa malamulowo anali acibadwa, koma anali malamulo ndithu. Mwacitsanzo, makolo athu oyamba anali kudziŵa kuti anafunika kucita zinthu monga kudya, kupuma, na kugona kuti akhalebe na moyo. Kodi iwo anali kuona kuti kucita zimenezi kunali kuwalanda ufulu? Iyai, cifukwa Yehova anawalenga m’njila yakuti azimvela bwino na kukondwela pocita zinthu zimenezi. (Sal. 104:14, 15; Mlal. 3:12, 13) Yehova analamula Adamu na Hava kuti abeleke ana na kudzaza dziko lapansi, komanso kuti azilisamalila. Kodi lamulo limeneli linawaphwanyila ufulu? Kutalitali! Mulungu anapeleka lamuloli kwa anthu pofuna kuwapatsa mwayi wom’thandiza pokwanilitsa colinga cake copanga dziko lapansi kukhala paladaiso, kuti anthu angwilo akhalemo kwamuyaya. (Sal. 127:3; Yes. 45:18) Adamu na Hava akanamvela Mulungu, akanasangalala na umoyo wa banja kwamuyaya. w18.04 4-5 ¶7-8
Mande, March 30
Onse amene anali ndi maganizo abwino amene akanawathandiza kukapeza moyo wosatha anakhala okhulupilila.—Mac. 13:48.
Ngati timaleza mtima ndi anthu amene timawalalikila, sitidzayembekezela kuti akangomvetsela coonadi ca m’Baibo, nthawi yomweyo adzamvetsetsa kapena kulabadila. Mwacitsanzo, ganizilani mmene tingathandizile munthu kumvetsa za ciyembekezo cathu cokakhala na moyo wamuyaya padziko lapansi m’paradaiso. Anthu ambili amakhulupilila kuti imfa ni mapeto a zonse. Ndipo ena amaganiza kuti anthu onse abwino amayenda kumwamba. M’bale wina anafotokoza mmene amathandizila anthu kumvetsetsa za ciyembekezo cimeneci. Coyamba, amaŵelenga Genesis 1:28. Kenako, amafunsa mwininyumba kuti, ‘Kodi Mulungu anafuna kuti anthu azikhala kuti, nanga anafuna kuti akhale na umoyo wotani?’ Ambili amayankha kuti, “Anafuna kuti tizikhala padziko lapansi, na umoyo wacimwemwe.” Ndiyeno, m’baleyo amaŵelenga Yesaya 55:11, na kufunsa ngati colinga ca Mulungu cinasintha. Nthawi zambili, mwininyumba amayankha kuti sicinasinthe. Potsiliza, m’baleyo amaŵelenga Salimo 37:10, 11, na kufunsa mwininyumba mmene umoyo wa anthu udzakhalila kutsogolo. Mwa kuseŵenzetsa njila imeneyi, m’baleyu wathandiza anthu ambili ndithu kudziŵa kuti Mulungu amafuna kuti anthu abwino akakhale na moyo wosatha pa dziko lapansi m’Paradaiso. w19.03 24 ¶14-15; 25 ¶19
Ciŵili, March 31
Muzimumvela.—Mat. 17:5.
Pamene Yehova anakamba mawu amenewa, anaonetselatu kuti amafuna kuti tizimvela mawu a Mwana wake. Yesu mwacikondi anaphunzitsa otsatila ake mmene angalalikilile uthenga wabwino, komanso anawakumbutsa mobweleza-bweleza kuti afunika kukhala maso. (Mat. 24:42; 28:19, 20) Cinanso, anawalangiza kuti afunika ‘kuyesetsa mwamphamvu kuloŵa pakhomo lopapatiza,’ ndiponso anawalimbikitsa kuti sayenela kubwelela m’mbuyo. (Luka 13:24) Kuwonjezela apo, Yesu anauzanso otsatila ake kuti afunika kukondana wina na mnzake, kukhalabe ogwilizana, na kusunga malamulo ake. (Yoh. 15:10, 12, 13) Malangizowa ni ofunikanso kwambili kwa ife monga mmene analili pa nthawi imene Yesu anawapeleka. Yesu anati: “Aliyense amene ali kumbali ya coonadi amamvela mawu anga.” (Yoh. 18:37) Timaonetsa kuti timamvela mawu ake pamene ‘tipitiliza kulolelana ndi kukhululukilana ndi mtima wonse.’ (Akol. 3:13; Luka 17:3, 4) Timaonetsanso kuti timamvela mawu ake, mwa kulalikila uthenga wabwino mokangalika “m’nthawi yabwino ndi m’nthawi yovuta.”—2 Tim. 4:2. w19.03 10 ¶9-10