LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • es22 masa. 88-97
  • September

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • September
  • Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2022
  • Tumitu
  • Cinayi, September 1
  • Cisanu, September 2
  • Ciŵelu, September 3
  • Sondo, September 4
  • Mande, September 5
  • Ciŵili, September 6
  • Citatu, September 7
  • Cinayi, September 8
  • Cisanu, September 9
  • Ciŵelu, September 10
  • Sondo, September 11
  • Mande, September 12
  • Ciŵili, September 13
  • Citatu, September 14
  • Cinayi, September 15
  • Cisanu, September 16
  • Ciŵelu, September 17
  • Sondo, September 18
  • Mande, September 19
  • Ciŵili, September 20
  • Citatu, September 21
  • Cinayi, September 22
  • Cisanu, September 23
  • Ciŵelu, September 24
  • Sondo, September 25
  • Mande, September 26
  • Ciŵili, September 27
  • Citatu, September 28
  • Cinayi, September 29
  • Cisanu, September 30
Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2022
es22 masa. 88-97

September

Cinayi, September 1

Zimenezi zikadzacitika ndidzatsanulila mzimu wanga pa camoyo ciliconse.—Yow. 2:28.

Petulo anasinthako mawu ena pogwila mawu a ulosi wa Yoweli. (Mac. 2:16, 17) M’malo moyamba na mawu akuti “zimenezi zikadzacitika,” Petulo anati: “Ndipo m’masiku otsiliza,” mzimu wa Mulungu udzatsanulidwa “pa anthu osiyanasiyana.” Izi zionetsa kuti panapita nthawi yaitali kuti ulosi umenewu wa Yoweli ukwanilitsidwe. Mulungu atatsanulila mzimu wake pa Akhristu a m’nthawi ya atumwi, nchito yolalikila inapita patsogolo kwambili moti m’kupita kwa nthawi uthenga wabwino unalengezedwa padziko lonse. Panthawi imene mtumwi Paulo anali kulembela kalata Akhristu a ku Kolose ca m’ma 61 C.E., anafotokoza kuti uthenga wabwino unafalikila kwambili cakuti unali utalalikidwa “m’cilengedwe conse ca pansi pa thambo.” (Akol. 1:23) Pamene Paulo anakamba kuti “m’cilengedwe conse,” anatanthauza madela amene iye na Akhristu ena anatha kufikako polalikila. Mothandizidwa na mphamvu ya mzimu woyela wa Yehova, nchito yolalikila yakula kwambili masiku ano—yafika “mpaka kumalekezelo a dziko lapansi”!—Mac. 13:47. w20.04 6-7 ¶15-16

Cisanu, September 2

Inetu ndidzafuna-funa nkhosa zanga ndi kuzisamalila.—Ezek. 34:11.

Yehova amakonda aliyense wa ife, kuphatikizapo nkhosa iliyonse imene yasocela. (Mat. 18:12-14) Kupitila mwa mneneli Ezekieli, Mulungu analonjeza kuti adzafuna-funa nkhosa zake zosocela na kuzithandiza kuti zikhalenso zolimba mwauzimu. Iye anafotokoza mwacindunji zimene adzacita. Zinthu zimenezo, n’zimenenso m’busa waciisiraeli anali kucita ngati nkhosa yasocela. (Ezek. 34:11-16) Coyamba, m’busa anali kufuna-funa nkhosa yosocelayo, ndipo izi zinali kufuna nthawi yoculuka na khama. Ndiyeno akaipeza, anali kuitenga na kukaiika pa gulu la nkhosa zinzake. Cinanso, ngati nkhosayo yavulala kapena ili na njala, m’busayo anali kuisamalila mwacikondi. Anali kumanga mabalawo, kuinyamula, na kuipatsa cakudya. Akulu amene ni abusa a “nkhosa za Mulungu,” afunika kucitanso zimenezi pothandiza aliyense amene analeka kugwilizana na mpingo. (1 Pet. 5:2, 3) Akulu amafuna-funa nkhosa zosocela, kuzithandiza kuti zibwelele ku gulu la nkhosa, komanso kuzionetsa cikondi mwa kupeleka thandizo lauzimu lofunikila. w20.06 20 ¶10

Ciŵelu, September 3

M’mindamo, mwayela kale ndipo m’mofunika kukolola.—Yoh. 4:35.

Kodi Yesu anakamba izi poganiza kuti anthu ambili adzamutsatila? Iyai. Malemba anali atakambilatu kuti ni anthu ocepa cabe amene adzamukhulupilila. (Yoh. 12:37, 38) Komanso, Yesu anali kukwanitsa kudziŵa za mumtima mwa munthu. Conco, anali kudziŵa kuti ambili sadzalabadila uthenga wake. (Mat. 9:4) Ngakhale kuti iye anaika kwambili maganizo ake pa anthu ocepa amene anamukhulupilila, analalikilabe mokangalika kwa anthu onse. Mosiyana na Yesu, ife sitikwanitsa kudziŵa zimene zili m’mitima ya anthu. Cotelo, tiyenela kupewelatu kuweluza anthu a m’gawo lathu kapena munthu aliyense. M’malomwake, tiyenela kuona kuti anthu angasinthe n’kukhala ophunzila a Yesu. Kumbukilani zimene Yesu anauza ophunzila ake. Iye anati m’mindamo mwayela kale, kutanthauza kuti ni mofunika kukolola. Anthu angasinthe n’kukhala ophunzila a Khristu. Yehova amaona anthu amenewa monga “zinthu zamtengo wapatali.” (Hag. 2:7) Ngati na ise timaona anthu mmene Yehova na Yesu amawaonela, tidzayetsetsa kuwadziŵa bwino, komanso kudziŵa zimene amacita nazo cidwi. Sitidzawaona ngati alendo, koma tidzawaona monga abale na alongo athu am’tsogolo. w20.04 13 ¶18-19

Sondo, September 4

Ndakuchani mabwenzi, cifukwa zonse zimene ndamva kwa Atate wanga ndakudziwitsani. —Yoh. 15:15.

Mawu a Mulungu amakamba momveka bwino kuti tifunika kukonda Yesu nthawi zonse kuti tikondweletse Yehova. Cimodzi mwa zimene tingacite kuti tikhale mabwenzi a Yesu ni kum’dziŵa bwino. Kuti tim’dziŵe bwino Yesu, tiyenela kuŵelenga mabuku a m’Baibo a Mateyu, Maliko, Luka, na Yohane. Pamene tisinkha-sinkha nkhani za m’Baibo zokamba za umoyo wa Yesu, timayamba kum’konda na kum’lemekeza cifukwa ca mmene anali kucitila zinthu mokoma mtima ndi anthu. Mwacitsanzo, olo kuti anali Mbuye, ophunzila ake sanali kucita nawo zinthu monga akapolo. M’malomwake, anali kuwafotokozela maganizo ake na mmene anali kumvelela. Iwo akakhala na cisoni, nayenso anali kumvela cisoni, ndiponso anali kulila nawo limodzi. (Yoh. 11:32-36) Ngakhale anthu otsutsa, anavomeleza kuti Yesu anali bwenzi la anthu amene analabadila uthenga wake. (Mat. 11:19) Ngati titengela citsanzo ca Yesu ca mmene anali kucitila zinthu na ophunzila ake, ubwenzi wathu na ena udzalimba. Tidzakhala acimwemwe, ndipo tidzayamba kum’konda kwambili Yesu na kum’lemekeza. w20.04 22 ¶9-10

Mande, September 5

Mfumu ya kum’mwela nayonso idzakonzekela nkhondo mwa kusonkhanitsa gulu lankhondo lalikulu ndi lamphamvu.—Dan. 11:25.

Pofika m’caka ca 1870, dziko la Britain linali kulamulila dela lalikulu kwambili kuposa dziko lina lililonse, ndiponso linali na gulu la asilikali lamphamvu kwambili pa dziko lonse. Mu ulosi wa Danieli, dzikoli likuimilidwa na nyanga yaing’ono imene inagonjetsa nyanga zina zitatu. Nyanga zitatuzo ziimila dziko la France, Spain, na Netherlands. (Dan. 7:7, 8) Dziko la Britain ndilo linali mfumu ya kum’mwela kuyambila mu 1870 mpaka mkati mwa Nkhondo Yoyamba Yapadziko Lonse. Panthawi imodzi-modziyo, dziko la America linakhala lolemela kwambili padziko lonse, ndipo linayamba kupanga mgwilizano wamphamvu na dziko la Britain. Panthawi ya Nkhondo Yoyamba ya Padziko Lonse, Britain na America anamenya nkhondo mogwilizana, cakuti ulamulilo wawo unakhala wamphamvu kwambili. Panthawiyo, maikowa anagwilizana kwambili, ndipo anapanga ulamulilo wamphamvu padziko lonse wa Britain na America. Monga mmene ulosi wa Danieli unakambila, mfumuyi inasonkhanitsa “gulu lankhondo lalikulu ndi lamphamvu.” M’nthawi yonse ya masiku otsiliza, maiko a Britain na America ndiwo akhala akulamulila monga mfumu ya kum’mwela. w20.05 4 ¶7-8

Ciŵili, September 6

Mitsinjeyo imabwelela kumalo kumene inacokela kuti ikayambilenso kuyenda.—Mlal. 1:7.

Padziko lapansi pali madzi cifukwa cakuti dziko lili pa mtunda woyenelela kucokela ku dzuŵa. Dziko likanakhalako pafupi na dzuŵa, sembe madzi onse anauma, ndipo padziko pakanakhala potentha kwambili ndiponso popanda camoyo ciliconse. Komanso, dziko likanakhala kutali pang’ono na dzuŵa, madzi onse akanaundana, ndipo padziko pakanakhala ayisi yekha-yekha na sinoo. Popeza kuti Yehova anaika dziko lapansi pamalo oyenelela, zungulile-zungulile wa madzi padzikoli umathandiza kuti pakhalebe zamoyo. Dzuŵa likawomba pa nyanja ndiponso pa mtunda, madzi amacita nthunzi n’kukwela kumwamba kukapanga mitambo. Pa caka, madzi amene amakwela kumwamba monga nthunzi cifukwa ca dzuŵa, amakhala ambili kuposa a m’nyanja zonse padziko lapansi, kupatulapo cabe a m’nyanja zamcele (maosheni). Madzi akakwela kumwamba monga nthunzi, amakhala kumeneko kwa masiku pafupi-fupi 10, kenako amagwa monga mvula kapena sinoo. Zikatelo, madziwo amabwelelanso ku nyanja na ku mitsinje, ndipo zomwe takamba zija zimayambanso kucitika. Yehova anapanga dongosolo limeneli n’colinga cakuti padziko pazikhala madzi nthawi zonse. Izi zionetsa kuti iye ni wanzelu komanso wamphamvu.—Yobu 36:27, 28. w20.05 22 ¶6.

Citatu, September 7

Mzimu woyela ukadzafika pa inu, mudzalandila mphamvu. —Mac. 1:8.

Yesu anatilangiza kuti tiyenela kupitiliza kupempha mzimu woyela kwa Mulungu. (Luka 11:9, 13) Yehova amaseŵenzetsa mzimu wake potipatsa “mphamvu yoposa yacibadwa.” (2 Akor. 4:7) Cifukwa ca mphamvu ya mzimu wa Mulungu, tingakwanitse kupilila mayeselo alionse amene tingakumane nawo. Mzimu woyela ungatithandizenso kukwanilitsa mautumiki amene tili nawo m’gulu la Mulungu na kukulitsa maluso amene tili nawo. Conco, ngati zinthu zikutiyendela bwino mu utumiki wathu, timadziŵa kuti zimenezo zatheka kokha cifukwa ca thandizo la mzimu wa Mulungu. Timaonetsa kuti timaona mzimu woyela kukhala mphatso yamtengo wapatali, mwa kupempha Yehova kuti atipatse mzimuwo kuti utithandize kudziŵa maganizo kapena zilakolako zoipa zimene zili mu mtima mwathu. (Sal. 139:23, 24) Tikapempha zimenezi, Yehova poseŵenzetsa mzimu wake angatithandize kudziŵa maganizo na zilakolako zoipa zimene tili nazo. Ndipo tiyenela kupempha Yehova kuti atipatse mzimu wake umene ungatithandize kuthetsa maganizo oipa kapena cilakolako coipaco. Tikatelo, tidzaonetsa kuti ndife otsimikiza mtima kupewa ciliconse cimene cingapangitse kuti Yehova aleke kutithandiza na mzimu wake woyela.—Aef. 4:30. w20.05 28-29 ¶10-12

Cinayi, September 8

Ine ndacititsa kuti iwo adziŵe dzina lanu.—Yoh. 17:26.

Ngati tiikila kumbuyo dzina la Yehova, ndiye kuti tikutengela citsanzo ca Yesu Khristu. Yesu anathandiza anthu kudziŵa dzina la Atate wake mwa kulichula, ndiponso mwa kuphunzitsa anthu coonadi ponena za Yehova. Mwacitsanzo, anatsutsa Afarisi amene anali kupangitsa anthu kuona kuti Yehova ni wankhanza, woumitsa zinthu, wosaganizila ena, komanso wopanda cifundo. Yesu anathandiza anthu kudziŵa kuti Atate wake ni wololela, woleza mtima, wokhululuka, komanso wacikondi. Cinanso, Yesu anali kucita zinthu motengela kwambili Atate wake. Mwa njila imeneyi, anathandiza anthu kum’dziŵa bwino Yehova. (Yoh. 14:9) Mofanana na Yesu, nafenso tingauzeko ena zimene timadziŵa ponena za Yehova. Tingawaphunzitse kuti iye ni Mulungu wacikondi komanso wokoma mtima kwambili. Tikatelo, timathandiza anthu kuona kuti zinthu zoipa zimene ena amakamba ponena za Yehova n’zabodza. Komanso ndiye kuti tikuyeletsa dzina la Yehova, cifukwa timathandiza anthu kuliona kuti ni loyela. Mwa zokamba na zocita zathu timathandiza anthu kum’dziŵa bwino Yehova. Kuwonjezela apo, timayeletsa dzina limeneli mwa kuthandiza anthu kudziŵa coonadi ponena za Mulungu. w20.06 6 ¶17-18

Cisanu, September 9

Tisakhale odzikuza, oyambitsa mpikisano pakati pathu, ndi ocitilana kaduka.—Agal. 5:26.

Tingaseŵenzetse malo ocezela pa intaneti pa zifukwa zabwino monga kukambilana na acibululu komanso mabwenzi athu. Koma mwina mwaonapo kuti anthu ena amaika zinthu pa intaneti n’colinga cakuti ena aziwakhumbila. Zimaoneka kuti iwo amangofuna kuti anthu ena azingoganizila za iwowo basi. Ena amafika ngakhale polemba mawu onyoza ndi acipongwe pa mapikica yawo kapena ya ena pa intaneti. Ife Akhristu timalangizidwa kuti tiyenela kukhala odzicepetsa komanso oganizila ena. Conco, timapewa kuseŵenzetsa malo ocezela pa intaneti mwanjila yolakwika imeneyi. (1 Pet. 3:8) Ngati mumaseŵenzetsa malo ocezela pa intaneti, dzifunseni kuti: ‘Kodi mameseji amene nimalemba, komanso mapikica na mavidiyo amene nimaika pa malo ocezela pa intaneti amapangitsa ena kuona kuti ndine wodzitama? Kodi izi zingapangitse ena kukhala na nsanje?’ Akhristu safunika kudziona kuti ni apamwamba kwambili kuposa ena kapena kufuna kudzipezela ulemu. Iwo amatsatila malangizo a m’Baibo a mu lemba la lelo. Tikakhala odzicepetsa, tidzapewa kutengela anthu odzikuza a m’dzikoli amene amafuna kuti ena aziwaona kuti ni apamwamba kwambili.—1 Yoh. 2:16. w20.07 6 ¶14-15

Ciŵelu, September 10

Kale ndinali wonyoza Mulungu, wozunza anthu ake ndiponso wacipongwe. Komabe anandicitila cifundo cifukwa ndinali wosadziŵa.—1 Tim. 1:13.

Mtumwi Paulo asanakhale wophunzila wa Khristu, anali mnyamata wacipongwe wozunza otsatila a Yesu. (Mac. 7:58) Yesu iyemwini analamula Paulo, amene anali kudziŵikanso kuti Saulo, kuti aleke kuzunza mpingo wacikhristu. Yesu anakamba na Paulo kucokela kumwamba, ndipo anamucititsa khungu. Kuti ayambenso kuona, iye anacita kupempha thandizo kwa anthu amene anali kuwazunzawo. Modzicepetsa, Paulo analandila thandizo kucokela kwa wophunzila wina wa Yesu dzina lake Hananiya, moti anayambanso kuona. (Mac. 9:3-9, 17, 18) Pambuyo pake, Paulo anakhala m’bale wodziŵika kwambili mumpingo wacikhristu. Koma sanaiŵale zimene Yesu anamuphunzitsa pa njila yopita ku Damasiko. Paulo anakhalabe wodzicepetsa, ndipo anali kulandila thandizo kwa abale na alongo ake. Iye anakamba kuti Akhristu anzake ‘anamuthandiza ndi kumulimbikitsa.’—Akol. 4:10, 11. w20.07 18-19 ¶16-17

Sondo, September 11

Atate wanu wavomeleza kukupatsani ufumu.—Luka 12:32.

Ngakhale kuti Yehova ni wamphamvuzonse, amagaŵilako ena maudindo. Mwacitsanzo, anasankha Yesu kukhala Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. Ndipo adzapatsa mwayi anthu 144 000 wolamulila pamodzi na Yesu. Yehova anaphunzitsa Yesu kuti ayenelele kukhala Mfumu komanso Mkulu wa Ansembe. (Aheb. 5:8, 9) Amaphunzitsanso Akhristu amene adzalamulila pamodzi na Yesu, ndipo akaŵapatsa nchito sawayang’anila pa ciliconse cimene akucita pa nchitoyo, cifukwa amawadalila kuti adzacita zimene iye afuna. (Chiv. 5:10) Ngati Atate wathu wakumwamba amene safunikila thandizo la wina aliyense amagaŵilako ena zocita, kuli bwanji ife? Mwacitsanzo, kodi ndinu mutu wa banja kapena mkulu mumpingo? Ngati n’conco, tengelani citsanzo ca Yehova mwa kugaŵilako ena zocita na kupewa kuwayang’anila pa ciliconse cimene akucita pa nchitoyo. Mukatengela citsanzo ca Yehova, nchito idzayenda komanso mudzathandiza ena kuphunzila nchitoyo. Kuwonjezela apo, mudzawathandiza kukhala na cidalilo pa nchitoyo.—Yes. 41:10. w20.08 9 ¶5-6

Mande, September 12

Mwana wa munthu anabwela kudzafuna-funa ndi kupulumutsa anthu osocela.—Luka 19:10.

Kodi Yehova amafuna kuti tiziziona bwanji nkhosa zake zosocela? Yesu anatipatsa citsanzo pa nkhani imeneyi. Iye anali kudziŵa kuti nkhosa iliyonse ya Yehova ni yamtengo wapatali pamaso pa Mulungu. Conco, anacita zonse zotheka kuti athandize “nkhosa zotayika za nyumba ya Isiraeli” kubwelela kwa Yehova. (Mat. 15:24) Komanso, Yesu pokhala m’busa wabwino, anayesetsa kuteteza nkhosa za Yehova kuti pasatayike iliyonse. (Yoh. 6:39) Mtumwi Paulo analimbikitsa akulu mumpingo wa ku Efeso kuti azitengela citsanzo ca Yesu. Anati: “Muthandize ofookawo, ndipo muzikumbukila mawu a Ambuye Yesu. Pajatu iye anati, ‘Kupatsa kumabweletsa cimwemwe coculuka kuposa kulandila.’” (Mac. 20:17, 35) N’zoonekelatu kuti akulu masiku ano ali na udindo waukulu wosamalila anthu a Yehova. M’bale Salvador amene ni mkulu mumpingo ku Spain anati: “Nikaganizila cikondi cacikulu cimene Yehova amaonetsa posamalila nkhosa zake zosocela, nimalimbikitsidwa kucita zonse zotheka pothandiza nkhosazo. Nidziŵa kuti Yehova amafuna kuti nizisamalila nkhosa zake.” w20.06 23 ¶15-16

Ciŵili, September 13

Zakalezo zapita.—Chiv. 21:4.

Yehova adzapitiliza kuleza nafe mtima mpaka kumapeto kwa zaka 1,000 pamene tidzakhala angwilo. Iye ni wokonzeka kutikhululukila macimo mpaka nthawiyo pamene tidzakhala angwilo. Conco, tiyenela kutengela citsanzo cake mwa kuona makhalidwe abwino mwa ena na kuwalezela mtima. Mulungu atalenga dziko lapansi, Yesu na angelo anakondwela kwambili. Koma ganizilaninso cimwemwe cimene iwo adzakhala naco akadzaona kuti dziko lapansi ladzala ndi anthu angwilo amene amakonda Yehova na kum’tumikila. Ganizilaninso cimwemwe cimene anthu okalamulila pamodzi na Khristu kumwamba adzakhala naco poona kuti mtundu wa anthu ukupindula na nchito yawo. (Chiv. 4:4, 9-11; 5:9, 10) Zidzakhala zosangalatsa kwambili kukhala m’dziko limene anthu azidzagwetsa misozi ya cisangalalo osati kulila cifukwa ca cisoni. M’dzikolo simudzakhala matenda, zopweteka, cisoni, na imfa. Mavuto onse adzathelatu. Pamene tikuyembekezela nthawiyo, tiyeni titsimikize mtima kutengela citsanzo ca Atate wathu wacikondi, wanzelu, komanso woleza mtima. Tikatelo, tidzakhalabe acimwemwe olo tikumane na mavuto otani. (Yak. 1:2-4) Ndithudi, ndife oyamikila kwambili kaamba ka lonjezo la Yehova lakuti “kudzakhala kuuka”!—Mac. 24:15. w20.08 19 ¶18-19

Citatu, September 14

Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu. —Mat. 24:14.

Baibo ni mphatso yocokela kwa Mulungu yoonetsa kuti iye amatikonda. Atate wathu wakumwamba anauzila amuna ena kuti alembe Baibo cifukwa iye amatikonda kwambili. Kupitila m’Baibo, Yehova amatithandiza kupeza mayankho pa mafunso ofunika kwambili amene timakhala nawo, monga akuti: Kodi tinacokela kuti? Kodi colinga ca moyo n’ciani? Kodi zinthu zidzakhala bwanji kutsogolo? Yehova afuna kuti ana ake onse adziŵe mayankho pa mafunso amenewa. N’cifukwa cake kwa zaka zambili, iye wakhala akusonkhezela anthu kumasulila Baibo m’vitundu vambili. Masiku ano, Baibo yathunthu kapena mbali yake cabe ipezeka m’vitundu voposa 3,000! Baibo ni buku limene lamasulidwa m’vitundu vambili na kufalitsidwa m’madela ambili kuposa buku lina lililonse. Tingaonetse kuti timayamikila mphatso ya Baibo mwa kuiŵelenga tsiku lililonse, kusinkha-sikha pa zimene taŵelengazo, na kuyesetsa kuseŵenzetsa zimene timaphunzila. Kuwonjezela apo, tingaonetse kuti timamuyamikila Mulungu cifukwa ca mphatso imeneyi, mwa kuyesetsa kuuzako anthu ambili coonadi ca m’Baibo mmene tingathele.—Sal. 1:1-3; Mat. 28:19, 20. w20.05 24-25 ¶15-16

Cinayi, September 15

Mawu a Yehova acititsa kuti ndizinyozedwa ndi kutonzedwa tsiku lonse.—Yer. 20:8.

Mneneli Yeremiya anapatsidwa gawo limene linali lovuta kwambili. Panthawi ina, analefuka kwambili cakuti anafuna kuleka kulalikila. Koma sanatelo. Cifukwa ciani? “Mawu a Yehova” anali monga moto mu mtima mwa Yeremiya, ndipo sakanatha kuusunga! (Yer. 20:9) Ni mmenenso zimakhalila kwa ife tikadzadza mtima wathu na maganizo athu na Mawu a Mulungu. Izi zitilimbikitsa kuŵelenga Baibo tsiku lililonse na kusinkha-sinkha mfundo zake. Cotulukapo cake n’cakuti tidzapitilizabe kuwonjezela cimwemwe cathu, ndipo utumiki wathu ungakhale wopindulitsa kwambili. (Yer. 15:16) Conco mukaona kuti mwalefuka, m’condeleleni Yehova kuti akuthandizeni. Iye adzakuthandizani kulimbana na zofooka zanu. Adzakucilikizani pamene mukudwala. Adzakuthandizaninso kukhala na maganizo oyenela pa utumiki umene mungapatsidwe. Cina, adzakuthandizani kuona nchito yolalikila moyenela. Koposa zonse, muzipemphela kwa Atate wanu wakumwamba na kumuuza mmene mumvelela. Na thandizo lake, mungapambane na kugonjetsa zolefula. w20.12 27 ¶20-21

Cisanu, September 16

[Udandaulile]. . . akazi acikulile ngati amayi ako. Akazi acitsikana uwadandaulile ngati alongo ako, ndipo pocita zimenezi usakhale ndi maganizo alionse oipa. —1 Tim. 5:1, 2.

Alongo ambili amaona kuti amakhala na mwayi waukulu woceza na olambila anzawo pa nthawi ya misonkhano. Conco, akabwela kumisonkhano tiyenela kuwalandila na manja aŵili, kukamba nawo, na kuwaonetsa kuti timawakonda na kuwaganizila. Mofanana na Yesu, nafenso tingapatule nthawi yoceza na alongo. (Luka 10:38-42) Mwina tingawaitanileko kunyumba kwathu kuti tidzadye nawo cakudya kapena kucita nawo zosangalatsa zina. Akabwela, tiyenela kuonetsetsa kuti maceza athu ni olimbikitsa. (Aroma 1:11, 12) Akulu ayenela kukhala na maganizo monga amene Yesu anali nawo. Iye anali kudziŵa kuti kukhala pa umbeta kungakhale kovuta kwa Akhristu ena. Koma mosapita m’mbali, Yesu anafotokoza kuti kukwatiwa kapena kukhala ndi ana sindiye kumene kumabweletsa cimwemwe cokhalitsa. (Luka 11:27, 28) M’malomwake, munthu amakhala na cimwemwe cokhalitsa ngati amaika patsogolo utumiki wake kwa Yehova. (Mat. 19:12) Akulu maka-maka ayenela kucita zinthu na akazi acikhristu monga alongo awo komanso amayi awo auzimu. Akulu angacite bwino kumapatulako nthawi yokamba na alongo misonkhano isanayambe ndiponso ikatha. w20.09 21-22 ¶7-9

Ciŵelu, September 17

[Mlimi] amayembekezelabe zipatso zofunika kwambili zotuluka m’nthaka . . . Nanunso khalani oleza mtima.—Yak. 5:7, 8.

Ku Isiraeli, mlimi anali kubyala mbewu zake mvula yoyamba ikagwa, capakati pa mwezi wa October, ndipo anali kukolola mbewuzo pambuyo pa mvula yothela, capakati pa mwezi wa April. (Maliko 4:28) Ndithudi, ni cinthu canzelu kutengela citsanzo ca mlimi ca kuleza mtima. Komabe, kucita zimenezi nthawi zina kungakhale kovuta. Nthawi zambili, ife anthu opanda ungwilo timafuna kuonelatu nthawi yomweyo phindu la nchito imene tagwila. Koma tifunika kukumbukila citsanzo ca mlimi. Ngati mlimi afuna kuti mbewu zake zikule bwino na kubala zipatso, amafunika kukhala woleza mtima. Amafunika kugaula, kubyala, na kulimilila. Nafenso timafunika kukhala oleza mtima pogwila nchito yolalikila. Mwacitsanzo, tikakhala oleza mtima sitidzalefuka ngati anthu samvetsela uthenga wathu. M’malomwake, tidzapitiliza kusakila anthu omvetsela uthengawo. Ndiponso, timafunika kukhalabe oleza mtima olo kwa anthu omvetsela uthenga wathu. Sitingakakamize wophunzila Baibo kuti akule m’cikhulupililo. Nthawi zina, ngakhale ophunzila a Yesu anali kucedwa kugwila tanthauzo la zimene iye anali kuwaphunzitsa. (Yoh. 14:9) Timafunika kucita khama kuti tithandize ophunzila Baibo athu kuthetsa tsankho m’mitima yawo na kukhala acikondi. Conco, tiyeni tizikumbukila kuti kwathu ni kubyala na kuthilila, koma wokulitsa ni Mulungu.—1 Akor. 3:6. w20.09 11 ¶10-11

Sondo, September 18

Ndidzatamanda Yehova ndi mtima wanga wonse, Pakati pa gulu la owongoka mtima ndi pamsonkhano wawo.—Sal. 111:1.

Tonsefe timafuna kuti ophunzila athu apite patsogolo kuti akabatizike. Njila imodzi imene tingawathandizile, ni mwa kuwalimbikitsa kumapezeka pa misonkhano yampingo. Aphunzitsi aluso amakamba kuti ophunzila amene amafulumila kuyamba kusonkhana, ndiwo amapita patsogolo mwamsanga. Aphunzitsi ena amauza ophunzila awo kuti zimene akuphunzila ni hafu cabe ya maphunzilo a Baibo, hafu ina angailandile ku misonkhano ya mpingo. Ŵelengani Aheberi 10:24, 25 na wophunzila wanu, na kum’fotokozela mapindu amene angapeze akamapezeka pa misonkhano. Mwacimwemwe, muuzenkoni zimene munaphunzila pa misonkhano yaposacedwa. Izi zingakhale zolimbikitsa kuposa kungom’pempha kuti akapezeke ku misonkhano. Zimene wophuzila wanu adzaona pa msonkhano wake woyamba, zidzaposa msonkhano uliwonse wa cipembedzo umene anapezekapo. (1 Akor. 14:24, 25) Iye adzapeza abale na alongo amene ni zitsanzo zabwino kwa iye, ndipo angam’thandizenso kupita patsogolo kuti akabatizike. w20.10 10-11 ¶14-15

Mande, September 19

Kodi mphunzitsi winanso ndani wofanana [na Mulungu]? —Yobu 36:22.

Mzimu wa Mulungu udzakuthandizani kuseŵenzetsa zimene mumaŵelenga na kuphunzila m’Mawu ake. Pemphelani mmene wamasalimo anacitila kuti: “Inu Yehova, ndilangizeni za njila yanu. Ndidzayenda m’coonadi canu. Ndipatseni mtima wosagawanika kuti ndiope dzina lanu.” (Sal. 86:11) Conco, pitilizani kudya cakudya cauzimu cimene Yehova amapeleka kupitilila m’Mawu ake na gulu lake. Koma colinga canu sikungopeza cidziŵitso cabe ayi. Muyenela kukhomeleza coonadi pamtima panu na kuseŵenzetsa mfundo zake mu umoyo wanu. Mzimu wa Yehova ungakuthandizeni kucita zimenezi. Muyenelanso kulimbikitsa abale na alongo anu. (Aheb. 10:24, 25) Cifukwa ciani? Cifukwa ni banja lanu lauzimu. Pemphani mzimu wa Mulungu kuti uzikuthandizani kupeleka ndemanga zogwila mtima pa misonkhano, komanso kuti muzisamalila bwino mbali zanu papulogilamu. Mukatelo, mudzaonetsa Yehova na mwana wake kuti mumakonda “nkhosa” zawo za mtengo wapatali. (Yoh. 21:15-17) Conco, mvetselani kwa Mlangizi wanu Wamkulu mwa kupindula mokwanila na cakudya cauzimu coculuka cimene iye amapeleka. w20.10 24-25 ¶15-17

Ciŵili, September 20

Ophunzila ake onse anathawa ndi kumusiya yekha.—Maliko 14:50.

Kodi Yesu anacita zinthu motani na atumwi ake amene anafooka panthawi ina? Ataukitsidwa, iye anauza ena mwa otsatila ake kuti: “Musaope! Pitani, kauzeni abale anga [kuti n’naukitsidwa].” (Mat. 28:10a) Yesu sanawakane atumwi ake. Ngakhale kuti iwo anamusiya panthawi ina, anawachabe “abale anga.” Mofanana na Yehova, Yesu anali wacifundo komanso wokhululuka. (2 Maf. 13:23) Mofananamo, timawadela nkhawa kwambili amene analeka kulalikila. Iwo ni abale na alongo athu, ndipo timawakonda! Timakumbukilabe nchito zoonetsa cikondi zimene abale athu amenewa anacita kumbuyoko—ena kwa zaka zambili. (Aheb. 6:10) Timawayewa kwambili! (Luka 15:4-7) Tizilimbikitsa ozilala kuyambanso kupezeka ku misonkhano ya mpingo. Ngati wozilala akabwela ku Nyumba ya Ufumu tiyenela kukhala patsogolo kum’landila na manja aŵili. w20.11 6 ¶14-17

Citatu, September 21

Musapitilile zinthu zolembedwa.—1 Akor. 4:6.

Yakobo na Yohane, anabwela kwa Yesu pamodzi na amayi ŵawo, na kum’pempha cinacake cimene sunali udindo wake kuwapatsa. Mosazengeleza, Yesu anawayankha kuti Atate wake wakumwamba ndiwo okha ali na mphamvu yosankha amene adzakhala ku dzanja lake la manja na lamanzele mu Ufumu wa Mulungu. (Mat. 20:20-23) Apa Yesu anaonetsa kuti anali kuzindikila zinthu zimene sunali udindo wake kucita. Iye anali wodzicepetsa. Sanayese ngakhale pang’ono kucita zimene Yehova sanamulamule kucita. (Yoh. 12:49) Kodi tingatengele bwanji citsanzo cabwino cimeneci ca Yesu? Timatengela citsanzo ca Yesu ca kudzicepetsa mwa kutsatila malangizo a m’Baibo a mu lemba la lelo. Conco ngati ena atipempha malangizo, tiyenela kupewa kuwakakamiza kutsatila maganizo athu kapena kungowayankha popanda kuganizilapo mosamala pa nkhaniyo. M’malomwake, tiyenela kuwaunikila malangizo a m’Baibo komanso a m’zofalitsa zathu. Tikatelo, tidzaonetsa kuti timazindikila zinthu zimene si udindo wathu kucita. Tidzaonetsanso kuti ndife odzicepetsa, ndipo timazindikila kuti ‘malamulo olungama’ a Mulungu Wamphamvuzonse ndiwo abwino kwambili kuposa maganizo athu.—Chiv. 15:3, 4. w20.08 11-12 ¶14-15

Cinayi, September 22

Usakhale wolungama mopitilila muyezo kapena kudzionetsela kuti ndiwe wanzelu kwambili, kuopela kuti ungadzibweletsele ciwonongeko—Mlal. 7:16.

Ngati muona kuti mufunika kupatsa uphungu mnzanu, muyenela kukumbukila ciani? Musanam’fikile mnzanuyo, dzifunseni kuti, ‘Kodi nakhala “wolungama mopitilila muyezo”?’ Munthu wolungama mopitilila muyezo amaweluza ena pa miyezo yake osati ya Yehova, ndipo nthawi zambili sakhala wacifundo. Ngati pambuyo podziunika, muona kuti mufunika ndithu kukambilana naye mnzanuyo, kam’thandizeni kuliona bwino-bwino vutolo, na kum’funsa mafunso aulemu amene angam’thandize kuzindikila colakwa cake. Onetsetsani kuti zimene mukukamba n’zozikidwa pa Malemba, pokumbukilanso kuti mnzanuyo adzayankha mlandu osati kwa imwe koma kwa Yehova. (Aroma 14:10) Popeleka uphungu kwa wina, dalilani nzelu zopezeka m’Mawu a Mulungu, na kutengela citsanzo ca Yesu pokhala wacifundo. (Miy. 3:5; Mat. 12:20) Cifukwa ciani? Cifukwa Yehova adzacita nafe monga mmene ifenso timacitila na ena.—Yak. 2:13. w20.11 21 ¶13

Cisanu, September 23

Lekani kuweluza poona maonekedwe akunja, koma muziweluza ndi ciweluzo colungama.—Yoh. 7:24.

Kodi mungakondwele ngati anthu amakuweluzani potengela mtundu wa khungu lanu, maonekedwe a nkhope yanu, kapena potengela kuti ndinu woyonda kapena wonenepa? Mwacidziŵikile, simungakondwele. Conco, n’zolimbikitsa kwambili kudziŵa kuti Yehova satiweluza potengela maonekedwe athu! Mwacitsanzo, pamene Samueli anaona ana a Jese, sanakwanitse kuona zimene Yehova anaona. Yehova anali atauza Samueli kuti mmodzi wa ana a Jese adzakhala mfumu ya Isiraeli. Koma kodi ni mwana uti ameneyo? Samueli ataona Eliyabu, mwana woyamba wa Jese, anati: “Mosakayikila wodzozedwa wake waonekela pamaso pa Yehova.” Eliyabu anali wocititsa kaso m’maonekedwe, moti Samueli anaganiza kuti ndiye asankhidwe kukhala mfumu. “Koma Yehova anauza Samueli kuti: ‘Usaone maonekedwe ake ndi kutalika kwa msinkhu wake, pakuti ine ndamukana ameneyu.’” Kodi tiphunzilapo ciani? Malinga n’zimene Yehova anakamba, tiphunzilapo kuti: “Munthu amaona zooneka ndi maso, koma Yehova amaona mmene mtima ulili.” (1 Sam. 16:1, 6, 7) Tifunika kutengela citsanzo ca Yehova pamene ticita zinthu na abale ndi alongo athu. w20.04 14 ¶1; 15 ¶3

Ciŵelu, September 24

Kwezani maso anu muone m’mindamo, mwayela kale ndipo m’mofunika kukolola.—Yoh. 4:35.

Yesu anali kuyenda kudutsa m’minda. Ndipo mwacidziŵikile minda imeneyo inali ya balele womela kumene. (Yoh. 4:3-6) Kunali kutatsala miyezi pafupi-fupi inayi kuti baleleyo ace. Conco, ophunzila ake ayenela kuti anadabwa pamene Yesu anawauza kuti: “Kwezani maso anu muone m’mindamo, mwayela kale ndipo m’mofunika kukolola. (Yoh. 4:35, 36) Kodi iye anatanthauza ciani? N’zoonekelatu kuti apa Yesu anali kukamba za kusonkhanitsa anthu osati mbewu. Ganizilani zimene zinacitika iye asanakambe zimenezi. Yesu anali atangolalikila mayi wacisamariya, olo kuti Ayuda sanali kugwilizana na Asamariya. Mayiyo anamvetsela. Pamene Yesu anali kukamba kuti m’minda “mwayela kale ndipo m’mofunika kukolola,” gulu la Asamariya amene anamva za iye kwa mkazi wacisamariya uja linali m’njila kubwela kwa Yesu kuti lidzaphunzile zambili. (Yoh. 4:9, 39-42) Ponena za cocitika cimeneci, buku lina lofotokoza Baibo linati: “Cifukwa cofunitsitsa kumvetsela uthenga wa Yesu, anthuwo . . . anali monga mbewu zakuca, zofunika kukolola.” w20.04 8 ¶1-2

Sondo, September 25

Tiyeni tiganizilane kuti tilimbikitsane pa cikondi ndi nchito zabwino.—Aheb. 10:24.

Misonkhano yathu imatithandiza kukulitsa maluso athu pa kamenyedwe ka nkhondo, titelo kunena kwake, mwa kutiphunzitsa kagwilidwe ka nchito yolalikila. Mwacitsanzo, timaphunzila mmene tingaseŵenzetsele zida zophunzitsila za mu Thuboksi Yathu. Conco muzikonzekela bwino misonkhano ya mpingo. Misonkhano ili mkati muzimvetsela mwachelu. Pambuyo pa misonkhano, seŵenzetsani zimene mwaphunzila. Mwa kucita zimenezi, mudzakhala “msilikali wabwino wa Khristu Yesu.” (2 Tim. 2:3) Tilinso na thandizo la angelo amphamvu miyanda-miyanda. Ganizilani zimene mngelo mmodzi cabe angacite! (Yes. 37:36) Ndiyeno ganizilani zimene gulu lankhondo lamphamvu la angelo lingakwanitse kucita. Palibe munthu kapena ciŵanda cimene cili na mphamvu kuposa gulu lamphamvu lankhondo la Yehova. Yehova ni wamphamvu zacikwane-kwane. Conco akakhala nafe, nthawi zonse tidzakhala amphamvu kuposa adani athu kaya akhale oculuka motani. (Ower. 6:16) Mawu amenewa ni oona. Muzikumbukila mfundo imeneyi nthawi zonse mukalefulidwa na zokamba kapena zocita za mnzanu wa kunchito, wa kusukulu, kapena wacibale wosakhulupilila. Kumbukilani kuti simuli mwekha pa nkhondoyi. Inu mukutsatila malangizo amene Yehova akupeleka. w21.03 29 ¶13-14

Mande, September 26

Ngati akufa sadzauka, “tiyeni tidye ndi kumwa, pakuti mawa tifa.”—1 Akor. 15:32.

Mtumwi Paulo mwina anagwila mawu Yesaya 22:13, imene ionetsa maganizo amene Aisiraeli anali nawo. M’malo moyandikila kwa Mulungu, iwo anali kufuna kukhala umoyo wodzikondweletsa okha. Maganizo a Aisiraeli amenewo anali akuti, ‘tiyeni tikondwele lelo, pakuti mawa tifa,’ ndipo maganizo amenewa ni ofala ngakhale masiku ano. Timadziŵa kuti Yehova adzaukitsa akufa. Conco tiyenela kukhala osamala na anthu amene timasankha kuti akhale mabwenzi athu. Abale a ku Korinto anafunika kupewa kuceza na anthu amene sanali kukhulupilila kuti akufa adzauka. Pamenepa pali phunzilo kwa ife. Sipangakhale zotulukapo zabwino ngati timaceza na anthu amene zakutsogolo alibe nazo nchito, amene amangokhalila zalelo. Kuceza na anthu otelo kungawononge makhalidwe abwino a Mkhristu woona na kusintha kaonedwe kake ka zinthu. Ndipo anthuwo angam’pangitse kuyamba kucita zinthu zoipa zimene Mulungu sakondwela nazo. N’cifukwa cake mtumwi Paulo anakamba mwamphamvu kuti: “Dzukani ku tulo tanu kuti mukhale olungama ndipo musamacite chimo.”—1 Akor. 15:33, 34. w20.12 9 ¶3, 5-6

Ciŵili, September 27

Mutu wa mwamuna aliyense ndi Khristu. Mutu wa mkazi ndi mwamuna, ndipo mutu wa Khristu ndiye Mulungu.—1 Akor. 11:3.

Vesiyi ifotokoza mmene Yehova analinganizila banja lake kumwamba na padziko lapansi. Umutu umaphatikizapo mbali ziŵili zikulu-zikulu—ulamulilo komanso mouseŵenzetsela. Yehova ni “mutu” kapena kuti ali na ulamulilo wonse, ndipo ana ake onse, angelo komanso anthu adzayankha mlandu pa mmene amaseŵenzetsela ulamulilo umene anapatsidwa. (Aroma 14:10; Aef. 3:14, 15) Yehova anapatsa Yesu ulamulilo wokhala mutu wa mpingo. Koma Yesu adzayankha kwa Yehova pa mmene amacitila nafe zinthu. (1 Akor. 15:27) Yehova anapatsanso mwamuna ulamulilo pa mkazi wake komanso ana ake. Kodi mwamuna angakhale bwanji mutu wa banja wabwino? Coyamba ayenela kudziŵa zimene Yehova amafuna kuti iye azicita. Ayenelanso kudziŵa cifukwa cake Yehova anakhazikitsa dongosolo la umutu na zimene angacite kuti atengele citsanzo ca Yehova na Yesu. N’cifukwa ciani kucita zimenezi nkofunika? Cifukwa Yehova anapatsa mitu ya mabanja ulamulilo, ndipo amayembekezela kuti iwo aziuseŵenzetsa bwino.—Luka 12:48b. w21.02 2 ¶1

Citatu, September 28

Ine Yehova ndine Mulungu wanu, amene ndimakuphunzitsani kuti zinthu zikuyendeleni bwino. —Yes. 48:17.

Tingacitenso bwino kutengela citsanzo ca Yehova mwa kusankha kuiŵala zinthu zina. Yehova angakwanitse kukumbukila zinthu zonse. Koma tikacita chimo n’kulapa, iye amasankha kutikhululukila na kuiŵala zolakwa zimene tinacita. (Sal. 25:7; 130:3, 4) Yehova amafuna kuti nafenso tizikhululukila anthu na kuiŵalako zimene anatilakwila ngati alapa. (Mat. 6:14; Luka 17:3, 4) Tingaonetse kuyamikila mphatso yapadela ya ubongo mwa kuuseŵenzetsa polemekeza Yehova amene anatipatsa mphatsoyi. Anthu ena amaseŵenzetsa ubongo wawo pokwanilitsa zolinga zadyela. Amadziikila miyezo yawo ya cabwino na coipa. Koma popeza kuti Yehova ndiye anatilenga, n’zosacita kufunsa kuti miyezo yake ya cabwino na coipa ndiyo yabwino kwambili kuposa imene tingadziikile tokha. (Aroma 12:1, 2) Tikamatsatila miyezo yake, timakhala na mtendele mu umoyo wathu. (Yes. 48:18) Cinanso, timazindikila colinga cimene Yehova anatilengela, comwe ni kum’lemekeza na kucita zinthu zom’kondweletsa monga Mlengi komanso Tate wathu.—Miy. 27:11. w20.05 23-24 ¶13-14

Cinayi, September 29

Khalani ndi cikondi ceniceni pakati panu.—Aroma 12:10.

Kodi tingaonetse bwanji cikondi cacikulu kwa abale na alongo athu masiku ano? Tikawadziŵa bwino Akhristu anzathu, cimakhala cosavuta kuwamvetsa, na kuwaonetsa cikondi ceni-ceni. Tingakhale nawo paubwenzi mosasamala kanthu za msinkhu kapena cikhalidwe cawo. Kumbukilani kuti Yonatani anali wamkulu na zaka pafupifupi 30 kuposa Davide. Ngakhale n’telo, iye anakhala naye paubwenzi wolimba. Kodi pali wina mu mpingo mwanu amene ni wamkulu kapena wamng’ono pa imwe, amene mungam’pange bwenzi lanu? Mukacita zimenezi, mudzaonetsa kuti ‘mumakonda gulu lonse la abale.’ (1 Pet. 2:17) Kodi kuonetsa cikondi cacikulu kwa okhulupilila anzathu, kutanthauza kuti aliyense mumpingo tidzakhala oyandikana naye mofanana? Ayi, zimenezo n’zosatheka. Sikulakwa kukhala woyandikana kwambili na anthu ena kuposa ena, mwina cifukwa cokonda zinthu zofanana. Yesu anacha atumwi ake onse kuti “mabwenzi,” koma anali kukonda kwambili Yohane. (Yoh. 13:23; 15:15; 20:2) Ngakhale n’telo, Yesu sanali kucita zinthu mokondela Yohane ayi.—Maliko 10:35-40. w21.01 23 ¶12-13

Cisanu, September 30

Pa zinthu zonse mumaopa kwambili milungu kuposa mmene ena amacitila.—Mac. 17:22.

Mtumwi Paulo sanakambe nawo mofanana ndi mmene anakambila kwa Ayuda m’sunagoge. Iye anali kuyang’ana mosamala zinthu za kumeneko, ndiponso kuyesetsa kudziŵa miyambo yawo ya cipembedzo. (Mac. 17:23) Kenako, iye anaganizila mfundo za coonadi ca m’Baibo zimene anthuwo akanatha kuzikhulupilila mosavuta. Motelo, Paulo anasintha ulaliki wake. Anauza anthu a ku Atene kuti uthenga wake ni wocokela kwa “Mulungu Wosadziwika,” amene iwo anali kumulambila. Ngakhale kuti anthu amenewo sanali kudziŵa Malemba, Paulo anali kuwaonabe kuti angasinthe n’kukhala Akhristu. Anali kuwaona monga mbewu zakuca zofunika kukolola, ndipo anasintha kalalikidwe kake ka uthenga wabwino. Mofanana na Paulo, muzikhala chelu. Muziyang’ana na kuganizila mosamala zinthu zimene zingakuthandizeni kudziŵa zomwe anthu a m’gawo lanu amakhulupilila. Kodi mwininyumba anaikongoletsa bwanji nyumba yake? Kodi dzina lake, kavalidwe na kudzikonza kwake, kapena mmene amakambila zionetsa kuti ni wacipembedzo citi? w20.04 9-10 ¶7-8

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani