LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • es22 masa. 47-57
  • May

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • May
  • Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2022
  • Tumitu
  • Sondo, May 1
  • Mande, May 2
  • Ciŵili, May 3
  • Citatu, May 4
  • Cinayi, May 5
  • Cisanu, May 6
  • Ciŵelu, May 7
  • Sondo, May 8
  • Mande, May 9
  • Ciŵili, May 10
  • Citatu, May 11
  • Cinayi, May 12
  • Cisanu, May 13
  • Ciŵelu, May 14
  • Sondo, May 15
  • Mande, May 16
  • Ciŵili, May 17
  • Citatu, May 18
  • Cinayi, May 19
  • Cisanu, May 20
  • Ciŵelu, May 21
  • Sondo, May 22
  • Mande, May 23
  • Ciŵili, May 24
  • Citatu, May 25
  • Cinayi, May 26
  • Cisanu, May 27
  • Ciŵelu, May 28
  • Sondo, May 29
  • Mande, May 30
  • Ciŵili, May 31
Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2022
es22 masa. 47-57

May

Sondo, May 1

Anapitiliza kuwamvela. —Luka 2:51.

Ali wamng’ono, Yesu anasankha kukhala wogonjela kwa makolo ake. Iye sanakanepo cilangizo ca makolo ake poganiza kuti anali kudziŵa zambili kuposa iwo. Mosakaikila, Yesu anayesetsa kukwanilitsa udindo wake monga mwana wamkulu m’banja. Analimbikilanso kuphunzila nchito ya atate ake omulela ya ukalipentala, kuti azithandizila pa zofunika za banja. Zioneka kuti Yesu anauzidwa na makolo ake za kubadwa kwake kozizwitsa, komanso mauthenga amene angelo a Mulungu anabweletsa okamba za iye. (Luka 2:8-19, 25-38) Yesu sanadalile cabe zimene anali kuuzidwa. Iye anali kuŵelenganso Malemba payekha. Tidziŵa bwanji kuti Yesu anali woŵelenga Mawu a Mulungu wakhama? Cifukwa ali wamng’ono, aphunzitsi ku Yerusalemu “anadabwa kwambili ndi mayankho ake komanso poona kuti anali womvetsa zinthu kwambili.” (Luka 2:46, 47) Ndipo ali na zaka 12 cabe, Yesu anali atadziŵa kale kuti Yehova anali Tate wake.—Luka 2:42, 43, 49. w20.10 29-30 ¶13-14

Mande, May 2

Khristu anaukitsidwa kwa akufa.—1 Akor. 15:12.

Kukhulupilila kuti Yesu anaukitsidwa n’kofunika kwambili pa ciyembekezo cathu ca kuuka kwa akufa. Pamene mtumwi Paulo anayamba kufotokoza za kuuka kwa akufa anafotokoza mfundo zitatu izi zosatsutsika: (1) “Khristu anafela macimo athu.” (2) “Anaikidwa m’manda.” (3) “Anaukitsidwa tsiku lacitatu, mogwilizana ndi Malemba.” (1 Akorinto 15:3, 4) Kodi imfa ya Yesu, kuikidwa kwake m’manda, komanso kuukitsidwa kwake zili na tanthauzo lanji kwa ife? Mneneli Yesaya analosela kuti Mesiya anali ‘kudzadulidwa m’dziko la amoyo,’ ndipo “manda ake adzakhala limodzi ndi a anthu oipa.” Koma panali kudzacitikanso cinthu cina. Mneneliyo anakambanso kuti Mesiya anali ‘kudzanyamula chimo la anthu ambili.’ Yesu anacita zimenezi mwa kupeleka moyo wake monga dipo. (Yes. 53:8, 9, 12; Mat. 20:28; Aroma 5:8) Conco, imfa ya Yesu, kuikidwa kwake m’manda, na kuukitsidwa kwake, ni maziko olimba a ciyembekezo cathu cakuti tidzamasulidwa ku uchimo na imfa, komanso kuti tidzaonananso na okondedwa athu amene anamwalila. w20.12 2-3 ¶4-6; 5 ¶11

Ciŵili, May 3

Ineyo, kuposa wina aliyense, ndili ndi zifukwa zodalila zinthu zimene anthu amaziona kuti ndi zofunika. Ngati alipo munthu woganiza kuti ali ndi zifukwa zodalila zinthu zimene anthu amaziona kuti ndi zofunika, ine ndiye woposa ameneyo.—Afil. 3:4.

Nthawi zambili, mtumwi Paulo anali kulalikila m’masunagoge a Ayuda. Mwacitsanzo, m’sunagoge wa ku Tesalonika, Paulo “kwa masabata atatu anakambilana [na Ayuda] mfundo za m’Malemba.” (Mac. 17:1, 2) Mwacionekele, iye anali kukhala womasuka kulalikila m’sunagoge. Paulo anali Myuda. (Mac. 26:4, 5) Ndipo anali kuwadziŵa bwino Ayuda, moti anakwanitsa kuwalalikila mopanda mantha. (Afil. 3: 5) Paulo atathamangitsidwa ndi anthu otsutsa ku Tesalonika komanso ku Bereya, anakafika ku Atene. Ali kumeneko, anayambanso “kukambilana ndi Ayuda ndi anthu ena opembedza Mulungu” m’sunagoge. (Mac. 17:17) Koma pamene Paulo anali kulalikila pamsika, omvetsela ake anali osiyana ndi a ku sunagoge. Panali akatswili a nzelu za anthu, komanso anthu ena amene sanali Ayuda. Anthuwo anali kuona uthenga wa Paulo monga “ciphunzitso catsopano.” Iwo anamuuza kuti: “Zimene ukufotokozazi ndi zinthu zacilendo m’makutu mwathu.”—Mac. 17:18-20. w20.04 9 ¶5-6

Citatu, May 4

Pamene ndikufuna kucita cinthu cabwino, coipa cimakhala cili ndi ine.—Aroma 7:21.

Musamadziimbe mlandu mopitilila malile ngati mukulimbana na cofooka cina cake. Kumbukilani kuti palibe aliyense wa ife amene angakhale wolungama pamaso pa Mulungu cifukwa ca nchito zake. Tonsefe timafunikila cisomo ca Mulungu kupitila mu dipo la Yesu. (Aef. 1:7; 1 Yoh. 4:10) Tingapemphe abale na alongo athu amene ni banja lathu lauzimu kuti atilimbikitse! Iwo angatimvetsele tikafuna kufotokoza nkhawa zathu, ndipo angatilimbikitse. (Miy. 12:25; 1 Ates. 5:14) Mlongo Joy wa ku Nigeria amene anali kuvutika na maganizo olefula anati: “N’kanacita ciani popanda abale na alongo? Cilimbikitso ca abale na alongo anga ni umboni wakuti Yehova amayankha mapemphelo anga. Naphunzilanso kwa iwo mmene ningalimbikitsile ena amene ni olefuka.” Komabe, tiyenela kukumbukila kuti nthawi zina abale na alongo athu sangadziŵe kuti tikufunikila cilimbikitso. Conco, tingafunikile kuyamba ndife kufikila Mkhristu mnzathu wokhwima kuuzimu na kumuuza kuti tikufuna thandizo. w20.12 23-24 ¶7-8

Cinayi, May 5

Ndakuchani mabwenzi. —Yoh. 15:15.

Nthawi zambili, cinthu coyamba cimene munthu amacita kuti apange ubwenzi wolimba na munthu wina ni kupatula nthawi yoceza naye. Akamaceza, kufotokozelana za mumtima, komanso zimene akumana nazo pa umoyo, amapanga ubwenzi. Koma kupanga ubwenzi wolimba na Yesu kungakhale kovutilapo. Cimodzi mwa zifukwazo n’cakuti Yesu sitinamuonepo. Akhristu ambili m’nthawi ya atumwi, nawonso sanamuonepo Yesu. Olo zinali telo, mtumwi Petulo anati: “Ngakhale simukumuona panopa, mumakhulupilila mwa iye.” (1 Pet. 1:8) Cotelo, n’zotheka kupanga ubwenzi wolimba na Yesu ngakhale kuti sitinamuonepo. Cifukwa cina n’cakuti sitikwanitsa kukamba na Yesu. Pamene tipemphela, timangokamba na Yehova. N’zoona kuti timapemphela kupitila m’dzina la Yesu, koma sitikamba naye. Ndipo Yesu safuna kuti tizipemphela kwa iye. Cifukwa ciani? Cifukwa pemphelo ni mbali ya kulambila, ndipo Yehova yekha ndiye woyenela kumulambila. (Mat. 4:10) Ngakhale n’conco, n’zotheka ndithu kuonetsa kuti timam’konda Yesu. w20.04 20 ¶1-3

Cisanu, May 6

[Mulungu] adzakulimbitsani ndi kukupatsani mphamvu. —1 Pet. 5:10.

Ocita mpikisano wothamanga ku Girisi anali kulimbana na zopinga, monga kulema komanso kuphweteka kwa thupi. Kuti zinthu ziwayendele bwino, anali kungodalila mphamvu zawo na mapulakatisi amene anali kucita. Mofanana na ocita mpikisano wothamanga amenewo, nafenso timaphunzitsidwa mmene tingathamangile pa mpikisano wathu wokalandila moyo. Koma ife tili na mwayi umene ocita mpikisano wothamanga weni-weni alibe. Tingapeze mphamvu kucokela kwa Yehova, gwelo la mphamvu zopanda malile. Yehova analonjeza kuti ngati tim’dalila, adzatiphunzitsa na kutipatsa mphamvu. Mtumwi Paulo anakumana na mavuto ambili. Anthu ena anali kumunyoza na kum’zunza, ndipo nthawi zina anali kukhala wofooka. Kuwonjezela apo, anali kuvutika na “munga m’thupi.” (2 Akor. 12:7) Iye sanaone mavutowo monga cifukwa colekela kutumikila Yehova. Koma anawaona monga mpata woonetsela kuti anali kudalila Yehova. (2 Akor. 12:9, 10) Ndipo cifukwa coona zinthu mwa njila imeneyi, Yehova anamuthandiza kupilila mavuto ake onse. w20.04 29 ¶13-14

Ciŵelu, May 7

Palibe munthu angabwele kwa ine akapanda kukokedwa ndi Atate.—Yoh. 6:44.

Tili na cuma cina cosaoneka, cimene ni mwayi ‘wogwila nchito limodzi’ na Yehova, Yesu, ndiponso angelo. (2 Akor. 6:1) Timaseŵenzela nawo limodzi pamene tikugwila nchito yolalikila. Paulo pokamba za iyemwini komanso za anthu ena amene amagwila nchitoyi, anati: “Ndife anchito anzake a Mulungu.” (1 Akor. 3:9) Tikamagwila nchito yolalikila, timakhalanso anchito anzake a Yesu. Kumbukilani kuti iye atalamula otsatila ake kuti, “pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzila anga,” anakambanso kuti: “Ine ndili pamodzi ndi inu.” (Mat. 28:19, 20) Nanga kodi angelo amatithandiza bwanji? Iwo amatitsogolela pamene tikulengeza “uthenga wabwino wosatha . . . kwa anthu okhala padziko lapansi.” Kunena zoona, umenewu ni mwayi waukulu! (Chiv. 14:6) Ni madalitso otani amene timapeza pa nchito yolalikila cifukwa ca thandizo la Yehova, Yesu, na angelo? Pamene tilalikila uthenga wa Ufumu, mbewu zina za coonadi zimagwela pa nthaka yabwino na kukula. (Mat. 13:18, 23) Ndani amene amacititsa kuti mbewu za coonadi zimenezi zikule na kubala zipatso? Yesu anafotokoza zimenezo mu lemba la tsiku lalelo. w20.05 30 ¶14-15

Sondo, May 8

Musamatengele nzelu za nthawi ino.—Aroma 12:2.

Mabanja mamiliyoni ambili amasokonezeka cifukwa cosudzulana. Cikwati cikatha, makolowo amakhala okwiilana kwambili, ndipo ana amaona kuti sakondedwa. Ngakhale anthu a m’banja limodzi amene amakhala m’nyumba imodzi zingatheke kuti sagwilizana kweni-kweni. Mlangizi wina wa za mabanja anati: “Amayi, atate, komanso ana, kaŵili-kaŵili sacitila zinthu pamodzi. M’malomwake, amatangwanika kwambili na kompyuta, tabuleti, foni, kapena maseŵela a pa kompyuta. Ngakhale kuti anthu amenewa amakhala m’nyumba imodzi, sadziŵana bwino.” Koma sitifuna kutengela mzimu wa dziko wopanda cikondi. M’malomwake, tiyenela kuonetsa cikondi ceni-ceni kwa a m’banja lathu, maka-maka kwa abale na alongo athu a m’cikhulupililo. (Aroma 12:10) Kodi cikondi ceni-ceni n’ciani? Mawuwa amakamba za ubale wolimba wapakati pa anthu a m’banja limodzi. Cikondi cotelo n’cimene tiyenela kukulitsa m’banja lathu lauzimu, inde pakati pa abale na alongo athu acikhristu. Ngati tionetsa cikondi ceni-ceni, tidzathandiza kusunga mgwilizano, umene ni wofunika kwambili pa kulambila koona.—Mika 2:12. w21.01 20 ¶1-2

Mande, May 9

Ndipatseni mtima wosagawanika kuti ndiope dzina lanu. —Sal. 86:11.

Timu imene ni yogwilizana nthawi zambili imawina. Mtima wathu tingauyelekezele na timu yowina imeneyo, malinga ngati zoganiza zathu, mmene timamvelela, komanso zolaka-laka zathu, zonse zikhala zogwilizana na mfundo za Yehova. Musaiŵale kuti Satana amafuna kugaŵanitsa mtima wanu. Amafuna kuti muzilakalaka kucita zinthu zimene mudziŵa kuti Mulungu amaletsa. Koma kuti mupitilize kutumikila Yehova, mufunika kukhala na mtima wosagaŵanika kapena kuti wathunthu. (Mat. 22:36-38) Musalole kuti Satana apangitse mtima wanu kukhala wogaŵanika. Monga Davide, tiyeni nafenso tizipemphela kwa Yehova kuti: “Ndipatseni mtima wosagawanika kuti ndiope dzina lanu.” Citani zonse zotheka kuti muzicita zinthu mogwilizana na pemphelo limeneli pa umoyo wanu. Tsiku lililonse popanga zosankha, kaya zazing’ono kapena zazikulu, muziyesetsa kuonetsa kuti mumaopa kwambili dzina loyela la Yehova. Mukatelo, monga Mboni ya Yehova, mudzathandiza kuyeletsa dzina la Yehova. (Miy. 27:11) Ndipo tonsefe tidzatha kukamba monga mmene mneneli Mika anakambila kuti: “Ife tidzayenda m’dzina la Yehova Mulungu wathu mpaka kalekale, inde mpaka muyaya.”—Mika 4:5. w20.06 13 ¶17-18

Ciŵili, May 10

Iyo idzapita ndi ukali waukulu kuti ikafafanize ndi kuwononga ambili.—Dan. 11:44.

Mfumu ya kumpoto na maboma ena padzikoli akadzaukila anthu a Mulungu, adzaputa mkwiyo wa Mulungu Wamphamvuzonse, ndipo izi zidzayambitsa nkhondo ya Aramagedo. (Chiv. 16:14, 16) Panthawiyo, mfumu ya kumpoto pamodzi na mitundu ina yonse imene idzakhala Gogi wa Magogi, idzawonongedwa kothelatu, ndipo “sipadzapezeka woithandiza.” (Dan. 11:45) Vesi yoyamba m’caputa 12 ca buku la Danieli, imafotokoza mmene mfumu ya kumpoto na maboma ogwilizana nayo adzawonongedwela. Imafotokozanso mmene Yehova adzatipulumutsila. (Dan. 12:1) Kodi vesiyi imatanthauza ciani? Mikayeli ni dzina lina la Mfumu yathu, Khristu Yesu. Kuyambila mu 1914 pamene Ufumu unakhazikitsidwa kumwamba, Khristu ‘anaimilila kuti azithandiza’ anthu a Mulungu. Koma posacedwapa, iye “adzaimilila,” kutanthauza kuti adzawononga adani ake pankhondo ya Aramagedo. Nkhondo imeneyo ndiyo idzakhala cocitika cothela pa “nthawi ya masautso” aakulu kwambili amene Danieli anakamba kuti sanacitikepo.—Chiv. 6:2; 7:14. w20.05 15-16 ¶15-17

Citatu, May 11

Yosefe uja, . . . anapita naye ku Iguputo.—Gen. 39:1.

Pamene Yosefe anali kapolo komanso mkaidi, analibe ufulu woyenda ndipo palibe zimene akanacita pa vuto lake. Kodi n’ciani cinam’thandiza kuti asataye mtima? M’malo mosumika maganizo ake pa zimene sakanatha kucita, iye anagwila molimbika nchito imene anapatsidwa. Yosefe anali kuonabe kuti Yehova ndiye anali wofunika kwambili mu umoyo wake. Ndipo cotulukapo cake n’cakuti Yehova anadalitsa zonse zimene Yosefe anacita. (Gen. 39:21-23) Nkhaniyi itikumbutsa kuti dzikoli n’lankhanza, ndipo anthu adzaticitila zinthu zopanda cilungamo. Ngakhale Mkhristu mnzathu angatikhumudwitse. Koma ngati timaona Yehova monga Thanthwe lathu, kapena malo athu othawilapo, sitidzataya mtima kapena kuleka kum’tumikila. (Sal. 62:6, 7; 1 Pet. 5:10) Kumbukilaninso kuti Yosefe ayenela kuti anali na zaka pafupifupi 17 pamene Yehova anam’pangitsa kulota maloto. N’zacidziŵikile kuti Yehova amadalilanso atumiki ake acicepele. Masiku ano acicepele ambili ali monga Yosefe. Nawonso ali na cikhulupililo mwa Yehova. Ena mwa iwo amaikidwa m’ndende mopanda cilungamo, cifukwa cofuna kukhalabe okhulupilika kwa Mulungu.—Sal. 110:3. w20.12 16 ¶3; 17 ¶5, 7

Cinayi, May 12

Anaitanitsa atumwiwo. Ndiyeno anangowakwapula ndi kuwalamula kuti asiye kulankhula m’dzina la Yesu.—Mac 5:40.

Mtumwi Petulo na mtumwi Yohane anaona kuti unali mwayi kuzunzidwa cifukwa cotsatila Yesu, komanso cifukwa couzako ena ziphunzitso zake. (Mac. 4:18-21; 5:27-29, 41, 42) Ophunzilawo analibe cifukwa cocitila manyazi. Ngakhale kuti anthu sanali kuwalemekeza Akhristu oyambilila, iwo anacita zambili pothandiza ena kuposa anthu otsutsawo. Mwacitsanzo, mabuku ouzilidwa amene Akhristuwo analemba apitiliza kuthandiza anthu mamiliyoni ambili na kuwapatsa ciyembekezo. Ufumu umene anali kulalikila ukulamulila kumwamba tsopano, moti posacedwa udzalamulila mtundu wonse wa anthu. (Mat. 24:14) Koma ufumu wamphamvu wa Roma, umene unali kuzunza Akhristu panthawiyo unatha, ndipo tsopano ni mbili cabe ya makedzana, pamene ophunzila okhulupilikawo, pano tikamba ni mafumu kumwamba. Cinanso, otsutsawo anafa. Ndipo ngati angadzaukitsidwe, adzakhala nzika za Ufumu wa Mulungu, umene unali kulalikidwa na Akhristu amene iwo anali kuwazonda.—Chiv. 5:10. w20.07 15 ¶4

Cisanu, May 13

[Abulahamu] anali kuyembekezela mzinda wokhala ndi maziko enieni, mzinda umene Mulungu ndiye anaumanga ndi kuupanga. —Aheb. 11:10.

Abulahamu anali kukhulupilila kwambili malonjezo a Mulungu, moti zinali ngati kuti akuona Wodzozedwa wa Mulungu kapena kuti Mesiya, amene anali kudzakhala Mfumu mu Ufumu wa Mulungu. N’cifukwa cake Yesu anauza Ayuda a m’nthawi yake kuti: “Atate wanu Abulahamu anali wosangalala poyembekezela kuona tsiku langa, ndipo analiona moti anakondwela.” (Yoh. 8:56) Conco, n’zoonekelatu kuti Abulahamu anali kudziŵa kuti mbadwa zake zidzalamulila mu Ufumu umene Yehova adzakhazikitsa. Ndipo anayembekezela lonjezo la Yehova limenelo moleza mtima. Kodi Abulahamu anaonetsa bwanji kuti anali kuyembekezela mzinda, kapena kuti Ufumu wokhazikitsidwa na Mulungu? Coyamba, iye sanakhale nzika ya ufumu uliwonse pano padziko lapansi. Abulahamu anali kusamuka-samuka. Anasankha kusakhala pamalo amodzi, ndiponso sanacilikize mfumu iliyonse ya umunthu. Kuwonjezela apo, iye sanayese kukhazikitsa ufumu wake-wake. M’malomwake, anapitiliza kumvela Yehova na kumuyembekezela kuti adzakwanilitsa lonjezo lake. Mwa kucita zimenezi, Abulahamu anaonetsa kuti anali na cikhulupililo cacikulu mwa Yehova. w20.08 3 ¶4-5

Ciŵelu, May 14

Cifukwa munthu amene wafa wamasuka ku ucimo wake. —Aroma 6:7.

Yehova analonjeza kuti mu ulamulilo wa Khristu, palibe aliyense amene adzakamba kuti: “Ndikudwala.” (Yes. 33:24) Conco, akufa adzaukitsidwa na matupi athanzi. Koma sadzakhala angwilo nthawi yomweyo, cifukwa ngati angadzaukitsidwe ali na maganizo angwilo komanso thupi langwilo, mwina abululu awo sadzakwanitsa kuwazindikila. Cioneka kuti pang’ono-m’pang’ono anthu onse adzakhala angwilo mu Ulamulilo wa Khristu wa Zaka 1,000. Ulamulilo wa zaka 1,000 umenewu ukadzatha, m’pamene Yesu adzabwezela Ufumu kwa Atate wake. Panthawiyo Ufumu wa Mulungu udzakhala utatsiliza nchito yake kuphatikizapo kuthandiza anthu kukhala angwilo. (1 Akor. 15:24-28; Chiv. 20:1-3) Ganizilani cabe mmene mudzamvelela pamene mudzalandila okondedwa anu amene anamwalila. Kodi mudzasekelela kwambili kapena mudzagwetsa misozi ya cisangalalo? Kodi mudzafuula mosangalala poimba nyimbo zotamanda Yehova? N’zodziŵikilatu kuti mudzam’konda kwambili Atate wanu wacikondi na Mwana wake cifukwa ca mphatso yabwino ngako imeneyi ya ciukililo. w20.08 16-17 ¶9-10

Sondo, May 15

Aliyense ali ndi mphatso yake yocokela kwa Mulungu. Wina m’njila iyi, winanso m’njila inayo. —1 Akor. 7:7.

Mtumwi Paulo analimbikitsa Akhristu kuganizila ngati angathe kutumikila Yehova monga mbeta. (1 Akor. 7:8, 9) Ndithudi Paulo sanali kuona Akhristu amene anali mbeta kukhala otsikilapo. Ndiye cifukwa cake anasankha Timoteyo, m’bale wosakwatila, kuti asamalile maudindo akulu-akulu. (Afil. 2:19-22) Conco, kungakhale kulakwa kuganiza kuti m’bale ni woyenelela kapena ni wosayenelela, cabe cifukwa ali pabanja kapena sali pabanja. (1 Akor. 7:32-35, 38) Yesu ngakhale Paulo sanaphunzitse zakuti Akhristu onse afunika kuloŵa m’banja kapena kukhala mbeta. Nanga tingakambe ciani za cikwati na umbeta? Nsanja ya Mlonda ya October 1, 2012, inakamba momveka bwino kuti: “Kunena zoona, zonsezi [cikwati na umbeta] ndi mphatso zocokela kwa Mulungu. . . . Yehova saona kuti kusakhala pabanja ni cinthu cocititsa manyazi kapena comvetsa cisoni.” Conco, tiyenela kulemekeza abale na alongo mu mpingo amene ni mbeta. w20.08 28 ¶8-9

Mande, May 16

Kunena za tsikulo ndi ola lake, palibe amene akudziŵa, . . . koma Atate yekha.—Mat. 24:36.

M’maiko ena, anthu amaonetsa cidwi kwambili akamvela uthenga wabwino. Amacita kulaka-laka kuti kubwele munthu amene angawauzeko uthenga wabwino. Koma m’maiko ena, anthu sacita cidwi kweni-kweni ndi za Mulungu kapena Baibo. Kodi anthu ambili m’gawo lanu amaulandila motani uthenga wabwino? Kaya anthu ni acidwi kapena ayi, Yehova amafuna kuti tipitilize kugwila nchito yolalikila mpaka pamene adzatiuze kuti yatha. Yehova anaika kale nthawi pamene nchito yolalikila idzatha. Ndipo nchitoyo ikadzatha, “mapeto adzafika.” (Mat. 24:14) Yesu anakambilatu zocitika zimene zidzaonetsa kuti tili m’masiku otsiliza. Iye anadziŵa kuti zocitika zimenezo zingathe kulepheletsa otsatila ake kuikabe maganizo awo pa nchito yolalikila. Pa cifukwa cimeneci, iye anawalangiza kuti ayenela ‘kukhalabe maso.’ (Mat. 24:42) M’masiku a Nowa, panali zinthu zambili zimene zinalepheletsa anthu kumvela macenjezo amene iye anali kupeleka. Masiku anonso, zinthu zofanana na zimenezo zingatilepheletse kukhalabe maso. (Mat. 24:37-39; 2 Pet. 2:5) Conco, tifunika kuikabe maganizo athu pa nchito imene Yehova anatipatsa. w20.09 8 ¶1-2, 4

Ciŵili, May 17

Onse ofuna kukhala ndi moyo wodzipeleka kwa Mulungu mwa Khristu Yesu, nawonso adzazunzidwa.—2 Tim. 3:12.

Satana ali na “mkwiyo waukulu,” ndipo kungakhale kudzinamiza kuganiza kuti tingakwanitse kuuthaŵa mkwiyo wake. (Chiv. 12:12) Posacedwapa, tonse cikhulupililo cathu cidzayesedwa. Patsala kanthawi kocepa, padzikoli pakhala “cisautso cacikulu cimene sicinacitikepo kucokela pa ciyambi ca dziko mpaka tsopano.” (Mat. 24:21) Panthawi imeneyo, abululu ŵathu akhoza kudzatiukila, ndipo nchito yathu ingadzaletsedwe. (Mat. 10:35, 36) Mofanana na Mfumu Asa, kodi aliyense wa ife adzadalila Yehova kuti adzatithandiza na kutiteteza? (2 Mbiri. 14:11) Yehova wakhala akutikonzekeletsa mwauzimu kaamba ka zinthu zimene tidzakumana nazo kutsogoloku. Pofuna kutithandiza kukhalabe olimba mwauzimu, Yehova akutsogolela “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu” kuti azitipatsa “cakudya [cabwino cauzimu] pa nthawi yoyenela.” (Mat. 24:45) Koma aliyense wa ife ayenela kucita khama kuti alimbitse cikhulupililo cake mwa Yehova.—Aheb. 10:38, 39. w20.09 18 ¶16-18

Citatu, May 18

Mtima wa mfumu uli ngati mitsinje yamadzi m’dzanja la Yehova. Amautembenuzila kulikonse kumene iye akufuna.—Miy. 21:1.

Ngati n’zogwilizana na colinga cake, Yehova angaseŵenzetse mzimu wake woyela wamphamvu kupangitsa anthu a ulamulilo kucita zimene iye akufuna. Anthu angakumbe mfolo wopatutsila madzi kumene iwo akufuna. Mofananamo, Yehova angaseŵenzetse mzimu wake woyela kupatutsa maganizo a olamulila kuti acite zinthu mogwilizana na cifunilo cake. Izi zikacitika, anthu a ulamulilo amakhala na mtima wopanga zigamulo zokomela anthu a Mulungu. (Yelekezelani na Ezara 7:21, 25, 26.) Kodi tiyenela kucita ciani? Tingapemphelele anthu a ulamulilo pamene akupeleka zigamulo zokhudza umoyo na utumiki wathu. (1 Tim. 2:1, 2; Neh. 1:11) Mofanana na Akhristu oyambilila, timawapemphelela kwambili abale na alongo athu amene ali m’ndende.—Mac. 12:5; Aheb. 13:3. w20.11 15 ¶13-14

Cinayi, May 19

Mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzila anga. Muziwabatiza.—Mat. 28:19.

Ngati ndimwe amene munali kuphunzila Baibo na wophunzila wa Yesu watsopano ameneyo, cimakhala cokondweletsa ngako kucitila umboni ubatizo wake! (1 Ates. 2:19, 20) Ophunzila obatizika atsopano amenewa ni ‘makalata ocitila umboni,’ kwa amene anali kuwaphunzitsa Baibo, komanso ku mpingo wonse. (2 Akor. 3:1-3) N’zokondweletsa kwambili kuona kuti pazaka zinayizi, pa avaleji timacitila lipoti maphunzilo a Baibo pafupi-fupi 10,000,000 mwezi uliwonse padziko lonse. Ndipo m’zaka zimenezi, pa avaleji, anthu opitila 280,000 anali kubatizika caka ciliconse monga Mboni za Yehova komanso ophunzila atsopano a Yesu Khristu. Kodi tingawathandize bwanji maphunzilo a Baibo amenewa ofika mamiliyoni kuti akabatizike? Yehova moleza mtima akupelekabe mwayi kwa anthu kuti akhale ophunzila a Khristu. Conco, tifunika kucita zonse zotheka kuti tiwathandize kupita patsogolo mwamsanga kuti akabatizike. Nthawi yotsalayi ni yocepa kwambili!—1 Akor. 7:29a; 1 Pet. 4:7. w20.10 6 ¶1-2

Cisanu, May 20

Mulungu amatsutsa odzikweza, koma odzicepetsa amawasonyeza kukoma mtima kwake kwakukulu.—Yak. 4:6.

Mfumu Sauli sanamvele Yehova. Ndipo pamene mneneli Samueli anakamba naye za nkhaniyi, Sauli anakana kuvomeleza colakwa cake. M’malo mwake, iye anadzilungamitsa mwa kupeputsa colakwa cake na kukankhila ena colakwaco. (1 Sam. 15:13-24) Panthawi ina kumbuyoko, Sauli anaonetsanso khalidwe limeneli. (1 Sam. 13:10-14) N’zacisoni kuti analola mtima wake kudzikuza. Cifukwa sanafune kusintha kaganizidwe kake, Yehova anam’dzudzula na kumukana. Kuti titengepo cenjezo pa citsanzo coipa ca Sauli, tingacite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi nikaŵelenga uphungu wonikhudza m’Mawu a Mulungu nimayesa kudzilungamitsa? Kodi nimayesa kupeputsa zotulukapo zake? Kodi nimakankhila kwa wina mlandu wa zocita zanga?’ Ngati yankho ni inde pa iliyonse ya mafunsowa, tifunika kusintha kaganizidwe kathu na kaonedwe kathu ka zinthu. Apo ayi, tidzakhala wodzikuza kwambili cakuti Yehova adzatikana kuti tisakhalenso bwenzi lake. w20.11 20 ¶4-5

Ciŵelu, May 21

Kumbukila Mlengi wako Wamkulu masiku a unyamata wako, asanafike masiku oipa komanso zisanafike zaka zimene udzati: “Moyo sukundisangalatsa.”—Mlal. 12:1.

Acicepele sankhani amene mufuna kutumikila. Mufunika kum’dziŵa bwino Yehova, cifunilo cake, komanso mmene mungacitile cifunilo cake mu umoyo wanu. (Aroma 12:2) Mukatelo, mudzapanga cosankha cofunika kopambana mu umoyo wanu, ca kutumikila Yehova. (Yos. 24:15) Ngati mukhala na pulogilamu yokhazikika ya kuŵelenga na kuphunzila Baibo, cikondi canu pa Yehova cidzakula ndipo cikhulupililo canu mwa iye cidzalimbila-limbila. Sankhani kuika cifunilo ca Yehova patsogolo mu wanu. Dziko la Satanali limalonjeza kuti ngati museŵenzetsa maluso anu kuti mudzipindulitse nokha, mudzakhala acimwemwe. Koma zoona zake n’zakuti, amene amaika mtima wonse pa zolinga za kuthupi ‘amadzibweletsela zopweteka zambili pathupi lawo.’ (1 Tim. 6:9, 10) Koma ngati mumvela Yehova na kusankha kuika cifunilo cake patsogolo, mudzakhala na umoyo wopindulitsa, ndipo ‘mudzacita zinthu mwanzelu.’—Yos. 1:8. w20.10 30-31 ¶17-18

Sondo, May 22

Ndiyenela kukalengeza uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu . . . , cifukwa ndi zimene anandituma kudzacita.—Luka 4:43.

M’nthawi ya Akhristu oyambilila. Uthenga umene Yesu analalikila unapeleka ciyembekezo kwa anthu onse. Analamula otsatila ake kupitiliza nchito imene iye anayambitsa, yocitila umboni “mpaka kumalekezelo a dziko lapansi.” (Mac. 1:8.) Koma iwo sakanakwanitsa kugwila nchitoyo mwa mphamvu zawo. Anafunikila mzimu woyela—“mthandizi” amene Yesu anawalonjeza. (Yoh. 14:26; Zek. 4:6) Otsatila a Yesu analandila mzimu woyelawo pa Pentekosite wa mu 33 C.E. Mothandizidwa na mzimu woyelawo, pamenepo anayamba kulalikila, cakuti m’nthawi yocepa, anthu masauzande analandila uthenga wabwino. (Mac. 2:41; 4:4) Citsutso citabuka, ophunzilawo sanacite mantha ayi. Anatembenukila kwa Mulungu kuti awathandize. Iwo anapemphela kuti: “Lolani kuti akapolo anu apitilize kulankhula mawu anu molimba mtima.” Ndiyeno anadzazidwa na mzimu woyela, na kupitiliza “kulankhula mawu a Mulungu molimba mtima.”—Mac. 4:18-20, 29, 31. w20.10 21 ¶4-5

Mande, May 23

Khristu anafela macimo athu, malinga ndi Malemba. . . kenako anaukitsidwa tsiku.—1 Akor. 15:3, 4.

Tingatsimikize bwanji kuti Yehova anamuukitsadi Yesu? Panali mboni zambili zoona na maso zimene zinatsimikizila kuti Yesu anaukitsidwadi. (1 Akor. 15:5-7) Mboni yoyamba imene mtumwi Paulo anachula anali mtumwi Petulo (Kefa). Kagulu kena ka ophunzila kanatsimikizila kuti Petulo anaona Yesu ataukitsidwa. (Luka 24:33, 34) Kuwonjezela apo, atumwi nawonso anamuona Yesu ataukitsidwa. Ndiyeno Khristu “anaonekelanso kwa abale oposa 500 pa nthawi imodzi,” mwina ku msonkhano wosangalatsa wa ku Galileya wochulidwa pa Mateyu 28:16-20. Yesu ‘anaonekelanso kwa Yakobo,’ amene ayenela kuti anali m’bale wake wa Yesu, amene poyamba sanakhulupilile kuti Yesu anali Mesiya. (Yoh. 7:5) Yakobo ataona kuti Yesu waukitsidwa, anakhulupilila mwa iye. Ndipo cofunika kudziŵa n’cakuti ca m’ma 55 C.E. pamene Paulo anali kulemba kalatayi, mboni zambili zoona na maso zinali zikalipo. Conco, aliyense amene akanakaikila za nkhaniyi akanafunsa mwacindunji mboni zodalilika zimenezo. w20.12 3 ¶5, 7-8

Ciŵili, May 24

Yehova adzacilikiza wonyozekayo pamene akudwala pabedi lake.—Sal. 41:3.

Ngati sitimvela bwino, maka-maka ngati tidwala matenda okhalitsa, cingakhale cosavuta kuyamba kuganizila zinthu zolefula. Conco, dalilani Yehova kuti akucilikizeni. Ngakhale kuti iye saticilitsa mozizwitsa masiku ano, angatitonthoze na kutipatsa mphamvu zofunikila kuti tipilile. (Sal. 94:19) Mwacitsanzo, angalimbikitse Akhristu anzathu kudzatithandizako nchito zina za pakhomo. Angalimbikitsenso abale athu kupemphela nafe. Kapena angatithandize kukumbukila mfundo zolimbikitsa zopezeka m’Mawu ake. Mwacitsanzo, angatikumbutse za ciyembekezo cathu cabwino ca umoyo wangwilo wopanda matenda, komanso wopanda zowawa m’dziko latsopano. (Aroma 15:4) Tingaone kuti tikulephela kucita zambili mu ulaliki. Mlongo wina dzina lake Laurel anasungidwa m’makina omuthandiza kupuma kwa zaka 37! Anali na khansa, ndipo anacitidwa maopaleshoni akulu-akulu, komanso anali na matenda okhalitsa apakhungu. Koma sanam’tseke pakamwa. Anali kulalikila manasi, na ena amene anali kubwela ku nyumba kwake ndipo anathandiza anthu 17 kudziŵa coonadi ca m’Baibo! w20.12 24 ¶9; 25 ¶12

Citatu, May 25

Yehova ali kumbali yanga, sindidzaopa. Munthu wocokela kufumbi angandicite ciani?—Sal. 118:6.

Mtumwi Paulo anali kufunikila thandizo. Ca mu 56 C.E., gulu la laciwawa linagwila Paulo na kum’guguzila kunja kwa kacisi ku Yerusalemu kuti akamuphe. Tsiku lotsatila, Paulo atapelekedwa ku Khoti Yapamwamba ya Ayuda, adani ake anatsala pang’ono kum’khadzula-khadzula. (Mac. 21:30-32; 22:30; 23:6-10) Panthawiyo, n’kutheka kuti Paulo anafika podzifunsa kuti, ‘Kodi nidzapilila mavutowa mpaka liti?’ Kodi Paulo analandila thandizo lotani? Usiku wotsatila Paulo atamangidwa, “Ambuye,” Yesu, anaimilila pambali pake na kumuuza kuti: “Limba mtima! Pakuti wandicitila umboni mokwanila mu Yerusalemu, ndipo ukandicitilanso umboni ku Roma.” (Mac. 23:11) Cinalidi cilimbikitso ca panthawi yake! Yesu anayamikila Paulo cifukwa cocitila umboni mu Yerusalemu. Ndipo analonjeza Paulo kuti adzafika bwino-bwino ku Roma, ndipo akacitilanso umboni kumeneko. Pambuyo polandila cilimbikitso cimeneco, Paulo ayenela anamva kukhala wotetezeka monga mwana wofungatiwa na atate ake. w20.11 12 ¶1, 3; 13 ¶4

Cinayi, May 26

Ciyembekezo cimene tili nacoci. . . , n’cotsimikizika ndiponso cokhazikika.—Aheb. 6:19.

Ciyembekezo cathu ca Ufumu “cili ngati nangula wa miyoyo yathu,” ndipo cimatithandiza kukhalabe olimba ngakhale pa mikhalidwe yovuta kapena tikakhala na nkhawa. Sinkha-sinkhani pa lonjezo la Yehova lakuti kutsogolo maganizo olefula adzathelatu. (Yes. 65:17) Yelekezani kuti muli m’dziko latsopano la mtendele, mmene simudzakhalanso zinthu zobweletsa nkhawa. (Mika. 4:4) Mudzalimbitsanso ciyembekezo canu pamene muuzako ena za ciyembekezo cimeneci. Conco, citani zonse zotheka pa nchito yolalikila na kupanga ophunzila. Mukatelo, ‘ciyembekezo canu cidzakhala cotsimikizika mpaka mapeto.’ (Aheb. 6:11) Pamene mapeto a dongosolo lino akuyandikila, tidzakumana na mavuto ambili amene angatibweletsele nkhawa. Tiyenela kukhala osatekeseka pamene tikumana na mavuto, osati mwa mphamvu zathu, koma mwa kudalila kwathu Yehova. Tiyeni tionetse mwa zocita zathu kuti timakhulupilila lonjezo la Yehova lakuti: “Mudzakhala amphamvu mukakhala osatekeseka ndi acikhulupililo.”—Yes. 30:15. w21.01 7 ¶17-18

Cisanu, May 27

Yehova ndi wacikondi cacikulu.—Yak. 5:11.

Onani kuti Yakobo 5:11 ichula cikondi cacikulu ca Yehova pamodzi na khalidwe la cifundo, limene limatipangitsanso kufuna kumuyandikila. (Eks. 34:6) Imodzi mwa njila zimene Yehova amationetsela cifundo ni mwa kutikhululukila zolakwa zathu. (Sal. 51:1) M’Baibo, mawu akuti cifundo amaphatikizapo zambili osati cabe kukhululukila ena. Cifundo ni mmene munthu amakhudzikila mtima kwambili akaona wina akuvutika, ndipo amakakamizika kucitapo kanthu kuti am’thandize munthuyo. Yehova amanena kuti ni wofunitsitsa kwambili kutithandiza, kuposa ngakhale mmene mayi amamvelela pofuna kuthandiza mwana wake. (Yes. 49:15) Tikamavutika, mwa cifundo cake Yehova amakhudzika kuti atithandize. (Sal. 37:39; 1 Akor. 10:13) Tingaonetse cifundo abale na alongo athu mwa kuwakhululukila, komanso kupewa kuwasungila cakukhosi akatilakwila. (Aef. 4:32) Koma njila yaikulu imene tingaonetsele cifundo, ni mwa kuthandiza abale na alongo athu akakhala pa mavuto. Timatengela Yehova amene ni citsanzo capamwamba kwambili pa kuonetsa cifundo.—Aef. 5:1. w21.01 21 ¶5

Ciŵelu, May 28

Khristu . . . [anakusiilani] citsanzo kuti mutsatile mapazi ake mosamala kwambili.—1 Pet. 2:21.

Pali zinthu zimene mutu wa banja ayenela kupewa. Sayenela kutangwanika kwambili na nchito ya kuthupi cakuti n’kulephela kusamalila bwino banja lake mwauzimu, komanso kulithandiza kumva kuti n’lotetezeka. Amafunikanso kuphunzitsa banja lake. Yehova amatiphunzitsa na kutilangiza cifukwa amafuna kutithandiza. (Aheb. 12:7-9) Mofanana na Atate wake, Yesu mwacikondi amaphunzitsa anthu amene ali pansi pa ulamulilo wake. (Yoh. 15:14, 15) Amapeleka uphungu mwamphamvu koma mokoma mtima. (Mat. 20:24-28) Iye amadziŵa kuti ndife opanda ungwilo, ndipo nthawi zambili timalakwa. (Mat. 26:41) Mutu wa banja amene amatengela citsanzo ca Yehova na Yesu amakumbukila kuti a m’banja lake ni opanda ungwilo. Iye ‘sapsela mtima’ mkazi wake kapena ana ake. (Akol. 3:19) M’malomwake, amaseŵenzetsa mfundo ya pa Agalatiya 6:1 na kuthandiza a m’banja lake “ndi mzimu wofatsa” pokumbukila kuti nayenso ni wopanda ungwilo. Mofanana na Yesu, iye amazindikila kuti njila yabwino yophunzitsila banja lake ni kukhala citsanzo cabwino. w21.02 6-7 ¶16-18

Sondo, May 29

Copuma ciliconse citamande Ya.—Sal. 150:6.

Kupitila mu nsembe ya dipo, Yehova anagula moyo wa aliyense mumpingo. (Maliko 10:45; Mac. 20:28; 1 Akor. 15:21, 22) Conco m’pake kuti anasankha Yesu, amene anapeleka moyo wake monga dipo kuti akhale mutu wa mpingo. Pokhala mutu wathu, Yesu ali na mphamvu zopanga malamulo amene munthu aliyense payekha, mabanja, komanso mpingo uyenela kutsatila. Iye alinso na mphamvu zoonetsetsa kuti malamulowo akutsatilidwa. (Agal. 6:2) Koma Yesu sapanga cabe malamulo. Amatidyetsa komanso amakonda aliyense wa ife. (Aef. 5:29) Alongo amaonetsa kuti amalemekeza Khristu mwa kutsatila citsogozo ca amuna amene iye anawaika monga otsogolela. Abale amaonetsa kuti amamvetsa dongosolo la umutu mwa kulemekeza alongo. Ngati onse mumpingo amvetsa na kulemekeza dongosolo la umutu, mumpingo mumakhala mtendele. Ndipo koposa zonse, timatamanda Atate wathu wakumwamba wacikondi, Yehova. w21.02 18-19 ¶14-17

Mande, May 30

Davide anayamba kufunsila kwa Yehova.—1 Sam. 30:8.

Panthawi imene Davide na asilikali ake anali kukhala othaŵa-thaŵa, anasiya mabanja awo n’kupita kukamenya nkhondo. Pamene asilikaliwo anali kunkhondo, adani anafunkha zinthu m’nyumba zawo na kutenga mabanja awo n’kupita nawo. Pokhala kuti Davide anali katswili pa nkhondo, akanaganiza kuti angapeze njila yabwino kwambili yopulumutsila anthu amene anagwidwawo. Koma Davide anayang’ana kwa Yehova kuti amutsogolele. Davide anafunsila kwa Yehova kuti: “Kodi ndithamangitse gulu la acifwambali?” Yehova anauza Davide kuti acite zimenezo ndipo anamutsimikizila kuti adzapambana. (1 Sam. 30:7-10) Kodi mungaphunzilepo ciani pa cocitika cimeneci? Funsilani malangizo kwa ena musanapange zosankha. Funsilani kwa makolo anu. Mungapezenso malangizo abwino mwa kukambilana na akulu amene ni aciyambakale. Yehova amawadalila amuna oikidwa amenewa, ndipo inunso mungawadalile. Yehova amawaona kuti ni “mphatso” mumpingo. (Aef. 4:8) Mukamatengela cikhulupililo cawo na kumvela malangizo anzelu amene iwo angapeleke, mudzapindula kwambili. w21.03 4-5 ¶10-11

Ciŵili, May 31

[Palibe cidzatha] kutilekanitsa ndi cikondi ca Mulungu. —Aroma 8:38, 39.

Yesu anakamba kuti ngati sitiseŵenzetsa zimene timaphunzila, tili monga munthu amene wamanga nyumba yake pamcenga. Iye amagwila nchito molimbika koma amangowononga mphamvu zake. Cifukwa ciani? Cifukwa cimphepo na madzi zikawomba, nyumbayo imagwa. (Mat. 7:24-27) Mofananamo, ngati sitiseŵenzetsa zimene tinaphunzila, ndiye kuti tinangotaya cabe nthawi yathu. Ndipo cikhulupililo cathu cikayesedwa na mavuto kapena cizunzo, sicidzalimba. Koma tikaphunzila na kuseŵenzetsa zimene taphunzilazo, timapanga zosankha zabwino, timakhala na mtendele woculuka, komanso cikhulupililo cathu cimalimba. (Yes. 48:17, 18) Kuti tisungebe umphumphu wathu pa mayeselo, tiyenela kudalila Yehova mwa kum’fikila m’pemphelo na kukhalabe na pulogilamu yabwino yophunzila Baibo. Ndipo nthawi zonse tifunika kukumbukila kuti cimodzi mwa zinthu zofunika kwambili zimene tingacite ni kupeleka ulemelelo kwa Yehova. Tingakhale wotsimikiza kuti Yehova sadzatisiya konse ndipo palibe cimene wina aliyense angacite coletsa kuti Yehova atikonde.—Aheb 13:5, 6. w21.03 15 ¶6; 18 ¶20

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani