January
Ciŵelu, January 1
Kuyambila pamene unali wakhanda, wadziŵa malemba oyela amene angathe kukupatsa nzelu zokuthandiza kuti udzapulumuke kudzela m’cikhulupililo cokhudza Khristu Yesu.—2 Tim. 3:15.
Cikhulupililo ca Timoteyo cinazikidwa pa mfundo zimene zinamusonkhezela kukhala pa ubwenzi na Yehova. Na imwe mufunika kuŵelenga Baibo kuti mufike pokhulupilila kuti zimene Baibo imaphunzitsa ponena za Yehova n’zoona. Kuti inunso mukhulupilile kuti muli na coonadi, muyenela kumvetsetsa ziphunzitso zitatu zoyambilila na kukhutila nazo. Coyamba, mufunika kukhulupilila kuti Yehova Mulungu ndiye Mlengi wa zinthu zonse. (Eks. 3:14, 15; Aheb. 3:4; Chiv. 4:11) Caciŵili, mufunika kupeza umboni pa imwe mwekha wotsimikizila kuti Baibo ni uthenga wouzilidwa na Mulungu wopita kwa anthu. (2 Tim. 3:16, 17) Cacitatu, mufunika kukhulupilila kuti Yehova ali na gulu lolinganizidwa bwino la anthu amene amam’lambila motsogoleledwa na Khristu, na kuti gulu limenelo ni Mboni za Yehova. (Yes. 43:10-12; Yoh. 14:6; Mac. 15:14) Sikuti mufunika kudziŵa mfundo zonse za m’Baibo. Cofunika kwambili ni kuseŵenzetsa “luntha [lanu] la kuganiza” kuti mulimbitse cikhulupililo canu cakuti muli na coonadi.—Aroma 12:1. w20.07 10 ¶8-9
Sondo, January 2
Dzombelo silinaloledwe kupha anthuwo, koma linauzidwa kuti liwazunze miyezi isanu.—Chiv. 9:5.
Ulosi umenewu umakamba za gulu la dzombe lokhala na nkhope za anthu, ndiponso “zisoti zagolide zooneka ngati zacifumu” pamitu pawo. (Chiv. 9:7) Dzombelo likuzunza “anthu okhawo [adani a Mulungu] amene alibe cidindo ca Mulungu pamphumi pawo” kwa miyezi 5. Nthawi imeneyi ikufanana ndi nthawi imene dzombe limakhala na moyo. (Chiv. 9:4) N’zoonekelatu kuti ulosi umenewu ukamba za atumiki odzozedwa a Yehova. Iwo amalengeza uthenga waciweluzo wa Mulungu molimba mtima kwa anthu a m’dziko loipali, ndipo zotulukapo zake n’zakuti anthuwo amazunzika kwambili na uthengawo. Kodi apa titanthauza kuti dzombe lochulidwa pa Yoweli 2:7-9 n’losiyana na dzombe la m’buku la Chivumbulutso? Inde. M’Baibo, nthawi zina cinthu cimodzi cophiphilitsila cimakhala na matanthauzo osiyana malinga na nkhani yake. Mwacitsanzo, pa Chivumbulutso 5:5, Yesu akuchulidwa kuti ni “mkango wa fuko la Yuda,” koma pa 1 Petulo 5:8, Mdyelekezi akuchulidwa kuti ni “mkango wobangula.” w20.04 3 ¶8; 5 ¶10
Mande, January 3
Maso a Yehova ali paliponse. Amayang’ana anthu oipa ndi abwino omwe.—Miy. 15:3.
Hagara, mdzakazi wa Sarai, anacita zinthu mopanda nzelu pamene anakhala mkazi wa Abulamu. Hagara atakhala na pakati, anayamba kupeputsa Sarai, amene panthawiyo analibe mwana. Ubale wa Sarai na Hagara unasokonezeka, ndipo zinthu zinafika poipa moti Hagara anathaŵa panyumbapo. (Gen. 16:4-6) M’kaonedwe kathu kaumunthu, tingaganize kuti Hagara anali mkazi wonyada, wofunikadi kulangidwa. Koma Yehova sanamuone mwanjila imeneyi. Iye anatumiza mngelo wake kwa Hagara. Atam’peza, anamuthandiza kuti asinthe khalidwe lake, komanso anam’dalitsa. Hagara anazindikila kuti Yehova anali kumuyang’anila, ndiponso kuti anali kudziŵa bwino mmene zinthu zinalili mu umoyo wake. Iye anakhudzika kwambili na zimenezi, cakuti anafika pokamba kuti Yehova ni “Mulungu amene amaona ciliconse.”(Gen. 16:7-13) Kodi n’ciani cimene Yehova anaona mwa Hagara? Iye anali kudziŵa bwino za umoyo wake, kuphatikizapo mavuto onse amene anapitamo. Yehova anadziŵa kuti zimene Hagara anacita, zopeputsa Sarai, zinali zolakwika. Ngakhale n’telo, iye anacita zinthu mokoma mtima na Hagara cifukwa anadziŵa bwino mmene anali kumvelela, komanso mmene zinthu zinalili pa umoyo wake. w20.04 16 ¶8-9
Ciŵili, January 4
Ndathamanga panjilayo mpaka pa mapeto pake.—2 Tim. 4:7.
Mtumwi Paulo anakamba kuti Akhristu onse oona ali pa mpikisano wothamanga. (Aheb. 12:1) Ndipo tonse, kaya ndife acicepele kapena acikulile, amphamvu kapena ofooka, tifunika kuthamanga mopilila mpaka ku mapeto kuti tikalandile mphoto imene Yehova anatilonjeza. (Mat. 24:13) Pa nkhani yothamanga pa mpikisano, Paulo anali na ufulu wolankhula cifukwa ‘anathamanga panjilayo mpaka pa mapeto pake.’ (2 Tim. 4:7, 8) Koma kodi mpikisano wothamanga umene Paulo anakamba ni wotani maka-maka? Nthawi zina, Paulo pophunzitsa Akhristu mfundo zofunika, anali kufotokoza zinthu zimene zinali kucitika pa maseŵela ku Girisi wakale. (1 Akor. 9:25-27; 2 Tim. 2:5) Kangapo konse, iye anayelekezela umoyo wacikhristu na mpikisano wothamanga. (1 Akor. 9:24; Agal. 2:2; Afil. 2:16) Munthu amayamba kuthamanga pa ‘mpikisanowu’ akadzipatulila kwa Yehova na kubatizika. (1 Pet. 3:21) Ndipo Yehova akam’patsa mphoto ya moyo wosatha, ndiye kuti wafika pa mzele wotsiliza.—Mat. 25:31-34, 46; 2 Tim. 4:8. w20.04 26 ¶1-3
Citatu, January 5
Nyamulani zida zonse zankhondo zocokela kwa Mulungu.—Aef. 6:13.
“Ambuye [Mulungu] ndi wokhulupilika ndipo adzakulimbitsani ndi kukutetezani kwa woipitsitsayo.” (2 Ates. 3:3) Kodi Yehova amatiteteza bwanji? Yehova watipatsa zida zonse zankhondo zimene zingatiteteze ku misampha ya Satana. (Aef. 6:13-17) Zida zauzimu zankhondo zimenezi n’zolimba ndiponso zothandiza! Koma tingakhale otetezeka kokha ngati tavala zida zonse zankhondo na kusazivula. Mwacitsanzo Lamba wacoonadi aimila coonadi copezeka m’Mawu a Mulungu, Baibo. N’cifukwa ciani tifunika kuvala lamba ameneyu? Cifukwa Satana ni “tate wake wa bodza.” (Yoh. 8:44) Iye wakhala akunama bodza kwa zaka masauzande, ndipo ‘wasoceletsa dziko lonse lapansi kumene kuli anthu’! (Chiv. 12:9) Koma coonadi copezeka m’Baibo cimatiteteza kuti tisanyengedwe. Kodi timavala bwanji lamba wophiphilitsa ameneyu? Timacita zimenezi mwa kuphunzila zoona zokhudza Yehova, mwa kum’lambila mu “mzimu ndi coonadi,” komanso mwa kucita zinthu zonse moona mtima.—Yoh. 4:24; Aef. 4:25; Aheb. 13:18. w21.03 26-27 ¶3-5
Cinayi, January 6
Iyo idzaloŵanso m’Dziko Lokongola.—Dan. 11:41.
Dziko limenelo linali kuonedwa lokongola kwambili cifukwa cakuti n’kumene anthu anali kulambila Yehova. Koma kucokela pa Pentekosite wa mu 33 C.E., “dziko lokongola” si dela leni-leni padzikoli. Takamba telo cifukwa tsopano anthu a Yehova ali kulikonse padziko lapansi. Conco, masiku ano, “dziko lokongola” ni paradaiso wauzimu wa anthu a Yehova. Paradaiso ameneyu aphatikizapo zimene anthu a Yehova amacita pom’lambila, monga kusonkhana pamodzi na kulalikila. M’masiku otsiliza ano, mfumu ya kumpoto yaloŵa mobweleza-bweleza “m’Dziko Lokongola.” Mwacitsanzo, pamene boma la Nazi ku Germany linali mfumu ya kumpoto, linaloŵa “m’Dziko Lokongola” mwa kuzunza na kupha anthu a Mulungu. Izi zinacitika kwambili pa nkhondo yaciŵili ya padziko lonse. Pambuyo pa nkhondoyo, boma la Soviet Union n’limene linakhala mfumu ya kumpoto. Bomali nalonso linaloŵa “m’Dziko Lokongola” mwa kuzunza anthu a Mulungu na kuwathamangitsila ku Siberia, dela lakutali kwambili na kwawo. w20.05 13 ¶7-8
Cisanu, January 7
Ubwenzi wolimba ndi Yehova ndi wa anthu amene amamuopa. —Sal. 25:14.
Ganizilani za anthu ena amene anali mabwenzi a Mulungu, Khristu asanabwele padziko lapansi. Abulahamu anali munthu wa cikhulupililo colimba kwambili. Patapita zaka zoposa 1,000 kucokela pamene Abulahamu anamwalila, Yehova anamucha “bwenzi [lake].” (Yes. 41:8) Izi zionetsa kuti olo munthu afe, Yehova amamuonabe kuti ni bwenzi lake. Conco, m’maso mwa Yehova, Abulahamu akali moyo. (Luka 20:37, 38) Munthu wina wa m’nthawi yakale amene anali bwenzi la Mulungu ni Yobu. Pamene angelo onse anasonkhana kumwamba, Yehova anakamba monyadila za Yobu. Anakamba kuti Yobu anali “munthu wopanda colakwa ndi wowongoka mtima, woopa Mulungu ndi wopewa zoipa.” (Yobu 1:6-8) Nanga bwanji za Danieli, amene anatumikila Yehova mokhulupilika m’dziko la anthu osalambila Mulungu kwa zaka pafupi-fupi 80? Katatu konse angelo anauza Danieli, amene panthawiyo anali wokalamba, kuti anali “wokondedwa kwambili” kwa Mulungu. (Dan. 9:23; 10:11, 19) Sitikayikila kuti Yehova amacita kulaka-laka nthawi pamene adzaukitsa mabwenzi ake amene anamwalila.—Yobu 14:15. w20.05 26-27 ¶3-4
Ciŵelu, January 8
Ndiphunzitseni malamulo anu. —Sal. 119:68.
Wophunzila Baibo wakhama angaphunzile malamulo a Mulungu na kuwadziŵa bwino, mpaka kuyamba kuwalemekeza kwambili. Koma kodi izi zingamusonkhezele kukonda Yehova na kuyamba kumumvela? Kumbukilani Hava. Iye anali kulidziŵa bwino lamulo la Mulungu. Koma sanam’konde na mtima wonse Mulungu amene anapeleka lamulolo. Adamu nayenso sanali kum’konda Mulungu. (Gen. 3:1-6) Conco, pophunzitsa anthu Baibo, tisamangowaphunzitsa cabe malamulo a Mulungu. Malamulo a Yehova ni abwino kwambili. (Sal. 119:97, 111, 112) Koma ophunzila Baibo athu sangaone kuti malamulowo ni abwino ngati sanafike pomvetsetsa mfundo yakuti Yehova anaika malamulowo cifukwa cotikonda. Conco tingacite bwino kufunsa ophunzila athu kuti: “Muganiza kuti n’cifukwa ciani Mulungu amauza atumiki ake kuti azicita izi komanso kuti azipewa izi? Kodi zimenezi zionetsa kuti iye ni wotani?” Ngati tiphunzitsa ophunzila Baibo kuti aziganizila za Yehova, ndiponso kuti ayambe kukonda dzina lake laulemelelo, tidzawafika pamtima. Iwo adzayamba kukonda malamulo ake komanso Mulungu amene anapeleka malamulowo. Adzakhala na cikhulupililo colimba cimene cidzawathandiza kupilila mayeselo okhala ngati moto amene adzakumana nawo kutsogolo.—1 Akor. 3:12-15. w20.06 10 ¶10-11
Sondo, January 9
[Khala] wofulumila kumva, wodekha polankhula.—Yak. 1:19.
Tiyenela kukhala oleza mtima cifukwa zimatenga nthawi kuti munthu abwelele kwa Yehova. Ambili amene kale anali ozilala amakamba kuti anayambanso kugwilizana na mpingo pambuyo pocezeledwa mobweleza-bweleza na akulu komanso ofalitsa ena. Mlongo wina wa ku Southeast Asia, dzina lake Nancy, analemba kuti: “Mnzanga wina wapamtima mumpingo ananithandiza kwambili. Anali kunikonda kwambili monga mng’ono wake. Anali kunikumbutsa zinthu zokondweletsa zimene tinali kucita kale. Anali kunimvetsela moleza mtima pamene n’nali kufotokoza mmene n’nali kumvelela, ndipo sanali kuyopa kunipatsa malangizo. Anaonetsa kuti analidi bwenzi langa leni-leni, lokonzeka kunithandiza nthawi iliyonse.” Munthu akakhumudwa, amamvela kupweteka mumtima monga kuti ali na cilonda. Cifundo cili ngati mankhwala amphamvu amene angathandize munthu wotelo kumvelako bwino. Ena anazilala cifukwa cakuti winawake mumpingo anawakhumudwitsa zaka zambili zapitazo, ndipo akali okhumudwa. Pa cifukwa cimeneci, safuna kubwelela kwa Yehova. Mwina iwo amaona kuti anacitilidwa zinthu mopanda cilungamo. Amafuna munthu amene angawamvetsele, komanso amene angamvetsetse mmene akumvelela mumtima. w20.06 26 ¶10-11
Mande, January 10
Mwagonjetsa woipayo.—1 Yoh. 2:14.
Nthawi iliyonse mukakana kugonja ku mayeselo, zimakhala zopepukilako kucita coyenela. Kumbukilaninso kuti maganizo olakwika amene anthu a m’dzikoli ali nawo pa nkhani ya kugonana ni ocokela kwa Satana. Ngati mupewa kutsatila maganizo a dziko, ndiye kuti ‘mukugonjetsa woipayo.’ Timadziŵa kuti Yehova ndiye ali na udindo wotiuza kuti kucita zakuti-zakuti ni chimo. Ndipo timayesetsa kupewa kucita chimo. Koma tikacimwa, timavomeleza colakwa cathu kwa Yehova m’pemphelo. (1 Yoh. 1:9) Tikacita chimo lalikulu, timapempha thandizo kwa akulu, amene Yehova anawaika kuti azitisamalila. (Yak. 5:14-16) Komabe, sitiyenela kumangodziimba mlandu cifukwa ca macimo akale. Cifukwa ciani? Cifukwa Atate wathu wacikondi anapeleka nsembe ya dipo la Mwana wake n’colinga cakuti macimo athu azikhululukidwa. Yehova akakhululukila munthu wolapa, amakhululukadi na mtima wonse. Conco, palibe cimene cingatilepheletse kutumikila Yehova na cikumbumtima coyela.—1 Yoh. 2:1, 2, 12; 3:19, 20. w20.07 22-23 ¶9-10
Ciŵili, January 11
Pakuti inu ndinu kasupe wa moyo.—Sal. 36:9.
Panthawi ina, Yehova anali kukhala yekha. Koma sanali wosungulumwa, cifukwa iye ni wacikwane-kwane. Ndipo sadalila wina kuti akhale wosangalala. Olo n’telo, Yehova anafuna kuti ena akhale na moyo n’kumasangalala. Cifukwa ca cikondi cake, iye anayamba nchito yolenga. (1 Yoh. 4:19) Coyamba, Yehova analenga Mwana wake, Yesu. Ndiyeno kupitila mwa Mwana wake ameneyu, “zinthu zina zonse zinalengedwa,” kuphatikizapo angelo mamiliyoni ambili. (Akol. 1:16) Yesu anali kukondwela kwambili kuseŵenzela pamodzi na Atate wake. (Miy. 8:30) Nawonso angelo anali kukondwela. Iwo anali kuona pamene Yehova na Yesu Mmisili Waluso anali kulenga kumwamba na dziko lapansi. Kodi anaonetsa bwanji cisangalalo cawo? Baibo imakamba kuti dziko litalengedwa, iwo “anayamba kufuula ndi cisangalalo.” Ndipo mosakayikila anapitiliza kusangalala na zonse zimene Yehova analenga, maka-maka anthu. (Yobu 38:7; Miy. 8:31) Zolengedwa zonsezi zimaonetsa kuti Yehova ni wacikondi komanso wanzelu.—Sal. 104:24; Aroma 1:20. w20.08 14 ¶1-2
Citatu, January 12
Mitundu yonse idzadana nanu cifukwa ca dzina langa.—Mat. 24:9.
Yehova anatilenga kuti tizikonda ena komanso tizikondedwa. Conco ngati wina amatizonda, cimatiŵaŵa ndipo mwina tingakhale na mantha. M’bale wina analemba kuti: “Asilikali atanimenya, kunitukwana, komanso kuniopseza cifukwa cokhala Mboni ya Yehova, n’nacita mantha ndipo n’nacita manyazi.” Cidani cotelo cimakhala coŵaŵa kwambili, koma izi sizitidabwitsa. Yesu anakambilatu kuti tidzazondewa. N’cifukwa ciani dzikoli limadana na otsatila a Yesu. Cifukwa mofanana na Yesu ‘sitili mbali ya dzikoli.’ (Yoh. 15:17-19) Ndipo ngakhale kuti timalemekeza maboma a anthu, timakana kuwalambila kapena kulambila zizindikilo zoimila mabomawo. Timalambila Yehova cabe. Timacilikiza Mulungu kuti ndiye woyenela kulamulila anthu, ngakhale kuti Satana na “mbewu yake” amatsutsa mwamphamvu kuti Mulungu ndiye woyenela kulamulila anthu. (Gen. 3:1-5, 15) Timalalikila kuti Ufumu wa Mulungu wokha ndiwo udzathetsa mavuto a anthu, ndipo Ufumuwo posacedwa udzawononga onse amene amautsutsa. (Dan. 2:44; Chiv. 19:19-21) Umenewu ni uthenga wabwino kwa anthu ofatsa, koma ni uthenga woipa kwa anthu oipa. w21.03 20 ¶1-2
Cinayi, January 13
Tikudziwa kuti tinacokela kwa Mulungu.—1 Yoh. 5:19.
Yehova amalemekeza alongo poŵapatsa malo mu mpingo. Iwo ni zitsanzo zabwino kwambili pa nzelu, cikhulupililo, cangu, kulimba mtima, kuwolowa manja, komanso pa nchito zabwino. (Luka 8:2, 3; Mac. 16:14, 15; Aroma 16:3, 6; Afil. 4:3; Aheb. 11:11, 31, 35) Ndifenso odalitsika kukhala na okalamba ambili. Iwo angamakumane na mavuto osiyana-siyana okhudza thanzi cifukwa ca ukalamba. Ngakhale n’conco, okalamba amenewa amacita zimene angathe pa nchito yolalikila, ndipo mwamphamvu zawo zocepazo, amacitabe khama pa kulimbikitsa na kuphunzitsa ena mocitila zinthu. Ndiponso timapindula na cidziŵitso cawo. Iwo ni okongoladi kwa Yehova, komanso kwa ife. (Miy. 16:31) Ganizilaninso za acicepele athu. Pamene akukula, amakumana na mavuto osiyana-siyana m’dzikoli lolamulidwa na Satana Mdyelekezi, komanso losonkhezeledwa na maganizo ake oipa. Ngakhale n’telo, tonsefe timalimbikitsidwa poona acicepele athu akupeleka ndemanga pa misonkhano, kutengako mbali mu ulaliki, komanso kuteteza cikhulupililo cawo molimba mtima. Inde, na imwe acicepele muli na malo mu mpingo wa Yehova!—Sal. 8:2. w20.08 21-22 ¶9-11
Cisanu, January 14
Ndikukutumizani monga nkhosa pakati pa mimbulu.—Mat. 10:16.
Tikayamba kugwila nchito yolalikila na kudziŵika kuti lomba ndife Mboni za Yehova, tingakumane na mavuto amene ali ngati “cimphepo camkuntho.” Tingayambe kutsutsidwa na a m’banja lathu komanso anzathu, ndiponso tingakumane ndi anthu okana kumvetsela uthenga wathu. Kodi mungacite ciani kuti mukhale olimba mtima? Coyamba, mufunika kukhulupilila kuti Yesu, amene tsopano ali kumwamba, akupitiliza kutsogolela pa nchito yolalikila. (Yoh. 16:33; Chiv. 14:14-16) Caciŵili, muzikhulupilila kwambili lonjezo la Yehova lakuti adzakusamalilani. (Mat. 6:32-34) Mukakhala na cikhulupililo colimba, m’pamenenso mudzakhala wolimba mtima kwambili. Munaonetsa cikhulupililo cacikulu pamene munadziŵitsa anzanu na a m’banja lanu kuti mwayamba kuphunzila Baibo na Mboni za Yehova ndiponso kupezeka pamisonkhano yawo. Ndipo mosakayikila mwasintha kwambili khalidwe lanu na zinthu zambili mu umoyo wanu n’colinga cakuti muzitsatila mfundo zolungama za Yehova. Kuti mukwanitse kucita zimenezi, panafunikanso cikhulupililo na kulimba mtima. Pamene mupitiliza kukulitsa khalidwe la kulimba mtima, mungakhale na cidalilo cakuti ‘Yehova Mulungu wanu ali namwe kulikonse kumene mupiteko.’—Yoswa 1:7-9. w20.09 5 ¶11-12
Ciŵelu, January 15
Yehova anam’patsa mpumulo.—2 Mbiri 14:6.
Mfumu Asa anacita zinthu mwanzelu mwa kudalila Yehova na mtima wonse. Iye ni citsanzo cabwino kwambili kwa ife. Asa anatumikila Yehova panthawi yovuta komanso panthawi ya mtendele. Kuyambila ali mwana, “Asa anatumikila Yehova ndi mtima wathunthu.” (1 Maf. 15:14) Njila imodzi imene Asa anaonetsela kuti anali wodzipeleka potumikila Yehova ni mwa kuthetsa kulambila konama mu Yuda. Baibo imati “iye anacotsa maguwa ansembe acilendo, anagwetsa malo okwezeka, anaphwanya zipilala zopatulika ndi kudula mizati yopatulika.” (2 Mbiri 14:3, 5) Iye anacotsa ngakhale ambuye ake aakazi a Maaka pa udindo wawo wapamwamba mu ufumu wa Yuda. Cifukwa ciani? Cifukwa anali kulimbikitsa anthu kulambila fano. (1 Maf. 15:11-13) Kuwonjezela pa kuthetsa kulambila konama, palinso zina zimene Asa anacita. Iye analimbikitsa kulambila koona, ndipo anathandiza Ayuda kuyambanso kulambila Yehova. Yehova anadalitsa Asa ndi Aisiraeli mwa kucititsa dziko lawo kukhala pa mtendele. Kwa zaka 10 mu ulamulilo wa Asa, “m’dzikolo munalibe cosokoneza ciliconse.”—2 Mbiri 14:1, 4, 6. w20.09 14 ¶2-3
Sondo, January 16
Timoteyo, sunga bwino cimene cinaikidwa m’manja mwako.—1 Tim. 6:20.
Nthawi zambili, timapempha anthu ena kuti atisungileko zinthu zathu za mtengo wapatali. Mwacitsanzo, tingasungitse ndalama zathu ku banki. Tikatelo, timakhala na cidalilo cakuti ndalamazo zidzasungika bwino, ndipo sizidzatayika kapena kubedwa. Mtumwi Paulo anakumbutsa Timoteyo kuti analandila cinthu ca mtengo wapatali. Cinthu cimeneco ni cidziŵitso colondola conena za colinga ca Mulungu kwa anthu. Timoteyo anapatsidwanso mwayi ‘wolalikila mawu,’ ndiponso ‘wogwila nchito ya mlaliki.’ (2 Tim. 4:2, 5) Paulo analangiza Timoteyo kuti asunge bwino zinthu zimene zinaikidwa m’manja mwake. Mofanana na Timoteyo, nafenso Mulungu watisungiza zinthu zamtengo wapatali. Mokoma mtima, Yehova anatithandiza kumvetsetsa coonadi camtengo wapatali copezeka m’Mawu ake, Baibo. Coonadi ca m’Baibo cimeneci ni camtengo wapatali cifukwa cimatithandiza kudziŵa mmene tingakhalile paubale wabwino na Yehova, komanso mmene tingakhalile na cimwemwe ceni-ceni mu umoyo. Ngati timakhulupilila mfundo za coonadi zimenezi na kuzitsatila, timamasuka ku ziphunzitso zonama na kupewa makhalidwe oipa.—1 Akor. 6:9-11. w20.09 26 ¶1-3
Mande, January 17
Ndipo inuyo mukudziŵa zimene tinakucitilani pofuna kukutha ndizani.—1 Ates. 1:5.
Wophunzila wanu afunika aziona kuti mukukamba mwaumoyo komanso mwacidalilo pophunzitsa mfundo za coonadi ca m’Baibo. Kucita izi kudzam’thandiza kukonda zimene akuphunzila. Ngati n’koyenela, m’simbilenkoni mmene mfundo za m’Baibo zakuthandizilani pa umoyo wanu. Pamenepo adzaona kuti m’Baibo muli malangizo amene angam’thandize nayenso. Pophunzila naye Baibo, m’simbilenkoni wophunzila wanu za anthu amene anakumana na zopinga zolingana na zake ndipo anazigonjetsa. Mungapiteko na munthu wa mu mpingo wanu, amene citsanzo cake cingathandize wophunzila wanu. Thandizani wophunzila wanu kuona kuti n’cinthu canzelu kuseŵenzetsa mfundo za m’Baibo pa umoyo wake. Ngati wophunzilayo ali pabanja, kodi mnzake wa m’cikwati nayenso amaphunzila? Ngati ayi, m’pempheni kuti azikhalapo pa phunzilo. Llimbikitsani wophunzila wanu kuti aziuzako a m’banja lake na mabwenzi ake zimene amaphunzila.—Yoh. 1:40-45. w20.10 16 ¶7-9
Ciŵili, January 18
Ndi kuwakhomeleza mwa ana ako.—Deut. 6:7.
Monga makolo, Yosefe na Mariya anathandiza Yesu kukula monga munthu woyanjidwa na Mulungu. Iwo anatsatila malangizo a Yehova kwa makolo. (Deut. 6:6, 7) Yosefe na Mariya anali na cikondi cozama pa Yehova, ndipo colinga cawo cacikulu cinali kulimbikitsa ana awo kukhala na cikondi cofananaco. Yosefe na Mariya anali na pulogilamu yabwino yocita zauzimu monga banja. Mosakaikila, iwo anali kupezeka pa misonkhano ya wiki na wiki ku sunagoge wa ku Nazareti, komanso pa Pasika wa pacaka ku Yerusalemu. (Luka 2:41; 4:16) Iwo ayenela kuti anali kutengela mwayi maulendo amenewo opita ku Yerusalemu monga banja, kuphunzitsa Yesu na azing’ono ake zokhudza mbili ya anthu a Yehova. N’kutheka kuti pamaulendo amenewo, anali kuyendelanso malo ena ochulidwa m’Malemba. Pamene banja lawo linali kukula, mwacionekele sicinali copepuka kwa Yosefe na Mariya kukhalabe na pulogilamu yabwino yocita zauzimu. Koma cifukwa ca kulimbikila kwawo, iwo anadalitsidwa kwambili. Poika kulambila Yehova patsogolo, banja lawo linakhaladi lolimba mwauzimu. w20.10 28 ¶8-9
Citatu, January 19
Ezara anakonza mtima wake kuti aphunzile Cilamulo ca Yehova . . . ndiponso kuti aphunzitse [malamulo].—Ezara 7:10.
Ngati mwapemphedwa kuti mukakhalepo pa phunzilo, zingakhale bwino kukonzekela phunzilo limenelo. M’bale David amene tam’gwila mawu kuciyambi anakamba kuti: “Nimayamikila ngati munthu amene napita naye ku phunzilo wakonzekela, cifukwa amatha kupelekapo ndemanga zothandiza.” Kuwonjezela apo, wophunzila adzaona kuti nonse aŵili mwakonzekela bwino ndipo izi zidzam’patsa citsanzo cabwino. Ngakhale kuti simungakonzekele mwacikwane-kwane nkhaniyo, pezani ndithu nthawi yoona mfundo zikulu-zikulu na kuzisunga m’maganizo. Pemphelo ni lofunika kwambili pa phunzilo la Baibo. Conco, ganizilani pasadakhale zimene mungakambe ngati mungapemphedwe kupeleka pemphelo. Mukatelo, pemphelo lanu lidzakhala lopindulitsa. (Sal. 141:2) Mlongo Hanae wa ku Japan, amakumbukilabe mapemphelo amene mlongo wina, amene anali kubwela na mphunzitsi wake wa Baibo anali kupeleka. Iye ananena kuti: “N’naona kuti iye anali paubwenzi wolimba na Yehova, ndipo nanenso n’nafuna kukhala monga iye. N’naonanso kuti anali kunikonda cifukwa anali kuchula dzina langa m’mapemphelo ake.” w21.03 9-10 ¶7-8
Cinayi, January 20
Limba mtima! . . . ukandicitilanso umboni ku Roma.—Mac. 23:11.
Yesu analimbikitsa Mtumwi Paulo kuti adzafika ku Roma. Komabe, Ayuda ena anakonza ciwembu cakuti akakhalizile Paulo panjila kuti akamuphe. Koma mkulu wa asilikali aciroma, Kalaudiyo Lusiya, atadziŵa za ciwembuco, anapulumutsa Paulo. Iye mwamsanga analamula gulu la asilikali kuti am’pelekeze Paulo ku Kaisareya. Atafika Kaisareya, Bwanamkubwa Felike analamula kuti Paulo “amusunge m’nyumba ya mfumu Herode ndi kumuyang’anila.” Apa lomba aciwembu aja ofuna kupha Paulo palibe zimene akanacita. (Mac. 23:12-35) Bwanamkubwa tsopano anali Fesito m’malo mwa Felike. Popeza Fesito ‘anafuna kuti Ayudawo amukonde,’ anafunsa Paulo kuti: “Kodi ukufuna kupita ku Yerusalemu, kuti nkhani imeneyi ikaweluzidwe kumeneko pamaso panga?” Paulo anadziŵa zakuti akapita ku Yerusalemu akhoza kukaphedwa. Conco iye anati: “Ndikupempha kuti ndikaonekele kwa Kaisara!” Fesito anauza Paulo kuti: “Popeza kuti wapempha kukaonekela kwa Kaisara, udzapitadi kwa Kaisara.” Posapita nthawi, Paulo anafika ku Roma, kutali na Ayuda amene anali kufuna kumupha.—Mac. 25:6-12. w20.11 13 ¶4; 14 ¶8-10
Cisanu, January 21
Mitima yathu ingatitsutse. —1 Yoh. 3:20.
Tonsefe timadziimba mlandu nthawi zina. Mwacitsanzo, ena amadziimba mlandu pa zoipa zimene anacita asanaphunzile coonadi. (Aroma 3:23) Timafuna kucita zoyenela, koma “tonsefe timapunthwa nthawi zambili.” (Yak. 3:2; Aroma 7:21-23) Koma ngakhale kuti kudziimba mlandu si cinthu cokondweletsa, kungakhaleko na ubwino wake. Cifukwa ciani? Kungatilimbikitse kuwongolela njila zathu, na kusafuna kudzabwelezanso zolakwazo. (Aheb. 12:12, 13) Komabe, zingatheke kudziimba mlandu mopitilila malile—kutanthauza kumadziimbabe mlandu ngakhale pambuyo pakuti talapa ndipo Yehova waonetsa kuti watikhululukila. Kudziimba mlandu koteloko n’kovulaza. (Sal. 31:10; 38:3, 4) Tifunika kudziteteza ku msampha wodziimba mlandu mopitilila malile. Tangoganizani mmene Satana angakondwele ngati tingayambe kuganiza kuti ndine wolephela ndipo Yehova ananifulatila kale, pamene iye Yehova anatikhululukila.—Yelekezelani na 2 Akorinto 2:5-7, 11. w20.11 27 ¶12-13
Ciŵelu, January 22
Ndithudi, ndayeletsa mtima wanga pacabe, ndipo ndasamba m’manja mwanga pacabe posonyeza kuti ndine wopanda colakwa.—Sal. 73:13.
Amene analemba Salimo 73 anali Mlevi. Conco iye anali na mwayi wapadela wotumikila pamalo a Yehova olambilila. Ngakhale n’conco, iye analefuka panthawi ina mu umoyo wake. Cifukwa ciani? Anayamba kucitila kaduka anthu oipa, komanso odzikuza, osati cifukwa ca zoipa zimene anali kucita, koma cifukwa cakuti anali kuoneka kuti zinthu zikuwayendela bwino. (Sal. 73:2-9, 11-14) Iwo anali kuoneka kuti ali na zonse, cuma, umoyo wabwino, komanso wopanda nkhawa. Mlevi anayenela kuona zinthu mmene Yehova amazionela. Mwakucita zimenezi, anakhala pamtendele ndipo anakhalanso wacimwemwe. Iye anati: “Palibe wina wondisangalatsa padziko lapansi koma inu nokha [Yehova].” (Sal. 73:25) Mofananamo na ise tisamacitile kaduka anthu oipa amene angaoneke kuti zinthu zikuwayendela mu umoyo. Cimwemwe cawo si ceni-ceni, ndipo n’cakanthawi (Mlal. 8:12, 13) Kuwacitila kaduka kungatilefule, ndipo kungativulaze mwauzimu. Conco, ngati mwazindikila kuti mwayamba kucitila kaduka anthu oipa amene akuoneka kuti zinthu zikuwayendela, citani zimene Mlevi uja anacita. Mvelani malangizo a Mulungu acikondi na kugwilizana na anthu amene amacita cifunilo ca Mulungu. Ngati mumam’konda kwambili Yehova kuposa cina ciliconse, mudzapeza cimwemwe ceni-ceni. Ndipo mudzakhalabe panjila ya ku “moyo weniweniwo.”—1 Tim. 6:19. w20.12 19 ¶14-16
Sondo, January 23
Pakuti cimene tiyenela kupemphelela monga mmene tiyenela kupemphela sitikucidziŵa, koma mzimu umacondelela m’malo mwathu ndi madandaulo amene sitinathe kuwafotokoza.—Aroma 8:26.
Pamene mutulila Yehova nkhawa zanu m’pemphelo, muziphatikizamo mawu oyamikila. Tiyenela kuganizila za madalitso amene tili nawo, ngakhale pamene zinthu n’zovuta kwambili. Ngati nthawi zina mumasowa mawu oyenelela pofotokoza nkhawa zanu, kumbukilani kuti Yehova amayankha mapemphelo ngakhale a mawu ocepa akuti ‘Conde n’thandizeni!’ (2 Mbiri 18:31) Dalilani nzelu za Yehova osati zanu. Kalekale, ca m’ma 700 B.C.E., Ayuda anacita mantha atamva kuti Asuri adzawaukila. Cifukwa ca nkhawa yakuti adzagonjetsedwa na Asuri, iwo anapempha Aiguputo kuti awathandize. (Yes. 30:1, 2) Yehova anawacenjeza kuti kudalila Aiguputo kudzawabweletsela mavuto aakulu. (Yes. 30:7, 12, 13) Kupitila mwa mneneli Yesaya, Yehova anauza anthuwo mmene akanapezela citetezo ceni-ceni. Mneneliyo anati: “Mudzakhala amphamvu mukakhala osatekeseka ndi acikhulupililo” mwa Yehova.—Yes. 30:15b. w21.01 3-4 ¶8-9
Mande, January 24
Ndinamva ciwelengelo ca amene anadindidwa cidindo, anthu okwana 144,000.—Chiv. 7:4.
Abale a Khristu adzakhala mafumu ndi ansembe pamodzi naye kumwamba, monga mphoto ya kukhulupilika kwawo. (Chiv. 20:6) Onse amene amapanga gawo lakumwamba la banja la Mulungu, adzakondwela kwambili kuona odzozedwa a 144,000 akulandila mphoto yawo kumwamba. Mtumwi Yohane atafotokoza za mafumu na ansembe 144,000 amenewa, anaona cina cocititsa cidwi, “khamu lalikulu” limene linapulumuka Aramagedo. Mosiyana na gulu loyamba, gulu laciŵili limeneli ni lalikulu ndipo lilibe ciŵelengelo coikika. (Chiv. 7:9, 10) Iwo ‘anavala mikanjo yoyela,’ kuonetsa kuti ni ‘opanda banga’ locokela m’dziko la Satana, ndipo akhalabe okhulupilika kwa Mulungu komanso kwa Khristu. (Yak. 1:27) Iwo anali kufuula kuti anapulumutsidwa cifukwa ca zimene Yehova na Yesu, Mwanawankhosa wa Mulungu anawacitila. Cina, iwo ananyamula nthambi za kanjedza m’manja mwawo, kuonetsa kuti mwacimwemwe amavomeleza Yesu kukhala Mfumu yosankhidwa na Yehova.—Yelekezelani na Yohane 12:12, 13. w21.01 15-16 ¶6-7
Ciŵili, January 25
Kudzicepetsa kwanu n’kumene kumandikweza.—2 Sam. 22:36.
Mwamuna angakhale mutu wa banja wabwino mwa kutengela citsanzo ca Yehova na Yesu ca mmene amaseŵenzetsela umutu wawo. Mwacitsanzo, ganizilani za khalidwe la kudzicepetsa. Yehova ni wanzelu kwambili kuposa wina aliyense. Ngakhale n’telo, amamvetsela malingalilo a atumiki ake. (Gen. 18:23, 24, 32) Yehova ni wangwilo, koma sayembekezela kuti ife tizicita zinthu mwangwilo. M’malomwake, amathandiza anthu opanda ungwilo amene amam’tumikila kuti zinthu ziziwayendela bwino. (Sal. 113:6, 7) Ndipo Baibo imafotokoza Yehova kuti ni “mthandizi.” (Sal. 27:9; Aheb. 13:6) Mfumu Davide anazindikila kuti angakwanitse kugwila nchito yaikulu imene anapatsidwa, cabe cifukwa ca kudzicepetsa kwa Yehova. Ganizilani citsanzo ca Yesu. Ngakhale kuti anali Mphunzitsi komanso Mbuye wa ophunzila ake, anasambitsa mapazi awo. Yesu iye mwini anati: “Ndakupatsani citsanzo kuti mmene ine ndacitila kwa inu, inunso muzicita cimodzimodzi.” (Yoh. 13:12-17) Ngakhale kuti Yesu anali na ulamulilo waukulu, sanayembekezele kutumikilidwa. M’malomwake, anali kutumikila ena.—Mat. 20:28. w21.02 3-4 ¶8-10
Citatu, January 26
Kukongola kwa anyamata ndiko mphamvu zawo.—Miy. 20:29.
Imwe abale acinyamata, mungacite zambili mumpingo. Ambili a imwe muli na nyonga komanso mphamvu. Ndimwe ofunika kwambili mumpingo mwanu. Mwina mukuyembekezela mwacidwi nthawi pamene mudzaikidwa kukhala mtumiki wothandiza. Komabe, mwina mungamaganize kuti ena amakuonani kuti ndinu wamng’ono kwambili, kapena simudziŵa zambili moti sangakupatseni nchito zofunika. Ngakhale kuti ndinu wamng’ono, pali zinthu zimene mungacite palipano kuti abale na alongo mumpingo mwanu azikudalilani na kukulemekezani. Imwe abale acinyamata, kodi muli na maluso amene angakhale othandiza kwa ena mumpingo? Ambili a imwe muli nawo. Mwacitsanzo, acikulile ambili amayamikila kuwaonetsa mmene angaseŵenzetsele matabuleti komanso zipangizo zina pocita phunzilo laumwini na misonkhano. Cidziŵitso canu poseŵenzetsa zipangizo zimenezi cingakhale cothandiza kwambili kwa acikulile. Pa zilizonse zimene mucita, muzikondweletsa Atate wanu wakumwamba. w21.03 2 ¶1, 3; 7 ¶18
Cinayi, January 27
Pakuti aliyense ayenela kunyamula katundu wake.—Agal. 6:5.
Ngakhale kuti mkazi ni wophunzila kwambili kuposa mwamuna wake, ni udindo wa mwamuna wake kutsogolela pa kulambila kwa pabanja komanso pa zocitika zina zauzimu.(Aef. 6:4) Mkazi amafunika kugonjela mwamuna wake, koma amafunikanso kulimbitsa cikhulupililo cake payekha. Conco, afunika kupatula nthawi yocita phunzilo laumwini na kusinkha-sinkha. Kucita zimenezi kudzam’thandiza kukonda Yehova na kumulemekeza, komanso kupeza cimwemwe pamene agonjela mwamuna wake. Akazi amene amagonjela amuna awo cifukwa cokonda Yehova, amapeza cimwemwe coculuka komanso amakhala okhutila kuposa aja amene amakana dongosolo la Yehova la umutu. Iwo amapeleka citsanzo cabwino kwa anyamata na atsikana. Amathandizanso kuti m’banja na mu mpingo, mukhale cikondi na mtendele. (Tito 2:3-5) Masiku ano, atumiki a Yehova okhulupilika ambili ni akazi.—Sal. 68:11. w21.02 13 ¶21-23
Cisanu, January 28
Yandikilani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikilani.—Yak 4:8.
Mtumwi Paulo anapeleka citsanzo cabwino zedi pankhani ya kulimba mtima na kupilila. Inde, nthawi zina anali kulefuka. Koma anakwanitsa kupilila cifukwa anadalila Yehova kuti am’patse mphamvu zofunikila. (2 Akor. 12:8-10; Afil. 4:13) Nafenso tingakhale amphamvu komanso olimba mtima ngati modzicepetsa tizindikila kuti timafunikila thandizo la Yehova. (Yak. 4:10). Tizikhala otsimikiza kuti mayeso amene timakumana nawo si cilango cocokela kwa Yehova. Yakobo akutitsimikizila kuti: “Munthu akakhala pa mayeselo asamanene kuti: ‘Mulungu akundiyesa.’ Pakuti Mulungu sangayesedwe ndi zinthu zoipa ndipo iye sayesa munthu ndi zinthu zoipa.” (Yak. 1:13) Tikatsimikizila kuti mfundo imeneyi ni ya zoona, timayandikana kwambili na Atate wathu wacikondi wakumwambaYehova “sasintha.” (Yak. 1:17) Anathandiza Akhristu oyambilila pa mayeso awo, ndipo adzathandizanso aliyense wa ife masiku ano. Pemphani Yehova mocokela pansi pamtima kuti akupatseni nzelu, cikhulupililo, na kulimba mtima. Iye adzayankha mapemphelo anu. w21.02 31 ¶19-21
Ciŵelu, January 29
Citsulo cimanola citsulo cinzake. Momwemonso munthu amanola munthu mnzake.—Miy. 27:17.
Pangani ubwenzi na wophunzilayo. Pamene wophunzilayo apitiliza kubwela kumisonkhano, pitilizani kumuonetsa cidwi. (Afil. 2:4) Popanda kuloŵelela nkhani zake zaumwini, mungamuyamikile pa masinthidwe amene wapanga, na kumufunsa za mmene phunzilo la Baibo likuyendela, za banja lake komanso nchito yake. Kukambilana zimenezi kudzakuthandizani kuti muyambe kugwilizana kwambili. Ngati mwakhala bwenzi la wophunzilayo, mudzam’thandiza kupita patsogolo kuti akabatizike. Pamene wophunzila apita patsogolo na kupanga masinthidwe, m’thandizeni kumva kuti ni wofunika mumpingo. Mungacite zimenezi mwa kukhala woceleza. (Aheb. 13:2) Wophunzila Baibo akayenelela kukhala wofalitsa, mungam’pemphe kupita naye mu ulaliki. M’bale Diego wa ku Brazil anakamba kuti: “Abale ambili anali kunipempha kuti nipite nawo mu ulaliki. Imeneyi inali njila yabwino yakuti niŵadziwe bwino. Pamene n’naŵadziŵa bwino, n’naphunzila zambili, ndipo n’namvela kuti nili pafupi kwambili na Yehova na Yesu.” w21.03 12 ¶15-16
Sondo, January 30
Musabwezele coipa pa coipa. —Aroma 12:17.
Yesu anauza otsatila ake kukonda adani awo. (Mat. 5:44, 45) Kodi kucita zimenezi n’kopepuka? Kutalitali! Koma n’zotheka na thandizo la mzimu woyela wa Mulungu. Makhalidwe amene mzimu wa Mulungu umabala ndiwo cikondi, komanso kuleza mtima, ubwino, kufatsa, komanso kudziletsa. (Agal. 5:22, 23) Makhalidwe amenewa amatithandiza kupilila cidani. Anthu ambili amene anali otsutsa anasintha mitima yawo cifukwa cakuti mwamuna, mkazi, mwana, kapena munthu wokhala naye pafupi anaonetsa makhalidwe aumulungu amenewa. Ambili a iwo akhala abale na alongo athu. Conco ngati zimakuvutani kukonda anthu amene amakuzondani, cabe cifukwa cakuti mumatumikila Yehova, pemphani mzimu woyela. (Luka 11:13) Ndipo khalani na cikhulupililo cakuti kumvela Mulungu, nthawi zonse kumakhala kopindulitsa. (Miy. 3:5-7) Cidani cingakhale cacikulu komanso coŵaŵa, koma cikondi n’camphamvu koposa. Cimakopa mtima. Komanso cimakondweletsa mtima wa Yehova. Koma ngakhale otsutsa apitilize kutizonda, tingakhalebe acimwemwe. w21.03 23 ¶13; 24 ¶15, 17
Mande, January 31
Pali mtundu umene waloŵa m’dziko langa. Mtunduwo ndi wamphamvu ndipo anthu ake ndi osaŵelengeka.—Yow. 1:6.
Mneneli Yoweli anali kulosela za kuukila kwa gulu la asilikali. (Yow. 2:1, 8, 11) Yehova anakamba kuti adzaseŵenzetsa ‘gulu lake lankhondo lamphamvu’ (asilikali a Babulo) popeleka cilango kwa Aisiraeli osamvela. (Yow. 2:25) M’pake kuti gulu limeneli la asilikali oukila likuchedwa “mdani wa kumpoto,” cifukwa asilikali a Babulo anali kudzaukila Aisiraeli kucokela kumpoto. (Yow. 2:20) Gulu la asilikali limeneli likuyelekezeledwa na gulu la dzombe locita zinthu mwadongosolo. Pokamba za asilikaliwo, Yoweli anati: “[Msilikali aliyense] wamphamvu . . . akuyenda panjila yake. . . . Iwo amathamangila m’mizinda . . . Amakwela nyumba ndipo amalowa m’nyumbamo kudzela pawindo ngati mbala.” (Yow. 2:8, 9) Yelekezelani kuti mukuona mmene zinthu zinalili pa nthawiyo! Asilikali ali pali ponse. Palibe pamene munthu angabisale. Palibe amene angapulumuke ku lupanga la asilikali a Babulo. Monga dzombe, Ababulo (kapena kuti Akasidi) anaukila mzinda wa Yerusalemu mu 607 B.C.E. Baibo imati: “Mfumu ya Akasidi . . . sinacitile cisoni mnyamata kapena namwali, wacikulile kapena nkhalamba yothelatu. 2 Mbiri 36:17. w20.04 5 ¶11-12