April
Cisanu, April 1
Zinthu zonse zimene zinalembedwa kalekale zinalembedwa kuti zitilangize.—Aroma 15:4.
Kodi mukukumana na ciyeso cacikulu? Mwina wina mumpingo anakukhumudwitsani. (Yak. 3:2) Kapena anzanu a kunchito kapena kusukulu amakunyozani cifukwa cotumikila Yehova. (1 Pet. 4:3, 4) Kapenanso a m’banja lanu amakuletsani kupezeka kumisonkhano, kapena kuuzako ena za cikhulupililo canu. (Mat. 10:35, 36) Ngati ciyeso cakula, mwina mungaganize zoleka kutumikila Yehova. Koma mungakhale na cidalilo cakuti mosasamala kanthu za vuto limene mukukumana nalo, Yehova adzakupatsani nzelu zokuthandizani kulimbana na vutolo, na kukupatsani mphamvu kuti mulipilile. M’Mawu ake, Yehova anafotokoza bwino-bwino mmene anthu opanda ungwilo anapililila mayeso aakulu. Cifukwa ciani? Kuti tiphunzile kwa iwo. Izi n’zimene Yehova analimbikitsa mtumwi Paulo kulemba. Kuŵelenga nkhani zimenezi, kungatitonthoze na kutipatsa ciyembekezo. Koma kuti tipindule, pali zina zimene tiyenela kucita kuposa kungoŵelenga cabe Baibo. Tifunika kulola Malemba kuumba kaganizidwe kathu na kukhudza mitima yathu. w21.03 14 ¶1-2
Ciŵelu, April 2
[Onani] m’mindamo, mwayela kale ndipo m’mofunika kukolola. —Yoh. 4:35.
Kodi mumaona anthu amene mumawalalikila monga mbewu zakuca zofunika kukolola? Kuona anthu mwa njila imeneyi, kudzakuthandizani m’njila zitatu. Coyamba, kudzakulimbikitsani kulalikila mwacangu. Nthawi yokolola ni yocepa. Motelo, tifunika kuigwilitsila nchito mwanzelu. Caciŵili, mudzakondwela poona kuti anthu akulabadila uthenga wabwino. Baibo imakamba kuti ‘anthu amasangalala pa nthawi yokolola.’ (Yes. 9:3) Ndipo cacitatu, mudzayamba kuona kuti munthu aliyense amene mwakumana naye angasinthe n’kukhala wophunzila wa Yesu. Conco, mudzayesetsa kusintha ulaliki wanu kuti ugwilizane na zimene amakonda. N’kutheka kuti ophunzila ena a Yesu anali kuona kuti Asamariya sangakhale ophunzila ake. Koma iye sanali kuwaona mwanjila imeneyi. Anali kuwaona kuti angasinthe n’kukhala ophunzila ake. Nafenso tiyenela kuona anthu a m’gawo lathu kuti angasinthe n’kukhala ophunzila a Khristu. Mtumwi Paulo ni citsanzo cabwino cimene tiyenela kutengela. Iye anadziŵa zikhulupililo za anthu amene anali kuwalalikila, zinthu zimene zikanawacititsa cidwi, komanso anali kuwaona kuti angasinthe n’kukhala ophunzila a Yesu. w20.04 8-9 ¶3-4
Sondo, April 3
Manda ndiponso malo a ciwonongeko zili pamaso pa Yehova. Ndiye kuli bwanji mitima ya ana a anthu?—Miy. 15:11.
M’malo mofulumila kuweluza munthu pa zimene wacita, yesetsani kumvetsetsa mmene akumvelela. Yehova yekha ndiye amatimvetsetsa mokwanila. Conco, mupempheni kuti akuthandizeni kuona abale na alongo anu mmene iye amawaonela, ndiponso kudziŵa mmene mungaonetsele cifundo kwa iwo. Simuyenela kucita kusankha abale na alongo ofunika kuwaonetsa cifundo cacikulu. Mavuto ambili amene abale athu onse amakumana nawo, ni ofanana na amene anakumana nawo Yona, Eliya, Hagara, na Loti. Nthawi zina, mavutowo amakhala odzibweletsela okha. Koma kukamba zoona, tonsefe tinakumanapo na mavuto odzibweletsela tekha. Telo m’pomveka kuti Yehova amatilangiza kuti tizimvelelana cifundo. (1 Pet. 3:8) Ngati timvela Yehova, timalimbitsa mgwilizano wocititsa cidwi wa banja lathu la padziko lonse, lokhala ndi anthu a mitundu yosiyana-siyana. Conco, pocita zinthu na abale na alongo athu, tiyeni tiziyesetsa kuwamvetsela, kuwadziŵa bwino, na kuwaonetsa cifundo. w20.04 18-19 ¶15-17
Mande, April 4
Khristu anavutika cifukwa ca inu, ndipo anakusiyilani citsanzo kuti mutsatile mapazi ake mosamala kwambili.—1 Pet. 2:21.
Yesu anatipatsa citsanzo cabwino kwambili pa nkhani yomvela Yehova. Conco, njila imodzi yofunika kwambili imene timaonetsela kuti timamvela Yehova ni mwa kutsatila citsanzo ca Yesu mosamala kwambili. (Yoh. 8:29) Kuti tipitilize kuyenda m’coonadi, tifunika kukhulupilila kuti Yehova ni Mulungu wa coonadi, ndipo ciliconse cimene amatiuza m’Mawu ake, Baibo, ni coonadi. Tifunikanso kukhulupilila kuti Yesu ni Mesiya wolonjezedwa. Anthu ambili masiku ano amakayikila zakuti Yesu anadzozedwa monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. Yohane anacenjeza Akhristu anzake kuti panali “anthu onyenga ambili,” amene akanasoceletsa Akhristu amene anali na cikhulupililo cocepa mwa Yehova na Yesu. (2 Yoh. 7-11) Yohane analemba kuti: “Kodi wabodza angakhalenso ndani, kuposa amene amatsutsa kuti Yesu ndiye Khristu?” (1 Yoh. 2:22) Kuti tisasoceletsedwe, palibenso cina cimene tingacite kuposa kuphunzila Mawu a Mulungu. Ngati tacita zimenezi, m’pamene tingadziŵe bwino Yehova na Yesu. (Yoh. 17:3) Ndipo tikatelo, tidzafika pokhutila kuti cimene tili naco ni coonadi. w20.07 21 ¶4-5
Ciŵili, April 5
Tsimikizani mtima kuti simuikila m’bale wanu . . . copunthwitsa.—Aroma 14:13.
Njila imodzi imene tingapewele kukhala “copunthwitsa” kwa anzathu othamanga nawo pa mpikisanowu, ni mwa kukhala ololela ngati m’poyenela, m’malo mongoumilila maganizo athu. (Aroma 14:19-21; 1 Akor. 8:9, 13) Pambali imeneyi, timasiyana ndi munthu wothamanga pa mpikisano weni-weni, amene amayesetsa kuthamanga mwamphamvu n’colinga cakuti akalandile mphoto ni iyeyo. Othamangawo amangoganizila za iwo okha basi, moti ena amacita kukankha anzawo kuti akhale patsogolo ndiwo. Koma ife sitipikisana na Akhristu anzathu. (Agal. 5:26; 6:4) M’malomwake, colinga cathu ni kuthandiza anthu ambili mmene tingathele, kuti tonse tikwanitse kuthamanga mpaka kukafika pa mzele wotsiliza na kukalandila mphoto ya moyo. Motelo, timayesetsa kutsatila malangizo ouzilidwa akuti, “musamaganizile zofuna zanu zokha, koma muziganizilanso zofuna za ena.” (Afil. 2:4) Pampikisano wathu wothamanga, mokoma mtima Yehova analonjeza kuti ngati tithamanga mopilila mpaka ku mapeto, adzatipatsa mphoto ya moyo wosatha, kaya kumwamba kapena m’paradaiso pano padziko lapansi. Mphoto imeneyi ni yotsimikizilika. w20.04 28 ¶10; 29 ¶12
Citatu, April 6
Amenewa ndi amene atuluka m’cisautso cacikulu.—Chiv. 7:14.
Akhristu mamiliyoni ambili adzapulumuka na kuloŵa m’dziko latsopano. Oukitsidwawo adzakhala mboni zoona ndi maso, kugonjetsedwa kwina kwa imfa. Inde, kuukitsidwa kwa anthu mabiliyoni amene anafa. Ganizilani za cimwemwe cimene tidzakhala naco zimenezi zikadzacitika! (Mac. 24:15) Ndipo onse amene amatumikila Yehova mokhulupilika na mtima onse, adzagonjetsa imfa yobadwa nayo. Iwo adzakhala na moyo kwamuyaya. Mkhristu aliyense, ayenela kukhala woyamikila pa mawu olimbikitsa amene Paulo analembela Akhristu a ku Korinto ponena za kuuka kwa akufa. Tili na zifukwa zambili zomvela malangizo a Paulo otilimbikitsa kukhala otangwanika kwambili “mu nchito ya Ambuye.” (1 Akor. 15:58) Ngati timayesetsa kugwila nchito imeneyi, tingayembekezele kudzasangalala na madalitso a kutsogolo. Tsogolo limenelo lidzakhala labwino kwambili kuposa cina ciliconse cimene tingaganizile. Mmene moyo udzakhalile kutsogolo udzakhala umboni wakuti zonse zimene tinacita m’nchito ya Ambuye, sizinapite pacabe. w20.12 13 ¶16-17
Cinayi, April 7
Magulu awo ankhondo atasonkhana pamodzi kuti amenyane ndi wokwera pahachi uja ndi gulu lake lankhondo.—Chiv. 19:19.
Cioneka kuti maulosi a pa Ezekieli 38:10-23; Danieli 2:43-45; Danieli 11:44 mpaka caputa 12:1; komanso Chivumbulutso 16:13-16, 21 amafotokoza zocitika zimodzi-modzi. Ngati zilidi conco, ndiye kuti zinthu zotsatilazi n’zimene zidzacitika kutsogolo. Pa nthawi inayake mkati mwa cisautso cacikulu, “mafumu a dziko lonse lapansi kumene kuli anthu” adzapanga mgwilizano wa mitundu. (Chiv. 16:13, 14) M’Baibo, mgwilizano umenewo umachedwa “Gogi wa kudziko la Magogi.” (Ezek. 38:2) Mgwilizano wa mitundu umenewu udzaukila anthu a Mulungu komaliza kuti uwafafanize kothelatu. M’masomphenya aulosi okhudza nthawiyi, mtumwi Yohane anaona matalala akulu-akulu kwambili akugwela adani a Mulungu. Zioneka kuti matalala amenewa akuimila uthenga woŵaŵa waciweluzo, umene anthu a Yehova azikalengeza. Zimenezo zidzakwiyitsa Gogi wa Magogi kuti aukile anthu a Mulungu n’colinga cakuti awafafaniziletu padziko lapansi.—Chiv. 16:21. w20.05 15 ¶13-14
Cisanu, April 8
Ngati inu, ngakhale kuti ndinu oipa, mumadziŵa kupatsa ana anu mphatso zabwino, kuli bwanji Atate wakumwamba! Ndithudi iye adzapeleka mowolowa manja mzimu woyela kwa amene akum’pempha!—Luka 11:13.
Mphamvu yogwila nchito ya Mulungu ni mphatso imene tifunika kuiyamikila. Tiyenela kumaganizila zimene mzimu woyela ukucita masiku ano. Yesu asanapite kumwamba, anauza ophunzila ake kuti: “Mzimu woyela ukadzafika pa inu, mudzalandila mphamvu. Pamenepo mudzakhala mboni zanga . . . mpaka kumalekezelo a dziko lapansi.” (Mac. 1:8) Cifukwa ca thandizo la mzimu woyela, atumiki a Yehova oposa 8.5 miliyoni ocokela kulikonse padzikoli, asonkhanitsidwa kukhala gulu la Yehova. Kuwonjezela apo, tili m’paradaiso wauzimu cifukwa mzimu wa Mulungu umatithandiza kukulitsa makhalidwe abwino, monga cikondi, cimwemwe, mtendele, kuleza mtima, kukoma mtima, ubwino, cikhulupililo, kufatsa, komanso kudziletsa. Awa ni “makhalidwe amene mzimu woyela” umabala. (Agal. 5:22, 23) Ndithudi! Mzimu woyela ni mphatso yamtengo wapatali! w20.05 28 ¶10; 29 ¶13
Ciŵelu, April 9
Popeza imfa inafika kudzela mwa munthu mmodzi, kuuka kwa akufa kunafikanso kudzela mwa munthu mmodzi.—1 Akor. 15:21.
Pali zifukwa zingapo zimene tingakambile kuti anthu amene adzalandila oukitsidwa adzakwanitsa kuwadziŵa okondedwa awo. Mwacitsanzo, tikaganizila mmene Yehova anaukitsila anthu kale, cioneka kuti iye poukitsa anthu adzawapangila matupi atsopano olingana na amene anali nawo poyamba. Komanso azikakamba na kuganiza mmene anali kucitila atatsala pang’ono kumwalila. Kumbukilani kuti Yesu anayelekezela imfa na tulo. Ndiponso anayelekezela kuukitsa munthu kwa akufa na kumuutsa ku tulo. (Mat. 9:18, 24; Yoh. 11:11-13) Munthu akauka ku tulo, maonekedwe ake na mawu ake sizisintha. Komanso amakumbukila zimene anali kucita asanagone. Mwacitsanzo, ganizilani za Lazaro. Iye anali wakufa kwa masiku anayi, ndipo thupi lake linali litayamba kuwola. Koma Yesu atamuukitsa, azilongosi ake anamuzindikila nthawi yomweyo, ndipo mwacidziŵikile nayenso Lazaro anawakumbukila.—Yoh. 11:38-44; 12:1, 2. w20.08 14 ¶3; 16 ¶8
Sondo, April 10
Cipulumutso cathu cacokela kwa Mulungu wathu, amene wakhala pampando wacifumu, ndi kwa Mwanawankhosa.—Chiv. 7:10.
Odzozedwa na a nkhosa zina ni ofanana. Magulu onse aŵili ni ofunika kwambili kwa Mulungu. Malipilo amene iye anapeleka pogula odzozedwa na a nkhosa zina anali ofanana. Inde! Moyo wa Mwana wake wokondeka. Kusiyana kumene kulipo pakati pa magulu aŵili amenewa n’kwakuti ali na ziyembekezo zosiyana. Koma magulu onse aŵili afunika kukhalabe okhulupilika kwa Mulungu na Khristu. (Sal. 31:23) Ndipo kumbukilani kuti mzimu wa Mulungu ungagwile nchito mofanana pa aliyense wa ife. Izi zitanthauza kuti Yehova angapeleke mzimu wake woyela kwa munthu aliyense payekha malinga na zofunikila zake. Yehova anapatsa mtumiki wake aliyense wodzipatulila ciyembekezo cabwino kwambili ca kutsogolo. (Yer. 29:11) Cikumbutso ca imfa ya Khristu cimapatsa aliyense wa ife mwayi waukulu wotamanda Mulungu na Khristu, pa zimene aticitila kuti tikasangalale na moyo wosatha. Mosakaikila, Cikumbutso ni msonkhano wofunika koposa kwa Akhristu oona. w21.01 18 ¶16; 19 ¶19
Mande, April 11
Muzicita zimenezi.—1 Akor. 11:25.
Ciŵelengelo coculuka ca amene amapezeka pa Cikumbutso ali na ciyembekezo codzakhala padziko lapansi. Nanga n’cifukwa ciani amapezekapo? Pa cifukwa cofanana na cimene anthu amapezekela ku cikwati ca mnzawo, nawonso amapezeka ku mwambo umenewu. Iwo amapezekapo cifukwa amafuna kuonetsa cikondi cawo kwa amene akukwatilana na kuwacilikiza. Mofananamo, a nkhosa zina amapezeka pa Cikumbutso cifukwa amafuna kuonetsa cikondi cawo na kucilikiza Khristu komanso odzozedwa. Komanso, a nkhosa zina amapezeka pa Cikumbutso pofuna kuonetsa ciyamikilo cawo kaamba ka nsembe ya Yesu, imene imazipangitsa kukhala zotheka kwa iwo kudzakhala padziko lapansi kwamuyaya. Cifukwa cina cofunika cimene a nkhosa zina amapezekela pa Cikumbutso ni kumvela lamulo la Yesu. Yesu atakhazikitsa Mgonelo wapadela na atumwi ake okhulupilika, iye anawauza kuti: “Muzicita zimenezi pondikumbukila.” (1 Akor. 11:23-26) Conco, iwo adzapitilizabe kupezeka pa Mgonelo wa Ambuye nthawi zonse pamene odzozedwa ali na moyo padziko lapansi. Ndipo a nkhosa zina amaitanila aliyense kuti apezeke nawo pa Cikumbutso. w21.01 17-18 ¶13-14
Kuŵelenga Baibo kwa Cikumbutso: (Zocitika usana: Nisani 9) Yohane 12:12-19; Maliko 11:1-11
Ciŵili, April 12
Mulungu anatisonyeza ife cikondi cake pakuti anatumiza m’dziko Mwana wake wobadwa yekha kuti tipeze moyo kudzela mwa iye.—1 Yoh. 4:9.
Kambili timaganiza kuti cikondi cimatanthauza mmene timamvelela wina akatiuza mawu okoma mtima. Koma cikondi ceni-ceni, cimafunika kuonekelanso m’zocita. (Yelekezelani na Yakobo 2:17, 26) Mwacitsanzo, Yehova amatikonda. (1 Yoh. 4:19) Iye amaonetsa kuti amatikonda kupitila m’mawu abwino opezeka m’Baibo. (Sal. 25:10; Aroma 8:38, 39) Komabe, tidziŵa kuti Mulungu amatikonda, osati cabe cifukwa ca zimene amatiuza, koma kupitilanso m’zocita zake. Yehova analola kuti Mwana wake avutike na kutifela. (Yoh. 3:16) Kodi tingakaikile zakuti Yehova amatikonda kwambili? Timaonetsa kuti timakonda Yehova na Yesu mwa kuwamvela. (Yoh. 14:15; 1 Yoh. 5:3) Ndipo Yesu anatilamula kuti tizikondana. (Yoh. 13:34, 35) Sitiyenela kuonetsa cabe cikondi kwa abale na alongo athu m’mawu koma tiyenelanso kuonetsa kuti timawakonda mwa zocita zathu. —1 Yohane 3:18. w21.01 9 ¶6; 10 ¶8
Kuŵelenga Baibo kwa Cikumbutso: (Zocitika usana: Nisani 10) Yohane 12:20-50
Citatu, April 13
Ndakuchani mabwenzi, cifukwa zonse zimene ndamva kwa Atate wanga ndakudziwitsani. —Yoh. 15:15.
Akhristu odzozedwa na mzimu woyela ali na ciyembekezo cokakhala na Yesu kwamuyaya, komanso kukatumikila naye pamodzi mu Ufumu wa Mulungu. Iwo azikakhaladi naye Khristu, azikamuona, komanso kukambilana naye. (Yoh. 14:2, 3) Nawonso Akhristu amene ali na ciyembekezo codzakhala pa dziko lapansi, Yesu adzawasamalila mwacikondi. Olo kuti iwo sazikamuona Yesu, ubwenzi wawo na iye udzapitiliza kulimba, pamene akusangalala na moyo umene Yehova adzawapatsa kupitila mwa Yesu. (Yes. 9:6, 7) Yesu akutipempha kuti tikhale mabwenzi ake. Tikakhala mabwenzi ake, timapeza madalitso ambili. Mwacitsanzo, monga mabwenzi ake, iye amatikonda na kuticilikiza. Tili na mwayi wodzakhala na moyo wamuyaya. Koposa zonse, kukhala pa ubwenzi na Yesu kumatipatsa mwayi wamtengo wapatali kwambili, wokhala bwenzi la Atate wake, Yehova. Ndithudi, ni mwayi kukhala bwenzi la Yesu! w20.04 25 ¶15-16
Kuŵelenga Baibo kwa Cikumbutso: (Zocitika usana: Nisani 11) Luka 21:1-36
Cinayi, April 14
Mwa Khristu onse adzapatsidwa moyo.—1 Akor. 15:22.
Mtumwi Paulo analemba kalata yake kwa Akhristu odzozedwa a ku Korinto, amene anali kudzaukitsidwa kukakhala na moyo kumwamba. Akhristu amenewo ‘anayeletsedwa mwa Khristu Yesu, ndipo anaitanidwa kuti akhale oyela.’ Paulo anakambanso za “anthu amene anagona mu imfa mwa Khristu.” (1 Akor. 1:2; 15:18; 2 Akor. 5:17) M’kalata ina youzilidwa, Paulo analemba kuti awo amene ‘agwilizana na Yesu pokhala ndi imfa yofanana ndi yake, adzagwilizananso naye poukitsidwa mofanana ndi iye.’ (Aroma 6:3-5) Yesu anaukitsidwa na thupi lamzimu ndipo anayenda kumwamba. Conco, zidzakhalanso cimodzi-modzi kwa onse amene ali “mwa Khristu,” kutanthauza Akhristu onse odzozedwa na mzimu. Paulo analemba kuti Khristu anaukitsidwa monga “cipatso coyambilila ca amene akugona mu imfa.” (1 Akor. 15:20) Kumbukilani kuti ena monga Lazaro, anaukitsidwa n’kukhalanso na moyo padziko lapansi. Koma Yesu yekha ndiye anali woyamba kuukitsidwa kwa akufa na thupi lamzimu na kulandila moyo wosatha. w20.12 5-6 ¶15-16
Kuŵelenga Baibo kwa Cikumbutso: (Zocitika usana: Nisani 12) Mateyu 26:1-5, 14-16; Luka 22:1-6
TSIKU LA CIKUMBUTSO
Dzuŵa Likaloŵa
Cisanu, April 15
Tizikakhala ndi Ambuye nthawi zonse.—1 Ates. 4:17.
Akhristu odzozedwa akangotsiliza moyo wawo wa padziko lapansi masiku ano, nthawi yomweyo amaukitsidwa kukakhala na moyo kumwamba. Mawu a mtumwi Paulo apa 1 Akorinto 15:51, 52 amatsimikizila zimenezi. Iye anati: “Si tonse amene tidzagona mu imfa, koma tonse tidzasandulika, m’kamphindi, m’kuphethila kwa diso, pa kulila kwa lipenga lomaliza.” Mawu a Paulo amenewa akukwanilitsidwa masiku ano. Abale a Khristu amenewa akangoukitsidwa, amakhala na cimwemwe cacikulu. Baibo imatiuza nchito imene adzagwila kumwamba, awo amene adzasandulika “m’kuphethila kwa diso.” Ponena za iwo Yesu akuti: “Amene wapambana pa nkhondo ndi kutsatila zocita zanga kufikila mapeto, ndidzamupatsa ulamulilo pa mitundu ya anthu. Iyeyo adzakusa anthu ndi ndodo yacitsulo, ngati imenenso ine ndailandila kwa Atate wanga. Anthuwo adzaphwanyidwaphwanyidwa ngati mbiya zadothi.”—Chiv. 2:26, 27. w20.12 12 ¶14-15
Kuŵelenga Baibo kwa Cikumbutso: (Zocitika usana: Nisani 13) Mateyu 26:17-19; Maliko 14:12-16; Luka 22:7-13 (Zocitika dzuŵa litaloŵa: Nisani 14) Yohane 13:1-5; 14:1-3
Ciŵelu, April 16
Khristu anaukitsidwa kwa akufa.—1 Akor. 15:20.
Anamuyelekezela na zipatso zoyambilila zimene Aisiraeli anali kupeleka nsembe kwa Mulungu. Kuwonjezela apo, pamene Paulo anachula Yesu kuti “cipatso coyambilila,” anatanthauza kuti ena adzaukitsidwa pambuyo pake kukakhala na moyo wa kumwamba. Atumwi na Akhristu ena odzozedwa anali kudzatsatila Yesu. (1 Akor. 15:18) Iwo anali kudzaukitsidwa mofanana na mmene Yesu anaukitsidwila. Kuuka kopita kumwamba kunali kusanayambe panthawi imene Paulo analembela kalata Akhristu a ku Korinto. Koma Paulo anaonetsa kuti izi zidzacitika kutsogolo. Iye anati: “Aliyense pamalo pake: Coyamba Khristu, amene ndi cipatso coyambilila, kenako ake a Khristu pa nthawi ya kukhalapo kwake.” (1 Akor. 15:23; 1 Ates. 4:15, 16) Masiku ano, tili m’nthawi ya “kukhalapo” kwa Khristu. Atumwi na Akhristu ena odzozedwa na mzimu amene anamwalila, anafunika kuyembekezela nthawi ya kukhalapo kwa Khristu imeneyi kuti akalandile mphoto yawo kumwamba na ‘kugwilizana na Yesu ataukitsidwa mofanana ndi iye.’—Aroma 6:5. w20.12 5 ¶12; 6 ¶16-17
Kuŵelenga Baibo kwa Cikumbutso: (Zocitika usana: Nisani 14) Yohane 19:1-42
Sondo, April 17
Thupi limafesedwa lili lokhoza kuwonongeka, limaukitsidwa losakhoza kuwonongeka. —1 Akor. 15:42.
Mtumwi Paulo anali kukamba za munthu woukitsidwa na thupi la kumwamba, kutanthauza kuti “thupi lauzimu.” (1 Akor. 15:43, 44) Pamene Yesu anali padziko lapansi, anali na thupi lanyama. Koma ataukitsidwa “anakhala mzimu wopatsa moyo,” ndipo anabwelela kumwamba. Mofananamo, Akhristu odzozedwa amaukitsidwa na moyo wamzimu. Paulo anafotokoza kuti: “Monga tilili m’cifanizilo ca wopangidwa ndi fumbi uja, tidzakhalanso m’cifanizilo ca wakumwambayo.” (1 Akor. 15:45-49) Mfundo yofunika kudziŵa ni yakuti Yesu sanaukitsidwe na thupi lanyama. Paulo anakamba momveka bwino kuti: “Mnofu ndi magazi sizingalowe ufumu wa Mulungu” wakumwamba. (1 Akor. 15:50) Atumwi komanso Akhristu anzawo odzozedwasadzaukitsidwa kupita kumwamba na matupi okhoza kuwonongeka a mnofu ndi magazi. w20.12 10-11 ¶10-12
Kuŵelenga Baibo kwa Cikumbutso: (Zocitika usana: Nisani 15) Mateyu 27:62-66 (Zocitika dzuŵa litaloŵa: Nisani 16) Yohane 20:1
Mande, April 18
Imfa iwe, kupambana kwako kuli kuti? Imfawe, mphamvu yako ili kuti—1 Akor. 15:55.
Mulungu anauzila ena mwa ophunzila a Yesu a m’nthawi ya Akhristu oyambilila, kulemba za kuuka kopita kumwamba. Mtumwi Yohane anafotokoza kuti: “Tsopano ndife ana a Mulungu, koma padakali pano sizinaonekelebe kuti tidzakhala otani. Tikudziwa kuti akadzaonekela, tidzakhala ngati iyeyo.” (1 Yoh. 3:2) Conco, Akhristu odzozedwa sadziŵa mmene adzakhalile akadzaukitsidwa kukakhala na moyo kumwamba na matupi amzimu. Komabe, iwo adzaona Yehova pamaso-m’pamaso akakalandila mphoto yawo kumwamba. Baibo siifotokoza zonse za ciukililo copita kumwamba. Koma mtumwi Paulo anafotokozapo mfundo zina pa nkhaniyi. Akhristu odzozedwa adzakhala limodzi na Khristu pamene ‘adzathetsa maboma onse, ulamulilo onse, ndi mphamvu zonse,’ kuphatikizapo “imfa . . . mdani womalizila.” Pothela pake, Yesu pamodzi na olamulila anzake adzadzipeleka kukhala pansi pa ulamulilo wa Yehova na kupeleka zinthu zonse kwa iye. (1 Akor. 15:24-28) Imeneyi idzakhala nthawi yokondweletsa ngako! w20.12 8 ¶2
Kuŵelenga Baibo kwa Cikumbutso: (Zocitika usana: Nisani 16) Yohane 20:2-18
Ciŵili, April 19
Ndili ndi ciyembekezo. . . kuti kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama omwe.—Mac. 24:15.
Nanga bwanji za Akhristu onse okhulupilika amene alibe ciyembekezo cokakhala na Khristu kumwamba? Nawonso ali na ciyembekezo ca kuukitsidwa. Baibo imakamba kuti mtumwi Paulo na ena amene amapita kumwamba ali “pa kuuka koyambilila kucokela kwa akufa.” (Afil. 3:11) Zimenezi zionetsa kuti padzakhalanso kuuka kwina kumene kudzatsatilapo. Ndipo n’zogwilizana na zimene Yobu anakamba ponena za tsogolo lake. (Yobu 14:15) “Ake a Khristu pa nthawi ya kukhalapo kwake” adzakhala kumwamba pamodzi na Yesu akadzacotsapo maboma onse, ulamulilo wonse komanso mphamvu. Ngakhale “imfa nayonso, monga mdani womalizila, idzawonongedwa.” Mosakaikila, onse amene adzaukitsidwa kukakhala na moyo kumwamba sadzafanso. (1 Akor. 15:24-26) Amene ali na ciyembekezo codzakhala padziko angakhale na ciyembekezo kucokela pa mawu a Paulo a mu lemba la lelo. N’zodziŵikilatu kuti munthu wosalungama sangapite kumwamba. Conco mawu amenewa akamba za kuuka kwa akufa kutsogolo pano padziko lapansi. w20.12 6-7 ¶18-19
Citatu, April 20
[Khristu] anandikonda ndi kudzipeleka yekha cifukwa ca ine.—Agal. 2:20.
Koma mwina tingadzifunse kuti, ‘Kodi ningatsimikize bwanji kuti Yehova sananifulatile?’ Kudzifunsa kwanu funso limeneli, kuonetsa kuti mtima wanu ukukuuzani kuti Yehova angakukhululukileni. Zaka zambili kumbuyoku, magazini ina ya Nsanja ya Mlonda inakamba kuti: “Ti[nga]gwe n’kulephela mobweleza-bweleza pa cizoloŵezi cina coipa cimene cinazika kwambili mizu mu umoyo wathu wakale . . . Musaganize kuti munacita chimo losakhululukidwa. Umu ni mmene Satana amafuna kuti muzionela. Ndipo ngati mudzimvela cisoni pa khalidwe lanu, umenewo ni umboni wakuti simunafike pokhala munthu woipa amene Yehova sangakhululukile. Musaleme kutembenukila kwa Mulungu modzicepetsa komanso mocokela pansi pamtima, kuti akukhululukileni, akuyeletseni komanso akuthandizeni. Asanakhale Mkhristu, Paulo anacita macimo aakulu ambili. Paulo anali kukumbukila zimene anacita kumbuyoko. (1 Tim. 1:12-15) Anali kuona dipo kukhala mphatso yake imene Mulungu anam’patsa. Mwa ici, Paulo anapewa msampha wodziimba mlandu mopitilila malile, na kuika maganizo ake pa kucita zonse zotheka potumikila Yehova. w20.11 27 ¶14; 29 ¶17
Cinayi, April 21
Ngati wina akusowa nzelu, azipempha kwa Mulungu, ndipo adzamupatsa, popeza iye amapeleka mowolowa manja kwa onse ndiponso amapeleka mosatonza. —Yak. 1:5.
Satana amaseŵenzetsa zinthu zina zambili potiyesa kuti ticite zoipa. Kodi timacita ciani tikayesedwa? N’capafupi kukhala na maganizo odzikhululukila. Mwacitsanzo, tingaganize kuti: ‘Nikacita izi sanganicotse mumpingo. Conco zilibe vuto kweni-kweni.’ Maganizo otelo ni olakwika kwambili. Telo tingacite bwino kudzifunsa mafunso monga akuti: ‘Kodi n’kutheka kuti Satana akuseŵenzetsa mayeselo amenewa pofuna kugaŵanitsa mtima wanga? Ngati nagonja ku zilako-lako zoipa, kodi sinidzabweletsa citonzo pa dzina la Yehova? Kodi kucita izi kudzanipangitsa kuyandikila kwambili Mulungu, kapena kudzanipangitsa kutalikilana naye?’ Mungacite bwino kumasinkha-sinkha pa mafunso ngati amenewa. Ndipo pemphani nzelu kwa Mulungu kuti muthe kuyankha mafunso amenewa moona mtima. Kucita izi kudzakutetezani kwambili. Mudzakwanitsa kukana mayeselo molimba mtima, monga mmene Yesu anacitila pamene anati: “Coka Satana!” (Mat. 4:10) Kukhala na mtima wogaŵanika si kwabwino. w20.06 12-13 ¶16-17
Cisanu, April 22
Ndikuuza aliyense wa inu kumeneko kuti musamadziganizile kuposa mmene muyenela kudziganizila. Koma aliyense aziganiza m’njila yakuti akhale munthu woganiza bwino.—Aroma 12:3.
Timamvela Yehova modzicepetsa cifukwa timadziŵa kuti nthawi zonse iye ndiye amadziŵa zimene zili zabwino kwa ife. (Aef. 4:22-24) Kudzicepetsa kumatisonkhezela kuika cifunilo ca Yehova patsogolo osati zofuna zathu. Kumatisonkhezelanso kuona ena kukhala otiposa. Ndipo zotsatilapo zake n’zakuti timakhala pa ubale wabwino na Yehova komanso na okhulupilila anzathu. (Afil. 2:3) Komabe, ngati sitingasamale tingayambe kutengela makhalidwe a anthu a m’dzikoli, omwe ni odzikuza komanso odzikonda. Cioneka kuti izi n’zimene zinacitika kwa Akhristu ena m’nthawi ya atumwi, cifukwa mtumwi Paulo analembela Akhristu a ku Roma kuti: “Ndikuuza aliyense wa inu kumeneko kuti musamadziganizile kuposa mmene muyenela kudziganizila. Koma aliyense aziganiza m’njila yakuti akhale munthu woganiza bwino.” Apa Paulo sanatanthauze kuti tizidziona kuti ndife osafunika. Koma anatanthauza kuti tiyenela kukhala odzicepetsa. Kudzicepetsa kumatithandiza kuti tizidziona moyenela na kupewa kudziona ofunika kwambili kuposa ena. w20.07 2 ¶1-2
Ciŵelu, April 23
M’dzikolo munalibe cosokoneza ciliconse, komanso palibe anacita naye nkhondo.—2 Mbiri 14:6.
M’nthawi ya Mfumu Asa, mtendele umene Ayuda anali nawo, m’kupita kwa nthawi unatha. Gulu lankhondo lalikulu la asilikali amphamvu okwana 1 miliyoni, linabwela kudzawaukila kucokela ku Itiyopiya. Mtsogoleli wawo Zera, sanali kukayika kuti iye pamodzi na gulu lake lankhondo adzagonjetsa Ayuda. Koma Asa anadalila Mulungu wake, Yehova, osati kukula kwa gulu lake lankhondo. Iye anapemphela kwa Yehova kuti: “Tithandizeni Yehova Mulungu wathu cifukwa tikudalila inu, ndipo tabwela m’dzina lanu kudzamenyana ndi khamuli.” (2 Mbiri 14:11) Ngakhale kuti gulu lankhondo la Aitiyopiya linali na asilikali ambili kuwilikiza kaŵili poyelekezela na asilikali a Asa, Asa anali kudziŵa kuti Yehova ali na mphamvu zoculuka moti adzathandiza anthu ake. Ndipo Yehova sanamugwilitse mwala. Anamuthandizadi. Gulu lankhondo la Aitopiya linagonjetsedwa mocititsa manyazi. (2 Mbiri 14:8-13) Olo kuti sitidziŵa bwino-bwino zimene zingacitikile aliyense wa ife kutsogolo, cimene tidziŵa n’cakuti mtendele umene tili nawo palipano ni wosakhalitsa. Kumbukilani kuti Yesu anakambilatu kuti m’masiku otsiliza, “mitundu yonse idzadana” na ophunzila ake.—Mat. 24:9. w20.09 17-18 ¶14-16
Sondo, April 24
Ndimasangalala ndi . . . zitonzo.—2 Akor. 12:10.
Palibe amene amakondwela akamanyozedwa. Komabe, ngati tikhumudwa kwambili adani athu akamatinyoza, tikhoza kufooka. (Miy. 24:10) Ndiye kodi tiyenela kumvela bwanji otsutsa akamatinyoza? Monga Paulo, n’zotheka ‘kusangalala ndi . . . zitonzo.’ Cifukwa ciani? Cifukwa kunyozedwa na kutsutsidwa kumaonetsa kuti ndifedi ophunzila a Yesu. (1 Pet. 4:14) Yesu anakamba kuti otsatila ake adzazunzidwa. (Yoh. 15:18-20) Izi n’zimene zinacitikila Akhristu oyambilila. Panthawiyo, anthu otengela cikhalidwe ca Agiriki anali kuona Akhristu ngati anthu osaphunzila komanso otsika. Nawonso Ayuda anali kuona Akhristu ngati “osaphunzila ndiponso anthu wamba,” monga mmene anali kuonela mtumwi Petulo na mtumwi Yohane. (Mac. 4:13) Akhristu anali kuonedwa ngati anthu ofooka cifukwa sanali kutengako mbali m’zandale kapena kuloŵa usilikali, ndipo anthu anali kuwasala. Kodi Akhristu oyambililawo analola kuti zoipa zimene otsutsa anali kuwanenela ziwafooketse? Iyai. w20.07 14-15 ¶3-4
Mande, April 25
Tiyeni tipitilize kukondana, cifukwa cikondi cimacokela kwa Mulungu, ndipo aliyense amene ali ndi cikondi, ndi mwana wa Mulungu ndipo akudziŵa Mulungu. —1 Yoh. 4:7.
Mtumwi Yohane anali kuwakonda kwambili abale ake auzimu ndiponso anali kudela nkhawa umoyo wawo wauzimu. Cikondi cake cimeneco cimaonekela bwino tikaganizila malangizo amene iye anawapatsa m’makalata ake atatu ouzilidwa. Ndithudi, n’zolimbikitsa ngako kudziŵa kuti amuna na akazi odzozedwa amene adzalamulila na Khristu, nawonso ni acikondi ndipo amadela nkhawa ena mofanana na Yohane. (1 Yoh. 2:27) Tiyeni tiyesetse kutsatila malangizo amene anapeleka. Tiyeni titsimikize mtima kuyendabe m’coonadi, kutanthauza kumvela Yehova pa zilizonse zimene timacita pa umoyo wathu. Tiziŵelenga Mawu ake na kuwadalila. Tiyenelanso kulimbitsa cikhulupililo cathu mwa Yesu. Tizikana kutsatila nzelu za anthu komanso ziphunzitso za ampatuko. Tiyeni tizipewa kukhala na umoyo wapaŵili komanso tisalole ena kutinyengelela kuti ticite chimo. Tizitsatila mfundo za Yehova za makhalidwe abwino. Cinanso, tizithandiza abale athu kukhalabe olimba kuuzimu mwa kuwakhululukila akatilakwila, komanso mwa kuthandiza amene afunika thandizo. Tikatelo, ndiye kuti olo tikumane na mavuto otani, tidzapitilizabe kuyenda m’coonadi. w20.07 24-25 ¶15-17
Ciŵili, April 26
Mulungu anaika ziwalo m’thupi, ciliconse m’malo ake, mmene iye anafunila.—1 Akor. 12:18.
Mtumiki wa Mulungu aliyense, Yehova ndiye anamuitana mu mpingo wake. Ngakhale kuti timacita mbali zosiyana mu mpingo, tonsefe ndife ofunika ndipo timadalilana wina na mnzake. Mtumwi Paulo anagogomeza kuti palibe aliyense wa ife amene ayenela kuyang’ana mtumiki wa Yehova mnzake, n’kumati: “Ndilibe nawe nchito.” (1 Akor. 12:21) Kuti mu mpingo mukhale mtendele, tifunika kuona wina aliyense kukhala wofunika na kuseŵenzela pamodzi mogwilizana. (Aef. 4:16) Ngati timagwilizana, aliyense adzaona kuti amakondedwa, ndipo mpingo udzakhala wolimba. Akulu onse mu mpingo amaikidwa na mzimu woyela wa Yehova. Koma aliyense wa iwo ali na mphatso komanso maluso osiyana. (1 Akor. 12:17) Mwina ena anangoikidwa kumene pa udindo, ndipo ali na cidziŵitso cocepelako poyelekeza na akulu ena. Mwinanso ena sakwanitsa kucita zambili cifukwa ca ukalamba na matenda. Ngakhale n’conco, palibe mkulu aliyense amene ayenela kuyang’ana mkulu mnzake n’kumati, “Ndilibe nawe nchito.” M’malo mwake, mkulu aliyense ayenela kumvela uphungu wa Paulo wa pa Aroma 12:10. w20.08 26 ¶1-2; 27 ¶4
Citatu, April 27
Pakuti zocitika za padzikoli zikusintha.—1 Akor. 7:31.
Yehova amatitsogolela panjila ya ku moyo kupitila m’gawo la padziko lapansi la gulu lake. Mosakaikila, timatsatila mosavuta kamvedwe katsopano ka coonadi, kapena mfundo zokhudza makhalidwe. Koma kodi timacita bwanji gulu la Mulungu likapanga masinthidwe okhudza umoyo wathu mwacindunji, monga kugulitsa Nyumba ya Ufumu imene timasonkhanilamo? Koma tidzasungabe cimwemwe cathu ngati tikumbukila kuti amene tikumuseŵenzela ni Yehova, ndipo ni amene akutsogolela gulu lake. (Akol. 3:23, 24) Mfumu Davide anapeleka citsanzo cabwino pocita zopeleka zomangila kacisi. Iye anati: “Ndine ndani ine, ndipo anthu anga ndani kuti tithe kupeleka nsembe zaufulu ngati zimenezi? Pakuti ciliconse n’cocokela kwa inu, ndipo tapeleka kwa inu zocokela m’dzanja lanu.” (1 Mbiri 29:14) Tikacita zopeleka, nafenso tikupatsa Yehova zocokelanso kwa iye. Ngakhale n’conco, Yehova amayamikila nthawi yathu, mphamvu zathu, komanso cuma cathu cimene timapeleka pocilikiza nchito imene afuna kuti icitike.—2 Akor. 9:7. w20.11 22-23 ¶14-16
Cinayi, April 28
Woyang’ana mitambo sadzakolola.—Mlal. 11:4.
Ife Mboni za Yehova sitiona kuti nchito yathu yatiyendela bwino mwa kuŵelenga anthu amene tawathandiza kubwela m’gulu la Mulungu. (Luka 8:11-15) Cofunika kwambili ni kupitiliza kulalikila uthenga wabwino na kuphunzitsa anthu. Tikatelo, Yehova amationa kuti tikucita bwino pa nchito yathu. N’cifukwa ciani takamba conco? Cifukwa kucita zimenezi kumaonetsa kuti timamvela Mulungu na Mwana wake. (Maliko 13:10; Mac. 5:28, 29) Tili na cifukwa cina cogwilila nchito yolalikila masiku ano. Cifukwa cake n’cakuti mapeto a dzikoli ali pafupi kwambili. Nthawi imene yatsala kuti tigwile nchitoyi yacepa kwambili. Conco, musazengeleze kapena kuyembekezela kuti zinthu zikhaliletu bwino kuti muyambe kugwila nawo nchito yofunika kwambili imeneyi.Ino ndiyo nthawi yofunika kukulitsa mtima wofuna kugwila nchito yolalikila, yophunzila zambili za m’Baibo, yokulitsa khalidwe la kulimba mtima, ndiponso yophunzila kucita zinthu mwakhama. Loŵani m’gulu la asodzi oposa 8 miliyoni, ndipo mudzapeza cimwemwe cimene Yehova amapeleka. (Neh. 8:10; Luka 5:10) Tsimikizani mtima kugwila nawo nchito yolalikila za Ufumu mmene mungathele, na kupitiliza kuigwila mpaka pamene Yehova adzanene kuti yatha. w20.09 7 ¶18-20
Cisanu, April 29
Sunga bwino cimene cinaikidwa m’manja mwako.—1 Tim. 6:20.
Tiyenela kupewa kukhala na mtima wofuna kudziunjikila zinthu zakuthupi. Apo ayi, “cinyengo camphamvu ca cuma” cingapangitse kuti tileke kukonda Yehova, kuyamikila Mawu ake, ndiponso kuuzako ena mawuwo. (Mat. 13:22) Kuti nafenso titeteze zinthu zimene Yehova anatipatsa, tifunika kucitapo kanthu mwamsanga tikaona kuti cinacake cifuna kutitayitsa zinthu zimenezo. Tingadziŵiletu zimene tingacite ngati pangacitike ngozi kapena vuto lina lalikulu. Mofananamo, tingaganiziletu pasadakhale zimene tingacite ngati mwadzidzidzi taona zinthu zosayenela, zaciwawa, kapena nkhani za ampatuko poseŵenzetsa intaneti, potamba filimu, kapena potamba pulogilamu inayake pa TV. Ngati takonzekela pasadakhale, tingacitepo kanthu mwamsanga kuti tidziteteze ku zinthu zimene zingatiwononge mwauzimu. Izi zidzatithandiza kukhalabe oyela pamaso pa Yehova. (Sal. 101:3; 1 Tim. 4:12) Timafunika kusunga bwino zinthu zamtengo wapatali zimene Yehova watipatsa, zomwe ni coonadi camtengo wapatali ca m’Baibo komanso mwayi wophunzitsako ena coonadico. Tikatelo, tidzakhala na cikumbumtima coyela, umoyo waphindu, na cimwemwe cimene cimabwela cifukwa cothandiza ena kudziŵa Yehova. w20.09 30 ¶16-19
Ciŵelu, April 30
Maso ako adzayamba kuona Mlangizi wako Wamkulu.—Yes. 30: 20.
Kodi ndimwe wobatizika? Ngati inde, ndiye kuti munalengeza poyela kuti mumakhulupilila Yehova, ndipo ndimwe wofunitsitsa kutumikila m’gulu lake. Masiku ano, njila imene Yehova amatsogolela gulu lake imaonetsa makhalidwe ake, colinga cake, na miyezo yake. Pa makhalidwe a Yehova, onani atatu amene amaonekela m’gulu lake. Loyamba, “Mulungu alibe tsankho.” (Mac. 10:34) Cikondi ndico cinalimbikitsa Yehova kupeleka Mwana wake monga “dipo lokwanila ndendende m’malo mwa onse.” (1 Tim. 2:6; Yoh. 3:16) Yehova amaseŵenzetsa anthu ake kulalikila uthenga wabwino kwa onse amene angamvetsele, kuti athandize ambili kupindula na dipo limeneli. Laciŵili, Yehova ni Mulungu wadongosolo komanso wamtendele. (1 Akor. 14:33, 40) Conco, m’pake kuti olambila ake amam’tumikila mwadongosolo komanso mwamtendele. Lacitatu, Yehova ni “Mlangizi Wamkulu.” (Yes. 30:21) Conco, gulu lake limaika patsogolo kuphunzitsa Mawu ake ouzilidwa, ponse paŵili mu mpingo na mu ulaliki. w20.10 20 ¶1-3