July
Citatu, July 1
Pitilizani kuzindikila cifunilo ca Yehova.—Aef. 5:17.
Tikukhala m’nthawi “yapadela komanso yovuta,” ndipo mavuto adzapitiliza kuwonjezeka mpaka pamene Yehova adzawononga dziko loipali na kubweletsa mtendele weni-weni. (2 Tim. 3:1) Conco, tingacite bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi nimayang’ana kwa ndani nikafuna thandizo na citsogozo?’ Zaka zambili m’mbuyomo, wamasalimo anakamba kuti tifunika kuyang’ana kwa Yehova pamene tifuna thandizo. (Sal 123:1-4) Iye anayelekezela kuyang’ana kwa Yehova na mmene mtumiki amayang’anila kwa mbuye wake. Kodi wamasalimo anatanthauza ciani pamenepa? Mtumiki amayang’ana kwa mbuye wake kuti am’patse cakudya na kum’teteza. Komanso amafuna kudziŵa zimene mbuye wakeyo afuna kuti iye acite, ndipo akadziŵa amacita zimenezo. Mofananamo, tifunika kuphunzila Mawu a Mulungu tsiku lililonse kuti tidziŵe zimene Yehova afuna kuti ticite. Ndipo tikadziŵa, tifunika kucita zimenezo. Tikatelo, m’pamene Yehova adzatikomela mtima tikafuna thandizo. w18.07 12 ¶1-2
Cinayi, July 2
Ngati Mwana wakumasulani, mudzakhaladi omasuka.—Yoh. 8:36.
Yesu anali kukamba za kumasuka ku ‘ukapolo wa ucimo,’ umene wasautsa anthu kwambili kuposa ukapolo wina uliwonse. (Yoh. 8:34) Ucimo umatisonkhezela kucita zoipa. Komanso umatilepheletsa kucita zinthu zimene tidziŵa kuti ndiye zabwino, kapena zimene tiona kuti tingazikwanitse. Mwanjila imeneyi, ise anthu ndise akapolo a ucimo. Zotulukapo za ukapolo umenewu n’zakuti timakhala na nkhawa, timavutika, ndipo pamapeto pake timafa. (Aroma 6:23) Tikadzamasulidwa ku ukapolo wa ucimo, m’pamene tidzakhala na ufulu weni-weni ngati umene makolo athu oyambilila anali nawo. Pamene Yesu anakamba kuti “mukamasunga mawu anga nthawi zonse,” anaonetsa kuti pali zinthu zina zimene tifunika kucita kapena malamulo amene tifunika kutsatila kuti iye atimasule. (Yoh. 8:31) Monga Akhristu odzipeleka, tinadzikana tekha ndipo tinasankha kukhala na umoyo wotsatila ziphunzitso za Khristu monga ophunzila ake. (Mat.16:24) Monga mmene Yesu analonjezela, tidzakhala na ufulu weni-weni pamene tidzalandila madalitso onse a nsembe ya dipo lake. w18.04 7 ¶14-16
Cisanu, July 3
Inu nokha ndiye mumadziŵa bwino mtima wa ana a anthu.—2 Mbiri 6:30.
Yehova amawaganizila anthu ake, ngakhale pamene ali na maganizo olakwika pa nkhani ina. Mwacitsanzo, ganizilani za Yona. Yehova anam’tuma kuti akalengeze uthenga waciweluzo kwa anthu a ku Nineve. Anineve atalapa, Mulungu anaganiza kuti asawawononge. Koma Yona sanakondwele nazo zimenezi. Iye ‘anakwiya koopsa,’ cifukwa uthenga wake waciweluzo sunakwanilitsike. Koma Yehova anacita naye zinthu moleza mtima, ndipo anam’thandiza kusintha maganizo. (Yona 3:10–4:11) M’kupita kwa nthawi, Yona anamvetsetsa mfundo imene Yehova anafuna kum’phunzitsa. Ndipo Yehova anafika mpaka pomugwilitsila nchito kulemba nkhaniyi kuti tonsefe tiphunzilepo kanthu. (Aroma 15:4) Mmene Yehova anacitila zinthu ndi anthu ake, zimatitsimikizila kuti amamvelela cifundo atumiki ake. Iye amaona mavuto amene aliyense wa ife amakumana nawo. Iye amadziŵa bwino maganizo athu, mmene timvelela mkati mwa mtima, komanso zolephela zathu. Ndipo “sadzalola kuti muyesedwe kufika pamene simungapilile.” (1 Akor. 10:13) Kukamba zoona, mawu amenewa ni olimbikitsa kwambili. w19.03 15-16 ¶6-7
Ciŵelu, July 4
Kwa iye zinthu zonse zili poonekela ndipo amatha kuziona bwino-bwino. Ndipotu ife tikuyenela kudzayankha pa zocita zathu kwa Mulungu amene amaona zonseyo.—Aheb. 4:13.
Mu Cilamulo ca Mose, akulu anali na udindo woweluza Aisiraeli pa nkhani zokhudza kulambila, komanso pa milandu ing’ono-ing’ono na ikulu-kulu. Ganizilani zitsanzo izi: Ngati Mwisiraeli wapha munthu, sanali kuphedwa nthawi yomweyo. Akulu a mu mzinda anali kufufuza nkhaniyo coyamba kuti adziŵe ngati wolakwayo anafunikadi kuphedwa kapena ayi. (Deut. 19:2-7, 11-13) Akuluwo anali kuweluzanso Aisiraeli pa nkhani zina zosiyana-siyana, monga zokhudza mikangano ya malo kapena katundu, ngakhalenso mikangano ya m’banja. (Eks. 21:35; Deut. 22:13-19) Pamene akulu anaweluza mwacilungamo, komanso Aisiraeli n’kumvela Cilamulo, aliyense anali kupindula. Ndipo mtunduwo unali kucititsa Yehova kulandila ulemelelo. (Lev. 20:7, 8; Yes. 48:17, 18) Apa tingaone kuti zilizonse zimene timacita mu umoyo wathu, zimam’khudza Yehova. Iye amafuna kuti tizicita zinthu mwacikondi komanso mwacilungamo ndi ena. Ndipo amaona zonse zimene timacita na kukamba, ngakhale zamseli. w19.02 23 ¶16-18
Sondo, July 5
Analola kuti asautsidwe, koma sanatsegule pakamwa pake. —Yes. 53:7.
Ngati tili na nkhawa kapena tikuvutika maganizo, cimakhala covuta kukhala wofatsa. Tingayambe kukwiya na nkhani za zii. Tingayambenso kukamba mokhadzula, komanso kucita zinthu mopanda cikondi. Conco, ngati mukuvutika maganizo, muziganizila citsanzo ca Yesu. Cakumapeto kwa moyo wake padziko lapansi, Yesu anavutika maganizo kwambili. Iye anali kudziŵa kuti adzazunzidwa kwambili, komanso kuti adzaphedwa. (Yoh. 3:14, 15; Agal. 3:13) Patatsala miyezi ingapo asanaphedwe, Yesu anakamba kuti anavutika kwambili mumtima. (Luka 12:50) Ndipo kutatsala masiku ocepa asanaphedwe, iye anati: “Moyo wanga ukusautsika.” Yesu anaonetsa kuti ni wodzicepetsa komanso wogonjela pamene anakhuthulila Mulungu nkhawa zake m’pemphelo. (Yoh. 12:27, 28) Nthawiyo itafika, Yesu molimba mtima anadzipeleka kwa adani a Mulungu, ndipo iwo anamupha mwankhanza ndi momunyazitsa. Ngakhale anavutika maganizo komanso kuzunzidwa kwambili, iye anacitabe cifunilo ca Mulungu. Ndithudi, Yesu n’citsanzo cabwino kwambili pankhani yokhalabe ofatsa pamene tivutika!—Yes. 53:7, 10. w19.02 11 ¶14-15
Mande, July 6
Tiyeni tiganizilane kuti tilimbikitsane pa cikondi ndi nchito zabwino.—Aheb. 10:24.
Kuti tizipezeka pa misonkhano nthawi zonse, timafunika kulimba mtima poyang’anizana na mavuto. Mwacitsanzo, abale na alongo athu ena amayesetsa kupezeka pa misonkhano, mosasamala kanthu za mavuto monga matenda, zofooketsa, na cisoni cacikulu. Palinso ena amene amalimba mtima kupezeka pa misonkhano, ngakhale kuti amatsutsidwa kwambili na a m’banja mwawo, kapena akulu-akulu a boma. Komanso, ganizilani mmene citsanzo cathu cimakhudzila abale amene ali m’ndende cifukwa ca cikhulupililo cawo. (Aheb. 13:3) Iwo akamvela kuti tikutumikilabe Yehova olo kuti tikukumana na mayeselo, amalimba mtima, cikhulupililo cawo cimalimbilako, ndiponso amalimbikitsidwa kukhalabe okhulupilika. Pamene Paulo anali m’ndende ku Roma, iye anali kukondwela kwambili akamvela kuti abale ake akutumikila Mulungu mokhulupilika. (Afil. 1:3-5, 12-14) Paulo atatsala pang’ono kumasulidwa kapena atangomasulidwa kumene, analembela kalata Akhristu aciheberi. M’kalatayo, Paulo analimbikitsa Akhristu okhulupilika amenewo kuti apitilize kukondana, komanso kuti asaleke kusonkhana pamodzi.—Aheb. 10:25; 13:1. w19.01 28 ¶9
Ciŵili, July 7
Dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.—1 Yoh. 5:19.
Satana ni wopanduka, amanyalanyaza miyezo ya Yehova, ndiponso ni wodzikonda. Iye amafuna kuti ife titengele zocita zake. Wasoceletsa anthu ambili a m’dzikoli. Iye amafuna kuti tizigwilizana na anthu oipa amenewo, olo kuti tidziŵa kuti kucita zimenezo ‘kungawononge’ makhalidwe ndi maganizo athu. (1 Akor. 15:33) Satana amafunanso kuipitsa mtima wathu mwa kuticititsa kuyamba kudalila nzelu za anthu m’malo modalila malangizo a Yehova. (Akol. 2:8) Ganizilani mfundo imodzi imene Satana amalimbikitsa. Iye amasonkhezela anthu kukhala na mtima wofunitsitsa kulemela. Ena amene amakhala na maganizo amenewa amalemeladi, koma enanso salemela. Mulimonsemo, zotulukapo zake zimakhala zoipa. N’cifukwa ciani takamba conco? Cifukwa cakuti pofunitsitsa kulemela, amalolela kuika paciopsezo moyo wawo, banja lawo, ngakhale ubwenzi wawo na Mulungu. (1 Tim. 6:10) Koma ife timayamikila kuti Atate wathu wanzelu Yehova, amatiphunzitsa kuona ndalama m’njila yoyenela.—Mlal. 7:12; Luka 12:15. w19.01 15 ¶6; 17 ¶9
Citatu, July 8
Wacita bwino kwambili, kapolo wabwino ndi wokhulupilika iwe! Unakhulupilika pa zinthu zocepa. Ndikuika kuti uziyang’anila zinthu zambili. Sangalala limodzi ndi ine mbuye wako.—Mat. 25:21.
Pamene Mwana wa Yehova anabwela pa dziko, anapeleka citsanzo cabwino kwambili ca mmene tingalimbikitsile ena. Koma ngakhale iye asanabwele, atumiki a Yehova anali kudziŵa kuti kulimbikitsa ena n’kofunika. Mwacitsanzo, Asuri ataopseza kuti adzaononga Yerusalemu, Hezekiya anasonkhanitsa akulu-akulu a asilikali ndi anthu a mu Yerusalemu kuti awalimbikitse. “Pamenepo, anthuwo anayamba kulimba mtima cifukwa ca mawu [ake].” (2 Mbiri 32:6-8) Pa nthawi ina, Yobu anaphunzitsa anzake atatu njila yabwino yolimbikitsila ena. Anacita izi olo kuti pa nthawiyo, iye anali kufunikilanso citonthozo. Yobu anauza anzakewo kuti cikanakhala kuti iwo ni amene anali kuvutika, ‘akanawalimbikitsa ndi mawu a m’kamwa mwake, ndipo citonthozo ca milomo yake’ cikanawatsitsimula. (Yobu 16:1-5) Pambuyo pake, Yobu analandila cilimbikitso kucokela kwa Elihu, komanso analimbikitsidwa mwacindunji na Yehova.—Yobu 33:24, 25; 36:1, 11; 42:7, 10. w18.04 16 ¶6; 17 ¶8-9
Cinayi, July 9
Ndikulimbitsa. Ndithu ndikuthandiza.—Yes. 41:10.
Pofotokoza mmene Yehova adzalimbitsila anthu ake, Yesaya anati: “Yehova. . .adzabwela ngati wamphamvu ndipo [“mkono,” NW-E] wake uzidzalamulila m’malo mwa iyeyo.” (Yes. 40:10) Kaŵili-kaŵili, Baibo imaseŵenzetsa liwu lakuti “mkono” kuphiphilitsila mphamvu. Conco, mawu akuti “mkono wa [Yehova] udzalamulila” atikumbutsa zakuti Yehova ni Mfumu yamphamvu. Iye anaseŵenzetsa mphamvu zake zopanda malile polimbitsa atumiki ake akale na kuwateteza. Ndipo masiku anonso, amalimbitsa na kuteteza atumiki ake amene amam’dalila. (Deut. 1:30, 31; Yes. 43:10.) Yehova amasunga lonjezo lake lakuti: “Ndikulimbitsa,” maka-maka pamene adani athu akutizunza. M’maiko ena, adani athu akuyesetsa mwamphamvu kuletsa nchito yathu yolalikila kapena kutseka maofesi athu. Ngakhale n’conco, sititaya mtima na zimenezi, cifukwa zimene Yehova watilonjeza zimatilimbikitsa kwambili. Iye akuti: “Cida ciliconse cimene cidzapangidwe kuti cikuvulaze sicidzapambana.”—Yes. 54:17. w19.01 5-6 ¶12-13
Cisanu, July 10
Odala ndi anthu amene amazindikila zosoŵa zawo zauzimu. —Mat. 5:3.
Mosiyana na zinyama, ise anthu tili na zosoŵa zauzimu. Ndipo ni Mlengi wathu cabe amene angatipatse zosoŵa zimenezi. (Mat. 4:4) Ngati imwe acicepele mumvetsela kwa Yehova, mudzakhala na nzelu, luso la kuzindikila, na cimwemwe. Mulungu amakupatsani zosoŵa zanu zauzimu kupitila m’Mawu ake, Baibo. Komanso, amacita izi mwa kupeleka cakudya cauzimu coculuka kupitila mwa “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu.” (Mat. 24:45) Ndipo kukamba zoona, cakudya cauzimu cimene tili naco n’ca mwana alilenji. (Yes. 65:13, 14) Cakudya cauzimu cimene Mulungu amapeleka cidzakuthandizani kukhala oganiza bwino ndi anzelu. Makhalidwe amenewa adzakutetezani m’njila zambili. (Miy. 2:10-14) Mwacitsanzo, adzakuthandizani kuzindikila ziphunzitso zabodza, monga cakuti kulibe Mlengi. Adzakutetezaninso ku bodza lakuti kukhala na cuma ndiye cisinsi copezela cimwemwe. Cinanso, kuganiza bwino na nzelu zidzakuthandizani kupewa zilako-lako zoipa komanso makhalidwe amene angakubweletseleni mavuto. Conco, pitilizani kufuna-funa nzelu zocokela kwa Mulungu na luntha la kuganiza, ndipo muziona zimenezi monga cuma canu ca mtengo wapatali. w18.12 20 ¶6-7
Ciŵelu, July 11
Masiku a anthu anga adzakhala ngati masiku a mtengo. —Yes. 65:22.
Lembali lakamba kuti idzafika nthawi pamene masiku athu “adzakhala ngati masiku a mtengo.” Mitengo ina imakhala zaka masauzande ambili. Ngati anthu adzakhala na zaka zambili conco, ndiye kuti adzakhala na thanzi labwino. Zinthu pa dziko zikadzakhala monga mmene ulosi wa Yesaya umakambila, ndiye kuti tinganene kuti dziko lakhala paradaiso. Ndipo zoonadi, ulosi umenewu udzakwanilitsika! Maulosiwa aonetsa kuti kutsogolo dziko lapansi lidzakhala paradaiso. Anthu padziko lonse adzadalitsidwa na Mulungu. Sitidzayopa anthu kapena zilombo zolusa. Ndipo akhungu, ogontha, na olemala adzacilitsidwa. Anthu adzamanga nyumba zawo-zawo, komanso adzabyala minda ya zakudya zabwino. Adzakhala na moyo kwa zaka zambili kuposa zimene mitengo imakhala. Inde, Baibo imaonetsa kuti paradaiso alikodi. Komabe, anthu ena angakambe kuti uku n’kukokomeza cabe maulosi a m’Baibo. Kodi muli na umboni womveka wakuti paradaiso idzakhalapodi pa dziko lapansi? Munthu wamkulu woposa onse amene anakhalako anapeleka umboni wamphamvu pa nkhaniyi.—Luka 23:43. w18.12 5 ¶13-15
Sondo, July 12
Sandulikani mwa kusintha maganizo anu.—Aroma. 12:2.
Maganizo a munthu amatha kusintha. Ndipo kuti maganizo athu asinthe, mbali yaikulu zimadalila pa zimene timalola kuti ziloŵe mu mtima mwathu, komanso zimene timakonda kuziganizila. Ngati timayesetsa kuganizila mmene Yehova amaonela zinthu, timafika pozindikila kuti maganizo ake ndiwo oyenela. Tikatelo, cimakhala cosavuta kusintha maganizo athu kuti agwilizane ndi maganizo ake. Komabe, malinga n’zimene Aroma 12:2 yakamba, kuti tisinthe maganizo athu kukhala ogwilizana ndi a Yehova, tifunika kuleka ‘kutengela nzelu za nthawi ino.’ Tiyenela kuleka kuloŵetsa mu mtima mwathu maganizo oipa amene ni osagwilizana na maganizo a Mulungu. Kuti timvetsetse kufunika kocita zimenezi, tiyelekezele na cakudya. Tikambe kuti munthu winawake amayesetsa kudya zakudya zopatsa thanzi n’colinga cakuti akhale na thanzi labwino. Koma kodi izi zingakhale na phindu iliyonse ngati pa nthawi imodzi-modziyo munthuyo amadya zakudya zina zoipa? Iyai. Na ise n’cimodzi-modzi. Sitingathe kuwongola maganizo athu ngati timasinkha-sinkha zinthu zabwino, koma pa nthawi imodzi-modzi n’kumawaipitsa mwa kuganizila zinthu zoipa. w18.11 21 ¶14-15
Mande, July 13
Khalani olimba, mutamanga kwambili coonadi m’ciuno mwanu.—Aef. 6:14.
Tifunika kuyesetsa kucita zinthu mogwilizana na coonadi tsiku lililonse. Tiyenela kumanga coonadi m’ciuno mwathu. M’nthawi zakale, msilikali anali kumanga lamba m’ciuno pofuna kuteteza ciunoco na ziwalo zina za m’thupi lake. Komabe, kuti lambayo amuteteze, anafunika kum’manga kwambili. Ngati sanam’mange kwambili, kapena kunjata, sanali kum’teteza mokwanila. Kodi lamba wathu wa coonadi amatiteteza bwanji? Ngati timanga kwambili coonadi monga lamba m’ciuno mwathu, cidzatiteteza kuti tisasoceletsedwe na maganizo olakwika, komanso cidzatithandiza kupanga zosankha mwanzelu. Ndipo ngati takumana na ciyeso kapena mavuto, coonadi ca m’Baibo cidzatilimbikitsa kuti tisagonje pa kucita zabwino. Mofanana ndi msilikali amene sangapite ku nkhondo alibe lamba, na ise sitifunika kuvula lamba wathu wa coonadi kapena kum’manga pang’ono. M’malomwake, tifunika kum’manga zolimba mwa kupitiliza kucita zinthu mogwilizana ndi coonadi. w18.11 12 ¶15
Ciŵili, July 14
Gula coonadi ndipo usacigulitse.—Miy. 23:23.
Kuti tipeze coonadi m’Mawu a Mulungu, pamafunika khama. Tifunika kukhala okonzeka kudzimana ciliconse kuti tipeze coonadi. Monga mmene wolemba buku la Miyambo anakambila, ‘tikagula’ kapena kuti kupeza “coonadi,” tifunika kusamala kuti ‘tisacigulitse’ kapena kucitaya. Ngakhale cinthu camahala timafunika kutailapo cinacake kuti ticipeze. Liwu la Ciheberi lomasulidwa kuti “kugula” pa Miyambo 23:23, lingatanthauzenso “kupeza.” Liwu lakuti “kugula” litanthauza kusinthanitsa cinthu cinacake na cina camtengo wapatali. Ndipo liwu lakuti “kupeza” lionetsa kufunika kocita khama. Kuti timvetsetse tanthauzo la kugula coonadi, tiyelekezele motele. Tikambe kuti winawake wakuuzani kuti ku maketi kuli “mabanana amahala.” Kodi nthocizo zingabwele zokha mozizwitsa ku nyumba kwathu? Iyai. Tidzafunika kucitapo kanthu. N’zoona kuti n’zamahala, koma tidzafunika kutailapo nthawi na mphamvu zathu mwa kupita ku maketi kukazitenga. N’cimodzimodzi na coonadi. Sitimacigula na ndalama. Komabe, timafunika kucita khama kuti ticipeze. w18.11 4 ¶4-5
Citatu, July 15
Nkhope yake inawala ngati dzuŵa. Malaya ake akunja anawala kwambili.—Mat. 17:2.
Tsiku lina Yesu anatenga Petulo, Yakobo, na Yohane n’kukwela nawo m’phili lalitali. Ali kumeneko, anaona masomphenya ocititsa cidwi. Nkhope ya Yesu na malaya ake zinawala kwambili. Kenako panaonekela anthu ena aŵili, Mose na Eliya. Iwo anayamba kukambilana na Yesu za imfa yake na kuukitsidwa kwake. (Luka 9:29-32) Ndiyeno, mtambo woyela unawaphimba. Kenako anamvela mawu a Mulungu kucokela mumtambowo. Masomphenyawa, anaonetsa ulemelelo komanso mphamvu zimene Yesu adzakhala nazo monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. Mwacionekele, izi zinam’limbikitsa Khristu na kum’patsa mphamvu yopilila mazunzo na imfa yoŵaŵa. Masomphenyawa analimbitsanso cikhulupililo ca atumwi ake. Ndipo izi zinawakonzekeletsa kaamba ka mayeselo amene anali kudzakumana nawo, komanso nchito yaikulu imene anali kudzagwila kutsogolo. Patapita zaka pafupi-fupi 30, mtumwi Petulo anakambapo za masomphenya a kusandulika kwa Yesu, kuonetsa kuti anali kuwakumbukilabe bwino masomphenyawo.—2 Pet. 1:16-18. w19.03 10 ¶7-8
Cinayi, July 16
Tikusonyeza mwa njila ina iliyonse kuti ndife atumiki a Mulungu . . . olankhula zoona.—2 Akor. 6:4, 7.
Kodi Akhristu oona amasiyana bwanji na anthu a m’zipembedzo zonama? Iwo ‘amalankhula zoona.’ (Zek. 8:16, 17) Timakamba zoona, kaya pa nkhani yaikulu kapena yaing’ono, kwa anthu osawadziŵa, anzathu a ku nchito, mabwenzi athu, ndi kwa okondedwa athu. Bwanji ngati ndimwe wacicepele, ndipo simufuna kutsalila pa zimene anzanu amacita? Musalole kukhala na umoyo wapaŵili, kuoneka monga muli na khalidwe labwino mukakhala pa nyumba kapena ku misonkhano. Koma mumasinthilatu mukakhala na acicepele a kudziko, kapena mukakhala pa malo ocezela pa intaneti. Kumeneko ni kukhala umoyo waciphamaso. Mumanama kwa makolo anu, Akhristu anzanu, komanso kwa Mulungu. (Sal. 26:4, 5) Komabe, Yehova amadziŵa ngati ‘timam’lemekeza ndi milomo yokha, koma mitima yathu ili kutali ndi iye.’ (Maliko 7:6) Conco, n’cinthu canzelu kumvela malangizo a m’Baibo akuti: “Mtima wako usamasilile anthu ocimwa, koma iwe uziopa Yehova tsiku lonse.”—Miy. 23:17. w18.10 9 ¶14-15
Cisanu, July 17
Mulungu ndiye cikondi, ndipo munthu amene amapitiliza kusonyeza cikondi, amakhalabe wogwilizana ndi Mulungu ndiponso Mulungu amakhala wogwilizana naye.—1 Yoh. 4:16.
Anthu a Mulungu ni banja lauzimu, ndipo amadziŵika na khalidwe la cikondi. (1 Yoh. 4:21) Nthawi zina, cikondi cawo cimaonekela pa zinthu zazikulu zimene amacita pothandiza abale awo. Koma cimaonekela kwambili pa zinthu zing’ono-zing’ono zimene amacitilana kaŵili-kaŵili, monga kukamba mawu olimbikitsa na kucita zinthu mokoma mtima. Tikakhala okoma mtima na oganizila ena, ndiye kuti ‘tikutsanzila Mulungu, monga ana ake okondedwa.’ (Aef. 5:1) Yesu anatengela kwambili Atate wake. Iye anati: “Bwelani kwa ine nonsenu ogwila nchito yolemetsa ndi olemedwa, ndipo ndidzakutsitsimutsani. . . , cifukwa ndine wofatsa ndi wodzicepetsa.” (Mat. 11:28, 29) Ngati titengela Khristu mwa ‘kucita zinthu moganizila anthu onyozeka,’ tidzayanjidwa na Atate wathu wakumwamba komanso tidzapeza cimwemwe coculuka. (Sal. 41:1) Conco tiyeni tipitilize kuonetsa kuti timaganizila ena m’banja, mu mpingo, na mu ulaliki. w18.09 28 ¶1-2
Ciŵelu, July 18
Ndife anchito anzake a Mulungu.—1 Akor. 3:9.
Masoka azacilengedwe akacitika, ise anthu a Mulungu timakhala na mipata yoseŵenza na Mulungu mwa kuthandiza Akhristu anzathu m’njila zambili. Mwacitsanzo, timapeleka ndalama zothandizila anthu amene akhudzidwa na tsokalo. (Yoh. 13:34, 35; Mac. 11:27-30) Tikhozanso kuthandiza mwa kugwila nawo nchito yoyeletsa, kapena kukonzanso nyumba za okhudzidwawo. Mlongo wina wa ku Poland, dzina lake Gabriela, amene nyumba yake inawonongekelatu na madzi osefukila, anakondwela pamene abale a m’mipingo ya pafupi anabwela kudzam’thandiza. Iye anati: “Olo kuti n’nataya zinthu zambili, sinidandaula kwambili na zimenezo. Koma lekani nikuuzeni mapindu amene napeza. Zimene zinacitikazi zanithandiza kuona kuti kukhala mu mpingo wacikhristu ni mwayi waukulu, komanso kumabweletsa cimwemwe.” Ambili amene amalandila thandizo pakacitika masoka azacilengedwe amamvela cimodzi-modzi. Ndipo anthu amene amaseŵenza na Yehova mwa kupeleka thandizo pa zocitika ngati zimenezi, nawonso amapeza cimwemwe coculuka.—Mac. 20:35; 2 Akor. 9:6, 7. w18.08 26 ¶12
Sondo, July 19
Uteteze mtima wako.—Miy. 4:23.
Kuti tikwanitse kuteteza mtima wathu, tifunika kudziŵa zimene zingauwononge na kucitapo kanthu mwamsanga kuti tiucinjilize. Liwu lakuti ‘kuteteza’ litikumbutsa za nchito ya mlonda. M’nthawi yakale, mlonda anali kukhala pamwamba pa mpanda wa mzinda, ndipo akaona kuti kukubwela adani, anali kucenjeza anthu. Kuganizila zimene alonda anali kucita, kungatithandize kudziŵa zimene tifunika kucita kuti tisalole Satana kuipitsa maganizo athu. M’masiku akale, mlonda anali kuseŵenza mothandizana ndi alonda a pa geti ya mzinda. (2 Sam. 18:24-26) Capamodzi, iwo anali kuteteza mzinda wawo mwa kuonetsetsa kuti mageti onse ni otseka ngati kukubwela adani. (Neh. 7:1-3) Cikumbumtima cathu cophunzitsidwa Baibo naconso cimagwila nchito ngati mlonda wathu. Cimaticenjeza ngati Satana afuna kuwononga mtima wathu wophiphilitsa. M’mawu ena, cimaticenjeza ngati Satana afuna kutisonkhezela kukhala na maganizo oipa, zolinga, kapena zilakolako zoipa. Conco, nthawi zonse cikumbumtima cathu cikaticenjeza, tifunika kumvetsela na kutseka geti ya mtima wathu, titelo kukamba kwake. w19.01 17 ¶10-11
Mande, July 20
Atumikile monga atumiki, popeza ndi opanda cifukwa cowanenezela.—1 Tim. 3:10.
Abale acinyamata afunika kupendedwa mogwilizana na ziyenelezo za m’Mawu a Mulungu, osati maganizo kapena miyambo ya anthu. (2 Tim. 3:16, 17) Kutengela miyambo ya anthu yaconco kungapangitse kuti abale oyenelela azingokhala osaikidwa pa udindo. Mwacitsanzo, m’dziko lina mtumiki wothandiza woyenelela anapatsidwa maudindo ambili akulu-akulu. Olo kuti akulu mu mpingo wake anaona kuti m’baleyo akukwanilitsa ziyenelezo za m’Malemba zokhalila mkulu, iwo sanam’muyeneleze kuti aikidwe pa udindowu. Cifukwa ciani? Akulu ena acikulile mu mpingowo anali kuumilila kuti m’baleyo akali wacicepele cakuti sangayenelele kukhala mkulu. N’zomvetsa cisoni kuti m’baleyo sanapatsidwe mwayi wokhala mkulu cabe cifukwa cakuti anali kumuona monga wacicepele kwambili. Malipoti aonetsa kuti m’maiko enanso, anthu ali na maganizo otelo. Conco n’kofunika kwambili kuti tizidalila Malemba m’malo modalila nzelu zathu. Tikatelo, tidzaonetsa kuti timamvela zimene Yesu anatilamula zakuti sitiyenela kuweluza ena potengela maonekedwe awo akunja.—Yoh. 7:24. w18.08 12 ¶16-17
Ciŵili, July 21
Munthu aliyense woyankhila nkhani asanaimvetsetse n’ngopusa, ndipo amacita manyazi.—Miy. 18:13.
Pali vuto limene lingakhalepo ngati tili na cizoloŵezi cothamangila kutumila ena imelo kapena mameseji amene talandila. Ku maiko ena, cipembedzo ca Mboni za Yehova n’coletsedwa. M’maiko aconco, otsutsa angafalitse mwadala nkhani zabodza pofuna kutiyofyeza kapena kuticititsa kuyamba kukayikilana. Ganizilani zimene zinacitika m’dziko limene kale linali kuchedwa Soviet Union. Gulu la apolisi acisinsi, lochedwa KGB, linafalitsa nkhani yabodza yakuti abale ena oyang’anila pa nthambi anapandukila gulu la Yehova. Ambili anakhulupilila nkhaniyo cakuti anadzilekanitsa na gulu la Yehova. Zinali zomvetsa cisoni kwambili! Koma cokondweletsa n’cakuti ambili anabwelela. Ngakhale zinali conco, ena sanabwelele. Cikhulupililo cawo cinasweka ngati ngalawa. (1 Tim. 1:19) Kodi tingapewe bwanji vuto ngati limeneli? Musamafalitse nkhani zofooketsa kapena zopanda umboni. Musamangokhulupilila zilizonse zimene mwamva. Koma muziyesetsa kudziŵa zoona zeni-zeni pa nkhaniyo. w18.08 4 ¶8
Citatu, July 22
Ndithu ndikukuuza lelo, iwe udzakhala ndi ine m’Paradaiso. —Luka 23:43.
Olemba mipukutu ya Baibo yakale kwambili ya Cigiriki, nthawi zina sanali kugwilitsila nchito zizindikilo za m’kalembedwe. Conco, tingafunse kuti: Kodi pa lembali Yesu anakamba kuti, “Ndithu ndikukuuza, lelo iwe udzakhala ndi ine m’Paradaiso”? Kapena anakamba kuti: “Ndithu ndikukuuza lelo, iwe udzakhala ndi ine m’Paradaiso”? Kumbukilani kuti Yesu anali atauza ophunzila ake kuti: “Mwana wa munthu adzakhala mumtima wa dziko lapansi masiku atatu, usana ndi usiku.” (Mat. 12:40; 16:21; 17:22, 23; Maliko 10:34; Mac. 10:39, 40) Conco, Yesu na cigaŵenga cija sanapite ku Paradaiso pa tsiku limene iwo anafa. Yesu anakhala “m’Manda” kwa masiku angapo, kufikila pamene Mulungu anamuukitsa. (Mac. 2:31, 32) Pamene Yesu analonjeza Paradaiso kwa cigaŵenga cija, sanali kukamba za paradaiso wakumwamba. N’cifukwa ciani takamba conco? Cifukwa cimodzi n’cakuti cigaŵengaco sicinali kudziŵa kuti Yesu anali atacita pangano na atumwi ake okhulupilika kuti adzakhala naye mu Ufumu kumwamba. (Luka 22:29) Kuwonjezela apo, cigaŵengaco sicinabatizike kapena kudzozedwa na mzimu woyela. (Yoh. 3:3-6, 12) Conco, paradaiso amene Yesu analonjeza kwa cigaŵengaco ni wa pa dziko lapansi amene anali kudzakwanilitsidwa m’tsogolo. w18.12 6 ¶17-18, 20-21
Cinayi, July 23
Tipangile mulungu woti atitsogolele, cifukwa sitikudziŵa zimene zacitikila Mose.—Eks. 32:1.
Posapita nthawi, Aisraeli anayamba kulambila mwana wa ng’ombe. Olo kuti anali atacita chimo, Aisiraeli ayenela kuti anali kuganiza kuti akali ku mbali ya Yehova. Izi zionekela bwino pa zimene Aroni anakamba. Iye ananena kuti kulambila mwana wa ng’ombeko cinali “cikondwelelo ca Yehova.” Kodi Yehova anamvela bwanji? Anaona kuti anthuwo am’pandukila. Yehova anauza Mose kuti iwo ‘anacita zinthu zowawonongetsa’ komanso kuti ‘anapatuka mofulumila panjila imene iye anawalamula kuyendamo.’ Yehova anakwiya kwambili cakuti anafuna kufafaniza mtundu wonse wa Isiraeli. (Eks. 32:5-10) Komabe, Yehova anaganiza zakuti asawononge mtundu wonse wa Aisiraeli. (Eks. 32:14) Olo kuti Aroni ndiye anapanga fanolo, iye analapa na kukhala ku mbali ya Yehova pamodzi na alevi anzake. Koma Aisiraeli masauzande anaphedwa cifukwa ca kulambila fano, ndipo amene anali ku mbali ya Yehova analonjezedwa kuti adzadalitsidwa.—Eks. 32:26-29. w18.07 20 ¶13-16
Cisanu, July 24
Cenjelani ndi alembi . . . Amakonda kupatsidwa moni m’misika . . . Amakondanso malo olemekezeka kwambili pa cakudya camadzulo.—Luka 20:46.
Kodi cofunika kwambili ni kuyesetsa kukhala wodziŵika kwa ndani? Anthu m’dzikoli amafuna kukhala odziŵika kwambili kwa ena pa zamaphunzilo, bizinesi, kapena pa zamaseŵela. Koma ise timafuna kukhala odziŵika kwa Mulungu, monga mmene Paulo anakambila, pamene anati: “Tsopano pamene mwadziŵa Mulungu, kapena tinene kuti tsopano pamene mwadziŵidwa ndi Mulungu, mukubwelelanso bwanji ku mfundo zacibwanabwana, zomwe ndi zosathandiza ndiponso zopanda pake, n’kumafuna kukhalanso akapolo ake?” (Agal. 4:9) Ndithudi! Ni mwayi waukulu kwambili ‘kudziŵidwa ndi Mulungu,’ Wolamulila Wamkulu wa cilengedwe conse. Iye ni wokonzeka kupanga ubwenzi wabwino na ise. Monga mmene katswili wina anakambila, tikakhala mabwenzi ake, iye “amationa kukhala ofunika kwambili na kutikonda.” Komanso, tikakhala mabwenzi a Yehova, m’pamene timaona kuti umoyo wathu uli na phindu.—Mlal. 12:13, 14. w18.07 8 ¶3-4
Ciŵelu, July 25
Ndimasinkhasinkha zikumbutso zanu.—Sal. 119:99.
Kuti tipindule na malamulo a Mulungu, tifunika kumayakonda na kuyalemekeza. (Amosi 5:15) Koma kodi tingacite bwanji zimenezi? Cofunika kwambili ni kuphunzila kuona zinthu mmene Yehova amazionela. Mwacitsanzo, tiyelekezele kuti imwe muli na vuto losoŵa tulo. Mutapita kucipatala, dokota wakupatsani malangizo okhudza kadyedwe, kucita maseŵela olimbitsa thupi, na kusintha zinthu zina mu umoyo wanu. Pambuyo potsatila malangizowo, mukuona kuti mwayamba kugona bwino tsopano. Mwacionekele, mungamuyamikile dokotayo cifukwa cokuthandizani kuthetsa vuto lanu. Mofanana ndi zimenezi, Mlengi wathu watipatsa malamulo amene angatiteteze ku zotulukapo zoipa za ucimo na kutithandiza kukhala na umoyo wabwino. Ganizilani cabe mmene timapindulila cifukwa comvela malamulo a m’Baibo oletsa kunama, kucita cinyengo, kuba, ciwelewele, ciwawa, na zamizimu. (Miy. 6:16-19; Chiv. 21:8) Tikaona mapindu amene timapeza cifukwa comvela malamulo a Yehova, timayamba kukonda na kuyamikila kwambili Yehova na malamulo ake. w18.06 17 ¶5-6
Sondo, July 26
Kodi ndiwe mfumu ya Ayuda?—Yoh. 18:33.
N’kutheka kuti Pilato anali kudela nkhawa kuti mwina Yesu angayambitse msokonezo pa zandale. Iyi ndiyo inali nkhawa yaikulu ya Pilato mu ulamulilo wake wonse. Yesu anamuyankha kuti: “Ufumu wanga suli mbali ya dziko lino.” (Yoh. 18:36) Yesu sanafune kutenga mbali m’zandale cifukwa Ufumu wake ni wakumwamba. Iye anauza Pilato kuti cimene anabwelela pa dziko lapansi ni “kudzacitila umboni coonadi.” (Yoh. 18:37) Na ise ngati timaidziŵa bwino nchito yathu mofanana ndi Yesu, tidzapewa kucilikiza ngakhale mwakacetecete magulu andale omenyela ufulu wodzilamulila. Nthawi zina, kucita izi kungakhale kovuta. Woyang’anila dela wina anati: “Masiku ano, anthu ambili m’dela lathu amafunitsitsa kuti zinthu zisinthe pa zandale. Mzimu wokonda dziko lako ukukulila-kulila, ndipo ambili amakhulupilila kuti kukhala na ufulu wodzilamulila kungawathandize kukhala na umoyo wabwino. Koma cokondweletsa n’cakuti abale amaika mtima wawo wonse pa nchito yolalikila uthenga wabwino wa Ufumu. Izi zathandiza kuti akhalebe ogwilizana. Iwo amadalila Mulungu kuti ndiye adzathetsa zinthu zopanda cilungamo na mavuto ena amene timakumana nawo.” w18.06 4-5 ¶6-7
Mande, July 27
Tsutsani Mdyelekezi ndipo adzakuthaŵani.—Yak. 4:7.
Ni mabuku atatu cabe a m’Malemba Aciheberi amene amachulako dzina lakuti Satana, limene limatanthauza “Wotsutsa.” Mabuku amenewa ni 1 Mbiri, Yobu, na Zekariya. N’cifukwa ciani Mulungu sanavumbule zambili zokhudza mdani ameneyu Mesiya asanabwele? Mwacionekele, Yehova sanafune kuchukitsa Satana mwa kuuzila atumiki ake kulemba zambili zokhudza iye na zocita zake m’Malemba Aciheberi. Colinga cacikulu cimene Yehova anauzila anthu kulemba cigawo cimeneci ca Baibo, cinali cakuti adziŵikitse Mesiya na kutsogolela anthu ake kwa iye. (Luka 24:44; Agal. 3:24) Colinga cake citakwanilitsidwa komanso Mesiya atabwela, Yehova anamuseŵenzetsa pamodzi na ophunzila ake povumbula zambili zokhudza Satana na angelo amene anakhala ku mbali yake. Kucita izi kunali koyenela, cifukwa Yesu na odzozedwa amene adzalamulila nawo pamodzi, ni amene Yehova adzawaseŵenzetsa pophwanya Satana na otsatila ake. (Aroma 16:20; Chiv. 17:14; 20:10. Kumbukilani kuti mphamvu za Mdyelekezi zili na pothela. Ku mbali yathu tili na Yehova, Yesu, na angelo okhulupilika. Mwa thandizo lawo, tingakwanitse kumutsutsa Satana. w18.05 22-23 ¶2-4
Ciŵili, July 28
Nthambi iliyonse mwa ine yosabala zipatso amaidula.—Yoh. 15:2.
Yehova amationa kukhala atumiki ake kokha ngati tibala zipatso. (Mat. 13:23; 21:43) Conco, kulingana na fanizo la pa Yoh. 15:1-5, zipatso zimene Mkhristu aliyense afunika kubala sizitanthauza ophunzila atsopano amene tingapange iyai. (Mat. 28:19) Cikanakhala kuti zimatanthauza ophunzila amene timapanga, ndiye kuti atumiki okhulupilika amene sakhala na mwayi wopanga ophunzila cifukwa colalikila m’gawo louma, akanakhala ngati nthambi zosabala za m’fanizo la Yesu. Koma sizingakhale conco iyai. Cifukwa ciani? Cifukwa cakuti sitingakakamize anthu kukhala ophunzila a Khristu. Ndipo Yehova ni wacikondi. Satilamula kucita zinthu zimene sitingakwanitse. Koma nthawi zonse, amatilamula kucita zimene tingakwanitse. Conco, iye sangaone atumiki ake kukhala osayenelela, cabe cifukwa cakuti alibe maphunzilo a Baibo. (Deut. 30:11-14) Nanga zipatso zimene tifunika kubala n’ciani? Mwacionekele, zipatso zimenezi zimatanthauza nchito imene aliyense wa ise angakwanitse kucita. Nchito yanji? Yolalikila uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu.—Mat. 24:14. w18.05 14 ¶8-9
Citatu, July 29
Inu ndinu ocokela kwa atate wanu Mdyelekezi, . . . iye ndi wabodza komanso tate wake wa bodza.—Yoh. 8:44.
Ena amachedwa na maina monga akuti a pasta, ansembe, abusa, arabi, ndi maina ena ambili. Mofanana ndi atsogoleli acipembedzo a m’nthawi ya Yesu, anthu amenewa “akupondeleza coonadi” ca Mawu a Mulungu, ndipo ‘asinthanitsa coonadi ca Mulungu ndi bodza.’ (Aroma 1:18, 25) Iwo amafalitsa ziphunzitso zabodza, monga cakuti munthu ali na mzimu wosafa, ca Helo wa moto, komanso cakuti munthu akafa amakabadwanso kwina. Amafalitsanso ciphunzitso copusa cakuti Mulungu amavomeleza mathanyula (kugonana kwa amuna kapena akazi okha-okha), komanso vikwati va amuna kapena akazi okha-okha. Atsogoleli andale nawonso asoceletsa anthu na mabodza awo. Posacedwa, tidzamvela bodza lam’kunkhuniza, pamene anthu adzalengeza kuti akwanitsa kukhazikitsa “bata ndi mtendele” pa dziko lapansi. Koma “ciwonongeko codzidzimutsa cidzafika pa iwo nthawi yomweyo.” Tiyenela kusamala kuti tisakasoceletsedwe na bodza lawo lakuti pa dziko pali mtendele, koma pamene m’ceni-ceni pali mavuto ambili. Ise Akhristu ‘tikudziwa bwino kuti tsiku la Yehova lidzabwela ndendende ngati mbala usiku.’—1 Ates. 5:1-4. w18.10 7-8 ¶6-8
Cinayi, July 30
Muthandize ofookawo, ndipo muzikumbukila mawu a Ambuye Yesu. Pajatu iye anati, ‘Kupatsa kumabweletsa cimwemwe coculuka kuposa kulandila.’—Mac. 20:35.
Yesu Khristu amapeleka cilimbikitso na citsogozo kwa abale na alongo olefuka na opsinjika maganizo. Amacita izi kupitila mwa abale ake odzozedwa ndi “akalonga,” amene ni akulu a m’gulu la nkhosa zina. Akulu amenewa si “olamulila” cikhulupililo ca ena, koma ni ‘anchito anzathu’ amene amatithandiza kukhala na cimwemwe. (Yes. 32:1, 2; 2 Akor. 1:24) Mtumwi Paulo anatisiila citsanzo cimene tiyenela kutengela. Polembela kalata Akhristu a ku Tesalonika amene anali kukumana na cizunzo, iye anati: “Popeza timakukondani kwambili, tinali okonzeka kukupatsani uthenga wabwino wa Mulungu. Ndipotu osati uthenga wokha ayi, komanso miyoyo yathu yeni-yeniyo, cifukwa tinakukondani kwambili.” (1 Ates. 2:8) Pokamba na akulu a mu mpingo wa ku Efeso, Paulo anaonetsa kuti kulimbikitsa ena na mawu cabe, nthawi zina sikukhala kokwanila. Iye anawauza mawu a mu lemba lalelo. w18.04 21-22 ¶6-8
Cisanu, July 31
Yehova ndiye Mzimu, ndipo pamene pali mzimu wa Yehova, pali ufulu.—2 Akor. 3:17.
Kuti tikhale na ufulu umenewu na kupindula nawo, tifunika ‘kutembenukila kwa Yehova,’ kutanthauza kukhala naye paubwenzi wabwino. (2 Akor. 3:16) Aisiraeli m’cipululu sanayamikile zimene Yehova anali kuwacitila. Iwo anaumitsa mitima yawo na maganizo awo, ndipo ufulu umene anakhala nawo atatulutsiwa mu Iguputo, anali kungouseŵenzetsa pokhutilitsa zofuna zawo na zilakolako zawo. (Aheb. 3:8-10) Ufulu umene mzimu wa Yehova umabweletsa, ni wapamwamba ngako kuposa ufulu umene munthu amakhala nawo akamasulidwa mu ukapolo wakuthupi. Mosiyana kwambili na ufulu uliwonse wocokela kwa anthu, mzimu wa Yehova ungatimasule ku ukapolo wa ucimo na imfa, ndi ku ukapolo wa cipembedzo conama na miyambo yake. (Aroma 6:23; 8:2) Ndithudi! Uwu ni ufulu waukulu kwambili. Ndipo munthu angakhale na ufulu umenewu olo pamene ali m’jele.—Gen. 39:20-23. w18.04 9 ¶3-5