LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • es20 masa. 88-98
  • September

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • September
  • Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2020
  • Tumitu
  • Ciŵili, September 1
  • Citatu, September 2
  • Cinayi, September 3
  • Cisanu, September 4
  • Ciŵelu, September 5
  • Sondo, September 6
  • Mande, September 7
  • Ciŵili, September 8
  • Citatu, September 9
  • Cinayi, September 10
  • Cisanu, September 11
  • Ciŵelu, September 12
  • Sondo, September 13
  • Mande, September 14
  • Ciŵili, September 15
  • Citatu, September 16
  • Cinayi, September 17
  • Cisanu, September 18
  • Ciŵelu, September 19
  • Sondo, September 20
  • Mande, September 21
  • Ciŵili, September 22
  • Citatu, September 23
  • Cinayi, September 24
  • Cisanu, September 25
  • Ciŵelu, September 26
  • Sondo, September 27
  • Mande, September 28
  • Ciŵili, September 29
  • Citatu, September 30
Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2020
es20 masa. 88-98

September

Ciŵili, September 1

Ngakhale kuti simunamuonepo, mumamukonda.—1 Pet. 1:8.

Yesu anamvelelanso cifundo Marita na Mariya. Iye “anagwetsa misozi” ataona cisoni cimene iwo anali naco kaamba ka imfa ya m’bale wawo Lazaro. (Yohane 11:32-35) Sikuti iye anagwetsa misozi pa cifukwa cabe cakuti anataikilidwa bwenzi lake lapamtima. Ndi iko komwe, iye anali kudziŵa kuti adzamuukitsa Lazaro. Yesu anagwetsa misozi cifukwa anakhudzidwa kwambili ataona cisoni cacikulu cimene mabwenzi ake anali naco cifukwa ca imfa ya Lazaro. Kudziŵa kuti Yesu anali wacifundo n’kolimbikitsa ngako kwa ife. Timam’konda cifukwa cakuti anali kumvelela cifundo anthu ena. Timalimbikitsidwa kudziŵa kuti iye, tsopano akulamulila monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. Ndipo posacedwa adzacotsapo mavuto onse. Popeza kuti Yesu anakhalapo munthu padziko lapansi, iye ndiye woyenelela kwambili kupulumutsa anthu ku mavuto onse amene ulamulilo wa Satana wabweletsa. Ndithudi, ndife odala kukhala na Wolamulila amene ‘amatimvela cisoni pa zofooka zathu.’—Aheb. 2:17, 18; 4:15, 16. w19.03 17 ¶12-13

Citatu, September 2

Palibe munthu angabwele kwa ine akapanda kukokedwa ndi Atate amene anandituma ine. —Yoh. 6:44.

Pamene tigwila nchito yathu yolalikila, tifunika kukumbukila kuti pali zinthu zina zimene sitingakwanitse kucita. Timaphunzitsa anthu coonadi ponena za Mulungu, koma Yehova ndiye amacita mbali yaikulu panchitoyi. (1 Akor. 3:6, 7) Iye ndiye amakoka anthu. Cinanso, kuti munthu alabadile uthenga wabwino, kweni-kweni zimadalila mmene mtima wake ulili. (Mat. 13:4-8) Tisaiŵale kuti anthu ambili m’nthawi ya Yesu sanalabadile uthenga wake, ngakhale kuti iye anali Mphunzitsi waluso kuposa munthu aliyense. Conco, sitifunika kugwa mphwayi ngati anthu ambili amene timawalalikila, salabadila uthenga wathu. Ngati timvelela cifundo ena mu ulaliki, padzakhala zotulukapo zabwino. Tidzayamba kukondwela kwambili na nchito imeneyi. Ndipo tidzakhala na cimwemwe coculuka cimene cimabwela cifukwa copatsa. Komanso, cidzakhala cosavuta kuti anthu amene ali “ndi maganizo abwino, amene angawathandize kukapeza moyo wosatha” amvetsele uthenga wabwino. (Mac. 13:48) Conco, “ngati tingathe, tiyeni ticitile onse zabwino.” (Agal. 6:10) Tikatelo, tidzakhala na cimwemwe podziŵa kuti zocita zathu zikupeleka ulemelelo kwa Atate wathu wakumwamba.—Mat. 5:16. w19.03 25 ¶18-19

Cinayi, September 3

Ndidzakutamandani pakati pa mpingo.—Sal. 22:22.

Mfumu Davide analemba kuti: “Yehova ndi wamkulu ndi woyenela kutamandidwa kwambili.” (Sal. 145:3) Iye anali kum’konda Yehova. Izi zinam’sonkhezela kutamanda Mulungu “pakati pa mpingo.” (1 Mbiri 29:10-13; Sal. 40:5) Masiku ano, njila imodzi imene timatamandila Yehova ni mwa kupeleka ndemanga pa misonkhano. Tonse timakondwela kumvetsela ndemanga zosiyana-siyana za abale na alongo pa misonkhano. Mwacitsanzo, timayamikila ndemanga zazifupi komanso zocokela pansi pa mtima zimene acicepele amapeleka. Timalimbikitsidwa pomvetsela abale na alongo akufotokoza mwacimwemwe mfundo za coonadi zimene anapeza pokonzekela. Cinanso, timawayamikila abale na alongo amene ‘amalimba mtima’ kupeleka ndemanga pa misonkhano, olo kuti ni amanyazi kapena akuphunzila kumene citundu. (1 Ates. 2:2) Kodi tingaonetse bwanji kuti timawayamikila? Pambuyo pa misonkhano, tingawauze kuti tayamikila ndemanga yawo yolimbikitsa. Tingaonetsenso kuyamikila mwa kupeleka ndemanga pa misonkhano. Tikatelo, timalimbikitsanso ena, m’malo mongoyembekezela kuti iwo atilimbikitse.—Aroma 1:11, 12. w19.01 8 ¶1-2; 9 ¶6

Cisanu, September 4

Sonyezani kuti ndinu oyamikila.—Akol. 3:15.

