February
Ciŵili, February 1
Modzicepetsa, [muziona] ena kukhala okuposani.—Afil. 2:3.
Adziŵeni bwino abale na alongo anu. Muzicezako nawo misonkhano ikalibe kuyamba komanso ikatha, muziyenda nawo mu ulaliki, ndipo ngati n’zotheka mungawaitanileko ku cakudya. Mukatelo, mungazindikile kuti mlongo uja amene mumamuona ngati si waubwenzi, kweni-kweni ni wamanyazi cabe, ndipo m’bale wa ndalama zambili uja si wokonda cuma, koma kweni-kweni ni wowoloŵa manja. Kapenanso mungazindikile kuti banja limene limakonda kubwela mocedwa ku misonkhano likukumana na citsutso. (Yobu 6:29) N’zoona kuti sitiyenela ‘kulowelela nkhani za eni.’ (1 Tim. 5:13) Komabe, ni bwino kuwadziŵa bwino abale na alongo athu, komanso kudziŵa zimene akukumana nazo. Tikatelo, tidzatha kuwamvetsetsa. Mukayesetsa kum’dziŵa bwino m’bale kapena mlongo amene zocita zake sizikukondweletsani, mudzakwanitsa kumumvetsetsa. Pamafunika khama kuti tiwadziŵe bwino abale athu. Ndipo tikayesetsa kufutukula mtima wathu potsatila malangizo a m’Baibo, ndiye kuti tikutengela Yehova amene amakonda “anthu, kaya akhale a mtundu wotani.”—1 Tim. 2:3, 4; 2 Akor. 6:11-13. w20.04 16-17 ¶10-12
Citatu, February 2
Palibe amene ali ndi cikondi cacikulu kuposa ca munthu amene wapeleka moyo wake cifukwa ca mabwenzi ake.—Yoh. 15:13.
Usiku wakuti aphedwa maŵa, Yesu anakumbutsa ophunzila ake kuti azikondana. Iye anadziŵa kuti cikondi codzimana, cidzawathandiza kukhalabe ogwilizana komanso kupilila cidani ca dzikoli. Ganizilani citsanzo ca mpingo wa ku Tesalonika. Kucokela pamene unakhazikitsidwa, abale na alongo mumpingowo anali kuzunzidwa. Ngakhale n’telo, iwo anakhala zitsanzo zabwino pa nkhani ya kukhulupilika na cikondi. (1 Ates. 1:3, 6, 7) Paulo anawalimbikitsa kupitiliza kuonetsa cikondi “mowonjezeleka.” (1 Ates. 4:9, 10) Cikondi cinali kuwasonkhezela kulimbikitsa anthu opsinjika maganizo komanso kucilikiza ofooka. (1 Ates. 5:14) Iwo anatsatila malangizo a Paulo, cifukwa m’kalata yake yaciŵili imene analemba patapita pafupi-fupi caka cimodzi, Paulo ponena za iwo anati: “Cikondi ca aliyense wa inu kwa mnzake cikuwilikiza.” (2 Ates. 1:3-5) Cikondi cawo cinawathandiza kupilila mazunzo na mavuto ena. w21.03 22 ¶11
Cinayi, February 3
Tithamange mopilila mpikisano umene atiikilawu. —Aheb. 12:1.
Kuti tikalandile mphoto ya moyo wosatha, tifunika kuyenda pa njila ya coonadi. (Mac. 20:24; 1 Pet. 2:21) Komabe, Satana na otsatila ake amafuna kuti tileke kuyenda pa njila imeneyi. Amafuna kuti tipitilize “kuthamanga nawo limodzi m’cithaphwi ca makhalidwe oipa.” (1 Pet. 4:4) Iwo amatinyodola cifukwa coyenda pa njila ya coonadi. Amakamba kuti njila imene iwo akuyendamo ndiyo yabwino, yopatsa ufulu. Koma limenelo ni bodza. (2 Pet. 2:19) Apa tingaone kuti kusankha njila yoyenela n’kofunika kwambili. Satana amafuna kuti tonse ticoke pa njila yopapatiza ‘yoloŵela ku moyo,’ n’kuyamba kuthamanga m’njila yaikulu ndi yotakasuka imene anthu ambili m’dzikoli akuthamangamo. Anthu ambili amaona kuti njila imeneyi ndiyo yabwino komanso yosavuta kuyendamo. Koma m’ceni-ceni, njilayi ni yopita “kuciwonongeko.” (Mat. 7:13, 14) Kuti tisapatuke pa njila yoyenela, tifunika kudalila Yehova na kumumvela. w20.04 26 ¶1; 27 ¶5, 7
Cisanu, February 4
Ndikucondelela nonse kuti muzipeleka mapembedzelo kwa Mulungu, muzipeleka mapemphelo, muzipemphelelana . . . kuti tikhale ndi moyo wabata ndi wamtendele, ndiponso kuti tikhale odzipeleka kwa Mulungu mokwanila. —1 Tim. 2:1, 2.
M’zaka zaposacedwa, nalonso boma la Russia na maiko ogwilizana nalo aloŵa “m’Dziko Lokongola.” (Dan. 11:41) Motani? Mu 2017, mfumu ya kumpoto yatsopano imeneyi inaletsa nchito ya Mboni za Yehova m’dzikolo, ndiponso inaponya m’ndende ena mwa abale na alongo athu. Bomali linaletsanso mabuku athu, kuphatikizapo Baibulo la Dziko Latsopano. Kuwonjezela apo, linalanda ofesi yathu ya nthambi ya m’dzikolo, Nyumba zina za Ufumu, na Mabwalo ena a Misonkhano. Izi zitacitika, mu 2018 Bungwe Lolamulila linaona kuti Russia na maiko ogwilizana naye ndiwo mfumu ya kumpoto. Koma ngakhale anthu a Yehova azunzidwe bwanji na boma, iwo salimbana nalo kapena kuyesa kusintha ulamulilo. M’malomwake, amatsatila malangizo a m’Baibo akuti tiyenela kupemphelela “anthu onse apamwamba,” maka-maka ngati akupanga zosankha zimene zingakhudze ufulu wa kulambila. w20.05 14 ¶9.
Ciŵelu, February 5
Nthawi zonse uzisamala ndi zimene umacita komanso zimene umaphunzitsa. —1 Tim. 4:16.
Makolo, kuti ana anu akhulupilile kuti zimene amaphunzila ni coonadi.afunika kupanga ubale wawo-wawo na Mulungu komanso kukhulupilila kuti zimene Baibo imaphunzitsa n’zoona. Kuti muphunzitse ana anu coonadi ponena za Mulungu, mufunika kukhala citsanzo cabwino pa nkhani yoŵelenga Baibo mwakhama. Mufunikanso kukhala na nthawi yosinkha-sinkha pa zimene aŵelengazo. Mukatelo, mudzakwanitsa kuthandiza ana anu kuti nawonso azicita zimenezi. Mufunika kuphunzitsa ana anu kuseŵenzetsa zida zathu zofufuzila, monga mmene mumathandizila maphunzilo anu a Baibo. Mwa kucita zimenezi, mudzathandiza anawo kukonda Yehova na kukhulupilila kapolo wokhulupilika ndi wanzelu, amene iye amamuseŵenzetsa potipatsa cakudya cauzimu. (Mat. 24:45-47) Musamangowaphunzitsa cabe mfundo zoyambilila za m’Baibo ana anu. Athandizeni kukhala na cikhulupililo colimba mwa kuwaphunzitsa “zinthu zozama za Mulungu,” kulingana na zaka zawo komanso luso lawo lomvetsa zinthu.—1 Akor. 2:10. w20.07 11 ¶10, 12-13
Sondo, February 6
Pakuti munthu wocita zaciphamaso Yehova amanyansidwa naye, koma amakonda anthu owongoka mtima.—Miy. 3:32.
Masiku ano, anthu mamiliyoni ali pa ubwenzi wolimba na Yehova. Zimakhala zotheka kwa ife kukhala pa ubwenzi na Yehova cifukwa cokhulupilila nsembe ya dipo la Yesu. Cifukwa ca dipo limeneli, Yehova amatilola kudzipatulila kwa iye na kubatizika. Tikacita zinthu zofunika zimenezi, timaloŵa m’gulu la Akhristu mamiliyoni odzipatulila komanso obatizika, amene ali pa ubwenzi wolimba na Yehova, Mulungu wamkulu-kulu m’cilengedwe conse! Tingaonetse bwanji kuti timaona kuti ubwenzi wathu na Mulungu ni wamtengo wapatali? Abulahamu na Yobu anakhalabe okhulupilika kwa Mulungu kwa zaka zoposa 100. Nafenso tifunika kukhalabe okhulupilika olo kuti tatumikila Yehova kwa nthawi yaitali m’dziko loipali. Mofanana na Danieli, tifunika kuona ubwenzi wathu na Mulungu kukhala wofunika kwambili kuposa moyo wathu. (Dan. 6:7, 10, 16, 22) Ndi thandizo la Yehova, tingathe kupilila mayeselo alionse amene tingakumane nawo n’kukhalabe pa ubwenzi wolimba na iye.—Afil. 4:13. w20.05 27 ¶5-6
Mande, February 7
Ndipatseni mtima wosagawanika.—Sal. 86:11.
Mfumu Davide anaona mkazi wa munthu wina akusamba. Iye anali kulidziŵa lamulo la Yehova lakuti, “Usalakelake mkazi wa mnzako.” (Eks. 20:17) Olo zinali conco, cioneka kuti anapitiliza kuyang’ana mkaziyo moti mtima wake unagaŵanika. Iye anali kulaka-laka mkazi uja Bati-seba, ndipo pa nthawi imodzi-modziyo anali kufuna kukondweletsa Yehova. Ngakhale kuti kwa nthawi yaitali Davide anali kukonda Yehova na kumuopa, panthawiyi anagonja ku cilako-lako cadyela, ndipo anacita zinthu zoipa kwambili. Iye anabweletsa citonzo pa dzina la Yehova. Komanso, anabweletsa mavuto aakulu kwa anthu osalakwa, kuphatikizapo a m’banja lake. (2 Sam. 11:1-5, 14-17; 12:7-12) Yehova anathandiza Davide kuzindikila kuti chimo limene anacita linali lalikulu, ndipo iye analapa moti anakhalanso pa ubale wabwino na Yehova. (2 Sam. 12:13; Sal. 51:2-4, 17) Davide anali kukumbukila mavuto amene anakumana nawo cifukwa colola mtima wake kukhala wogaŵanika. Kodi Yehova anam’thandiza Davide kukhalanso na mtima wosagaŵanika, kapena kuti wathunthu? Inde anamuthandiza. Tikutelo cifukwa patapita nthawi, Yehova anakamba kuti Davide anatumikila “Yehova Mulungu wake ndi mtima wathunthu.”—1 Maf. 11:4; 15:3. w20.06 11 ¶12-13
Ciŵili, February 8
Ndinali kuwakoka . . . . ndi zingwe zacikondi.—Hos. 11:4, mawu amunsi.
Baibo imayelekezela cikondi ca Yehova pa anthu ake na cingwe, kapena kuti nthambo. Kodi cikondi ca Mulungu cili ngati cingwe m’njila yotani? Cabwino, tiyeni tiyelekezele motele: Tikambe kuti mwagwela mu cimgodi conoka, ndipo mukulephela kutulukamo. Kuti mutulukemo, pafunika munthu wina amene angakuponyeleni nthambo na kukudonselani kunja. Malinga na zimene Yehova anakamba mu lemba lalelo, mwacikondi anali “kuwakoka” Aisiraeli amene anasocela. Mulungu amamvelanso cimodzi-modzi akaganizila za anthu amene analeka kum’tumikila, ndipo akusautsika na mavuto komanso nkhawa za pa umoyo. Zili monga kuti iwo ali m’cimgodi conoka. Yehova amafuna kuti iwo adziŵe kuti iye amawakonda. Amafunanso kuwakoka kuti abwelele kwa iye. Ndipo iye angaseŵenzetse imwe poonetsa cikondi cake pa iwo. Tifunika kutsimikizila ozilala kuti Yehova amawakonda ndiponso kuti nafenso timawakonda. w20.06 27 ¶12-13
Citatu, February 9
Wodala ndi munthu wopilila mayeselo.—Yak. 1:12.
Pamene wophunzila Sitefano anaphedwa, Akhristu ambili anathaŵa mu Yerusalemu ndipo “anabalalikila m’zigawo za Yudeya ndi Samariya,” mpaka kukafika kumadela akutali a Kupuro na Antiokeya. (Mac. 7:58–8:1; 11:19) Ophunzila amenewa anakumana na mavuto ambili. Ngakhale n’telo, iwo anapitiliza kulalikila uthenga wabwino mwakhama kulikonse kumene anapita, ndipo mipingo inakhazikitsidwa mu Ufumu wonse wa Roma. (1 Pet. 1:1) Koma Akhristu oyambilila amenewo, anali kudzakumananso na mavuto ena aakulu kutsogolo. Mwacitsanzo, ca mu 50 C.E., Mfumu ya Roma dzina lake Kalaudiyo analamula kuti Ayuda onse acoke m’dziko la Roma. Conco Ayuda amene anakhala Akhristu anakakamizika kusiya nyumba zawo na kukakhala kwina. (Mac. 18:1-3) Ca mu 61 C.E., mtumwi Paulo analemba kuti Akhristu anzake anali kunyozedwa pamaso pa anthu, kuponyedwa m’ndende, komanso kulandidwa zinthu zawo. (Aheb. 10:32-34) Ndipo mofanana na anthu ena, Akhristuwo anali kuvutika na umphawi komanso matenda.—Aroma 15:26; Afil. 2:25-27. w21.02 26-27 ¶2-4
Cinayi, February 10
Mdyerekezi watsikila kwa inu, ndipo ali ndi mkwiyo waukulu podziwa kuti wangotsala ndi kanthawi kocepa.—Chiv. 12:12.
Palibe cimene Satana na onse amene ali ku mbali yake angacite, comwe cingatilepheletse kuyendabe m’coonadi. (2 Yoh. 8, 9) Tifunika kuyembekezela kuzondewa na dzikoli. (1 Yoh. 3:13) Yohane anatikumbutsa kuti “dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.” (1 Yoh. 5:19) Pamene tikuyandikila mapeto a dzikoli, mkwiyo wa Satana ukukulila-kulila. Kuwonjezela potiukila mwacinyengo, monga kutikopa kuti ticite ciwelewele kapena kufalitsa mabodza kupitila mwa anthu ampatuko, Satana amatiukilanso mwacindunji. Mwacitsanzo, amasonkhezela adani athu kuti azitizunza mwankhanza. Iye adziŵa kuti wangotsala na nthawi yocepa yoti aletse nchito yathu yolalikila, kapena yoti awononge cikhulupililo cathu. Telo n’zosadabwitsa kuti m’maiko ena, nchito yathu ni yoletsedwa, ndipo m’maiko enanso abale athu alibe ufulu wokwanila wa kulambila. Ngakhale n’conco, abale na alongo athu m’maiko amenewo akupilila. Uwu ni umboni wakuti olo Satana atayesa bwanji kulimbana nafe, tingakwanitse kukhalabe okhulupilika. w20.07 24 ¶12-13
Cisanu, February 11
Mphatso imene Mulungu amapeleka ndi moyo wosatha kudzela mwa Khristu Yesu Ambuye wathu. —Aroma 6:23.
Colinga ca Yehova cinali cakuti anthu akhale na moyo wamuyaya m’dziko lokongola limene iye analenga. Koma pamene Adamu na Hava anapandukila Atate wawo wacikondi, ucimo na imfa zinaloŵa m’dziko. (Aroma 5:12) Kodi Yehova anacita ciani? Nthawi yomweyo, iye anakambilatu zimene adzacita kuti apulumutse mtundu wa anthu. (Gen. 3:15) Yehova anakonza zakuti adzapeleke dipo n’colinga cakuti ana a Adamu na Hava amasuke ku ucimo na imfa. Ndiyeno anapatsa munthu aliyense mwayi wosankha kumutumikila kuti akapeze moyo wosatha. (Yoh. 3:16; 1 Akor. 15:21, 22) Yehova kupitila mwa Mwana wake, adzaukitsa anthu mamiliyoni ambili. Cioneka kuti akufawo sadzaukitsidwa panthawi imodzi. N’cifukwa ciani takamba conco? Cifukwa ngati onse adzaukitsidwa pa nthawi imodzi, mwina padziko lapansi pangadzakhale cipwilikiti. Koma Yehova sacita zinthu mopanda dongosolo. Iye adziŵa kuti dongosolo n’lofunika kuti anthu apitilize kukhala mwamtendele.—1 Akor. 14:33. w20.08 14 ¶3; 15 ¶5
Ciŵelu, February 12
Uzisamala ndi zimene umacita komanso zimene umaphunzitsa.—1 Tim. 4:16.
Wophunzila ayenela kumvetsa kuti colinga ni kum’thandiza kuti akayambe kutumikila Yehova monga Mboni yake. Sitepu na sitepu, wophunzila Baibo woona mtima angakwanilitse colinga cake ca kubatizika! Coyamba, wophunzilayo amafika pom’dziŵa Yehova, kum’konda na kukhulupilila mwa iye. (Yoh. 3:16; 17:3) Kenako amayamba kupanga ubwenzi wolimba na Yehova, na kugwilizana kwambili na mpingo. (Aheb. 10:24,25; Yak. 4:8) Pothela pake wophunzilayo amalekelatu makhalidwe onse oipa, na kulapa macimo ake. (Mac. 3:19) Panthawiyo, cikhulupililo cake cimam’limbikitsa kuuzako ena mfundo za coonadi. (2 Akor. 4:13) M’kupita kwa nthawi amadzipatulila kwa Yehova, pambuyo pake n’kubatizika kuonetsa umboni wakuti anadzipatulila. (1 Pet. 3:21; 4:2) Ndipo limakhala tsiku lokondweletsa cotani nanga kwa tonsefe! Conco, pamene wophunzila wanu akutenga sitepu iliyonse yotsogolela ku colinga cake, muzimuyamikila mocokela pansi pamtima, na kum’limbikitsa kupitabe patsogolo. w20.10 17-18 ¶12-13
Sondo, February 13
Ngati phazi linganene kuti: “Popeza sindine dzanja, sindili mbali ya thupi,” cimeneco si cifukwa copangitsa phazi kusakhala mbali ya thup.—1 Akor. 12:15.
Ngati muyesa kudzilinganiza na ena mu mpingo, mudzayamba kudziona kuti ndinu wosafunika. Ena mu mpingo angakhale aphunzitsi aluso, adongosolo, kapena abusa aluso polimbikitsa ena. Mwina mumaona kuti imwe simungafike pa mlingo umenewo. Kumeneko kungakhale kudzicepetsa. (Afil. 2:3) Koma samalani. Ngati nthawi zonse mumadziyelekezela ndi ena amene ali na maluso kuposa imwe, mungakhumudwe na kulefuka. Mungafike poona kuti ndimwe osafunikila mu mpingo, monga taonela m’citsanzo ca Paulo. Yehova anapeleka mphatso zozizwitsa za mzimu woyela kwa Akhristu ena a m’nthawi ya atumwi. Koma sikuti Akhristu onse analandila mphatso zofanana ayi. (1 Ako. 12:4-11) Koma aliyense wa iwo anali wofunika. Lelolino, sitilandila mphatso zozizwitsa za mzimu woyela. Ndipo monga zinalili kalelo, masiku anonso tingakhale na maluso osiyana-siyana, koma tonsefe ndife ofunika kwa Yehova. w20.08 23 ¶13-15
Mande, February 14
Yehova ali kumbali yanga, sindidzaopa.—Sal. 118:6.
Mukapemphela kwa Yehova kuti akuthandizeni kukhala wolimba mtima. Yehova adzayankha mapemphelo anu ndipo sadzakusiyani olo pang’ono. (Mac. 4:29, 31) Iye ni wokonzeka nthawi zonse kukuthandizani. Muyenelanso kuganizila mmene iye anakuthandizilani kulimbana na mavuto enaake ndiponso mmene anakuthandizilani kusintha khalidwe lanu. Musakayikile kuti Mulungu, amene anapulumutsa anthu ake pa Nyanja Yofiila angakuthandizeni kukhala wophunzila wa Khristu. (Eks. 14:13) Khalani na cikhulupililo monga cimene wamasalimo wina amene anakamba mawu a mu lemba la lelo anali naco. Yehova angathandizenso ofalitsa atsopano kukhala olimba mtima. Ganizilaninso citsanzo ca mlongo Tomoyo. Atafika pa nyumba yoyamba patsiku limene anayamba kulalikila ku nyumba na nyumba, mwininyumba anamukalipila amvekele: “Sinifuna kukamba na a Mboni za Yehova!” Kenako anatseka citseko mwamphamvu. Tomoyo sanaope, koma anauza mlongo amene anali naye kuti: “Mwamvela zimene akamba? Sin’nakambe ciliconse, koma adziŵa kuti ndine Mboni ya Yehova. Namvela bwino ngako!” Tsopano mlongo Tomoyo akutumikila monga mpainiya wanthawi zonse. w20.09 6 ¶13-14
Ciŵili, February 15
Asa anacita zabwino ndi zoyenela pamaso pa Yehova Mulungu wake.—2 Mbiri 14:2.
Asa anauza Ayuda kuti Yehova ndiye ‘anawapatsa mpumulo pakati pa adani awo onse owazungulila.’ (2 Mbiri. 14:6, 7) Koma iye sanaone kuti nthawi ya mtendele imeneyo ni yofunika kungokhala phee osacita kalikonse. M’malomwake, anayamba kumanga mizinda, mipanda, nsanja, komanso makomo a zitseko ziŵili-ziŵili. Iye anauza Ayuda kuti: ‘Malo m’dzikoli akalipo.’ Kodi Asa anatanthauza ciani pamenepa? Anatanthauza kuti Ayuda anali na ufulu woyenda m’dziko limene Mulungu anawapatsa na kumanga popanda kuvutitsidwa na adani awo. Iye analimbikitsa anthuwo kuseŵenzetsa bwino nthawi ya mtendele imeneyo. Asa anaseŵenzetsanso nthawi ya mtendele imeneyo kuwonjezela mphamvu ya gulu lake lankhondo. (2 Mbiri 14:8) Kodi izi zitanthauza kuti iye sanali kudalila Yehova? Iyai. Koma anacita izi cifukwa anadziŵa kuti iye monga mfumu, anali na udindo wokonzekeletsa anthu ake kaamba ka mavuto obwela m’tsogolo. Asa anali kudziŵa kuti nthawi ya mtendele imene Ayuda anali kusangalala nayo siidzakhalitsa, ndipo ni mmenedi zinakhalila. w20.09 15 ¶4-5
Citatu, February 16
Musapitilile zinthu zolembedwa.—1 Akor. 4:6.
Na zolinga zabwino, mkulu angapange malamulo amene aona kuti adzateteza nkhosa za Mulungu. Komabe, pali mbali zosiyana kwambili pakati pa udindo wa mkulu, na uja wa mutu wa banja. Mwacitsanzo, Yehova anapatsa akulu udindo wokhala oweluza na kucotsa anthu osalapa mumpingo. (1 Akor. 5:11-13) Kumbali ina, Yehova anapatsa mitu ya mabanja ulamulilo umene akulu alibe. Mwacitsanzo, anapatsa mutu wa banja mphamvu zopanga malamulo m’banja mwake na kuonetsetsa kuti akutsatilidwa. (Aroma 7:2) Mutu wa banja alinso na ufulu woika nthawi imene ana ake ayenela kufika panyumba m’madzulo. Komanso, ali na mphamvu zopeleka cilango kwa ana ake ngati alephela kutsatila lamulo limenelo. (Aef. 6:1) Ndipo saiŵala kuti mwamuna amene ni mutu wa banja wacikondi, amafunsila kwa mkazi wake asanapange malamulo pa nyumba, cifukwa iwo ni “thupi limodzi.”—Mat. 19:6. w21.02 16-18 ¶10-13
Cinayi, February 17
[Nzelu] N’zamtengo wapatali kuposa miyala ya korali, ndipo zonse zimene umakonda sizingafanane nazo.—Miy. 3:15.
Palinso cifukwa cina cimene cimapangitsa coonadi ca m’Mawu a Mulungu kukhala camtengo wapatali. Cifukwa cake n’cakuti Yehova amaulula coonadi cimeneci kwa anthu okhawo odzicepetsa amene ali na “maganizo abwino.” (Mac. 13:48) Anthu odzicepetsa amenewa amakhulupilila kuti Yehova amaseŵenzetsa kapolo wokhulupilika ndi wanzelu potiphunzitsa coonadi masiku ano. (Mat. 11:25; 24:45) Pa ife tekha, sitingakwanitse kumvetsetsa coonadi, ndipo palibe cina camtengo wapatali kuposa kumvetsetsa coonadi. (Miy. 3:13) Yehova anatipatsanso mwayi wophunzitsako ena coonadi ponena za iye na colinga cake. (Mat. 24:14) Uthenga umene timalalikila ni wamtengo wapatali kwambili cifukwa umathandiza anthu kubwela m’banja la Yehova. Umawapatsanso mwayi wokapeza moyo wosatha. (1 Tim. 4:16) Conco, mosasamala kanthu za kuculuka kwa zimene timakwanitsa kucita mu ulaliki, timathandiza pa nchito yofunika kwambili imene ikucitika masiku ano. (1 Tim. 2:3, 4) Ni mwayi waukulu cotani nanga kukhala anchito anzake a Mulungu!—1 Akor. 3:9. w20.09 26-27 ¶4-5
Cisanu, February 18
Kumeneko tinapeza abale ndipo anaticondelela kuti tikhale nawo.—Mac. 28:14.
Pa ulendo wake wa ku Roma, mtumwi Paulo mobweleza-bweleza analandila thandizo limene Yehova anapeleka kupitila mwa Akhristu anzake. Mwacitsanzo, anzake a Paulo aŵili okhulupilika, Arisitako na Luka, anadzipeleka kuti apita naye limodzi ku Roma. Iwo anaika miyoyo yawo paciwopsezo kuti apelekeze Paulo, ngakhale kuti Baibo si ionetsa kuti Yesu nawonso anawapatsa citsimikizo cakuti adzafika bwino ku Roma. Pambuyo pake ali pa ulendo wowopsawo m’pamene anadziŵa kuti miyoyo yawo idzatetezeka. Atafika mu mzinda wa Sidoni, Yuliyo analola Paulo “kupita kwa mabwenzi ake kuti akamusamalile.” (Mac. 27:1-3) Ndipo atafika mu mzinda wa Potiyolo, Paulo na anzake ‘anapeza abale ndipo anawacondelela kuti akhale nawo masiku 7.’ Abale na alongo m’madela amenewo anasamalila Paulo na anzake pa zosoŵa zakuthupi. Ndipo omucelezawo ayenela kuti anakondwela kwambili, iye atawafotokozela zocitika zolimbikitsa.—Yelekezelani na Machitidwe 15:2, 3. w20.11 15-16 ¶15-17
Ciŵelu, February 19
[Kudzipeleka] kwa Mulungu . . . kumakhudza lonjezo la moyo uno ndi moyo umene ukubwelawo.—1 Tim. 4:8.
Kodi inu makolo oopa Mulungu mungaphunzile ciani kwa Yosefe na Mariya? Cofunika koposa, kuphunzitsa ana anu mwa mawu na zocita zanu, kuti mumam’konda kwambili Yehova. Dziŵani kuti mphatso yopambana imene mungapatse ana anu, ni kuwaphunzitsa kukonda Yehova. Ndipo cinthu cimodzi cofunika kwambili cimene mungawaphunzitse, ni mmene angakhalile na pulogilamu yokhazikika ya kuŵelenga, kupemphela, kupezeka pa misonkhano, komanso kutengako mbali mu ulaliki. (1 Tim. 6:6) Komabe, mufunikanso kupezela ana anu zinthu zakuthupi. (1 Tim. 5:8) Koma musaiŵale kuti cimene cidzathandiza ana anu kukapulumuka mapeto a dongosolo lino lakale, na kuloŵa m’dziko latsopano la Mulungu, ni ubale wawo wolimba na Yehova, osati zinthu zakuthupi. (Ezek. 7:19) N’zolimbikitsa kuona kuti makolo ambili acikhristu amapanga zosankha zabwino zauzimu zothandiza mabanja awo. Ana okulila m’mabanja otelo, nthawi zambili amakula na makhalidwe abwino, ndipo amakhala oyamikila kuti analeledwa mwa njila imeneyi.—Miy. 10:22. w20.10 28-29 ¶10-11
Sondo, February 20
Musalole kuti zimenezi zikucitikileni ngakhale pang’ono.—Mat. 16:22.
Nthawi zina mtumwi Petulo anakamba kapena kucita zinthu zimene anadziimba nazo mlandu pambuyo pake. Yesu atauza atumwi ake kuti adzavutika na kufa, Petulo anadzudzula Yesu mawu ali pamwambawa. (Mat. 16:21-23) Yesu anam’patsa uphungu Petulo. Cigulu ca anthu citabwela kudzagwila Yesu, Petulo anacita zinthu mopupuluma, anadula khutu la kapolo wa mkulu wansembe. (Yoh. 18:10, 11) Apanso Yesu anam’patsa uphungu mtumwiyo. Kuwonjezela apo, Petulo modzikuza anakamba kuti ngakhale atumwi ena onse atamusiya Yesu, iye sangacite zimenezo ngakhale pang’ono. (Mat. 26:33) Koma kudzidalila kwambili kumeneko kunapangitsa kuti Petulo akane Mbuye wake katatu cifukwa cowopa anthu. Ali wolefuka kwambili maganizo, Petulo “anatuluka panja n’kuyamba kulila mopwetekedwa mtima kwambili.” (Mat. 26:69-75) Iye ayenela kuti anakaikila ngati Yesu adzam’khululukila. Komabe, Petulo sanalole kuti zinthu zofooketsa zimulefule. Iye atapunthwa anapitilizabe kutumikila Yehova pamodzi na atumwi ena.—Yoh. 21:1-3; Mac. 1:15, 16. w20.12 20 ¶17-18
Mande, February 21
Inunso amuna pitilizani kukhala ndi akazi anu mowadziŵa bwino, ndi kuwapatsa ulemu monga ciwiya cosalimba.—1 Pet. 3:7.
Mutu wa banja angaonetse kudzicepetsa m’njila zambili. Mwacitsanzo, iye sayembekezela kuti mkazi wake na ana ake azicita zinthu mwangwilo. Amamvela na kulingalilapo pa malingalilo a ena m’banja, ngakhale kuti malingalilowo ni osiyana na ake. Pamwamba pa izi, mwamuna wodzicepetsa amagwilako nchito zapakhomo, ngakhale kuti anthu angaone kuti zimenezi ni nchito za akazi. Kucita izi kungakhale kovuta. Cifukwa ciani? Mlongo Rachel anati: “Kudela limene n’nakulila, ngati mwamuna athandiza mkazi wake kutsuka mbale kapena kuyeletsa panyumba, anthu komanso acibale ake amakaikila zakuti ni ‘mwamuna weni-weni.’ Amaganiza kuti mwamunayo amalephela kumulamulila mkazi wake.” Ngati maganizo amenewa ni ofala kumene mumakhala, kumbukilani kuti Yesu anasambitsa mapazi a ophunzila ake, ngakhale kuti nchitoyo inali kuonedwa kuti ni ya kapolo. Mutu wa banja wabwino sadela nkhawa zakuti anthu adzamuona bwanji, koma amacita zinthu zokondweletsa mkazi wake na ana ake. w21.02 2 ¶3; 4 ¶11
Ciŵili, February 22
Cinthu cimodzi cimene ndikucita: Ndikuiŵala zinthu zakumbuyo ndipo ndikuyesetsa kuti ndikapeze zakutsogolo. Ndikuyesetsa kucita zimenezi mpaka nditapeza mphoto.—Afil. 3:13, 14.
Kukumbukila zabwino zakumbuyo ni mphatso yocokela kwa Yehova. Koma kaya umoyo wathu unali wabwino motani kale, si kanthu pouyelekezela na umoyo wa m’dziko latsopano. Ena angatikhumudwitse, koma tikasankha kuwakhululukila, tidzaika maganizo athu pa kutumikilabe Yehova. Kudziimba mlandu mopitilila malile kungatilepheletse kutumikila Yehova mwacimwemwe. Conco mofanana na Paulo, tiyeni tikhulupilile kuti Yehova anatikhululukiladi. (1 Tim. 1:12-15) Tili na ciyembekezo cokhala na moyo wosatha. Ndipo m’dziko la Mulungu latsopano, sitidzavutitsidwa na maganizo a zinthu zakale. Pokamba za nthawiyo, Baibo imati: “Zinthu zakale sizidzakumbukilidwanso.” (Yes. 65:17) Tangoganizani: Ena a ife takalamba tikutumikila Yehova, koma m’dziko latsopano, tidzakhalanso acinyamata. (Yobu 33:25) Conco, tiyeni tonsefe tikaniletu kusakhala mu umoyo wakale. M’malomwake, tiyang’ane kutsogolo ku dziko latsopano, na kucita zonse zotheka kuti tikaloŵe! w20.11 24 ¶4; 29 ¶18-19
Citatu, February 23
Ndinaona khamu lalikulu la anthu . . . anapitilzabe kufuula ndi mawu okweza, kuti: “Cipulumutso cathu cacokela kwa Mulungu wathu, . . . ndi kwa Mwanawankhosa.” —Chiv. 7:9, 10.
Kodi kutsogolo kudzacitika ciani? Panthawi ya cisautso cacikulu, Yehova adzatipulumutsa m’njila ziŵili zocititsa cidwi. Yoyamba, iye adzapulumutsa atumiki ake okhulupilika panthawi imene adzacititsa mafumu a dzikoli kuwononga Babulo wamkulu, Ufumu wa cipembedzo conama. (Chiv. 17:16-18; 18:2, 4) Yaciŵili, iye adzapulumutsa anthu ake pamene adzawononga mbali zotsala za dziko la Satana pa Aramagedo. (Chiv. 16:14, 16) Ngati timamatilabe kwa Yehova, Satana sadzativulaza kothelatu. Ndipo iye ni amene adzawonongedwa kothelatu. (Aroma 16:20) Conco, valani zida zonse zankhondo ndipo musazivule! Musayese kumenya mwekha nkhondo. Cilikizani abale na alongo anu. Ndipo tsatilani malangizo a Yehova. Mukacita zimenezi mudzakhala na cidalilo cakuti atate wanu wakumwamba wacikondi, adzakulimbitsani na kukutetezani.—Yes. 41:10. w21.03 30 ¶16-17
Cinayi, February 24
Mudzakhala amphamvu mukakhala osatekeseka ndi acikhulupililo.—Yes. 30:15.
Kodi tingaonetse bwanji kuti timam’dalila Yehova? Mwa kutsatila malangizo amene Yehova amatipatsa. M’Baibo, muli nkhani zambili zoonetsa kufunika kokhala osatekeseka, komanso kuika cidalilo cathu mwa Yehova. Pamene muŵelenga nkhani zimenezi, muziona zimene zinathandiza atumiki a Mulungu kukhala osatekeseka pamene anali kutsutsidwa kwambili. Mwacitsanzo, khoti lalikulu la Ayuda litagamula kuti atumwi aleke kulalikila, iwo sanacite mantha. M’malomwake, anakamba molimba mtima kuti: “Ife tiyenela kumvela Mulungu monga wolamulila, osati anthu.” (Mac. 5:29) Ngakhale pambuyo pokwapulidwa, atumwiwo sanacite mantha. Cifukwa ciani? Cifukwa anadziŵa kuti Yehova anali ku mbali yawo. Iye anali kukondwela nawo. Conco, iwo anapitiliza kulalikila uthenga wabwino. (Mac. 5:40-42) Mofananamo, pamene wophunzila Sitefano anatsala pang’ono kuphedwa, iye anakhalabe na mtendele wa mumtima ndipo “nkhope yake inali ngati nkhope ya mngelo.” (Mac. 6:12-15) Cifukwa ciani? Cifukwa anadziŵa kuti anali woyanjidwa na Yehova. w21.01 4 ¶10-11
Cisanu, February 25
Acapa mikanjo yawo ndi kuiyeletsa m’magazi a Mwanawankhosa.—Chiv. 7:14.
Izi zitanthauza kuti iwo ali na cikumbumtima coyela ndiponso ali na kaimidwe kolungama pamaso pa Yehova. (Yes. 1:18) Iwo ni Akhristu obatizika odzipatulila, amene amakhulupilila kwambili nsembe ya Yesu ndipo ali paubale wabwino na Yehova. (Yoh. 3:36; 1 Pet. 3:21) Conco, iwo ni oyenelela kuimilila pamaso pa mpando wacifumu wa Mulungu, kuti azim’citila “utumiki wopatulika usana ndi usiku” m’bwalo la padziko lapansi la kacisi wauzimu. (Chiv. 7:15) Ngakhale palipano, iwo amacita mbali yaikulu pa nchito yolalikila za Ufumu na kupanga ophunzila, ndipo amaika cifunilo ca Mulungu patsogolo mu umoyo wawo. (Mat. 6:33; 24:14; 28:19, 20) A khamu lalikulu amene adzatuluka m’cisautso cacikulu ni otsimikiza kuti Mulungu adzapitilizabe kuwasamalila, cifukwa “wokhala pampando wacifumuyo adzatambasulila hema wake pamwamba pawo kuti awateteze.” A nkhosa zina adzaona kukwanilitsidwa kwa lonjezo limene akhala akuliyembekezela lakuti: “[Mulungu] adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo.”—Chiv. 21:3, 4. w21.01 16 ¶9-10
Ciŵelu, February 26
Ndidzatsanulila mbali ya mzimu wanga pa anthu osiyanasiyana, ndipo ana anu aamuna ndi ana anu aakazi adzanenela.—Mac. 2:17.
Timakondwela kukhala m’banja la Yehova ndipo tonsefe timacita zonse zotheka polemekeza dongosolo la umutu limene Yehova anakhazikitsa. Baibo imaonetsa kuti kwa Yehova, amuna komanso akazi ni ofunika mofanana. Mwacitsanzo, imaonetsa kuti m’nthawi ya atumwi, Yehova anapeleka mzimu woyela kwa akazi komanso kwa amuna, ndipo anawapatsa mphamvu yocita zozizwitsa monga kulankhula zinenelo zosiyana-siyana. (Mac. 2:1-4, 15-18) Onse, amuna na akazi anadzozedwa na mzimu woyela, ndipo ali na ciyembekezo cokalamulila pamodzi na Khristu. (Agal. 3:26-29) Akazi komanso amuna, adzalandila mphoto ya moyo wosatha padziko lapansi. (Chiv. 7:9, 10, 13-15) Ndipo onse, amuna na akazi, anapatsidwa nchito yolalikila na kuphunzitsa anthu uthenga wabwino. (Mat. 28:19, 20) Buku la Macitidwe limafotokoza nchito ya mlongo wina dzina lake Purisikila, amene pamodzi na mwamuna wake Akula, anathandiza kufotokoza coonadi molondola kwa mwamuna wina wophunzila bwino, dzina lake Apolo.—Mac. 18:24-26. w21.02 14 ¶1; 15 ¶4
Sondo, February 27
Ukhale chelu ndi kuyang’anila gulu lonse la nkhosa . . . muwete mpingo wa Mulungu.—Mac. 20:28.
Akulu muli na udindo waukulu wothandiza ofalitsa kukhala aluso mu ulaliki, kuphatikizapo kuwathandiza pa nchito yawo yophunzitsa anthu Baibo. Ngati wina acita manyazi kutsogoza phunzilo la Baibo imwe mulipo, dzipelekeni kuti mutsogoze ndinu. Akulu angacite zambili pothandiza aphunzitsi a Baibo na kuwalimbikitsa kupitilizabe kugwila nchito yawo. (1 Ates. 5:11) Ngakhale kuti palipano sitikutsogoza phunzilo la Baibo, tingathandizebe wina wake kukula mwauzimu. Popanda kukambapo kwambili, tingacilikize mphunzitsi pa phunzilo na ndemanga zathu zokonzekela bwino. Tingapange ophunzila kukhala mabwenzi athu akabwela ku Nyumba ya Ufumu, komanso tingakhale zitsanzo zabwino kwa iwo. Ndipo akulu angalimbikitse ophunzila mwa kupatula nthawi yoceza nawo, komanso angalimbikitse aphunzitsi mwa kuwathandiza na kuwayamikila. Kukamba zoona, palibe cina cosangalatsa kuposa kudziŵa kuti tinacitako ngakhale kagawo kocepa pothandiza wina kukonda Atate wathu Yehova na kum’tumikila! w21.03 13 ¶18-19
Mande, February 28
Ubwenzi wolimba ndi Yehova ndi wa anthu amene amamuopa. —Sal. 25:14.
Davide anaonetsa kuti anali munthu wodalilika. Mwacitsanzo, ali mnyamata anali kusamalila mwakhama nkhosa za atate ake. Nchito imeneyo inali yoopsa. Patapita nthawi, Davide anafotokozela Mfumu Sauli kuti: “Ine mtumiki wanu ndinakhala m’busa wa nkhosa za bambo anga. Ndiyeno kunabwela mkango komanso cimbalangondo moti ciliconse mwa zilombo zimenezi cinagwila nkhosa ya m’gululo. Pamenepo ine ndinatsatila cilomboco n’kucipha, ndipo ndinapulumutsa nkhosa m’kamwa mwake.” (1 Sam. 17:34, 35) Davide anali kuona kuti ni udindo wake kusamalila nkhosa zimenezo, ndipo anagwebana na zilombo zolusa kuti ateteze nkhosazo. Abale acinyamata angatengele citsanzo ca Davide mwa kugwila molimbika nchito iliyonse imene apatsidwa. Wacicepele Davide, anakhala pa ubale wolimba na Yehova. Ubale umenewo unali wofunika kwambili kwa Davide kuposa kulimba mtima kapena luso lake poseŵenzetsa coimbila ca zingwe. Yehova sanali cabe Mulungu wa Davide koma analinso bwenzi lake, inde bwenzi lake lapamtima. Abale acinyamata, cinthu cofunika kwambili cimene mungacite ni kulimbitsa ubale wanu na Atate wanu wakumwamba. w21.03 3 ¶4-5