LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • es20 masa. 118-128
  • December

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • December
  • Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2020
  • Tumitu
  • Ciŵili, December 1
  • Citatu, December 2
  • Cinayi, December 3
  • Cisanu, December 4
  • Ciŵelu, December 5
  • Sondo, December 6
  • Mande, December 7
  • Ciŵili, December 8
  • Citatu, December 9
  • Cinayi, December 10
  • Cisanu, December 11
  • Ciŵelu, December 12
  • Sondo, December 13
  • Mande, December 14
  • Ciŵili, December 15
  • Citatu, December 16
  • Cinayi, December 17
  • Cisanu, December 18
  • Ciŵelu, December 19
  • Sondo, December 20
  • Mande, December 21
  • Ciŵili, December 22
  • Citatu, December 23
  • Cinayi, December 24
  • Cisanu, December 25
  • Ciŵelu, December 26
  • Sondo, December 27
  • Mande, December 28
  • Ciŵili, December 29
  • Citatu, December 30
  • Cinayi, December 31
Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2020
es20 masa. 118-128

December

Ciŵili, December 1

Anawamvela cifundo. —Maliko 6:34.

Mbali imodzi yocititsa cidwi kwambili ya umunthu wa Yesu ni yakuti, iye amamvetsa mavuto amene ife anthu opanda ungwilo timakumana nawo. Pamene iye anali padziko lapansi, anali ‘kusangalala ndi anthu amene anali kusangalala,’ komanso ‘kulila ndi anthu amene anali kulila.’ (Aroma 12:15) Mwacitsanzo, tsiku lina Yesu anatumiza ophunzila ake 70 kuti akalalikile, ndipo ulaliki unayenda bwino. Atabwelako ali osangalala, nayenso Yesu “anakondwela kwambili mwa mzimu woyela.” (Luka 10:17-21) Koma panthawi ina, Yesu ataona mmene imfa ya Lazaro inakhudzila acibale na mabwenzi ake, “anadzuma povutika mumtima ndi kumva cisoni.” (Yoh. 11:33) N’ciani cinathandiza Yesu, munthu wangwilo, kuti azimvelela cifundo kwambili anthu opanda ungwilo? Cacikulu cimene cinam’thandiza n’cakuti anali kukonda anthu. ‘Zinthu zimene zinali kumusangalatsa, zinali zokhudzana ndi ana a anthu.’ (Miy. 8:31) Cikondi cake pa anthu, cinam’sonkhezela kudziŵa bwino mmene anthuwo amaganizila. Mtumwi Yohane anati: “[Yesu] anali kudziwa zimene zili m’mitima ya anthu.”—Yoh. 2:25. w19.03 20 ¶1-2

Citatu, December 2

Tatambasulani dzanja lanu ndi kukhudza zonse zimene ali nazo, ndipo muona, akutukwanani m’maso muli gwa!—Yobu 1:11.

Satana anawononga cuma conse ca Yobu, anapha anchito ake, na kumuwonongela mbili yake yabwino. Anamuphelanso ana ake onse 10. Kenako, anamugwetsela matenda oopsa a zilonda, zimene zinakuta thupi lake lonse, kuyambila ku mutu mpaka ku phazi. Cifukwa ca cisoni komanso kuthedwa nzelu, mkazi wake anamuuza kuti angotukwana Mulungu kuti afe. Yobu anafika polaka-laka kufa cabe, koma sanaleke kukhala na mtima wamphumphu. Ndiyeno, Satana anaseŵenzetsa njila ina. Anagwilitsila nchito amuna atatu, amene anali anzake a Yobu. Amuna amenewo anapita kukaona Yobu, ndipo anakhala kumeneko kwa masiku angapo. Koma sanam’tonthoze. M’malomwake, anali kungomunena na kum’dzudzula mwakhanza. Anali kukamba kuti Mulungu ndiye anamubweletsela mavuto, komanso kuti analibe nazo kanthu zakuti iye ali na mtima wamphumphu. Anafika pokamba mawu oonetsa kuti Yobu anali munthu woipa, ndipo anali kulandila malipilo a zoipa zake.—Yobu 1:13-22; 2:7-11; 15:4, 5; 22:3-6; 25:4-6. w19.02 4-5 ¶7-8

Cinayi, December 3

Ciyambi ca nzelu ndico kuopa Yehova.—Sal. 111:10.

Mantha ena amakhala oyenelela. Mwacitsanzo, tifunika kukhala na mantha oyenelela oopa kukhumudwitsa Yehova. Adamu na Hava akanakhala na mantha aconco, sembe sanam’pandukile Yehova. Koma anam’pandukila. Atam’pandukila, maso awo anatseguka, kutanthauza kuti anazindikila kuti ni ocimwa. Anazindikilanso kuti adzapatsila ana awo ucimo na imfa. Ataona kapena kuti kuzindikila kuti ni ocimwa, anacita manyazi na umalisece wawo, cakuti anadzipangila zovala zamasamba. (Gen. 3:7, 21) Kukhala na mantha oyenelela oopa kukhumudwitsa Yehova n’kofunika. Koma bwanji ponena za imfa. Kodi tiyenela kuiopa kwambili? Iyai, cifukwa Yehova anakonza njila yotithandiza kuti tikapeze moyo wosatha. Ndipo ngati tacimwa, koma n’kulapa mocokela pansi pamtima, iye amatikhululukila. Yehova amatikhululukila cifukwa timakhulupilila nsembe ya dipo la Mwana wake. Njila imodzi yaikulu imene timaonetsela kuti tili na cikhulupililo ni mwa kudzipatulila kwa Mulungu na kubatizika.—1 Pet. 3:21. w19.03 5-6 ¶12-13

Cisanu, December 4

Sipanatsale ndi mmodzi yemwe kupatulapo Kalebe mwana wa Yefune, ndi Yoswa mwana wa Nuni.—Num. 26:65.

Aisiraeli anali na zifukwa zambili zoyamikilila Yehova. Mwacitsanzo, iye anawamasula ku ukapolo ku Iguputo pambuyo pogwetsela dzikolo milili 10. Kenako, Mulungu anawapulumutsa mwa kuwononga asilikali onse a Iguputo pa Nyanja Yofiila. Aisiraeli anam’yamikila ngako Yehova, moti anaimba nyimbo yacipambano yom’tamanda. Koma kodi iwo anakhalabe na mtima woyamikila? Pamene Aisiraeli anakumana na mavuto ena, anaiŵala zabwino zonse zimene Yehova anawacitila. Ndipo anayamba kucita zinthu zoonetsa kusayamikila. (Sal. 106:7) Zinthu zotani? Baibo imati: “Khamu lonse la ana a Isiraeli linayamba kung’ung’udzila Mose ndi Aroni.” M’ceni-ceni, iwo anali kung’ung’udza motsutsana na Yehova. (Eks. 16:2, 8) Yehova sanakondwele na mtima wosayamikila umene anthu ake anaonetsa. Conco, anakambilatu kuti m’badwo wonse wa Aisiraeli udzafela m’cipululu, kusiyapo cabe Yoswa na Kalebe.—Num. 14:22-24. w19.02 16-17 ¶12-13

Ciŵelu, December 5

Ndine wofatsa ndi wodzicepetsa.—Mat. 11:29.

Yesu sanadzifunile yekha ulemu mwa kuyambitsa mwambo wapamwamba wokumbukila imfa yake. M’malomwake, anauza ophunzila ake kuti azim’kumbukila kamodzi pa caka mwa kucita mwambo wa cikumbutso wosalila zambili. (Yoh. 13:15; 1 Akor. 11:23-25) Ndithudi, Yesu anaonetsa kuti ni wodzicepetsa mwa kuyambitsa mwambo wosalila zambili koma woyenelela. N’zokondweletsa kudziŵa kuti kudzicepetsa, ni limodzi mwa makhalidwe aakulu a Mfumu yathu yakumwamba (Afil. 2:5-8) Kodi tingatengele bwanji khalidwe la Yesu la kudzicepetsa? Tingacite izi mwa kuika zofuna za ena patsogolo pa zofuna zathu. (Afil. 2:3, 4) Ganizilaninso zimene zinacitika madzulo pa tsiku lothela la moyo wa Yesu pa dziko lapansi. Yesu anali kudziŵa kuti watsala pang’ono kufa imfa yoŵaŵa. Koma anali kudela nkhawa kwambili atumwi ake okhulupilika, poganizila za cisoni cimene adzakhala naco cifukwa ca imfa yake. Conco, madzulo amenewo, iye anathela nthawi yoculuka kulangiza ophunzila ake na kuwalimbikitsa. (Yoh. 14:25-31) Yesu anaonetsa kudzicepetsa mwa kuika zofuna za ena patsogolo pa zofuna zake. Ndithudi, iye anatisiila citsanzo cabwino kwambili cimene tiyenela kutengela! w19.01 21 ¶5-6

Sondo, December 6

Inu Yehova, conde kondwelani ndi nsembe zaufulu za pakamwa panga.—Sal. 119:108.

Kodi mumakhuta befu cifukwa ca mantha nthawi iliyonse mukafuna kupeleka ndemanga pa misonkhano? Ngati n’conco, dziŵani kuti sindimwe mwekha. Ambili a ife timakhalako na mantha popeleka ndemanga pa misonkhano. Mantha amenewa angakhale cizindikilo cakuti muli na khalidwe labwino. Angaonetse kuti ndimwe wodzicepetsa, komanso kuti mumaona ena kukhala okuposani. Ndipo Yehova amakonda anthu odzicepetsa. (Sal. 138:6; Afil. 2:3) Koma Yehova amafunanso kuti muzimutamanda, na kulimbikitsa abale na alongo pa misonkhano. (1 Ates. 5:11) Iye amakukondani, ndipo adzakuthandizani kukhala wolimba mtima kuti mukwanitse kupeleka ndemanga. Ganizilani mfundo za m’Malemba zotsatilazi. Baibo imakamba kuti tonse timalakwitsa pa zokamba zathu. (Yak. 3:2) Cinanso, Yehova, kuphatikizapo Akhristu anzathu sayembekezela kuti tizicita zinthu mwangwilo. (Sal. 103:12-14) Iwo ni abale na alongo athu, ndipo amatikonda. (Maliko 10:29, 30; Yoh. 13:35) Amadziŵa kuti nthawi zina timalephela kupeleka ndemanga zathu ndendende mmene tinakonzekelela. w19.01 8 ¶3; 10-11 ¶10-11

Mande, December 7

Kumbukila Mlengi wako Wamkulu masiku a unyamata wako. —Mlal. 12:1.

Kucita zimenezi n’kotheka, olo kuti nthawi zina kumakhala kovuta. Yehova afuna kuti musangalale na umoyo wopambana komanso wokhutilitsa. Ndipo mwa thandizo la Mulungu, mungakhale na umoyo wacimwemwe, osati cabe pamene muli wacicepele, koma mu umoyo wanu wonse. Kuti tidziŵe mmene tingacitile zimenezi, tiyeni tikambilane zimene zinathandiza Aisiraeli kulanda Dziko Lolonjezedwa. Aisiraeli atayandikila Dziko Lolonjezedwa, Mulungu sanawalamule kuti ayambe kuphunzila maluso omenyela nkhondo. (Deut. 28:1, 2) M’malomwake, anangowalangiza kuti amvele malamulo ake na kum’dalila. (Yos. 1:7-9) M’kaonedwe ka umunthu, malangizo amenewa angaoneke ngati osathandiza. Koma anali malangizo abwino koposa, cakuti Yehova anathandiza anthu ake kugonjetsa Akanani. (Yos. 24:11-13) Izi zionetsa kuti kumvela Mulungu kumafuna cikhulupililo. Ndipo munthu akakhala na cikhulupililo, nthawi zonse zinthu zimamuyendela bwino mu umoyo. Ni mmene zinalili kalelo, ndipo masiku anonso zili conco. w18.12 25 ¶3-4

Ciŵili, December 8

Ambuye, tingapitenso kwa ndani? Inu ndi amene muli ndi mawu amoyo wosatha.—Yoh. 6:68.

Ena akhumudwa cifukwa ca kusintha kwa kamvedwe ka lemba linalake. Komanso, ena ayamba kugwilizana ndi ampatuko kapena anthu otsutsa amene amapotoza ziphunzitso zathu. Zotulukapo zake, iwo ayamba ‘kucoka’ kwa Yehova, ndipo aleka kugwilizana na mpingo wacikhristu. (Aheb. 3:12-14) Ndithudi, cikanakhala bwino anthu amenewo akanasungabe cikhulupililo cawo na kupitiliza kudalila Yesu, monga mmene mtumwi Petulo anacitila. Akhristu ena anasiya coonadi mwapang’ono-ng’ono, mwina ngakhale mosazindikila. Anthu amene amasiya coonadi pang’ono-pang’ono ali monga boti imene imafendela yokha pang’ono-pang’ono kucoka pa doko. Baibo imakamba kuti iwo ‘amatengeka pang’ono-pang’ono’ n’kusiya cikhulupililo. (Aheb. 2:1) Mosiyana na munthu amene amacoka m’coonadi mwadala, munthu amene amatengeka pang’ono-pang’ono, amasiya coonadi mosazindikila. Ngakhale n’conco, munthu wotelo amasokoneza ubwenzi wake na Yehova, ndipo m’kupita kwa nthawi ubwenziwo ungatheletu. w18.11 9 ¶5-6

Citatu, December 9

Anthu ako adzadzipeleka mofunitsitsa.—Sal. 110:3.

Kodi mumafuna kulandila maphunzilo owonjezeleka kuti mukwanitse kutumikila Mulungu mokwanila? Ngati n’conco, mungacite bwino kufunsila Sukulu ya Alengezi a Ufumu. Sukulu imeneyi imaphunzitsa amuna na akazi auzimu amene ali mu utumiki wa nthawi zonse, kuti akathandize kupititsa patsogolo zinthu za Ufumu m’magawo osiyana-siyana. Akhristu amene amafunsila sukuluyi ayenela kukhala okonzeka kucita utumiki uliwonse umene angapatsidwe akatsiliza maphunzilo awo. Kodi mungakonde kuloŵako sukuluyi kuti mukhale na mwayi wowonjezela zocita mu utumiki wanu? (1 Akor. 9:23) Pokhala anthu a Yehova, timayesetsa kukhala oolowa manja, okoma mtima, abwino, komanso acikondi kwa anansi athu. Timathandiza anzathu tsiku lililonse. Kucita zimenezi kumatibweletsela cimwemwe na mtendele. (Agal. 5:22, 23) Mulimonse mmene zinthu zilili mu umoyo wanu, mungathe kupeza cimwemwe mwa kutengela khalidwe la Yehova la kuolowa manja, komanso mwa kukhala mmodzi wa anchito anzake okondedwa.—Miy. 3:9, 10. w18.08 27 ¶16-18

Cinayi, December 10

Cimene Mulungu wacimanga pamodzi, munthu asacilekanitse.—Mat. 19:6.

Mwina tingafunse kuti: ‘Kodi pali maziko alionse a cisudzulo amene amapatsa Mkhristu ufulu wokwatilanso?’ Yesu anafotokoza maganizo ake pa nkhaniyi. Anati: “Aliyense wosiya mkazi wake ndi kukwatila wina, wacita cigololo molakwila mkaziyo. Ndipo ngati mkazi wasiya mwamuna wake, ndiyeno n’kukwatiwa ndi wina, wacita cigololo.” (Maliko 10:11, 12; Luka 16:18) Conco, n’zoonekelatu kuti Yesu anali kulemekeza cikwati, ndipo anali kufuna kuti enanso azicilemekeza. Malinga n’zimene Yesu anakamba, ngati Mkhristu wasudzula mwamuna kapena mkazi wake wosalakwa n’kukakwatila wina, ndiye kuti wacita cigololo. Zili conco cifukwa kusudzulana pa zifukwa zina, kupatulapo dama, sikuthetsa cikwati pa maso pa Mulungu. Iye amaonabe aŵiliwo kukhala “thupi limodzi.” Komanso Yesu anakamba kuti, ngati mwamuna wasudzula mkazi wake wosalakwa, amaika mkaziyo pa mayeselo ocita cigololo. Motani? M’masiku amenewo, mkazi akasudzulidwa anali kukakamizika kukwatiwanso kuti azipeza zofunikila mu umoyo. Cikwati cotelo n’cigololo. w18.12 11 ¶8-9

Cisanu, December 11

Ine ndidzaimabe pamalo a mlonda.—Hab. 2:1.

Zimene Habakuku anakambilana na Yehova zinam’khazika mtima pansi. Ndipo anatsimikiza mtima kupitiliza kuyembekezela Yehova. Patapita nthawi, Habakuku anakambanso mawu ena oonetsa kuti anatsimikiza mtima kuyembekezela pa Mulungu. Anati: “Ndidzayembekezela mofatsa tsiku la nsautso.” (Hab. 3:16) Habakuku anatsimikiza mtima kuyembekezela Yehova. Kodi ise tiphunzilapo ciani? Coyamba, olo tikumane na mavuto abwanji, tisaleke kupemphela kwa Yehova. Caciŵili, tizimvela zimene Yehova amatiphunzitsa kupitila m’Mawu ake komanso m’gulu lake. Cacitatu, tiziyembekezela Yehova moleza mtima, tili na cikhulupililo cakuti adzathetsa mavuto athu pa nthawi yake yoyenela. Ngati tipitiliza kupemphela kwa Yehova mocokela pansi pa mtima, kumvetsela kwa iye, na kumuyembekezela moleza mtima monga anacitila Habakuku, tidzakhala na mtendele wa mu mtima. Mtendele umenewo udzatithandiza kupilila mavuto. Cinanso, ciyembekezo cimatithandiza kukhala woleza mtima kwambili. Ndipo kuleza mtima kumatithandiza kukhalabe acimwemwe ngakhale tikumane na mavuto ambili. Ciyembekezo cimatithandizanso kukhala na cikhulupililo cakuti Atate wathu wakumwamba sadzalephela kucitapo kanthu.—Aroma 12:12. w18.11 15-16 ¶11-12

Ciŵelu, December 12

Akazi azidzikongoletsa ndi zovala zoyenela, povala mwaulemu ndi mwanzelu.—1 Tim. 2:9.

Kodi Mulungu amaiona bwanji nkhani yokhumudwitsa ena? Yesu anati: “Aliyense wokhumudwitsa mmodzi wa tiana tokhulupililati, zingakhale bwino kwambili kuti amumangilile cimwala camphelo m’khosi mwake, ngati cimene bulu amayendetsa, ndi kumuponya m’nyanja.” (Maliko 9:42) Mawu amenewa aonetsa kuti kukhumudwitsa ena ni nkhani yaikulu kwambili. Popeza kuti Yesu anatengela ndendende makhalidwe a Atate wake, ndiye kuti Yehova nayenso amaipidwa kwambili ngati munthu amacita mwadala zinthu zimene zingakhumudwitse mmodzi wa otsatila a Yesu. (Yoh. 14:9) Kodi timaona nkhaniyi mmene Yehova na Yesu amaionela? Kodi mumayendela maganizo a Yehova pa nkhaniyi? Nanga kodi zocita zanu zimaonetsadi kuti mumayendela maganizo ake? Mwacitsanzo, tinene kuti mwakopeka na sitayelo inayake ya kavalidwe na kudzikongoletsa, imene ingakhumudwitse ena mu mpingo kapena kudzutsa cilakolako coipa mu mtima mwawo. Kodi mudzapewa masitayelo otelo cifukwa coganizila Akhristu ena? w18.11 25 ¶9-10

Sondo, December 13

Pamenepo Satana anamuyankha Yehova kuti: “Kodi mukuganiza kuti Yobu amangoopa Mulungu pacabe? . . . tatambasulani dzanja lanu ndi kukhudza zonse zimene ali nazo, ndipo muona, akutukwanani m’maso muli gwa!”—Yobu 1:9, 11.

N’cifukwa ciani kukhala na mtima wamphumphu n’kofunika kwambili kwa aliyense wa ife? Cifukwa Satana anatsutsa ulamulilo wa Yehova, komanso aliyense wa ife. Mngelo wopanduka ameneyu anaipitsa dzina la Mulungu mwa kukamba mawu oonetsa kuti Mulungu ni Wolamulila woipa, wodzikonda, komanso wacinyengo. N’zomvetsa cisoni kuti Adamu na Hava anapandukila Yehova, na kukhala ku mbali ya Satana. (Gen. 3:1-6) Umoyo wa mu Edeni unawapatsa mwayi waukulu wolimbitsa cikondi cawo pa Yehova. Koma pamene Satana anawayesa, cikondi cawo pa Mulungu sicinali cathunthu. Cinali copeleŵela. Pambuyo pake, panabukanso funso lina lakuti: Kodi n’zotheka munthu kukhalabe wokhulupilika kwa Yehova Mulungu cifukwa com’konda? M’mawu ena tingati, kodi anthu angakwanitse kukhala na mtima wamphumphu? Funso limeneli linabuka m’masiku a Yobu. (Yobu 1:8-11) Mofanana ndi ife, Yobu anali wopanda ungwilo, ndipo nthawi zina anali kulakwa. Ngakhale n’conco, Yehova anam’konda Yobu cifukwa ca mtima wake wamphumphu. w19.02 3-4 ¶6-7

Mande, December 14

Anapita . . . n’kukagulitsa zinthu zonse zimene anali nazo ndi kukagula ngaleyo.—Mat. 13:46.

Pofuna kuonetsa kuti coonadi ca Ufumu wa Mulungu n’camtengo wapatali kwa anthu amene acipeza, Yesu anakamba fanizo la wamalonda woyendayenda amene anali kusakila ngale zabwino. Iye anapeza ngale imodzi imene inali yamtengo wapatali kwambili kwa iye cakuti ‘mwamsanga’ anapita kukagulitsa zinthu zake zonse kuti akagule ngaleyo. (Mat. 13:45, 46) Mofananamo, coonadi conena za Ufumu wa Mulungu, komanso mfundo zonse za coonadi zimene tinaphunzila m’Baibo, n’zamtengo wapatali kwambili cakuti tinatailapo zambili kuti ticipeze. Tikamaona coonadi kukhala camtengo wapatali, sitidzayesa n’komwe ‘kucigulitsa’. (Miy. 23:23) Koma n’zacisoni kuti atumiki ena a Mulungu analeka kuona coonadi kukhala camtengo wapatali, ndipo anafika ngakhale pocigulitsa. Tisalole zaconco kuticitikila! Tingaonetse kuti timakonda kwambili coonadi na kuti sitingayese kucigulitsa, mwa kumvela malangizo a m’Baibo akuti ‘tipitilizebe kuyenda m’coonadi.’ (3 Yoh. 2-4) Kuyenda m’coonadi kumaphatikizapo kucikonda, kapena kuti kucita zinthu mogwilizana na coonadi, komanso kuciika patsogolo mu umoyo wathu. w18.11 9 ¶3

Ciŵili, December 15

Mwa cikhulupililo, makoma a Yeriko anagwa, atawazungulila masiku 7.—Aheb. 11:30.

Aisiraeli analamulidwa kuti asauthile nkhondo mzinda wa Yeriko, koma kuti auzungulile kamodzi pa tsiku kwa masiku 6, ndiponso kuti pa tsiku la 7, akauzungulile maulendo 7. N’kutheka kuti ena mwa asilikali a Isiraeli, mu mtima mwawo anali kukamba kuti, ‘Tikungotaya nthawi cabe na kuwononga mphamvu!’ Koma M’tsogoleli wosaoneka wa Aisiraeli anali kudziŵa zimene anali kucita. Mapulani a mtsogoleliyu anathandiza kuti cikhulupililo ca Aisiraeli cilimbe kwambili. Komanso anathandiza kuti Aisiraeli asagwebane mwacindunji na asilikali amphamvu a mu Yeriko. (Yos. 6:2-5) Tiphunzilapo ciani pa nkhaniyi? Nthawi zina sitingamvetsetse zifukwa zimene gulu la Mulungu lapangila masinthidwe ena ake. Mwacitsanzo, mwina poyamba sitinamvetsetse cifukwa cake gulu la Mulungu linali kutilimbikitsa kuseŵenzetsa mafoni na matabuleti mu ulaliki, pa misonkhano, kapena pa phunzilo laumwini. Koma mwacidziŵikile, tsopano taona mapindu oseŵenzetsa zida zimenezi ngati n’kotheka. Tikaona ubwino wa masinthidwe amene apangidwa, olo kuti mwina poyamba tinali kukayikila, cikhulupililo na mgwilizano wathu zimalimba. w18.10 23 ¶8-9

Citatu, December 16

Ambuye, kodi mubwezeletsa ufumu kwa Isiraeli pa nthawi ino? —Mac. 1:6.

Ziyembekezo zimene anthu anali nazo zokhudza Mesiya, monga zimene ophunzila a Yesu anali nazo, n’zimene zinacititsa kuti anthu a ku Galileya aganize zolonga Yesu ufumu. Mwacionekele, iwo anaona kuti Yesu angakhale mtsogoleli wabwino ngako. Iye anali wodziŵa kulankhula, anali kucilitsa odwala, komanso anakwanitsa ngakhale kupatsa cakudya anthu amene anali na njala. Pambuyo podyetsa amuna pafupi-fupi 5,000, Yesu anazindikila zimene anthuwo anafuna kucita. Baibo imati: “Yesu atadziŵa kuti iwo akufuna kumugwila kuti amuveke ufumu, anacoka ndi kupitanso ku phili yekha-yekha.” (Yoh. 6:10-15) Tsiku lotsatila pamene anali ku tsidya lina la nyanja ya Galileya, Yesu anaona kuti maganizo ofuna kumulonga ufumu amene anthuwo anali nawo, acepako. Conco, anawafotokozela colinga ceni-ceni ca utumiki wake. Anawauza kuti sanabwele kudzawapatsa zinthu zakuthupi, koma kudzawaphunzitsa za Ufumu wa Mulungu. Anati: “Musamagwile nchito kuti mungopeza cakudya cimene cimawonongeka, koma kuti mupeze cakudya cokhalitsa, copeleka moyo wosatha.”—Yoh. 6:25-27. w18.06 4 ¶4-5

Cinayi, December 17

Bango lophwanyika sadzalithyola, ndipo cingwe ca nyale comwe catsala pang’ono kuzima sadzacizimitsa.—Yes. 42:3.

Yesu anali kuwamvetsetsa anthu, amene mophiphilitsila anali monga bango lophwanyika, kapena ngati nyale imene yatsala pang’ono kuzima. Ndiye cifukwa cake iye anali kucita nawo zinthu moleza mtima, mokoma mtima, ndi mowaganizila. (Maliko 10:14) N’zoona kuti luso lathu la kuzindikila na kuphunzitsa silingafanane na limene Yesu anali nalo. Komabe, tingakwanitse kucita zinthu moganizila anthu a m’gawo lathu, ndipo izi n’zimene tiyenela kucita. Zimene zingaonetse kuti timawaganizila ni kakambidwe kathu powalalikila, nthawi imene timawafikila, na utali wa makambilano athu. Masiku ano, anthu mamiliyoni ambili-mbili ni “onyukanyuka ndi otayika” cifukwa copondelezedwa na atsogoleli acipembedzo, andale, komanso anthu azamalonda acinyengo ndi ankhanza. (Mat. 9:36) Zotulukapo zake n’zakuti anthu ambili amakonda kukayikila ena, ndipo alibe ciyembekezo. Conco, n’kofunika kwambili kuti zokamba zathu mu ulaliki komanso mmene timakambila zizionetsa kuti ndise okoma mtima ndi acifundo. Anthu ambili amakopeka na uthenga wathu, osati cabe cifukwa cakuti timadziŵa bwino Malemba na kuwafotokoza mwaluso. Koma amakopekanso cifukwa cakuti timawaonetsa cidwi na kuwaganizila. w18.09 31 ¶13-14

Cisanu, December 18

Odala ndi anthu amene amazindikila zosoŵa zawo zauzimu. —Mat. 5:3.

Tingaonetse bwanji kuti timazindikila zosoŵa zathu zauzimu? Tingacite izi mwa kuphunzila Mawu a Mulungu wathu wacimwemwe, kutsatila miyezo yake, na kuika patsogolo zinthu zokhudza kulambila. Tikatelo, tidzakhala na cimwemwe coculuka, ndipo tidzalimbitsa cikhulupililo cathu m’malonjezo a Mulungu. (Tito 2:13) Kupanga ubwenzi wolimba na Yehova n’kofunika kwambili kuti tikhale na cimwemwe cokhalitsa. Mouzilidwa, mtumwi Paulo analemba kuti: “Nthawi zonse kondwelani mwa Ambuye [Yehova]. Ndibwelezanso, kondwelani.” (Afil. 4:4) Kuti tikhale pa ubwenzi na Mulungu, tifunika kupeza nzelu zocokela kwa iye. (Miy. 3:13, 18) Komabe, kuti tikhaledi na cimwemwe cokhalitsa, tifunika kumaseŵenzetsa zimene timaŵelenga m’Mawu a Mulungu. Pogogomeza kufunika kocita zimene timaphunzila, Yesu anati: “Ngati zimenezi mukuzidziŵa, ndinu odala mukamazicita.” (Yoh. 13:17; Yak. 1:25) Kuseŵenzetsa zimene timaphunzila n’kumene kungatithandize kupeza zosoŵa zathu zauzimu, komanso kukhala na cimwemwe cokhalitsa. w18.09 18 ¶4-6.

Ciŵelu, December 19

[Epafura] amakupemphelelani mwakhama nthawi zonse. —Akol. 4:12.

Epafura anali kuwadziŵa bwino abale a ku Kolose, komanso anali kuwakonda kwambili. Olo kuti iye anali “mkaidi mnzake” wa Paulo, sanaleke kuganizila zosoŵa zauzimu za Akhristu anzake. (Filim. 23, NWT) Ndipo anacitapo kanthu kuti awathandize. Anawapemphelela. Iye anali na mtima woganizila ena kwambili. Ifenso tingacite bwino kumapemphelela Akhristu anzathu na kuwachula maina powapemphelela. Mapemphelo aconco amagwila nchito mwamphamvu kwambili. (2 Akor. 1:11; Yak. 5:16) Kodi n’ndani amene mungawapemphelele mwa kuwachula maina? Mofanana na Epafura, abale na alongo athu ambili amapemphelela Akhristu a mu mpingo mwawo, kapena mabanja amene akusamalila maudindo aakulu. Amapemphelelanso Akhristu amene afuna kupanga zosankha zazikulu, kapenanso amene akukumana na ziyeso. Kuwonjezela apo, sitiyenela kuiŵala kupemphelela abale na alongo amene anafeledwa, amene akhudzidwa na tsoka la zacilengedwe kapena nkhondo, komanso amene akukumana na mavuto a zacuma. Kukamba zoona, pali abale na alongo ambili amene tifunika kumawapemphelela, ndipo angapindule na mapemphelo athu. w18.09 5-6 ¶12-13

Sondo, December 20

Kupatsa kumabweletsa cimwemwe coculuka kuposa kulandila. —Mac. 20:35.

Paulo sanali kukamba za kupatsa ena zinthu zakuthupi cabe, koma anali kukambanso za kupatsa ena cilimbikitso, malangizo, komanso thandizo kwa amene akufunikila zinthu zimenezi. (Mac. 20:31-35) Mwa mawu na citsanzo cake, mtumwiyu anatiphunzitsa kuti tiyenela kudzipeleka pothandiza ena mwa kuseŵenzetsa nthawi na mphamvu zathu, komanso kuwalimbikitsa na kuwaonetsa cikondi. Akatswili a za cikhalidwe ca anthu nawonso azindikila kuti kupatsa kumathandiza anthu kukhala acimwemwe. Nkhani ina inati, “anthu amakhala acimwemwe kwambili akacitila ena zabwino.” Akatswiliwo amakamba kuti kuthandiza ena n’kofunika kuti munthu akhale na umoyo “waphindu na wokhutilitsa, cifukwa kumakwanilitsa zosoŵa zazikulu za anthu.” Ndiye cifukwa cake nthawi zambili akatswili amalimbikitsa anthu kuti azidzipeleka pa nchito zacitukuko kuti akhale na thanzi labwino komanso acimwemwe. Izi n’zosadabwitsa kwa ise amene timakhulupilila Baibo, imene ni Mawu a Mlengi wathu wacikondi, Yehova.—2 Tim. 3:16, 17. w18.08 22 ¶17-18

Mande, December 21

Lekani kuweluza poona maonekedwe akunja, koma muziweluza ndi ciweluzo colungama.—Yoh. 7:24.

Zimene Yesaya anakamba mu ulosi wake wonena za Ambuye wathu Yesu Khristu n’zolimbikitsa kwambili. Iye anakamba kuti Yesu “sadzaweluza potengela zimene wangoona ndi maso ake, kapena kudzudzula potengela zimene wangomva ndi makutu ake. Adzaweluza mwacilungamo anthu onyozeka.” (Yes. 11:3, 4) N’cifukwa ciani zimenezi n’zolimbikitsa? Cifukwa m’dzikoli anthu ambili ni atsankho ndipo amacita zinthu mokondela. Conco, tikuyembekezela mwacidwi nthawi imene tidzakhala na woweluza wacilungamo, Yesu Khristu, amene sadzatiweluza poona maonekedwe athu akunja. Tsiku lililonse timaweluza anthu ena. Koma popeza ndise opanda ungwilo, sitikwanitsa kuweluza mwacilungamo ngati mmene Yesu amacitila. Timakonda kuweluza motengela zimene timaona. Koma pamene Yesu anali pa dzikoli, anatilamula kuti: tileke kuweluza ‘poona maonekedwe akunja, koma tiziweluza ndi ciweluzo colungama.’ Mwa ici, n’zoonekelatu kuti Yesu amafuna kuti titengeleko citsanzo cake mwa kupewa kuweluza ena poona maonekedwe awo akunja. w18.08 8 ¶1-2

Ciŵili, December 22

[Udzamva] mawu kumbuyo kwako, akuti: “Njila ndi iyi. [Yenda] mmenemu.”—Yes. 30:21.

N’zoona kuti Mulungu sakamba nafe kucokela kumwamba. Komabe, amatipatsa malangizo kupitila m’Mawu ake olembedwa, Baibo. Kuwonjezela apo, pogwilitsila nchito mzimu wake, Yehova amalimbikitsa “mtumiki woyang’anila nyumba wokhulupilika” kupitiliza kupeleka cakudya cauzimu kwa atumiki ake. (Luka 12:42) Kukamba zoona, masiku ano timalandila cakudya cauzimu ca mwana alilenji, kupitila m’mabuku na zofalitsa zina za pa webusaiti yathu, monga mavidiyo na zomvetsela. Tiyeni tizikumbukila mawu amene Yehova anakamba pamene Mwana wake anali padziko lapansi. Lolani kuti Mawu a Mulungu, olembedwa m’Baibo, alimbitse cikhulupililo canu cakuti Yehova akuona zonse, ndipo adzathetsa mavuto onse amene Satana na dziko lake abweletsa pakati pathu. Conco, tikhale na colinga comvetsela mwachelu Mawu a Yehova. Tikatelo, tidzatha kupilila mavuto alionse amene tikumana nawo pali pano, komanso a kutsogolo. Baibo imati: “Mukufunika kupilila, kuti mutacita cifunilo ca Mulungu, mudzalandile zimene Mulungu walonjeza.”—Aheb. 10:36. w19.03 13 ¶17-18

Citatu, December 23

Yehova analankhula ndi Yoswa . . . : “Mose mtumiki wanga wamwalila. Tsopano konzeka limodzi ndi anthu onsewa, kuti muwoloke Yorodanoyu.”—Yos. 1:1, 2.

Popeza Mose anali mtsogoleli wa Aisiraeli kwa zaka zambili, Yoswa ayenela kuti anali na nkhawa yakuti kaya anthu a Mulungu adzamugonjela monga mtsogoleli wawo watsopano kapena ayi. (Deut. 34:8, 10-12) Pokamba za Yoswa 1:1, 2, buku lina lofotokoza Baibo limati: “M’masiku akale komanso masiku ano, nthawi yosintha mtsogoleli m’dziko ni nthawi imene citetezo ca dziko cimakhala pa ciopsezo kwambili.” M’pomveka kuti Yoswa anali na nkhawa. Komabe, patapita cabe masiku angapo, iye anacita zimene Mulungu anam’lamula. (Yos. 1:9-11) Yoswa anadalila Yehova, ndipo anadalitsidwa. Baibo imaonetsa kuti Yehova anatsogolela Yoswa na Aisiraeli poseŵenzetsa mngelo. Mngelo ameneyo ayenela kuti anali Mawu, Mwana wa Mulungu woyamba kubadwa. (Eks. 23:20-23; Yoh. 1:1) Ndi thandizo la Yehova, Aisiraeli anapitilizabe kugonjela mtsogoleli wawo watsopano, Yoswa, amene analoŵa m’malo mwa Mose. w18.10 22-23 ¶1-4

Cinayi, December 24

Buku la cikumbutso linayamba kulembedwa pamaso pake. Buku limeneli linali lonena za anthu oopa Yehova.—Mal. 3:16.

Yehova amawadziŵa bwino anthu amene amam’tumikila na mtima wonse moti amalemba maina awo ‘m’buku la cikumbutso.’ Kulembedwa dzina ‘m’buku la cikumbutso’ la Yehova monga anthu ake kumabwela na udindo wake. Malaki anakamba kuti tiyenela ‘kuopa Yehova ndi kuganizila za dzina lake.’ Koma ngati tingayambe kulambila munthu kapena cinthu cina ciliconse, ndiye kuti dzina lathu lingacotsedwe m’buku la moyo lophiphilitsila la Yehova. (Eks. 32:33; Sal. 69:28) Conco, kudzipatulila kwa Yehova kumaphatikizapo zambili, osati kungolonjeza kuti tidzacita cifunilo cake na kubatizika. Zinthu zimenezi zimakhala za kanthawi kocepa, ndipo posapita nthawi zikhoza kuiŵalika. Koma kuti tionetse kuti tili ku mbali ya Yehova, tifunika kukhala omvela nthawi zonse, kwa moyo wathu wonse.—1 Pet. 4:1, 2. w18.07 23-24 ¶7-9

Cisanu, December 25

Pamene tasiya ciphunzitso coyambilila ca Khristu tsopano, tiyeni tiyesetse mwakhama kuti tikhale okhwima mwauzimu.—Aheb. 6:1.

Izi sizicitika zokha. Tifunika ‘kuyesetsa mwakhama,’ kapena kuti kugwililapo nchito. Kukhala okhwima mwauzimu kumaphatikizapo kuwonjezela cidziŵitso na luso lathu la kuzindikila. Ndiye cifukwa cake nthawi zambili timalimbikitsidwa kuti tiziŵelenga Baibo tsiku lililonse. (Sal. 1:1-3) Kodi imwe munadziikila colinga coŵelenga Baibo tsiku lililonse? Kucita zimenezi kungakuthandizeni kudziŵa bwino malamulo a Yehova na mfundo zake. Kungakuthandizeninso kukhala na cidziŵitso cozama ca Mawu a Mulungu. Lamulo lalikulu kwambili kwa ise Akhristu ni lakuti tiyenela kukondana. Yesu anauza ophunzila ake kuti: “Mwakutelo, onse adzadziŵa kuti ndinu ophunzila anga, ngati mukukondana.” (Yoh. 13:35) Yakobo, m’bale wake wa Yesu, anakamba kuti cikondi ni “lamulo lacifumu.” (Yak. 2:8) Nayenso Paulo anati: “Cilamulo cimakwanilitsidwa m’cikondi.” (Aroma 13:10) N’zosadabwitsa kuti Baibo imagogomeza kufunika kwa cikondi cifukwa “Mulungu ndiye cikondi.”—1 Yoh. 4:8. w18.06 19 ¶14-15

Ciŵelu, December 26

Iwo anamukwiyitsa, ndipo Mose anayamba kulankhula mosalingalila bwino.—Sal. 106:33.

Ngakhale kuti Aisiraeli anaputa mkwiyo wa Yehova, Mose ndiye anakwiya. Cifukwa colephela kudziletsa, iye analankhula mosasamala popanda kuganizila zotulukapo zake. Mose analola zocita za ena kumulepheletsa kuyang’anabe kwa Yehova. Pa cocitika coyamba, iye anacita zinthu moyenela. (Eks. 7:6) Koma n’kutheka kuti pambuyo potsogolela Aisiraeli opanduka kwa zaka zambili, iye analema komanso anakhumudwa na zocita zawo. Ndipo mwina Mose anayamba kuganizila kwambili za mmene anali kumvelela, m’malo moganizila za mmene angapelekele ulemelelo kwa Yehova. Ngati mneneli wokhulupilika Mose anacenjenekewa mpaka kulakwila Mulungu, na ise zaconco zingaticitikile mosavuta. Mofanana ndi Mose, tatsala pang’ono kuloŵa m’dziko latsopano limene Yehova anatilonjeza. (2 Pet. 3:13) Palibe aliyense amene angafune kuphonya mwayi wapadela umenewu. Koma kuti mwayi umenewu usakatiphonye, tifunika kuikabe maso athu pa Yehova na kumumvela nthawi zonse.—1 Yoh. 2:17. w18.07 15 ¶14-16

Sondo, December 27

Mwagonjetsa woipayo. —1 Yoh. 2:14.

Satana sangakwanitse kukakamiza anthu kucita zimene iwo safuna. (Yak. 1:14) Mosadziŵa, anthu ambili amacita zinthu mogwilizana ndi colinga cake. Koma akaphunzila coonadi, aliyense payekha amakhala na ufulu wodzisankhila amene afuna kum’tumikila. (Mac. 3:17; 17:30) Ngati tatsimikiza mtima kucita cifunilo ca Mulungu, Satana sangakwanitse kutitaitsa cikhulupililo cathu. (Yobu 2:3; 27:5) Palinso zina zimene Satana na ziŵanda zake sangakwanitse kucita. Mwacitsanzo, palibe paliponse m’Malemba pamene paonetsa kuti iwo angakwanitse kudziŵa zimene zili m’maganizo kapena mumtima wa munthu. Ni Yehova na Yesu cabe amene amakwanitsa kucita zimenezi. (1 Sam. 16:7; Maliko 2:8) Ngati tiyesetsa kukamba na kucita zinthu mogwilizana na cifunilo ca Mulungu, Yehova sadzalola Mdyelekezi kutiwononga kothelatu. (Sal. 34:7) Tifunika kum’dziŵa bwino mdani wathu, koma sitifunika kumuyopa. Mwa thandizo la Yehova, ngakhale ise anthu opanda ungwilo tikhoza kum’gonjetsa Satana. Ngati timutsutsa, iye adzatithaŵa.—Yak. 4:7; 1 Pet. 5:9. w18.05 26 ¶15-17

Mande, December 28

Peleka nchito zako kwa Yehova, ndipo zolinga zako ndithu zidzakhazikika.—Miy. 16:3.

Tiyelekezele kuti mufuna kupita ku tauni inayake yakutali kukacita zina zake zofunika kwambili. Kuti mukafike kumeneko, mufunika kukwela basi. Koma pamene mufika pa sitesheni ya basi, mupeza kuti pali mabasi yambili. Imwe mufunika kukwela basi yoyenelela imene ikakufikitseni kumene mufuna kupita. Kungokwela basi iliyonse imene mwakonda kungacititse kuti musocele. Acicepele masiku ano ali ngati anthu amene ali pa sitesheni ya basi. Nthawi zina, kupanga zosankha kumawavuta. Imwe acicepele, kodi n’ciani cingakuthandizeni kupanga zosankha mwanzelu? Muyenela kukhala na colinga mu umoyo wanu. Kodi mudzalunjika maganizo anu pa kukhala na zolinga zokondweletsa Yehova? Izi zitanthauza kuti muyenela kuika iye patsogolo pa ciliconse cimene mumacita mu umoyo wanu, kaya ni zokhudza maphunzilo, nchito, maudindo a m’banja, na zina zaconco. Zitanthauzanso kuti muyenela kuyesetsa kukwanilitsa zolinga zauzimu. Acicepele amene amaika mtima wawo wonse pa kutumikila Yehova, angakhale na cidalilo cakuti iye adzawadalitsa na kuwathandiza kukhala na umoyo wopambana. w18.04 25 ¶1-3

Ciŵili, December 29

Kalanga ine mwana wanga! Wandiwelamitsa ndi cisoni ndipo ine ndikukupitikitsa.—Ower. 11:35.

Yefita anasungabe lumbilo lake. Anatumiza mwana wake wamkazi namwali ku Silo kuti akatumikile ku cihema kwa moyo wake wonse. (Ower. 11:30-35) Izi ziyenela kuti zinali zovuta kwa Yefita. Koma zinali zovuta ngako kwa mwana wakeyo. Olo zinali conco, mtsikanayo anavomela na mtima wonse kucita zimene atate wake anasankha. (Ower. 11:36, 37) Iye analolela kukhala wosakwatiwa na wopanda ana, ndipo analibenso mwayi wosunga dzina la banja lawo kapena wolandila coloŵa. Conco, mtsikana ameneyu anali kufunikila kwambili citonthozo na cilimbikitso. Baibo imati: “Mu Isiraeli munakhala cizoloŵezi cakuti, caka ndi caka ana aakazi a mu Isiraeli anali kupita kukayamikila mwana wamkazi wa Yefita wa ku Giliyadi, maulendo anayi pa caka.” (Ower. 11:39, 40) Akhristu amene sali pabanja, amene akuseŵenzetsa umbeta wawo popititsa patsogolo “zinthu za Ambuye,” nawonso tiyenela kuwalimbikitsa na kuwayamikila kwambili.—1 Akor. 7:32-35. w18.04 17 ¶10-11

Citatu, December 30

Angelo . . . sanasunge malo awo oyambilila koma anasiya malo awo okhala.—Yuda 6.

Gulu lalikulu ndithu la angelo linakhala ku mbali ya Satana popandukila Mulungu. Cigumula cisanacitike, Satana anasonkhezela ena mwa angelo amenewa kubwela pa dziko lapansi na kuyamba kugonana ndi akazi. Baibo imafotokoza zimenezi mophiphilitsa mwa kunena kuti cinjoka cinakokolola gawo limodzi mwa magawo atatu a nyenyezi zakumwamba. (Gen. 6:1-4; Chiv. 12:3, 4) Pamene angelowo anacoka m’banja la Mulungu, anayamba kulamulidwa na Satana. Koma angelo opanduka amenewa sali gulu laciwawa lopanda dongosolo. Satana anakhazikitsa ufumu wake mokopelako Ufumu wa Mulungu, ndipo anadziika mfumu. Kumene aliliko, Satana analinganiza magulu a ziŵanda n’kupanga maboma osaoneka, ndipo anapatsa ziŵandazo mphamvu, na kuziika kukhala olamulila dziko. (Aef. 6:12) Kupitila m’gulu lake la ziŵanda, Satana ali na mphamvu pa maboma onse a anthu. w18.05 23 ¶5-6

Cinayi, December 31

Ndidzatamanda Yehova amene wandipatsa malangizo. Ndithudi, usiku impso zanga zandiwongolela.—Sal. 16:7.

Nthawi zina, Mulungu amaonetsa cikondi cake kwa ise mwa kutipatsa uphungu mwacikondi. Pa nthawi ina, Davide anayamikila uphungu wacikondi umene Mulungu anam’patsa. Davide anali kusinkha-sinkha pa Mawu a Mulungu kuti adziŵe mmene Mulungu amaonela zinthu, na kuyamba kuyendela maganizo ake. Komanso, anali kulola Mawu ake kumuwongolela. Na imwe ngati mucita zimenezi, mudzayamba kukonda kwambili Mulungu, ndipo mudzakhala wofunitsitsa kumumvela. Izi zidzakuthandizaninso kukula mwauzimu na kukhala ozikika mozama m’coonadi. Mlongo wina dzina lake Christin anati: “Pamene niŵelenga nkhani inayake, kufufuza na kuisinkha-sinkha, nimaona ngati kuti Yehova analembela ine nkhaniyo.” Mukakhala munthu wauzimu, Mulungu amakupatsani nzelu na kukuthandizani kukhala wozindikila. Izi zimakuthandizani kuti muziona dzikoli na tsogolo lake monga mmene iye amalionela. N’cifukwa ciani Mulungu amakupatsani nzelu na kukuthandizani kukhala wozindikila? Cifukwa amafuna kuti muzipanga zosankha mwanzelu. Amafunanso kuti mudziikile zolinga zaphindu mu umoyo wanu, ndi kuti mukhale na ciyembekezo ca tsogolo labwino.—Yes. 26:3. w18.12 26 ¶9-10

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani