LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • es20 masa. 98-108
  • October

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • October
  • Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2020
  • Tumitu
  • Cinayi, October 1
  • Cisanu, October 2
  • Ciŵelu, October 3
  • Sondo, October 4
  • Mande, October 5
  • Ciŵili, October 6
  • Citatu, October 7
  • Cinayi, October 8
  • Cisanu, October 9
  • Ciŵelu, October 10
  • Sondo, October 11
  • Mande, October 12
  • Ciŵili, October 13
  • Citatu, October 14
  • Cinayi, October 15
  • Cisanu, October 16
  • Ciŵelu, October 17
  • Sondo, October 18
  • Mande, October 19
  • Ciŵili, October 20
  • Citatu, October 21
  • Cinayi, October 22
  • Cisanu, October 23
  • Ciŵelu, October 24
  • Sondo, October 25
  • Mande, October 26
  • Ciŵili, October 27
  • Citatu, October 28
  • Cinayi, October 29
  • Cisanu, October 30
  • Ciŵelu, October 31
Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2020
es20 masa. 98-108

October

Cinayi, October 1

Lilani ndi anthu amene akulila.—Aroma 12:15.

Sitingathe kudziŵa za mu mtima mwa munthu monga mmene Yehova na Yesu amacitila. Ngakhale n’telo, tingakwanitse kuzindikila zosoŵa za ena komanso mmene akumvelela. (2 Akor. 11:29) Mosiyana ndi anthu odzikonda amene ali m’dzikoli, ife timapewa kuganizila ‘zofuna zathu zokha, koma timaganizilanso zofuna za ena.’ (Afil. 2:4) Akulu mu mpingo ndiwo afunika kuonetsa kwambili khalidwe la cifundo. Iwo amadziŵa kuti adzayankha mlandu kaamba ka mmene amasamalila nkhosa za Mulungu zimene zaikizidwa m’manja mwawo. (Aheb. 13:17) Kuti akulu akwanitse kuthandiza bwino Akhristu anzawo, afunika kukhala acifundo. Kodi iwo angaonetse bwanji kuti ni acifundo? Mkulu wacifundo amapeza nthawi yokambilanako na abale na alongo. Amawafunsa mafunso na kuwamvetsela mwachelu na moleza mtima. Kucita izi n’kofunika kwambili, maka-maka ngati m’bale kapena mlongo afuna kum’fotokozela maganizo ake na kumuuza mmene akumvelela, koma akulephela kufotokoza bwino-bwino. (Miy. 20:5) Ngati mkulu amapatula nthawi yocezako na Akhristu anzake, iwo amayamba kum’dalila kwambili, ndipo ubwenzi na cikondi pakati pa iye na Akhristuwo zimalimba.—Mac. 20:37. w19.03 17 ¶14-17

Cisanu, October 2

Mawu olankhulidwa pa nthawi yoyenela ali ngati zipatso za maapozi agolide m’mbale zasiliva.—Miy. 25:11.

Kuyamikila ena kuli monga cakudya cabwino. Tikapatsidwa cakudya cabwino, timakondwela. Komanso tikapatsa ena cakudya cabwino, nawonso amakondwela. Mofananamo, anthu ena akatiyamikila pa zimene timacita, timakondwela. Komanso, tikayamikila ena pa zimene amacita, nawonso amakondwela. Zili conco cifukwa ngati munthu tamuyamikila, amaona kuti zinthu zimene anaticitila kapena kutipatsa sizinapite pacabe. Zotulukapo zake n’zakuti ubwenzi wathu na iye umalimba. Kukamba mawu oyamikila n’kofunika ngako. Tangoyelekezelani cabe mmene maapozi opangidwa na golide angakongolele ataikidwa m’mbale ya siliva! Kodi mungamvele bwanji mutalandila mphatso ngati imeneyo? Umu ni mmenenso mawu anu oyamikila ena amakhalila. Cinanso n’cakuti, maapozi agolide angakhalepo kwa zaka zambili-mbili osawonongeka. Mofananamo, mawu oyamikila amene tingakambe kwa munthu, angawakumbukile kwa zaka zambili, mwina kwa moyo wake wonse. w19.02 15 ¶5-6

Ciŵelu, October 3

Munthu wakhala wodziŵa zabwino ndi zoipa ngati ife.—Gen. 3:22.

Pamene Adamu na Hava anadya cipatso ca mtengo wodziŵitsa cabwino na coipa, anaonetselatu kuti sanali kudalila Yehova na miyezo yake. Iwo anasankha kudziikila miyezo yawo ya cabwino na coipa. Koma ganizilani cabe zimene iwo anataya. Anataya mwayi wokhala paubwenzi na Yehova. Anatayanso mwayi wokhala na moyo wosatha. Ndipo anapatsila ana awo ucimo na imfa. (Aroma 5:12) Zimene Adamu na Hava anasankha kucita n’zosiyana kwambili na zimene nduna ya ku Itiyopiya inacita pambuyo polalikidwa na Filipo. Ndunayo inayamikila kwambili itamva zimene Yehova na Yesu anaticitila, cakuti nthawi yomweyo inabatizika. (Mac. 8:34-38) Tikadzipatulila kwa Mulungu na kubatizika monga mmene nduna ya ku Itiyopiya inacitila, timaonetsa poyela kuti timayamikila zimene Yehova na Yesu anaticitila. Timaonetsanso kuti timadalila Yehova, na kuzindikila kuti iye ndiye woyenela kutiikila miyezo ya cabwino na coipa. w19.03 2 ¶1-2

Sondo, October 4

Sindidzasiya kukhala ndi mtima wosagawanika.—Yobu 27:5.

Kwa atumiki a Mulungu, kukhala na mtima wamphumphu kumatanthauza kukonda Yehova na mtima wonse, komanso kudzipeleka kwathunthu kwa iye, moti pa zosankha zawo zonse, amaika Mulungu patsogolo. M’Baibo, mawu akuti, “mtima wamphumphu,” kweni-kweni amatanthauza cinthu cathunthu, cabwino-bwino, kapena conse. Mwacitsanzo, nyama zopelekedwa kwa Yehova zinafunika kukhala zopanda cilema. (Lev. 22: 21, 22) Aisiraeli sanaloledwe kupeleka nsembe nyama zodwala, zopanda mwendo umodzi, khutu, kapena diso. Yehova anali kufuna kuti nyama yopelekedwa nsembe izikhala yathunthu, komanso yabwino-bwino. (Mal. 1:6-9) Izi zionetsa kuti Yehova amafuna kuti tikhale na mtima wamphumphu kapena kuti wathunthu. Tiyelekezele motele: Tikapita ku msika, sitingagule cipatso conyemeka, buku long’ambika mapeji, kapena cipangizo cowonongeka mbali zina. Timafuna kugula cinthu cimene n’cathunthu, komanso cabwino-bwino. Yehova naye amafuna kuti tikhale okhulupilika kwathunthu kwa iye. Amafunanso kuti tizim’konda na mtima wonse. w19.02 3 ¶3

Mande, October 5

Ndimakonda kwambili cilamulo canu! Ndimasinkha-sinkha cilamuloco tsiku lonse.—Sal. 119:97.

Kuti titeteze mtima wathu, tifunika kuutseka kuti musaloŵe zinthu zimene zingauipitse. Koma nthawi zina tiyenela kumautsegula kuti muloŵe zinthu zabwino. M’mizinda yakale, mlonda wa pa geti anali kutseka geti ya mzinda kuti adani asaloŵe. Koma nthawi zina, anali kuitsegula pofuna kupeleka mpata woloŵetsa zakudya na zinthu zina mu mzindawo. Cikanakhala kuti mageti sanali kutsegulidwa, sembe anthu anali kufa na njala. Mofananamo, tifunika kumatsegula mtima wathu kaŵili-kaŵili kuti maganizo a Mulungu azititsogolela. Baibo ni buku imene ili na maganizo a Yehova. Conco, nthawi zonse tikamaiŵelenga, timayamba kutengela maganizo a Yehova, zocita zake, na mmene amamvelela. Koma kodi tingacite ciani kuti tizipindula mokwanila na zimene timaŵelenga m’Baibo? Pemphelo limatithandiza ‘kuona zinthu zocititsa cidwi’ za m’Mawu ake. (Sal. 119:18) Cinanso, tifunika kusinkha-sinkha pa zimene timaŵelenga. Ngati tipemphela, kuŵelenga Baibo na kusinkha-sinkha, Mawu a Mulungu amafika “mkati mwa mtima [wathu],” ndipo timayamba kuwakonda kwambili.—Miy. 4:20-22. w19.01 18 ¶14-15

Ciŵili, October 6

Tiyeni nthawi zonse tizitamanda Mulungu. Tizicita zimenezi monga nsembe imene tikupeleka kwa Mulungu.—Aheb. 13:15.

Yehova amadziŵa kuti tili na maluso osiyana-siyana, komanso zocitika mu umoyo wathu zimasiyana-siyana. Ndipo amayamikila kwambili ndemanga zilizonse zimene tingapeleke pa misonkhano. Mwacitsanzo, iye anali kulandila nsembe zosiyana-siyana kucokela kwa Aisiraeli. Aisiraeli ena anali kukwanitsa kupeleka nkhosa kapena mbuzi. Koma Aisiraeli osauka anali kupeleka “njiwa ziŵili kapena ana aŵili a nkhunda.” Ngati Mwisiraeli sanakwanitse kupeleka mbalame ziŵili, Yehova anali kulola kuti angopeleka “ufa wosalala wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa.” (Lev. 5:7, 11) Ngakhale kuti ufa unali wotsika mtengo, Yehova anali kulandila nsembeyo, malinga ngati unali “ufa wosalala.” Umu ni mmene Mulungu wathu wokoma mtima, amaonela ndemanga zathu. Iye sayembekezela kuti popeleka ndemanga, tonse tizilankhula mwaluso kwambili monga Apolo, kapena mogwila mtima kwambili monga Paulo. (Mac. 18:24; 26:28) Cimene Yehova amafuna cabe, n’cakuti tizipeleka ndemanga zabwino mmene tingathele, malinga na luso lathu. Kumbukilani mkazi wamasiye amene anapeleka tumakobidi tuŵili twatung’ono. Cifukwa anapeleka zonse zimene akanatha, Yehova anakondwela naye kwambili.—Luka 21:1-4. w19.01 8-9 ¶3-5

Citatu, October 7

Anthu onse adzadana nanu cifukwa ca dzina langa.—Mat. 10:22.

Monga otsatila a Yesu, timayembekezela kuzondewa. Yesu anakambilatu kuti ophunzila ake adzazunzidwa kwambili m’masiku otsiliza. (Mat. 24:9; Yoh. 15:20) Zimene Yesaya analosela zionetsa kuti kuwonjezela pa kutizonda, adani athu adzaseŵenzetsa zida zosiyana-siyana polimbana nafe. Zida zimenezo, ni cinyengo camacenjela, mabodza amkunkhuniza, cizunzo coopsa, na zina zotelo. (Mat. 5:11) N’zoona kuti Yehova sadzaletsa adani athu kuseŵenzetsa zida zimenezi polimbana nafe. (Aef. 6:12; Chiv. 12:17) Koma sitifunika kucita mantha. Yehova anakamba kuti, “Cida ciliconse” (Yes. 54:17) cimene cidzaseŵenzetsedwa kuti citivulaze “sicidzapambana.” Monga mmene cipupa cingatitetezele ku mvula yoopsa yamkuntho, nayenso Yehova amatiteteza kwa “anthu ankhanza” amene amazunza anzawo. (Yes. 25:4, 5) Ndithudi, adani athu sadzakwanitsa kutiwononga kothelatu! (Yes. 65:17) Adani onse a anthu a Mulungu “sadzakhalanso ngati kanthu ndipo adzatha.”—Yes. 41:11, 12. w19.01 6-7 ¶13-16.

Cinayi, October 8

Pamene pali mzimu wa Yehova, pali ufulu.—2 Akor. 3:17.

Acicepele, Yehova ni Mulungu waufulu, ndipo anakupatsani mtima wofuna kukhala na ufulu. Komabe, iye amafuna kuti muziseŵenzetsa ufulu wanu mwanzelu, cifukwa kucita zimenezi n’citetezo kwa imwe. Mwina mudziŵako ena amene amatamba zamalisece, kucita zaciwelewele, maseŵela oika moyo paciopsezo, kumwa moŵa mwaucidakwa, na kuseŵenzetsa am’kolabongo. N’zoona kuti angasangalale na zinthu zimenezi kwa kanthawi. Koma nthawi zambili zotulukapo zake zimakhala mavuto aakulu, monga matenda, ngakhale imfa kumene. Kuwonjezela apo, amakhala akapolo a zilako-lako zawo. (Agal. 6:7, 8) Acicepele amene amacita zinthu zimenezi angaone monga ali pa ufulu, koma m’ceni-ceni amadziika mu ukapolo. (Tito 3:3) Mosiyana na zimenezi, kutsatila miyezo ya m’Baibo kumatiteteza. Conco, n’zoonekelatu kuti kumvela Yehova kungakuthandizeni kukhala na ufulu komanso thanzi labwino. (Sal. 19:7-11) Cinanso, ngati museŵenzetsa ufulu wanu mwanzelu, kapena kuti mogwilizana na malamulo angwilo a Mulungu komanso mfundo zake, mumaonetsa kuti ndimwe munthu wodalilika. Yehova komanso makolo anu adzakudalilani, nokupatsani ufulu woculukilapo. Ndipo colinga ca Mulungu n’cakuti kutsogolo adzapatse atumiki ake okhulupilika ufulu weni-weni, umene Baibo imaucha “ufulu waulemelelo wa ana a Mulungu.”—Aroma 8:21. w18.12 22-23 ¶16-17

Cisanu, October 9

Mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake, n’kudziphatika kwa mkazi wake, ndipo iwo adzakhala thupi limodzi.—Gen. 2:24.

Kucimwa kwa Adamu kunasintha zinthu zambili. Mwacitsanzo, kunabweletsa imfa, imene imakhudza cikwati. Pofotokoza zakuti Akhristu sali pansi pa Cilamulo ca Mose, mtumwi Paulo anakambako za mmene imfa imakhudzila cikwati. Iye anakamba kuti imfa imathetsa cikwati, komanso kuti mkazi kapena mwamuna wofeledwa amakhala na ufulu wokwatilanso. (Aroma 7:1-3) Cilamulo cimene Mulungu anapatsa Aisiraeli cinali na malangizo okhudza cikwati. Cinali kulola anthu kukwatila cipali. Mcitidwe umenewu unalipo kale pamene Mulungu anali kupeleka Cilamulo kwa Aisiraeli. Koma Mulungu anapeleka malangizo oletsa amuna kucitila nkhanza akazi awo. Mwacitsanzo, ngati Mwisiraeli wakwatila kapolo, ndipo pambuyo pake n’kukwatila mkazi wina waciŵili, sanafunike kuleka kupatsa mkazi woyambayo cakudya, zovala, na mangawa a m’cikwati. Mulungu anali kufuna kuti azimuteteza na kumusamalila mkaziyo. (Eks. 21:9, 10) N’zoona kuti sitili pansi pa Cilamulo ca Mose. Koma izi zitiphunzitsa kuti Yehova amaona cikwati kukhala camtengo wapatali. Kodi zimenezi sizikulimbikitsani kulemekeza cikwati? w18.12 10 ¶3; 11 ¶5-6

Ciŵelu, October 10

Simungakhulupilile ngakhale wina atakufotokozelani.—Hab. 1:5.

Pambuyo pouza Yehova nkhawa zake, n’kutheka kuti Habakuku anayamba kudela nkhawa kuti mwina Yehova adzamudzudzula. Koma pokhala Tate wacifundo ndi woganizila ena, Yehova sanam’dzudzule cifukwa cofotokoza madandaulo ake moona mtima. Mulungu anadziŵa kuti Habakuku anali kucondelela thandizo cifukwa covutika mtima na zoipa zimene zinali kucitika. Conco, Yehova anauza Habakuku zimene zinali pafupi kucitikila Ayuda osamvela. N’kutheka kuti Habakuku ndiye anali woyamba kuuziwa na Yehova kuti kwatsala kanthawi kocepa kuti Ayuda aciwawa awonongedwe. Yehova anatsimikizila Habakuku kuti anali wokonzeka kucitapo kanthu. Anamuuza kuti adzaseŵenzetsa Akasidi, kapena kuti Ababulo polanga Ayuda oipa ndi aciwawa amenewo. Pamene Yehova anaseŵenzetsa mawu akuti “m’masiku anu,” iye anaonetsa kuti ciweluzoco cidzabwela mneneli Habakuku akali moyo, kapena Aisiraeli ena amene analipo pa nthawiyo asanafe. Habakuku sanayembekezele kuti Yehova angamuyankhe mwanjila imeneyi. Zimene Yehova anamuuza, zakuti adzaseŵenzetsa Ababulo polanga anthu ake, zinaonetsa kuti mavuto adzawonjezeka pakati pa Ayuda. w18.11 15 ¶7-8

Sondo, October 11

[Cifunilo ca Mulungu n’cakuti] anthu, kaya akhale a mtundu wotani, apulumuke ndi kukhala odziŵa coonadi molondola. —1 Tim. 2:4.

Kodi imwe mumawaona bwanji anthu a mitundu yosiyana-siyana amene sanaphunzile coonadi? Mtumwi Paulo anali kulalikila m’masunagoge kwa Ayuda amene anali kum’dziŵa kale Mulungu woona. Koma anali kulalikilanso kwa anthu a mitundu ina amene anali kulambila mafano. Mwacitsanzo, paulendo woyamba wa Paulo wa umishonale, anthu a ku Lusitara anayamba kuona Paulo na Baranaba monga milungu imene inasanduka anthu. Anayamba kuwachula na maina a milungu yawo yonama, Zeu na Heme. Kodi Paulo na Baranaba ananyadila cifukwa cotamandidwa mwanjila imeneyi? Kodi anaona kuti anali kulandila madalitso pambuyo pozunzidwa m’mizinda iŵili imene analalikilako asanafike ku Lusitara? Kodi anaganiza kuti kuchuka kwawo kudzathandiza kupititsa patsogolo nchito yofalitsa uthenga wabwino? Kutalitali! Poonetsa kusagwilizana na zimene anthuwo anali kucita, mwamsanga Paulo na Baranaba anang’amba zovala zawo, na kuthamanga kukaloŵa m’khamu la anthulo akufuula kuti: “Anthu inu, mukucitilanji zimenezi? Ifenso ndife anthu okhala ndi zofooka ngati inu nomwe.”—Mac. 14:8-15. w18.09 4-5 ¶8-9

Mande, October 12

Kodi zoonadi inu simukudziŵa kuti anthu osalungama sadzaloŵa mu ufumu wa Mulungu? . . . Ndipo ena mwa inu munali otelo. Koma mwasambitsidwa kukhala oyela; . . . mwayesedwa olungama. —1 Akor. 6:9, 11.

Kuti tilabadile coonadi na kuyamba kutsatila miyezo ya m’Baibo ya makhalidwe abwino, tifunika kukhala okonzeka kusintha maganizo na kuleka makhalidwe oipa. Onani zimene Petulo anakamba pa nkhaniyi. Iye anati: “Monga ana omvela, lekani kukhala motsatila zilakolako zimene munali nazo kale pamene munali osadziŵa. Koma . . . khalani oyela m’makhalidwe anu onse.” (1 Pet. 1:14, 15) Mzinda wa Korinto unali wodzala na makhalidwe oipa. Conco, kuti anthu a mu mzindawo agule coonadi, anafunika kupanga masinthidwe aakulu mu umoyo wawo. Mofananamo, anthu ambili masiku ano asiya makhalidwe oipa n’colinga cakuti agule coonadi. Petulo anakumbutsanso Akhristu a m’nthawi yake kuti: “Nthawi imene yapitayi inali yokwanila kwa inu kucita cifunilo ca anthu a m’dzikoli pamene munali kucita zinthu zosonyeza khalidwe lotayilila, zilakolako zoipa, kumwa vinyo mopitilila muyezo, maphwando aphokoso, kumwa kwa mpikisano, ndi kupembedza mafano kosaloleka.”—1 Pet. 4:3. w18.11 6 ¶13

Ciŵili, October 13

Onse amene anali ndi maganizo abwino amene akanawathandiza kukapeza moyo wosatha anakhala okhulupilila.—Mac. 13:48.

Kodi tingawapeze bwanji anthu amene ali na ‘maganizo amene angawathandize kukapeza moyo wosatha’? Monga mmene zinalili m’nthawi ya atumwi, anthu amenewa tingawapeze kokha mwa kugwila nchito yolalikila. Tifunika kutsatila malangizo amene Yesu anapeleka. Iye anati: “Mukaloŵa mumzinda kapena m’mudzi uliwonse, fufuzani mmenemo yemwe ali woyenelela.” (Mat. 10:11) Timadziŵa kuti pali anthu odzikuza, osaona mtima, kapena opanda cidwi na zinthu zauzimu, amene sangalabadile uthenga wabwino. Conco, timasakila anthu amene ni oona mtima, odzicepetsa, komanso amene ali na njala ya coonadi. Tingayelekezele nchito imeneyi na zimene Yesu anali kucita pogwila nchito yake ya ukalipentala. Iye anali kusakila mapulanga abwino amene angawaseŵenzetse popanga mipando, mathebo, zitseko, majoko, na zinthu zina. Akapeza pulanga yabwino, anali kutenga zida zake na kupanga cinthu cimene akufuna. Na ise tiyenela kuyesetsa kusakila anthu oona mtima na kuwapanga kukhala ophunzila a Khristu.—Mat. 28:19, 20. w18.10 12 ¶3-4

Citatu, October 14

Filipo anapita kumzinda wa Samariya ndi kuyamba kulalikila za Khristu kwa anthu akumeneko.—Mac. 8:5.

Mlaliki Filipo ni citsanzo cabwino cifukwa anaikabe mtima wake pa nchito yolalikila, ngakhale pamene zinthu zinasintha. Sitefano ataphedwa cifukwa ca cikhulupililo cake, mu Yerusalemu munabuka cizunzo cacikulu. Pa nthawiyo, Filipo anali atangopatsidwa kumene utumiki watsopano. (Mac. 6:1-6) Koma pamene ophunzila a Khristu anamwazikana cifukwa ca cizunzo, Filipo sanangokhala phee n’kumaonelela zimene zikucitika. Iye anapita kukalalikila ku Samariya. Pa nthawiyo, anthu ambili a kumeneko anali asanamveleko uthenga wabwino. (Mat. 10:5; Mac. 8:1, 5) Filipo anali wokonzeka kupita kulikonse kumene mzimu wa Mulungu unam’tsogolela. Ndiye cifukwa cake Yehova anam’tumiza kukalalikila ku gawo latsopano. Iye anali munthu wopanda tsankho. Koma Ayuda ambili anali kuona Asamariya monga anthu otsika. Conco, pamene Filipo anapita kukalalikila ku Samariya, Asamariya ambili ayenela kuti anatsitsimulidwa na uthenga wake. Baibo imakamba kuti makamu a anthu anali “kuchela khutu ndi mtima umodzi.” (Mac. 8:6-8) Filipo anaikabe mtima wake pa nchito yolalikila. Mwa ici, Yehova anam’dalitsa kwambili pamodzi na banja lake.—Mac. 21:8, 9. w18.10 29-30 ¶14-16

Cinayi, October 15

Tiyeni tiganizilane kuti tilimbikitsane pa cikondi ndi nchito zabwino.—Aheb. 10:24.

Tsiku lina pamene Yesu anali ku Dekapole, anthu “anam’bweletsela munthu wogontha komanso wovutika kulankhula.” (Maliko 7:31-35) Yesu sanam’cilitsile pa gulu munthuyo. Koma ‘anam’tenga ndi kucoka naye pakhamu la anthulo.’ Kenako anam’cilitsa. N’cifukwa ciani anacita zimenezi? Zioneka kuti munthuyo sanali kukhala womasuka pa gulu cifukwa ca vuto lakelo. Pozindikila zimenezi, mwina n’cifukwa cake Yesu anamutengela pambali. Ise sitingathe kucilitsa anthu mozizwitsa. Koma tingathe kuganizila zosoŵa za Akhristu anzathu na kuwathandiza. Ndipo izi n’zimene tiyenela kucita. Yesu anadziŵa mmene munthu wogontha uja anali kumvelela, ndipo anacita zinthu mom’ganizila. Mofananamo, muzicita zinthu moganizila okalamba ndi odwala. Mpingo wacikhristu umadziŵika kwambili na cikondi, osati cabe mzimu wa cangu pa nchito. (Yoh. 13:34, 35) Cikondi cimeneci cimatilimbikitsa kuyesetsa kuthandiza acikulile na olemala kupezeka pa misonkhano na kulalikila uthenga wabwino wa Ufumu. Timacita izi olo kuti zimene iwo angacite mu ulaliki n’zocepa.—Mat. 13:23. w18.09 29-30 ¶7-8

Cisanu, October 16

Aliyense wa ife azikondweletsa mnzake pa zinthu zabwino zomulimbikitsa.—Aroma 15:2.

Mtumiki aliyense wa Yehova ni wamtengo wapatali kwa iye na kwa mwana wake Yesu, amene anapeleka moyo wake monga nsembe ya dipo. (Agal. 2:20) Timawakonda kwambili abale na alongo athu. Ndipo timafuna kucita nawo zinthu mokoma mtima ndi mwacikondi. Conco, kuti tikhale anthu olimbikitsa, tiyenela ‘kutsatila zinthu zobweletsa mtendele ndiponso zolimbikitsana.’ (Aroma 14:19) Tonse tikuyembekezela mwacidwi nthawi imene dziko lapansi lidzakhala Paradaiso, mmene simudzakhala zinthu zilizonse zofooketsa. Simudzakhala matenda, nkhondo, imfa, cizunzo, mavuto a m’banja, na zokhumudwitsa. Pofika kumapeto kwa zaka 1000, anthu adzakhala angwilo. Ndipo anthu amene adzapyola ciyeso comaliza adzakhala padziko lapansi monga ana a Yehova Mulungu. Iwo adzakhala na “ufulu waulemelelo wa ana a Mulungu.” (Aroma 8:21) Conco, tiyeni tipitilize kuonetsana cikondi cimene cimamangilila, komanso kuthandizana kuti tonse tikalandile mphoto yokondweletsa imeneyo. w18.09 14 ¶10; 16 ¶18

Ciŵelu, October 17

Ndimakonda kwambili cilamulo canu! Ndimasinkhasinkha cilamuloco tsiku lonse.—Sal. 119:97.

Kuŵelenga Mawu a Mulungu kofuna kuphunzila zinthu n’kosiyana ndi kuŵelenga wamba, kapena kungoconga mayankho m’nkhani inayake yophunzila. Pamene tiŵelenga, tifunika kuganizila zimene nkhaniyo itiphunzitsa ponena za Yehova, njila zake, ndiponso mmene amaonela zinthu. Timafunikanso kumvetsetsa cifukwa cake Mulungu amatilamula kucita zinthu zina na kutiletsa kucita zina. Cinanso, tifunika kudzifunsa kuti, ‘Malinga n’zimene naŵelenga, n’ciani cimene nifunika kusintha pa zocita zanga komanso pa kaganizidwe kanga?’ Sikuti pa phunzilo lililonse laumwini, tiyenela kusinkha-sinkha zonse zimenezi. Koma kuti tipindule na phunzilolo, tiyenela kumapatula nthawi yokwanila yosinkha-sinkha pa zimene taŵelenga. Mwina tingapatule hafu ya nthawi imene timathela pocita phunzilo laumwini kuti tisinkhe-sinkhe. (1 Tim. 4:15) Ngati nthawi zonse timasinkha-sinkha Mawu a Mulungu, timafika ‘pozindikila,’ kapena kuti kukhutila kuti kaonedwe ka zinthu ka Yehova ndiko kabwino koposa. Conco, timayamba kuona zinthu monga mmene iye amazionela. Ndipo maganizo athu amasintha. (Aroma 12:2) Motelo, pang’ono-m’pang’ono, timayamba kuyendela maganizo a Yehova. w18.11 24 ¶5-6

Sondo, October 18

Ndife anchito anzake a Mulungu.—1 Akor. 3:9.

M’nthawi ya atumwi, Paulo anakamba kuti iye na Akhristu anzake anali “anchito anzake a Mulungu” cifukwa ca nchito yawo yofesa na kuthilila mbewu za coonadi. (1 Akor. 3:6) Na ise masiku ano, tingaonetse kuti ndise “anchito anzake a Mulungu” mwa kuseŵenzetsa mowolowa manja nthawi yathu, cuma, na mphamvu zathu pa nchito yolalikila imene tapatsidwa. Kukamba zoona, umenewu ni mwayi waukulu ngako! Kuseŵenzetsa nthawi na mphamvu zathu mowolowa manja pa nchito yolalikila na kupanga ophunzila kumabweletsa cimwemwe coculuka. Ofalitsa ambili amene anakhalapo na mwayi wotsogoza maphunzilo a Baibo opita patsogolo, angakuuzeni kuti kucita zimenezi n’kokondweletsa kwambili. Cimakhala cokondweletsa ngako kuona nkhope za anthu oona mtima zikuwala na cimwemwe, pambuyo pomvetsetsa mfundo za coonadi ca m’Baibo. Zimakondweletsanso kuwaona akukula m’cikhulupililo, akusintha umoyo wawo, na kuyamba kuuzako ena coonadi cimene aphunzila. Yesu nayenso anakondwela kwambili pamene ophunzila 70 amene anawatumiza kukalalikila “anabwelela ali osangalala,” cifukwa utumiki wawo unayenda bwino.—Luka 10:17-21. w18.08 20 ¶11-12

Mande, October 19

Munthu wodalila mtima wake ndi wopusa.—Miy. 28:26.

Zingakhale msampha ngati tayamba kudalila kwambili luso lathu lomvetsa zinthu. Tingayambe kuganiza kuti tikangoona kapena kumva zinthu zina zake, tikhoza kuzimvetsetsa olo kuti sitidziŵa mfundo zonse. Kusemphana maganizo na Mkhristu mnzathu mu mpingo cifukwa cosiyana zibadwa, ni vuto limene lingatilepheletse kufufuza zoona pa nkhani imene tamvela. Ngati nthawi zonse timaganizila pa zimene anatilakwila, tingayambe kumukayikila m’bale wathuyo. Ndipo tikamvela nkhani inayake yoipa yokhudza m’baleyo, mwamsanga tingaikhulupilile. Tiphunzilanji pamenepa? Kusungila abale athu cakukhosi kungatilengetse kukhulupilila zinthu zabodza zimene tilibe nazo umboni. (1 Tim. 6:4, 5) Tingapewe vuto limeneli mwa kusalola nsanje na kaduka kuzika mizu mu mtima mwathu. M’malo mwake, tiyenela kukwanilitsa udindo umene tili nawo, wokonda Akhristu anzathu na kuwakhululukila na mtima wonse.—Akol. 3:12-14. w18.08 6 ¶15; 7 ¶18

Ciŵili, October 20

Kumwamba ndi kwa Yehova, . . . dziko lapansi ndi zonse zili mmenemo ndi zake zonsezo.—Deut. 10:14.

Popeza kuti Yehova ndiye anatilenga, tonse ndise anthu ake. (Sal. 100:3; Chiv. 4:11) Komabe, kuyambila kalekale, Yehova wakhala akusankha anthu ena, kuti akhale anthu ake apadela. Mwacitsanzo, Salimo 135 imakamba za olambila Yehova okhulupilika a m’nthawi ya Isiraeli kuti anali “cuma cake capadela.” (Sal. 135:4) Komanso buku la Hoseya linakambilatu kuti m’tsogolo anthu ena amene si Aisiraeli adzakhala anthu a Yehova. (Hos. 2:23) Ulosi umenewu unakwanilitsika pamene Yehova anayamba kusankha anthu a mitundu ina kuti nawonso akhale m’gulu la okalamulila pamodzi na Khristu kumwamba. (Mac. 10:45; Aroma 9:23-26) “Mtundu woyela” umenewu ni “cuma capadela” ca Yehova. Anthu a mu mtundu umenewu anadzozedwa na mzimu woyela komanso anasankhidwa kuti akakhale na moyo kumwamba. (1 Pet. 2:9, 10) Nanga bwanji za Akhristu ambili okhulupilika amene ali na ciyembekezo codzakhala na moyo kwamuyaya pa dziko lapansi? Amenewa Yehova amawaonanso kuti ndi ‘anthu ake osankhidwa mwapadela.’—Yes. 65:22. w18.07 22 ¶1-2

Citatu, October 21

Khalani ndi maganizo amenewa, amenenso Khristu Yesu anali nawo . . . Anasiya zonse zimene anali nazo n’kukhala ngati kapolo.—Afil. 2:5, 7.

Akhristu oona amatengela Khristu, amene anatipatsa citsanzo cabwino ngako pankhani ya kuwolowa manja. (Mat. 20:28) Tingacite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi n’ciani cina cimene ningacite coonetsa kuti nikutsatila citsanzo ca Yesu mosamala kwambili?’ (1 Pet. 2:21) Yehova angatiyanje ngati titengela citsanzo cake cabwino, komanso ca Khristu pankhani ya kuwolowa manja. Tingacite izi mwa kukhala oganizila ena na kupeza njila zowathandizila pa zosoŵa zawo. Zimene Yesu anakamba m’fanizo la Msamariya wacifundo, zionetselatu kuti ophunzila ake ayenela kukhala odzipeleka pothandiza anthu ena, kaya akhale a mtundu wotani. (Luka 10:29-37) Kodi mukumbukila funso imene inacititsa Yesu kukamba fanizo la Msamariya wacifundo? Myuda wina anamufunsa kuti: “Nanga mnzanga amene ndikuyenela kumukonda ndani kwenikweni?” Yankho imene Yesu anapeleka ionetsa kuti ngati tifuna kuti Mulungu atiyanje, tiyenela kukhala ofunitsitsa kuthandiza ena mmene Msamariya wacifundo anacitila. w18.08 19 ¶5-6

Cinayi, October 22

Mngelo uja . . . anati: “Mtendele ukhale nawe, iwe wodalitsidwa koposawe, Yehova ali nawe.” —Luka 1:28.

Kodi Yehova anam’dalitsa bwanji Mariya cifukwa colela Mwana wake mokhulupilika? Mulungu anaonetsetsa kuti mawu na zocita zake zalembedwa m’Baibo. Cioneka kuti zinali zosatheka kwa Mariya kuyenda na Yesu mu utumiki wake wa zaka zitatu na hafu. Mariya anatsala ku Nazareti, mwina cifukwa cakuti anali mayi wamasiye. Mwa ici, iye sanakhale na mwayi woona zocitika zambili zocititsa cidwi zimene ena anaona. Olo zinali conco, anakwanitsa kupezekapo pa nthawi ya imfa ya Yesu. (Yoh. 19:26) Patapita nthawi, Mariya anapezeka ku Yerusalemu pamodzi na ophunzila ena, patatsala masiku angapo kuti ophunzilawo adzozedwe na mzimu woyela pa Pentekosite. (Mac. 1:13, 14) Mwacionekele, nayenso anadzozedwa pamodzi na ophunzila ena amene analipo. Ngati zinalidi conco, ndiye kuti iye anapatsidwa mwayi wokakhala na Yesu kumwamba kwamuyaya. Ndithudi! Yehova anam’dalitsa kwambili Mariya cifukwa com’tumikila mokhulupilika. w18.07 9 ¶11; 10 ¶14

Cisanu, October 23

Citani zonse ku ulemelelo wa Mulungu.—1 Akor. 10:31.

Mu utumiki wake wonse, Yesu anaphunzitsa mfundo za coonadi pofuna kuthandiza ophunzila ake kuzindikila zotulukapo za khalidwe loipa kapena maganizo oipa. Mwacitsanzo, anawaphunzitsa kuti kusunga mkwiyo kungasonkhezele munthu kucita ciwawa, ndipo cilakolako coipa cingapangitse munthu kucita ciwelewele. (Mat. 5:21, 22, 27, 28) Kuti tiphunzitse bwino cikumbumtima cathu, tiyenela kulola mfundo za Mulungu kutitsogolela. Tikacita izi, Mulungu adzalandila ulemelelo. Pa nkhani zina, Akhristu angapange zosankha zosiyana olo kuti onse ali na zikumbumtima zophunzitsidwa bwino Baibo. Mwacitsanzo, ganizilani nkhani ya kumwa moŵa. Baibo siiletsa kumwa moŵa pang’ono. Koma imaticenjeza kuti tifunika kupewa kumwa kwambili ndi ucakolwa. (Miy. 20:1; 1 Tim. 3:8) Komabe, izi sizitanthauza kuti ngati Mkhristu amamwa pa mlingo woyenela, ndiye kuti basi zonse zili bwino. Pali mbali zina zimene afunika kuziganizila. Mwacitsanzo, olo kuti cikumbumtima cake sicingamuvutitse, iye afunikanso kuganizila cikumbumtima ca ena. w18.06 18 ¶10-11

Ciŵelu, October 24

Cenjelani ndi cofufumitsa ca Afarisi ndi ca Herode.—Maliko 8:15

Mpake kuti Yesu anacenjeza ophunzila ake mwamphamvu kuti akhale maso na cofufumitsa, kapena kuti ziphunzitso zimene Afarisi, Asaduki, ndi a cipani ca Herode anali kulimbikitsa. (Mat. 16:6, 12) N’zocititsa cidwi kuti Yesu anauza ophunzila ake zimenezi pasanapite nthawi itali kucokela pamene anthu anafuna kumulonga ufumu. Ngati cipembedzo citenga mbali m’zandale, kaŵili-kaŵili zotulukapo zake zimakhala ciwawa. Yesu anauza ophunzila ake kuti safunika kutengako mbali m’zandale. Ici n’cimodzi mwa zifukwa zimene ansembe aakulu na Afarisi anapangila ciwembu copha Yesu. Anali kuyopa kuti anthu adzayamba kulemekeza kwambili iye m’malo mwa iwo. Ndipo pamapeto pake iwo sadzakhalanso na mphamvu pa zandale ndi pa za cipembedzo. Iwo anati: “Ngati timulekelela, onse adzakhulupilila mwa iye, ndipo Aroma adzabwela kudzatenga malo athu ndi mtundu wathu.” (Yoh. 11:48) N’cifukwa cake Mkulu wa Ansembe, Kayafa, anali patsogolo popanga ciwembu ca kupha Yesu.—Yoh. 11:49-53; 18:14. w18.06 6 ¶12-13

Sondo, October 25

Cikondi canu cisakhale ca ciphamaso.—Aroma 12:9.

Nyambo yokopa kwambili imene Satana amaseŵenzetsa ni zamizimu. Masiku ano, iye amalimbikitsa anthu kucita cidwi na ziŵanda poseŵenzetsa zipembedzo zonama na zosangalatsa zosiyana-siyana. Zinthu monga mafilimu, maseŵela a pa kompyuta, na zosangalatsa zina, zimalengetsa anthu kuona ngati zamizimu n’zokondweletsa. Kodi tingapewe bwanji kukodwa mu msampha umenewu? Sitiyenela kuyembekezela kuti gulu la Mulungu lidzacita kutindandalikila zosangalatsa zoyenela na zosayenela. Aliyense payekha afunika kuphunzitsa cikumbumtima cake kuti cizimutsogolela mogwilizana na miyezo ya Mulungu. (Aheb. 5:14) Komanso, tidzakwanitsa kupanga zosankha mwanzelu ngati titsatila malangizo a mtumwi Paulo. Tingadzifunse kuti: ‘Kodi kucita zosangalatsa zimenezi kudzaonetsa kuti ndine wacinyengo? Ngati anthu amene nimaphunzila nawo Baibo kapena amene nimacitako maulendo obwelelako aonako zosangalatsa zanga, kodi angaone kuti nimacitadi zimene nimawaphunzitsa?’ Ngati tiyesetsa kucita zinthu mogwilizana na zimene timaphunzitsa, tidzakhala otetezeka ku misampha ya Satana.—1 Yoh. 3:18. w18.05 25 ¶13

Mande, October 26

Cimene ndikufunitsitsa mumtima mwanga ndiponso pembedzelo langa kwa Mulungu ndi lakuti Aisiraeli apulumutsidwe.—Aroma 10:1.

Kodi tingatengele bwanji citsanzo ca Paulo? Coyamba, tiyenela kuyesetsa na mtima wonse kusakila anthu ‘amene ali ndi maganizo abwino amene angawathandize kukapeza moyo wosatha.’ Caciŵili, tiyenela kucondelela Yehova m’pemphelo kuti atsegule mitima ya anthu oona mtima. (Mac. 13:48; 16:14) Silvana, mpainiya amene watumikila kwa zaka pafupi-fupi 30, anati: “Nikalibe kufika pa nyumba ya munthu m’gawo langa, nimapemphela kwa Yehova kuti anithandize kukhala na maganizo oyenelela.” Timapemphelanso kwa Mulungu kuti, kupitila mwa angelo, atithandize kupeza anthu oona mtima. (Mat. 10:11-13; Chiv. 14:6) Robert, amene watumikila monga mpainiya kwa zaka zoposa 30, anati: “Kuseŵenzela pamodzi na angelo amene amadziŵa bwino zocitika mu umoyo wa anthu n’kokondweletsa.” Cacitatu, timayesetsa kuona zabwino mwa anthu, kuphatikizapo zizindikilo zoonetsa kuti angathe kukhala atumiki a Mulungu. Carl, mkulu anati, “Nimayesetsa kuona zizindikilo zilizonse zoonetsa kuti munthu ni woona mtima, monga kumwetulila, nkhope ya ubwenzi, kapena funso locokela pansi pa mtima.” Inde, monga Paulo, tingapitilize kubala zipatso mopilila. w18.05 15 ¶13; 16 ¶15

Ciŵili, October 27

Tiyeni tiganizilane kuti tilimbikitsane . . . , ndipo tiwonjezele kucita zimenezi, makamaka pamene mukuona kuti tsikulo likuyandikila.—Aheb. 10:24, 25.

Tikamva kuti anthu amene tinawathandiza kuphunzila coonadi akutumikila Mulungu mokhulupilika, timalimbikitsidwa ngako, monga mmene mtumwi Yohane analimbikitsidwila. Iye analemba kuti: “Palibe cimene cimandisangalatsa kwambili kuposa kumva kuti ana anga akuyendabe m’coonadi.” (3 Yoh. 4) Apainiya ambili amalimbikitsiwa kwambili akadziŵa kuti ena mwa anthu amene iwo anawaphunzitsa coonadi akali kutumikila Yehova mokhulupilika, mwinanso kuti akucita upainiya. Conco ngati mpainiya wafooka, tingamulimbikitse mwa kum’kumbutsa zabwino zimene wakhala akucita pothandiza ena. Oyang’anila dela ambili amakamba kuti iwo na azikazi awo amalimbikitsiwa ngako akalandila kakalata kowayamikila pambuyo pocezela mpingo. Ni mmenenso akulu, apainiya, na atumiki a pa Beteli amamvelela akayamikilidwa cifukwa cotumikila mokhulupilika. w18.04 23 ¶14-15

Citatu, October 28

[Mfumu isaculukitse] akazi kuti mtima wake ungapatuke. —Deut. 17:17.

Solomo sanamvele lamulo limeneli cakuti m’kupita kwa nthawi anakwatila akazi 700. Komanso anatenga akazi ena apambali 300. (1 Maf. 11:3) Akazi ake ambili sanali Aisiraeli, ndipo anali kulambila mafano. Conco pamenepa, Solomo anaphwanyanso lamulo la Mulungu loletsa kukwatila akazi a mitundu ina. (Deut. 7:3, 4) Cifukwa cakuti Solomo anali kunyalanyaza malamulo a Yehova, m’kupita kwa nthawi anacita macimo aakulu kwambili. Iye anamangila guwa la nsembe mulungu wamkazi wochedwa Asitoreti ndi guwa lina la mulungu wochedwa Kemosi. Ndipo anayamba kulambila mafano pamodzi ndi azikazi ake. Iye anacita kumanga maguwa ansembewo pa phili loyang’anana ndi mzinda wa Yerusalemu, kumene anamangako kacisi wa Yehova. (1 Maf. 11:5-8; 2 Maf. 23:13) Mwina Solomo anaganiza kuti Yehova adzanyalanyaza zolakwa zake malinga ngati apitiliza kupeleka nsembe pa kacisi. Koma Yehova sanyalanyaza macimo. w18.07 18-19 ¶7-9

Cinayi, October 29

Nyamulani cishango cacikulu cacikhulupililo, cimene mudzathe kuzimitsila mivi yonse yoyaka moto ya woipayo.—Aef. 6:16.

Mivi ina “yoyaka moto” imene Satana angakuponyeleni ndiyo kufalitsa mabodza akuti Yehova sakuonani monga ofunika ndiponso sakukondani. Ida wa zaka 19, wakhala akuvutika na maganizo odziona monga wosafunika. Iye anati: “Nthawi zambili, nimaona ngati kuti Yehova ali nane patali ndipo safuna kukhala Mnzanga.” Kodi Ida amacita ciani polimbana na vuto imeneyi? Iye anati: “Misonkhano imalimbitsa kwambili cikhulupililo canga. Kale, n’nali kungopezeka pa misonkhano koma osayankhapo, poganiza kuti palibe aliyense amene angamvetsele zokamba zanga. Koma lomba nimakonzekela misonkhano na kuyesetsa kuyankhapo, kaŵili kapena katatu. Citsanzo ca Ida citiphunzitsa mfundo inayake yofunika kwambili. Cishango ceni-ceni cimene msilikali anganyamule, saizi yake siimasintha, koma cishango cathu cacikhulupililo cingakule kapena kucepa. Zimadalila pa zimene timacita. (Mat. 14:31; 2 Ates. 1:3) Conco, kukulitsa cikhulupililo cathu n’kofunika ngako. w18.05 29-30 ¶12-14

Cisanu, October 30

Ndicite ciani kuti ndipulumuke?—Mac. 16:30.

Woyang’anila ndende uja anamvetsela na kupempha thandizo pambuyo pakuti civomezi cacitika. (Mac. 16:25-34) N’cimodzi-modzi masiku ano. Anthu ena amene poyamba sanali kulabadila uthenga wathu wa m’Baibo, angayambe kumvetsela na kusakila thandizo pambuyo pokumana ndi mavuto aakulu mosayembekezeleka. Angakhale kuti anacotsedwa nchito mosayembekezela ndipo ni othedwa nzelu. Ena angakhale na nkhawa kwambili pambuyo powapeza na matenda aakulu, kapena angakhale na cisoni cacikulu cifukwa ca imfa ya munthu amene anali kum’konda. Iwo angayambe kudzifunsa mafunso okhudza colinga ca moyo, amene poyamba sanali kuwaganizila. Mwina angadzifunse kuti, ‘Kodi ningacite ciani kuti nikapulumuke?’ Ndipo tikakumana nawo mu ulaliki, kwa nthawi yoyamba mu umoyo wawo, angafune kumvetsela uthenga wathu wopatsa ciyembekezo. Conco, pamene tipitiliza kugwila nchito yolalikila mokhulupilika, timakhala okonzeka kupeleka cilimbikitso kwa anthu panthawi imene akufunikila thandizo.—Yes. 61:1. w18.05 19-20 ¶10-12

Ciŵelu, October 31

Mzimu wa Yehova uli pa ine, cifukwa iye anandidzoza kuti ndilengeze uthenga wabwino.—Luka 4:18.

Lelolino, anthu ambili akali ocititsidwa khungu na mulungu wa nthawi ino ndipo ni akapolo a cuma, cipembedzo conama, na cikhalidwe cawo. (2 Akor. 4:4) Conco, ni mwayi wathu kutengela citsanzo ca Yesu mwa kuthandiza anthu kudziŵa Yehova, Mulungu waufulu, na kuyamba kumulambila. (Mat. 28:19, 20) Imeneyi si nchito yopepuka, ili na zovuta zambili. M’maiko ena, anthu ambili alibe cidwi, ndipo ena ni otsutsa. Conco, aliyense afunika kudzifunsa kuti: ‘Kodi ningaseŵenzetse ufulu wanga kuti niwonjezele zocita pocilikiza nchito ya Ufumu?’ N’zolimbikitsa ngako kuti Akhristu ambili azindikila kuti nchito imeneyi ifunika kugwilidwa mwacangu, cakuti ena akukhala na umoyo wosalila zambili pofuna kuwonjezela zocita mu ulaliki. (1 Akor. 9:19, 23) Ena a iwo amatumikila m’magawo awo, ena anakukila kosoŵa. Ha! N’zokondweletsa cotani nanga kuona mmene abale na alongo akuseŵenzetsela mwanzelu ufulu wawo potumikila Yehova!—Sal. 110:3. w18.04 11-12 ¶13-14

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani