April
Citatu, April 1
[Yesu anauza] Petulo kuti: “Pita kumbuyo kwanga, Satana! . . . zimene umaganiza si maganizo a Mulungu, koma maganizo a anthu.”—Mat. 16:23.
Nanga bwanji ise? Kodi timayendela maganizo a Mulungu kapena a dziko? N’zacidziŵikile kuti pofika pano, tinasintha makhalidwe athu kuti akhale ogwilizana na malamulo a Mulungu. Koma bwanji za maganizo athu? Kodi timayesetsa kuwawongola kuti agwilizane na maganizo a Yehova? Kucita izi kumafuna kulimbika. Koma kutengela maganizo a dziko n’kosavuta. Zili conco cifukwa mzimu wa dziko uli paliponse. (Aef. 2:2) Komanso, tingathe kukopeka mosavuta na maganizo a dziko cifukwa amalimbikitsa khalidwe la kudzikonda. Conco, n’zosavuta munthu kutengela maganizo a dziko. Koma kutengela maganizo a Yehova, kumafuna kulimbika. Kutengela maganizo a dziko kungacititse kuti tikhale odzikonda komanso osafuna kuuzidwa zocita. (Maliko 7:21, 22) Conco, m’pofunika kuti tiziyesetsa kukhala na “maganizo a Mulungu,” osati “maganizo a anthu.” w18.11 18 ¶1; 19 ¶3-4
Cinayi, April 2
Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, amene ndimakondwela naye.—Mat. 3:17.
Yesu ayenela kuti analimbikitsidwa ngako pamene Yehova anakamba mawu katatu konse kucokela kumwamba oonetsa kuti anali kumudziŵa. Koyamba, Yesu atangobatizika mu mtsinje wa Yorodano, Yehova anakamba mawu amene ali pamwambawa. Mwacidziŵikile, kuwonjezela pa Yesu, Yohane M’batizi yekha ndiye anamvako mawu amenewa. Kaciŵili, patatsala pafupi-fupi caka cimodzi kuti Yesu aphedwe, ophunzila ake atatu anamva Yehova akukamba za Yesu kuti: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, amene ndikukondwela naye, muzimumvela.” (Mat. 17:5) Kothela, patangotsala masiku oŵelengeka kuti Yesu aphedwe, Yehova anakambanso naye kucokela kumwamba. (Yoh. 12:28) Yesu anali kudziŵa kuti anthu adzamunamizila kuti ni munthu wonyoza Mulungu. Anali kudziŵanso kuti adzafa imfa yonyozeka. Olo zinali conco, iye anapemphela kuti cifunilo ca Yehova cicitike osati cake. (Mat. 26:39, 42) Yesu “anapilila mtengo wozunzikilapo,” ndipo “sanasamale kuti zocititsa manyazi zimucitikila.” Iye sanafune kukhala wodziŵika m’dzikoli, koma anafuna kukhala wodziŵika kwa Atate wake.—Aheb. 12:2. w18.07 10-11 ¶15-16
Kuŵelenga Baibo pa nyengo ya Cikumbutso: (Zocitika dzuŵa litaloŵa: Nisani 9) Maliko 14:3-9
Cisanu, April 3
Atate, ngati mukufuna, ndicotseleni kapu iyi.—Luka 22:42.
Atangoyambitsa Mgonelo wa Ambuye, Yesu anaonetsa kulimba mtima kwakukulu. Motani? Iye anadzipeleka kucita cifunilo ca Atate wake, olo kuti anali kudziŵa kuti kucita izi, kudzapangitsa kuti aphedwe pa mlandu wocititsa manyazi wakuti ananyoza Mulungu. (Mat. 26:65, 66) Yesu anakhalabe wokhulupilika mpaka imfa yake, n’colinga cakuti alemekeze dzina la Yehova na kukweza ucifumu wake, ndiponso kuti atsegulile anthu omvela njila yokapeza moyo wosatha. Panthawi imodzi-modziyo, Yesu anakonzekeletsa ophunzila ake kaamba ka mayeselo amene anatsala pang’ono kukumana nawo. Yesu anaonetsanso kulimba mtima mwa kupewa kumangodela nkhawa za mavuto amene anali pafupi kukumana nawo. M’malomwake, anaika mtima wake pa kuthandiza na kulimbikitsa atumwi ake okhulupilika. Mwacitsanzo, pambuyo potulutsa Yudasi, Yesu anayambitsa mwambo wa Cikumbutso. Mwambowu unali kudzakumbutsa otsatila ake odzozedwa za madalitso amene adzapeza cifukwa ca magazi amene iye adzakhetsa, komanso cifukwa cokhala m’pangano latsopano.—1 Akor. 10:16, 17. w19.01 22 ¶7-8
Kuŵelenga Baibo pa nyengo ya Cikumbutso: (Zocitika m’masana: Nisani 9) Maliko 11:1-11
Ciŵelu, April 4
Atate lemekezani dzina lanu. —Yoh. 12:28.
Yehova anayankha kucokela kumwamba kuti: “Ndalilemekeza ndipo ndidzalilemekezanso.” Yesu anasautsika mtima cifukwa coganizila udindo waukulu umene anali nawo wokhalabe wokhulupilika kwa Yehova. Iye anali kudziŵa kuti adzakwapulidwa mwankhanza, komanso kuti adzafa imfa yoŵaŵa. (Mat. 26:38) Ngakhale n’telo, anali kufunitsitsa kulemekeza dzina la Atate wake. Yesu anaimbidwa mlandu wonyoza Mulungu, ndipo anali kudela nkhawa kuti imfa yake idzabweletsa citonzo pa dzina la Mulungu. Mofanana ndi Yesu, nafenso tingadele nkhawa cifukwa ca kutonzedwa kwa dzina la Yehova. N’kuthekanso kuti monga mmene zinalili kwa Yesu, nafenso tikucitilidwa zinthu zopanda cilungamo. Kapena tili na nkhawa cifukwa ca mabodza amene otsutsa amafalitsa ponena za ife. Tingadelenso nkhawa poganizila citonzo cimene mabodza amenewa abweletsa pa dzina la Yehova. Ngati tili na nkhawa cifukwa ca zimenezi, mawu a Yehova angatilimbikitse kwambili. Yehova sadzalephela kulemekeza dzina lake.—Sal. 94:22, 23; Yes. 65:17. w19.03 11-12 ¶14-16
Kuŵelenga Baibo pa nyengo ya Cikumbutso: (Zocitika m’masana: Nisani 10) Maliko 11:12-19
Sondo, April 5
Yesu Khristu anayamba kuuza ophunzila ake kuti n’koyenela kuti iye . . . [akazunzidwe] kwambili . . . Ndiyeno akaphedwa. —Mat. 16:21.
Ophunzila a Yesu anadabwa na zimene iye anawauza. Iwo anali kuyembekezela kuti Yesu adzabwezeletsa ufumu kwa Isiraeli, koma iye anawauza kuti watsala pang’ono kuzunzidwa na kuphedwa. Atamva izi, Petulo anauza Yesu kuti: “Dzikomeleni mtima Ambuye. Musalole kuti zimenezi zikucitikileni ngakhale pang’ono.” Koma Yesu anam’dzudzula. Amvekele: “Pita kumbuyo kwanga, Satana! Ndiwe copunthwitsa kwa ine, cifukwa zimene umaganiza si maganizo a Mulungu, koma maganizo a anthu.” (Mat. 16:23; Mac. 1:6) Pamene anakamba mawu aya, Yesu anaonetsa kuti maganizo a Mulungu ni osiyana na maganizo a dziko la Satanali. (1 Yoh. 5:19) Zimene Petulo anakamba zinaonetsa kuti anali na mzimu wa dziko, wokana kucita zoyenela pofuna kupewa mavuto. Koma Yesu anadziŵa kuti maganizo a Atate wake ni osiyana na maganizo amenewa. Zimene Yesu anayankha Petulo zinaonetsa kuti sanafune kutengela maganizo a dziko, koma anafuna kuyendela maganizo a Yehova. w18.11 18 ¶1-2
Kuŵelenga Baibo pa nyengo ya Cikumbutso: (Zocitika m’masana: Nisan 11) Maliko 11:20–12:27, 41-44
Mande, April 6
Lengezanibe imfa ya Ambuye, mpaka iye adzafike.—1 Akor. 11:26.
Ganizilani zimene Yehova amaona pamene anthu mamiliyoni ambili padziko lonse asonkhana kuti acite Mgonelo wa Ambuye. Iye samangoyang’ana kuculuka kwa ciŵelengelo ca anthu amene asonkhana, koma amayang’ana munthu aliyense payekha amene wapezekapo. Mwacitsanzo, amaona anthu amene amayesetsa kupezekapo caka ciliconse. Ena mwa iwo angakhale anthu amene akukumana na cizunzo cacikulu. Komanso ena sapezeka nthawi zonse pa misonkhano ina, koma amaona kuti kupezeka pa Cikumbutso n’kofunika. Yehova amayang’ananso anthu ena amene apezeka pa Cikumbutso mwina kwa nthawi yoyamba. Anthu amenewa amapezekapo mwina cifukwa cofuna kudziŵa mmene mwambowu umacitikila. Mwacionekele, Yehova amakondwela akaona kuti anthu ambili asonkhana kuti acite Cikumbutso. (Luka 22:19) Iye amacita cidwi na zifukwa zimene zasonkhezela anthu kupezeka pa msonkhanowu. Kodi ife timafunitsitsa kuphunzitsidwa ndi Yehova komanso gulu lake?—Yes. 30:20; Yoh. 6:45. w19.01 26 ¶1-3
Kuŵelenga Baibo pa nyengo ya Cikumbutso: (Zocitika m’masana: Nisani 12) Maliko 14:1, 2, 10, 11; Mateyu 26:1-5, 14-16
Tsiku la Cikumbutso
Dzuŵa Likaloŵa
Ciŵili, April 7
Khristu anatifela.—Aroma 5:8.
Yesu anali wokonzeka kufela ophunzila ake, na kuika zofuna zawo patsogolo pa zofuna zake. Mwacitsanzo, ngakhale pamene anali wolema na wopanikizika maganizo, iye sanaleke kulimbikitsa ophunzila ake. (Luka 22:39-46) Cinanso, anali kuganizila kwambili pa zabwino zimene angacitile ena, osati pa zimene anali kufuna kuti ena am’citile. (Mat. 20:28) Tili m’gulu lokhalo la Akhristu oona, amene ali pa ubale weni-weni, ndipo timayesetsa kuitanila anthu ena ambili kuti abwele m’gulu limeneli. Koma timafunitsitsa kuthandiza “abale ndi alongo athu m’cikhulupililo,” amene anazilala mwauzimu. (Agal. 6:10) Timaonetsa kuti timawakonda mwa kuwalimbikitsa kuti azipezeka pa misonkhano, maka-maka pa Cikumbutso. Ndipo mofanana na Yehova na Yesu, timakondwela kwambili pamene Mkhristu wozilala wabwelela kwa Yehova.—Mat. 18:14. w19.01 29 ¶12, 14; 30 ¶15
Kuŵelenga Baibo pa nyengo ya Cikumbutso: (Zocitika m’masana: Nisani 13) Maliko 14:12-16; Mateyu 26:17-19 (Zocitika dzuŵa litaloŵa: Nisani 14) Maliko 14:17-72
Citatu, April 8
Mkate uwu ukuimila thupi langa. . . . Vinyoyu akuimila “magazi anga a pangano.”—Mat. 26:26-28.
Poyambitsa mwambo wokumbukila imfa yake, Yesu anaseŵenzetsa zakudya zimene zinatsala pa mwambo wa Pasika. Anangoseŵenzetsa mkate wopanda cofufumitsa komanso vinyo. Yesu anauza atumwi ake kuti mkate na vinyo zinali kuimila thupi lake langwilo na magazi ake, amene anali kudzawapeleka cifukwa ca iwo. Atumwi ayenela kuti sanadabwe kuona kuti mwambo wapadela umene Yesu anayambitsa unali wosalila zambili. Cifukwa ciani takamba conco? Miyezi ingapo kumbuyoko, pamene Yesu anali ku nyumba kwa mabwenzi ake, Lazaro, Marita, na Mariya,Yesu anayamba kuphunzitsa. Koma Marita anatangwanika na kukonzela Yesu zakudya zambili, monga mlendo wawo wolemekezeka. Yesu ataona zimenezo, mwacikondi anam’patsa uphungu Marita. Anamuuza kuti si nthawi zonse pamene kukonza zakudya zambili kumakhala kofunikila. (Luka 10:40-42) Pambuyo pake, atatsala pang’ono kupeleka moyo wake monga nsembe, Yesu anacita zinthu mogwilizana na malangizo ake amenewa. Anacita zimenezi mwa kuyambitsa mwambo wa Cikumbutso wosalila zambili. w19.01 20-21 ¶3-4
Kuŵelenga Baibo pa nyengo ya Cikumbutso: (Zocitika m’masana: Nisani 14) Maliko 15:1-47
Cinayi, April 9
Atate, ndiloleni kuti ndikhale pambali panu, ndipo mundipatse ulemelelo umene ndinali nawo. —Yoh. 17:5.
Yehova anam’dalitsa Yesu m’njila imene iye sanali kuyembekezela. Anamuukitsa n’kumuika “pamalo apamwamba” ndipo anamupatsa cinthu cimene aliyense anali asanalandilepo. Anamupatsa moyo wosafa. (Afil. 2:9; 1 Tim. 6:16) Zoonadi! Pamenepa Mulungu anaonetsa m’njila yapadela kwambili kuti anayamikila utumiki wokhulupilika wa Yesu. N’ciani cingatithandize kupewa mtima wofuna kuyanjidwa na dzikoli? Tizikumbukila kuti Yehova nthawi zonse amadziŵa atumiki ake okhulupilika, komanso kuti nthawi zambili amawadalitsa m’njila imene iwo sanali kuyembekezela. Na ise sitingadziŵe madalitso onse amene Yehova adzatipatsa m’tsogolo. Koma pali pano, pamene tikupilila mavuto na mayeselo m’dziko loipali, tiyeni nthawi zonse tizikumbukila kuti dzikoli likupita. (1 Yoh. 2:17) Atate wathu wakumwamba, Yehova, ‘si wosalungama woti angaiwale nchito yathu ndi cikondi cimene timacisonyeza pa dzina lake.’—Aheb. 6:10. w18.07 11 ¶17-18
Kuŵelenga Baibo pa nyengo ya Cikumbutso: (Zocitika m’masana: Nisani 15) Mateyu 27:62-66 (Zocitika dzuŵa litaloŵa: Nisani 16) Maliko 16:1
Cisanu, April 10
Ndikupemphela . . . kuti onsewa akhale amodzi.—Yoh. 17:20, 21.
Pamene Yesu anali kudya cakudya cothela camadzulo na atumwi ake, anali kudela nkhawa kwambili za mgwilizano wawo. Popemphela nawo pamodzi, iye anakamba kuti anali kufuna kuti ophunzila ake onse akhale amodzi, monga mmene iye na Atate ake alili amodzi. Iye anafuna kuti mgwilizano wawo udzakhale umboni wamphamvu woonetsa kuti Yehova anamutuma pa dziko lapansi kukacita cifunilo cake. Cikondi cinali kudzakhala cizindikilo ca ophunzila oona a Yesu, komanso cinali kudzawathandiza kukhala ogwilizana. (Yoh. 13:34, 35) M’pomveka kuti Yesu anagogomeza kwambili kufunika kwa mgwilizano. Iye anali ataona kuti atumwi ake sanali ogwilizana kweni-kweni. Mwacitsanzo, ganizilani zimene zinacitika pa nthawi ya cakudya cothela cimene iye anadya na ophunzila ake. Monga mmene anali kucitila m’mbuyomo, atumwiwo anayambanso kukangana “za amene anali kuoneka wamkulu kwambili” pakati pawo. (Luka 22:24-27; Maliko 9:33, 34) Pa nthawi inanso, Yakobo na Yohane anapempha Yesu kuti adzawapatse malo apamwamba mu Ufumu wake. Anapempha kuti wina adzakhale kudzanja lake lamanja, wina ku lamanzele.—Maliko 10:35-40. w18.06 8 ¶1-2
Kuŵelenga Baibo pa nyengo ya Cikumbutso: (Zocitika m’masana: Nisani 16) Maliko 16:2-8
Ciŵelu, April 11
Mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake, n’kudziphatika kwa mkazi wake, ndipo iwo adzakhala thupi limodzi.—Gen. 2:24.
Yehova amafuna kuti anthu ali pa banja azikondana kwambili, moti cikondi cawo n’kukhalapo kwa moyo wawo wonse. (Mat. 19:3-6) Kucita cigololo ni chimo lalikulu kwambili, komanso n’kupanda cikondi. Ndiye cifukwa cake, lamulo la namba 7 pa Malamulo Khumi, linaletsa kucita cigololo. (Deut. 5:18) Kucita cigololo “n’kucimwila Mulungu,” ndiponso n’kucitila nkhanza mnzako wa m’cikwati. (Gen. 39:7-9) Mwamuna kapena mkazi akacita cigololo, mnzake wosalakwayo angavutike maganizo kwa zaka zambili.Yehova amafunanso kuti ana azikhala acimwemwe komanso otetezeka. Yehova analamula makolo Aciisiraeli kuti azisamalila ana awo mwakuthupi ndi mwauzimu. Iwo anafunika kuseŵenzetsa mpata uliwonse pothandiza ana awo kukonda Yehova, kumvetsetsa Cilamulo cake, na kucilemekeza. (Deut. 6:6-9; 7:13) Makolo anafunika kukonda ana awo monga colowa, kapena kuti mphatso yocokela kwa Yehova. Ndipo sanafunike kuwanyalanyaza kapena kuwazunza.—Sal. 127:3. w19.02 21 ¶5, 7
Sondo, April 12
Mulungu adzadziŵa kuti ndili ndi mtima wosagawanika.—Yobu 31:6.
Yobu anakhalabe na mtima wamphumphu cifukwa anaika maganizo ake pa mphoto imene Mulungu anam’lonjeza. Anali kudziŵa kuti Mulungu anali kuona na kuyamikila kukhulupilika kwake. Yobu anali kukhulupilila kuti olo akumane na mavuto, Yehova adzamudalitsa pamapeto pake. Cikhulupililo cimeneci cinam’limbikitsa kupitiliza kukhala na mtima wamphumphu. Yehova anakondwela ngako cifukwa ca kukhulupilika kwa Yobu, cakuti anamukhuthulila madalitso ambili. (Yobu 42:12-17; Yak. 5:11) Ndipo kutsogoloku, adzalandila madalitso osaneneka. Kumbukilani kuti Mulungu wathu sanasinthe. (Mal. 3:6) Kukumbukila kuti iye amayamikila tikakhala na mtima wamphumphu, kudzatithandiza kukhala na ciyembekezo camphamvu ca tsogolo labwino.(1 Ates. 5:8, 9) Nthawi zina, mungaone kuti anzanu ambili sakucita zimenezi. Koma musataye mtima, simuli mwekha. Muli pakati pa gulu la anthu okhulupilika mamiliyoni, amene akuyesetsa kukhalabe na mtima wamphumphu. Komanso mudzakhala pa gulu la amuna na akazi okhulupilika akale, amene anakhalabe na mtima wamphumphu, olo pamene anawopsezedwa kuti adzaphedwa.—Aheb. 11:36-38; 12:1. w19.02 7 ¶15-16
Mande, April 13
Nonsenu mukhale amaganizo amodzi, omvelana cisoni, okonda abale, acifundo cacikulu, ndiponso amaganizo odzicepetsa. —1 Pet. 3:8.
Pamene nyengo ya Cikumbutso ikutha, tingacite bwino kudzifunsa mafunso awa: ‘Kodi ningatengele bwanji citsanzo ca Yesu poonetsa cikondi kwa ena? Kodi nimaika zosoŵa za Akhristu anzanga patsogolo pa zosoŵa zanga? Kodi nimayembekezela abale na alongo kucita zambili kuposa zimene angakwanitse, kapena nimazindikila zimene sangakwanitse?’ Tiyeni nthawi zonse titengele citsanzo ca Yesu mwa kumvela ena cisoni. Posacedwa, tidzaleka kucita Cikumbutso ca imfa ya Khristu. Yesu ‘akadzafika’ pa cisautso cacikulu, adzasonkhanitsila “osankhidwa ake” kumwamba. Ndipo zikadzakhala conco, sitidzacitanso Cikumbutso. (1 Akor. 11:26; Mat. 24:31) Ngakhale tikadzaleka kucita Cikumbutso, sitikayikila kuti tidzapitiliza kuona mwambo umenewo monga cizindikilo ca kudzicepetsa kwakukulu, kulimba mtima, komanso cikondi cacikulu cimene Yesu anaonetsa. w19.01 25 ¶17-19
Ciŵili, April 14
Mumakondwela ndi coonadi cocokela pansi pa mtima. Ndipo mundidziŵitse nzelu mumtima mwanga.—Sal. 51:6.
Umunthu wa mkati timafunika kuusamalila. Kuti timvetsetse kufunika kocita zimenezi, tiyeni tiyelekezele na thanzi lathu. Coyamba, kuti tikhalebe na thanzi labwino timafunika kudya zakudya zopatsa thanzi, komanso kucita maseŵela olimbitsa thupi kaŵili-kaŵili. Mofananamo, kuti tikhalebe athanzi mwauzimu, timafunika kudya cakudya cauzimu. Cinanso, nthawi zonse timafunika kucita zinthu zoonetsa kuti tili na cikhulupililo mwa Yehova. Ndipo tingaonetse kuti tili na cikhulupililo mwa kuseŵenzetsa zimene timaphunzila, komanso kuuzako ena zimene timakhulupilila. (Aroma 10:8-10; Yak. 2:26) Caciŵili, nthawi zina tingapusitsike na maonekedwe akunja a munthu, n’kuganiza kuti ni wathanzi, pamene m’thupi mwake muli matenda. Mofananamo, tingakhale na pulogilamu yazauzimu, n’kumaganiza kuti tili na cikhulupililo colimba. Koma pa nthawi imodzi-modzi, zilakolako zoipa zingakhale kuti zikukula mu mtima mwathu. (1 Akor. 10:12; Yak. 1:14, 15) Tizikumbukila kuti Satana amafuna kuipitsa mtima wathu mwa kutipangitsa kutengela maganizo ake. w19.01 15 ¶4-5
Citatu, April 15
Pita, iwenso uzikacita zomwezo.—Luka 10:37.
Tingacite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi nimacita zinthu monga mmene Msamariya wacifundo anacitila? (Luka 10:30-35) Kodi ningawonjezele zimene nimacita poonetsa cifundo mwa kuyesetsa kuthandiza anthu amene akuvutika? Mwacitsanzo, kodi mungathandizeko Akhristu okalamba, alongo amasiye, ndi ana amene makolo awo si Mboni? Komanso bwanji osacitapo kanthu kuti ‘mulimbikitse a mtima wacisoni?’ (1 Ates. 5:14; Yak. 1:27) Kuonetsa ena cifundo ni mbali imodzi ya kupatsa, ndipo kupatsa kumabweletsa cimwemwe. Komanso, tikakhala acifundo timakhala acimwemwe cifukwa timadziŵa kuti tikucita zinthu zokondweletsa Yehova. (Mac. 20:35; Aheb. 13:16) Mfumu Davide pokamba za munthu amene amacita zinthu moganizila ena, anati: “Yehova adzamuteteza ndi kumusunga ali wamoyo. Adzachedwa wodala padziko lapansi.” (Sal. 41:1, 2) Tikakhala acifundo, Yehova nayenso amaticitila cifundo. Ndipo izi zingapangitse kuti tikakhale na moyo wacimwemwe kwamuyaya.—Yak. 2:13. w18.09 19-20 ¶11-12
Cinayi, April 16
Usacite mantha, pakuti ndili nawe. Usayang’ane uku ndi uku mwamantha, pakuti ine ndine Mulungu wako. Ndikulimbitsa. Ndithu ndikuthandiza.—Yes. 41:10.
Mlongo wina, dzina lake Yoshiko, anauzidwa mawu odandaulitsa. Adokotala anamuuza kuti pakapita miyezi yocepa cabe, adzamwalila. Kodi iye anacita ciani? Anakumbukila lemba lake la pamtima, lemba la tsiku lalelo. Ndiyeno modekha, Mlongoyo anauza adokotala kuti sanali kuyopa kufa, cifukwa Yehova anali atagwila dzanja lake. Uthenga wacitonthozo wa m’lembali, unathandiza mlongo wathu ameneyu kudalila Yehova na mtima wake wonse. Na ife, lembali lingatitonthoze pamene takumana na mavuto aakulu. Yehova anauzila mneneli Yesaya kulemba uthenga wa pa lembali, pofuna kutonthoza Ayuda amene anali kudzatengewa kupita ku ukapolo ku Babulo. Ngakhale n’conco, Yehova anadziŵa kuti uthengawu udzatonthozanso atumiki ake a kutsogolo. (Yes. 40:8; Aroma 15:4) Masiku ano, tikukhala ‘m’nthawi yapadela komanso yovuta.’ Conco, kuposa kale lonse, uthenga wolimbikitsa wa m’buku la Yesaya ni wofunika kwambili kwa ife.—2 Tim. 3:1. w19.01 2 ¶1-2
Cisanu, April 17
Ngati wosakhulupililayo wacoka, acoke.—1 Akor. 7:15.
Anthu akapatukana, cikwati cawo cimakhala kuti cikalipo ndipo ngakhale kuti apatukane, amakumanabe na zovuta zinazake. Mtumwi Paulo anafotokoza ubwino umene umakhalapo ngati okwatilana asankha kuti asapatukane. Anati: “Mwamuna wosakhulupilila amayeletsedwa cifukwa ca mkazi wake, ndiponso mkazi wosakhulupilila amayeletsedwa cifukwa ca m’baleyo, apo ayi, ana anu akanakhala osayela, koma tsopano ndi oyela.” (1 Akor. 7:14) Akhristu ambili okhulupilika anapitilizabe kukhala na mnzawo wa m’cikwati wosakhulupilila, olo kuti anali kukumana na mavuto aakulu. Iwo anadzionela okha ubwino wocita zimenezi, pamene mnzawoyo anakhala Mboni. (1 Akor. 7:16; 1 Pet. 3:1, 2) Masiku ano, mu mpingo wacikhristu pa dziko lonse muli abale na alongo ambili amene ali na vikwati volimba ndipo amakhala mwacimwemwe. Mwacionekele, ngakhale mu mpingo mwanu muli mabanja ambili acimwemwe. M’mabanja amenewo muli abale okhulupilika amene amakonda akazi awo, komanso alongo odzipeleka amene amakonda amuna awo. Izi zimaonetsa kuti n’zotheka cikwati kukhala colemekezeka.—Aheb. 13:4. w18.12 14 ¶18-19
Ciŵelu, April 18
Yehova Mulungu atatelo, anakonza munda ku Edeni, . . . ndipo m’mundamo anaikamo munthu amene anamuumbayo.—Gen. 2:8.
Liwu lakuti Edeni limatanthauza ‘Cisangalalo.’ Ndipo liwuli n’loyenelela cifukwa Edeni anali malo okondweletsa kwambili kukhalamo. Anali malo okongola, munali cakudya cambili, komanso anthu anali kukhala mwamtendele na vinyama. (Gen. 1:29-31) Pa·ra’dei·sos ni liwu la Cigiriki limene akalimasulila m’Ciheberi limatanthauza “munda.” Pokamba za liwu lakuti pa·ra’dei·sos, buku la Cyclopaedia lolembedwa na M’Clintock na Strong limati: “M’giriki wina wapaulendo atamvela liwuli, anaganizila za paki yaikulu bwino, yokongola ndi yosaipitsidwa na ciliconse, imene mulibe zoopsa zilizonse. Muli mitengo yooneka bwino, yambili mwa iyo yobala zipatso, imene ikuthililidwa na mitsinje ya madzi abwino, ndipo m’mbali mwa mitsinjeyo muli insa kapena nkhosa zambili zimene zikuyenda-yenda.” Izi zionetsa kuti munda wa Edeni unalidi paradaiso. (Yelekezelani na Genesis 2:15, 16) Mulungu anaika Adamu na Hava m’paradaiso wokongola ngati ameneyo. Koma iwo sanayenelele kukhalamo cifukwa cakuti sanamvele Mulungu. Conco, iwo ndi ana awo anataya mwayi wokhala m’Paradaiso. (Gen. 3:23, 24) Olo kuti m’munda wa Edeni munakhala mopanda anthu, mundawo uyenela kuti unalipobe mpaka pamene Cigumula ca Nowa cinacitika. w18.12 3-4 ¶3-5
Sondo, April 19
Ine Yehova ndine. . . amene ndimakuphunzitsani kuti zinthu zikuyendeleni bwino.—Yes. 48:17.
Makolo amayesetsa kuphunzitsa ana awo mfundo za makhalidwe abwino. Ngati anawo asankha kutsatila mfundo za makhalidwe abwino zimene makolo awo anawaphunzitsa, amapanga zosankha mwanzelu. Akatelo, amapewa kudzibweletsela mavuto. Molingana na kholo labwino, Yehova amafuna kuti ise ana ake tikhale na umoyo wacimwemwe kwambili. (Yes. 48:18) Mwa ici, iye watiphunzitsa mfundo za makhalidwe abwino. Yehova amafuna kuti tiziona zinthu mmene iye amazionela, komanso kuti tizitsatila mfundo zake za makhalidwe abwino. Kucita izi sikutilanda ufulu, koma kumatithandiza kukulitsa luso la kuganiza. (Sal. 92:5; Miy. 2:1-5; Yes. 55:9) Ngati titsatila mfundo za Yehova, timakhalabe na mwayi wocita zinthu malinga n’zokonda zathu. Ndipo timatha kupanga zosankha zimene zingatibweletsele cimwemwe. (Sal. 1:2, 3) Zoonadi, kutengela maganizo a Yehova n’kwabwino komanso n’kothandiza. w18.11 19 ¶7-8
Mande, April 20
Amakunyozani.—1 Pet. 4:4.
Kuti tipitilize kuyenda m’coonadi, sitifunika kugonja ngati ena amatitsutsa. Pamene tinayamba kuyenda m’coonadi, mgwilizano wathu na acibululu komanso anthu ena amene si Mboni unasintha. Ena anangololela, koma ena anayamba kutitsutsa kwambili. Acibululu, anzathu a ku nchito, ndiponso anzathu a ku sukulu, angayese kutikopa kuti ticiteko zikondwelelo zosemphana na Malemba. Tingacite ciani kuti tisagonje ngati anthu akutituntha kuti ticite nawo miyambo na zikondwelelo zosalemekeza Yehova? Tizikumbukila nthawi zonse mmene Yehova amaonela miyambo na zikondwelelo zimenezo. Kuŵelenganso nkhani za m’mabuku athu, zofotokoza mmene zikondwelelo zofala zinayambila n’kothandiza. Ngati tikumbukila zifukwa za m’Malemba zimene siticitila nawo zikondwelelo zimenezo, timakhala okhutila kuti tikuyenda m’njila ‘yovomelezeka kwa Ambuye.’ (Aef. 5:10) Kukhulupilila Yehova na Mawu ake a coonadi kudzatiteteza ku msampha ‘woopa anthu.’—Miy. 29:25. w18.11 11 ¶10, 12
Ciŵili, April 21
Yehova anali ndi Yosefe, ndipo ciliconse cimene iye anali kucita Yehova anali kucidalitsa. —Gen. 39:23.
Zinthu zikasintha mosayembekezeleka mu umoyo wathu, n’zosavuta kukhwethemuka maganizo cifukwa ca nkhawa. Zaconco zikanamucitikilanso Yosefe. Koma iye sanalole nkhawa kumufooketsa. M’malomwake, anacita zonse zotheka malinga na mmene zinthu zinalili mu umoyo wake, ndipo Yehova anam’dalitsa. Olo pamene anali m’ndende, Yosefe anali kugwila mwakhama nchito imene mkulu wa ndende anam’patsa, monga mmene anali kucitila potumikila Potifara. (Gen. 39:21, 22) Mofanana na Yosefe, na ise nthawi zina tingakumane na zinthu zothetsa nzelu. Komabe, ngati tikhalabe oleza mtima na kucita zonse zotheka malinga na mmene zinthu zilili, Yehova adzatidalitsa. (Sal. 37:5) N’zoona kuti nthawi zina ‘tingathedwe nzelu.’ Koma monga mmene mtumwi Paulo anakambila, sitidzathedwa nzelu mpaka “kusoŵelatu pothaŵila.” (2 Akor. 4:8) Mawu a Paulo amenewa adzakwanilitsidwa pa ise, maka-maka ngati tiikabe mtima wathu pa nchito yolalikila. w18.10 29 ¶11, 13
Citatu, April 22
Mulungu si wosalungama woti angaiŵale nchito yanu ndi cikondi cimene munacisonyeza pa dzina lake.—Aheb. 6:10.
Kodi mumamvela bwanji ngati munthu amene mumam’dziŵa na kum’lemekeza waiŵala dzina lanu, kapena ngati wakamba kuti sakudziŵani? Zingakhale zovutitsa maganizo. Cifukwa ciani? Cifukwa cakuti mwacibadwa, ise tonse timafuna kuti anthu ena azitidziŵa. Izi zimaphatikizapo zambili osati kudziŵa cabe dzina lathu. Timafunanso kuti azidziŵa kuti ndise anthu abwanji na kuti tacita zotani mu umoyo wathu. (Num. 11:16; Yobu 31:6) Mofanana na zilako-lako zina zacibadwa zimene tili nazo, cilako-lako cofuna kukhala wodziŵika kwa ena cingatisoceletse. Izi zingacitike cifukwa ndise opanda ungwilo. Tingayambe kudzifunila ulemu wopambanitsa. Dziko la Satanali limasonkhezela anthu kukhala na mtima wofuna kuchuka na kulemekezedwa kwambili, m’malo mopeleka ulemelelo kwa Atate wathu wakumwamba, Yehova Mulungu, amene ndiye woyenela kulambilidwa na kulandila ulemelelo.—Chiv. 4:11. w18.07 7 ¶1-2
Cinayi, April 23
Dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.—1 Yoh. 5:19.
N’zosadabwitsa kuti Satana na viŵanda vake amasonkhezela anthu amene ali na maudindo apamwamba kuti ‘azilankhula mabodza.’ (1 Tim. 4:1, 2) Atsogoleli onama acipembedzo ndiwo ali na mlandu waukulu kwambili cifukwa ca mabodza amene amaphunzitsa. Zili conco cifukwa ngati munthu wakhulupilila ciphunzitso cabodza na kucita zinthu zimene Mulungu amazonda, angataye mwayi wokapeza moyo wosatha. (Hos. 4:9) Yesu anadziŵa kuti atsogoleli acipembedzo a m’nthawi yake anali na mlandu wosoceletsa anthu. Iye anawadzudzula mosapita m’mbali. Anati: “Tsoka kwa inu alembi ndi Afarisi, onyenga inu! Cifukwa mumatha mitunda kuti mukatembenuze munthu mmodzi, koma akatembenuka mumam’sandutsa woyenela kuponyedwa m’Gehena [ciwonongeko cothelatu] kuposa inuyo.” (Mat. 23:15, ftn.) Yesu anawadzudzula mwamphamvu atsogoleli onama amenewo. Iwo analidi ‘ocokela kwa atate wawo Mdyerekezi.’—Yoh. 8:44. w18.10 7 ¶5-6
Cisanu, April 24
Ndinu odala pamene anthu akukunyozani ndi kukuzunzani. . . cifukwa ca ine.—Mat. 5:11.
Kodi pamenepa Yesu anatanthauzanji? Iye anapitiliza kuti: “Kondwelani, dumphani ndi cimwemwe, cifukwa mphoto yanu ndi yaikulu kumwamba, pakuti umu ndi mmenenso anazunzila aneneli amene analipo inu musanakhaleko.” (Mat. 5:11, 12) Atumwi atakwapulidwa na kuuziwa kuti aleke kulalikila, “anacoka pamaso pa Khoti Lalikulu la Ayuda, ali osangalala.” Sikuti anasangalala cifukwa cokwapulidwa. Koma “cifukwa cakuti Mulungu anawaona kuti ndi oyenela kucitilidwa cipongwe cifukwa ca dzina la Yesu.”(Mac. 5:41) Masiku anonso, anthu a Yehova amapilila mwacimwemwe pamene akuvutika cifukwa ca dzina la Yesu, kapena pamene akukumana na mayeselo aakulu. (Yak. 1:2-4) Molingana na atumwi, sitikondwela cifukwa covutika. Koma tikakhalabe okhulupilika kwa Yehova pamene tikumana na mayeselo, iye amatithandiza kupilila molimba mtima komanso mwacimwemwe. Ngati tili pa ubwenzi wabwino na “Mulungu wacimwemwe,” tingakhalebe osangalala olo pamene tikuzunzidwa cifukwa ca cikhulupililo cathu, kutsutsidwa na acibululu.—1 Tim. 1:11. w18.09 21 ¶18-20
Ciŵelu, April 25
Amangodzaza ndi mavuto ndi zopweteka.—Sal. 90:10.
Tikukhala m’masiku ‘ovuta’, ndipo umoyo ni ‘wodzala na mavuto na zopweteka.’ Ndiye cifukwa cake anthu oculuka amakhala na nkhawa kwambili. Ndipo ambili amaona kuti cili bwino kungodzipha cabe. (2 Tim. 3:1-5) Ofufuza amakamba kuti anthu oposa 800,000 amadzipha caka ciliconse. Zimenezi zitanthauza kuti pa masekondi 40 aliwonse, munthu wina amadzipha. N’zomvetsa cisoni kuti ngakhale ena mwa atumiki a Mulungu, amataya mtima kwambili mpaka kufika podzipha. Masiku ano, abale na alongo athu ambili akukumana na mavuto aakulu, ndipo amafunika kulimbikitsidwa mwacikondi. Ena akukumana na cizunzo, komanso ena amanyozewa. Palinso ena amene anzawo ku nchito amawatsutsa na kuwajeda. Ndipo ena amakhala olema kwambili cifukwa cogwila nchito ya ovataimu, kapena cifukwa coseŵenza modzipanikiza kuti atsilize nchito pa nthawi imene apatsidwa. Komanso, ena akukumana na mavuto m’banja mwawo, monga kutsutsidwa na mwamuna kapena mkazi wawo wosakhulupilila. Cifukwa ca mavuto amenewa ndi ena, ambili mu mpingo amakhala olema komanso opanikizika maganizo. w18.09 13 ¶3, 5
Sondo, April 26
Palibe cimene cimandisangalatsa kwambili kuposa kumva kuti ana anga akuyendabe m’coonadi.—3 Yoh. 4.
Makolo acikhristu amaseŵenza na Yehova pamene athandiza ana awo kukhala na zolinga zauzimu. Makolo ambili amene anacita zimenezi, pambuyo pake anaona ana awo akucoka pa nyumba kukacita utumiki wa nthawi zonse kutali na kwawo. Ena ni amishonale, ena akucita upainiya ku madela osoŵa, ndipo enanso akutumikila pa Beteli. N’zoona kuti makolowo saonana kawili-kawili ndi ana awo. Komabe, makolo amene ali na mtima wodzimana amalimbikitsa ana awo kupitiliza utumiki wawo. Cifukwa ciani? Cifukwa cakuti amapeza cimwemwe coculuka poona kuti ana awo akuika zinthu za Ufumu patsogolo. Mwacionekele, ambili mwa makolo amenewa amamvela monga mmene Hana anamvelela. Iye anakamba kuti ‘anabweleketsa’ mwana wake Samueli kwa Yehova. Makolo amenewa amaona kuti kuseŵenza na Yehova mwa njila imeneyi ni mwayi waukulu. Iwo saona kuti analakwitsa kulimbikitsa ana awo kuyamba kutumikila Yehova.—1 Sam. 1:28. w18.08 24 ¶4
Mande, April 27
Zidzakhalatu zovuta kuti munthu wolemela adzaloŵe mu ufumu wakumwamba.—Mat. 19:23
Yesu sanakambe kuti wolemela sadzaloŵa mu Ufumuwo. Iye anakambanso kuti: “Odala ndinu osaukanu, cifukwa ufumu wa Mulungu ndi wanu.” (Luka 6:20) Komabe, izi sizinatanthauze kuti anthu onse osauka anali odalitsidwa mwapadela komanso kuti anamvetsela uthenga wa Yesu. Panali anthu ambili osauka amene sanamvetsele. Conco, mfundo ni yakuti: Kulemela kapena kusauka si cizindikilo cakuti munthu ali pa ubwenzi wabwino na Yehova. Ndise odala kuti tili na abale na alongo ambili, osauka na olemela, amene amakonda Yehova na kum’tumikila na mtima wonse. Malemba amalangiza Akhristu olemela kuti “asamadalile cuma cosadalilika, koma adalile Mulungu.” (1 Tim. 6:17-19.) Koma Mawu a Mulungu amacenjeza anthu onse a Mulungu, olemela na osauka omwe, kuti ayenela kupewa kukonda ndalama. (1 Tim. 6:9, 10) Zoonadi, ngati tiyesetsa kuona abale athu monga mmene Yehova amawaonela, tidzapewa kuwaweluza potengela kuti ni olemela kapena osauka. w18.08 10-11 ¶11-12
Ciŵili, April 28
Gonjelani Mulungu.—Yak. 4:7.
Mwacionekele, ise tonse timafunitsitsa kuonetsa kuti timamuyamikila Yehova potipatsa mwayi wokhala anthu ake. Timadziŵa kuti kudzipatulila kwa iye ndiye cinthu canzelu kwambili cimene tinacita mu umoyo wathu. Timayesetsa kukana zoipa. Komanso, timakonda na kulemekeza olambila anzathu, podziŵa kuti nawonso ni anthu a Yehova. (Aroma 12:10) Baibo inalonjeza kuti: “Yehova sadzataya anthu ake.” (Sal. 94:14) Iye sangatitaye olo titakumana na mavuto aakulu bwanji. Ngakhale imfa siingathe kutilekanitsa na cikondi ca Yehova. (Aroma 8:38, 39) “Cotelo kaya tikhale ndi moyo kapena tife, ndife a Yehova.” (Aroma 14:8) Ndipo tikuyembekezela mwacidwi nthawi imene Yehova adzaukitsa mabwenzi ake onse okhulupilika amene anafa. (Mat. 22:32) Ngakhale lomba, tikulandila madalitso ambili. Mpake kuti Baibo imati, “wodala ndi mtundu umene Mulungu wawo ndi Yehova, anthu amene iye wawasankha kukhala colowa cake.”—Sal. 33:12. w18.07 26 ¶18-19
Citatu, April 29
Zinthu zonse ndi zololeka, koma si zonse zimene zili zaphindu. Zinthu zonse ndi zololeka, koma si zonse zimene zili zolimbikitsa. —1 Akor. 10:23.
Anthu ena angaganize kuti popeza munthu ali na ufulu wosankha pa nkhani monga maphunzilo, kapena nchito, angacite ciliconse cimene afuna, malinga ngati cikumbumtima cake cimulola. Mwina angaganizile mawu amene Paulo anakamba kwa Akhristu a ku Korinto akuti: “N’cifukwa ciani ufulu wanga ukulamulidwa ndi cikumbumtima ca munthu wina?” (1 Akor. 10:29) N’zoona kuti tili na ufulu wodzisankhila pa nkhani ngati zimenezi. Koma tizikumbukila kuti ufulu wathu uli na malile, ndipo zosankha zathu zonse zimakhala na zotulukapo zake. N’cifukwa cake Paulo asanakambe mawu amenewa anakamba mawu a mu lemba la tsiku la lelo. Izi zionetsa kuti pali zinthu zina zofunika kwambili zimene tiyenela kuziganizila popanga zosankha zaumwini, m’malo mongoganizila zokonda zathu. w18.04 10 ¶10
Cinayi, April 30
Bwelelani kwa ine ndipo ine ndibwelela kwa inu.—Mal. 3:7.
Mkhristu masiku ano angakambe kuti amalambila Yehova, koma n’kumacita zinthu zina zimene iye amazonda. (Yuda 11) Mwacitsanzo, iye angalole maganizo a ciwelewele ndi a dyela kuzika mizu mu mtima mwake. Kapena angayambe kusungila Mkhristu mnzake cidani. (1 Yoh. 2:15-17; 3:15) Maganizo aconco angapangitse Mkhristuyo kucita chimo. Koma pa nthawi imodzi-modzi, iye angakhale kuti ni wacangu mu ulaliki ndipo amapezeka pa misonkhano nthawi zonse. Mwina anthu ena sangadziŵe maganizo athu na zocita zathu, koma Yehova amaona zonse ndipo amadziŵa ngati timam’tumikiladi mokhulupilika kapena ayi. (Yer. 17:9, 10) Ngakhale n’conco, Yehova amayesetsabe kutithandiza. Ngati munthu wayamba kuyenda njila yolakwika, Yehova amam’langiza kuti: ‘Bwelela kwa ine.’ Maka-maka ngati tikulimbana ndi zofooka zinazake, Yehova amafuna kuti tiziyesetse kukana zoipa. (Yes. 55:7) Tikacita zimenezi, iyenso adzakhala kumbali yathu mwa kutilimbikitsa na kutipatsa mphamvu zimene zingatithandize ‘kugonjetsa’ zilakolako zathu za ucimo.—Gen. 4:7. w18.07 18 ¶5-6