Panali amuna 10 odwala khate, amene analibiletu ciyembekezo cakuti adzacila. Koma tsiku lina, anaona Yesu, Mphunzitsi Waluso akudutsa capatali. Iwo anali atamvela kuti Yesu anali kucilitsa matenda a mtundu uliwonse. Conco, anafuula mokweza mawu kuti: “Yesu, Mlangizi, ticitileni cifundo!” Ndipo onse 10 anacilitsidwadi. Mwacidziŵikile, onse anayamikila kukoma mtima kumene Yesu anawaonetsa. Koma mmodzi wa iwo sanangoyamikila cabe mumtima mwake. Anacitapo kanthu mwa kupita kwa Yesu kukaonetsa kuyamikila kwake. Mtima wake woyamikila unam’sonkhezela kutamanda Mulungu “mokweza mawu.”(Luka 17:12-19) Mofanana na Msamariya uja, timafuna kuonetsa kuti timawayamikila anthu amene amacita zinthu zabwino. Yehova amapeleka citsanzo cabwino pa nkhani yoyamikila ena. Njila imodzi imene amacitila zimenezi ni mwa kudalitsa anthu ocita zinthu zom’kondweletsa. (2 Sam. 22:21; Sal. 13:6; Mat. 10:40, 41) Ndipo Malemba amatilimbikitsa ‘kutsanzila Mulungu, monga ana ake okondedwa.’ (Aef. 5:1) Conco, cifukwa cacikulu cimene timaonetsela kuyamikila, n’cakuti timafuna kutengela citsanzo ca Yehova. w19.02 14 ¶1-2; 14 ¶4

Ciŵelu, September 5

Sindidzasiya kukhala ndi mtima wosagawanika.—Yobu 27:5.

Mtsikana ku sukulu, mwaulemu akukana kutengamo mbali m’cikondwelelo cinacake cimene n’cosagwilizana na mfundo za Mulungu. M’bale wacicepele wamanyazi amene akulalikila ku nyumba na nyumba, akupita kukalalikila panyumba pamene pamakhala mnyamata wina wa ku sukulu kwawo, amene amakonda kunyoza Mboni za Yehova. M’bale wina amene amagwila nchito molimbika kuti asamalile banja lake, abwana ake am’pempha kuti acite zinthu zinazake zacinyengo panchito. M’baleyo anafotokozela abwana ake kuti Mulungu safuna kuti atumiki ake azicita cinyengo kapena kuphwanya malamulo. Conco, iye anakana kucita zimenezo, olo kuti zikanapangitsa kuti acotsedwe nchito. (Aroma 13:1-4; Aheb. 13:18) Ni makhalidwe abwino ati amene mwaona mwa Akhristu atatu amenewa? Mwina mwaonako angapo, monga kulimba mtima na kuona mtima. Koma pali khalidwe lina lapamwamba kwambili limene onse ali nalo. Ali na mtima wamphumphu. Onse atatu ni okhulupilika kwa Yehova. Aliyense wa iwo wakana kuphwanya mfundo za Mulungu. Cimene cawalimbikitsa kucita zimenezi ni mtima wawo wamphumphu. Mwacionekele, Yehova ananyadila kuona atumiki ake amenewa akucita zinthu zoonetsa kuti ali na mtima wamphumphu. Na ife, timafuna kukondweletsa Atate wathu wakumwamba. w19.02 2 ¶1-2

Sondo, September 6

Cilamulo ndico mthunzi cabe wa zinthu zabwino zimene zikubwela.—Aheb. 10:1.

Cilamulo cinali kuteteza maka-maka anthu amene sakanakwanitsa kudziteteza okha, monga ana amasiye, akazi amasiye, komanso alendo. Oweluza a mu Isiraeli anauzidwa kuti, “Usapotoze ciweluzo ca mlandu wa mlendo kapena mlandu wa mwana wamasiye, ndipo usalande mkazi wamasiye covala cake monga cikole.” (Deut. 24:17) Yehova anali kuonetsa cifundo na cikondi capadela kwa anthu ovutika, osoŵelatu thandizo. Ndipo amene anali kuvutitsa anthu otelo, Yehova anali kuwalanga (Eks. 22:22-24) Yehova amafuna kuti anthu amene wawapatsa udindo wa uyang’anilo, azisamalila anthu ake mwacikondi. Iye amazonda khalidwe loipa la ciwelewele. Ndipo amafuna kuti aliyense, maka-maka anthu ooneka ngati osatetezeka, azicitilidwa zinthu mwacilungamo ndi kuti azikhala motetezeka. Tikaona kuti Yehova amaticitila zinthu mwacilungamo, timayamba kum’konda kwambili. Ndipo kukonda Mulungu na Malamulo ake olungama, kumatisonkhezela kukonda anthu anzathu na kuwacitila zinthu mwacilungamo. w19.02 24-25 ¶22-26

Mande, September 7

[Kanani] moyo wosaopa Mulungu ndi zilakolako za dziko.—Tito 2:12.

Onani citsanzo coonetsa mmene tingadzitetezele kuti Satana asaipitse maganizo athu. Yehova anatiphunzitsa kuti, “dama ndi conyansa camtundu uliwonse [siziyenela kuchulidwa] n’komwe pakati [pathu].” (Aef. 5:3) Koma kodi tingacite ciani ngati anzathu ku nchito kapena ku sukulu ayamba kukamba nkhani zosayenela zokhudza kugonana? Cikumbumtima cathu, cimene cili monga mlonda, cingaticenjeze. (Aroma 2:15) Koma kodi tidzacimvela? Mwina tingakopeke kuti timvetsele zimene akukamba, kapena kuonako zithunzi zoipa zimene akutamba. Koma imeneyi ndiyo nthawi yofunika kutseka mageti a mtima wathu, mwa kusintha nkhani yokambilana kapena kungocokapo. Pamafunika kulimba mtima kuti tikane pamene anzathu akutituntha kuganizila zinthu zosayenela kapena kucita zoipa. Koma Yehova amaona zoyesa-yesa zathu. Ndipo tiyenela kukhala na cidalilo cakuti iye adzatipatsa mphamvu na nzelu kuti tikwanitse kukana maganizo a Satana.—2 Mbiri 16:9; Yes. 40:29; Yak. 1:5. w19.01 17-18 ¶12-13

Ciŵili, September 8

Ineyo ndinaganizila nchito zonse zimene manja anga anagwila . . . , ndinaona kuti zonse zinali zacabecabe. . . panalibe caphindu ciliconse.—Mlal. 2:11.

Solomo anali munthu wolemela kwambili, komanso anali na ulamulilo wamphamvu. Iye anacita zinthu zosiyana-siyana zom’kondweletsa kuti aone ngati padzakhala zotulukapo zabwino. (Mlal. 2:1-10) Solomo anamanga nyumba zambili, anadzipangila minda na mapaki okongola, ndipo anacita ciliconse cimene mtima wake unali kulaka-laka. Kodi anamvela bwanji pambuyo pake? Kodi anakhutila? Kodi anapeza cimwemwe? Solomo iye mwini anatifotokozela m’lemba latsiku la lelo. Ndithudi, apa pali phunzilo lamphamvu kwambili kwa imwe acicepele! Yehova amafuna kuti muzimumvela kuti mupewe mavuto. Koma pamafunika cikhulupililo kuti muzimumvela na kuika cifunilo cake patsogolo. Kukhala na cikhulupililo n’kofunika kwambili, ndipo mukakhala naco simudzagwilitsidwa mwala. Yehova sadzaiŵala “cikondi cimene munacisonyeza pa dzina lake.” (Aheb. 6:10) Conco, yesetsani kulimbitsa cikhulupililo canu. Mukatelo, mudzatha kupanga zosankha mwanzelu, ndipo mudzaona kuti Atate wanu wakumwamba amakufunilani zabwino.—Sal. 32:8. w18.12 22 ¶14-15

Citatu, September 9

Mulungu akuonetsa cikondi cake kwa ife, moti pamene tinali ocimwa, Khristu anatifela. —Aroma 5:8.

Munthu wauzimu amakhulupilila Mulungu, komanso amaona zinthu mmene iye amazionela. Munthu wotelo amadalila malangizo a Mulungu, ndipo amayesetsa kumumvela. (1 Akor. 2:12, 13) Davide ni citsanzo cabwino pa nkhaniyi. Iye anati: “Yehova ndiye gawo langa, gawo limene ndinapatsidwa, komanso cikho canga.” (Sal. 16:5) Pamene Davide anakamba kuti Yehova ni “gawo” lake, anatanthauza kuti anali pa ubwenzi wabwino na Mulungu, amene analinso malo ake othaŵilako. (Sal. 16:1) Kodi kukhala pa ubwenzi na Mulungu kunam’pangitsa kumvela bwanji? Davide anati: “Moyo wanga ukukondwela.” Inde, kukhala pa ubwenzi wolimba na Mulungu kunam’thandiza Davide kukhala wacimwemwe kwambili mu umoyo wake. (Sal. 16:9,11) Anthu amene amakonda zosangalatsa na cuma sangakhale na cimwemwe monga cimene Davide anali naco. (1 Tim. 6:9, 10) Kulimbitsa cikhulupililo canu mwa Yehova na kum’tumikila kudzakuthandizani kukhala na umoyo wa phindu komanso wacimwemwe. Kodi mungalimbitse bwanji cikhulupililo canu? Muzipatula nthawi yomudziŵa bwino Mulungu. Mungacite izi mwa kuŵelenga Mawu ake, kuyang’ana cilengedwe cake, komanso kusinkha-sinkha za makhalidwe ake, kuphatikizapo cikondi cake pa imwe.—Aroma 1:20. w18.12 25 ¶7-8

Cinayi, September 10

Ukwati ukhale wolemekezeka kwa onse.—Aheb. 13:4.

Mtumwi Paulo analemba kuti: “Ukwati ukhale wolemekezeka kwa onse, ndipo pogona pa anthu okwatilana pakhale posaipitsidwa.” (Aheb. 13:4) Pamenepa, Paulo sanali kungofotokoza mmene cikwati ciyenela kukhalila. Koma anali kupeleka malangizo. Anali kulangiza Akhristu kuti ayenela kuona cikwati kukhala colemekezeka, komanso camtengo wapatali. Kodi umu ni mmene imwe mumaonela cikwati, maka-maka canu ngati muli pa banja? Ngati tilemekeza cikwati, ndiye kuti tikutengela citsanzo cabwino kwambili ca Yesu. Iye anali kulemekeza cikwati. Pamene Afarisi anafunsa Yesu za kusudzulana, iye anawakumbutsa mawu amene Mulungu anakamba pa cikwati coyamba, akuti: “Pa cifukwa cimeneci, mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake, ndipo aŵiliwo adzakhala thupi limodzi.” Kenako, Yesu anakamba kuti: “Cimene Mulungu wacimanga pamodzi, munthu asacilekanitse.” (Maliko 10:2-12; Gen. 2:24) Apa Yesu anaonetsa kuti Mulungu ndiye anayambitsa cikwati, ndipo anagogomeza kuti ciyenela kukhala mgwilizano wacikhalile. Mulungu sanauze Adamu na Hava kuti ngati afuna angasudzulane na kuthetsa cikwati cawo. Lamulo limene Mulungu anakhazikitsa pa cikwati ca mu Edeni, linali lakuti cikwati ciyenela kukhala ca anthu ‘aŵili,’ mwamuna mmodzi na mkazi mmodzi. Ndipo aŵiliwo ayenela kukhala pa mgwilizano wacikhalile. w18.12 10-11 ¶2-4

Cisanu, September 11

Sandulikani mwa kusintha maganizo anu.—Aroma 12:2.

Pamene tinaphunzila coonadi, tinazindikila kufunika komvela malamulo a Yehova. Koma pamene tikukula mwauzimu, timaphunzila zambili zokhudza Yehova, monga zimene iye amakonda, zimene amazonda, komanso mmene amaonela zinthu pa nkhani zosiyana-siyana. Ndipo izi zimakhudza zocita na zosankha zathu. Kuphunzila kuona zinthu mmene Yehova amazionela n’kokondweletsa, koma nthawi zina kumakhala kovuta. Zili conco cifukwa kupanda ungwilo kungatilepheletse kukhala na kaonedwe ka Yehova pa zinthu zina. Mwacitsanzo, nthawi zina cingakhale covuta kuona zinthu mmene Yehova amazionela pa nkhani ya kukonda cuma, nchito yolalikila, khalidwe la ciwelewele, kuseŵenzetsa magazi molakwika, na nkhani zina. Kodi tingacite ciani kuti tipitilize kuona zinthu mmene Mulungu amazionela? Kuti tipeze yankho, tifunika kusintha maganizo athu mwa kuŵelenga Mawu a Mulungu na kuwasinkha-sinkha. Kucita zimenezi kumatithandiza kuti tidziŵe bwino mmene iye amaonela zinthu, komanso kuti tisinthe maganizo athu kukhala ogwilizana ndi ake. w18.11 23-24 ¶2-4

Ciŵelu, September 12

Kodi ndidzapempha thandizo kuti mundipulumutse ku ciwawa koma inu osandimva kufikila liti? —Hab. 1:2.

M’nthawi ya Habakuku, zinthu zinali zovuta kwambili. Iye anakhumudwa kwambili cifukwa anthu ambili pa nthawiyo anali na makhalidwe oipa komanso aciwawa. Iye anayamba kudzifunsa kuti, ‘Kodi zoipa zonsezi zidzatha liti? N’cifukwa ciani Yehova sakucitapo kanthu mwamsanga?’ Habakuku anaona kuti kulikonse mu Yuda, anthu anali kupondeleza anzawo na kucita zinthu zopanda cilungamo. Iye anafika pothedwa nzelu. Pa nthawi yovuta imeneyi, Habakuku anapempha Yehova kuti acitepo kanthu. N’kutheka kuti iye anayamba kuganiza kuti Yehova sakuwaganizilanso anthu ake. Anaona ngati kuti Mulungu sadzacitapo kanthu mwamsanga. Kodi na imwe nthawi zina mumamvela monga mmene mtumiki wa Mulungu ameneyu anamvelela? Kodi Habakuku analeka kudalila Yehova? Kodi analeka kukhulupilila malonjezo a Mulungu? Kutalitali! Kumbukilani kuti iye anauza Yehova nkhawa zake na mavuto ake. Izi zionetsa kuti sanaleke kudalila Yehova. Komabe, Habakuku anavutika maganizo posamvetsetsa cifukwa cake Yehova sanagwepo mwamsanga. Komanso sanamvetsetse cifukwa cimene analolela kuti iye akumane na mavuto aakulu. w18.11 14 ¶4-5

Sondo, September 13

Lekani kudziunjikila cuma padziko lapansi.—Mat. 6:19.

Pamene Yesu anaitana Petulo na Andireya kuti akhale, “asodzi a anthu,” iwo “anasiya maukonde awo.” (Mat. 4:18-20) Sikuti anthu onse amene amaphunzila coonadi masiku ano, angafunike kusiya nchito yawo. Zili conco cifukwa ambili mwa iwo ali na udindo wa m’Malemba wosamalila mabanja awo. (1 Tim. 5:8) Koma nthawi zambili, anthu akaphunzila coonadi, amafunika kusintha kaonedwe kawo ka zinthu zakuthupi. Komanso, amafunika kusintha zinthu zimene amaika patsogolo mu umoyo wawo. Ganizilani citsanzo ca Maria. Maseŵela a gofu anali monga cakudya cake. Ndipo colinga cake cinali cokapeza nchito ya ndalama zambili monga katswili wa maseŵelawa. Koma atatsiliza maphunzilowo, Maria anayamba kuphunzila Baibo, ndipo anacikonda coonadi. Iye anakondwela na mmene coonadi cinamuthandizila kusintha umoyo wake. Maria anazindikila kuti n’zosatheka kwa iye kufuna-funa cuma cauzimu ndi cakuthupi pa nthawi imodzi. (Mat. 6:24) Iye anasiya colinga cake cokhala katswili wa maseŵela a gofu. Maria tsopano akutumikila monga mpainiya, ndipo anakamba kuti ali na “umoyo wacimwemwe kwambili komanso waphindu.” w18.11 5 ¶9-10

Mande, September 14

Iyeyu [ni] mmisili wamatabwa, mwana wa Mariya.—Maliko 6:3.

Atafika zaka 30, Yesu analeka kugwila nchito ya ukalipentala, cifukwa anadziŵa kuti kutumikila Mulungu ndiyo nchito yofunika kwambili. Iye anakamba kuti cimodzi mwa zifukwa zimene Mulungu anam’tumila pa dziko lapansi, cinali cakuti adzalalikile uthenga wabwino wa Ufumu. (Mat. 20:28; Luka 3:23; 4:43) Yesu anali kuika nchito yolalikila patsogolo mu umoyo wake, ndipo anali kufuna kuti anthu ena azigwila naye nchito imeneyi. (Mat. 9:35-38) Ambili a ise sindise akalipentala. Koma mwacionekele, ndise alaliki a uthenga wabwino. Nchito imeneyi ni yofunika kwambili, cifukwa Mulungu ndiye mwini wake, ndipo ise ndise “anchito anzake.” (1 Akor. 3:9; 2 Akor. 6:4) Timakhulupilila kuti “mawu onse [a Yehova] ndi coonadi cokha-cokha.” (Sal. 119:159, 160) Ndiye cifukwa cake timafuna ‘kuphunzitsa ndi kufotokoza bwino mau a coonadi’ mu ulaliki. (2 Tim. 2:15) Kuti tikwanitse kucita izi, tifunika kupitiliza kukulitsa luso loseŵenzetsa Baibo, imene ni cida cacikulu cimene timagwilitsila nchito pophunzitsa anthu coonadi ponena za Yehova, Yesu, komanso Ufumu wa Mulungu. w18.10 11 ¶1-2

Ciŵili, September 15

Muthandize ofookawo, ndipo muzikumbukila mawu a Ambuye Yesu.—Mac. 20:35.

Ngati mwamuna atengela citsanzo ca mutu wake, Yesu Khristu, mkazi amayamba ‘kumulemekeza kwambili.’ (Aef. 5:22-25, 33) Ndipo mkazi amene amalemekeza mwamuna wake, amayesetsa kucita naye zinthu mom’ganizila. Ngati makolo amacita zinthu moganizilana, amapeleka citsanzo cabwino kwa ana awo. Makolo ali na udindo waukulu wophunzitsa ana kukhala oganizila ena. Mwacitsanzo, angaphunzitse ana awo kuti asamathamange-thamange kapena kuseŵela m’Nyumba ya Ufumu. Komanso, pa maceza acikhristu, makolo angauze ana awo kuti apatse mpata acikulile wotenga cakudya iwo asanatenge. Ngati mwana waticitila zina zake zabwino, monga kutitsegulila citseko, tingacite bwino kumuyamikila. Kucita izi kungam’limbikitse, komanso kungakhomeleze mumtima mwake mfundo yakuti, “Kupatsa kumabweletsa cimwemwe coculuka kuposa kulandila.” w18.09 29 ¶5-6

Citatu, September 16

Mtsogoleli wanu ndi mmodzi, Khristu.—Mat. 23:10.

Malangizo amene Mfumu yathu, Yesu Khristu, amapeleka amaonetsa kuti iye amaganizila za tsogolo lathu. Conco, tiziganizila za madalitso amene tapeza cifukwa cocita zinthu mogwilizana na masinthidwe aposacedwa. Mwacitsanzo, pa kulambila kwanu kwa pabanja, mungakambilane za mmene mwapindulila na masinthidwe okhudza misonkhano kapena ulaliki. Kucita izi kudzakulimbikitsani kwambili. Tikamaganizila ubwino wa malangizo a gulu la Yehova komanso mapindu amene timapeza, tidzalimbikitsidwa kutsatila malangizowo mwacimwemwe. Mwacitsanzo, tsopano taona kuti kucepetsa ciŵelengelo ca mabuku amene timapulinta, kwathandiza kuti tisamawononge ndalama zambili. Komanso, kuseŵenzetsa zipangizo zamakono, kwapangitsa kuti nchito ya Ufumu ipite patsogolo pa dziko lonse lapansi. Conco tiziseŵenzetsa kwambili mafoni na matabuleti poŵelenga na kuphunzila zofalitsa zathu, ngati tingakwanitse kutelo. Mwa kucita izi, tidzaonetsa kuti tili na maganizo monga a Khristu ofuna kuseŵenzetsa mwanzelu cuma ca gulu. Ngati titsatila malangizo a Khristu mokhulupilika, tidzalimbitsa mgwilizano komanso cikhulupililo ca ena. w18.10 25-26 ¶17-19

Cinayi, September 17

Timakukondani kwambili, tinali okonzeka kukupatsani uthenga wabwino wa Mulungu. Ndipotu osati uthenga wokha ayi, komanso miyoyo yathu yeni-yeniyo.—1 Ates. 2:8.

Ngati ticita zinthu mokoma mtima kwa ena, Yehova angatiseŵenzetse poyankha mapemphelo a munthu wovutika maganizo. (2 Akor. 1:3-6) Komabe musamayembekezele kuti abale na alongo anu azicita zinthu popanda kulakwitsa. Kuyembekezela kuti abale athu nthawi zonse azicita zinthu mosalakwitsa n’kudzinamiza, ndipo kungapangitse kuti tisamakhale acimwemwe. (Mlal. 7:21, 22) Kumbukilani kuti Yehova sayembekezela atumiki ake kucita zinthu mwangwilo. Ngati titengela citsanzo cake, tidzakhala okonzeka kunyalanyaza zophophonya za Akhristu anzathu. (Aef. 4:2, 32) Pewani kukamba monga mukuwaimba mlandu wakuti sacita zambili potumikila Yehova, kapena kuwayelekezela ndi ena. M’malomwake, khalani na cizoloŵezi cowayamikila pa zimene akucita mu utumiki wawo. Kucita izi kungawalimbikitse, ndiponso kungawapatse “cifukwa cosangalalila” mu utumiki wawo.—Agal. 6:4. w18.09 16 ¶16-17

Cisanu, September 18

Cakudya canga ndico kucita cifunilo ca amene anandituma ndi kutsiliza nchito yake.—Yoh. 4:34.

Kwa Yesu, kudya cakudya cauzimu kunali kuphatikizapo kucita zimene Mulungu anamulamula. Kodi kucita zimenezi kuli ngati kudya cakudya m’njila yotani? Monga mmene kudya cakudya cabwino cakuthupi kumatithandizila kukhala osangalala komanso athanzi, kucita cifunilo ca Mulungu kumatithandiza kukhala na cikhulupililo colimba kuti tikapeze moyo wosatha. Kucita zinthu mogwilizana na malangizo a Mulungu ndiyo nzelu. (Sal. 107:43) Ngati tiyesetsa kucita zinthu mwanzelu, tidzapeza mapindu ambili. Baibo imati: “Zonse zimene umakonda sizingafanane nazo . . . Zidzakhala ngati mtengo wa moyo kwa iye, ndipo ozigwilitsitsa adzachedwa odala.” (Miy. 3:13-18) Yesu anati: “Ngati zimenezi mukuzidziŵa, ndinu odala mukamazicita.” (Yoh. 13:17) Ophunzila a Yesu anafunika kupitiliza kucita zimene Yesu anawalamula kuti akhalebe acimwemwe kapena kuti odala. Mu umoyo wawo wonse, iwo anafunika kupitiliza kucita zimene Yesu anawaphunzitsa, komanso kutengela citsanzo cake. w18.09 4 ¶4-5

Ciŵelu, September 19

Mulungu analenga munthu m’cifanizilo cake.—Gen. 1:27.

Mulungu anapatsa mwamuna na mkazi oyambilila malangizo amene akanawathandiza kucita zinthu moganizila ena. N’zoona kuti panthawiyo anali aŵili cabe m’munda wa Edeni. Koma Yehova anawadalitsa na kuwauza kuti abalane, adzadze dziko lapansi, na kuliyang’anila. (Gen. 1:28) Mlengi wathu anaonetsa kuti anali kuganizila za ubwino wa zolengedwa zake. Conco, nawonso makolo athu oyambilila anafunika kuganizila tsogolo la ana awo amene anali kudzabadwa m’tsogolo. Mulungu anali kufuna kuti dziko lonse lidzakhale Paradaiso kuti Adamu ndi ana ake adzakhalemo mosangalala. Adamu na Hava akanakwanitsa kugwila nchito yopanga dziko lonse kukhala Paradaiso, mothandizidwa ndi ana awo amene anali kudzabadwa m’tsogolo. Adamu na Hava akanapanda kucimwa, dziko lapansi likanadzala na anthu angwilo okha-okha. Anthu angwilo amenewo akanafunika kucita zinthu mogwilizana kwambili na Yehova kuti akwanilitse colinga cake copanga dziko lonse kukhala paradaiso. Kucita izi kukanawapatsa mwayi woloŵa mu mpumulo wa Mulungu. (Aheb. 4:11) Ndithudi, nchito imeneyo ikanakhala yopatsa cimwemwe ngako. Ndipo Yehova akanawadalitsa kwambili cifukwa ca mtima wawo wopanda dyela ndi woganizila ena. w18.08 18 ¶2; 19-20 ¶8-9

Sondo, September 20

Anandinenela ine mtumiki wanu misece kwa inu mbuyanga mfumu.—2 Sam. 19:27.

Nanga bwanji ngati munthu wina wakunenelani zinthu zoipa? Yesu na Yohane M’batizi anakumanapo na vuto limeneli. (Mat. 11:18, 19) Kodi Yesu anacita ciani pamene anthu ena anamunenela zoipa? Sanataye nthawi na mphamvu zake poyesa kuteteza mbili yake. M’malomwake, anangolimbikitsa anthu kuti adzionele okha zimene iye anali kucita na kuphunzitsa. Iye anati, “nzelu imatsimikizilika kuti ndi yolungama cifukwa ca nchito zake.” (Mat. 11:19) Pamenepa pali phunzilo labwino limene tiyenela kutengapo. Nthawi zina, anthu angakambe zinthu zabodza kapena zoipa ponena za ise. Ndipo tingakhale wofunitsitsa kucitapo kanthu kuti titeteze mbili yathu komanso kuti cilungamo cionekele. Kodi n’ciani cothandiza cimene tingacite? Ngati wina wafalitsa nkhani yabodza ponena za ise, tiyenela kucita zinthu m’njila yakuti anthu adzionele okha kuti zimene munthuyo anakamba n’zabodza. Citsanzo ca Yesu pankhaniyi cionetsa kuti mbili yathu ya khalidwe labwino ingathe kufafaniza mabodza onse amene anthu angatinenele. w18.08 6 ¶11-13

Mande, September 21

Muziopa Yehova Mulungu wanu. Muzim’tumikila, [ndi] kum’mamatila.—Deut. 10:20.

Nkhani ya kusamvela kwa Kaini, Solomo, ndi ya Aisiraeli pa Phili la Sinai, zonse zili na mbali inayake yofanana. Anthu onsewa anali na mwayi ‘wolapa na kutembenuka.’ (Mac. 3:19) N’zoonekelatu kuti Yehova saleka mwamsanga kuthandiza anthu amene ayamba kuyenda njila yolakwika. Mwacitsanzo, Yehova anam’khululukila Aroni pa zimene anacita. Masiku ano, Yehova amaticenjeza kupitila m’Nkhani za m’Baibo, zofalitsa, komanso kupyolela m’malangizo ocokela kwa Akhristu anzathu. Tikamvela malangizo amenewa, iye amaticitila cifundo. Kukoma mtima kwa Yehova kuli na colinga. (2 Akor. 6:1) Kumatipatsa mwayi ‘wokana moyo wosaopa Mulungu ndi zilakolako za dziko.’ (Tito 2:11-14) Popeza tikali “m’nthawi” yovuta, tidzapitiliza kukumana na mavuto amene adzayesa kukhulupilika kwathu kwa Yehova. w18.07 21 ¶20-21

Ciŵili, September 22

Yehova amadziŵa anthu ake.—2 Tim. 2:19.

N’ciani cingatithandize kukhala na mtima wofunitsitsa kudziŵika kwa Yehova osati ku dziko? Tiyenela kukumbukila mfundo ziŵili zofunika kwambili. Yoyamba, Yehova nthawi zonse amadziŵa anthu amene amam’tumikila mokhulupilika. (Aheb. 6:10; 11:6) Iye amayamikila zimene mtumiki wake aliyense amacita, ndipo amaona kuti kunyalanyaza atumiki ake okhulupilika kungakhale kupanda cilungamo. Iye “amadziŵa njila za olungama,” komanso amawapulumutsa akakhala pa mayeselo.” (Sal. 1:6; 2 Pet. 2:9) Mfundo yaciŵili ni yakuti, Yehova angaonetse kuti amatidziŵa mwa kuticitila zinthu zimene sitinali kuyembekezela. Malemba amaonetsa kuti anthu amene amacita zabwino n’colinga cakuti anthu ena awaone, sadzalandila mphoto iliyonse yocokela kwa Yehova. Cifukwa ciani? Cifukwa cakuti akulandililatu mphoto yawo yonse. (Mat. 6:1-5) Koma Yesu anakamba kuti Atate ŵake amayang’ana anthu amene amacitila anzawo zabwino, olo kuti anthu ena sanaone. Akaona zimene acita, amawadalitsa mogwilizana ndi nchito zawozo. w18.07 9 ¶8, 10

Citatu, September 23

Zinthu zimene Mulungu waziyeletsa usiyiletu kuzinena kuti n’zoipitsidwa.—Mac. 10:15.

Petulo anathedwa nzelu cifukwa sanamvetsetse tanthauzo la zimene anamvazo. Nthawi yomweyo, kunafika amuna otumidwa na Koneliyo. Ndiyeno atalamulidwa mwa mzimu woyela, Petulo ananyamuka pamodzi na amunawo kupita ku nyumba ya Koneliyo. Petulo akanakhalabe na mtima woweluza ena motengela maonekedwe akunja, sembe sanangene m’nyumba ya Koneliyo. Panthawiyo, Ayuda sanali kuloŵa m’nyumba za anthu a mitundu ina. Nanga n’cifukwa ciani Petulo analimba mtima mpaka kungena m’nyumba ya Koneliyo? Analimbikitsidwa na masomphenya amene anaona, komanso citsimikizo ca mzimu woyela. Mwacionekele, Petulo atamvetsela zimene Koneliyo anakamba, anakhudzidwa kwambili. N’cifukwa cake anati: “Ndazindikila ndithu kuti Mulungu alibe tsankho. Iye amalandila munthu wocokela mu mtundu uliwonse, amene amamuopa ndi kucita cilungamo.” (Mac. 10:34, 35) Petulo anakondwela ngako atamvetsetsa mfundo ya coonadi imeneyi. w18.08 9 ¶3-4

Cinayi, September 24

Danani ndi coipa.—Amosi 5:15.

Mwina timayesetsa kupewa zinthu zimene Mulungu amazonda. Koma pali nkhani zina zimene palibe malamulo acindunji a m’Malemba. Pa nkhani zaconco, kodi tingadziŵe bwanji zimene zili zovomelezeka na zokondweletsa kwa Mulungu? Apa m’pamene cikumbumtima cathu cophunzitsidwa Baibo cimathandiza. Mwacikondi cake, Yehova anatipatsa mfundo zimene tingazigwilitsile nchito mogwilizana na cikumbumtima cathu cophunzitsidwa Baibo. Iye anati: “Ine Yehova ndine Mulungu wanu, amene ndimakuphunzitsani kuti zinthu zikuyendeleni bwino, amene ndimakucititsani kuti muyende m’njila imene muyenela kuyendamo.” (Yes. 48:17, 18) Ngati tiganizila mozama mfundo za m’Baibo na kuzilola kutifika pa mtima, tingawongolele cikumbumtima cathu. Ndipo cikumbumtima cotelo cidzatithandiza kupanga zosankha mwanzelu. Mfundo za m’Baibo ni ‘mfundo za coonadi zofunika kwambili kapena ziphunzitso zimene zimatitsogolela popanga zosankha kapena kucita zinthu.’ Kumvetsetsa mfundozo kumaphatikizapo kudziŵa bwino maganizo a Mulungu, amene ndiye Wopeleka malamulo, komanso kumvetsetsa zifukwa zimene anapelekela malamulowo. w18.06 17 ¶5; 18 ¶8-10

Cisanu, September 25

Kodi n’kololeka kupeleka msonkho kwa Kaisara kapena ayi? —Mat. 22:17.

“Acipani ca Herode” anayambitsa nkhaniyi poganiza kuti ngati Yesu angakambe kuti Ayuda asamapeleke msonkhowo, Aroma adzamuimba mlandu woukila boma. Komanso, Yesu akanakamba kuti Ayuda afunika kupeleka msonkhowo, ndiye kuti ophunzila ake sembe anayamba kumuzonda. Yesu anacita zinthu mosamala kuti asatengeko mbali pa mikangano imeneyi ya misonkho. Yesu anali kudziŵa kuti okhometsa msonkho ambili anali acinyengo. Koma iye sanafune kuti zimenezo zimusokoneze na kumulepheletsa kuika maganizo ake pa nkhani yofunika maningi ya Ufumu wa Mulungu, umene udzathetsa mavuto onse. Mwa ici, iye anapeleka citsanzo cabwino kwa otsatila ake onse. Iwo ayenela kupewa kutengako mbali m’mikangano ya ndale, olo anthu ena andale aoneke kuti akucita zabwino kapena zacilungamo kusiyana ndi ena. Akhristu amafuna-funa Ufumu wa Mulungu na cilungamo cake. Ndiye cifukwa cake amapewa kukhala na maganizo amphamvu ofuna kutsutsa zinthu zina zopanda cilungamo zimene boma lingacite. (Mat. 6:33) A Mboni za Yehova ambili anakwanitsa kuthetsa maganizo olakwika amene anali nawo pa zandale. w18.06 5-6 ¶9-11

Ciŵelu, September 26

Ana a Mulungu woona anayamba kuona kuti ana aakazi a anthu anali okongola.—Gen. 6:2.

Kuwonjezela pa kukopa angelowo na khalidwe la ciwelewele, mwina Satana anawakopanso mwa kuwalonjeza kuti adzakhala na mphamvu yolamulila anthu onse. Mwina colinga cake cinali cakuti alepheletse kubwela kwa ‘mbewu ya mkazi,’ imene Mulungu analonjeza. (Gen. 3:15) Mulimonsemo, pa nthawiyo Yehova analepheletsa zolinga na zoyesa-yesa za Satana ndi angelo opandukawo mwa kubweletsa Cigumula. Conco, sitifunika kudelela msampha wa ciwelewele kapena kuopsa kwa khalidwe la kunyada. Kumbukilani kuti kwa zaka zambili-mbili, angelo amene anakhala ku mbali ya Satana anali kutumikila pamaso pa Mulungu. Ngakhale n’conco, ambili analola zilakolako zoipa kuzika mizu m’mitima yawo na kukula. Mofananamo, mwina tatumikila Mulungu m’gulu lake kwa zaka zambili. Koma ngakhale tili m’malo otetezeka mwauzimu, zilakolako zoipa zikhoza kuzika mizu m’mitima yathu. (1 Akor. 10:12) Conco, n’kofunika kwambili kuti nthawi zonse tizisanthula mtima wathu, kukaniza maganizo oipa, na kupewa mzimu wonyada.—Agal. 5:26; Ako. 3:5. w18.05 25 ¶11-12

Sondo, September 27

Ndili ndi cisoni cacikulu ndiponso mtima ukundipweteka nthawi zonse.—Aroma 9:2.

Paulo anapwetekedwa mtima poona mmene Ayuda anali kutsutsila uthenga wa Ufumu. Olo zinali conco, iye sanaleke kuwalalikila. Onani zimene iye analemba m’kalata yake yopita kwa Akhristu a ku Roma pofotokoza mmene anali kuonela Ayuda. Iye anati: “Cimene ndikufunitsitsa mumtima mwanga ndiponso pembedzelo langa kwa Mulungu ndi lakuti Aisiraeli apulumutsidwe. Pakuti ndikuwacitila umboni kuti ndi odzipeleka potumikila Mulungu, koma samudziŵa molondola.” (Aroma 10:1, 2) Paulo anakamba kuti anapitiliza kulalikila kwa Ayuda cifukwa anali ‘kufunitsitsa mumtima mwake’ kucita zimenezo. Iye anali kufunitsitsa kuti Ayuda ena akapulumuke. (Aroma 11:13, 14) Iye anali kucondelela Mulungu m’pemphelo kuti athandize Ayuda kulabadila uthenga wa Ufumu. Paulo anakamba kuti Ayuda anali “odzipeleka potumikila Mulungu.” Iye anaona kuti anthu amenewo anali na mtima wofuna kucita zabwino. Paulo anali kudziŵa kuti anthu oona mtima komanso odzipeleka pa zinthu zabwino, angathe kusintha n’kukhala otsatila a Khristu acangu. w18.05 13 ¶4; 15-16 ¶13-14

Mande, September 28

[Muzilankhula mawu] olimbikitsa monga mmene kungafunikile, kuti asangalatse owamva.—Aef. 4:29.

Kulimbikitsa ena si udindo wa akulu cabe. Paulo analangiza Akhristu kuti azikamba mawu “olimbikitsa monga mmene kungafunikile, kuti asangalatse owamva.” (Aef. 4:29) Aliyense wa ise ayenela kukhala chelu kuti adziŵe zimene ena ‘akufunikila.’ Komanso, polangiza Akhristu aciheberi, Paulo anati: “Limbitsani manja amene ali lende ndi mawondo olobodoka, ndipo pitilizani kuwongola njila zimene mapazi anu akuyendamo, kuti ciwalo cimene cavulala cisaguluke polumikizila, koma cicilitsidwe.” (Aheb. 12:12, 13) Ise tonse, kuphatikizapo acicepele, tingalimbikitse Akhristu anzathu mwa kukamba mawu olimbikitsa. Paulo analangiza kuti: “Cotelo, ngati pakati panu pali kulimbikitsana kulikonse mwa Khristu, kaya kutonthozana kulikonse kwa cikondi, kaya mzimu woganizilana, kaya cikondi cacikulu ciliconse ndi cifundo, cititsani cimwemwe canga kusefukila pokhala ndi maganizo amodzi, ndi cikondi cofanana. Mukhalenso ogwilizana mu mzimu umodzi, ndi mtima umodzi. Musacite ciliconse ndi mtima wokonda mikangano kapena wodzikuza, koma modzicepetsa, ndi kuona ena kukhala okuposani. Musamaganizile zofuna zanu zokha, koma muziganizilanso zofuna za ena.”—Afil. 2:1-4. w18.04 22 ¶10; 23 ¶12

Ciŵili, September 29

Khalani mfulu, . . . monga akapolo a Mulungu.—1 Pet. 2:16.

Cifukwa cacikulu cimene Yehova, kupitila mwa Yesu, anatimasulila ku ukapolo wa cilamulo ca ucimo na imfa n’cakuti tidzipeleke kwa Mulungu “monga akapolo” ake. N’ciani cofunika kwambili cimene tiyenela kucita kuti tipewe kuseŵenzetsa molakwika ufulu wathu, na kuti tisakhalenso akapolo a zilakolako zathu kapena a zolinga zakuthupi? Tifunika kulimbikila kucita zinthu zauzimu. (Agal. 5:16) Mwacitsanzo, ganizilani za Nowa na banja lake. Iwo anali kukhala m’dziko lokonda ciwawa na ciwelewele. Koma anapewa kutengela zilakolako na zolinga za anthu amene anali kukhala nawo. N’ciani cinawathandiza? Anali kutangwanika na nchito imene Yehova anawapatsa, yomanga cingalawa, kusonkhanitsa zakudya zawo ndi za nyama, na kulalikila uthenga wocenjeza anthu. Baibo imati: “Nowa anacita zonse motsatila zimene Mulungu anamulamula. Anacitadi momwemo.” (Gen. 6:22) Mwa ici, Nowa na banja lake anapulumuka ciwonongeko ca dziko la pa nthawiyo.—Aheb. 11:7. w18.04 10 ¶8; 11 ¶11-12

Citatu, September 30

Ndikupatsani ulamulilo pa maufumu onsewa ndi ulemelelo wawo wonse, cifukwa unapelekedwa kwa ine. Ndikhoza kuupeleka kwa aliyense amene ndakonda kum’patsa.—Luka 4:6.

Satana na ziŵanda amaseŵenzetsa maboma, cipembedzo conama, komanso anthu oyendetsa zamalonda ‘posoceletsa dziko lonse lapansi kumene kuli anthu.’ (Chiv. 12:9) Poseŵenzetsa cipembedzo conama, iye amafalitsa mabodza ponena za Yehova. Kuwonjezela apo, Mdyelekezi amacita ciliconse cotheka kuti aiwalitse anthu ambili dzina la Mulungu. (Yer. 23:26, 27) Zotulukapo zake n’zakuti anthu oona mtima asoceletsedwa, ndipo mosadziŵa amalambila ziŵanda m’malo molambila Mulungu. (1 Akor. 10:20; 2 Akor. 11:13-15) Cinanso, Satana amafalitsa mabodza poseŵenzetsa anthu oyendetsa zamalonda. Mwacitsanzo, iwo amalimbikitsa mfundo yakuti cuma na ndalama zambili ndiye zimapatsa munthu cimwemwe ceni-ceni. (Miy. 18:11) Anthu amene amakhulupilila bodza limeneli amaseŵenzetsa moyo wawo wonse kutumikila “Cuma” m’malo motumikila Mulungu. (Mat. 6:24) M’kupita kwa nthawi, kukonda kwawo Cuma kumatsiliza cikondi cimene anali naco pa Mulungu.—Mat. 13:22; 1 Yoh. 2:15, 16. w18.05 23-24 ¶6-7

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani