November
Sondo, November 1
Iye wakudya cakudya ici adzakhala ndi moyo kosatha.—Yoh. 6:58.
Cifukwa cotumikila Yehova, tili na ciyembekezo cakuti posacedwa, Yehova adzatipatsa zonse zimene Adamu na Hava anataya, kuphatikizapo moyo wosatha. Adamu na Hava anasankha kupandukila Yehova cifukwa sanakulitse cikondi cawo pa iye. Olo zinali conco, Yehova anawalola kukhala na moyo kwa zaka zambili ndithu, n’colinga cakuti abeleke ana na kudziikila okha malangizo olelela anawo. Posapita nthawi, zotulukapo za kusamvela kwa Adamu na Hava, zinaonetsa kuti iwo sanacite zinthu mwanzelu. Mwana wawo wamkulu anapha mng’ono wake wosalakwa. Ndipo m’kupita kwa nthawi, ciwawa komanso dyela zinaculuka pakati pa anthu. (Gen. 4:8; 6:11-13) Komabe, Yehova anakonza njila yopulumutsila ana onse a Adamu na Hava amene amasankha kum’tumikila. (Yoh. 6:38-40, 57) Pamene muphunzila zambili zokhudza kuleza mtima kwa Yehova na cikondi cake, cikondi canu pa iye cidzakula. Komanso, mudzapewa kutengela zocita za Adamu na Hava. M’malomwake, mudzasankha kudzipatulila kwa Yehova. w19.03 2 ¶3; 4 ¶9
Mande, November 2
Nonsenu mukhale . . . omvelana cisoni.—1 Pet. 3:8.
Kuti muonetse khalidwe la cifundo kwa ena, yesetsani kuganizila zimene anthu a m’banja mwanu komanso Akhristu anzanu akupitamo. Muzicita cidwi na Akhristu acinyamata mu mpingo, odwala, okalamba, komanso amene ataikilidwa okondedwa awo mu imfa. Afunseni mmene zinthu zikuyendela mu umoyo wawo. Amvetseleni mwachelu pamene afotokoza nkhawa zawo. Onetsani kuti mukumvetsetsa mavuto amene akupitamo. Citani zilizonse zimene mungathe kuti muwathandize. Tikacita zimenezi, ndiye kuti tikuonetsa cikondi ceni-ceni m’zocita zathu. (1 Yoh. 3:18) Tifunika kukhala ololela pamene tithandiza ena. Cifukwa ciani? Cifukwa cakuti anthu amacita zinthu mosiyana-siyana akakumana na mavuto. Ena amakhala omasuka kukamba mmene amvelela, pamene ena samasuka kufotokoza. Conco, pamene tithandiza ena, tifunika kupewa kuwafunsa mafunso pa nkhani zaumwini. (1 Ates. 4:11) Nthawi zina, munthu angamasuke na kutifotokozela mmene akumvelela. Koma mwina tingaone kuti maganizo ake ni osiyana na mmene ife tionela zinthu. Zikakhala telo, sitifunika kum’tsutsa, koma tiyenela kumvetsetsa mmene iye akumvelela. Tiyenela kukhala ofulumila kumva, koma odekha polankhula.—Mat. 7:1; Yak. 1:19. w19.03 19 ¶18-19
Ciŵili, November 3
Ndinacita mantha kwambili. —Neh. 2:2.
Kodi mumacita mantha pokamba za coonadi pa gulu? Kumbukilani Nehemiya. Iye anali kutumikila m’nyumba ya mfumu yamphamvu. Koma pa nthawi ina, anakhala wacisoni atamva kuti mpanda wa Yerusalemu unagwa, ndipo zipata zake zinatenthedwa na moto. (Neh. 1:1-4) Pamene mfumu inafunsa Nehemiya cifukwa cake nkhope yake inali yacisoni, iye anacita mantha kwambili. Koma mwamsanga, anapemphela kwa Mulungu, ndipo kenako anayankha. Poyankha pempho la Nehemiya, mfumuyo inacita zambili pothandiza anthu a Mulungu. (Neh. 2:1-8) Citsanzo cina n’ca Yona. Pamene Yehova anam’tuma kuti akapeleke uthenga waciweluzo kwa anthu a ku Nineve, Yona anacita mantha kwambili cakuti anathaŵa n’kuloŵela kwina. (Yona 1:1-3) Koma mwa thandizo la Yehova, Yona anakwanitsa kupita ku Nineve kukalalikila. Ndipo cifukwa ca uthenga umene analengeza, anthu a ku Nineve analapa moti sanawonongedwe. (Yona 3:5-10) Citsanzo ca Nehemiya citiphunzitsa kufunika kopemphela tikalibe kupeleka ndemanga. Citsanzo ca Yona citiphunzitsa kuti ngakhale titakhala na mantha aakulu, Yehova angatithandize kucita cifunilo cake. w19.01 11 ¶12
Citatu, November 4
Palibe amene anasiya nyumba kapena [banja] cifukwa ca ine, ndi cifukwa ca uthenga wabwino, amene panopa sadzapeza zoculuka kuwilikiza maulendo 100 m’nthawi ino . . . ndipo m’nthawi imene ikubwelayo, adzapeza moyo wosatha.—Maliko 10:29, 30.
Tikayamba kutsatila mfundo za coonadi cimene taphunzila, mgwilizano wathu na anzathu komanso acibululu ungasokonezeke. Cifukwa ciani? Kumbukilani kuti Yesu anapemphelela ophunzila ake kuti: “Ayeletseni ndi coonadi. Mawu anu ndiwo coonadi.” (Yoh. 17:17) Mawu akuti “ayeletseni” angatanthauzenso kuti “apatuleni.” Pamene taphunzila coonadi, timakhala ngati tapatulidwa m’dzikoli, cifukwa sitiyendelanso nzelu za anthu a m’dzikoli. Timaoneka osiyana ndi anthu ena cifukwa ca mfundo zimene timayendela. Timatsatila mfundo za m’Baibo. Sikuti timafuna kusokoneza mgwilizano. Koma nthawi zina, anzathu komanso acibululu angayambe kutisala kapena kutitsutsa cifukwa cakuti taphunzila coonadi. Izi n’zosadabwitsa, cifukwa Yesu anati: “Kunena zoona, adani a munthu adzakhala a m’banja lake leni-leni.” (Mat. 10:36) Koma iye analonjeza kuti tikagula coonadi, tidzapeza madalitso oculuka kuposa zilizonse zimene tingadzimane. w18.11 6 ¶11
Cinayi, November 5
Mipingo yonse ya anthu a mitundu ina [ikuwayamikila].—Aroma. 16:4.
Mtumwi Paulo anali kuona Akhristu anzake kukhala ofunika kwambili. Anaonetsa zimenezi m’zokamba zake. Nthawi zonse popemphela, Paulo anali kuyamika Mulungu kaamba ka iwo. Komanso, m’makalata amene anawalembela, anali kukambamo mawu owayamikila. Mwacitsanzo, pa Aroma 16: 1-15, Paulo anachula maina 27 a Akhristu anzake. Paulo anakamba kuti Purisika ndi Akula “anaika miyoyo yawo paciswe” cifukwa ca iye. Anakambanso kuti Febe “anateteza abale ambilimbili,” kuphatikizapo iyeyo. Paulo anawayamikila abale na alongo ake okondedwa cifukwa cotumikila mwakhama. (Aroma 16:1-15) Paulo anali kudziŵa kuti panali zinthu zina zimene abale na alongo sanali kucita bwino. Ngakhale n’telo, iye anakamba kwambili za makhalidwe awo abwino. N’zosakayikitsa kuti pamene kalatayo inali kuŵelengedwa mu mpingo, Akhristuwo analimbikitsidwa kwambili. Mwacionekele, izi zinacititsa kuti ubwenzi wawo na Paulo ulimbileko. Kodi imwe muli na cizolowezi coyamikila abale na alongo mu mpingo pa zabwino zimene amakamba na kucita? w19.02 16 ¶8-9
Cisanu, November 6
Sindidzasiya kukhala ndi mtima wosagawanika.—Yobu 27:5.
Kodi ife anthu opanda ungwilo sitingakwanitse kukhala na mtima wamphumphu? Iyai. N’zoona kuti timalakwitsa nthawi zambili. Koma izi sizifunika kutigwetsa mphwayi. Cifukwa ciani? Yehova sayang’ana kwambili pa zolakwa zathu. Mawu ake amati: “Inu Ya, mukanakhala kuti mumayang’anitsitsa zolakwa, ndani akanaima pamaso panu, inu Yehova?” (Sal. 130:3) Iye amadziŵa kuti ndife opanda ungwilo, komanso ocimwa, ndipo ni wokonzeka kutikhululukila na mtima wonse. (Sal. 86:5) Komanso, Yehova amadziŵa zimene tingakwanitse kucita, ndipo satiyembekezela kucita zimene sitingakwanitse. (Sal. 103:12-14) Kwa atumiki a Yehova, cinsinsi cokhalila na mtima wamphumphu ni cikondi. Tifunika kukonda Mulungu na mtima wonse, komanso kukhala wodzipeleka kwathunthu kwa iye. Tikatelo, ndiye kuti olo tiyesedwe bwanji, tidzakhalabe okhulupilika. (1 Mbiri 28:9; Mat. 22:37) Timadziŵa kuti mfundo za Yehova n’zolungama, ndipo timafuna kukondweletsa Atate wathu wakumwamba. Cikondi cathu pa Mulungu cimatisonkhezela kuika cifunilo cake patsogolo popanga zosankha. Mwa ici, ife timaonetsa kuti tili na mtima wamphumphu. w19.02 3 ¶4-5
Ciŵelu, November 7
Uteteze mtima wako.—Miy. 4:23.
Nthawi iliyonse tikaona mapindu amene amabwela cifukwa cocita zinthu zoyenela, cikhulupililo cathu cimalimbilako. (Yak. 1:2, 3) Timamvela bwino kudziŵa kuti tacita zinthu zokondweletsa Yehova monga ana ake, ndipo cifuno cathu cocita zinthu zom’kondweletsa cimakulila-kulila. (Miy. 27:11) Tikakumana na mayeselo, timaona kuti ni mpata wabwino woonetsela kuti ndife odzipeleka na mtima wonse kutumikila Atate wathu wacikondi, Yehova. (Sal. 119:113) Mwa njila imeneyi, timaonetsa kuti timakonda Yehova na mtima wathu wonse, na kuti ndife ofunitsitsa kumvela malamulo ake na kucita cifunilo cake. (1 Maf. 8:61) Ngakhale n’conco, nthawi zina tingalakwitse zinthu zina cifukwa ndife opanda ungwilo. Ngati talakwitsa, tiziganizila citsanzo ca Mfumu Hezekiya. Iye anacitapo zolakwa. Koma analapa, na kupitiliza kutumikila Yehova “ndi mtima wathunthu.” (Yes. 38:3-6; 2 Mbiri 29:1, 2; 32:25, 26) Conco, tiyenela kukaniza zoyesa-yesa za Satana zofuna kuticititsa kutengela maganizo ake. Tizipemphela kuti tikhale na “mtima womvela,” na kukhalabe okhulupilika kwa Yehova.—1 Maf. 3:9; Sal. 139:23, 24. w19.01 18-19 ¶17-18
Sondo, November 8
Tiyeni nthawi zonse tizitamanda Mulungu. Tizicita zimenezi monga nsembe imene tikupeleka kwa Mulungu, yomwe ndi cipatso ca milomo yathu. Timagwilitsa nchito milomo imeneyi polengeza dzina lake kwa anthu ena.—Aheb. 13:15.
Ngati tipeleka ndemanga pa misonkhano, na ife timapindula. (Yes. 48:17) Kodi timapindula bwanji? Coyamba, mtima wofuna kukapelekapo ndemanga pa misonkhano umatilimbikitsa kukonzekela bwino. Tikakonzekela bwino, m’pamene timamvetsetsa Mawu a Mulungu amene timaphunzila. Ndipo tikawamvetsetsa, cimakhala cosavuta kuseŵenzetsa zimene taphunzilazo. Caciŵilli, timakondwela kwambili na misonkhano ngati timatengamo mbali. Cacitatu, popeza kuti pamafunika khama kuti tipeleke ndemanga pa misonkhano, mfundo zimene tayankha sitingaziiŵale mwamsanga. Cina, timakondweletsa Yehova ngati tionetsa cikhulupililo cathu mwa kuyankhapo pa misonkhano. Timadziŵa kuti Yehova amamvetsela ndemanga zathu, ndipo amayamikila kwambili khama limene timaonetsa kuti tipelekepo ndemanga pa misonkhano. (Mal 3:16) Iye amaonetsa kuyamikila kumeneku mwa kutithandiza pamene tiyesetsa kucita zinthu zom’kondweletsa. (Mal. 3:10) Monga taonela, tili na zifukwa zomveka zopelekela ndemanga pa misonkhano. w19.01 8 ¶3; 9-10 ¶7-9
Mande, November 9
Nyansidwani ndi coipa, gwilitsitsani cabwino.—Aroma. 12:9.
Yehova amacita nase zinthu mwanzelu kwambili ise atumiki ake. Iye sanatipatse malamulo ambili-mbili. Koma moleza mtima amatiphunzitsa kuti tizicitilana zinthu mwacikondi. Iye amafuna kuti tizitsatila mfundo zake za makhalidwe abwino na kuzonda zoipa. Pa Ulaliki wa pa Phili, Mwana wake Yesu anafotokoza cimene cimapangitsa anthu kucita zoipa. (Mat. 5:27, 28) Pokhala Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, m’dziko latsopano Khristu adzapitiliza kutiphunzitsa kuona zabwino na zoipa monga mmene iye amazionela. (Aheb. 1:9) Komanso, adzatithandiza kukhala angwilo. Panthawiyo, sitidzakhalanso na zilakolako za ucimo, kapena kukumana na zoŵaŵa zobwela cifukwa ca ucimo. Ndiyeno, tidzakondwela na “ufulu waulemelelo” umene Yehova analonjeza. (Aroma 8:21) Komabe, ngakhale m’dziko latsopano, ufulu umene tidzakhala nawo, udzakhala na malile. Ufulu umakhala weni-weni ngati timauseŵenzetsa motsogoleledwa na cikondi monga mmene Mulungu amacitila.—1 Yoh. 4:7, 8. w18.12 23 ¶19-20
Ciŵili, November 10
Azimulembela kalata yothetsela ukwati . . . n’kumucotsa panyumba pake.—Deut. 24:1.
Nanga m’Cilamulo munali malangizo otani pa nkhani ya kusudzulana? Olo kuti Mulungu sanali kufuna kuti mwamuna na mkazi azisudzulana, nthawi zina anali kulola mwamuna kusudzula mkazi wake ngati “wam’peza ndi vuto linalake.” Cilamulo sicinafotokoze mwacindunji kuti “vuto” limenelo linali ciani maka-maka. Koma liyenela kuti linali vuto lalikulu ndi locititsa manyazi, osati colakwa cacing’ono ayi. (Deut. 23:14) Koma pofika m’nthawi ya Yesu, Ayuda ambili anali kusudzulana “pa cifukwa ciliconse.” (Mat. 19:3) Mwacionekele, ise sitingafune kutengela khalidwe loipa limeneli. Zimene mneneli Malaki analemba zimatithandiza kudziŵa mmene Mulungu amaonela nkhani ya kusudzulana. M’nthawi yake, amuna ambili aciisiraeli anali kusudzula akazi a pa unyamata wawo popanda zifukwa zomveka, mwina n’colinga cakuti akwatile kamtsikana kacikunja. Malaki anafotokoza mmene Mulungu anali kuonela khalidweli. Analemba kuti: “Ine [Mulungu] ndimadana ndi zakuti anthu azithetsa mabanja.” (Mal. 2:14-16) Izi n’zogwilizana na zimene Mulungu anakamba zokhudza cikwati coyamba. Iye anati: “Mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake, n’kudziphatika kwa mkazi wake, ndipo iwo adzakhala thupi limodzi.” (Gen. 2:24) Pambuyo pake, Yesu anatilimbikitsa kuona cikwati mmene Atate wake amacionela. Anati: “Cimene Mulungu wacimanga pamodzi, munthu asacilekanitse.”—Mat. 19:6. w18.12 11 ¶7-8
Citatu, November 11
Zokolola n’zoculuka, koma anchito ndi ocepa.—Mat. 9:37.
Malinga na mmene zinthu zilili mu umoyo wawo, Akhristu ena amadzipeleka kukatumikila ku madela akutali. Iwo ali na mtima monga wa mneneli Yesaya. Yehova atamufunsa kuti: “Kodi nditumiza ndani, ndipo ndani apite m’malo mwa ife?” Yesaya anayankha kuti: “Ine ndilipo! Nditumizeni.” (Yes. 6: 8) Malinga na mmene zinthu zilili mu umoyo wanu, kodi ndimwe wokonzeka kucita utumiki uliwonse m’gulu la Mulungu? Pokamba za nchito yolalikila na kupanga ophunzila, Yesu anati: “Conco pemphani Mwini zokolola kuti atumize anchito kukakolola.” (Mat. 9:38) Kodi mungadzipeleke kukatumikila kumalo osoŵa, mwina monga mpainiya? Kapena kodi mungathandizeko wina kucita zimenezo? Abale na alongo ambili amaona kuti njila yabwino kwambili yoonetsela kuti amakonda Mulungu na anansi awo, n’kukacita upainiya ku madela kapena ku magawo osoŵa. Kodi ni njila zina ziti zimene mungawonjezele nazo utumiki wanu? Dziŵani kuti tikawonjezela zocita mu utumiki wathu, timapeza cimwemwe coculuka. w18.08 27 ¶14-15
Cinayi, November 12
Moyo wanu ukhale wosakonda ndalama, koma mukhale okhutila ndi zimene muli nazo pa nthawiyo.—Aheb. 13:5.
Mabuku a Uthenga Wabwino amaonetsa bwino maganizo a Yehova pa nkhani ya zinthu zakuthupi. Mulungu anasankha Mariya na Yosefe kuti adzalele Mwana wake, olo kuti iwo sanali olemela. (Lev. 12:8; Luka 2:24) Yesu atabadwa, Mariya ‘anamugoneka modyelamo ziweto, cifukwa anasoŵa malo m’nyumba ya alendo.’ (Luka 2:7) Yehova akanafuna, sembe anapeza njila yakuti Mwana wake akabadwile m’nyumba yabwino. Koma iye anaona kuti cofunika kwambili n’cakuti Yesu akaleledwe na makolo okonda zinthu zauzimu. Nkhani imeneyi yokamba za kubadwa kwa Yesu, ingatithandize kumvetsetsa mmene Yehova amaonela zinthu zakuthupi. Makolo ena amayesetsa kuthandiza ana awo kuti adzakhale na zinthu zambili zakuthupi, ngakhale kuti kucita zimenezo kungawononge ubwenzi wa anawo na Yehova. Koma monga taonela, Yehova amaona kuti zinthu zauzimu ndizo zofunika kwambili. Kodi mumayendela maganizo a Yehova pa nkhaniyi? Nanga zocita zanu zimaonetsa kuti muli na maganizo otani? w18.11 24 ¶7-8
Cisanu, November 13
Odala ndi anthu amene Mulungu wawo ndi Yehova.—Sal. 144:15.
Popeza Mulungu ni Gwelo la cimwemwe, amafunanso kuti ise tizikhala acimwemwe. Conco watipatsa zifukwa zambili zokhalila acimwemwe (Deut. 12:7; Mlal. 3:12, 13) Koma masiku yano, n’zovuta munthu kukhala wacimwemwe. Cifukwa ciani? Pali mavuto ambili amene angatilepheletse kukhala acimwemwe. Mwacitsanzo, munthu amene tinali kum’konda angamwalile kapena kucotsedwa mu mpingo. Palinso mavuto ena monga kutha kwa cikwati kapena nchito, mikangano ya m’banja, kapena kusakambitsana bwino. Ena amakumana na mavuto monga kusekewa na anzawo ku sukulu kapena kunchito, kuzunzidwa kapena kuikidwa m’ndende cifukwa ca cikhulupililo cawo. Timakumananso na mavuto monga kufooka kwa thanzi, matenda osathelapo, komanso kuvutika maganizo. Zonsezi zingatilepheletse kukhala acimwemwe. Ngakhale zili conco, Yesu Khristu, Mfumu ‘yacimwemwe ndi yamphamvu yokhayo,’ ni wokonzeka kutitonthoza na kutithandiza kukhala acimwemwe. (1 Tim. 6:15; Mat. 11:28-30) Mu ulaliki wake wa pa phili, Yesu anachula makhalidwe osiyana-siyana amene angatithandize kukhala acimwemwe, olo pamene tikumana na mavuto aakulu m’dziko la Satanali. w18.09 17-18 ¶1-3
Ciŵelu, November 14
Musamadzicekeceke kapena kumeta nsidze zanu cifukwa ca anthu akufa.—Deut. 14:1.
Cimodzi mwa zinthu zimene zimavuta kwambili kuti munthu aleke akayamba kuphunzila coonadi, ni miyambo yosagwilizana na Malemba. (Miy. 23:23) Anthu ena siciwavuta kumvetsetsa zifukwa zimene Malemba amaletsela kucita miyambo imeneyi. Koma kuti aileke, amadodoma cifukwa coopa acibululu, anzawo a ku nchito, na mabwenzi. Zimakhala zovuta kwambili, maka-maka ngati miyambo imeneyo iphatikizapo kulemekeza acibululu amene anamwalila. Koma kuganizila citsanzo ca anthu amene anaonetsa kulimba mtima, kungatilimbikitse kuleka miyambo yosagwilizana na Malemba. Kodi anthu a ku Efeso ongotembenukila kumene ku Cikhristu, amene poyamba anali kucita zamatsenga, anacitanji kuti asiye miyambo yosagwilizana na Malemba ndi kugula coonadi? Baibo imati: “[Iwo] anasonkhanitsa mabuku awo pamodzi ndi kuwatentha pamaso pa onse. Ndipo atawonkhetsa mitengo yake, anapeza ndalama zasiliva zokwana 50,000.” (Mac. 19:19, 20) Akhristu okhulupilika amenewo anataya zambili kuti agule coonadi, ndipo anapeza madalitso osaneneka. w18.11 7 ¶15-16
Sondo, November 15
Atamaliza kucita mdulidwe pamtundu wonsewo, anthuwo anakhala m’malo awo mumsasa mpaka atacila.—Yos. 5:8.
Aisiraeli atangowoloka Yorodano, Yoswa anakumana na munthu ali na lupanga m’dzanja lake. Munthuyo anali “kalonga wa gulu lankhondo la Yehova,” amene anabwela kudzateteza anthu a Mulungu. (Yos. 5:13-15) Kupitila mwa mkulu wa angeloyo, Yehova anapatsa Yoswa malangizo omveka bwino a zimene anayenela kucita kuti awononge mzinda wa Yeriko. Poyamba, ena mwa malangizowo sanali kuoneka monga othandiza kweni-kweni. Mwacitsanzo, Yehova analamula kuti amuna onse a Isiraeli adulidwe. Izi zikanacititsa kuti anthuwo asathe kumenya nkhondo kwa masiku angapo cifukwa ca ululu. (Gen. 34:24, 25; Yos. 5:2) Mwacidziŵikile, asilikali a Aisiraeli odulidwawo anali kudela nkhawa kuti adzateteza bwanji mabanja awo ngati adani atawaukila. Koma posapita nthawi, iwo anamvela kuti amuna a mu Yeriko ali na mantha kwambili, cakuti mzindawo “unatsekedwa mwamphamvu cifukwa ca ana a Isiraeli.” (Yos. 6:1) Mwacionekele, izi zinalimbikitsa Aisiraeli kudalila kwambili malangizo a Mulungu. w18.10 23 ¶5-7
Mande, November 16
Anthu inu, mukucitilanji zimenezi? Ifenso ndife anthu okhala ndi zofooka ngati inu nomwe.—Mac. 14:15.
Kodi tingatengele bwanji citsanzo ca Paulo ca kudzicepetsa? Coyamba, sitiyenela kuyembekezela kapena kulolela kuti ena azititamanda kapena kutilemekeza kwambili cifukwa ca zinthu zimene tacita mwa mphamvu za Yehova. Aliyense wa ise angacite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi nimawaona bwanji anthu amene nimawalalikila? Kodi nimaonetsa tsankho kwa anthu ena a m’dela langa?’ Padziko lonse lapansi, Mboni za Yehova zakhala zikufufuza mosamala m’magawo awo, kuti zione ngati mukali anthu ena amene angamvetsele uthenga wabwino. Kuti acite izi, nthawi zina amafunika kuphunzila citundu kapena cikhalidwe ca anthu amene amasalidwa m’dela lawo. Akhristu amene amalalikila kwa anthu aconco afunika kupewelatu mzimu wodziona monga apamwamba. Koma ayenela kuyesetsa kuwadziŵa bwino anthuwo kuti awafike pa mtima na uthenga wa Ufumu. w18.09 5 ¶9, 11
Ciŵili, November 17
Yudasi Mgalileya. . . , anakopa anthu ndipo anamutsatila. —Mac. 5:37.
Aroma anapha Yudasi. Kuwonjezela pa kupha Yudasi na anthu ena oukila boma, Ayuda ena ambili anali kuyembekezela mwacidwi kubwela kwa Mesiya. Iwo anali kuyembekezela kuti Mesiya akadzabwela, adzabweletsa ulemelelo m’dziko lawo na kulimasula ku ulamulilo wa Aroma. (Luka 2:38; 3:15) Ambili anali kukhulupilila kuti Mesiya adzakhazikitsa ufumu wake mu Isiraeli. Ndipo zikadzakhala conco, Ayuda mamiliyoni ambili amene anabalalikila m’maiko ena adzabwelelanso m’dziko lawo. Kumbukilani kuti nthawi ina, Yohane Mbatizi anafunsa Yesu kuti: “Kodi Mesiya amene tikumuyembekezela uja ndinu kapena tiyembekezele wina?” (Mat. 11:2, 3) Mwina Yohane anafuna kudziŵa ngati kudzabwela munthu wina amene adzakwanilitsa zonse zimene Ayuda anali kuyembekezela. Nawonso ophunzila aŵili amene anakumana ndi Yesu panjila yopita ku Emau, pambuyo pakuti waukitsidwa, anaona kuti zinthu zina zokhudza Mesiya zimene anali kuyembekezela sizinakwanilitsike. (Luka 24:21) Patapita nthawi yocepa, atumwi a Yesu anam’funsa kuti: “Ambuye, kodi mubwezeletsa ufumu kwa Isiraeli pa nthawi ino?”—Mac. 1:6. w18.06 4 ¶3-4
Citatu, November 18
Munthu amene sadziŵa zinthu amakhulupilila mawu alionse, koma wocenjela amaganizila za mmene akuyendela.—Miy. 14:15.
Tifunika kukhala wosamala kwambili maka-maka ngati tamvela nkhani inayake yokhudza anthu a Yehova. Tisaiŵale kuti Satana amaneneza atumiki okhulupilika a Mulungu. (Chiv. 12:10) N’cifukwa cake Yesu anakamba kuti otsutsa ‘adzatinamizila zoipa’ za mtundu uliwonse. (Mat. 5:11) Ngati tikumbukila mfundo imeneyi, sitidzadabwa tikamvela nkhani zoipa zoneneza anthu a Yehova. Kodi mumakonda kutuma imelo kapena mameseji kwa anzanu? Ngati n’conco, ndiye kuti mukamvela nkhani inayake yocititsa cidwi imene yangofalitsidwa kumene, mwina mumalakalaka kukhala woyamba kuuzako anzanu nkhaniyo. Komabe, musanatume meseji kapena imelo, dzifunseni kuti: ‘Kodi nkhani imene nifuna kutumayi ni ya zoona? Kodi nidziŵadi zoona pa nkhaniyi?’ Ngati mulibe umboni, simuyenela kuitumiza, cifukwa mosadziŵa, mungafalitse nkhani yabodza pakati pa abale. M’malomwake, muyenela kungoifafaniza. w18.08 3 ¶3; 4 ¶6-7
Cinayi, November 19
Khalani opatsa ndipo inunso anthu adzakupatsani.—Luka 6:38.
Yesu amafuna kuti tipeze cimwemwe mwa kukhala owolowa manja. Anthu ambili amayamikila tikawapatsa mowolowa manja. N’zoona kuti si onse amene amayamikila. Koma akakhala na mtima woyamikila, nawonso amasonkhezeleka kukhala owolowa manja. Conco, khalani owolowa manja, kaya anthu aoneke kuti ayamikila kapena ayi. Simungadziŵe mmene kuwolowa manja kwanu kungakhudzile ena. Anthu owolowa manja sapatsa ena zinthu n’colinga cakuti anthuwo adzawabwezele zinazake m’tsogolo. Yesu anali kuganizila mfundo imeneyi pamene anati: “Ukakonza phwando, uziitana anthu osauka, otsimphina, olumala, ndi akhungu. Ukatelo udzakhala wodala, cifukwa alibe coti adzabweze kwa iwe.” (Luka 14:13, 14) Lemba lina limati: “Wa diso labwino [“munthu wowolowa manja”, NWT] adzadalitsidwa.” Linanso limati: “Wodala ndi munthu amene amacita zinthu moganizila munthu wonyozeka.” (Miy. 22:9; Sal. 41:1) Conco, tiyenela kukhala opatsa cifukwa cakuti kuthandiza ena kumatikondweletsa. w18.08 21-22 ¶15-16
Cisanu, November 20
Khulupilila Yehova ndi mtima wako wonse, ndipo usadalile luso lako lomvetsa zinthu. Uzim’kumbukila m’njila zako zonse, ndipo iye adzawongola njila zako. —Miy. 3:5, 6.
Kudziŵa zoona zeni-zeni na kuzipenda mosamala n’kovuta masiku ano cifukwa pali nkhani zambili zabodza komanso zosoceletsa. Vuto linanso n’lakuti ndise opanda ungwilo. Nanga n’ciani cingatithandize? Tiyenela kudziŵa mfundo za m’Baibo na kuziseŵenzetsa. Imodzi mwa mfundozo ni yakuti sitiyenela kuyankhila nkhani tisanaimvetsetse. Kucita zimenezi n’kupusa, ndipo zotulukapo zake tikhoza kucititsidwa manyazi. (Miy. 18:13) Mfundo ina ya m’Baibo ni yakuti, sitiyenela kukhulupilila mawu aliwonse amene tamvela. (Miy. 14:15) Ndipo yothela ni yakuti, olo kuti ndise aciyambakale m’coonadi ndipo timadziŵa zambili, sitiyenela kudalila luso lathu lomvetsa zinthu. Mfundo za m’Baibo zidzatiteteza ngati popanga zosankha tiyesetsa kuseŵenzetsa mfundo zolondola zimene tamvela kucokela ku magwelo odalilika. w18.08 7 ¶19
Ciŵelu, November 21
Kuli bwanji ndi Atate wa moyo wathu wauzimu. Kodi sitiyenela kuwagonjela?—Aheb. 12:9.
Pamene tinabatizika, tinaonetsa poyela kuti tsopano ndise a Yehova komanso kuti ndise ofunitsitsa kumumvela. Izi n’zimene Yesu anacita. Pamene anali kubatizika, zinali ngati kuti akuuza Yehova kuti: “Ndimakondwela ndi kucita cifunilo canu, inu Mulungu wanga.” (Sal. 40:7, 8) Kodi Yehova anamvela bwanji Yesu atabatizika? Baibo imakamba kuti: “Atabatizidwa, nthawi yomweyo Yesu anavuuka m’madzimo. Pamenepo kumwamba kunatseguka, ndipo Yohane anaona mzimu wa Mulungu ukutsika ngati nkhunda kudzamutela. Panamvekanso mawu ocokela kumwamba onena kuti: ‘Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, amene ndimakondwela naye.’” (Mat. 3:16, 17) Ngakhale kuti Yesu ni Mwana wa Mulungu, Yehova anakondwela poona kuti iye wasankha kudzipatulila kuti acite cifunilo cake. Mofananamo, Yehova amakondwela tikadzipatulila kwa iye, ndipo adzatidalitsa.—Sal. 149:4. w18.07 23 ¶4-5
Sondo, November 22
Kodi ticite kukutulutsilani madzi m’thanthweli?—Num. 20:10.
Mwa kukamba mawu akuti “ticite,” mwacionekele Mose anali kutanthauza kuti wotulutsa madzi adzakhala iye na Aroni. Zimene Mose anakamba sizinali zopeleka ulemu kwa Yehova, Gwelo leni-leni la cozizwitsaco. Mogwilizana na mfundo imeneyi, lemba la Salimo 106:32, 33 limati: “Iwo anaputa mkwiyo [wa Mulungu] pa madzi a ku Meriba, moti Mose sizinamuyendele bwino cifukwa ca anthu amenewa. Iwo anamukwiyitsa ndipo Mose anayamba kulankhula mosalingalila bwino.” (Num. 27:14) Mulimonse mmene zinakhalila, cimene tidziŵa n’cakuti zimene Mose anacita zinapangitsa kuti Yehova asapatsidwe ulemu womuyenelela. Pokamba ndi Mose na Aroni, Yehova anati: “Amuna inu munapandukila malangizo anga.” (Num. 20:24) Cimeneci cinalidi colakwa cacikulu! M’mbuyomo, Yehova anaweluza mtundu wonse wa Isiraeli kuti sudzaloŵa m’dziko la Kanani cifukwa ca kupanduka kwawo. (Num. 14:26-30, 34) Conco, zimene Yehova anacita poweluza Mose kuti sadzaloŵa m’Dziko Lolonjezedwa cinali cilungamo. Mose anaonetsa mzimu wopanduka. w18.07 14 ¶9, 12; 15 ¶13
Mande, November 23
Ndi bwino kusadya nyama kapena kusamwa vinyo kapena kusacita kalikonse kamene kamakhumudwitsa m’bale wako.—Aroma 14:21.
Kodi mungapewe kucita zinthu zina n’colinga cakuti musakhumudwitse cikumbumtima ca ena, olo kuti muli na ufulu wocita zinthuzo? Mosakayikila, mungatelo. Kumbukilani kuti ena mwa abale athu asanaphunzile coonadi, anali na vuto la kumwa kwambili moŵa. Koma lomba ni otsimikiza mtima kupewelatu khalidwe limeneli. Mwacionekele, palibe aliyense wa ise amene angafune kucita zinthu zimene zingasonkhezele m’bale wathu kuyambilanso khalidwe limene lingamuwononge mwauzimu. (1 Akor. 6:9, 10) Conco, si cikondi kukakamiza m’bale kumwa moŵa ngati iye wakana. Pamene Timoteyo anali na zaka pafupi-fupi 20 kapena kupitililako pang’ono, analolela kudulidwa pofuna kuti asakakhumudwitse Ayuda amene anali kukawalalikila. Iye anali na maganizo monga a mtumwi Paulo. (Mac. 16:3; 1 Akor. 9:19-23) Mofanana ndi Timoteyo, kodi ndimwe wokonzeka kudzimana zinthu zina pofuna kuthandiza ena? w18.06 18-19 ¶12-13
Ciŵili, November 24
Ndidzapatsa mitundu ya anthu cilankhulo coyela.—Zef. 3:9.
Yehova amakoka anthu oona mtima kuti azim’lambila monga banja lake lauzimu. (Yoh. 6:44) Ngati mwakumana na munthu amene si Mboni kwa nthawi yoyamba, pamakhala zambili zimene simudziŵa zokhudza munthuyo. Mwina mungadziŵeko cabe maonekedwe ake kapena dzina lake ngati wakuuzani. Koma bwanji ngati mwakumana na mtumiki wa Yehova? Olo atakhala kuti ni wa cikhalidwe cina, dziko lina, kapena mtundu wina, pamakhala zambili zimene mumadziŵa zokhudza iye, komanso zimene iye amadziŵa zokhudza imwe. Mwacitsanzo, mwamsanga mumazindikila kuti nonse mumakamba “cilankhulo coyela,” cimene ni coonadi. Conco, mumadziŵa kuti zimene mumakhulupilila n’zofanana, kaya ni zokhudza Mulungu, mfundo za makhalidwe abwino, ciyembekezo ca kutsogolo, na zina zambili. Kudziŵa zimenezi n’kofunika kwambili cifukwa n’kumene kumathandiza kuti muyambe kudalilana, ndipo kumayala maziko a ubwenzi wabwino komanso wolimba. w18.12 21 ¶9-10
Citatu, November 25
Mukapanda kudulidwa . . . , simungapulumuke.—Mac. 15:1.
Motsogoleledwa na Khristu, bungwe lolamulila linagamula kuti kunali kosafunikila kuti Akhristu a mitundu ina azicita mdulidwe. (Mac. 15:19, 20) Koma patapita zaka pambuyo pa cigamulo cimeneci, Akhristu ambili aciyuda anapitiliza kucita mdulidwe ana awo. Mwina tingadzifunse kuti, ‘N’cifukwa ciani Yesu analola kuti nkhani ya mdulidwe itenge nthawi yaitali conco osathetsedwa, pamene imfa yake inali itathetsa kale Cilamulo ca Mose?’ (Akol. 2:13, 14) Kwa ena, zimatenga nthawi kuti ayambe kucita zinthu mogwilizana na kamvedwe katsopano ka coonadi. Akhristu aciyuda anafunika nthawi yokwanila kuti asinthe kaonedwe kawo ka zinthu. (Yoh. 16:12) Kwa Akhristu ena, cinakhala covuta kuvomeleza kuti mdulidwe sunalinso cizindikilo cakuti ali pa ubwenzi wapadela na Mulungu. (Gen. 17:9-12) Komanso, Akhristu ena aciyuda anali kucita mdulidwe cifukwa coopa kuzunzidwa na Ayuda anzawo, amene anali kucita mdulidwe. (Agal. 6:12) Olo zinali conco, m’kupita kwa nthawi, Khristu anapeleka malangizo owonjezeleka pa nkhaniyi, kupitila m’makalata ouzilidwa amene Paulo analemba.—Aroma 2:28, 29; Agal. 3:23-25. w18.10 24-25 ¶10-12
Cinayi, November 26
Kayafa . . . analangiza Ayuda uja kuti kunali kopindulitsa kwa iwo kuti munthu mmodzi afele anthu onse.—Yoh. 18:14.
Kayafa anatuma asilikali kuti akagwile Yesu usiku. Yesu anali kudziŵa za ciwembu cimeneci. Conco, pamene Yesu anali kudya cakudya pamodzi na atumwi ake pa tsiku lakuti iye adzaphedwa maŵa, anawauza kuti atenge malupanga aŵili. Iye anali kufuna kuwaphunzitsa mfundo inayake yofunika kwambili. (Luka 22:36-38) Usiku wa tsiku limenelo, Petulo anatenga lupanga na kutema nalo mmodzi wa anthu amene anabwela kudzagwila Yesu. Mwacionekele, iye anakwiya poona kupanda cilungamo kumene anthuwo anaonetsa pobwela kudzagwila Yesu usiku. (Yoh. 18:10) Koma Yesu anauza Petulo kuti: “Bwezela lupanga lako m’cimake, pakuti onse ogwila lupanga adzafa ndi lupanga.” (Mat. 26:52, 53) Mfundo yamphamvu imeneyi ni yogwilizana ndi pemphelo limene iye anapeleka madzulo a tsikulo, lakuti ophunzila ake sayenela kukhala mbali ya dziko. (Yoh. 17:16) Iwo anafunika kuyembekezela Mulungu kuti ndiye adzathetsa zinthu zopanda cilungamo. Conco, ise Akhristu timakhalabe ogwilizana ndi amtendele. Ndipo pamene Yehova aona kusagwilizana kwa anthu padzikoli, amanyadila kuona mgwilizano umene uli pakati pa anthu ake.—Zef. 3:17. w18.06 6-7 ¶13-14, 16
Cisanu, November 27
Cinjokaco cinakwiya ndi mkazi uja, moti cinapita kukacita nkhondo ndi otsala a mbewu yake.—Chiv. 12:17.
Kuwonjezela pa kuseŵenzetsa nyambo, Satana amatiyofya kuti ticite zinthu zosakhulupilika pamaso pa Yehova. Mwacitsanzo, angasonkhezele maboma kuti aletse nchito yathu yolalikila. Kapena angasonkhezele anzathu kunchito kapena kusukulu kuti azitiseka cifukwa cotsatila makhalidwe abwino a m’Baibo. (1 Pet. 4:4) Angasonkhezelenso abululu athu amene amatikonda kuti azitiletsa kupita ku misonkhano. (Mat. 10:36) N’ciani cingatithandize kupilila? Coyamba, sitiyenela kudabwa na mavuto aconco, cifukwa Satana ali pa nkhondo na ise. (Chiv. 2:10) Cina, tifunika kukumbukila nkhani yaikulu imene imalengetsa kuti tizikumana na mavuto amenewa. Paja Satana amakamba kuti timatumikila Yehova kokha ngati zinthu zili bwino. Amakambanso kuti ngati tingakumane na mavuto, tingamusiye Mulungu. (Yobu 1:9-11; 2:4, 5) Koposa zonse, tifunika kudalila Yehova kuti atipatse mphamvu kuti tipilile. Kumbukilani kuti iye analonjeza kuti sadzatisiya.—Aheb. 13:5. w18.05 26 ¶14
Ciŵelu, November 28
Cifukwa sukudziŵa pamene padzacite bwino.—Mlal. 11:6.
Ngakhale zioneke kuti uthenga wa Ufumu umene timalalikila suwafika pa mtima anthu, sitiyenela kudelela mphamvu ya uthenga umenewu. N’zoona kuti anthu ambili samvetsela uthenga wathu. Ngakhale n’conco, iwo amaona zimene timacita. Amaona kavalidwe kathu kabwino, khalidwe laulemu, na mtima wathu waubwenzi. M’kupita kwa nthawi, khalidwe lathu labwino lingathandize anthu ena kusintha maganizo awo olakwika ponena za Mboni za Yehova. M’bale Sergio na mlongo Olinda, amene ni apainiya anati: “Kwa kanthawi ndithu, sitinali kupita pa malo athu ocitila ulaliki wa poyela cifukwa codwala. Tsiku lina titapitanso pa malowo, munthu wina wopita na njila anatifunsa kuti, ‘N’cifukwa ninji simunali kuoneka? Tinakusowani.’” Sitiyenela kulola ‘dzanja lathu kupuma’ pa nchito yofesa mbewu za Ufumu. Tikatelo, tidzakhalabe na mwayi wamtengo wapatali wocitila “umboni ku mitundu yonse.” (Mat. 24:14) Koposa zonse, tidzakhala na cimwemwe coculuka, cimene cimabwela cifukwa codziŵa kuti Yehova amatikonda, popeza iye amakonda onse amene ‘amabala zipatso mwa kupilila!’—Luka 8:15. w18.05 16 ¶16-18
Sondo, November 29
Atamandike Mulungu . . . amene amatitonthoza . . . m’masautso athu onse.—2 Akor. 1:3, 4.
Kungocokela pamene anthu anacimwa na kukhala opanda ungwilo, Yehova waonetsa kuti ni Mulungu amene amapeleka cilimbikitso. Adamu na Hava atangopanduka m’munda wa Edeni, Mulungu anapeleka ulosi wolimbikitsa umene unapatsa ciyembekezo mbadwa za Adamu zam’tsogolo. Ulosi wa pa Genesis 3:15, unapatsa anthu ciyembekezo cakuti m’tsogolo “njoka yakale ija,” Satana Mdyelekezi, adzawonongedwa pamodzi na nchito zake zonse zoipa. (Chiv. 12:9; 1 Yoh. 3:8) Mtumiki wa Yehova Nowa anali kukhala m’dziko la anthu osaopa Mulungu, ndipo iye yekha na banja lake na amene anali kulambila Yehova. Anthu ambili pa nthawiyo anali a ciwawa ndi a ciwelewele. Izi zikanacititsa kuti iye afooke. (Gen. 6:4, 5, 9 11; Yuda 6) Yehova anauza Nowa kuti adzawononga dziko loipa la pa nthawiyo, ndipo anamuuza zimene anayenela kucita kuti apulumutse banja lake. (Gen. 6:13-18) Kwa Nowa, Yehova anaonetsadi kuti ni Mulungu wa cilimbikitso. w18.04 15 ¶1-2
Mande, November 30
Pitilizani kutonthozana ndi kulimbikitsana monga mmene mukucitila.—1 Ates. 5:11.
N’kulakwa kuganiza kuti sitingakwanitse kulimbikitsa ena cifukwa cakuti ndise osamasuka kweni-kweni na ŵanthu. Kulimbikitsa ena sikulila zambili. Mwina mungangomwetulila popatsa moni munthu. Ngati iye sakumwetulila, ndiye kuti mwina pali cinacake cimene cikumuvutitsa maganizo, ndipo kungomumvetsela pamene akamba nkhawa zake kungamulimbikitse. (Yak. 1:19) Tonse tingakwanitse kulimbikitsa m’bale kapena mlongo wathu amene afunikila citonthozo. Mfumu Solomo inalemba kuti: “Mawu onenedwa pa nthawi yoyenela ndi abwino kwambili. Maso owala amapangitsa mtima kusangalala. Uthenga wabwino umanenepetsa mafupa.” (Miy. 15:23, 30) Paulo anaonetsa kuti ngakhale kuimba nyimbo za Ufumu capamodzi kungakhale kolimbikitsa. (Akol. 3:16; Mac. 16:25) Pamene tsiku la Yehova “likuyandikila,” kulimbikitsana kudzakhala kofunika ngako.—Aheb. 10:25. w18.04 23 ¶16; 24 ¶18-19