LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • es20 masa. 78-88
  • August

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • August
  • Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2020
  • Tumitu
  • Ciŵelu, August 1
  • Sondo, August 2
  • Mande, August 3
  • Ciŵili, August 4
  • Citatu, August 5
  • Cinayi, August 6
  • Cisanu, August 7
  • Ciŵelu, August 8
  • Sondo, August 9
  • Mande, August 10
  • Ciŵili, August 11
  • Citatu, August 12
  • Cinayi, August 13
  • Cisanu, August 14
  • Ciŵelu, August 15
  • Sondo, August 16
  • Mande, August 17
  • Ciŵili, August 18
  • Citatu, August 19
  • Cinayi, August 20
  • Cisanu, August 21
  • Ciŵelu, August 22
  • Sondo, August 23
  • Mande, August 24
  • Ciŵili, August 25
  • Citatu, August 26
  • Cinayi, August 27
  • Cisanu, August 28
  • Ciŵelu, August 29
  • Sondo, August 30
  • Mande, August 31
Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2020
es20 masa. 78-88

August

Ciŵelu, August 1

Mulungu akuonetsa cikondi cake kwa ife, moti pamene tinali ocimwa, Khristu anatifela. —Aroma 5:8.

Nthawi zambili tikapezeka pa misonkhano, timakumbutsidwa zabwino zimene Yehova na Yesu anaticitila. Cifukwa cakuti timayamikila kwambili dipo, timayesetsa nthawi zonse kutengela Yesu pa zocita zathu. (2 Akor. 5:14, 15) Kuwonjezela apo, mtima wathu woyamikila umatisonkhezela kutamanda Yehova kaamba ka dipo limene anapeleka. Njila imodzi imene tingam’tamandile ni mwa kupeleka ndemanga pa misonkhano. Tingaonetse kuti timakonda kwambili Yehova na Mwana wake, mwa kukhala okonzeka kudzimana zinthu zina kuti ticite zinthu zowakondweletsa. Nthawi zambili, timafunika kudzimana zinthu zina n’colinga cakuti tikapezeke pa misonkhano. Mwacitsanzo, mipingo yambili imacita msonkhano wa Umoyo na Utumiki mkati mwa wiki madzulo. Pa nthawiyi, ena timakhala kuti tangocoka kumene ku nchito, ndipo ndife olema. Msonkhano wina umacitika kumapeto kwa wiki, pamene ena amaona kuti ndiyo nthawi yopumula. Kodi Yehova amayamikila tikamayesetsa kupezeka pa misonkhano ngakhale pamene tili olema? N’zosacita kufunsa! Yehova amayamikila kwambili ngati ticita zilizonse zotheka kuti tikapezekepo pa misonkhano, poonetsa cikondi cathu pa iye.—Maliko 12:41-44. w19.01 29 ¶12-13

Sondo, August 2

Pamene Ambuye anaona mayiwo, anawamvela cifundo.—Luka 7:13.

Yesu anakumanapo na mavuto ena amene anthu a m’nthawi yake anali kukumana nawo. Mwacitsanzo, cioneka kuti iye anabadwila m’banja losauka. Pamene anali kuseŵenza na Yosefe, atate wake omulela, iye anaphunzila kugwila nchito zolemetsa. (Mat. 13:55; Maliko 6: 3) Komanso, zioneka kuti Yosefe anamwalila Yesu asanayambe utumiki wake. Conco, n’zoonekelatu kuti Yesu anaona mmene cimaŵaŵila ngati munthu amene umakonda wamwalila. Iye anali kudziŵanso bwino mavuto amene amakhalapo m’banja, ngati anthu ali na zikhulupililo zosiyana. (Yoh. 7: 5) Zokumana nazo zimenezi na zina, ziyenela kuti zinathandiza Yesu kumvetsetsa mavuto amene anthu ena anali kukumana nawo, komanso mmene anali kumvelela. Yesu anaonetsa bwino kwambili cifundo cake mwa kucita zozizwitsa. Iye sanacite zozizwitsa mwamwambo cabe. Koma anali ‘kugwidwa cifundo,’ poona anthu ovutika. (Mat. 20:29-34; Maliko 1:40-42) Yesu anawamvelela cifundo anthu amenewa, ndipo anafuna kuwathandiza.—Maliko 7:32-35; Luka 7:12-15. w19.03 16 ¶10-11

Mande, August 3

Pitilizani kulolelana ndi kukhululukilana ndi mtima wonse. —Akol. 3:13.

Usiku wakuti maŵa adzaphedwa, Yesu anavutika maganizo. Iye anafunika kukhala wokhulupilika mpaka imfa, cifukwa miyoyo ya anthu mabiliyoni ambili inadalila pa kukhulupilika kwake. (Aroma 5:18, 19) Kuwonjezela apo, zocita zake zikanakhudza dzina la Atate ŵake. (Yobu 2:4) Komanso, pamene anali kudya cakudya cothela pamodzi na atumwi ake, pakati pa atumwiwo “panabuka mkangano woopsa.” Iwo anali kukangana za “amene anali kuoneka wamkulu kwambili” pakati pawo. N’zocititsa cidwi kuona kuti Yesu sanakwiye. M’malomwake, anacita nawo zinthu modekha. Mokoma mtima, Yesu anawapatsanso malangizo mosapita m’mbali pa nkhaniyo. Ndiyeno, anawayamikila cifukwa coonetsa kukhulupilika mwa kukhalabe naye mu umoyo wake wonse (Luka 22:24-28; Yoh. 13:1-5, 12-15) N’zotheka kutengela citsanzo ca Yesu mwa kukhalabe odekha, olo pamene tili opanikizika maganizo. Tiyenela kukumbukila kuti tonsefe timakamba kapena kucita zinthu zimene zingakhumudwitse ena. (Miy. 12:18; Yak. 3:2, 5) Cinanso, tiyenela kukhala na cizoloŵezi coyamikila abale athu pa zabwino zimene amacita.—Aef. 4:29. w19.02 11 ¶16-17

Ciŵili, August 4

Yehova . . . adzakhazikitsa mpando wake wacifumu kuti aweluze.—Sal. 9:7.

Cilamulo cinacepetsa vuto la kunenezana milandu ya bodza. Munthu woimbidwa mlandu anali kukhala na ufulu wodziŵa munthu amene anali kumuimba mlandu. (Deut. 19:16-19; 25:1) Ndipo panafunikila mboni zosacepela ziŵili kuti munthuyo aweluzidwe kuti ni wolakwa. (Deut. 17:6; 19:15) Nanga bwanji ngati Mwisiraeli wacita colakwa cimene caonedwa na munthu mmodzi cabe? Sikuti munthuyo anali na mwayi wozemba cilango, cifukwa Yehova anali kuona zonse. Ndithudi, Yehova amapeleka citsanzo cabwino kwambili pa nkhani yocita zinthu mwacilungamo. Iye amadalitsa anthu amene amatsatila miyezo yake mokhulupilika. Koma amalanga anthu amene amaseŵenzetsa ulamulilo wawo molakwika. (2 Sam. 22:21-23; Ezek. 9:9, 10) Anthu ena angacite zoipa na kuganiza kuti azemba cilango. Koma panthawi yake yoyenela, Yehova adzawaweluza mogwilizana na zolakwa zawo. (Miy. 28:13) Ndipo ngati salapa, posacedwa adzazindikila kuti “kulandila cilango cocokela kwa Mulungu wamoyo n’cinthu coopsa.”—Aheb. 10:30, 31. w19.02 23-24 ¶20-21

Citatu, August 5

Mu Isiraeli simunakhalebe mneneli aliyense wofanana ndi Mose, amene Yehova anali kumudziŵa pamasom’pamaso.—Deut. 34:10.

Mose anali kukonda kuyang’ana kwa Yehova kuti am’patse malangizo. Baibo imati iye “anapitiliza kupilila moleza mtima ngati kuti akuona Wosaonekayo.” (Aheb 11:24-27) Pasanathe miyezi iŵili kucokela pamene Aisiraeli anacoka ku Iguputo, komanso asanafike ngakhale pa Phili la Sinai, pakati pawo panabuka vuto lalikulu. Anthuwo anayamba kudandaula cifukwa ca kusoŵa kwa madzi. Iwo anayamba kudandaulila Mose, ndipo vutolo linakula kwambili cakuti Mose anafuulila Yehova kuti: “Nditani nawo anthuwa? Angotsala pang’ono kundiponya miyala!” (Eks. 17:4) Poona zimenezi, Yehova anapatsa Mose malangizo omveka bwino. Anamuuza kuti atenge ndodo yake na kukamenya thanthwe ku Horebe, kuti madzi akatuluke m’thanthwelo. Nkhaniyo imati: “Mose anacitadi zomwezo, pamaso pa akulu a Isiraeli.” Aisiraeli anamwa madzi, ndipo vuto la kusoŵa madzi linatha.—Eks. 17:5, 6. w18.07 13 ¶4-5

Cinayi, August 6

Cikondi cimamangilila. —1 Akor. 8:1.

Yehova amatilimbikitsanso mwacikondi poseŵenzetsa mpingo. Aliyense wa ise angaonetse kuyamikila cikondi ca Yehova mwa kukonda na kulimbikitsa abale na alongo athu mwauzimu komanso kuwatonthoza. (1 Yoh. 4:19-21) Mtumwi Paulo anauza Akhristu anzake kuti: “Pitilizani kutonthozana ndi kulimbikitsana monga mmene mukucitila.” (1 Ates. 5:11) Aliyense mu mpingo, osati akulu cabe, angatengele citsanzo ca Yehova na Yesu mwa kutonthoza na kulimbikitsa abale na alongo athu. (Aroma 15:1, 2) Ena mu mpingo angakhale na matenda ovutika maganizo, ndipo angafunike kupeza cithandizo kwa madokota odziŵa za matendawa. (Luka 5:31) Akulu na ofalitsa mumpingo si akatswili a matenda a maganizo. Ngakhale n’conco, iwo angathandize mwa ‘kulankhula molimbikitsa kwa amtima wacisoni, kuthandiza ofooka, kukhala oleza mtima kwa onse.’—1 Ates. 5:14. w18.09 14-15 ¶10-11

Cisanu, August 7

Usayang’ane uku ndi uku mwamantha, pakuti ine ndine Mulungu wako.—Yes. 41:10.

Kuti tiyambe kudalila kwambili Yehova, tifunika kum’dziŵa bwino. Ndipo njila imodzi yokha imene tingam’dziŵile bwino, ni mwa kuŵelenga Baibo n’colinga cofuna kuimvetsetsa, komanso kusinkha-sinkha pa zimene timaŵelenga. M’Baibo, muli nkhani zofotokoza mmene Yehova anatetezela atumiki ake akale. Nkhani zimenezi, zimatithandiza kukhala na cidalilo cakuti Yehova adzatisamalila. Ganizilani za mawu ofanizila ogwila mtima, amene Yesaya anaseŵenzetsa poonetsa mmene Yehova amatitetezela. Iye anayelekezela Yehova na mbusa, komanso atumiki ake na nkhosa. Pokamba za Yehova, Yesaya anati: “Adzasonkhanitsa pamodzi ana a nkhosa ndi [“mkono,” NW-E] wake, ndipo adzawanyamulila pacifuwa pake.” (Yes. 40:11) Tikaona mmene Yehova amatitetezela na mkono wake wamphamvu, sitikhalanso na mantha. Kuti musacite mantha ngakhale mutakumana na mavuto, muzisinkha-sinkha mawu olimbikitsa amenewa a m’lemba la lelo. Adzakuthandizani kukhala olimba mukadzakumana na mavuto kutsogolo. w19.01 7 ¶17-18

Ciŵelu, August 8

Ndimakondwela ndi kucita cifunilo canu, inu Mulungu wanga. —Sal. 40:8.

Kodi muli na zolinga zauzimu zimene mukuyesetsa kuzikwanilitsa? Mwina munadziikila colinga cakuti muziŵelenga macaputa angapo a Baibo tsiku lililonse. Kapena mukuyesetsa kukulitsa luso la kukamba nkhani na kuphunzitsa. Kodi mumamvela bwanji ngati mwaona kuti mukupita patsogolo, kapena ngati wina waona kupita patsogolo kwanu na kukuyamikilani? Mwacionekele, mumamvela bwino komanso mumakhala na cimwemwe. Cifukwa ciani? Cifukwa mudziŵa kuti mukucita cifunilo ca Mulungu, monga mmene Yesu anacitila. (Miy. 27:11) Ngati muika maganizo anu pa kutumikila Yehova, mumakhala acimwemwe podziŵa kuti zimene mukucita sizingapite pacabe. Mtumwi Paulo anati: “Khalani olimba, osasunthika, okhala ndi zocita zambili nthawi zonse mu nchito ya Ambuye, podziŵa kuti zonse zimene mukucita mu nchito ya Ambuye sizidzapita pacabe.” (1 Akor. 15:58) Mosiyana na zimenezi, anthu amene amaika maganizo awo onse pa zolinga zakuthupi, angaoneke kuti zinthu zikuwayendela, koma pamapeto pake amagwilitsidwa mwala.—Luka 9:25. w18.12 22 ¶12-13

Sondo, August 9

Olungama adzalandila dziko lapansi.—Sal. 37:29.

Davide anakambilatu za nthawi pamene anthu pa dziko lapansi adzayamba kutsatila njila zolungama za Mulungu. (2 Pet. 3:13) Ulosi wa pa Yesaya 65:22 umati: “Masiku a anthu anga adzakhala ngati masiku a mtengo.” Izi zionetsa kuti anthu adzayamba kukhala na moyo kwa zaka masauzande ambili. Malinga n’zimene Chivumbulutso 21:1-4 imakamba, Mulungu adzakhala na anthu ake. Ndipo iye analonjeza kuti “imfa sidzakhalaponso” pakati pa atumiki ake amene adzakhala m’dziko latsopano. Adamu na Hava anataya mwayi wokhala m’Paradaiso m’munda wa Edeni. Koma ngakhale n’conco, Paradaiso adzabwezeletsedwa. Monga mmene Mulungu analonjezela, anthu pa dziko lapansi adzadalitsidwa. (Sal. 37:11) Mouzilidwa, Davide anakamba kuti ofatsa na olungama adzalandila dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya. Maulosi a m’buku la Yesaya afunika kukulitsa cikhumbo cathu cokasangalala na madalitso a kutsogolo amenewa. (Yes. 11:6-9; 35:5-10; 65:21-23) Kodi zimenezi zidzacitika liti? Zidzacitika pa nthawi imene Yesu adzakwanilitsa lonjezo lake kwa cigaŵenga caciyuda cija. (Luka 23:43) Ndipo na imwe mungakhale na mwayi wokakhala m’Paradaiso ameneyo. w18.12 7 ¶22-23

Mande, August 10

Uteteze mtima wako kuposa zonse zimene ziyenela kutetezedwa.—Miy. 4:23.

Kodi n’zotheka kupewelatu maganizo a dziko? Iyai. N’zosatheka cifuwa tikukhala m’dziko lomweli. (1 Akor. 5:9, 10) Mwacitsanzo, tikayenda mu ulaliki, timakambilana na anthu amene ali na zikhulupililo zabodza. Ngakhale kuti n’zosatheka kupewelatu maganizo a dziko, sitiyenela kuwalekelela akabwela mu mtima mwathu kapena kuwalola kuzika mizu. Mofanana ndi Yesu, mwamsanga tiyenela kukana maganizo alionse ogwilizana na zolinga za Satana. Kuwonjezela apo, pali zinthu zina zimene tingacite kuti tipewe kutengela nzelu za dziko. Mwacitsanzo, tiyenela kusamala posankha mabwenzi. Baibo imaticenjeza kuti ngati tigwilizana na anthu amene salambila Yehova, tingayambe kutengela maganizo awo. (Miy. 13:20; 1 Akor. 15:12, 32, 33) Tiyenelanso kupewa zosangalatsa zimene zimalimbikitsa ciphunzitso ca cisanduliko, zaciwawa, kapena zaciwelewele. Tikatelo, tidzapewa kuipitsa maganizo athu ndi mfundo ‘zotsutsana ndi kudziŵa Mulungu.’—2 Akor. 10:5. w18.11 21 ¶16-17

Ciŵili, August 11

Ndidzayenda m’coonadi canu.—Sal. 86:11.

N’ciani cingatithandize ‘kupitilizabe kuyenda m’coonadi’? Njila yoyamba ni kutengako mbali mokwanila pa nchito yophunzitsa anthu coonadi ca m’Baibo. Kucita izi kudzakuthandizani kugwilitsitsa lupanga lauzimu, limene ni “mawu a Mulungu.” (Aef. 6:17) Monga aphunzitsi a Mawu a Mulungu, ise tonse tifunika kuyesetsa kunola luso lathu, kuti tizitha ‘kuphunzitsa ndi kufotokoza bwino mawu a coonadi.” (2 Tim. 2:15) Pamene tiseŵenzetsa Baibo pothandiza ena kumvetsetsa coonadi na kukana ziphunzitso zabodza, timakhomeleza mawu a Mulungu mu mtima na m’maganizo mwathu. Kucita izi kumatilimbikitsa kuyendabe m’coonadi. Coonadi ni mphatso yamtengo wapatali imene Yehova watipatsa. Mphatso imeneyi imatithandiza kukhala pa ubwenzi wolimba na Atate wathu wakumwamba. Ubwenzi umenewu ni cinthu camtengo wapatali kwambili kuposa ciliconse cimene tili naco. Zimene Yehova watiphunzitsa kufika pano ni dyonkho cabe. Iye watilonjeza moyo wosatha. Ndipo panthawiyo tidzaphunzila mfundo zambili-mbili za coonadi, kuwonjezela pa zimene taphunzila kale. Conco, muziona coonadi monga ngale yamtengo wapatali. Pitilizani ‘kugula coonadi ndipo musacigulitse.’—Miy. 23:23. w18.11 8 ¶2; 12 ¶15-17

Citatu, August 12

Nowa, [anali] mlaliki wa cilungamo.—2 Pet. 2:5.

Nchito yolalikila imene Nowa anagwila Cigumula cisanafike, inaphatikizapo kucenjeza anthu za ciwonongeko cimene cinali kubwela. Kumbukilani kuti Yesu anati: “M’masiku amenewo cigumula cisanafike, anthu anali kudya ndi kumwa. Amuna anali kukwatila ndipo akazi anali kukwatiwa, kufikila tsiku limene Nowa analoŵa m’cingalawa. Anthu ananyalanyaza zimene zinali kucitika mpaka cigumula cinafika n’kuwaseselatu onsewo. Zidzatelonso ndi kukhalapo kwa Mwana wa munthu.” (Mat. 24:38, 39) Olo kuti anthu analibe cidwi, Nowa anapitiliza kulengeza mokhulupilika uthenga wocenjeza umene anapatsidwa. Masiku ano, timalalikila uthenga wa Ufumu pofuna kupatsa anthu mwayi wodziŵa colinga ca Mulungu kwa anthu. Mofanana ndi Yehova, timafunitsitsa kuti anthu amvetsele uthenga wathu na “kukhalabe ndi moyo.” (Ezek. 18:23) Pa nthawi imodzi-modzi, pamene tilalikila ku nyumba ndi nyumba komanso pa malo ena aliwonse, timacenjeza anthu ambili kuti Ufumu wa Mulungu udzabwela ndi kuwononga dziko loipali.—Ezek. 3:18, 19; Dan. 2:44; Chiv. 14:6, 7. w18.05 19 ¶8-9

Cinayi, August 13

Wotulutsa mawu okhulupilikaamanena zolungama.—Miy. 12:17.

Nanga bwanji ngati m’dziko limene mukhala muli ciletso ca boma, ndipo mwaitanidwa kuti akakufunseni mafunso ponena za abale anu? Kodi muyenela kucita ciani? Kodi muyenela kuwauza zonse zimene mudziŵa? Kodi Yesu anacita ciani pamene anali kufunsidwa mafunso na bwanamkubwa waciroma? Potsatila mfundo ya m’Malemba yakuti pali “nthawi yokhala cete ndi nthawi yolankhula,” nthawi zina Yesu sanali kuyankha ciliconse. (Mlal. 3:1, 7; Mat. 27:11-14) Zikakhala conco, tifunika kucita zinthu mozindikila, kuti tisaike moyo wa abale athu pa ciopsezo. (Miy. 10:19; 11:12) Mungacite bwanji ngati mnzanu wapamtima kapena m’bululu wanu wacita chimo lalikulu, ndipo imwe mudziŵa bwino zimene zinacitika? Kambani “zolungama,” kapena kuti zoona. Muli na udindo wouza akulu zoona, ndipo simufunika kusintha mfundo zina. Iwo amafunika kudziŵa bwino zeni-zeni zimene zinacitika kuti apeze njila yabwino yothandizila wocimwayo kukonzanso ubwenzi wake na Yehova.—Yak. 5:14, 15. w18.10 10 ¶17-18

Cisanu, August 14

Pitilizani kutonthozana ndi kulimbikitsana.—1 Ates. 5:11.

Kodi mungawalimbitse bwanji ena mwacikondi? Njila imodzi ni mwa kuwamvetsela mokoma mtima. (Yak. 1:19) Kumvetsela mwacifundo pamene munthu wovutika maganizo akutifotokozela nkhawa zake, kumaonetsa kuti tili na cikondi. Mungam’funse mafunso mosamala, oonetsa kuti mumam’dela nkhawa, n’colinga cakuti mudziŵe mmene akumvelela mumtima. Mukacita zimenezi, mudzadziŵa zimene mungacite kuti mum’limbikitse. Nkhope yanu iyenela kuonetsa kuti mukum’dela nkhawa komanso mumam’konda. Ngati akufotokoza vuto lake, mvetselani moleza mtima ndipo pewani kum’dula mawu. Kumvetsela moleza mtima kudzakuthandizani kumvetsetsa nkhawa zake. Mukatelo, iye adzayamba kukudalilani ndipo adzakhala wokonzeka kumvetsela zimene mungakambe pom’limbikitsa. Iye akaona kuti mumam’ganiziladi, adzalimbikitsidwa kwambili. w18.09 14 ¶10; 15 ¶13

Ciŵelu, August 15

Gula coonadi.—Miy. 23:23.

Nthawi ni cinthu cimene munthu aliyense amatailapo kuti apeze coonadi. Zimafuna nthawi kuti munthu amvetsele uthenga wa Ufumu na kuti aziŵelenga Baibo na mabuku ophunzilila Baibo. Zimafunanso nthawi kuti tizicita phunzilo laumwini, kukonzekela misonkhano komanso kukapezekapo. Conco, timafunika ‘kugula nthawi,’ kapena kuti kuiwombola ku zinthu zosafunika kweni-kweni. (Aef. 5:15, 16) Kodi zimatenga nthawi itali bwanji kuti munthu aphunzile mfundo zoyambilila za coonadi ca m’Baibo? Zimadalila mmene zinthu zilili mu umoyo wa munthuyo. Komabe, kuphunzila nzelu za Yehova, njila zake, na nchito zake, kulibe malile. (Aroma 11:33) Nsanja ya Mlonda yoyambilila inayelekezela mfundo imodzi ya coonadi na “duŵa laling’ono.” Ndiyeno, inakamba kuti: “Musakhutile ndi duŵa limodzi cabe la coonadi. Ngati kupeza duŵa limodzi, kapena kuti mfundo imodzi ya coonadi kunali kokwanila, Mulungu sakanapeleka mfundo zambili za coonadi. Pitilizani kusakila ena ambili, musaleke.” Olo tikakhale na moyo wamuyaya, sitidzakwanitsa kuphunzila zonse zokhudza Yehova. Masiku ano, cofunika kwambili ni kuseŵenzetsa nthawi yathu mwanzelu kuti tiphunzile mfundo zambili za coonadi mmene tingathele. w18.11 4 ¶7

Sondo, August 16

Amuna inu, pitilizani kukonda akazi anu.—Aef. 5:25.

Amuna amalangizidwa kuti ayenela kukhala na akazi awo “mowadziŵa bwino.” Mawu amenewa angamasulidwenso kuti “kuwaganizila kapena kuwamvetsetsa.” (1 Pet. 3:7) Kumvetsetsa munthu na kum’ganizila zimayendela pamodzi. Mwacitsanzo, mwamuna amene amamvetsetsa mkazi wake amadziŵa kuti mkaziyo, amene ni mnzake womuyenelela, ni wosiyana naye m’njila zambili. Koma samuona monga munthu wapansi. (Gen. 2:18) Conco, amayesetsa kucita zinthu mom’ganizila, na kum’patsa ulemu. Cinanso, mwamuna woganizila mkazi wake amayesetsa kukhala wosamala pocita zinthu na akazi ena. Iye amapewa kuceza mokopana na akazi ena, kapena kucita zinthu zoonetsa kuti amawakhumbila. Amapewa kucita izi ngakhale pa mawebusaiti amene amapitapo, kapena poseŵenzetsa njila zocezela pa intaneti. (Yobu 31:1) Inde, iye amayesetsa kukhala wokhulupilika kwa mkazi wake, osati cabe cifukwa cokonda mkaziyo, koma cifukwanso cokonda Mulungu na kuzonda coipa.—Sal. 19:14; 97:10. w18.09 29 ¶3-4

Mande, August 17

Aliyense wokhala ngati wamng’ono pakati pa nonsenu ndi amene ali wamkulu.—Luka 9:48.

N’cifukwa ciani nthawi zambili cimakhala covuta kucita zimene timaphunzila m’Mawu a Mulungu? Cifukwa cimodzi n’cakuti, kuti munthu acite coyenela amafunika kukhala wodzicepetsa. Koma kukhala odzicepetsa n’kovuta masiku ano. Tikukhala ‘m’masiku otsiliza’, ndipo anthu ambili ni “odzikonda, okonda ndalama, odzimva, odzikweza,” komanso “osadziletsa.” (2 Tim. 3:1-3) Monga atumiki a Mulungu, timadziŵa kuti makhalidwe amenewa ni oipa. Koma nthawi zina tingayambe kucita nsanje mu mtima mwathu tikaona kuti anthu amene amacita makhalidwe amenewa zinthu zikuwayendela bwino, ndipo akukhala mosangalala. (Sal. 37:1; 73:3) Tingafike pokayikila ngati kuika zofuna za ena patsogolo kulidi kwa phindu. Komanso tingayambe kuona kuti tikakhala odzicepetsa, anthu ena adzaleka kutilemekeza. Kutengela mzimu wodzikonda wa m’dzikoli kungawononge ubale umene tili nawo mu mpingo, komanso mbili yathu monga Akhristu oona. Koma zinthu zingatiyendele bwino ngati tiphunzila za atumiki okhulupilika ochulidwa m’Baibo na kutengela citsanzo cawo. w18.09 3 ¶1

Ciŵili, August 18

Kupatsa kumabweletsa cimwemwe coculuka.—Mac. 20:35.

Yehova anali yekha-yekha asanayambe kulenga zinthu. Kenako analenga angelo na anthu, nowapatsa mphatso ya moyo. Yehova, “Mulungu wacimwemwe,” amakonda kupatsa ena zinthu zabwino. (1 Tim. 1:11; Yak. 1:17) Ndipo popeza kuti amafuna kuti na ise tizikhala acimwemwe, amatiphunzitsa kukhala owoloŵa manja. (Aroma 1:20) Mulungu analenga anthu m’cifanizilo cake. (Gen. 1:27) Izi zitanthauza kuti tinalengedwa kuti tizitha kuonetsa makhalidwe monga ake. Conco, kuti tikhale acimwemwe, tiyenela kutengela Yehova mwa kukhala oganizila ena ndi opatsa mowolowa manja. (Afil. 2:3, 4; Yak. 1:5) N’cifukwa ciani zili conco? Cifukwa ni mmene Yehova anatilengela. Olo kuti ndise opanda ungwilo, tingatengele khalidwe la Yehova la kuwolowa manja. Yehova amafuna kuti tizitengela citsanzo cake. Iye amakondwela tikakhala owolowa manja.—Aef. 5:1. w18.08 18 ¶1-2; 19 ¶4

Citatu, August 19

Nkhosa zanga zimamva mawu anga.—Yoh. 10:27.

Otsatila a Khristu amaonetsa kuti amamvela mawu a Yesu mwa kucita zinthu mogwilizana ndi mawu ake. Iwo satangwanika na “nkhawa za moyo.” (Luka 21:34) M’malomwake, amaona kuti kumvela malamulo a Yesu n’kofunika kwambili, olo zinthu zivute bwanji mu umoyo wawo. Mosasamala kanthu za mavutowa, abale athu akhalabe okhulupilika kwa Yehova. Njila ina imene tingaonetsele kuti timamvela Yesu ni mwa kumvela na kugonjela anthu amene iye wawaika kukhala otsogolela pakati pathu. (Aheb. 13:7, 17) Gulu la Mulungu lapanga masinthidwe ambili m’zaka zaposacedwa. Ena mwa masinthidwe amenewa ni okhudza zida na njila zolalikilila, kacitidwe ka misonkhano ya mkati mwa wiki, komanso njila zomangila na kukonzanso Nyumba za Ufumu. Kukamba zoona, kusintha kumeneku kumatipindulitsa, ndipo kumaonetsa kuti gulu la Mulungu limatikonda. Timayamikila kwambili citsogozo cimeneci. Yehova adzatidalitsa kwambili ngati tiyesetsa kutsatila malangizo a panthawi yake, amene gulu lake limapeleka. w19.03 10-11 ¶11-12

Cinayi, August 20

Tisakhalenso. . . otengekatengeka. . . [ndi] anthu popeka mabodza.—Aef. 4:14.

Nkhani yabodza imene ili na mfundo zina zolondola imakhala yosoceletsa kwambili. Ganizilani zimene Aisiraeli okhala ku madzulo kwa mtsinje wa Yorodano anacita m’masiku a Yoswa. (Yos. 22:9-34) Nthawi ina, iwo anamvela kuti Aisiraeli okhala kum’maŵa anamanga guwa lansembe lalikulu ndi laulemelelo. Mfundo imeneyi inali yoona. Atangomvela zimenezi, Aisiraeli okhala ku madzulo kwa Yorodano anaganiza kuti abale awo apandukila Yehova. (Yoswa 22:9-12.) Koma mwayi wake unali wakuti asanacite izi, anatuma amuna odalilika kuti akafufuze zoona zeni-zeni za nkhaniyo. Kodi anapeza zotani? Anapeza kuti guwalo silinali lopelekelapo nsembe, koma linali cabe monga cikumbutso. Iwo analimanga n’colinga cakuti m’tsogolo, Aisiraeli onse akadziŵe kuti nawonso anali atumiki a Yehova okhulupilika. Mwacionekele, Aisiraeli enawa anakondwela ngako kuti sanaphe abale awo cifukwa cokhulupilila mphekesela, koma anafufuza coyamba kuti adziŵe zoona zeni-zeni za nkhaniyo. w18.08 5 ¶9-10

Cisanu, August 21

Amene akuyesa kuti ali cilili asamale kuti asagwe.—1 Akor. 10:12.

Monga mmene Paulo anakambila, ngakhale olambila oona angayambe makhalidwe ena oipa. Anthu ena amene amacita chimo, angakhale akumvabe kuti ali pa ubwenzi wolimba na Yehova. Komabe, kumvela cabe mu mtima kuti tili pa ubwenzi na Yehova kapena kudzionetsela kuti ndise okhulupilika kwa iye, sikutanthauza kuti Yehova akutiyanja. (1 Akor. 10:1-5) Monga mmene Aisiraeli anakhalila na nkhawa cifukwa ca kucedwa kwa Mose pa Phili la Sinai, Akhristu ena masiku ano angakhale na nkhawa cifukwa coona ngati kuti tsiku la Yehova laciweluzo ndi dziko latsopano zacedwa. Iwo angayambe kuganiza kuti kukali nthawi yaitali kuti zimenezi zidzacitike, kapenanso kuti sizidzacitika n’komwe. Ngati sitingacitepo kanthu, maganizo amenewa angacititse kuti tiyambe kuika patsogolo zolinga zakuthupi m’malo moika patsogolo cifunilo ca Yehova. Ndipo tingayambe kutengeka pang’ono-pang’ono n’kucoka kwa Yehova. M’kupita kwa nthawi, tingayambe kucita zinthu zoipa zimene poyamba sitinali kuganiza kuti tingazicite. w18.07 21 ¶17-18

Ciŵelu, August 22

Ndidzacita izinso zimene wanena, cifukwa ndakukomela mtima ndipo ndikukudziŵa bwino, ndi dzina lako lomwe.—Eks. 33:17.

Tingalandile madalitso ambili ngati Yehova amatidziŵa bwino. Koma kodi tingacite ciani kuti iye atidziŵe? Tiyenela kumukonda na kudzipatulila kwa iye (1 Akor. 8:3) Koma tifunika kusungabe ubwenzi wathu wamtengo wapatali na Atate wathu wakumwamba. Mofanana ndi Akhristu a ku Galatiya amene Paulo anawalembela kalata, na ise tifunika kupewa kukhala akapolo a zinthu “zacibwanabwana, zomwe ndi zosathandiza ndiponso zopanda pake” za m’dzikoli. Izi zingaphatikizepo mtima wofuna kutamandidwa na ena. (Agal. 4:9) Akhristu a m’nthawi ya atumwi amenewo, anali atapita kale patsogolo mwauzimu mpaka kufika pokhala odziŵika kwa Mulungu. Komabe, Paulo anakamba kuti abalewo anayamba ‘kubwelelanso’ ku zinthu zopanda pake. Zili ngati kuti Paulo anali kuwauza kuti: “Anthu inu mwapita kale patsogolo, nanga n’cifukwa ciani mukubwelelanso ku zinthu zacabe-cabe zimene munasiya m’mbuyo?” w18.07 8 ¶5-6

Sondo, August 23

Munthu wanzelu amamvetsela ndi kuphunzilamalangizo owonjezeleka.—Miy. 1:5.

Sitifunika kucita kuphwanya malamulo a Mulungu kuti tidziŵe kuopsa kocita zimenezo. Tingaphunzilepo kanthu pa zolakwa za ena, amene nkhani zawo zinalembedwa m’Mawu a Mulungu. Kukamba zoona, timalandila malangizo abwino kwambili kucokela kwa Mulungu. Imodzi mwa njila zimene timalandilila malangizowo ni mwa kuŵelenga na kusinkha-sinkha nkhani za anthu ochulidwa m’Baibo. Mwacitsanzo, ganizilani mavuto amene Mfumu Davide anakumana nawo cifukwa cophwanya lamulo la Yehova mwa kucita cigololo na Bati-seba. (2 Sam. 12:7-14) Pamene tiŵelenga nkhaniyi, tingacite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi Davide akanapewa bwanji mavuto amene anakumana nawo cifukwa cocita cigololo na Bati-seba? Ngati nitakumana na ciyeso cofanana na cimeneci, ningacite ciani? Kodi ningathaŵe monga mmene Yosefe anacitila, kapena ningagonje ngati Davide?’ (Gen. 39:11-15) Ngati tiganizila zotulukapo zoipa za chimo, tidzayamba kudana kwambili na coipa.—Amosi 5:15. w18.06 17 ¶5, 7

Mande, August 24

Pelekani zinthu za Kaisara kwa Kaisara.—Mat. 22:21.

Anthu ambili amatenga mbali m’zandale cifukwa coona zinthu zopanda cilungamo zimene zicitika. M’nthawi ya Yesu, nkhani ya kupeleka msonkho inali yovuta ngako. Anthu olamulidwa ndi Aroma, kuphatikizapo anthu amene Yesu anali kuwalalikila, anali kupeleka misonkho yambili, monga wa katundu, malo, ndi wa nyumba. Ndipo cimene cinawonjezela vuto n’cakuti anthu okhometsa msonkho anali acinyengo. Nthawi zina, iwo anali kucita kugula udindo wokhometsa msonkho kwa akulu-akulu a boma na kuuseŵenzetsa kuti apeze ndalama zambili. Zakeyu, mkulu wa okhometsa msonkho ku Yeriko, analemela kwambili cifukwa colanda anthu ndalama. (Luka 19:2, 8) Mwina, izi n’zimene okhometsa msonkho ambili anali kucita. Adani a Yesu anafuna kum’kola kuti atengeko mbali m’mikangano yokhudzana ndi za misonkho. Iwo anamuyesa pa nkhani ya kupeleka msonkho wa dinari imodzi, umene munthu aliyense wolamulidwa na Ufumu wa Roma anali kufunika kupeleka. (Mat. 22:16-18.) Ayuda ambili anali kuuzonda ngako msonkho umenewu, cifukwa unali kuonetsa kuti iwo ali pansi pa ulamulilo wa Aroma. w18.06 5-6 ¶8-10

Ciŵili, August 25

Ciliconse cimene munthu wafesa, adzakololanso comweco. —Agal. 6:7.

Zimene munthu amataya akasankha kukhala ku mbali ya Satana, nthawi zonse zimakhala zambili kuposa zimene angapeze kwa Satana. (Yobu 21:7-17; Agal. 6: 8) Kodi kudziŵa mphamvu za Satana kuli na ubwino wanji? Kumatithandiza kukhala na kaonedwe koyenela ka maboma a anthu. Komanso kumatilimbikitsa kugwila nchito yolalikila. Tidziŵa kuti Yehova amafuna kuti tizilemekeza maboma. (1 Pet. 2:17) Ndiponso amafuna kuti tizimvela malamulo a boma malinga ngati sawombana na malamulo ake. (Aroma 13:1-4) Ngakhale n’conco, timadziŵa kuti sitifunika kuloŵelela m’zandale mwa kukondela cipani kapena wolamulila winawake. (Yoh. 17:15, 16; 18:36) Cinanso, tidziŵa kuti Satana amafuna kuipitsa mbili ya Yehova na kuiŵalitsa anthu dzina lake. Kudziŵa izi, kumatisonkhezela kuphunzitsa ena mwakhama coonadi ponena za Mulungu wathu. Timanyadila kudziŵika na dzina lake komanso kuliseŵenzetsa, podziŵa kuti kukonda Mulungu kumabweletsa madalitso oculuka kuposa kukonda ndalama na zinthu zina.—Yes. 43:10; 1 Tim. 6:6-10. w18.05 24 ¶8-9

Citatu, August 26

Mkazi asasiye mwamuna wake.—1 Akor. 7:10.

Kodi m’cikwati mukabuka mavuto, ndiye kuti ni bwino kungopatukana? Malemba safotokoza mavuto amene angakhale maziko a kupatukana. Paulo analemba kuti: “Mkazi amene mwamuna wake ndi wosakhulupilila, koma mwamunayo akulola kukhala naye, asamusiye mwamuna wakeyo.” (1 Akor. 7:12, 13) Malangizo amenewa amagwilanso nchito masiku ano. Nthawi zina, “mwamuna wosakhulupilila” angacite zinthu zoonetsa kuti safuna ‘kukhalabe naye’ mkazi wake. Akhoza kumam’citila nkhanza kwambili, cakuti angaone kuti moyo wake uli paciopsezo. Mwinanso mwamunayo angamakane kusamalila mkaziyo pamodzi ndi ana. Kapenanso angamacite zinthu zolepheletsa mkaziyo kutumikila Yehova mokhulupilika. Zikakhala conco, alongo ena amasankha kupatukana na mwamuna wawo, cifukwa zocita zake zimaonetsa kuti safuna ‘kukhalabe naye’ mlongoyo. Koma alongo ena amene amakumana na mavuto ofananawo, amasankha kukhalabe naye mwamuna wotelo. Iwo amapilila na kuyesetsa kucita mbali yawo kuti akonze zinthu. w18.12 13-14 ¶14, 16; 14 ¶17

Cinayi, August 27

[Awa ndi] anthu amene. . . [amabeleka] zipatso mwa kupilila.—Luka 8:15.

M’fanizo la wofesa mbewu lopezeka pa Luka 8:5-8, 11-15, mbewu ikuimila “mawu a Mulungu,” kapena kuti uthenga wabwino wa Ufumu. Nthaka ikuimila mtima wa munthu wophiphilitsa. Mbewu imene inagwela pa nthaka yabwino inazika mizu, inamela, kenako ‘inabala zipatso kuwilikiza maulendo 100.’ Mofanana ndi nthaka yabwino ya m’fanizo la Yesu, tinalandila uthengawo na kuukhulupilila. Zotulukapo zake, uthenga wa Ufumu umene uli ngati mbewu unazika mizu mumtima mwathu na kukula n’kukhala monga mmela wa tiligu. Patapita nthawi, tinakhala wokonzeka kubala zipatso. Ndipo monga mmene taonela, zipatso zimene mmela wa tiligu umabala si tummela twatsopano tung’ono-tung’ono. Koma umabala mbewu. N’cimodzi-modzi na ise. Zipatso zimene timabala si ophunzila atsopano, koma ni mbewu zatsopano za Ufumu. Kodi timabala bwanji mbewu zatsopano za Ufumu? Mwa kulalikila uthenga wa Ufumu. Nthawi iliyonse pamene tilengeza uthenga wa Ufumu, timakhala ngati tikufesa mbewu zolingana ndi zimene zinafesedwa mumtima mwathu. (Luka 6:45; 8:1) Conco, fanizo la Yesu la wofesa mbewu litiphunzitsa kuti malinga ngati tipitiliza kulalikila uthenga wa Ufumu, ndiye kuti ‘tikubala zipatso mwa kupilila.’ w18.05 14 ¶10-11

Cisanu, August 28

Onse amene ndimawakonda, ndimawadzudzula ndi kuwalanga. Conco, khala wodzipeleka ndipo ulape.—Chiv. 3:19.

Paulo sanangolimbikitsa abale ake na mawu cabe, koma ‘anagwilitsila nchito zinthu zake zonse ndi kupeleka moyo wake wonse cifukwa ca miyoyo yawo.’ (2 Akor. 12:15) N’cimodzi-modzinso na akulu. Sayenela kulimbikitsa ndi kutonthoza Akhristu anzawo na mawu cabe, koma afunikanso kuwalimbikitsa mwa kuwaonetsa cidwi ceni-ceni. (1 Akor. 14:3) Nthawi zina, kulimbikitsana kungaphatikizepo kupeleka uphungu. Pa mbali imeneyinso, akulu ayenela kutengela citsanzo ca m’Baibo ca mmene tingapelekele uphungu m’njila yolimbikitsa. Citsanzo cabwino ngako pa nkhaniyi ni cimene Yesu anapeleka pambuyo pa imfa na kuukitsidwa kwake. Iye anapeleka uphungu wamphamvu ku mipingo ina ya m’cigawo ca Asia Minor. Kodi anaupeleka motani? Asanapeleke uphungu ku mpingo wa ku Efeso, Pegamo, na wa ku Tiyatira, coyamba anaiyamikila mipingoyo. (Chiv. 2:1-5, 12, 13, 18, 19) Akulu angacite bwino kutengela citsanzo ca Khristu pamene apeleka uphungu. w18.04 22 ¶8-9

Ciŵelu, August 29

Abambo, . . . [Lelani ana anu] m’malangizo a Yehova ndi kuwaphunzitsa kaganizidwe kake. —Aef. 6:4.

Makolo, mwacionekele mumacita zonse zotheka kuti muteteze ana anu ku matenda. Mumaonetsetsa kuti pa nyumba ni paukhondo, ndipo mumataya zilizonse zimene muona kuti zingabweletse matenda kwa imwe kapena kwa anawo. Mofanana na zimenezi, mufunika kuteteza ana anu ku zinthu zimene zingalengetse kuti atengele maganizo a Satana. Zinthu zimenezo ni monga mafilimu oipa, mapulogilamu a pa TV na mawebusaiti osayenela, komanso maseŵela oipa a pa kompyuta. Yehova wakupatsani udindo wothandiza ana anu kukhala naye pa ubwenzi wabwino. (Miy. 1:8) Conco, musaope kuika malamulo panyumba, ozikidwa pa mfundo za m’Baibo. Auzeni ana anu aang’ono zinthu zimene angatambe na zimene sayenela kutamba. Ndipo athandizeni kumvetsetsa zifukwa zimene mwaikila malamulowo. (Mat. 5:37) Pamene anawo akukula, aphunzitseni mfundo za Yehova kuti akhale na luso losiyanitsa cabwino na coipa. (Aheb. 5:14) Komanso, kumbukilani kuti ana amaphunzila zambili poona zocita zanu.—Deut. 6:6, 7; Aroma 2:21. w19.01 16 ¶8

Sondo, August 30

Inu okalamba pamodzi ndi ana. Onse . . . . atamande dzina la Yehova.—Sal. 148:12, 13.

Ngati ndimwe Mkhristu wacicepele, bwanji osakhala na colinga codziŵana bwino na acikulile mumpingo mwanu? Mungawafunse mwaulemu kuti akufotokozelenkoni zocitika za mu utumiki wawo. Mukacita zimenezi, mudzaphunzila zambili. Ndipo imwe na iwo mudzalimbikitsidwa kupitiliza kuonetsa kuwala kwa coonadi. Cinanso, ise tonse tiyenela kukhala na colinga colandila aliyense amene wabwela pa misonkhano. Ngati mwapatsidwa mwayi wotsogoza pa kukumana kokonzekela ulaliki, mungacite zambili pothandiza okalamba kutengamo mbali mu nchito yolalikila. Okalamba ayenela kupatsiwa gawo lowayenelela. Nthawi zina, mungawagaŵe na wacicepele kuti aziwathandizako pamene ayenda m’gawo. Muyenelanso kuwaganizila ofalitsa amene amalephela kucita zambili cifukwa ca kufooka kwa thanzi kapena pa zifukwa zina. Inde, kukhala ozindikila na oganizila ena kungathandize onse kuti azilalikila uthenga wabwino modzipeleka, kaya ni acicepele kapena acikulile, aciyambakale kapena acatsopano.—Lev. 19:32. w18.06 23-24 ¶10-12

Mande, August 31

[Seŵenzetsani] ufulu wanu, osati monga cophimbila zoipa, koma monga akapolo a Mulungu. —1 Pet. 2:16.

Tiyenela kuyamikila kwambili kuti Yehova anatimasula ku ukapolo wa ucimo na imfa. Cifukwa ca dipo, timatumikila Mulungu tili na cikumbumtima coyela ndipo timapeza cimwemwe ceni-ceni pocita zimenezi. (Sal. 40:8) Komabe, kuwonjezela pa kuyamikila ufulu wathu wamtengo wapatali umenewu, tiyenelanso kupewelatu kuuseŵenzetsa molakwika. Mtumwi Petulo anaticenjeza kuti sitiyenela kuona ufuluwu monga mwayi wokhutilitsila zilakolako zathu za thupi. Kodi cenjezo limeneli silikukumbutsani mavuto amene Aisiraeli anakumana nawo m’cipululu? Ise tifunika kukhala osamala kwambili, mwina kuposanso Aisiraeli. M’dziko la Satanali muli zinthu zambili zokopa monga zovala, zakudya, zakumwa, zosangalatsa, na zina zambili. Ndipo nthawi zambili anthu otsatsa malonda amaseŵenzetsa anthu ooneka bwino pofuna kutisonkhezela kugula zinthu zimene n’zosafunika kweni-kweni mu umoyo wathu. Conco, n’zosavuta kukopeka na misampha imeneyi na kuyamba kuseŵenzetsa ufulu wathu molakwika. w18.04 10 ¶7-8

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani