July
Cisanu, July 1
Ulamulilo wonse wapelekedwa kwa ine kumwamba ndi padziko lapansi.—Mat. 28:18.
Tifunika kukhala pa ubwenzi na Yesu kuti mapemphelo athu ayankhidwe. Izi sizitanthauza kungokamba mwamwambo cabe mawu akuti “m’dzina la Yesu,” kumapeto kwa pemphelo. Tifunika kudziŵa mmene Yehova amaseŵenzetsela Yesu poyankha mapemphelo athu. Yesu anauza atumwi kuti: “Ciliconse cimene mudzapemphe m’dzina langa, ine ndidzacicita.” (Yoh. 14:13) N’zoona kuti Yehova ndiye amamvetsela na kuyankha mapemphelo athu. Koma anapatsa mphamvu Yesu yocita zimene Yehovayo walamula. Conco, Mulungu asanayankhe mapemphelo athu, amaona ngati ife timatsatila malangizo amene Yesu anatipatsa. Mwacitsanzo, Yesu anati: “Mukamakhululukila anthu macimo awo, inunso Atate wanu wakumwamba adzakukhululukilani. Koma ngati simukhululukila anthu macimo awo, Atate wanu sadzakukhululukilani macimo anu.” (Mat. 6:14, 15) Ndithudi, n’kofunika kwambili kuti tizicitila ena zinthu mokoma mtima monga mmene Yehova na Yesu amacitila na ife! w20.04 22 ¶6
Ciŵelu, July 2
Tikucita izi kuti musiye zacabe-cabe zimenezi ndi kutembenukila kwa Mulungu wamoyo. —Mac. 14:15.
Mtumwi Paulo anali kuganizila zinthu zimene zikanacititsa cidwi omvetsela ake. Ndiyeno, anali kusintha ulaliki wake. Mwacitsanzo, khamu la anthu limene anakamba nalo ku Lusitara linali kudziŵako pang’ono cabe Malemba, kapena silinali kuwadziŵa n’komwe. Conco, Paulo anakamba nawo mfundo zimene akanazimvetsetsa. Anakamba za kuculuka kwa zokolola komanso mwayi wosangalala na moyo. Ndipo anaseŵenzetsa mawu na zitsanzo zimene iwo akanazimvetsetsa mosavuta. Seŵenzetsani luso la kuzindikila kuti mudziŵe nkhani zimene anthu a m’gawo lanu angacite nazo cidwi, ndiyeno sinthani ulaliki wanu kuti ugwilizane na zimene amakonda. Kodi mungadziŵe bwanji zimene munthu angacite nazo cidwi mukamufikila kuti mumulalikile kapena mukafika pakhomo pake? Khalani chelu. Mwacitsanzo, mwina mungam’peze akulima, kuŵelenga buku, kukonza njinga kapena motoka, kapenanso kucita zinthu zina. Ngati m’poyenela, mungaloŵele ku zimene iye akucita kuti muyambe kukambilana naye. (Yoh. 4:7) Ngakhale zovala zimene munthu wavala zingatithandize kudziŵa zinazake zokhudza munthuyo, monga dziko lake, nchito imene amagwila, kapena timu ya maseŵela imene amakonda. w20.04 11 ¶11-12
Sondo, July 3
[Mutulileni] nkhawa zanu zonse [Mulungu], pakuti amakudelani nkhawa.—1 Pet. 5:7.
Cifukwa cokhala na nkhawa yaikulu, abale na alongo ena amacita mantha kwambili, ndiponso amacita manyazi akakhala pa gulu. Ngakhale kuti cimawavuta kukhala pa gulu, amayesetsabe kupezeka pa misonkhano yampingo, yadela, komanso yacigawo. Iwo samasuka kukamba ndi anthu amene sawadziŵa. Olo n’telo, amayesetsa kulankhula ndi anthu mu ulaliki. Ngati muli na vuto laconco, dziŵani kuti simuli mwekha. Pali ambili amene ali na vuto limeneli. Dziŵani kuti Yehova amakondwela na khama limene mumaonetsa pomutumikila na mtima wonse. Kupitiliza kwanu kum’tumikila ni umboni wakuti iye akukudalitsani ndiponso akukupatsani mphamvu. (Afil. 4:6, 7) Ngati mupitiliza kutumikila Yehova olo kuti muli na mavuto amene amakulepheletsani kucita zambili, musakayikile kuti iye amakondwela na zimene mumacita. Ambili a ife sitili na thanzi labwino, koma tikuthamangabe mopilila pa mpikisano wokalandila moyo. (2 Akor. 4:16) Mwa thandizo la Yehova, tonse tidzathamanga pa mpikisano umenewu mpaka ku mapeto! w20.04 31 ¶20-21
Mande, July 4
Makhalidwe a Mulungu osaoneka . . . akuonekela bwino . . . m’zinthu zimene anapanga.—Aroma 1:20.
Nzelu za Yehova zimaonekela bwino tikaona mmene anapangila dziko lapansi, malo athu okhala. (Aheb. 3:4) Dziko linapangidwa mwapadela cifukwa lili na zonse zofunikila kuti anthufe tipitilize kukhala na moyo. Mwanjila ina, dziko lapansi tingaliyelekezele na nyumba yokhoma imene ili kutali kwambili, ndipo mkati mwake muli anthu ambili. Koma pali mbali zina zosiyana kwambili pakati pa nyumba yotelo na dziko lapansi. Mwacitsanzo, tiyelekezele kuti anthu amene ali m’nyumbayo auzidwa kuti azidzipangila okha mpweya wa oxygen, cakudya, madzi, komanso kuti asamataye kunja zonyansa na zinyalala. Kodi muganiza kuti angakhale na moyo kwa nthawi yaitali? Ayi. Anthuwo angafe posapita nthawi. Mosiyana na izi, dziko lapansi limakwanitsa kucilikiza zamoyo mabiliyoni ambili. Lili na zinthu zonse zimene timafunikila monga mpweya wa oxygen, zakudya, komanso madzi. Ndipo zinthu zofunika zimenezi sizikutha. Ngakhale kuti zonyansa zonse na zinyalala zimatayidwa pamene pano padziko lapansi, dzikoli limakhalabe lokongola komanso labwino kukhalamo. Kodi zimatheka bwanji zimenezi? Yehova anapanga dziko lapansi mwadongosolo kuti lizitha kusintha zonyansa n’kukhala zinthu zabwino zimene tingathe kuziseŵenzetsanso. w20.05 20 ¶3-4
Ciŵili, July 5
Kufa simudzafa ayi.—Gen. 3:4.
Satana anaipitsa dzina la Mulungu mwa kuuza Hava kuti Yehova ni wabodza. Mwa ici, Satana anakhala Mdyelekezi, kapena kuti woneneza. Hava ananyengeka kothelatu. Anakhulupilila zimene Satana anamuuza. (1 Tim. 2:14) Iye anakhulupilila kwambili Satana kuposa Yehova. Izi zinacititsa kuti Hava apange cosankha colakwika kwambili. Anasankha kusamvela Yehova, moti anadya cipatso cimene Yehova anawauza kuti asadye. Pambuyo pake, anapatsako Adamu. (Gen. 3:6) Bwanji tiyelekezele kuti Hava anayankha Satana kuti: “Sinikudziŵa iwe, koma Atate wanga, Yehova, nimawadziŵa, komanso nimawakonda na kuwakhulupilila. Iwo ndiwo anapatsa ine na mwamuna wanga zonse zimene tili nazo. Nanga n’cifukwa ciani ukuwanena? Coka apa!” Yehova akanakondwela kwambili kumva mwana wake wamkazi akukamba mawu ngati amenewa. (Miy. 27:11) Koma onse aŵili, Adamu na Hava, sanali kum’konda Yehova Atate wawo. Pa cifukwa cimeneci, analephela kuikila kumbuyo dzina. w20.06 4 ¶10-11
Citatu, July 6
Akazi amene akulengeza uthenga wabwino ndi khamu lalikulu. —Sal. 68:11.
Alongo athu tifunika kuwayamikila kwambili pa zonse zimene amacita mu utumiki wa Yehova. Nchito zina zimene amacita ni monga kumanga na kukonzanso nyumba zolambililamo, kuthandizila tumagulu tokamba citundu cina, komanso kudzipeleka kukathandizila nchito pa Beteli. Enanso amathandiza pa nchito yopeleka thandizo pakagwa masoka a zacilengedwe, kumasulila mabuku athu, komanso kutumikila monga apainiya ndiponso amishonale. Kuwonjezela apo, akazi amathandiza amuna awo kusamalila maudindo aakulu mumpingo ndi nchito zina m’gulu la Yehova. Popanda kuthandizidwa na akazi awo, abale apaudindo amenewa sangakwanitse kutumikila mokwanila pa udindo wawo monga “mphatso za amuna.” (Aef. 4:8) Akulu anzelu amazindikila kuti alongo ni “khamu lalikulu” la anchito odzipeleka, ndipo nthawi zambili amakhala aluso kwambili pa nchito yolalikila uthenga wabwino. Kuwonjezela apo, akulu amadziŵa kuti alongo acikulile okhulupilika amadziŵa bwino kuthandiza alongo acicepele polimbana na mavuto. (Tito 2:3-5) Kukamba zoona, timafunika kuwayamikila kwambili alongo athu amenewa! w20.09 23-24 ¶13-14
Cinayi, July 7
Atate wanga wakumwamba sakufuna kuti mmodzi wa tianati akawonongeke.—Mat. 18:14.
Yehova saiŵala atumiki ake amene kwa kanthawi analeka kusonkhana komanso kulalikila. Saiŵalanso nchito zimene iwo anacita pom’tumikila. (Aheb. 6:10) Mneneli Yesaya analemba mawu ocititsa cidwi oonetsa mmene Yehova amakondela anthu ake na kuwasamalila. Yesaya anati: “Iye adzaweta gulu lake lankhosa ngati m’busa. Adzasonkhanitsa pamodzi ana a nkhosa ndi dzanja lake, ndipo adzawanyamulila pacifuwa pake.” (Yes. 40:11) Kodi M’busa Wamkulu Yehova amamvela bwanji ngati imodzi mwa nkhosa zake yasocela? Yesu anaonetsa bwino mmene Yehova amamvelela pamene anafunsa ophunzila ake kuti: “Mukuganiza bwanji? Ngati munthu ali ndi nkhosa 100 ndipo imodzi mwa nkhosazo n’kusocela, kodi sangasiye nkhosa 99 zija m’phili ndi kupita kukafunafuna yosocelayo? Akaipeza, ndithu ndikunenetsa, amakondwela kwambili ndi nkhosa imeneyo kusiyana ndi nkhosa 99 zosasocela zija.”—Mat. 18:12, 13. w20.06 19-20 ¶8-9
Cisanu, July 8
Ngati munthu aliyense akuyesetsa kuti akhale woyang’anila, akufuna nchito yabwino.—1 Tim. 3:1.
Timaona kuti ni mwayi kutumikila Yehova pa utumiki uliwonse umene tingakwanitse. (Sal. 27:4; 84:10) Timayamikila ngati m’bale wadzipeleka kucita zambili m’gulu la Yehova. Koma m’bale akapatsidwa udindo, sayenela kudziona kuti ni wofunika kwambili kuposa ena. (Luka 17:7-10) Ayenela kukhala na colinga cotumikila ena modzicepetsa. (2 Akor. 12:15) M’Baibo muli zitsanzo zoticenjeza za anthu amene anacita zinthu modzikuza. Mwacitsanzo, Diotirefe anali munthu wodzikuza. Iye anali kufuna kukhala “woyamba pakati” pa ena mumpingo. (3 Yoh. 9) Nayenso Uziya pa nthawi ina anacita zinthu modzikuza. Anagwila nchito imene siinali udindo wake malinga na malamulo a Yehova. (2 Mbiri 26:16-21) Komanso, Abisalomu anakopa anthu mwacinyengo kuti akhale ku mbali yake cifukwa anali kufunitsitsa kukhala mfumu. (2 Sam. 15:2-6) Zitsanzo za m’Baibo zimenezi, zionetselatu kuti Yehova sakondwela ndi anthu amene amadzifunila ulemelelo. (Miy. 25:27) M’kupita kwa nthawi, anthu odzikuza komanso amene amafuna kuchuka amakumana na mavuto aakulu.—Miy. 16:18. w20.07 4 ¶7-8
Ciŵelu, July 9
Pakuti aliyense ayenela kunyamula katundu wake.—Agal. 6:5.
Mabanja ena acikhristu amasamukila kumaiko ena cifukwa cothaŵa kwawo, kapena kukafuna nchito. Zikakhala conco, ana awo kusukulu amaphunzila citundu ca ku dzikolo. Makolo nawonso angafunikile kuphunzila citundu ca ku dzikolo kuti apeze nchito. Koma bwanji ngati m’delalo muli mpingo kapena kagulu ka citundu cawo? Kodi banjali liyenela kumasonkhana ku mpingo uti? Kodi angafunikile kupita ku mpingo wa citundu ca ku dzikolo kapena wa citundu cawo? Mutu wa banja ufunika kusankha mpingo umene banja lake lizisonkhanako. Popeza iyi ni nkhani ya banja, iye afunika kupanga cosankha moganizila zimene zingapindulitse banja lake. Mulimonse mmene iye angasankhile, tiyenela kulemekeza cosankha cake na kulandila banjalo na manja aŵili mu mpingo wathu.—Aroma 15:7. w20.08 30 ¶17-18
Sondo, July 10
Mulungu anasankha zinthu zofooka za dziko.—1 Akor. 1:27.
Kuti Yehova atipatse mphamvu, sitiyenela kukhala na maganizo akuti mphamvu zakuthupi, maphunzilo, kumene tinakulila, kapena cuma, n’zimene zimatipangitsa kukhala anthu ofunika kwa Yehova. Ndipo pakati pa anthu a Mulungu “si ambili amene anthu amawaona kuti ndi anzelu, . . . si ambili amphamvu . . . si ambili a m’mabanja acifumu.” (1 Akor. 1:26) Conco, ngati pali zovuta zina zimene zimakupangitsani kudziona ngati ofooka, musalole kuti zikulefuleni potumikila Yehova. M’malomwake, muziona kuti zinthu zimenezo zimakupatsani mwayi woona mphamvu za Yehova zikugwila nchito pa inu. Mwacitsanzo, ngati mumaopa anthu amene amatsutsa zimene mumakhulupilila, pemphelani kwa Yehova kuti akulimbitseni mtima kuti mukwanitse kufotokoza zimene mumakhulupilila. (Aef. 6:19, 20) Ngati mukuvutika na matenda aakulu, pemphani Yehova kuti akupatseni mphamvu zofunikila kuti mupitilize kucita zilizonse zimene mungathe pom’tumikila. Mukamaona kuti Yehova akukuthandizani, cikhulupililo canu cimapitilizabe kukula ndipo mumakhala wolimba mwauzimu. w20.07 16 ¶9
Mande, July 11
[Funafuna] Ufumu coyamba. —Mat. 6:33.
Ngati tifuna kuika Ufumu wake patsogolo mu umoyo wathu, tifunika kukhala monga Abulahamu, amene anadzimana zinthu zina popanda kudandaula kuti akondweletse Mulungu. (Maliko 10:28-30; Aheb. 11:8-10) Musayembekezele kukhala na umoyo wopanda mavuto. Ngakhale anthu amene atumikila Yehova kwa moyo wawo wonse amakumananso na mavuto. (Yak. 1:2; 1 Pet. 5:9) Masiku ano tili na cifukwa comveka cosumikila maganizo athu pa madalitso akutsogolo. Zocitika padzikoli zionetselatu kuti tili kumapeto kweni-kweni kwa masiku otsiliza a dziko loipali. Limodzi mwa madalitso amene tidzasangalala nawo pansi pa Ufumu, ni kuona okondedwa athu akuukitsidwa. Panthawiyo, Yehova adzadalitsa Abulahamu cifukwa ca cikhulupililo cake na kuleza mtima kwake, mwa kumuukitsa pamodzi na banja lake kuti akhale na moyo pano padziko lapansi. Kodi mudzakhalamo kuti mukawalandile? Mudzakhalamo ngati mofanana na Abulahamu, ndimwe okonzeka kudzimana zinthu zina kaamba ka Ufumu wa Mulungu, ngati mukhalabe na cikhulupililo olo kuti mukumana na mavuto, komanso ngati muyesetsa kuyembekezela Yehova moleza mtima.—Mika 7:7. w20.08 5-6 ¶13-14; 7 ¶17
Ciŵili, July 12
Sonyeza kukhulupilika kwako mpaka imfa, ndipo ndidzakupatsa mphoto ya moyo.—Chiv. 2:10.
Tidziŵa kuti ngati adani athu angatiphe, Yehova adzatiukitsa. Tidziŵa kuti palibe ciliconse cimene angacite cimene cingatilekanitse na cikondi ca Yehova. (Aroma 8:35-39) Ndithudi, Yehova waonetsa nzelu zapadela potipatsa ciyembekezo cakuti akufa adzauka! Ciyembekezo cimeneci, cimatithandiza kuti tisamaope imfa ngati anthu amene ali kumbali ya Satana atiopseza kuti atipha tikakana kucita zinazake. Cimatithandizanso kukhala olimba mtima kuti tikhalebe okhulupilika kwa Yehova. Ngati adani a Yehova akuopsezani kuti akuphani, kodi mudzakhala na cidalilo cakuti Yehova adzakuukitsani? Kodi mungadziŵe bwanji kuti mudzakhala naco? Njila imodzi ni mwa kudzifunsa kuti, ‘Kodi zosankha zing’ono-zing’ono zimene nimapanga tsiku lililonse zimaonetsa kuti nimadaliladi Yehova?’ (Luka 16:10) Funso lina lingakhale lakuti, ‘Kodi mu umoyo wanga nimaonetsadi kuti nimakhulupilila lonjezo la Yehova lakuti adzanithandiza kupeza zosoŵa zanga zakuthupi ngati niika zinthu za Ufumu patsogolo?’ (Mat. 6:31-33) Ngati mwayankha kuti inde pa mafunso amenewa, ndimwe okonzeka kulimbana na ciyeso ciliconse cimene mungakumane naco kutsogolo.—Miy. 3:5, 6. w20.08 17-18 ¶15-16
Citatu, July 13
Cita ciliconse cotheka kuti usonyeze kuti ndiwe wovomelezeka pamaso pa Mulungu, wanchito wopanda cifukwa cocitila manyazi ndi nchito imene wagwila, ndiponso wophunzitsa ndi kufotokoza bwino mawu a coonadi.—2 Tim. 2:15.
Tifunika kukhala aluso kwambili poseŵenzetsa Mawu a Mulungu. Tingaphunzile ena mwa maluso amenewa pamisonkhano yathu. Koma kuti tikwanitse kuthandiza ena kukhulupilila kuti mfundo za coonadi ca m’Baibo n’zamtengo wapatali, tifunika kumaiŵelenga nthawi zonse. Timafunika kuphunzila Mawu a Mulungu kuti tilimbitse cikhulupililo cathu. Kucita izi kumafuna zambili osati kungoŵelenga cabe Baibo. Timafunikanso kusinkha-sinkha pa zimene taŵelenga na kufufuza m’mabuku athu, n’colinga cakuti timvetsetse na kuwaseŵenzetsa bwino Malemba. (1 Tim. 4:13-15) Tikatelo, tidzakwanitsa kuseŵenzetsa Mawu a Mulungu pophunzitsa ena. Kucita izi kumafunanso zambili osati kungoŵelengela munthu Baibo. Timafunika kuthandiza omvela athu kumvetsetsa vesi imene taŵelenga. Timafunanso kuwathandiza kuona mmene igwilila nchito pa iwo. Mwa kutsatila ndandanda yathu ya kuŵelenga Baibo nthawi zonse, tingakulitse luso lathu loseŵenzetsa bwino Mawu ouzilidwa a Mulungu pophunzitsa ena.—2 Tim. 3:16, 17. w20.09 28 ¶12
Cinayi, July 14
Ganizilani mozama za [Yesu] . . . , kuti musatope ndiponso kuti musalefuke.—Aheb. 12:3.
Kodi n’ciani cingatithandize kuikabe maganizo athu pa nchito yolalikila? Cimodzi cimene cingatithandize ni kuganizila zimene Yehova akucita pofuna kutithandiza mwauzimu. Mwacitsanzo, watipatsa cakudya cauzimu coculuka kupitila m’zofalitsa zopulintidwa na za pazipangizo, mavidiyo na zofalitsa zongomvetsela, komanso pa JW Broadcasting. Tangoganizilani! Pa webusaiti yathu pali zofalitsa na zinthu zina m’zitundu zopitilila 1,000. (Mat. 24:45-47) Cina cimene cingatithandize kuikabe maganizo athu pa nchito yolalikila ni kutengela citsanzo ca Yesu. Iye sanalole ciliconse kumuceutsa pa nchito yake yocitila umboni coonadi. (Yoh. 18:37) Iye sanakopeke pamene Satana anamuonetsa “maufumu onse a padziko ndi ulemelelo wawo.” Sanakopekenso pamene anthu anafuna kumulonga ufumu. (Mat. 4:8, 9; Yoh. 6:15) Iye sanakopeke na zinthu zakuthupi, kapena kucita mantha cifukwa ca citsutso coopsa. (Luka 9:58; Yoh. 8:59) Ngati cikhulupililo cathu cayesedwa, cimene cingatithandize kuikabe maganizo pa nchito yolalikila ni kukumbukila malangizo a mtumwi Paulo a mu lemba la lelo. w20.09 9-10 ¶6-7
Cisanu, July 15
Muzitsanzila ine, monga mmene inenso ndimatsanzilila Khristu.—1 Akor. 11:1.
N’zokondweletsa ngako kuti mumpingo tili na alongo ambili amene amatumikila mwakhama! Alongo amapeleka ndemanga pa misonkhano, komanso amatengako mbali pa nchito yolalikila. Ena amagwila nchito yokonzanso Nyumba za Ufumu, ndipo amaonetsa kuti amakonda Akhristu anzawo. Komabe, iwo amakumana na mavuto. Ena amasamalila makolo awo okalamba. Ena amatsutsidwa na a m’banja lawo. Enanso amalela okha ana, ndipo amagwila nchito mwakhama kuti apezele anawo zofunikila. N’cifukwa ciani tifunika kuthandiza alongo athu? Cifukwa cakuti anthu m’dzikoli kambili salemekeza akazi. Kuwonjezela apo, Baibo imatilimbikitsa kuti tiziwathandiza. Mwacitsanzo, mtumwi Paulo analangiza mpingo wa ku Roma kuti ulandile mlongo Febe na ‘kumuthandiza pa nkhani iliyonse imene angafune thandizo lawo.’ (Aroma 16:1, 2) Paulo anacokela m’gulu la anthu amene anali kuona kuti akazi ni anthu otsika komanso osafunika. Koma atakhala Mkhristu, anatengela citsanzo ca Yesu, ndipo anayamba kulemekeza akazi na kucita nawo zinthu mokoma mtima. w20.09 20 ¶1-2
Ciŵelu, July 16
Mukaphunzitse anthu . . . , kuti akhale ophunzila anga . . . , ndi kuwaphunzitsa kusunga zinthu zonse zimene ndinakulamulilani.—Mat. 28:19, 20.
Tifunika kuthandiza maphunzilo athu a Baibo kukhala na cikhumbo ca kulalikila uthenga wabwinoTingafunse wophunzila Baibo wathu mafunso monga aya: “Kodi mwapindula bwanji cifukwa coseŵenzetsa mfundo za m’Baibo? Kodi muganiza kuti ena afunika kumvela uthenga umenewu? Mungacite ciani kuti muwathandize?” (Miy. 3:27; Mat. 9:37, 38) Kumbukilani kuti Yesu anatilangiza kuphunzitsa anthu “kusunga zinthu zonse” zimene analamula. Mosakaikila, izi ziphatikizapo malamulo aŵili aakulu koposa—kukonda Mulungu na kukonda mnansi wathu. Malamulo onse aŵiliwa amakhudza nchito yolalikila na kupanga ophunzila. (Mat. 22:37-39) Cikondi ndiye cimene cimatilimbikitsa kulalikila uthenga wabwino. Komabe, ophunzila Baibo ena angacite mantha kutengako mbali mu nchito yolalikila. Koma tingatsimikizile ophunzilawo kuti mwa thandizo la Yehova, pang’ono-mpang’ono angathetse mantha awo oopa anthu.—Sal. 18:1-3; Miy. 29:25. w20.11 3 ¶6-8
Sondo, July 17
Sitinaleke kukupemphelelani.—Akol. 1:9.
Pokonzekela kukasogoza phunzilo, pemphelani kwa Yehova za wophunzila wanu na zosoŵa zake. M’pempheni kuti akuthandizeni kukaphunzitsa zocokela m’Baibo, mwa njila yom’fika pamtima wophunzila wanu. Musaiŵale kuti colinga canu ni kum’thandiza kupita patsogolo mpaka kukabatizika. Wophunzila afunika azikambilana na Yehova. Motani? Mwa kumvetsela kwa Yehova, komanso kukamba naye. Angamvetsele kwa Mulungu mwa kuŵelenga Baibo tsiku na tsiku. (Yos. 1:8; Sal. 1:1-3) Wophunzila wanu azikamba na Yehova mwa kupemphela tsiku lililonse. Muzipeleka mapemphelo okhudza mtima kuciyambi na kumapeto kwa phunzilo. Komanso, muzipemphela naye limodzi na kum’chula m’pemphelo. Pamene amvetsela mapemphelo anu, iye adzaphunzila kupemphela mocokela pansi pa mtima na kupeleka mapemphelo ake kwa Yehova Mulungu, kupitila m’dzina la Yesu Khristu. (Mat. 6:9; Yoh. 15:16) Tangoganizani mmene kuŵelenga Baibo tsiku na tsiku (ndiko kumvetsela kwa Yehova), komanso kupemphela kwa iye (ndiko kukamba na Yehova) kungathandizile wophunzila wanu kumuyandikila kwambili Mulungu!—Yak. 4:8. w20.10 8 ¶8; 9 ¶10-11
Mande, July 18
Kusunga umodzi wathu mwa mzimuwo, ndi mwamtendele monga comangila cotigwilizanitsa. —Aef. 4:3.
Monga zinalili m’nthawi ya Akhristu oyambilila, gulu la Yehova masiku anonso limayesetsa kusungitsa dongosolo na mtendele. (Mac. 16:4, 5) Mwacitsanzo, ngati mungapezeke pa Phunzilo la Nsanja ya Mlonda ku mpingo wina, ngakhale ku dziko lina, mungadziŵiletu mmene phunzilolo licitikile, ngakhalenso nkhani imene muphunzile. Panthawi yomweyo mudzakhala womasuka! Ndithudi, palibenso cina cingatheketse mgwilizano wotelewu, kupatulapo mzimu wa Mulungu! (Zef. 3:9) Kodi mungacite ciani? Dzifunseni kuti: ‘Kodi nimalimbikitsa mgwilizano na mtendele mu mpingo? Kodi nimagonjela kwa amene amatsogolela? Kodi ena mu mpingo anganidalile, maka-maka nikapatsidwa mbali zakuti nisamalile? Kodi nimasunga nthawi, kuthandiza ena, komanso kufunitsitsa kutumikila?’ (Yak. 3:17) Ngati muona kuti pali mbali zimene mufunika kuwongolela, pemphani mzimu woyela. Mukamalola mzimu woyela kuti ukuumbeni na kukutsogolelani pa zocita zanu, abale na alongo anu adzakukondani kwambili. Adzakuonani kuti ndimwe wofunika. w20.10 23 ¶12-13
Ciŵili, July 19
Muzicita zimene mawu amanena, osati kungomva cabe.—Yak. 1:22.
Mawu a Mulungu ali monga galasi kwa ife. (Yak. 1:23-25) Ambili a ife timayang’ana pa galasi m’mawa uliwonse tisanacoke pa nyumba. Kucita izi, kumatithandiza kuti tidzikonze bwino tisanaonekele kwa anthu. Mofananamo, tikamaŵelenga Baibo tsiku lililonse, tidzaona mbali zofunika kusintha pa kaganizidwe kanthu na kaonedwe kathu ka zinthu. Ambili amakonda kuŵelenga lemba la tsiku m’mawa uliwonse asanacoke panyumba. Amafuna kuti zimene aŵelenga zikhale m’maganizo awo. Ndiyeno tsiku lonselo, amayesa kupeza mipata yoseŵenzetsa uphungu wa m’Mawu a Mulungu. Kuwonjezela apo, tiyenelanso kukhala na pulogilamu yophunzila Baibo, yophatikizapo kuŵelenga na kusinkha-sinkha Mawu a Mulungu tsiku lililonse. Iyi ingaoneke kuti ni mbali yocepa, koma ni yofunika kwambili kuti tipitilizebe kuyenda panjila yopanikiza ya ku moyo. Mawu a Mulungu tingawayelekezele na makina a Ekiselo (X-ray), amene amaunika mkati mwa thupi la munthu. Koma kuti tipindule na uphungu wa m’Baibo, komanso wocokela kwa oimilako Mulungu, tiyenela kukhala odzicepetsa. w20.11 18 ¶3; 20 ¶8
Citatu, July 20
Mipingo inapitiliza kulimba m’cikhulupililo ndipo ciŵelengelo cinapitiliza kuwonjezeka tsiku ndi tsiku.—Mac. 16:5.
Ngakhale kuti Akhristu a m’nthawi ya atumwi anali kuzunzidwa kaŵili-kaŵili, nthawi zina anali kukhala pa mtendele. Kodi ophunzila okhulupilikawo anali kuigwilitsila nchito bwanji nthawi ya mtendele imeneyo? Anali kulalikila uthenga wabwino mwakhama. Buku la Machitidwe limakamba kuti iwo anali “kuyenda moopa Yehova.” Akhristuwo anapitiliza kulalikila uthenga wabwino, ndipo zotulukapo zake zinali zakuti mpingo “unali kukulilakulila.” N’zoonekelatu kuti Yehova anawadalitsa cifukwa cogwila nchito yolalikila mwakhama pa nthawi ya mtendele. (Mac. 9:26-31) Ophunzila a m’nthawi ya atumwi anali kulalikila uthenga wabwino pa mpata uliwonse umene apeza. Mwacitsanzo, pamene mtumwi Paulo anaona kuti khomo lalikulu la utumiki lamutsegukila ali ku Efeso, anayamba kulalikila na kupanga ophunzila mumzindawo. (1 Akor. 16:8, 9) Ophunzilawo anawonjezela cangu cawo polalikila “uthenga wabwino wa mawu a Yehova.” (Mac. 15:30-35) Kodi panakhala zotulukapo zotani? Lemba la tsiku la lelo latiuza. w20.09 16 ¶6-8
Cinayi, July 21
Imfa inafika kudzela mwa munthu mmodzi.—1 Akor. 15:21.
Adamu atacimwa, anabweletsa mavuto aakulu pa iyemwini komanso pa mbadwa zake. Mpaka pano timavutika na zotulukapo zoŵaŵa za kusamvela kwake. Koma cifukwa cakuti Mulungu anaukitsa Mwana wake, tili na ciyembekezo ca tsogolo labwino. “Kuuka kwa akufa kunafikanso kudzela mwa munthu mmodzi,” Yesu. Paulo anati: “Pakuti monga mwa Adamu onse akufa, momwemonso mwa Khristu onse adzapatsidwa moyo.” (1 Akor. 15:22) Kodi Paulo anatanthauzanji pamene anati “mwa Adamu onse akufa”? Paulo anali kukamba za mbadwa za Adamu, zimene zinatengela ucimo na kupanda ungwilo kucokela kwa Adamu, ndipo zimafa. (Aroma 5:12) Adamu sali pagulu la amene “adzapatsidwa moyo.” Dipo la Khristu siliphimbanso macimo a Adamu, cifukwa iye anali munthu wangwilo amene anasankha dala kusamvela Mulungu. Cilango ca Adamu n’cofanana na cimene adzalandila anthu amene “Mwana wa munthu” adzaŵaweluza kuti ni “mbuzi,” kutanthauza kuti ‘adzawonongedwa kothelatu.’—Mat. 25:31-33, 46; Aheb. 5:9. w20.12 5 ¶13-14
Cisanu, July 22
Yehova ali pamwamba, amaona wodzicepetsa.—Sal. 138:6.
Ngati sitinalandile utumiki winawake, tifunika kuganizila za Angelo okhulupilika. Panthawi ya ulamulilo wa Mfumu Ahabu, Yehova anapempha angelo kuti apeleke malingalilo a mmene angapusitsile mfumu yoipa imeneyo. Angelo osiyana-siyana anapeleka malingalilo awo. Koma Mulungu anasankha cabe lingalilo la mngelo mmodzi na kumuuza kuti lingalilo lakelo lidzagwiladi nchito. (1 Maf. 22:19-22) Kodi angelo okhulupilika enawo analefuka, mwina n’kuganiza kuti, ‘N’cifukwa n’ciani n’nadzivutitsa kupelekapo malingalilo anga?’ Palibe cionetsa kuti iwo anacita zimenezi. Angelo ni odzicepetsa kwambili, ndipo amafuna kuti ulemelelo wonse upite kwa Yehova. (Ower. 13:16-18; Chiv. 19:10) Ikani maganizo anu pa mwayi umene tili nawo wochedwa na dzina la Mulungu na kulengeza Ufumu wake. Mwayi wa mautumiki si ndiwo umatipangitsa kukhala ofunika kwambili kwa Mulungu. Koma tikakhala odzicepetsa m’pamene timakhala ofunika kwa Yehova komanso kwa abale athu. Conco, m’condeleleni Yehova kuti akuthandizeni kukhalabe wodzicepetsa. Muzisinkha-sinkha pa zitsanzo zabwino za anthu odzicepetsa ochulidwa m’Mawu ake. Khalani odzipeleka na mtima wonse kutumikila abale anu mulimonse mmene mungathele.—1 Pet. 5:5. w20.12 26 ¶16-17
Ciŵelu, July 23
Landilani cisoti colimba cacipulumutso, ndiponso lupanga la mzimu, lomwe ndilo mawu a Mulungu.—Aef. 6:17.
Cisoti colimba cacipulumutso ni ciyembekezo cimene Yehova amatipatsa. Ciyembekezo cimeneci cidzatipulumutsa ku imfa, cifukwa iye adzaukitsa onse ocita cifunilo cake. (1 Ates. 5:8; 1 Tim. 4:10; Tito 1:1, 2) Ciyembekezo cacipulumutso cimateteza kaganizidwe kathu. Ciyembekezo cimeneci cimatithandiza kusumika maganizo athu pa malonjezo a Mulungu, ndiponso cimatithandiza kuona mavuto moyenela. Timacivala cisoti cimeneci mwa kuona zinthu mmene Mulungu amazionela. Mwacitsanzo, timadalila Mulungu osati cuma cosadalilika. (Sal. 26:2; 104:34; 1 Tim. 6:17) Lupanga la mzimu ni Mawu a Mulungu, Baibo. Lupanga limeneli lili na mphamvu zotha kuvumbula cinyengo na kumasula anthu kuukapolo wa ziphunzitso zabodza, komanso ku zizoloŵezi zoipa. (2 Akor. 10:4, 5; 2 Tim. 3:16, 17; Aheb. 4:12) Timaphunzila moseŵenzetsela bwino lupanga limeneli mwa kucita phunzilo laumwini komanso kupitila m’maphunzilo amene timalandila m’gulu la Mulungu.—2 Tim. 2:15. w21.03 27 ¶4; 29 ¶10-11
Sondo, July 24
Ndinali pacilumba ca Patimo cifukwa colankhula za Mulungu ndi kucitila umboni za Yesu.—Chiv. 1:9.
Ngakhale pamene anali m’ndende kaamba kolalikila za Yesu, mtumwi Yohane anaonetsa kuti anali kukonda ena. Mwacitsanzo, iye analemba masomphenya amene analandila na kuwatumiza ku mipingo kuti adziŵe “zinthu zimene ziyenela kucitika posacedwapa.” (Chiv. 1:1) Ndipo zioneka kuti pambuyo potulutsidwa m’ndende pa cisumbu ca Patimo, Yohane analemba uthenga wake wabwino wokamba za umoyo na utumiki wa Yesu. Iye analembanso makalata atatu kuti alimbikitse abale na alongo ake. Na imwe mungatengele citsanzo ca Yohane ca kukhala na umoyo wodzimana Mungaonetse kuti mumakonda anthu mwa zimene musankha kucita na moyo wanu. Dziko la Satana limafuna kuti muthele nthawi yanu yonse na mphamvu zanu pofuna kudzipindulitsa nokha, mwa kufuna-funa ndalama komanso kuyesa kudzipangila dzina. Koma alengezi a Ufumu odzimana padziko lonse lapansi amathela nthawi yawo yoculuka pa kulalikila za uthenga wabwino, na kuthandiza anthu kuyandikila Yehova. w21.01 10 ¶9-10
Mande, July 25
Yonatani . . . anayamba kukonda Davide ngati mmene anali kudzikondela yekha.—1 Sam. 18:1.
Yonatani akanatha kucitila nsanje Davide. Monga mwana wa Mfumu Sauli, iye akanaumilila kuti ndiye woyenelela kuloŵa ufumu wa atate ake. (1 Sam. 20:31) Koma Yonatani anali wodzicepetsa, ndipo anali wokhulupilika kwa Yehova. Conco, iye anacilikiza Davide na mtima wonse podziŵa kuti Yehova ndiye anam’sankhilatu kukhala mfumu yakutsogolo. Iye analinso wokhulupilika kwa Davide, ngakhale kuti kucita zimenezi kunaputa mkwiyo wa Sauli. (1 Sam. 20:32-34) Yonatani anali na cikondi cacikulu pa Davide. Conco sanamuone monga wopikisana naye. Yonatani anali waluso polasa mivi na uta, ndipo anali msilikali wolimba mtima. Iye na atate ake, Sauli, anali kudziŵika kuti anali “aliwilo kuposa ciwombankhanga,” komanso “amphamvu kuposa mikango.” (2 Sam. 1:22, 23) Conco, Yonatani akanadzitukumula cifukwa ca zipambano zake. Komabe, analibe mzimu wa mpikisano ndipo sanam’citile nsanje Davide. M’malomwake, anali kucita cidwi na kulimba mtima kwa Davide, komanso kudalila kwake Yehova. Ndipo n’zocititsa cidwi kuti pamene Davide anapha Goliyati, Yonatani anayamba kukonda kwambili Davide monga mmene anali kudzikondela iye mwini. w21.01 21 ¶6; 22 ¶8-9
Ciŵili, July 26
Mutu wa mkazi ndi mwamuna.—1 Akor. 11:3.
Akhristu onse, ali pansi pa umutu wangwilo wa Yesu Khristu. Komabe, mkazi wacikhristu akaloŵa m’banja, amakhala pansi pa umutu wa mwamuna wopanda ungwilo. Zimenezi zingakhale zovuta. Conco, poganizila za munthu womanga naye banja, mkazi angacite bwino kudzifunsa kuti: ‘N’ciani cionetsa kuti m’baleyu adzakhala mutu wa banja wabwino? Kodi amaika zinthu zauzimu patsogolo mu umoyo wake? Ngati ayi, kodi angadzakhaledi mutu wa banja wabwino tikadzakwatilana?’ Mlongoyo angacitenso bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ine nili na makhalidwe otani amene adzatithandiza m’cikwati? Kodi ndine woleza mtima, komanso woolowa manja? Kodi nili paubale wolimba na Yehova?’ (Mlal. 4:9, 12) Cimwemwe cimene mkazi adzapeza m’banja, cimadalilanso pa zosankha zimene akupanga asanaloŵe m’banja. Alongo oculuka amapeleka citsanzo cabwino kwambili pankhani yogonjela amuna awo. Ndipo timawayamikila ngako! w21.02 8 ¶1-2
Citatu, July 27
Wolokelani ku Makedoniya kuno mudzatithandize.—Mac. 16:9.
M’zaka zaposacedwa, ofalitsa ambili adziikila colinga cophunzila citundu cina kuti awonjezele utumiki wawo kuti akatumikile mu mpingo umene ofalitsa Ufumu ni ocepa kwambili. Akhristu amenewo amadzipeleka mofunitsitsa kuti apititse patsogolo nchito ya Ufumu. Ngakhale kuti mwina zingawatengele zaka kuti adziŵe kukamba bwino citundu catsopano, iwo amathandiza mpingo m’njila zambili. Makhalidwe awo abwino komanso maluso awo zimalimbikitsa mpingo. Timaŵayamikila kwambili abale na alongo odzimana amenewo! Bungwe la akulu siliyenela kulephela kuyeneleza m’bale kukhala mkulu kapena mtumiki wothandiza cabe cifukwa sakwanitsa kukamba bwino citundu ca mpingo wawo. Akulu ayenela kuyang’ana pa ziyenelezo za m’Malemba, osati kudziŵa bwino citundu ca mpingowo.—1 Tim. 3:1-10, 12, 13; Tito 1:5-9. w20.08 30 ¶15-16
Cinayi, July 28
Abale anga, sangalalani pamene mukukumana ndi mayeselo osiyanasiyana.—Yak. 1:2.
Anthu angaganize kuti angakhale acimwemwe kokha ngati ali na thanzi labwino, ndalama zankhani-nkhani, komanso ngati m’banja muli mtendele. Koma cimwemwe cimene Yakobo analemba ni mbali ya cipatso cimene mzimu wa Mulungu umabala, ndipo sicidalila mmene zinthu zilili pa umoyo wa munthu. (Agal. 5:22) Mkhristu amapeza cimwemwe ceni-ceni cifukwa codziŵa kuti akukondweletsa Yehova na kutsatila citsanzo ca Yesu. (Luka 6:22, 23; Akol. 1:10, 11) Monga lawi loyaka mkati mwa nyale ya galasi, Mkhristu amakhalabe wacimwemwe mu mtima. Cimwemweco sicikutha ngati Mkhristuyo wadwala kapena ngati ali na ndalama zocepa. Cimakhalapobe ngakhale pamene akunyozedwa kapena kutsutsidwa na a m’banja lake kapena anthu ena. Cimwemwe cathu cimalimbilako pamene anthu otsutsa akufuna kutilanda cimwemweco. Mayeso amene timakumana nawo cifukwa ca cikhulupililo cathu amatsimikizila kuti ndifedi ophunzila oona a Khristu. (Mat. 10:22; 24:9; Yoh. 15:20) N’cifukwa cake Yakobo analemba mawu apa lemba la tsiku la lelo w21.02 28 ¶6
Cisanu, July 29
Mawu abwino ndi amene [amasangalatsa mtima].—Miy. 12:25.
Mukapeza mavesi a m’Baibo oonetsa kuti timapeza mphamvu mwa kukhala osatekeseka na kudalila Yehova, yesani kuloweza pamtima mavesiwo. Kuti muloŵeze mavesiwo, zingakhale zothandiza kuwaŵelenga motulutsa mawu kapena kuwalemba pena pake na kumawaŵelenga kaŵili-kaŵili. Yoswa analamulidwa kuŵelenga buku la Cilamulo nthawi zonse na kusinkha-sinkhapo kuti acite zinthu mwanzelu. Zimene anali kuŵelenga m’cilamuloco, zinali kudzam’thandizanso kugonjetsa mantha amene akanakhala nawo potsogolela anthu a Mulungu. (Yos. 1:8, 9) Mavesi ambili opezeka m’Mawu a Mulungu angakupatseni mtendele wamaganizo pa zocitika zimene zingakupangitseni kukhala na nkhawa kapena kucita mantha. (Sal. 27:1-3; Miy. 3:25, 26) Ku misonkhano yathu, timapindula na malangizo opelekedwa kupitila m’nkhani zimene zimakambidwa, ndemanga za abale na alongo, komanso mayanjano athu olimbikitsa. (Aheb. 10:24, 25) Tingalimbikitsidwenso kwambili mwa kuuzako mabwenzi athu odalilika a mu mpingo za nkhawa zathu. w21.01 6 ¶15-16
Ciŵelu, July 30
Ukhale citsanzo kwa okhulupilika.—1 Tim. 4:12.
Khalanibe odzicepetsa ndipo pitilizani kudalila Yehova. Pamene munali kubatizika, munaonetsa kuti muli na cikhulupililo cacikulu mwa Yehova ndipo mumam’dalila. Ndipo Yehova mokondwela anakupatsani mwayi wokhala m’banja lake. Koma cofunika kwambili tsopano ni kupitilizabe kudalila Yehova. Kudalila Yehova kungakhale kosavuta popanga zosankha zikulu-zikulu mu umoyo. Koma bwanji pa zosankha zina? M’pofunika kwambili kuti muzidalila Yehova popanga zosankha kuphatikizapo zija zokhudzana na zosangalatsa, nchito yakuthupi, komanso zolinga zimene mudzadziikila mu umoyo. Musadalile nzelu zanu. M’malomwake, fufuzani mfundo za m’Baibo zimene zingakuthandizeni popanga zosankha, ndipo citani zinthu mogwilizana na mfundo zimene mwapeza. (Miy. 3:5, 6) Mukacita zimenezi, mudzakondweletsa Yehova, ndipo abale na alongo mumpingo adzayamba kukulemekezani. N’zoona kuti monga tonsefe, ndinu opanda ungwilo ndipo nthawi zina mungalakwitse zinthu. Komabe, izi siziyenela kukulepheletsani kucita zonse zimene mungathe potumikila Yehova. w21.03 6 ¶14-15
Sondo, July 31
Ndinapulumutsidwa m’kamwa mwa mkango.—2 Tim. 4:17.
Kodi a m’banja lanu amakutsutsani? Kapena mumakhala m’dziko limene nchito ya anthu a Yehova ni yoletsedwa kwambili, kapena m’dziko limene mulibe ufulu wokwanila wa kulambila? Ngati n’telo, mungalimbikitsidwe mwa kuŵelenga 2 Timoteyo 1:12-16 na 4:6-11, 17-22. Mtumwi Paulo analemba mavesi amenewa ali mu ndende. Musanaŵelenge mavesiwo, muuzeni Yehova za vuto lanu na mmene mukumvelela cifukwa ca vutolo. Mufotokozeleni mosapita m’mbali. Ndiyeno pemphani Yehova kuti akuthandizeni kuzindikila mfundo za m’nkhani yokhudza mayeso amene Paulo anakumana nawo, zimene zingakuthandizeni kudziŵa zoyenela kucita pa ciyeso cimene mukukumana naco. Yehova anali atacenjezelatu Paulo kuti anali kufunika kupilila mazunzo cifukwa cokhala Mkhristu. (Mac. 21:11-13) Kodi Yehova anam’thandiza bwanji Paulo? Iye anayankha mapemphelo a Paulo, ndipo m’kupita kwa nthawi anam’patsa mphamvu. Mulungu anam’tsimikizila Paulo kuti adzalandila ndithu mphoto imene anaigwilila nchito molimbika. Iye anaseŵenzetsanso anzake a Paulo okhulupilika kum’patsa thandizo lofunikila. w21.03 17-18 ¶14-15, 19