LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • es20 masa. 47-57
  • May

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • May
  • Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2020
  • Tumitu
  • Cisanu, May 1
  • Ciŵelu, May 2
  • Sondo, May 3
  • Mande, May 4
  • Ciŵili, May 5
  • Citatu, May 6
  • Cinayi, May 7
  • Cisanu, May 8
  • Ciŵelu, May 9
  • Sondo, May 10
  • Mande, May 11
  • Ciŵili, May 12
  • Citatu, May 13
  • Cinayi, May 14
  • Cisanu, May 15
  • Ciŵelu, May 16
  • Sondo, May 17
  • Mande, May 18
  • Ciŵili, May 19
  • Citatu, May 20
  • Cinayi, May 21
  • Cisanu, May 22
  • Ciŵelu, May 23
  • Sondo, May 24
  • Mande, May 25
  • Ciŵili, May 26
  • Citatu, May 27
  • Cinayi, May 28
  • Cisanu, May 29
  • Ciŵelu, May 30
  • Sondo, May 31
Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2020
es20 masa. 47-57

May

Cisanu, May 1

Muzikonda mlendo wokhala pakati panu.—Deut. 10:19.

M’zaka zaposacedwa, m’maiko ambili mwakhala mukubwela anthu oculuka othaŵa kwawo. Bwanji osaphunzilako moni m’citundu cawo? Cinanso, mungaphunzileko mawu ocepa a m’citundu cawo amene angawakope cidwi. Ndiyeno, mungaŵalongoze webusaiti ya jw.org na kuwaonetsa mavidiyo na zofalitsa zimene zilipo m’citundu cawo. Mwacikondi, Yehova anatikonzela Msonkhano wa Umoyo na Utumiki Wathu n’colinga cakuti tikhale aluso kwambili mu ulaliki. Malangizo amene timalandila pa msonkhanowu amatithandiza kudziŵa bwino mocitila maulendo obwelelako ndi mocititsila maphunzilo a Baibo. Conco, makolo muzithandiza ana anu kuonetsa kuwala kwawo mwa kuwaphunzitsa kupeleka ndemanga m’mawu awo-awo. Mayankho aafupi na ocokela pansi pa mtima opelekedwa ndi ana, acititsa anthu ena acidwi kuzindikila kuti timaphunzila coonadi.—1 Akor. 14:25. w18.06 22-23 ¶7-9

Ciŵelu, May 2

Landilanani, monga mmene Khristu anatilandilila.—Aroma 15:7.

Tifunika kukumbukila kuti pa nthawi inayake, ise tonse tinali “alendo,” otalikilana ndi Mulungu. (Aef. 2:12) Koma “mwacikondi” cake, Yehova anatikokela kwa iye. (Hos. 11:4; Yoh. 6:44) Ndipo Khristu anatilandila. Iye anatitsegulila khomo, titelo kukamba kwake, n’colinga cakuti tikhale mbali ya banja la Mulungu. Ngakhale kuti ndise opanda ungwilo, Yesu anatilandila. Nanga ise n’kulekelanji kulandila ena? N’zodziŵikilatu kuti magaŵano, tsankho, na cidani zidzaonjezeka m’dzikoli pamene mapeto akuyandikila. (Agal. 5:19-21; 2 Tim. 3:13) Koma ise pokhala atumiki a Yehova, timafuna-funa nzelu yocokela kumwamba, imene ni yopanda tsankho komanso imalimbikitsa mtendele. (Yak. 3:17, 18) Timapeza cimwemwe ngati tiyesetsa kupanga ubwenzi ndi anthu ocokela m’maiko ena, kuonetsa mzimu wololela kwa anthu a cikhalidwe cina, kapena kuphunzila citundu cawo. Tikamacita zimenezi, mtendele wathu umakhala ngati mtsinje, ndipo cilungamo cathu cimakhala ngati mafunde a m’nyanja.—Yes. 48:17, 18. w18.06 12 ¶18-19

Sondo, May 3

[Vekani] mapazi anu nsapato zokonzekela uthenga wabwino wamtendele.—Aef. 6:15.

Msilikali waciroma ngati sanavale nsapato, ndiye kuti sanali wokonzeka kumenya nkhondo. Nsapato zake zokhala ngati masandasi zinali na nthambo zambili zacikumba zomangidwa bwino pamodzi kuti akazivala zizigwila bwino mapazi ake. Cifukwa ca mmene anali kuzipangila, nsapatozo zinali kukhala zolimba ndi zosavuta kuyenda nazo. Nsapato zimene asilikali aciroma anali kuvala zinali zopita nazo ku nkhondo. Koma nsapato zophiphilitsa zimene Akhristu amavala, zimawathandiza polalikila uthenga wa mtendele. (Yes. 52:7; Aroma 10:15) Ngakhale n’conco, Mkhristu amafunika kulimba mtima kuti alalikile pamene mpata wapezeka. Mnyamata wina wa zaka 20, dzina lake Bo, anati: “N’nali kuyopa kulalikila anzanga a m’kilasi. N’nali kucita manyazi. Koma niona kuti panalibe cifukwa cocitila manyazi. Lomba, nimakondwela kulalikila anzanga.” Acicepele ambili aona kuti ngati akonzekela bwino ulaliki, zimakhala zosavuta kulalikila uthenga wabwino kwa ena. w18.05 29 ¶9-11

Mande, May 4

[Pitilizani] kubala zipatso zambili.—Yoh. 15:8.

Yesu anauza atumwi kuti: “Ndikupatsani mtendele wanga.” (Yoh. 14:27) Kodi mphatso ya mtendele imeneyi imatithandiza bwanji kubala zipatso? Pamene tipilila pa nchito yolalikila, timakhala na mtendele waukulu wa mumtima, umene umabwela cifukwa codziŵa kuti ndise oyanjidwa na Yehova na Yesu. (Sal. 149:4; Aroma 5:3, 4; Akol. 3:15) Pambuyo pouza atumwi ake kuti afuna ‘cimwemwe cawo cisefukile,’ Yesu anawafotokozelanso za kufunika koonetsa cikondi codzimana. (Yoh. 15:11-13) Kenako, anawauza kuti: “Ndakuchani mabwenzi.” Ndithudi! Kukhala pa ubwenzi na Yesu ni mphatso ya mtengo wapatali. Nanga n’ciani cimene atumwiwo anafunika kucita kuti akhalebe mabwenzi ake? Anafunika ‘kupitiliza kubala zipatso zoculuka.’ (Yoh. 15:14-16) Zaka ziŵili m’mbuyomo, Yesu anali atalamula atumwi ake kuti: “Pitani ndi kulalikila kuti, ‘Ufumu wakumwamba wayandikila.’” (Mat. 10:7) Conco, pa usiku womaliza uja, iye anawalimbikitsa kuti ayenela kupilila pa nchito imene anawapatsa.—Mat. 24:13; Maliko 3:14. w18.05 20-21 ¶15-16

Ciŵili, May 5

Ciliconse cimene munthu wafesa, adzakololanso comweco. —Agal. 6:7.

Acicepele, muyenela kuika zolinga zauzimu patsogolo mu umoyo wanu. Mwina acicepele anzanu amaona kuti zosangalatsa ndiye zofunika kwambili mu umoyo wawo, ndipo angakupempheni kuti muzicita nawo zimenezi. M’kupita kwa nthawi, mudzafunika kuonetsa kuti ndimwe otsimikiza mtima kucita zinthu mogwilizana ndi zosankha zanu. Musalole kuti anzanu akulepheletseni kukwanilitsa zolinga zanu. Pali zinthu zingapo zimene mungacite kuti mupewe kutengela zocita za anzanu. Mwacitsanzo, pewani kupezeka m’zocitika zimene zingakuikeni pa ciyeso. (Miy. 22:3) Komanso, muziganizila mavuto amene mungakumane nawo cifukwa cogwilizana ndi anthu ocita zoipa. Cinanso cimene cingakuthandizeni ni kuzindikila kuti nthawi zina mumafunikila malangizo ocokela kwa ena. Kudzicepetsa kudzakuthandizani kulandila malangizo ocokela kwa makolo anu na Akhristu ena okhwima mwauzimu mumpingo (1 Petulo 5:5, 6) Kodi ndimwe odzicepetsadi cakuti mumalabadila mukapatsidwa malangizo? w18.04 28-29 ¶14-16

Citatu, May 6

Gwilani mwamphamvu zomwe zija, zimene muli nazo, mpaka nditabwela. Ndipo amene wapambana pa nkhondo ndi kutsatila zocita zanga kufikila mapeto, ndidzamupatsa ulamulilo pa mitundu ya anthu.—Chiv. 2:25, 26.

M’mauthenga a Yesu opita ku mipingo ya ku Asia Minor, iye anayamikila otsatila ake cifukwa ca nchito imene anacita. Mwacitsanzo, mu uthenga wake wopita ku mpingo wa Tiyatira, iye anayamba na mawu akuti: “Ndikudziŵa nchito zako, cikondi cako, cikhulupililo cako, utumiki wako, ndi kupilila kwako. Ndikudziŵanso kuti nchito zako zapanopa n’zambili kuposa zoyamba zija.” (Chiv. 2:19) Yesu anayamikila Akhristuwo cifukwa ca kuculuka kwa nchito zawo zabwino, komanso cifukwa ca makhalidwe abwino amene anawasonkhezela kugwila nchitozo. Ngakhale kuti colinga cake cinali kupeleka uphungu kwa Akhristu ena mu mpingomo, iye anayamba na kutsiliza uthenga wake na mawu olimbikitsa. (Chiv. 2:27, 28) Pokhala mutu wa mipingo yonse, Yesu ali na udindo waukulu kwambili, cakuti safunika kucita kutiyamikila pa nchito zimene timam’citila. Ngakhale n’telo, iye amayesetsa kutiyamikila. Ndithudi, iye n’citsanzo cabwino kwambili kwa akulu! w19.02 16 ¶10

Cinayi, May 7

Yudasi ndi Sila . . . analimbikitsa abalewo ndi mawu ambili ndipo anawapatsa mphamvu. —Mac. 15:32.

Bungwe Lolamulila la m’nthawi ya atumwi linali kulimbikitsa abale amene anali kutsogolela mu mpingo komanso Akhristu ena onse. Bungwelo linatumiza mamembala ake aŵili, Petulo na Yohane, kuti akapemphelele okhulupilila atsopano a kumeneko n’colinga cakuti alandile mzimu woyela. (Mac. 8:5, 14-17) Ndithudi, Filipo pamodzi na okhulupilila atsopanowo analimbikitsiwa ngako na thandizo limeneli locokela kwa abale a m’bungwe lolamulila! Masiku ano, Bungwe Lolamulila la Mboni za Yehova limapeleka cilimbikitso kwa atumiki a pa Beteli, atumiki ena a nthawi zonse apadela, na ku gulu lonse la abale padziko lapansi. Ndipo mofanana ndi m’nthawi ya atumwi, timakondwela na cilimbikitso cimeneci. Kuwonjezela apo, mu 2015 Bungwe Lolamulila linafalitsa kabuku kakuti Bwelelani kwa Yehova. Kabuku kameneka kakhala kolimbikitsa kwambili kwa abale na alongo oculuka pa dziko lonse. w18.04 19 ¶18-20

Cisanu, May 8

Mudzadziŵa coonadi, ndipo coonadi cidzakumasulani.—Yoh. 8:32.

Anthu ena amaganiza kuti kukhala na ufulu woculuka n’kumene kungawathandize kukhala na umoyo wabwino. Koma zoona zake n’zakuti kukhala na ufulu wopanda malile kumabweletsa mavuto. Ganizani cabe mmene zinthu zikanaipila pa dzikoli pakanakhala popanda malamulo aliwonse. M’pake kuti buku lakuti The World Book Encyclopedia limati: “Malamulo a m’dziko lililonse amapanga msakanizo wovuta kumvetsa wa maufulu ambili na ziletso zake.” Ndithudi, mawu akuti “wovuta kumvetsa” ndi oyenelela. Tangoganizilani cabe za mabuku masauzande-masauzande a zamalamulo amene anthu alemba, komanso maloya na oweluza ambili-mbili amene nchito yawo ni kufotokoza tanthauzo la malamulowo na kuonetsetsa kuti akutsatilidwa. Malinga n’zimene Yesu anakamba, pali zinthu ziŵili zimene tifunika kucita kuti tidzapeze ufulu weni-weni: Coyamba, kuphunzila coonadi cimene iye anaphunzitsa, ndipo caciŵili, kukhala wophunzila wake. Kucita izi kudzatithandiza kukapeza ufulu weni-weni. Ufulu womasuka ku ciani? Yesu anati: “Aliyense wocita chimo ndi kapolo wa chimo. . . . Ngati Mwana wakumasulani, mudzakhaladi omasuka.”—Yoh. 8:34, 36. w18.04 6-7 ¶13-14

Ciŵelu, May 9

Nonsenu mukhale . . . omvelana cisoni.—1 Pet. 3:8.

Timakondwela kukhala ndi anthu amene amatimvelela cifundo na kutidela nkhawa. Anthu acifundo amayesetsa kuzindikila zimene tikuganiza na mmene tikumvelela. Amayesetsanso kuganizila zosoŵa zathu, ndipo amatithandiza, mwina tisanapemphe thandizo n’komwe. Anthu amene ‘amatimvelela cisoni,’ timawakonda na kuwayamikila. Pokhala Akhristu, timafuna kuonetsa kuti timamvelela ena cifundo. Koma kucita zimenezi nthawi zina kumakhala kovuta. Cifukwa ciani? Cifukwa coyamba n’cakuti ndife anthu opanda ungwilo. (Aroma 3:23) Timakonda kuganizila zofuna zathu cabe. Conco, pamafunika khama kuti tizicita zinthu moganizila ena. Komanso, ena a ife zimativuta kumvelela ena cifundo cifukwa ca mmene tinakulila, kapena cifukwa ca zokumana nazo mu umoyo. Cinanso, tingayambe kutengela khalidwe la anthu amene tikhala nawo. Masiku otsiliza ano, anthu ambili saganizila anzawo. Ndipo ni “odzikonda.” (2 Tim. 3:1, 2) Komabe, tingakulitse khalidwe la cifundo mwa kutengela citsanzo ca Yehova Mulungu na Mwana wake, Yesu Khristu. w19.03 14 ¶1-3

Sondo, May 10

Uteteze mtima wako.—Miy. 4:23.

Lamulo lotsiliza pa Malamulo Khumi linali kuletsa kusilila mwansanje, kapena kuti kukhumbila cinthu ca mwini mosayenela. (Deut. 5:21; Aroma 7:7) Yehova anapeleka lamulo limeneli pofuna kuphunzitsa anthu ake mfundo yofunika. Iwo anafunika kuteteza mtima wawo, kutanthauza kupewa maganizo oipa na zilako-lako zosayenela. Yehova adziŵa kuti maganizo na zilako-lako zosayenela, n’zimene zimapangitsa munthu kucita zoipa. Zaconco n’zimene zinagwetsela Mfumu Davide m’chimo. Iye anali munthu wabwino. Koma panthawi ina, anakhumbila mkazi wa mwini. Cilako-lako cake cinabala chimo. (Yak. 1:14, 15) Davide anacita cigololo na mkaziyo, kenako anayesa kupusitsa mwamuna wake, ndipo pamapeto pake anamuphetsa mwamunayo. (2 Sam. 11:2-4; 12:7-11)Yehova saona cabe maonekedwe akunja a munthu. Koma amaonanso zimene zili mu mtima. (1 Sam. 16:7) Iye amaona zonse zimene timacita, kuganiza na kulaka-laka. Amayang’ana zabwino mwa ife, ndipo amatilimbikitsa kupitiliza kucita zabwino. Iye amafuna kuti maganizo oipa akabwela mu mtima mwathu, tiziwacotsa mwamsanga kuti asatigwetsele m’chimo.—2 Mbiri 16:9; Mat. 5:27-30. w19.02 21 ¶9; 22 ¶11

Mande, May 11

Bwelani kwa Yehova, inu nonse ofatsa a padziko lapansi . . . yesetsani kukhala ofatsa.—Zef. 2:3.

Baibo imakamba kuti Mose anali “munthu wofatsa kwambili kuposa anthu onse amene anali padziko lapansi.” (Num. 12:3) Kodi izi zitanthauza kuti anali wofooka, wamantha popanga zosankha, kapena woopa anthu? Ena amaganiza kuti umu ni mmene anthu ofatsa amakhalila. Koma zimenezi si zoona. Mose anali mtumiki wa Mulungu wolimba mtima, wamphamvu, komanso wosazengeleza pocita zinthu. Mwacitsanzo, na thandizo la Yehova, anayang’anizana na mfumu yamphamvu ya Iguputo. Komanso, anatsogolela Aisiraeli mwina okwana 3,000,000 kudutsa m’cipululu, na kuwathandiza kugonjetsa adani awo. Masiku ano, sitikumana na mavuto monga amene Mose anakumana nawo. Koma tsiku lililonse, timakumana ndi anthu ovuta, kapena zocitika zimene zingapangitse kuti cikhale covutilapo kukhala ofatsa. Ngakhale n’conco, pali cifukwa comveka cimene ciyenela kutilimbikitsa kuyesetsa kukhala ofatsa. Cifukwa cake n’cakuti Yehova walonjeza kuti “ofatsa adzalandila dziko lapansi.” (Sal. 37:11) Kodi inu mumadziona kuti ndinu wofatsa? Kodi umu ni mmenenso anthu ena amakuonelani? w19.02 8 ¶1-2

Ciŵili, May 12

Tsoka kwa amene akunena kuti cabwino n’coipa.—Yes. 5:20.

Anthu analengedwa na cikumbumtima kungoyambila pamene anthu analengedwa pa dziko lapansi. Mwacitsanzo, pamene Adamu na Hava anaphwanya lamulo la Yehova, anathaŵa n’kukabisala. Izi zionetsa kuti cikumbumtima cawo cinali kuwavutitsa. Anthu amene ali na cikumbumtima cosaphunzitsidwa bwino ali monga sitima ya pamadzi imene ili na kampasi yosaseŵenza bwino. Kuyenda pa sitima yaconco kungapangitse kuti ticite ngozi. Zili conco, cifukwa mphepo na mafunde a m’nyanja zingacititse kuti sitimayo iyambe kuyenda njila yolakwika. Koma kampasi yoseŵenza bwino ingathandize woyendetsa kudziŵa kumene afunika kuloŵela. Cikumbumtima cathu tingaciyelekezele na kampasi. Cikumbumtima ni mphamvu yacibadwa imene imatithandiza kuzindikila cabwino na coipa na kutitsogolela m’njila yoyenela. Koma kuti cikumbumtima cizititsogolela bwino, tifunika kuciphunzitsa. Ngati cikumbumtima ca munthu si cophunzitsidwa bwino, sicingamuletse kucita zoipa. (1 Tim. 4:1, 2) Cikumbumtima caconco cingaticititse kuona ngati “coipa n’cabwino.” w18.06 16-17 ¶1-3

Citatu, May 13

Musamatengele nzelu za nthawi ino.—Aroma. 12:2.

Tifunika kuzindikila na kukana mfundo za dziko zimene zimafalitsidwa m’njila zovutilapo kuzizindikila. Mwacitsanzo, tingamvetsele nyuzi pa wailesi kapena pa TV, yoonetsa kuti mfundo zinazake zandale n’zabwino. Kapena tingamvetsele nkhani imene colinga cake n’kulimbikitsa anthu kuona kuti zolinga za anthu komanso zocita zawo n’zothandiza komanso n’zabwino. Palinso mabuku na mafilimu ena amene amalimbikitsa anthu kuona kuti kuika zofuna zawo kapena za banja lawo patsogolo pa zonse n’kwabwino. Koma kucita izi n’kosagwilizana na mfundo za m’Baibo. Malemba amaonetsa kuti munthu amafunika kukonda Yehova kuposa zonse kuti akhale na umoyo wabwino komanso banja lacimwemwe. (Mat. 22:36-39) Koma izi sizitanthauza kuti kucita zosangalatsa zoyenela n’kulakwa. Ngakhale n’conco, ni bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi nimakwanitsa kuzindikila mfundo za dziko ngakhale pamene zikufalitsidwa m’njila yovutilapo kuizindikila? Kodi nimapewa kumvetsela mapulogilamu kapena kuŵelenga mabuku na zinthu zina zosayenela? Kodi nimayesetsa kuthandizanso ana anga kupewa zimenezi? Ngati ana anga amva kapena kuona zinthu zolakwika, kodi nimayesetsa kuwongolela maganizo awo mwa kuwaphunzitsa mmene Yehova amaonela zinthu?’ w18.11 21-22 ¶18-19

Cinayi, May 14

Usacite mantha, pakuti ndili nawe.—Yes. 41:10.

Yehova amaonetsa kuti ali nafe mwa kutisamalila na kutikonda. Onani zimene iye anakamba poonetsa kuti amatikonda kwambili. Anati: “Ndiwe wamtengo wapatali kwa ine, ndimakulemekeza ndipo ndimakukonda.” (Yes. 43:4) Palibe ciliconse m’cilengedwe cimene cingapangitse Yehova kuleka kukonda atumiki ake. Iye amacita nafe zinthu mokhulupilika kwambili. (Yes. 54:10) Yehova amalola kuti tikumane na mavuto. Komabe, iye watilonjeza kuti sadzalola kuti tikokoloke, kapena kuti kugonjetsedwa na mavuto okhala ngati “mitsinje.” Walonjezanso kuti sadzalola mayeselo onga “laŵi la moto” kutiwononga kothelatu. Iye watitsimikizila kuti adzakhala nafe, na kutithandiza kupilila mavuto na mayeselo. Kodi Yehova adzatithandiza bwanji? Adzatithandiza kukhala olimba mtima, n’colinga cakuti tikhalebe okhulupilika kwa iye, olo pamene tayang’anizana na imfa. (Yes. 41:13; 43:2) Ngati tikhulupilila lonjezo la Mulungu lakuti: “Ndili nawe,” na ife tidzakhala olimba pokumana na mayeselo. w19.01 3 ¶4-6

Cisanu, May 15

Mumtima mwa munthu mumakhala zolinga zambili, koma zolinga za Yehova n’zimene zidzakwanilitsidwe.—Miy. 19:21.

Ngati ndimwe wacicepele, mwina matica kapena anthu ena, amakulimbikitsani kucita maphunzilo apamwamba kuti mukapeze nchito ya ndalama zambili. Koma Yehova amakulimbikitsani kukhala na zolinga zosiyana na zimenezi. Iye amafuna kuti muzicita khama pa maphunzilo anu kuti mukadzatsiliza sukulu, mudzakwanitse kudzisamalila mwekha. (Akol. 3:23) Koma posankha zinthu zofunika kuika patsogolo mu umoyo wanu, Yehova amafuna kuti muzitsogoleledwa na mfundo zake zothandiza, zimene n’zogwilizana na colinga cake kwa ise masiku ano otsiliza.(Mat. 24:14) Yehova amadziŵa zimene zidzacitika pa dzikoli, ngakhale nthawi yeni-yeni imene lidzawonongedwa. (Yes. 46:10; Mat. 24:3, 36) Cinanso, Yehova ndiye amatidziŵa bwino. Amadziŵa zimene zingatithandize kukhala acimwemwe ndi okhutila, komanso zimene zingatibweletsele mavuto na kutilanda cimwemwe. Conco, olo malangizo ocokela kwa anthu ataoneka monga anzelu kwambili, sakhala othandiza ngati sagwilizana na Mawu a Mulungu. w18.12 19 ¶1-2

Ciŵelu, May 16

Woipa sadzakhalakonso. —Sal. 37:10.

“Ofatsa adzalandila dziko lapansi; nadzakondwela nawo mtendele woculuka.” Davide anauzilidwanso kulemba kuti: “Olungama adzalandila dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.” (Sal. 37:11, 29; 2 Sam. 23:2) Kodi muganiza kuti malonjezo amenewa anawalimbikitsa bwanji anthu amene anali kucita cifunilo ca Mulungu? Izi zinawapatsa ciyembekezo cakuti padziko lapansi pakadzakhala anthu olungama okha-okha, ndiye kuti dziko lidzakhala paradaiso monga mmene munda wa Edeni unalili. M’kupita kwa nthawi, Aisiraeli ambili analeka kulambila Yehova na kum’tumikila. Conco, Mulungu analola Ababulo kugonjetsa anthu ake, kuwononga dziko lawo, na kutenga ambili a iwo kupita nawo ku ukapolo. (2 Mbiri 36:15-21; Yer. 4:22-27) Komabe, aneneli a Mulungu anakambilatu kuti pambuyo pa zaka 70, anthu ake adzabwelela ku dziko lawo. Maulosi amene aneneliwo anakamba anakwanilitsika. Koma alinso na tanthauzo kwa ise masiku ano. Kutsogolo dziko lapansi lidzakhala paradaiso. w18.12 4-5 ¶9-10

Sondo, May 17

Monga momwe kumwamba kulili pamwamba kuposa dziko lapansi, momwemonso njila zanga n’zapamwamba kuposa njila zanu, ndiponso maganizo anga ndi apamwamba kuposa maganizo anu. —Yes. 55:9.

Ambili mwa malangizo a m’dzikoli ni osagwilizana na Malemba ngakhale pang’ono. Koma kodi malangizowo angakhale othandiza kulingana ndi nthawi imene tikukhalamo ? Yesu anati: “Nzelu imatsimikizilika kuti ndi yolungama cifukwa ca nchito zake.” (Mat. 11:19) Dzikoli lapita patsogolo kwambili pa zasayansi. Koma lakangiwa kuthetsa mavuto aakulu amene alanda anthu cimwemwe—mavuto monga nkhondo, kusankhana mitundu, na upandu. Nanga bwanji za kulekelela khalidwe la ciwelewele? Anthu ambili amavomeleza kuti kulekelela khalidweli kwawonjezela mavuto monga kusila kwa vikwati, matenda, na mavuto ena. Koma Akhristu oona pa dziko lonse, amene amayendela maganizo a Mulungu, amakhala na mabanja abwino, umoyo wathanzi, na mtendele pakati pawo. (Yes. 2:4; Mac. 10:34, 35; 1 Akor. 6:9-11) Kodi uwu si umboni wakuti maganizo a Yehova ni apamwamba kuposa maganizo a dziko? w18.11 20 ¶8-10

Mande, May 18

Kugwilizana ndi anthu oipa kumawononga makhalidwe abwino.—1 Akor. 15:33.

Timayesetsa kukhala bwino na abululu athu, komanso kucita nawo zinthu mokoma mtima. Komabe, tifunika kukhala osamala kuti tisanyalanyaze mfundo za coonadi pofuna kuwakondweletsa. Tifunika kupitiliza kucita zimene tingathe kuti tizikhala mwamtendele na abululu athu. Koma tiyenela kupanga ubwenzi wathithithi ndi anthu amene amakonda Yehova. Anthu onse amene amayenda m’coonadi afunika kukhala oyela. (Yes. 35:8; 1 Pet. 1:14-16) Pamene tinaphunzila coonadi, ise tonse tinasintha makhalidwe athu na kuyamba kutsatila mfundo zolungama za m’Baibo. Ena anali na makhalidwe oipa kwambili, koma anasintha. Mosasamala kanthu kuti tinali na khalidwe lotani tisanaphunzile coonadi, sitiyenela kusinthanitsa khalidwe loyela limene tili nalo na makhalidwe onyansa a m’dzikoli. Kodi tingapewe bwanji makhalidwe oipa? Tizikumbukila kuti pofuna kutithandiza kukhala oyela, Yehova anapeleka nsembe yamtengo wapatali kwambili, imene ni magazi a Mwana wake, Yesu Khristu. (1 Pet. 1:18, 19) Conco, kuti tikhalebe oyela pa maso pa Yehova, nthawi zonse tizikumbukila nsembe yamtengo wapatali ya dipo la Yesu. w18.11 11 ¶10-11

Ciŵili, May 19

Ndidzayembekezela moleza mtima Mulungu wa cipulumutso canga. Mulungu wanga adzandimvela.—Mika 7:7.

Atumiki ambili a nthawi zonse angavomeleze kuti kuikabe mtima wawo pa nchito yolalikila kwawathandiza kukhalabe olimba ngakhale pamene zinthu zasintha mu umoyo wawo. Monga mmene citsanzo cawo cionetsela, ngati ticita zonse zotheka malinga na mmene zinthu zilili mu umoyo wathu, komanso ngati tiyembekezela Yehova mwacidalilo, tidzakhalabe na mtendele wa mu mtima. Ndipo ngati tiikabe zauzimu patsogolo pamene zinthu zasintha mu umoyo wathu, ubwenzi wathu na Yehova ungalimbileko. Nthawi zina, zinthu mu umoyo zingasinthe mosayembekezeleka, mwina cifukwa ca kusintha kwa utumiki, matenda, kapena maudindo atsopano a m’banja. Zikakhala conco, musakayikile kuti Yehova amakukondani, ndipo adzakuthandizani pamene mufunika thandizo. (Aheb. 4:16; 1 Pet. 5:6, 7) Conco pali pano, muzicita zonse zimene mungathe malinga na mmene zinthu zilili mu umoyo wanu. Komanso muziyandikila Atate wanu wakumwamba m’pemphelo, ndipo phunzilani kum’dalila na mtima wonse cifukwa iye amakukondani. Mukatelo, mudzakhalabe na mtendele wa mu mtima olo pamene zinthu zasintha mu umoyo wanu. w18.10 30 ¶17; 31 ¶19, 22

Citatu, May 20

[Yehova] akudziŵa bwino mmene anatiumbila, amakumbukila kuti ndife fumbi.—Sal. 103:14.

M’Baibo muli zitsanzo zambili zoonetsa kuti Yehova amacita zinthu moganizila atumiki ake. Mwacitsanzo, onani mmene Mulungu anathandizila Samueli wacicepele kupeleka uthenga waciweluzo kwa Mkulu wa Ansembe Eli, monga mmene 1 Samueli 3:1-18 ionetsela. M’Cilamulo ca Yehova, munali lamulo lakuti ana afunika kumalemekeza acikulile, maka-maka atsogoleli. (Eks. 22:28; Lev. 19:32) Kodi muganiza kuti Samueli akanalimba mtima kupita kwa Eli m’maŵa kukamuuza uthenga woŵaŵa waciweluzo wocokela kwa Mulungu? Mwacionekele, yankho ni yakuti iyai. Ndipo Baibo imakamba kuti Samueli “anaopa kuuza Eli za masomphenya amene anaona.” Komabe, Mulungu anapangitsa Eli kuzindikila kuti Iye ndiye anali kuitana Samueli. Izi zinasonkhezela Eli kulamula Samueli kuti amufotokozele za masomphenyawo mosabisa “ngakhale mawu amodzi.” Samueli anamvela, ndipo “anamuuza mawu onse” Ndipo mawuwo anagwilizana na uthenga woyamba. (1 Sam. 2:27-36) Nkhani imeneyi ya Samueli na Eli ionetsa kuti Yehova ni wanzelu komanso woganizila ena kwambili. w18.09 23 ¶2; 24 ¶4-5

Cinayi, May 21

Inu Yehova, ndani amene angakhale mlendo m’cihema canu?. . . Ndi amene. . . amalankhula zoona mumtima mwake.—Sal. 15:1, 2.

Masiku ano, anthu ambili amakonda kukamba mabodza. Nkhani yakuti “Cifukwa Cake Timanama,” ya m’magazini yochedwa National Geographic inati: “Kunama kwakhala khalidwe lozika mizu kwambili pakati pa anthu.” Anthu amakonda kunama kuti adziteteze kapena kuti adzichukitse. Ena amanama kuti abise zolakwa zawo, kapena kuti apeze ndalama, nchito, kapena zinthu zina zimene afuna. Malinga n’zimene nkhaniyo inakamba, anthu “amakonda kunama pa zinthu zazing’ono kapena zazikulu, kwa anthu osawadziŵa, kapena kwa anzawo a ku nchito, kwa mabwenzi, kapena kwa okondedwa awo.” Kodi khalidwe la kunama labweletsa mavuto anji? Anthu amayamba kukayikilana, ndipo ubwenzi umasokonezeka. Popemphela kwa Yehova, wamasalimo Davide anati: “Mumakondwela ndi coonadi cocokela pansi pa mtima.” (Sal. 51:6) Davide anadziŵa kuti kukamba zoona kumadalila zimene zili mu mtima mwa munthu. Ndipo Akhristu oona, pa mbali iliyonse ya umoyo wawo, ‘amalankhulana zoona zokha-zokha.’—Zek. 8:16. w18.10 7 ¶4; 8 ¶9-10; 10 ¶19

Cisanu, May 22

Anapitiliza kuwatsogolela ndi kuwateteza ndipo iwo sanacite mantha.—Sal. 78:53.

Pamene Aisiraeli anali kutuluka mu Iguputo mu 1513 B.C.E., mwina ciŵelengelo cawo cinali kupitilila 3 miliyoni. Pa khamulo, panali anthu a mibadwo yosiyana-siyana. Panali ana, okalamba, komanso odwala kapena olemala. Panali kufunikadi Mtsogoleli woganizila ena kuti akwanitse kutsogolela bwino khamu limenelo potuluka mu Iguputo. Ndipo Yehova, kupitila mwa Mose, anaonetsadi kuti anali Mtsogoleli woyenelela. Ndiye cifukwa cake Aisiraeli anali kudzimva otetezeka pamene anali kutuluka mu Iguputo, dziko limene linali ngati ndiye kwawo. (Sal. 78:52) Kodi Yehova anacita ciani kuti anthuwo aone kuti ni otetezeka? Powatulutsa mu Iguputo, anaonetsetsa kuti akuyenda mwadongosolo. Baibo imati anayenda “mwa dongosolo lomenyela nkhondo.” (Eks. 13:18) Dongosolo limenelo linathandiza Aisiraeli kutsimikizila kuti Mulungu wawo anali kuwatsogolela. Cinanso, Yehova anaika zizindikilo zoonetsa kuti anali nawo. Anaika “mtambo masana” na “kuwala kwa moto” usiku. (Sal. 78:14) Zinali monga Yehova akuwauza kuti: “Musaope. Nili na imwe. Nidzakutsogolelani na kukutetezani.” w18.09 26 ¶11-12

Ciŵelu, May 23

Zikanakhala bwino mukanandibisa m’Manda, . . . mukanati mundiikile nthawi n’kudzandikumbukila.—Yobu 14:13.

M’nthawi yakale, atumiki ena okhulupilika a Mulungu anathedwa nzelu cifukwa ca mavuto awo, cakuti anafika polaka-laka kufa cabe. Mwacitsanzo, pamene mavuto ake anafika poipa kwambili, Yobu anati: “Moyo ndaukana, sindikufuna kukhala ndi moyo mpaka kalekale.” (Yobu 7:16) Komanso Yona, cifukwa cokhumudwa kwambili na mmene zinthu zinayendela pa nchito yake yolalikila, anakamba kuti: “Tsopano inu Yehova, cotsani moyo wanga, pakuti kuli bwino kuti ndife kusiyana n’kukhala ndi moyo.” (Yona 4:3) Pa nthawi ina, nayenso mneneli wokhulupilika Eliya anataya mtima cifukwa ca mavuto amene anakumana nawo, cakuti anapempha kuti afe. Iye anati: “Basi ndatopa nazo. Tsopano cotsani moyo wanga Yehova.” (1 Maf. 19:4) Koma Yehova anali kuwakonda kwambili atumiki ake odzipeleka amenewo, ndipo anali kufuna kuti akhalebe na moyo. Iye sanawaimbe mlandu cifukwa cokhala na maganizo ofuna kufa. M’malo mwake, anawathandiza kuthetsa maganizo amenewo na kuwalimbikitsa mwacikondi kuti apitilize kum’tumikila mokhulupilika. w18.09 13 ¶4

Sondo, May 24

Ndife anchito anzake a Mulungu.—1 Akor. 3:9.

Anchito anzake a Mulungu amadziŵika na khalidwe la kuceleza. M’Malemba Acigiriki Acikhristu, liwu lakuti “kuceleza” limatanthauza “kukomela mtima alendo.” (Aheb. 13:2) Mawu a Mulungu amafotokoza zocitika zosiyana-siyana zimene zimatiphunzitsa kuonetsa cikondi mwa kukhala oceleza. (Gen. 18:1-5) Tiyenela kuseŵenzetsa mpata uliwonse umene tapeza kuti tithandize ena, kaya ni “abale ndi alongo athu m’cikhulupililo” kapena ayi. (Agal. 6:10) Kodi mungaseŵenze na Mulungu mwa kuceleza atumiki a nthawi zonse amene abwela kudzacezela mpingo wanu? (3 Yoh. 5, 8) Kuceleza Akhristu amenewa kumatipatsa mwayi ‘wolimbikitsana mwa cikhulupililo.’ (Aroma 1:11, 12) Mawu a Mulungu amalimbikitsa amuna mu mpingo kuti ayenela kuseŵenza na Yehova mwa kukalamila maudindo na mautumiki ena m’gulu. (1 Tim. 3:1, 8, 9; 1 Pet. 5:2, 3) Abale amene amacita zimenezi ali na mtima wofuna kuthandiza ena mwauzimu, komanso pa mbali zina zofunikila. (Mac. 6:1-4) Abale amene amacita nchito za mu mpingo adzakuuzani kuti kuthandiza ena n’cinthu cokondweletsa ngako. w18.08 24 ¶6-7; 25 ¶10

Mande, May 25

Usadzudzule mwamuna wacikulile mokalipa, koma umudandaulile ngati bambo ako.—1 Tim. 5:1.

Olo kuti Timoteyo anali na mphamvu ya ulamulilo pa abale acikulile amenewo, anafunika kucita nawo zinthu mwacifundo komanso mwaulemu. Koma tifunika kusamala kuti tisatenge mfundo imeneyi molakwika. Mwacitsanzo, bwanji ngati Mkhristu wina wacikulile amacita chimo mwadala kapena amalimbikitsa ena kucita zinthu zimene Yehova amazonda? Kodi tiyenela kumulekelela? Iyai. Yehova sadzaweluza anthu poona maonekedwe awo akunja, komanso sadzalekelela munthu wocita macimo mwadala cifukwa cakuti ni wacikulile. Yesaya 65:20 imati: “Wocimwa, ngakhale ali ndi zaka 100, tembelelo lidzamugwela.” Mfundo yolingana na imeneyi inachulidwanso m’masomphenya amene Ezekieli anaona. (Ezek. 9:5-7) Conco, colinga cathu cacikulu ciyenela kukhala kulemekeza ‘Wamasiku Ambiliyo,’ Yehova Mulungu. (Dan. 7:9, 10, 13, 14) Ngati ticita izi, sitidzayopa kupeleka uphungu mwaulemu kwa munthu wofunikila thandizo, ngakhale kuti ni wacikulile.—Agal. 6:1. w18.08 11 ¶13-14

Ciŵili, May 26

Munthu amene sadziŵa zinthu amakhulupilila mawu alionse, koma wocenjela amaganizila za mmene akuyendela.—Miy. 14:15.

Pokhala Akhristu oona, tifunika kukulitsa luso lopenda mosamala zimene tamvela tisanazikhulupilile. (Miy. 3:21-23; 8:4, 5) Ngati tilibe luso limeneli, Satana na dziko lake angasokoneze kaganizidwe kathu mosavuta. (Aef. 5:6; Akol. 2:8) Ndipo ngati sitidziŵa zoona zeni-zeni pa nkhani inayake, tingayambe kukhulupilila mabodza. Masiku ano, timamvela nkhani zambili-mbili komanso zosiyana-siyana. Nkhanizo timazimvela pa mawebusaiti, pa TV, komanso m’njila zina zofalitsila nkhani. Anthu ena amamvelanso nkhani zambili pa imelo, mameseji, kapena kwa anzawo. Koma popeza kuti anthu amakonda kufalitsa nkhani zabodza komanso zosoceletsa, tifunika kukhala osamala. Tiyenela kumapenda mosamala zimene tamvela kuti tidziŵe ngati n’zoona. w18.08 3 ¶1, 3

Citatu, May 27

Mulungu wakukomela mtima.—Luka 1:30.

Pamene nthawi inafika yakuti Mwana wa Mulungu abadwe monga munthu, Yehova anasankha namwali wodzicepetsa Mariya, kuti adzakhale mayi wa mwana wapadela ameneyu. Mariya anali kukhala mu mzinda waung’ono wa Nazareti, kutali na Yerusalemu na kacisi wake waulemelelo. (Luka 1:26-33) Patapita nthawi, zimene Mariya anakamba kwa wacibale wake Elizabeti zionetsa kuti anali munthu wauzimu kwambili. (Luka 1:46-55) Zoonadi, Yehova anali kuona zimene Mariya anali kucita, ndipo cifukwa ca kukhulupilika kwake anam’patsa mwayi wapadela umene sanali kuuyembekezela. Mariya atabeleka Yesu, Yehova sanapatse mtsogoleli aliyense wochuka kapena olamulila a mu Yerusalemu ndi Betelehemu mwayi wodziŵa za kubadwa kwa Yesu. Koma angelo anaonekela kwa abusa amene anali kuŵeta nkhosa kuchile, kunja kwa Betelehemu. (Luka 2:8-14) Kenako, abusawo anapita kukaona mwanayo. (Luka 2:15-17) Mariya na Yosefe ayenela kuti anakondwela kwambili kuona Yesu akulemekezedwa mwanjila imeneyi. w18.07 9-10 ¶11-12

Cinayi, May 28

Yehova anamukwiyila kwambili Solomo.—1 Maf. 11:9.

N’cifukwa ciani Yehova anamukwiyila kwambili Solomo? Baibo imati: “Cifukwa mtima wake unapatuka kwa Yehova. . . , amene anamuonekela kaŵili konse. Pa nkhani imeneyi, Mulungu anali atamulamula kuti asatsatile milungu ina, koma iye sanasunge zimene Yehova analamula.” Pamapeto pake, Mulungu analeka kumuyanja na kum’cilikiza. Komanso iye atafa, ufumu wa Isiraeli unagaŵikana moti mafumu obwela pambuyo pake anakumana na mavuto ambili kwa zaka zoculuka. (1 Maf. 11:9-13) Molingana ndi zimene zinacitikila Solomo, vuto limodzi lalikulu limene lingaike umoyo wathu wauzimu paciopsezo ni kukhala pa ubwenzi ndi anthu amene sadziŵa kapena kulemekeza miyezo ya Yehova. Ena angakhale kuti amagwilizana na mpingo, koma ni ofooka mwauzimu. Enanso angakhale acibululu, maneba, ndiponso anzathu a kunchito kapena akusukulu amene salambila Yehova. Kaya mabwenzi athu ni a mumpingo kapena ayi, ngati iwo salemekeza miyezo ya Yehova, m’kupita kwa nthawi angaticititse kuwononga ubwenzi wathu na Mulungu. w18.07 19 ¶9-10

Cisanu, May 29

Dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.—1 Yoh. 5:19.

Satana amaseŵenzetsa mafilimu na mapulogalamu a pa TV pofuna kufalitsa maganizo ake. Iye amadziŵa kuti nkhani zopeka zimakondweletsa, ndipo zili na mphamvu yosonkhezela maganizo a munthu, zocita zake, komanso mmene amamvelela. Yesu anali kuseŵenzetsa tunkhani topeka kapena kuti mafanizo pophunzitsa mwaluso. Mwacitsanzo, iye anapeleka fanizo la Msamariya wacifundo, komanso la mwana woloŵelela. (Mat. 13:34; Luka 10:29-37; 15:11-32) Koma anthu amene amatengela maganizo a Satana angaseŵenzetse nkhani zopeka pofuna kutisoceletsa. Conco, tifunika kukhala oganiza bwino. Mafilimu na mapulogalamu ena a pa TV angatiphunzitse na kutisangalatsa popanda kuipitsa maganizo athu. Koma tifunika kukhala osamala. Posankha zosangalatsa, tingacite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi filimu kapena pulogalamu iyi ya pa TV imaonetsa kuti kutsatila zilako-lako za thupi kulibe vuto?’ (Agal. 5:19-21; Aef. 2:1-3) Nanga mungacite ciani ngati mwaona kuti pulogilamuyo imalimbikitsa maganizo a Satana? Ipeweni mmene mungapewele matenda oyambukila! w19.01 15-16 ¶6-7

Ciŵelu, May 30

Landilani cisoti colimba cacipulumutso.—Aef. 6:17.

Monga mmene cisoti cimatetezela mutu na ubongo wa msilikali, “ciyembekezo cacipulumutso” cimateteza maganizo athu, na kutithandiza kuti tiziganiza bwino. (1 Ates. 5:8; Miy. 3:21) Kodi Satana angatipangitse bwanji kuvula cisoti cathu? Ganizilani zimene iye anacita kwa Yesu. Satana anali kudziŵa kuti Yesu anali na ciyembekezo cokakhala mfumu yolamulila mtundu wa anthu. Koma Yesu anafunika kuyembekezela mpaka pa nthawi yoikika ya Yehova. Ndipo akalibe kukhala mfumu, iye anafunika kukumana na mavuto na kuphedwa. Koma Satana anapatsa Yesu mwayi wakuti angakhale mfumu mwamsanga nthawi ya Yehova isanakwane. Iye anauza Yesu kuti akamulambila kamodzi kokha cabe, adzakhala mfumu pa nthawi imeneyo. (Luka 4:5-7) Mofananamo, Satana amadziŵa kuti Yehova analonjeza kuti adzatipatsa zinthu zambili zabwino m’dziko latsopano. Koma tifunika kuziyembekezela, ndipo pali pano tikhoza kukumana na mavuto ambili. Conco, Satana amatiyesa mwa kutipatsa mwayi wakuti tikhale na zinthu zambili zakuthupi pa nthawi ino. Iye amafuna kuti tizifuna-funa zinthu zakuthupi coyamba, pofuna kudzipezela umoyo wabwino. Satana amafuna kuti tiziika zinthu za Ufumu pa malo aciŵili mu umoyo wathu.—Mat. 6:31-33. w18.05 30-31 ¶15-17

Sondo, May 31

Mtima wako ukusangalatse masiku a unyamata wako.—Mlal. 11:9.

Ndithudi, Yehova amafuna kuti imwe acicepele muzikhala acimwemwe. Muziika zolinga zauzimu patsogolo ndipo muzidalila Yehova pa zocita zanu zonse. Ngati mwayamba kucita izi mukali wamng’ono, sipatenga nthawi itali kuti muone kuti Yehova akukutsogolelani, kukutetezani, na kukudalitsani. Muziganizila na kutsatila malangizo opezeka m’Mawu ake. Mukatelo, ndiye kuti ‘mukukumbukila Mlengi wanu Wamkulu masiku a unyamata wanu.’ (Mlal. 12:1) Imwe acicepele acikhristu timakuyamikilani ngako cifukwa mukupitiliza kuika mtima wanu wonse pa kutumikila Yehova. Mumacita izi mwa kuyesetsa kukwanilitsa zolinga zanu zauzimu ndi kuika nchito yolalikila patsogolo mu umoyo wanu. Kuwonjezela apo, mumayesetsa kupewa kutangwanika na zinthu za m’dzikoli. Imwe acicepele, dziŵani kuti zonse zimene mumacita sizidzapita pacabe. Muli na abale na alongo acikondi amene amakucilikizani. Ndipo ngati mudalila Yehova, zolinga zanu zidzakwanilitsika. w18.04 29 ¶17, 19

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani