LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • es20 masa. 57-67
  • June

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • June
  • Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2020
  • Tumitu
  • Mande, June 1
  • Ciŵili, June 2
  • Citatu, June 3
  • Cinayi, June 4
  • Cisanu, June 5
  • Ciŵelu, June 6
  • Sondo, June 7
  • Mande, June 8
  • Ciŵili, June 9
  • Citatu, June 10
  • Cinayi, June 11
  • Cisanu, June 12
  • Ciŵelu, June 13
  • Sondo, June 14
  • Mande, June 15
  • Ciŵili, June 16
  • Citatu, June 17
  • Cinayi, June 18
  • Cisanu, June 19
  • Ciŵelu, June 20
  • Sondo, June 21
  • Mande, June 22
  • Ciŵili, June 23
  • Citatu, June 24
  • Cinayi, June 25
  • Cisanu, June 26
  • Ciŵelu, June 27
  • Sondo, June 28
  • Mande, June 29
  • Ciŵili, June 30
Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2020
es20 masa. 57-67

June

Mande, June 1

Ciliconse cimene mungapemphe Atate m’dzina langaakupatseni.—Yoh. 15:16.

Mwacionekele, mawu amenewa anawalimbikitsa ngako atumwi. Pa nthawiyo, Mtsogoleli wawo Khristu anali atatsala pang’ono kuphedwa, koma iwo sanali kumvetsetsa zimenezi. Olo zinali conco, atumwiwo sakanasiyidwa opanda thandizo lililonse. Yehova anali wokonzeka kuyankha mapemphelo awo, na kuwapatsa thandizo lililonse lofunikila kuti akwanitse kugwila nchito yolalikila uthenga wa Ufumu imene anapatsiwa. Ndipo mogwilizana ndi mawu a Yesu, posapita nthawi, iwo anadzionela okha mmene Yehova anayankhila mapemphelo awo. (Mac. 4:29, 31) Ni mmenenso zilili masiku ano. Pamene tipitiliza kubala zipatso mopilila, timakhala pa ubwenzi na Yesu. Komanso, timakhulupilila kuti Yehova ni wokonzeka kuyankha mapemphelo athu tikamupempha kuti atithandize kupilila mavuto aliwonse amene tingakumane nawo polalikila uthenga wabwino wa Ufumu. (Afil. 4:13) Kukamba zoona, ndise oyamikila ngako kuti mapemphelo athu amayankhidwa, komanso kuti tili na mwayi wokhala pa ubwenzi na Yesu. Mphatso zimenezi zocokela kwa Yehova zimatilimbikitsa kupitiliza kubala zipatso.—Yak. 1:17. w18.05 21 ¶17-18

Ciŵili, June 2

Tiyeni tilimbikitsane, ndipo tiwonjezele kucita zimenezi, makamaka pamene mukuona kuti tsikulo likuyandikila.—Aheb. 10:24, 25.

Panali patatsala zaka 5 cabe kuti Akhristu aciyuda okhala mu Yerusalemu aone cizindikilo cimene Yesu anawapatsa coonetsa kuti “tsiku . . la Yehova” layandikila, ndipo anafunika kuthaŵa mu mzindawo kuti apulumutse miyoyo yawo. (Mac. 2:19, 20; Luka 21:20-22) Tsiku la Yehova limenelo linafika mu 70 C.E. pamene Aroma anawononga Yerusalemu mogwilizana na ciweluzo ca Yehova. Masiku ano, tili na cifukwa comveka cokhulupilila kuti ‘tsiku la Yehova lalikulu ndi locititsa mantha’ lili pafupi. (Yow. 2:11) Mneneli Zefaniya anati: “Tsiku lalikulu la Yehova lili pafupi. Lili pafupi ndipo likubwela mofulumila kwambili.” (Zef. 1:14) Mawu aulosi ocenjeza amenewa akhudzanso ise masiku ano. Popeza kuti tsiku la Yehova layandikila, Paulo anatilangiza kuti, “tiganizilane kuti tilimbikitsane pa cikondi ndi nchito zabwino.” (Aheb. 10:24) Conco, tiyenela kumaganizila kwambili za umoyo wa abale na alongo athu kuti tiwalimbikitse pamene kuli kofunikila. w18.04 20 ¶1-2

Citatu, June 3

Ukhale wolimba mtima ndipo ucite zinthu mwamphamvu. Usacite mantha kapena kuopa, pakuti Yehova Mulungu wako ali nawe kulikonse kumene upiteko.—Yos. 1:9.

Yehova analimbikitsa Yoswa asanayambe kutsogolela anthu ake kuloŵa m’Dziko Lolonjezedwa! Yehova sanangolimbikitsa anthu ake aliyense payekha-payekha, koma anawalimbikitsanso onse monga gulu. Mwacitsanzo, Yehova anakamba mawu aulosi amene analimbikitsa Ayuda amene anali mu ukapolo ku Babulo. Anati: “Usacite mantha, pakuti ndili nawe. Usayang’ane uku ndi uku mwamantha, pakuti ine ndine Mulungu wako. Ndikulimbitsa. Ndithu ndikuthandiza. Ndikugwila mwamphamvu ndi dzanja langa lamanja lacilungamo.” (Yes. 41:10) Nawonso Akhristu oyambilila anali kudziŵa kuti Mulungu amatilimbikitsa. Iye amacita cimodzi-modzi kwa ise masiku ano (2 Akor. 1:3, 4) Ngakhale Yesu nayenso analimbikitsiwa na Atate wake. Pa ubatizo wake, Yesu anamvela mawu ocokela kumwamba akuti: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, amene ndimakondwela naye.” (Mat. 3:17) Mawu amenewa ayenela kuti anamulimbikitsa ngako Yesu pa utumiki wake wonse wa pa dziko lapansi. w18.04 16 ¶3-5

Cinayi, June 4

Usadye zipatso za mtengo wodziŵitsa cabwino ndi coipa.—Gen. 2:17.

Anthu ambili masiku ano akaŵelenga lamulo limene Yehova anapatsa Adamu, amaona kuti Adamu anamanidwa ufulu wocita zofuna zake. Koma iwo amaiŵala kuti olo kuti anthufe tili na ufulu wosankha zocita, sitinalengedwe na udindo wodziikila tekha miyezo ya cabwino na coipa. Adamu na Hava anali na ufulu wosankha kumvela Mulungu kapena kusamumvela. Komabe, Yehova yekha ndiye ali na udindo wodziŵitsa anthu cabwino na coipa, ndipo “mtengo wodziŵitsa cabwino ndi coipa,” umene unali m’munda wa Edeni, unali kuimila udindo wake umenewu. (Gen. 2:9) Conco, pamene Yehova anapatsa Adamu na Hava lamulo, anali kuwaphunzitsa njila yokhalila na ufulu weni-weni. Makolo athu oyambilila anasankha kusamvela Mulungu. Kodi zimene Adamu na Hava anasankha kucita zinawawonjezela ufulu? Iyai. Cifukwa cokana kutsogoleledwa na Mulungu, iwo anataya ufulu weni-weni umene anali nawo poyamba. w18.04 5-6 ¶9-12

Cisanu, June 5

Pamene iwo anali kuvutika m’masautso awo onse, iyenso anali kuvutika.—Yes. 63:9.

Kuphatikiza pomvelela cifundo atumiki ake amene akuvutika, Yehova amacitapo kanthu kuti awathandize. Mwacitsanzo, pamene Aisiraeli anali kuzunzidwa monga akapolo ku Iguputo, Yehova anali kuona zoŵaŵa zawo, ndipo anacitapo kanthu. Pokamba na Mose, Yehova anati: “Ndaona nsautso ya anthu anga . . . , ndipo ndamva kulila kwawo . . . Zoonadi, ndikudziŵa bwino zoŵaŵa zawo. Conco nditsikila kwa iwo kuti ndiwalanditse m’manja mwa Aiguputo.” (Eks. 3:7, 8) Yehova anamvelela cifundo anthu ake. Ndiye cifukwa cake anawamasula mu ukapolo. Zaka zambili pambuyo pake, pamene Aisiraeli anali m’Dziko Lolonjezedwa, adani anayamba kuwaukila. Kodi Yehova anamvela bwanji? Iye “anali kuwamvela cisoni akamva kubuula kwawo cifukwa ca owapondeleza ndi owakankha-kankha.” Apanso, cifundo cinam’sonkhezela Yehova kulanditsa anthu ake. Iye anawapatsa oweluza kuti awapulumutse kwa adani awo.—Ower. 2:16, 18. w19.03 15 ¶4-5

Ciŵelu, June 6

Kodi mayi angaiŵale mwana wake woyamwa, osamvela cisoni mwana wocokela m’mimba mwake? Ngakhale amayi amenewa akhoza kuiŵala, koma ine sindidzakuiŵala.—Yes. 49:15.

Malamulo aŵili oyambilila pa Malamulo Khumi, anali akuti Aisiraeli anafunika kulambila Yehova yekha, komanso kuti anayenela kupewa kulambila mafano. (Eks. 20:3-6) Sikuti Malamulo amenewa anapindulitsa Yehova ayi. M’malomwake, anapindulitsa anthu ake. Koma akayamba kulambila mafano, anali kukumana na mavuto. Komabe, anali kuwadalitsa anthu ake akakhala okhulupilika kwa iye, ndiponso akamacita zinthu mwacilungamo kwa wina na mnzake.(1 Maf. 10:4-9) Ngati anthu ena otumikila Mulungu akunyalanyaza malamulo ake na kuvutitsa Akhristu anzawo, sitiyenela kuimba mlandu Yehova. Koma tiyenela kukumbukila kuti Yehova amatikonda, ndipo amaona tikamavutitsidwa. Iye amatimvela cisoni kwambili, kuposa ngakhale cisoni ca mayi akaona mwana wake akuvutika. N’zoona kuti nthawi zina Yehova sangacitepo kanthu nthawi yomweyo. Komabe, panthawi yake, iye adzalanga anthu osalapa amene amavutitsa anzawo. w19.02 22-23 ¶13-15

Sondo, June 7

Komatu cifunilo canu cicitike, osati canga.—Luka 22:42.

Kutatsala mawiki angapo kuti ticite Cikumbutso, kaŵili-kaŵili pa misonkhano timaphunzila kwambili za citsanzo ca Yesu, komanso mmene anaonetsela kudzicepetsa popeleka moyo wake monga dipo. Izi zimatilimbikitsa kutengela citsanzo ca Yesu ca kudzicepetsa. Zimatilimbikitsanso kucita cifunilo ca Yehova, ngakhale pamene tiona kuti kucita izi n’kovuta.Timaganizila mmene iye anaonetsela kulimba mtima m’masiku othela a moyo wake. Iye anali kudziŵa bwino kuti posacedwa adani ake adzamucita cipongwe, kumumenya, na kumupha. (Mat. 20:17-19) Ngakhale n’conco, iye sanaope kuphedwa. Nthawi yakuti apelekedwe itafika, Yesu anauza atumwi ake okhulupilika, amene anali naye m’munda wa Getsemane kuti: “Nyamukani, tiyeni tizipita. Onani! Wondipeleka uja ali pafupi.” (Mat. 26:36, 46) Ndiyeno, pamene asilikali ndi anthu ena anabwela kuti amugwile, Yesu anawayandikila na kudzidziŵikitsa. Kenako, anauza asilikaliwo kuti awaleke ophunzila ake apite. (Yoh. 18:3-8) Ndithudi, Yesu anaonetsa kulimba mtima kwakukulu! Masiku ano, Akhristu odzozedwa na a nkhosa zina amayesetsa kutengela citsanzo ca Yesu ca kulimba mtima. w19.01 27-28 ¶7-8

Mande, June 8

Yesetsani kukhala ofatsa. —Zef. 2:3.

Katswili wa zojambula-jambula amasakaniza mitundu yosiyana-siyana kuti ajambule cithunzi cokongola. Mofananamo, kuti munthu akhale wofatsa, pali makhalidwe angapo abwino amene amafunika kukhala nawo. Ena mwa makhalidwe amenewo ni kudzicepetsa, kugonjela, kudekha, na kulimba mtima. Anthu okhawo amene ali odzicepetsa ndiwo amagonjela Mulungu na kucita zimene iye amafuna. Cimodzi cimene iye amafuna n’cakuti tikhale odekha. (Mat. 5:5; Agal. 5:23) Ngati ticita zimene Mulungu amafuna, Satana amakwiya kwambili. Conco, ngakhale kuti ndife odzicepetsa komanso odekha, anthu ambili m’dziko la Satanali amatizonda. (Yoh. 15:18, 19) Ndiye cifukwa cake tifunika kukhala olimba mtima kuti Satana asatigonjetse. Munthu amene si wofatsa amakhala wodzikweza, wa mtima wapacala, ndipo samvela Yehova. Umu ni mmene Satana alili. Conco, n’zosadabwitsa kuti iye amadana ndi anthu ofatsa. Amawazonda cifukwa khalidwe lawo labwino, limavumbula khalidwe lake loipa. Ndipo koposa pamenepa, iwo amapeleka umboni wakuti Satana ni wabodza. Cifukwa ciani takamba conco? Cifukwa olo Satana atayesa bwanji, sangakwanitse kuletsa anthu ofatsa kutumikila Yehova.—Yobu 2:3-5. w19.02 8-9 ¶3-5

Ciŵili, June 9

Usacite mantha, pakuti ndili nawe.—Yes. 41:10.

Yehova anadziŵa kuti panthawi ina, anthu a ku Babulo adzacita mantha. Mzinda wa Babulo unali kudzaukilidwa na asilikali amphamvu a Mediya ndi Perisiya. Yehova anakambilatu kuti adzaseŵenzetsa asilikali amenewa kuti amasule anthu ake ku ukapolo ku Babulo. (Yes. 41:2-4) Pamene Ababulo ndi anthu a mitundu ina anadziŵa kuti adani awo akubwela, anayesa kulimbikitsana mwa kuuzana kuti: “Limba mtima.” Iwo anapanganso mafano ambili, poganiza kuti adzawateteza. (Yes. 41:5-7) Koma Yehova analimbikitsa Ayuda amene anali ku ukapolo, mwa kuwauza kuti: “Iwe Isiraeli, [osati mitundu ina] ndiwe mtumiki wanga . . . Usayang’ane uku ndi uku mwamantha, pakuti ine ndine Mulungu wako.” (Yes. 41:8-10) Onani kuti Yehova anati: “Ine ndine Mulungu wako.” Mawu a Yehova amenewa anathandiza atumiki ake okhulupilika kudziŵa kuti iye sanawaiŵale, ndiponso kuti iwo akali anthu ake. Anawauza kuti, ‘adzawatenga ndi kuwapulumutsa.’ Mwacionekele, mawu otonthoza amenewa anawalimbikitsa ngako Ayuda amene anali ku ukapolo.—Yes. 46:3, 4. w19.01 4 ¶8

Citatu, June 10

Panamveka mawu ocokela kumwamba akuti: “Iwe ndiwe Mwana wanga wokondedwa, ndimakondwela nawe.”—Maliko 1:11.

Maliko 1:9-11 imafotokoza cocitika coyamba pa zocitika zitatu pamene Yehova anakamba na Yesu kucokela kumwamba. Pa nthawiyo, Yehova anati: “Iwe ndiwe Mwana wanga wokondedwa, ndimakondwela nawe.” Yesu ayenela kuti analimbikitsidwa kwambili kumvela mawu a Atate wake, oonetsa kuti amam’konda na kum’dalila. Mawu amenewa a Yehova anatsimikizila mfundo zitatu zofunika zokhudza Yesu. Yoyamba, ni yakuti Yesu ni Mwana wake. Yaciŵili, ni yakuti Yehova amam’konda Mwana wakeyo. Ndipo yacitatu, ni yakuti amakondwela naye. Mwa kukamba kuti, “Iwe ndiwe Mwana wanga” Yehova anaonetsa kuti Mwana wake wokondedwa, Yesu, anakhala pa ubale wapadela na iye. Pamene Yesu anali kumwamba, anali kale Mwana wa Mulungu. Koma pa ubatizo wake, iye anakhala Mwana wa Mulungu m’njila yapadela. Panthawiyo, Mulungu anaonetsa kuti Yesu, monga mwana wake wodzozedwa, tsopano ali na ciyembekezo cokakhala Mfumu yodzozedwa ya Ufumu wa Mulungu kumwamba, komanso Mkulu wa Ansembe. (Luka 1:31-33; Aheb. 1:8, 9; 2:17) Conco, m’pomveka kuti pa ubatizo wake, Yehova anamuuza kuti: “Iwe ndiwe Mwana wanga.”—Luka 3:22. w19.03 8 ¶3-4

Cinayi, June 11

Palibe nzelu. . . [zotsutsana] ndi Yehova.—Miy. 21:30.

Kupeleka malangizo olakwika kunayamba kale kwambili pamene Satana ananamiza makolo athu oyambilila. Podziika yekha monga mlangizi, Satana anauza Hava kuti iye na mwamuna wake adzakhala na cimwemwe coculuka ngati asankha kumangocita zofuna zawo popanda kutsogoleledwa na Mulungu. (Gen. 3:1-6) Satana anali na zolinga zadyela. Anali kufuna kuti Adamu na Hava, kuphatikizapo mbadwa zawo zakutsogolo, azimvela iye na kum’lambila m’malo molambila Yehova. Zonse zimene anali nazo anawapatsa ni Yehova. Iye anawapatsa banja labwino, malo okhala okongola, na matupi angwilo, amene akanakhala kwamuyaya. N’zodandaulitsa kuti Adamu na Hava sanamvele Mulungu. Mwa ici, iwo anawononga ubwenzi wawo na Yehova. Ndipo zotulukapo zake zinali zomvetsa cisoni kwambili. Mofanana na maluŵa amene amafota na kuuma akathothoka, Adamu na Hava anayamba kukalamba, ndipo pamapeto pake anafa. Kusamvela kwawo kunabweletsanso mavuto aakulu kwa ana awo. (Aroma 5:12) Ngakhale n’conco, anthu ambili masiku ano amasankhabe kusamvela Mulungu. Iwo amangofuna kucita zofuna zawo. (Aef. 2:1-3) Zotulukapo zake zionetsa kuti mawu a m’lemba la tsiku la lelo ni azoona. w18.12 20 ¶3-4

Cisanu, June 12

Timalankhula . . . osati ndi mawu ophunzitsidwa ndi nzelu za anthu, koma ndi mawu amene mzimu watiphunzitsa, pamene tikuphatikiza zocitika zauzimu ndi mawu auzimu.—1 Akor. 2:13.

Mtumwi Paulo anali munthu wanzelu komanso wophunzila kwambili, ndipo anali kudziŵa zitundu zosacepela ziŵili. (Mac. 5:34; 21:37, 39; 22:2, 3) Ngakhale zinali conco, iye anakana kuyendela nzelu za dziko mu umoyo wake. M’malomwake, anali kutsatila mfundo za m’Malemba. (Mac. 17:2; 1 Akor. 2:6, 7) Zotulukapo zake zinali zakuti zinthu zinamuyendela bwino mu utumiki wake, ndipo anakhala na ciyembekezo cokalandila mphoto yamuyaya. (2 Tim. 4:8) Malinga n’zimene takambilana, n’zoonekelatu kuti maganizo a Mulungu ni apamwamba kuposa a dzikoli. Ndipo ngati tiyendela maganizo ake, zinthu zidzatiyendela bwino, komanso tidzakhala na cimwemwe coculuka. Ngakhale n’conco, Yehova satikakamiza kuyendela maganizo ake. Nayenso “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu,” komanso akulu salamulila maganizo a wina aliyense wa ise. (Mat. 24:45; 2 Akor. 1:24) Koma Mkhristu aliyense payekha ali na udindo woyesetsa kuwongolela maganizo ake, kuti akhale ogwilizana na maganizo a Mulungu. w18.11 20 ¶12-13

Ciŵelu, June 13

Cisoni ndi kubuula zidzacoka.—Yes. 35:10.

Mulungu anakambilatu kupitila mwa mneneli Yesaya kuti anthu ake akadzabwelela ku dziko lawo, sadzakhala na zilizonse zowayopsa. Sadzaopa ngakhale zilombo zolusa kapena anthu a khalidwe laucinyama. Anakambanso kuti ana ndi akulu omwe, adzakhala motetezeka. (Yes. 11:6-9; 35:5-10; 51:3) Yesaya anakambanso kuti dziko lonse lapansi, osati la Isiraeli cabe, “lidzadzaza ndi anthu odziŵa Yehova ngati mmene madzi amadzazila nyanja.” Yesaya anabwelezanso mfundo yakuti Aisiraeli akadzabwelela ku dziko lawo sadzawopa zilombo zolusa kapena anthu oopsa. Iye anakambanso kuti dziko lawo lidzabala zipatso zambili, cifukwa kudzakhala madzi okwanila, monga mmene zinalili m’munda wa Edeni. (Gen. 2:10-14; Yer. 31:12) Kodi mbali zonse za ulosi umenewu zinakwanilitsika m’nthawi ya Aisiraeli? Iyai, cifukwa palibe umboni uliwonse woonetsa kuti Aisiraeli atabwelela ku dziko lawo kucoka ku ukapolo anacilitsidwa mozizwitsa. Mwacitsanzo, anthu akhungu sanayambe kuyang’ana. Conco, Mulungu anali kuonetsa kuti kutsogolo anthu adzacilitsidwa mwakuthupi m’paradaiso. w18.12 5 ¶11-12

Sondo, June 14

[Pitilizani] kuyenda m’coonadi.—3 Yoh. 3.

Kuyenda m’coonadi kulibe polekezela. Ndise ofunitsitsa kuyendabe pa njila imeneyi mpaka muyaya. Koma n’ciani cingatithandize ‘kupitilizabe kuyenda m’coonadi’? Pitilizani kuphunzila na kusinkhasinkha pa coonadi camtengo wapatali ca m’Mawu a Mulungu. Nthawi zonse tizipatula nthawi yogula coonadi, kapena kuti kuciphunzila. Tikatelo, tidzayamba kucikonda kwambili, ndipo sitidzayesa ngakhale pang’ono kucigulitsa. Kuwonjezela pa kugula coonadi, Miyambo 23:23 imakambanso kuti tiyenela kugula “nzelu, malangizo ndi kumvetsa zinthu.” Komabe, kudziŵa zinthu pakokha si kokwanila. Tifunika kumaseŵenzetsa coonadi cimene taphunzila. Kukhala womvetsa zinthu, kumatithandiza kuti tizitha kuona kugwilizana kwa mfundo za Yehova. Ndipo nzelu zimatisonkhezela kucita zimene tinaphunzila. Komanso, nthawi zina coonadi cimatiwongolela, mwa kutithandiza kudziŵa zimene tifunika kukonza mu umoyo wathu. Conco, tikalandila malangizo, nthawi zonse tiziyesetsa kugwililapo nchito. Malangizo ni amtengo wapatali kuposa siliva.—Miy. 8:10. w18.11 9 ¶3; 11 ¶13-14

Mande, June 15

Gula coonadi ndipo usacigulitse.—Miy. 23:23.

Kodi cinthu camtengo wapatali kwambili cimene muli naco n’ciani? Kodi mungacisinthanitse na cinthu cina cotsika mtengo? Kwa atumiki a Yehova odzipatulila, yankho pa mafunso aŵili onsewa ni yosavuta. Cinthu camtengo wapatali kwambili kwa ise ni ubwenzi wathu na Yehova, ndipo sitingausinthanitse na cina ciliconse. Timaonanso coonadi ca m’Baibo kukhala cinthu camtengo wapatali, cifukwa n’cimene catheketsa kuti tikhale pa ubwenzi wabwino na Atate wathu wakumwamba. (Akol. 1:9, 10) Kukamba zoona, Mlangizi wathu Wamkulu watiphunzitsa zambili kupitila m’Mawu ake, Baibo! Iye watiphunzitsa coonadi ponena za dzina lake komanso makhalidwe ake abwino. Watiphunzitsanso za mphatso yamtengo wapatali ya dipo, imene anaipeleka mwacikondi kupitila mwa Mwana wake, Yesu. Kuwonjezela apo, Yehova watiphunzitsa za Ufumu wa Mesiya, ndipo watipatsa ciyembekezo codzakhala m’Paradaiso pano pa dziko lapansi. Iye amatiphunzitsa kukhala na makhalidwe abwino. Timayamikila kwambili ziphunzitso za coonadi zimenezi cifukwa zimatithandiza kuyandikila Mlengi wathu. Zimatithandizanso kukhala na umoyo wacimwemwe. w18.11 3 ¶1-2

Ciŵili, June 16

Musamanamizane.—Akol. 3:9.

Anthu acinyengo sangabise zolakwa zawo pa maso pa Yehova, cifukwa kwa iye “zinthu zonse zili poonekela ndipo amatha kuziona bwino-bwino.” (Aheb. 4:13) Mwacitsanzo, Baibo imafotokoza mmene ‘Satana analimbitsila mtima’ banja lina lacikhristu kunamiza Mulungu m’nthawi ya atumwi. Hananiya na Safira anapangana kuti anamize atumwi. Atagulitsa munda wawo, anatenga ndalama zina n’kukapeleka kwa atumwi, zina n’kubisa. Iwo anacita izi kuti aoneke monga anthu owolowa manja kwambili mu mpingo. Koma Yehova anaona cinyengo cawo, ndipo anawalanga. (Mac. 5:1-10) Kodi Yehova amawaona bwanji anthu onama? Satana komanso anthu onse onama amene salapa, adzaponyewa “m’nyanja yamoto.” (Chiv. 20:10; 21:8; Sal. 5:6) Tidziŵa kuti Yehova “si munthu, woti anganene mabodza.” Komanso “n’zosatheka kuti Mulungu aname.” (Num. 23:19; Aheb. 6:18) Ndipo ‘Yehova amadana ndi . . . lilime lonama.’ (Miy. 6:16, 17) Conco, kuti tim’kondweletse, tifunika kumakamba zoona nthawi zonse. w18.10 8 ¶10-13

Citatu, June 17

Sinkhasinkha zinthu zimenezi mozama.—1 Tim. 4:15.

Tiyelekezele kuti abwana anu akupemphani kuti mupeleke ndalama zocilikizila cikondwelelo cokhudzana ndi cipembedzo conyenga. Kodi mungacite ciani? M’malo moyembekezela mpaka zaconco zikakucitikileni, mungacite bwino kusinkha-sinkha pasadakhale mmene Yehova amaonela nkhani zimenezi. Ndipo ngati zotelo zakucitikilani, sicidzakhala covuta kucita zinthu moyenelela kapena kuyankha mwanzelu. Kuganizila pasadakhale za kufunika kokhala wokhulupilika, kungakhalenso kothandiza ngati tadwala matenda aakulu mwadzidzidzi. N’zoona kuti timapewa kuikiwa magazi athunthu, kapena ciliconse mwa zigawo zake zinayi zikulu-zikulu. Komabe, njila zina za kucipatala zothandizila odwala poseŵenzetsa magazi, zimafuna kuti tidzipangile tekha cosankha mogwilizana na mfundo za m’Baibo, zimene zimaonetsa maganizo a Yehova. (Mac. 15:28, 29) Kodi nthawi yabwino yopanga cosankha pa nkhaniyi ni iti? Kodi ni pa nthawi imene tili m’cipatala, mwina tikumvela ululu, ndipo tikufunikila kupanga cosankha mwamsanga-msanga? Mwacionekele, yankho ni yakuti iyai. Ino ndiyo nthawi yabwino yofufuza mfundo zokhudza nkhaniyi, kusaina khadi ya DPA yoonetsa zosankha zathu pa cithandizo camankhwala, komanso kufotokozela madokota zosankha zathu. w18.11 24 ¶5; 26 ¶15-16

Cinayi, June 18

Munthu wondimvela adzakhala mwabata.—Miy. 1:33.

Yehova ni m’busa wacikondi amene amasamalila anthu ake. Amawakonda na kuwateteza kwa adani awo. Izi n’zolimbikitsa ngako, maka-maka masiku yano pamene tikuyandikila mapeto a dziko loipali. Yehova adzapitiliza kusamalila anthu ake ngakhale pa cisautso cacikulu, cimene cayandikila kwambili. (Chiv. 7:9, 10) Conco, pa cisautso cacikulu, anthu onse a Mulungu, kaya acicepele kapena okalamba, athanzi kapena olemala, sadzacita mantha kapena kutaya mtima. Koma adzacita zimene Yesu Khristu anakamba, zakuti: “Mudzaimilile cilili ndi kutukula mitu yanu, cifukwa cipulumutso canu cikuyandikila.” (Luka 21:28) Iwo sadzagwedezeka ngakhale poukilidwa na Gogi, mgwilizano wa mitundu. (Ezek. 38:2, 14-16) N’cifukwa ciani anthu a Mulungu sadzaopa? Cifukwa cakuti adziŵa kuti Yehova sasintha. Monga mmene anacitila m’nthawi ya Aisiraeli, iye nthawi zonse adzawapulumutsa na kuwasamalila mwacikondi.—Yes. 26:20. w18.09 26-27 ¶15-16

Cisanu, June 19

Cifukwa cakuti ndiwe wamtengo wapatali kwa ine, . . . ndimakukonda.—Yes. 43:4.

Aisiraeli ayenela kuti analimbikitsidwa ngako pamene anamva mawu a Yehova ali pamwambapa. Pokhala atumiki a Yehova, sitikayikila kuti iye amatikonda kwambili. Pokamba za olambila oona, mawu a Mulungu amati, Yehova ‘adzawapulumutsa cifukwa ndi wamphamvu. Iye adzakondwela nawo.’ (Zef. 3:16, 17) Yehova analonjeza anthu ake kuti adzawasamalila na kuwatonthoza olo atakumana na mavuto otani. Iye anati: ‘Inu mudzayamwadi. Ndidzakunyamulani m’manja ndipo ndidzakusisitani mwacikondi n’takuikani pamwendo. Mofanana ndi munthu amene mayi ake amamutonthoza, inenso ndidzakutonthozani anthu inu.’ (Yes. 66:12, 13) Kodi si mawu ocititsa cidwi amenewa? Yehova akudziyelekezela na mayi wacikondi amene wanyamula mwana wake m’manja, kapena amene akusisita mwanayo mwacikondi atamuika pamendo. Pamenepa, Yehova akuonetsa cikondi cacikulu cimene ali naco pa atumiki ake. Conco, tisamakayikile kuti Yehova amatikonda komanso amationa kuti ndise amtengo wapatali.—Yer. 31:3. w18.09 13 ¶6-7

Ciŵelu, June 20

Ndani lelo ali wokonzeka kupeleka mphatso kwa Yehova? —1 Mbiri 29:5.

Pa zocitika zosiyana-siyana m’mbili ya Aisiraeli, panali kufunika atumiki odzipeleka. (Eks. 36:2; Neh. 11: 2) Masiku ano, na ise tili na mipata yambili yoseŵenzetsa nthawi yathu, cuma, na maluso athu pothandiza Akhristu anzathu. Ndipo tikakhala odzipeleka, tidzapeza cimwemwe coculuka na madalitso ambili. Akhristu amene amadzipeleka pa nchito zosiyana-siyana m’gulu la Mulungu amapeza mabwenzi. Mwacitsanzo, ganizilani za Margie, mlongo amene wakhala akugwila nchito yomanga Nyumba za Ufumu kwa zaka 18. Pa zaka zonsezi, wakhala akuthandiza alongo acicepele na kuwaphunzitsa nchito. Iye amaona kuti kugwila nchitoyi ni njila yabwino yolimbikitsilana mwauzimu wina na mnzake. (Aroma 1:12) Pa nthawi ya mavuto, Margie wakhala akulimbikitsidwa na mabwenzi amene anapeza pomanga Nyumba za Ufumu. Kodi imwe munagwilako nchito yomanga Nyumba ya Ufumu? w18.08 25 ¶9, 11

Sondo, June 21

Usalole kuti munthu aliyense akudelele poona kuti ndiwe wamng’ono. M’malomwake, ukhale citsanzo kwa okhulupilika m’kalankhulidwe, m’makhalidwe, m’cikondi, m’cikhulupililo, ndi pa khalidwe loyela.—1 Tim. 4:12

Pamene Paulo anali kulemba mawuwa, mwina Timoteyo anali atangokwanitsa kumene zaka 30. Komabe, Paulo anali atamupatsa udindo waukulu. Olo kuti sitidziŵa cimene anam’patsila malangizo amenewa, mfundo imene tiphunzilapo ni yoonekelatu. Tisamaweluze abale acinyamata potengela cabe zaka zawo zakubadwa. Tizikumbukila kuti ngakhale Ambuye wathu Yesu, anacita utumiki wawo wa pa dziko lapansi atangokwanitsa kumene zaka za m’ma 30. N’kutheka kuti malinga na cikhalidwe ca kumene tikhala, anthu ambili salemekeza acinyamata. Conco, akulu mu mpingo akhoza kumazengeleza kuyeneleza abale acinyamata kuti atumikile monga atumiki othandiza kapena akulu. Koma akulu onse ayenela kukumbukila mfundo yakuti, Malemba sachula ciŵelengelo ca zaka zakubadwa zimene munthu afunika kufika kuti ayenelele kutumikila monga mtumiki wothandiza kapena mkulu.— 1 Tim. 3:1-10, 12, 13; Tito 1:5-9. w18.08 11-12 ¶15-16

Mande, June 22

Pewa nkhani . . . zimene ena monama amati ndiye “kudziŵa zinthu.”—1 Tim. 6:20.

Kuti tipange cosankha cabwino pa nkhani inayake, tifunika kudziŵa zoona zake za nkhaniyo. Conco, sitifunika kuŵelenga zilizonse, koma tiyenela kusankha mosamala nkhani zoŵelenga. (Afil. 4:8, 9.) Tisawononge nthawi yathu kumvetsela nkhani za pa mawebusaiti okayikitsa kapena kuŵelenga maimelo na mameseji a nkhani zopanda umboni. Tifunikanso kupewelatu mawebusaiti oyendetsedwa ndi anthu ampatuko. Iwo colinga cawo cimakhala kufooketsa anthu a Mulungu na kupotoza coonadi. Kuŵelenga na kumvetsela nkhani zabodza kungatipangitse zosankha zolakwika. Tifunika kupewelatu nkhani zabodza cifukwa zikhoza kuwononga kwambili maganizo na mtima wathu. Ganizilani zimene zinacitika m’nthawi ya Mose pamene azondi 10 mwa azondi 12 anabweletsa lipoti yoipa pambuyo pokazonda Dziko Lolonjezedwa. (Num. 13:25-33) Zokamba zawo zabodza komanso zosinjilila zinacititsa kuti anthu a Yehova ataye mtima. (Num. 14:1-4, 6-10) M’malo momvetsela lipoti ya zoona na kudalila Yehova, iwo anasankha kukhulupilila lipoti yoipayo. w18.08 4 ¶4-5

Ciŵili, June 23

Musasoceletsedwe. Kugwilizana ndi anthu oipa kumawononga makhalidwe abwino.—1 Akor. 15:33.

Anthu ambili aliko na makhalidwe ena abwino. Ngakhale anthu amene si Mboni sikuti nthawi zonse amacita zoipa. Ngati anthu amene mumadziŵana nawo ali conco, kodi ndiye kuti angakhale mabwenzi abwino? Ayi. Coyamba dzifunseni kuti, ‘Kodi kugwilizana nawo kudzakhudza bwanji ubwenzi wanga na Yehova? Kodi adzanithandiza kuulimbitsa? Kodi iwo amakonda kuganizila ciani? Mwacitsanzo, kodi amakonda kukamba za mafashoni, ndalama, zipangizo zamakono, zosangalatsa, kapena zolinga zakuthupi? Kodi zokamba zawo nthawi zambili zimaphatikizapo mijedo kapena nthabwala zotukwana?’ Kumbukilani kuti Yesu anati: “Pakamwa pamalankhula zosefukila mumtima.” (Mat. 12:34) Ngati mwaona kuti zocita za anzanu zikuika ubwenzi wanu na Yehova paciopsezo, citamponi kanthu mofulumila mwa kupewa kugwilizana nawo kwambili kapena kungothetsa ubwenziwo.—Miy. 13:20. w18.07 19 ¶11

Citatu, June 24

Moseyo anali munthu wofatsa kwambili kuposa anthu onse.—Num. 12:3.

Pamene Mose anali na zaka 80, Yehova anam’patsa nchito yakuti akatulutse Aisiraeli mu ukapolo ku Iguputo. (Eks. 3:10) Kangapo konse Mose anapeleka zifukwa zodzikhululukila. Koma Yehova anaonetsabe kuleza mtima, ndipo anapitiliza kum’limbikitsa mwa kum’patsa mphamvu yocita zozizwitsa. (Eks. 4:2-9, 21). Iye akanafuna, sembe anangom’kakamiza Mose kucita zimene anam’lamula. Koma anacita zinthu moleza mtima ndi mokoma mtima. Anayesetsa kum’limbikitsa mtumiki wake wodzicepetsa ameneyo. Kodi izi zinam’thandiza Mose? Inde, cakuti iye anakhala mtsogoleli wabwino, amene anali kuyesetsa kucita zinthu modekha ndi anthu komanso mowaganizila, monga mmene Yehova anacitila kwa iye. Ngati muli na mphamvu ya ulamulilo, n’kofunika kwambili kuti muzitengela citsanzo ca Yehova mwa kukhala woganizila ena, wokoma mtima, ndi woleza mtima pocita zinthu ndi amene mukuwayang’anila. (Akol. 3:19-21; 1 Pet. 5:1-3) Ngati muyesetsa kutengela citsanzo ca Yehova na Mose Wamkulu, Yesu Khristu, mudzakhala wofikilika komanso wotsitsimula kwa ena.—Mat. 11:28, 29. w18.09 24-25 ¶7-10

Cinayi, June 25

Ndi zabwino komanso zosangalatsa kwambili abale akakhala pamodzi mogwilizana!—Sal. 133:1.

Tingatsitsimule ena mwa kukhala aubwenzi na okoma mtima. Mwa ici, tidzalimbikitsa mgwilizano pakati pa abale na alongo mumpingo. Ngati munayamba kale kucita zimenezi, ndiye kuti mukucita bwino. Koma kodi ‘mungafutukule mtima wanu’ mwa kuwonjezela zimene mumacita polimbikitsa abale na alongo? (2 Akor. 6:11-13) Mungacite ciani kuti muwonjezele kuwala kwa coonadi ca m’Baibo m’dela lanu? Muyenela kukhala okoma mtima m’zokamba na zocita zanu. Mukatelo, anansi anu angakopeke na coonadi. Dzifunseni kuti: ‘Kodi anthu a m’dela langa amaniona bwanji? Kodi panyumba panga na katundu wanga zimakhala zaukhondo nthawi zonse? Kodi nimayesetsa kuthandiza ena?’ Cinanso, pamene muceza na abale na alongo, bwanji osawafunsako mmene kukoma mtima na khalidwe lawo labwino zakhudzila abululu awo, maneba, anzawo a kunchito, kapena a kusukulu? Mwacionekele, iwo adzakufotokozelani zocitika zolimbikitsa.—Aef. 5:9. w18.06 24 ¶13-14

Cisanu, June 26

Nthawi ikubwela pamene aliyense wakupha inu adzaganiza kuti wacita utumiki wopatulika kwa Mulungu.—Yoh. 16:2.

Umu ni mmene anthu amene anapha wophunzila wa Yesu, Sitefano, anali kuganizila. Ndipo pali enanso amene anacita zofanana ndi zimenezi. (Mac. 6:8, 12; 7:54-60) Anthu ambili acipembedzo akhala akucita zinthu zoipa, monga kupha anthu, n’kumakamba kuti akucita cifunilo ca Mulungu, pamene m’ceni-ceni akuphwanya malamulo ake. (Eks. 20:13) Ndithudi! Iwo asoceletsedwa kothelatu na cikumbumtima cawo. Tingacite ciani kuti cikumbumtima cathu cizititsogolela bwino? Malamulo na mfundo za m’Mawu a Mulungu ‘n’zopindulitsa pa kuphunzitsa, kudzudzula, kuwongola zinthu ndi kulangiza m’cilungamo.’ (2 Tim. 3:16) Conco, tifunika kumaŵelenga Baibo mwakhama, kusinkha-sinkha zimene imakamba, na kuziseŵenzetsa mu umoyo wathu. Tikatelo, tidzaphunzitsa cikumbumtima cathu kuti cizititsogolela mogwilizana na maganizo a Mulungu. Cikumbumtima caconco cikhoza kutithandiza kupanga zosankha mwanzelu. w18.06 17 ¶3-4

Ciŵelu, June 27

Landilani . . . lupanga la mzimu, lomwe ndilo mawu a Mulungu.—Aef. 6:17.

M’nthawi imene Paulo anali kulemba kalata yopita kwa Aefeso, lupanga limene asilikali aciroma anali kuseŵenzetsa linali lalitali masentimita 50. Ndipo linali kupangidwa m’njila yakuti lizigwilitsidwa nchito pa nkhondo yomenyana moyandikana. Cifukwa cimodzi cimene asilikali aciroma anali kucitila bwino pa nkhondo, n’cakuti tsiku lililonse anali kuyeseza mmene angaseŵenzetsele malupanga awo. Paulo anakamba kuti Mawu a Mulungu amene Yehova watipatsa ali monga lupanga. Komabe, tifunika kuphunzila mmene tingaseŵenzetsele mwaluso lupanga limeneli poikila kumbuyo zikhulupililo zathu, kapena powongolela maganizo athu. (2 Akor. 10:4, 5; 2 Tim. 2:15) Palibe cifukwa comuyopela Satana na ziŵanda zake. Iwo ni amphamvu, koma sikuti ni osagonjetseka. Kuwonjezela apo, sadzakhala na moyo kwamuyaya. Posacedwa, mu Ulamulilo wa Khristu wa Zaka 1,000, iwo adzaponyedwa ku phompho, kumene sadzakhalanso na mphamvu zocita ciliconse. Pambuyo pake, adzawonongedwa. (Chiv. 20:1-3, 7-10) Mdani wathu timam’dziŵa bwino. Timawadziŵanso bwino macenjela ake. Ndipo mwa thandizo la Yehova, tingathe kucilimika polimbana naye! w18.05 30 ¶15; 31 ¶19-21

Sondo, June 28

Njokayo inauza mkaziyo kuti: “Kufa simudzafa ayi.”—Gen. 3:4.

N’zoonekelatu kuti Adamu anali kudziŵa kuti njoka siingakambe. Conco, ayenela kuti anadziŵa kuti colengedwa camzimu n’cimene cinakamba na Hava kupitila mwa njoka. (Gen. 3:1-6) Adamu na Hava sanali kudziŵa zilizonse zokhudza colengedwa cimeneci. Olo zinali conco, mwadala Adamu anasankha kukana Atate wake wacikondi wakumwamba na kugwilizana ndi mngelo wosamudziŵayo potsutsa cifunilo ca Mulungu. (1 Tim. 2:14) Izi zitangocitika, Yehova anayamba kuvumbula zinthu zina zokhudza mdani ameneyu, amene anasoceletsa Adamu na Hava. Ndipo analonjeza kuti pamapeto pake, mngelo woipayu adzawonongedwa. Koma Yehova anacenjezanso kuti, kwa kanthawi, colengedwa cauzimu cimene cinakamba na Hava kupitila mwa njoka, cidzalimbana ndi anthu okonda Mulungu. (Gen. 3:15) Mwa nzelu zake, Yehova sanatiuze dzina leni-leni la mngelo amene anam’pandukila. Komanso Mulungu sanaulule ngakhale dzina lolongosola zocita za mdani ameneyu, mpaka patapita zaka 2,500 kucokela pamene iye anapanduka mu Edeni.—Yobu 1:6. w18.05 22 ¶1-2

Mande, June 29

[Awa ndi] anthu amene. . . [amabeleka] zipatso mwa kupilila.—Luka 8:15.

Ngati nthawi zina mumalefulidwa polalikila m’gawo la anthu opanda cidwi, musadabwe nazo. Olo mtumwi Paulo, nthawi ina anamvelapo conco. Mu utumiki wake wa zaka pafupi-fupi 30, iye anathandiza anthu ambili-mbili kukhala ophunzila a Khristu. (Mac. 14:21; 2 Akor. 3:2, 3) Komabe, sanakwanitse kuthandiza Ayuda ambili kukhala olambila oona. Ambili anali kumutsutsa, ndipo ena anali kum’zunza. (Mac. 14:19; 17:1, 4, 5, 13) Kodi mzimu wotsutsa wa Ayuda unamukhudza bwanji Paulo? Iye anati: “Ndikunena zoona mwa Khristu . . . ndili ndi cisoni cacikulu ndipo mtima ukundipweteka nthawi zonse.” (Aroma 9:1-3) N’cifukwa ciani Paulo anamvela conco? Cifukwa nchito yolalikila anali kuikonda. Anali kulalikila Ayuda cifukwa anali kuwadela nkhawa kwambili. Conco, cinamuŵaŵa kuona kuti iwo anakana cifundo ca Mulungu. Mofanana ndi Paulo, timalalikila anthu cifukwa timawakonda na mtima wonse.—Mat. 22:39; 1 Akor. 11:1. w18.05 13 ¶4-5

Ciŵili, June 30

Nkhawa mumtima mwa munthu ndi imene imauwelamitsa, koma mawu abwino ndi amene amausangalatsa.—Miy. 12:25.

Paulo anaonetsa kuti anthu amene ali na udindo wolimbikitsa ena, nawonso amafunikila cilimbikitso. Iye analembela Akhristu a ku Roma kuti: “Ndikulakalaka kukuonani kuti ndikugaŵileni mphatso inayake yauzimu kuti mukhale olimba, kapena kuti tidzalimbikitsane mwa cikhulupililo, canu ndi canga.” (Aroma 1:11, 12) Ndithudi, olo kuti Paulo anali kulimbikitsa kwambili Akhristu anzake, nayenso nthawi zina anafunika kulimbikitsidwa. (Aroma 15:30-32) Abale na alongo amene ali na umoyo wodzimana, tifunika kumawayamikila. Enanso amene amafunikila cilimbikitso ni abale na alongo amene sali pa banja cifukwa cofuna kumvela lamulo lakuti tiyenela kukwatila kokha “mwa Ambuye.” (1 Akor. 7:39) Komanso, Akhristu amene akupilila mokhulupilika cizunzo kapena matenda, amafunika kulimbikitsidwa.—2 Ates. 1:3-5. w18.04 21 ¶3-5

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani