LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • es22 masa. 77-87
  • August

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • August
  • Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2022
  • Tumitu
  • Mande, August 1
  • Ciŵili, August 2
  • Citatu, August 3
  • Cinayi, August 4
  • Cisanu, August 5
  • Ciŵelu, August 6
  • Sondo, August 7
  • Mande, August 8
  • Ciŵili, August 9
  • Citatu, August 10
  • Cinayi, August 11
  • Cisanu, August 12
  • Ciŵelu, August 13
  • Sondo, August 14
  • Mande, August 15
  • Ciŵili, August 16
  • Citatu, August 17
  • Cinayi, August 18
  • Cisanu, August 19
  • Ciŵelu, August 20
  • Sondo, August 21
  • Mande, August 22
  • Ciŵili, August 23
  • Citatu, August 24
  • Cinayi, August 25
  • Cisanu, August 26
  • Ciŵelu, August 27
  • Sondo, August 28
  • Mande, August 29
  • Ciŵili, August 30
  • Citatu, August 31
Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2022
es22 masa. 77-87

August

Mande, August 1

Simungathe kucita kalikonse popanda ine. —Yoh. 15:5.

Anthu okhawo amene ali pa ubwenzi wolimba na Yesu ndiwo adzapindula na nsembe yake ya dipo. Yesu anakamba kuti adzapeleka “moyo wake cifukwa ca mabwenzi ake.” (Yoh. 15:13) Atumiki a Yehova okhulupilika amene anakhalako Yesu asanabwele padziko lapansi, adzafunika kuphunzila za iye kuti ayambe kum’konda. Amuna na akazi amenewo adzaukitsidwa. Koma nawonso adzafunika kupanga ubwenzi na Yesu kuti akakhale na moyo wosatha. (Yoh. 17:3; Mac. 24:15; Aheb. 11:8-12, 24-26, 31) Timakondwela kuseŵenzela pamodzi na Yesu pa nchito yophunzitsa na kulalikila uthenga wabwino wa Ufumu. Pamene Yesu anali pa dziko lapansi, anali kugwila nchito yophunzitsa. Kungocokela pamene anabwelela kumwamba, iye monga mutu wa mpingo akupitiliza kutsogolela pa nchito yolalikila na kuphunzitsa. Yesu amaona na kuyamikila zonse zimene mumacita pothandiza anthu ambili mmene mungathele, kuti amudziŵe iye komanso kuti adziŵe Atate wake. Ndipo tingakwanitse kugwila nchitoyi kokha mothandizidwa na Yehova komanso Yesu.—Yoh. 15:4. w20.04 22 ¶7-8

Ciŵili, August 2

Mafumu aŵili amenewa . . . azidzalankhula bodza patebulo limodzi.—Dan. 11:27.

Maina akuti “mfumu ya kumpoto” komanso “mfumu ya kum’mwela,” kale anali kugwilitsidwa nchito pokamba za maulamulilo amphamvu andale amene anali kumpoto na kum’mwela kwa dziko la Isiraeli. (Dan. 10:14) Kuyambila kale mpaka kudzafika pa Pentekosite wa mu 33 C.E., Aisiraeli akuthupi ndiwo anali anthu a Mulungu. Koma kungocokela nthawiyo, Yehova anapeleka umboni woonekelatu wakuti anali kuona kuti ophunzila a Yesu okhulupilika ndiwo anthu ake. Conco, mbali yaikulu ya ulosi wa pa Danieli caputa 11, imakamba za otsatila a Khristu osati za Aisiraeli akuthupi. (Mac. 2:1-4; Aroma 9:6-8; Agal. 6:15, 16) M’kupita kwa nthawi, maulamulilo kapena kuti maboma oimila mfumu ya kumpoto na mfumu ya kum’mwela akhala akusintha-sintha. Ngakhale n’telo, pali mbali zina zimene sizinasinthe. Coyamba, zocita za mafumu amenewa zinakhudza kwambili anthu Mulungu. Caciŵili, zimene mafumuwa anacitila anthu a Mulungu zinaonetsa kuti anali kuzonda Mulungu woona, Yehova. Cacitatu, mafumu aŵiliwa anali kulimbilana ulamulilo. w20.05 3 ¶3-4

Citatu, August 3

Ndidzakhala amene ndidzafune kukhala.—Eks. 3:14.

Yehova amapangitsa zinthu kucitika mwa kukhala ciliconse cimene afuna, kuti akwanilitse colinga cake. Yehova angacititsenso atumiki ake opanda ungwilo kukhala ciliconse cimene iye afuna kuti am’tumikile na kukwanilitsa colinga cake. (Yes. 64:8) Mwa njila zimenezi, Yehova amapangitsa cifunilo cake kucitika. Ndipo palibe cimene cingamulepheletse kukwanilitsa zolinga zake. (Yes. 46:10, 11) Tingacite ciani kuti tizimulemekeza kwambili Atate wathu wakumwamba? Tingatelo mwa kusinkha-sinkha pa zimene iye wacita komanso zimene watithandiza kucita. Mwacitsanzo, tikamasinkha-sinkha pa zinthu zodabwitsa za m’cilengedwe, timacita cidwi kwambili poona zimene Yehova wacita. (Sal. 8:3, 4) Ndipo ngati tiganizila pa zimene Yehova watithandiza kucita pokwanilitsa cifunilo cake, timayamba kumulemekeza kwambili. Ndithudi, dzina la Yehova n’lofunika kulilemekeza kwambili! Dzinali limaphatikizapo zonse zokhudza mmene Atate wathu alili, zonse zimene wacita, komanso zonse zimene adzacita kutsogolo.—Sal. 89:7, 8. w20.06 9-10 ¶6-7

Cinayi, August 4

Mulungu. . . amapatsa anthu onse moyo [ndi] mpweya. —Mac 17:24, 25.

Oxygen ni mpweya umene ife anthu na zinyama timapuma kuti tikhalebe na moyo. Akatswili ena amakamba kuti pa caka, anthu na nyama amapuma mpweya wabwino wa oxygen wambili-mbili. Ngakhale n’telo, mpweya wabwino umenewu sukutha. Kuwonjezela apo, anthu na nyama amatulutsa mpweya “woipa” wochedwa carbon dioxide. Komabe, mpweya umenewu sufika poculuka kwambili mu mlengalenga. N’cifukwa ciani zili conco? Cifukwa Yehova analenga zomela zosiyana-siyana, zazikulu na zazing’ono, zimene zimatenga na kugwilitsila nchito mpweya wa carbon dioxide na kutulutsa mpweya wa oxygen. Kuzungulila kumeneku kwa mpweya kumathandiza kuti tizikhala na mpweya wa oxygen umene timapuma. Izi zionetsa kuti mfundo ya mu lemba yalelo. N’ciani cingatithandize kukhala oyamikila kwambili kaamba ka dziko lapansi, malo athu okhala opangidwa modabwitsa, na zonse zili mmenemo? (Sal. 115:16) Cimodzi cimene cingatithandize ni kusinkha-sinkha pa zimene Yehova analenga. Kucita izi kudzatisonkhezela kuti tiziyamikila Yehova tsiku lililonse cifukwa ca zinthu zabwino zimene amatipatsa. Tingaonetsenso kuti timayamikila mphatso ya dziko lapansi mwa kuyesetsa kusamalila bwino malo amene timakhala. w20.05 22 ¶5, 7

Cisanu, August 5

Ndidzayeletsa dzina langa lalikulu limene linali kudetsedwa pakati pa mitundu ina ya anthu. —Ezek. 36:23.

Pofuna kuthetsa nkhaniyi, Yehova anacita zinthu mwanzelu, moleza mtima, komanso mwacilungamo. Iye wacitanso zinthu zambili zoonetsa kuti ni wamphamvuzonse. Koposa zonse, cikondi cake cimaonekela m’zocita zake zonse. (1 Yoh. 4:8) Ndipo Yehova akupitilizabe kuyeletsa dzina lake. Satana akupitilizabe kudetsa dzina la Mulungu masiku ano. Iye amapangitsa anthu kukayikila zakuti Mulungu ni wamphamvu, wacilungamo, wanzelu, komanso wacikondi. Mwacitsanzo, amacititsa anthu kukayikila zakuti Yehova ni Mlengi. Ndipo anthu amene amakhulupilila kuti Mulungu aliko, Satana amawapangitsa kuona kuti Mulunguyo ni woumitsa zinthu komanso wopanda cilungamo. Amawapangitsanso kuona kuti mfundo zake n’zovuta kuzitsatila. Kuposa pamenepa, Satana amaphunzitsa anthu kuti Yehova ni Mulungu wopanda cifundo komanso wankhanza, amene amashoka anthu ku moto wa helo. Anthu akakhulupilila mabodza amenewa, cimakhala cosavuta kwa iwo kukana ulamulilo wa Yehova. Ndipo na imwe Satana adzayesetsa kukupatutsani kuti muleke kumvela Yehova. Kodi mudzalola kuti akugonjetseni? w20.06 5 ¶13-15

Ciŵelu, August 6

Sipadzakhala Mgiriki kapena Myuda, kudulidwa kapena kusadulidwa, mlendo, Msukuti, kapolo, kapena mfulu, koma Khristu ndiye zinthu zonse ndipo ali mwa onse.—Akol. 3:11.

Monga taonela, m’mipingo yambili muli abale na alongo amene akuyesetsa kuphunzila citundu catsopano pa zifukwa zosiyana-siyana. N’zoona kuti zingakhale zovuta kwa iwo kuti alankhule bwino-bwino. Koma ngati sitiyang’ana kwambili pa kalankhulidwe kawo, tidzaona cikondi cawo pa Yehova na mtima wawo wofunitsitsa kum’tumikila. Ndiyeno poona makhalidwe awo abwino amenewo, tidzawakonda na kuwalemekeza kwambili abale na alongo athu amenewo. Sitidzakamba kuti, “Ndilibe nanu nchito,” cabe cifukwa sakamba bwino-bwino citundu cathu. (1 Akor. 12:21) Yehova anatipatsa mwayi waukulu kwambili potiitana mu mpingo wake. Kaya ndife amuna, akazi, mbeta, okwatila, okwatiwa, acicepele, okalamba, kaya timadziŵa kukamba bwino citundu cina kapena ayi, tonsefe ndife ofunika kwambili kwa Yehova, komanso kwa wina na mnzake. (Aroma 12:4, 5; Akol. 3:10) Tiyeni tizifuna-funa mipata yoyamikila malo athu na malo a anthu ena mu mpingo wa Yehova. w20.08 31 ¶20-22

Sondo, August 7

Anthu ena anakhala kumbali yake ndipo anakhala otsatila a Yesu.—Mac. 17:34.

Mtumwi Paulo sanaleke kulalikila anthu a ku Atene olo kuti ambili mu mzindawo anali kupembedza mafano, kucita zaciwelewele, na kukhulupilila nzelu za anthu. Komanso iye sanaleke kuwalalikila ngakhale kuti anali kumunyoza. Paja nayenso Paulo asanakhale Mkhristu anali “wonyoza Mulungu, wozunza anthu ake ndiponso wacipongwe.” (1 Tim. 1:13) Yesu anaona kuti Paulo angasinthe n’kukhala wophunzila wake. Mofananamo, Paulo nayenso anali kukhulupilila kuti anthu a ku Atene angasinthe n’kukhala ophunzila a Yesu. Ndipo izi n’zimenedi ena mwa iwo anacita. (Mac. 9:13-15) M’nthawi ya atumwi, anthu a mitundu yosiyana-siyana anasintha n’kukhala ophunzila a Yesu. Mwacitsanzo, pamene Paulo analembela kalata Akhristu a mu mzinda wa Korinto ku Girisi, anakamba kuti ena mumpingowo asanakhale Akhristu, anali zigaŵenga ndiponso anali na makhalidwe otayilila. Kenako anati: “Ena mwa inu munali otelo. Koma mwasambitsidwa kukhala oyela.” (1 Akor. 6:9-11) Mukanakhala imwe, kodi sembe muona kuti anthuwo angasinthe n’kukhala ophunzila a Yesu? w20.04 12 ¶15-16

Mande, August 8

Basi ndatopa nazo! . . . cotsani moyo wanga.—1 Maf. 19:4.

Akulu sayenela kuthamangila kuimba mlandu Mkhristu amene wayamba kukamba na kucita zinthu zoonetsa kuti akukayikila zoti kutumikila Yehova kuli na phindu. M’malomwake, afunika kuyesetsa kumvetsetsa cifukwa cake iye amakamba na kucita zinthu mwa njila imeneyo. Akatelo, m’pamene angakwanitse kuseŵenzetsa bwino Malemba pom’limbikitsa. Mneneli Eliya anathaŵa Mfumukazi Yezebeli. (1 Maf. 19:1-3) Iye anayamba kuona ngati kuti nchito yake ya uneneli inalibe phindu cakuti analaka-laka kuti afe cabe. (1 Maf. 19:10) Yehova sanamuimbe mlandu Eliya, koma anamutsimikizila kuti sanali yekha, komanso anamuuza kuti ayenela kudalila mphamvu za Mulungu. Anamuuzanso kuti panali nchito yaikulu imene iye anafunika kucita. Yehova anamvetsela mokoma mtima pamene Eliya anali kufotokoza nkhawa zake, ndipo anamupatsa nchito zina zakuti acite. (1 Maf. 19:11-16, 18) Kodi tiphunzilapo ciani pamenepa? Tonsefe, maka-maka akulu, tiyenela kucita zinthu mokoma mtima na nkhosa za Yehova. Ngati wina mumpingo akukamba kuti ni wokhumudwa kapena akuona kuti Yehova sangamukhululukile, akulu ayenela kumumvetsela pamene akufotokoza nkhawa zake mocokela pansi pamtima. Ndiyeno, ayenela kutsimikizila munthuyo, amene ali ngati nkhosa yotaika, kuti Yehova amam’konda. w20.06 22 ¶13-14

Ciŵili, August 9

Bwenzi lenileni limakukonda nthawi zonse.—Miy. 17:17.

Yehova amafuna kuti tizisangalala poceza na a m’banja lathu komanso mabwenzi athu. (Sal. 133:1) Yesu anali na mabwenzi abwino. (Yoh. 15:15) Baibo imafotokoza mapindu amene timapeza tikakhala na mabwenzi abwino. (Miy. 18:24) Imatiuzanso kuti si bwino kudzipatula. (Miy. 18:1) Anthu ambili amaona kuti kuceza pa intaneti kumawathandiza kukhala na mabwenzi ambili, ndiponso kumawathandiza kuti asamakhale osungulumwa. Komabe, tiyenela kukhala osamala tikamaseŵenzetsa malo ocezela pa intaneti. Ocita kafuku-fuku anapeza kuti anthu amene amataila nthawi yaitali kuona zimene anzawo aika pa malo ocezela pa intaneti, pamapeto pake akhoza kumakhala osungulumwa komanso ovutika maganizo. Cifukwa ciani? Cifukwa cimodzi cingakhale cakuti zithunzi zimene anthu amaika pa intaneti, nthawi zambili zimakhala zija zoonetsa zocitika zapadela mu umoyo wawo, wa mabwenzi awo, komanso zoonetsa malo ocititsa cidwi amene iwo anapitako. Munthu amene amaona zithunzi zimenezo, angayambe kudziona kuti ni wotsalila komanso kuti umoyo wake ni wosasangalatsa. w20.07 5-6 ¶12-13

Citatu, August 10

Atumwi ndi akulu anasonkhana pamodzi kuti akambilane nkhani imeneyi.—Mac 15:6.

Nsanja ya Mlonda ya cizungu ya October 1, 1988, inati: “Akulu azikumbukila kuti Khristu mwa mzimu woyela, angapangitse mkulu aliyense pa bungwe la akulu kutulutsa mfundo ya m’Baibo imene ingathandize pa nkhani imene akukambilana, kapena popanga cigamulo cofunika. (Mac. 15:7-15) Pa bungwe la akulu, palibe mkulu aliyense amene mzimu woyela umagwila nchito kwambili pa iye kuposa anzake.” Mkulu amene amalemekeza akulu anzake amapewa kukhala woyamba nthawi zonse kulankhulapo pa miting’i ya akulu. Amapewanso kulankhulapo kwambili kuposa ena, ndipo saona kuti malingalilo ake nthawi zonse ndiwo oyenela. M’malomwake, amafotokoza malingalilo ake modzicepetsa. Amamvetselanso mwachelu ena akamapelekapo ndemanga zawo. Ndipo cofunika kwambili, iye amakhala wokonzeka kukambilana mfundo za m’Malemba, komanso kutsatila zitsogozo za “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu.” (Mat. 24:45-47) Ngati akulu akambilana mwacikondi komanso mwaulemu, mzimu woyela wa Mulungu udzakhala pakati pawo, ndipo udzaŵathandiza kupanga zosankha zoyenela.—Yak. 3:17, 18. w20.08 27 ¶5-6

Cinayi, August 11

Pitilizani kugonjetsa coipa mwa kucita cabwino.—Aroma 12:21.

Adani a mtumwi Paulo anali amphamvu kwambili kuposa iye. Kaŵili-kaŵili iwo anali kusonkhezela anthu kuti amumenye na kumuponya m’ndende. Paulo anali kucitilidwa zinthu zoipa ndi anthu amene anafunika kukhala mabwenzi ake. Ena mumpingo anali kumutsutsa. (2 Akor. 12:11; Afil. 3:18) Paulo anagonjetsa onse amene anali kumutsutsa. Motani? Anapitiliza kulalikila ngakhale kuti anthu anali kumutsutsa. Anakhalabe wokhulupilika kwa abale na alongo ake ngakhale pamene anacita zinthu zomukhumudwitsa. Koposa zonse, anakhalabe wokhulupilika kwa Mulungu mu umoyo wake wonse. (2 Tim. 4:8) Paulo anakwanitsa kupilila mavuto onsewa osati mwa mphamvu zake ayi, koma cifukwa codalila Yehova. Kodi mumanyozedwa kapena kuzunzidwa? Colinga cathu ni kugonjetsa coipa mwa kuthandiza anthu kuphunzila za Yehova na Mawu ake. Timathandiza anthu kuphunzila za Yehova mwa kuseŵenzetsa Baibo poyankha mafunso awo, kucita zinthu mwaulemu komanso mokoma mtima ndi anthu amene amaticitila zoipa, ndiponso mwa kucitila onse zabwino, ngakhale adani athu.—Mat. 5:44; 1 Pet. 3:15-17. w20.07 17-18 ¶14-15

Cisanu, August 12

Kudzicepetsa kwanu n’kumene kumandikweza.—2 Sam. 22:36.

Kodi n’koyenela kukamba kuti Yehova ni wodzicepetsa? Inde n’koyenela. Panthawi ina Davide anaivomeleza mfundo ili pamwambapa. (Sal. 18:35) N’kutheka kuti Davide panthawiyi anali kuganizila za tsiku limene mneneli Samueli anabwela ku kunyumba kwawo kukadzoza mfumu ya Isiraeli ya m’tsogolo. Davide anali wamng’ono kwambili pa anyamata 8 a Jese, koma ndiye anasankhidwa na Yehova kuti aloŵe m’malo Mfumu Sauli. (1 Sam. 16:1, 10-13) N’zodziŵikilatu kuti Davide anali kuona Yehova monga mmene wamasalimo wina anali kumuonela. Ponena za Yehova, wamasalimoyo anati: “Iye amatsika m’munsi kuti aone kumwamba ndi dziko lapansi. Amadzutsa munthu wonyozeka kumucotsa m’fumbi. Amakweza munthu wosauka . . . kuti amukhazike pamodzi ndi anthu olemekezeka.” (Sal. 113:6-8) Njila imodzi imene Yehova amaonetsela kudzicepetsa ni mmene amacitila zinthu ndi anthu omwe ni opanda ungwilo. Iye watipatsa mwayi wom’lambila, ndipo kuposa pamenepo watipatsanso mwayi wokhala mabwenzi ake. (Sal. 25:14) Kuti zitheke kukhala naye paubwenzi, Yehova anapeleka mwana wake monga nsembe yotiwombola ku macimo athu. Ndithudi, Mulungu watisonyeza cifundo cacikulu! w20.08 8 ¶1-3

Ciŵelu, August 13

[Yehova] safuna kuti wina aliyense adzawonongedwe, koma amafuna kuti anthu onse alape.—2 Pet. 3:9.

Yehova anaikilatu tsiku na nthawi pamene adzawononga dziko loipali. (Mat. 24:36) Iye ni woleza mtima, ndipo sadzawononga dzikoli nthawiyo ikalibe kukwana. Mulungu amalaka-laka kuukitsa akufa, koma akulezabe mtima. (Yobu 14:14, 15) Iye akuyembekezela nthawi yoyenela yakuti akaukitse akufa. (Yoh. 5:28) Tili na zifukwa zabwino zokhalila oyamikila kaamba ka kuleza mtima kwa Yehova. Tangoganizilani! Cifukwa ca kuleza mtima kwa Yehova, anthu ambili kuphatikizapo ife amene, takhala na mwayi wolapa macimo athu. Yehova amafuna kuti anthu ambili akhale na mwayi wokapeza moyo wosatha. Conco, tiyeni tizionetsa kuti timayamikila kuleza mtima kwake. Kodi tingaonetse bwanji kuyamikila? Mwa kuyesetsa kusakila anthu a ‘maganizo abwino amene angawathandize kukapeza moyo wosatha,’ komanso kuwathandiza kuti ayambe kukonda Yehova na kum’tumikila. (Mac. 13:48) Tikatelo, tidzawathandiza kuti apindule na kuleza mtima kwa Yehova, monga mmene ife tapindulila. w20.08 18 ¶17

Sondo, August 14

Ndidziwitseni njila zanu, inu Yehova. Ndiphunzitseni kuyenda m’njila zanu.—Sal. 25:4.

Mukamaphunzila Baibo na wophunzila wanu, zimene akuphunzila zizim’fika pamtima, osati cabe kum’kopa maganizo. Cifukwa ciani? Mtima wathu, umene uphatikizapo zolakalaka zathu, komanso mmene timvelela, umatilimbikitsa kucitapo kanthu. Yesu anali mphunzitsi waluso amene anali kukopa maganizo a anthu. Koma anthu anali kum’tsatila cifukwa analinso kuwafika pamtima. (Luka 24:15, 27, 32) Wophunzila wanu afunika aziona Yehova kukhala weniweni, amene angapalane naye ubwenzi, ndipo azimuona kukhala Take wake, Mulungu wake, komanso Bwenzi lake. (Sal. 25:5) Pamene mukuphunzila Baibo, gogomezani za makhalidwe abwino a Mulungu wathu. (Eks. 34:5, 6; 1 Pet. 5:6, 7) Pankhani iliyonse imene mukuphunzila, gogomezani za makhalidwe a Yehova. Thandizani wophunzila wanu kuyamikila makhalidwe abwino a Yehova monga cikondi, kukoma mtima, na cifundo. Yesu anakamba kuti “lamulo lalikulu kwambili komanso loyamba,” n’lakuti “uzikonda Yehova Mulungu wako.” (Mat. 22:37, 38) Thandizani wophunzila wanu kukhala na cikondi cozama pa Mulungu. w20.10 10 ¶12

Mande, August 15

Yesu anali kukonda onsewa, Marita ndi m’bale wake, ndiponso Lazaro.—Yoh. 11:5.

Yesu anali kucita zinthu mwaulemu ndi akazi onse. (Yoh. 4:27) Iye anali kulemekeza kwambili akazi amene anali kucita cifunilo ca Atate wake. Anali kuwaona monga alongo ake, ndipo anawachula pamodzi na amuna amene iye anali kuwaona kuti ni banja lake lauzimu. (Mat. 12:50) Yesu anali bwenzi labwino kwa iwo. Ganizilani ubwenzi umene unalipo pakati pa iye na Mariya komanso Marita, alongo amene mwacidziŵikile anali osakwatiwa. (Luka 10:38-42) N’zoonekelatu kuti mwa zokamba na zocita zake, Yesu anapangitsa alongowo kukhala omasuka. Mwacitsanzo, Mariya anamasuka kukhala pansi pafupi na iye monga wophunzila wake. Nayenso Marita ataona kuti Mariya sakumuthandiza nchito, anamasuka kuuza Yesu dandaulo lake. Panthawi ya maceza imeneyo, Yesu anaphunzitsa azimayi aŵiliwa mfundo zofunika zauzimu. Ndipo iye anaonetsa kuti anali kuwakonda azimayiwa pamodzi na mlongo wawo Lazaro, mwa kupita kukawacezela pa nthawi zina. (Yoh. 12:1-3) Conco, n’zosadabwitsa kuti Lazaro atadwala kwambili, Mariya na Marita anamasuka kupempha thandizo kwa Yesu.—Yoh. 11:3. w20.09 20 ¶3; 21 ¶6

Ciŵili, August 16

Anthu anali kuganiza kuti ufumu wa Mulungu uonekela nthawi yomweyo.—Luka 19:11.

Ophunzila a Yesu anali kuyembekezela kuti ufumu wa Mulungu “uonekela nthawi yomweyo” kuti uwapulumutse ku ulamulilo wopondeleza wa Aroma. Na ife timalaka-laka tsiku limene Ufumu wa Mulungu udzacotsapo zoipa zonse na kutiloŵetsa m’dziko latsopano mmene mudzakhala cilungamo. (2 Pet. 3:​13) Koma tifunika kukhala oleza mtima pamene tikuyembekezela nthawi pamene Yehova adzakonza zinthu. Yehova anapatsa Nowa nthawi yokwanila yomanga cingalawa komanso yogwila nchito yolalikila monga “mlaliki wa cilungamo.” (2 Pet. 2:5; 1 Pet. 3:​20) Yehova anamvetsela pamene Abulahamu anamufunsa mafunso mobweleza-bweleza ponena za cosankha cake cakuti adzawononga anthu okhala m’mizinda yoipa ya Sodomu na Gomora. (Gen. 18:20-​33) Kwa zaka zambili, Yehova analeza mtima kwambili na mtundu wosakhulupilika wa Aisiraeli. (Neh. 9:​30, 31) Masiku ano, Yehova waonetsanso kuti ni woleza mtima. Iye wapatsa anthu onse amene afuna kukhala mabwenzi ake nthawi yokwanila yakuti “alape.” (2 Pet. 3:9; Yoh. 6:​44; 1 Tim. 2:​3, 4) Citsanzo ca Yehova cimeneci citiphunzitsa kuti nafenso tifunika kukhala oleza mtima pamene tikupitiliza kugwila nchito yolalikila na kuphunzitsa. w20.09 10 ¶8-9

Citatu, August 17

Kudzakhala kuuka.—Mac. 24:15.

Yehova poukitsa akufa, adzabwezeletsa maganizo awo na umunthu wawo, moti adzakhala mmene analili asanamwalile. Kodi zimenezi zionetsa ciani? Zionetsa kuti Yehova amakukondani kwambili ndipo amadziŵa bwino maganizo anu, zokamba, na zocita zanu. Amadziŵanso bwino mmene mumamvelela. Conco ngati mwamwalila, Yehova pokuukitsani adzakwanitsa kubwezeletsa maganizo anu na umunthu wanu wonse. Mfumu Davide anali kudziŵa kuti Yehova amatidziŵa bwino aliyense payekha. (Sal. 139:1-4) Kodi tiyenela kumvela bwanji poona kuti Yehova amatidziŵa bwino kwambili? Popeza kuti Yehova amatidziŵa bwino, sitiyenela kukhala na nkhawa yakuti iye amangoyang’ana pa zofooka zathu. Cifukwa ciani? Kumbukilani kuti Yehova amatikonda kwambili. Iye amaona aliyense wa ife kukhala wamtengo wapatali. Amadziŵa bwino zonse zimene zimaticitikila pa umoyo komanso mmene zimatikhudzila. Kukamba zoona, zimenezi n’zolimbikitsa kwambili! Conco tisataye mtima poganiza kuti tili tekha. Pa mphindi iliyonse, tsiku lililonse, Yehova amakhala nafe pafupi kuti atithandize.—2 Mbiri 16:9. w20.08 17 ¶13-14

Cinayi, August 18

Ndidzakupatsa nzelu ndi kukulangiza njila yoti uyendemo.—Sal. 32:8.

Yehova amakondwela kwambili kuphunzitsa anthu ake. Amafuna kuti iwo am’dziŵe bwino, azim’konda, komanso kuti akhale kwamuyaya monga ana ake okondeka. Zonsezi sizikanatheka popanda maphunzilo amene iye amapeleka. (Yoh. 17:3) Yehova anaseŵenzetsa mpingo wa Akhristu oyambilila kuphunzitsa anthu ake. (Akol. 1:9, 10) Ndipo mzimu woyela—“mthandizi” amene Yesu analonjeza—unaŵathandiza kwakukulu. (Yoh. 14:16) Unawathandiza ophunzilawo kumvetsetsa Mawu a Mulungu, ndipo unawakumbutsa zambili zimene Yesu anakamba na kucita, zimene pambuyo pake zinalembedwa m’mabuku a Uthenga Wabwino. Cidziŵitso cimeneci, cinalimbitsa cikhulupililo ca Akristu oyambilila, komanso kukulitsa cikondi cawo pa Mulungu, Mwana wake, komanso kwa wina na mnzake. M’nthawi zamakono, Yehova ananenelatu kuti “m’masiku otsiliza,” anthu a mitundu yonse adzakhamukila ku phili lake lophiphilitsila kuti akaphunzitsidwe njila zake. (Yes. 2:2, 3) Ulosiwu ukukwanilitsidwa m’maso mwathu. w20.10 24 ¶14-15

Cisanu, August 19

Munthu wanzelu amamvetsela ndi kuphunzila malangizo owonjezeleka.—Miy. 1:5.

Kodi n’ciani cingapangitse munthu kukana uphungu wabwino wocokela kwa mnzake wacikondi? Kunyada. Anthu onyada amakonda “zowakomela m’khutu.” Iwo ‘amasiya kumvetsela coonadi.’ (2 Tim. 4:3, 4) Pokhala odzitukumula amadziona kuti amadziŵa zonse. Koma mtumwi Paulo analemba kuti: “Ngati wina akudziona kuti ndi wofunika pamene si wotelo, akudzinyenga.” (Agal. 6:3) Mfumu Solomo anafotokoza mfundoyi momveka bwino. Iye analemba kuti: “Mwana wosauka koma wanzelu ali bwino kuposa mfumu yokalamba koma yopusa, imene sionanso kufunika kocenjezedwa.” (Mlal. 4:13) Onani citsanzo ca mtumwi Petulo, pamene anapatsidwa uphungu na mtumwi Paulo pamaso pa anthu. (Agal. 2:11-14) Petulo akanakhumudwa nawo uphungu wa Paulo, akanaika maganizo pa kapelekedwe ka uphunguwo, komanso malo pamene anaupelekela. Koma Petulo anacita mwanzelu. Analandila uphunguwo, ndipo sanasungile Paulo cakukhosi. M’malomwake, patapita nthawi iye anachula Paulo kuti ‘m’bale wokondedwa.’—2 Pet. 3:15. w20.11 21 ¶9, 11-12

Ciŵelu, August 20

[Kupanga] ophunzila. . . , ndi kuwaphunzitsa.—Mat. 28:19, 20.

N’ciani maka-maka cingathandize maphunzilo a Baibo kupita patsogolo mwauzimu? Kupezeka ku misonkhano yathu. Malangizo a m’Malemba amene amapelekedwa ku misonkhano adzawathandiza kuti cidziŵitso cawo cikule, adzalimbitsa cikhulupililo cawo, na kuwathandiza kukulitsa cikondi cawo pa Mulungu. (Mac. 15:30-32) Wofalitsa angauze wophunzila mmene kukulitsa cikondi cake pa Yehova kunam’limbikitsila kumvela malamulo a Mulungu. (2 Akor. 7:1; Afil. 4:13) Wophunzila akadziŵa ofalitsa okhulupilika osiyana-siyana, angaphunzile pa zitsanzo zawo zabwino, ndipo angamvetse tanthauzo la kusunga lamulo la Khristu lokonda Mulungu na mnansi. (Yoh. 13:35; 1 Tim. 4:12) Ofalitsa ena amene ali na mavuto amene iyenso akukumana nawo, amazindikila kuti n’zotheka kupanga masinthidwe ofunikila kuti munthu akhale wophunzila wa Khristu. (Deut. 30:11) Aliyense mu mpingo angathandizile m’njila zambili kuti ophunzila Baibo apite patsogolo.—Mat. 5:16. w20.11 5 ¶10-12

Sondo, August 21

Ndinamenyana ndi zilombo ku Efeso.—1 Akor. 15:32.

Mwina mtumwi Paulo anatanthauza kumenyana na nyama zenizeni m’bwalo la maseŵela ku Efeso. (2 Akor. 1:8; 4:10; 11:23) Kapena mwina anali kutanthauza Ayuda ankhanza na anthu ena amene anali monga “zilombo.” (Mac. 19:26-34; 1 Akor. 16:9) Kaya Paulo anali kutanthauza ciani, iye anakumana na mavuto aakulu. Ngakhale n’telo, anayang’anabe kutsogolo mwacidalilo. (1 Akor. 15:30, 31; 2 Akor. 4:16-18) Tikukhala m’nthawi yovuta kwambili. Ena mwa abale na alongo athu, anacitilidwapo zaupandu. Ena amakhala m’madela mmene mumacitika nkhondo, ndipo miyoyo yawo imakhala pa ciwopsezo. Enanso amatumikila Yehova m’maiko amene nchito yolalikila ni yoletsedwa, kapena alibe ufulu wokwanila wa kulambila. Komabe, iwo amatumikila Yehova na kum’lambila ngakhale kuti amaika miyoyo yawo na ufulu wawo paciwopsezo. Abale na alongo athu onsewa, ni zitsanzo zabwino kwa ife. Iwo sacita mantha cifukwa adziŵa kuti ngakhale ataye miyoyo yawo pali pano, Yehova wawasungila moyo wabwino ngako kutsogolo. w20.12 9 ¶3-4

Mande, August 22

Ndife anchito anzake a Mulungu. Inuyo ndinu munda wa Mulungu umene ukulimidwa, nyumba ya Mulungu.—1 Akor. 3:9.

Kodi nthawi zina mumalefuka cifukwa cakuti ambili m’gawo lanu alibe cidwi, kapena cifukwa cakuti sapezeka pakhomo? Zikakhala conco, n’ciani cingatithandize kukhalabe acimwemwe kapena kuwonjezela cimwemwe cathu? Tifunika kuona utumiki wathu moyenela. Kodi izi zitanthauza ciani? Ikani maganizo anu pa kulengeza dzina la Mulungu na Ufumu wake. Yesu anakamba momveka bwino kuti si ambili amene adzapeza msewu wopita ku moyo. (Mat. 7:13, 14) Tikakhala mu ulaliki, timakhala na mwayi woseŵenza na Yehova, Yesu, komanso angelo. (Mat. 28:19, 20; Chiv. 14:6, 7) Yehova ndiye amakoka anthu kwa iye. (Yoh. 6:44) Conco, ngati munthu sanamvetsele uthenga wathu, mwina adzamvetsela tikadzam’fikila panthawi ina. Mlongo Deborah anati: “Satana amaseŵenzetsa zolefula monga cida camphamvu kuti atifooketse.” Koma Yehova Mulungu ni wamphamvu kuposa cida ciliconse cimene Satana angaseŵenzetse. w20.12 26 ¶18-19; 27 ¶21

Ciŵili, August 23

Tiyeni tipitilize kukondana, cifukwa cikondi cimacokela kwa Mulungu.—1 Yoh. 4:7.

Akhristu ambili okhulupilika amagwila nchito nthawi zonse kuti azidzisamalila na kusamalila mabanja awo. Ngakhale n’telo, ofalitsa okhulupilika amenewa, amacilikiza gulu la Mulungu mulimonse mmene angathele. Mwacitsanzo, ena amagwila nchito yopeleka thandizo pakacitika matsoka. Ena amagwila nchito zomanga za gulu, ndipo aliyense ali na mwayi wocita zopeleka zothandiza panchito yapadziko lonse. Amacita zimenezi cifukwa cokonda Mulungu na anthu anzawo. Wiki iliyonse timaonetsa kuti timakonda abale na alongo athu, mwa kupezeka pamisonkhano ya mpingo na kutengako mbali. Ngakhale kuti ndife olema, timapitabe ku misonkhano imeneyi. Ngakhale kuti mwina tingacite mantha, timapelekapo ndemanga. Ngakhale kuti aliyense wa ife ali na mavuto ake, timalimbikitsa ena misonkhano isanayambe kapena pambuyo pake. (Aheb. 10:24, 25) Timayamikila cotani nanga nchito imene ofalitsa anzathu amenewa amagwila! w21.01 10 ¶11

Citatu, August 24

Tisakhale odzikuza.—Agal. 5:26.

Anthu odzikuza cimawavuta kuyamikila ena, amafuna kuti iwo ndiwo azitamandidwa. Amakonda kudziyelekezela na ena komanso amalimbikitsa mzimu wa mpikisano. M’malo mophunzitsako ena nchito na kuwapatsa udindo, amagwila okha nchitoyo poganiza kuti ena sangaigwile bwino mmene iwo amafunila. Munthu wodzikuza amadziona wapamwamba kuposa ena, ndipo amacitila nsanje anthu amene amacita bwino kuposa iye. Tikazindikila kuti tiliko na vuto la kudzikuza, tiyenela kupemphela kwa Yehova mocokela pansi pa mtima kuti atithandize kusintha maganizo athu, n’colinga cakuti khalidwe limeneli lisazike mizu mumtima mwathu. (Aroma 12:2) Ndife oyamikila ngako kuti Yehova watipatsa citsanzo cabwino pa nkhani ya kudzicepetsa! (Sal. 18:35) Timaona kudzicepetsa kwake tikaganizila mmene amacitila zinthu na atumiki ake, ndipo timafuna kutengela citsanzo cake. Kuwonjezela apo, timafuna kutengela zitsanzo zabwino za anthu odzicepetsa ochulidwa m’Baibo, amene anali na mwayi woyenda na Mulungu. Tiyeni nthawi zonse tizipeleka ulemelelo kwa Yehova cifukwa iye ndiye woyenela kulandila ulemu na ulemelelo.—Chiv. 4:11. w20.08 13 ¶19-20

Cinayi, August 25

Oloŵa m’banjawo adzakhala ndi nsautso m’thupi mwawo. —1 Akor. 7:28.

Cikwati ni mphatso yabwino kwambili yocokela kwa Mulungu, koma anthu ni opanda ungwilo. (1 Yoh. 1:8) N’cifukwa cake Mawu a Mulungu amacenjeza okwatilana kuti adzakumana na mavuto amene amafotokozedwa kuti “nsautso m’thupi mwawo.” Yehova amayembekezela kuti amuna acikhristu azisamalila mabanja awo kuuzimu, kuwaonetsa cikondi, na kuwasamalila kuthupi. (1 Tim. 5:8) Komabe, ngakhale kuti akazi okwatiwa amakhala otangwanika, ayenela kupatula nthawi tsiku lililonse yoŵelenga Mawu a Mulungu na kuwasinkha-sinkha, komanso kufikila Yehova m’pemphelo mocokela pansi pamtima. Kucita izi kungakhale kovuta. Akazi okwatiwa amakhala otangwanika kwambili. Komabe, m’pofunika ndithu kuti azipatulabe nthawi yocita zimenezo. Cifukwa ciani? Cifukwa Yehova amafuna kuti aliyense wa ife akhalebe paubwenzi wolimba na iye. (Mac. 17:27) M’pomveka kuti mkazi angafunike kulimbikila kuti agonjele mwamuna wake wopanda ungwilo. Komabe, zidzakhala zosavuta kukwanilitsa gawo limene Yehova anam’patsa, ngati amvetsa na kuvomeleza zifukwa zake za m’Malemba. w21.02 9 ¶3, 6-7

Cisanu, August 26

Cikhulupililo canu cikayesedwa, cimabala kupilila.—Yak. 1:3.

Mayeso tingawayelekezele na moto umene amaseŵenzetsa posula lupanga. Lupanga akalicotsa pa moto amaliviika m’madzi, ndipo limalimba kwambili. Mofananamo, tikamapilila mayeso cikhulupililo cathu cimalimba. Ndiye cifukwa cake Yakobo analemba kuti: “Mulole kuti kupilila kumalize kugwila nchito yake, kuti mukhale okwanila ndi opanda cilema m’mbali zonse.” (Yak. 1:4) Tikadziŵa kuti mayeso amene timakumana nawo amalimbitsa cikhulupililo cathu, tingawapilile mwacimwemwe. M’kalata yake, Yakobo anakambanso ena mwa mavuto amene angatilande cimwemwe. Vuto limodzi ni kusadziŵa zimene tingacite. Tikakumana na mayeso, tiyenela kuyang’ana kwa Yehova kuti atithandize kupanga zosankha zom’kondweletsa, zopindulitsa abale na alongo athu, komanso zimene zingatithandize kusunga umphumphu wathu. (Yer. 10:23) Timafunikila nzelu kuti tidziŵe zoyenela kucita, komanso zimene tingakambe kwa anthu amene amatitsutsa. Cifukwa ca kusadziŵa zimene tingacite, tingaone kuti tilibe mtengo wogwila pa mavuto athu, ndipo mwamsanga tingataye cimwemwe cathu. w21.02 28 ¶7-9

Ciŵelu, August 27

Kondanani kwambili kucokela mumtima.—1 Pet. 1:22.

Yehova amapeleka citsanzo cabwino kwa ife. Cikondi cake n’cacikulu kwambili, cakuti tikakhalabe okhulupilika kwa iye, adzapitiliza kutikonda mpaka kale-kale. (Aroma 8:38, 39) Liwu la Cigiliki limene linamasulidwa kuti “kwambili” lili na lingalilo la “kunyindilila” kapena kuti “kuyesetsa.” Nthawi zina tingafunike kuyesetsa kapena kuti kulimbikila kuti tionetse cikondi ceni-ceni kwa okhulupilila anzathu. Ena akatikhumudwitsa tiyenela kupitiliza ‘kulolelana m’cikondi na kuyesetsa ndi mtima wonse kusunga umodzi wathu mwa mzimuwo ndi mwamtendele monga comangila cotigwilizanitsa.’ (Aef. 4:1-3) Sitifunika kusumika maganizo pa zifooko za abale athu. Ndipo tidzayesetsa kuona abale athu mmene Yehova amawaonela. (1 Sam. 16:7; Sal. 130:3) Nthawi zina zimakhala zovuta kuonetsa cikondi ceni-ceni kwa abale na alongo athu, maka-maka ngati timadziŵa zifooko zawo. Zioneka kuti Akhristu ena m’nthawi ya atumwi analinso na vuto limeneli. Zioneka kuti ni mmene zinalili kwa Eodiya na Suntuke. Mtumwi Paulo anawalimbikitsa kuti “akhale amaganizo amodzi mwa Ambuye.”—Afil. 4:2, 3. w21.01 22-23 ¶10-11

Sondo, August 28

Ndikulembela inu anyamata cifukwa ndinu olimba ndipo mawu a Mulungu akhaladi mwa inu ndiponso mwagonjetsa woipayo. —1 Yoh. 2:14.

Acikulile amakuyamikilani kwambili imwe acinyamata amene mumatumikila nawo Yehova limodzi “mogwilizana”! (Zef. 3:9) Iwo amakondwela kuona kuti mumagwila mokangalika, molimbika, komanso mwacangu nchito imene mwapatsidwa. Amakukondani kwambili. Imwe abale acinyamata, kumbukilani kuti Yehova amakukondani komanso amakudalilani. Iye anakambilatu kuti m’masiku otsiliza, padzakhala gulu la anyamata amene adzadzipeleka mofunitsitsa. (Sal. 110:1-3) Amadziŵa kuti mumam’konda, ndipo mumafuna kum’tumikila mmene mungathele. Conco, khalani oleza mtima kwa ena, ngakhalenso kwa inu mwini pa zimene mukufuna. Mukalakwitsa zinthu, phunzilamponi kanthu na kulandila cilango cimene mwapatsidwa, ndipo onani cilangoco kuti cacokela kwa Yehova. (Aheb. 12:6) Gwilani mwakhama nchito iliyonse imene mwapatsidwa. Ndipo cofunika kwambili, m’zocita zanu zonse muzikondweletsa Atate wanu wakumwamba.—Miy. 27:11. w21.03 7 ¶17-18

Mande, August 29

Ukafooka pa tsiku la masautso, mphamvu zako zidzakhala zocepa.—Miy. 24:10

Tingalefuke na zinthu zambili. Zina mwa zinthu zimenezi ni zofooka zathu, komanso matenda. Zingaphatikizeponso kusalandila utumiki umene timaulaka-laka m’gulu la Yehova kapena kulalikila m’gawo limene anthu ambili alibe cidwi. N’cosavuta kuyamba kuona zofooka zathu mosayenela. Kukhala na kapenyedwe kameneka, kungatipangitse kuganiza kuti cifukwa ca zolakwa zathu, Yehova sangatilandile m’dziko lake latsopano. Kuganiza mwa njila imeneyi kungativulaze. Baibo imakamba kuti kupatulapo Yesu Khristu, anthu “onse ndi ocimwa.” (Aroma 3:23) Koma Yehova sakhalila kutipeza zifukwa kapena kutiyembekezela kucita zinthu mwangwilo. M’malo mwake, ni Tate wacikondi amene amafuna kutithandiza. Kuwonjezela apo ni woleza mtima. Iye amadziŵa kuti ambili a ife zimativuta kucita zoyenela ndipo izi zimatipangitsa kudziona mosayenela. Koma iye ni wokonzeka kutithandiza.—Aroma 7:18, 19. w20.12 22 ¶1-3

Ciŵili, August 30

Pomalizila abale, ndikuti pitilizani kukondwela, kusintha maganizo anu.—2 Akor 13:11.

Tonsefe tili paulendo. Kumene talinga, kapena kuti colinga cathu, ni kukakhala m’dziko latsopano pansi pa ulamulilo wacikondi wa Yehova. Tsiku lililonse, timayesetsa kuyenda panjila yopita ku moyo. Koma monga mmene Yesu anakambila, njila imeneyo ni yopanikiza ndipo nthawi zina zimativuta kuyendamo. (Mat. 7:13, 14) Ndife opanda ungwilo, ndipo n’capafupi kupatuka panjila imeneyi. (Agal. 6:1) Kuti tipitilize kuyenda panjila yopanikiza imeneyi ya ku moyo, tiyenela kukhalabe okonzeka kusintha kaganizidwe kathu, kaonedwe kathu ka zinthu, na zocita zathu. Mtumwi Paulo anatilimbikitsa kuti tifunika “kusintha maganizo” athu. Si capafupi kudzipenda mofikapo kuti tidziŵe maganizo athu komanso mmene timamvelela. Mtima wathu ni wonyenga, ndipo izi zingapangitse kuti zikhale zovuta kudziŵa kumene ukutitsogolela. (Yer. 17:9) N’cosavuta kudzinyenga tokha na “maganizo onama.” (Yak. 1:22) Conco, tiyenela kuseŵenzetsa Mawu a Mulungu podzifufuza. Mawu a Mulungu amavumbula zamkati mwa mtima wathu, ‘zimene timaganiza komanso zolinga za mtima wathu.’—Aheb. 4:12, 13. w20.11 18 ¶1-3

Citatu, August 31

Posonyezana ulemu, khalani patsogolo.—Aroma 12:10.

Anthu odzicepetsa nthawi zambili amakhala acimwemwe. N’cifukwa ciani zimakhala conco? Cifukwa anthu odzicepetsa amazindikila zimene sangakwanitse kucita, ndipo amayamikila thandizo iliyonse imene ena angaŵapatse. Mwacitsanzo, ganizilani zimene zinacitika pamene Yesu anacilitsa anthu 10 akhate. Pa anthu 10 amenewo, ni mmodzi yekha amene anabwelela kwa Yesu kukamuyamikila cifukwa comucilitsa matenda ake oopsawo. Munthu wodzicepetsa ameneyu anazindikila kuti payekha sakanatha kudzicilitsa. Conco, anayamikila thandizo limene analandila, ndipo anatamanda Mulungu. (Luka 17:11-19) Nthawi zambili anthu odzicepetsa amakhala bwino na ena ndiponso amapanga ubwenzi wolimba na ena. Cifukwa ciani? Cifukwa modzicepetsa amazindikila kuti anthu ena ali na makhalidwe abwino ndipo amayamba kuwadalila. Anthu odzicepetsa amakondwela ngati ena zinthu zikuwayendela bwino mu utumiki wawo ndipo sazengeleza kuwayamikila na kuwalemekeza. w20.08 12 ¶17-18

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani