LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • es22 masa. 98-108
  • October

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • October
  • Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2022
  • Tumitu
  • Ciŵelu, October 1
  • Sondo, October 2
  • Mande, October 3
  • Ciŵili, October 4
  • Citatu, October 5
  • Cinayi, October 6
  • Cisanu, October 7
  • Ciŵelu, October 8
  • Sondo, October 9
  • Mande, October 10
  • Ciŵili, October 11
  • Citatu, October 12
  • Cinayi, October 13
  • Cisanu, October 14
  • Ciŵelu, October 15
  • Sondo, October 16
  • Mande, October 17
  • Ciŵili, October 18
  • Citatu, October 19
  • Cinayi, October 20
  • Cisanu, October 21
  • Ciŵelu, October 22
  • Sondo, October 23
  • Mande, October 24
  • Ciŵili, October 25
  • Citatu, October 26
  • Cinayi, October 27
  • Cisanu, October 28
  • Ciŵelu, October 29
  • Sondo, October 30
  • Mande, October 31
Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2022
es22 masa. 98-108

October

Ciŵelu, October 1

“Ndani akudziŵa maganizo a Yehova kuti amulangize?” Koma ifeyo tili ndi maganizo a Khristu.—1 Akor. 2:16.

Tikam’dziŵa bwino Yesu, tidzatengela kaganizidwe kake komanso kucita zinthu monga iye. Tikadziŵa bwino maganizo a Yesu na kutengela kaganizidwe kake, ubwenzi wathu na iye udzalimba kwambili. Kodi tingatengele bwanji citsanzo ca Yesu? Onani mfundo iyi: Yesu anali kuganizila kwambili za mmene angathandizile ena m’malo modzikondweletsa iye mwini. (Mat. 20:28; Aroma 15:1-3) Cifukwa cokhala na maganizo amenewa, iye anali wodzimana komanso wa mtima wokhululuka. Sanali kukwiya msanga ena akam’nena. (Yoh. 1:46, 47) Ndipo sanali kuona munthu molakwika cifukwa cokumbukila zolakwa zimene anacita m’mbuyomo. (1 Tim. 1:12-14) Yesu anati: “Mwakutelo, onse adzadziwa kuti ndinu ophunzila anga, ngati mukukondana.” (Yoh. 13:35) Conco, dzifunseni kuti, “Kodi nimatengela citsanzo ca Yesu mwa kucita zonse zimene ningathe kuti nikhalebe pa mtendele na abale na alongo anga?” w20.04 24 ¶11

Sondo, October 2

Iwo adzayeletsa dzina langa. —Yes. 29:23.

Olo kuti tikhala m’dziko lodzala ndi anthu amene amanyoza dzina la Yehova na kulidetsa, tili na mwayi woikila kumbuyo dzina lake mwa kuuza anthu kuti iye ni woyela, wolungama, wabwino, komanso wacikondi. Tilinso na mwayi wocilikiza ulamulilo wake. Tingatelo mwa kuthandiza anthu kuona kuti ulamulilo wa Yehova ndiwo wokha wabwino, umene udzapangitsa kuti m’cilengedwe conse mukhale mtendele na cimwemwe. (Sal. 37:9, 37; 146:5, 6, 10) Pamene tiphunzitsa ena coonadi ca m’Baibo, timagogomezela kwambili za ulamulilo wa Mulungu. Timakamba kuti iye ndiye woyenela kulamulila cilengedwe conse, ndipo mfundo imeneyi ni yosatsutsika. Kuphunzitsa anthu malamulo a Mulungu n’kofunika kwambili. Koma colinga cathu cacikulu powaphunzitsa ni kuwathandiza kuti ayambe kukonda Yehova, Atate wathu, ndiponso kuti akhale okhulupilika kwa iye. Cotelo, pamene tikuphunzitsa anthu za Yehova, tifunika kugogomezela pa makhalidwe ake abwino kuti am’dziŵe kuti ni Mulungu wotani kwenikweni. (Yes. 63:7) Tikamaphunzitsa mwa njila imeneyi, timathandiza anthu kuyamba kum’konda Yehova. Zikatelo, amayamba kumumvela cifukwa cofuna kukhala okhulupilika kwa iye. w20.06 6 ¶16; 7 ¶19

Mande, October 3

Anapatsa munthu pakamwa ndani . . . ? Kodi si ine, Yehova?—Eks. 4:11.

Ubongo wa munthu unapangidwa modabwitsa kwambili. Pamene mwana ali m’mimba mwa mayi ake, ubongo wake umapangidwa mwadongosolo kwambili. Ndipo pa mphindi iliyonse, maselo atsopano masauzande ambili a ubongo amapangika. Akatswili amakamba kuti ubongo wa munthu wamkulu umakhala na maselo pafupi-fupi 100 biliyoni. Ndipo umalemela pafupi-fupi kilogilamu imodzi na hafu. Cimodzi mwa zinthu zimene timakwanitsa kucita cifukwa ca ubongo wathu ni kulankhula. Kuti munthu akambe liwu limodzi cabe, ubongo wake umafunika kugwilizanitsa kayendedwe ka minofu pafupi-fupi 100 ya lilime, m’melo, milomo, nsagwada, komanso ya m’cifuwa. Ndipo kuti akwanitse kukamba mawu omveka bwino, minofu imeneyi imafunika kuyenda mwadongosolo. Zotsatila za kafuku-fuku wina zimene zinafalitsidwa mu 2019, zionetsa kuti makanda ongobadwa kumene amakwanitsa kumva mawu na kukhudzika na zimene amvela. Kafuku-fuku ameneyu agwilizana na mfundo imene akatswili ambili amakhulupilila, yakuti anthufe timabadwa na luso lokwanitsa kumva na kuphunzila vitundu. Kukamba zoona, kulankhula ni mphatso yocokela kwa Mulungu. w20.05 22-23 ¶8-9.

Ciŵili, October 4

Anali kuyembekezela mzinda wokhala ndi maziko enieni, mzinda umene Mulungu ndiye anaumanga ndi kuupanga.—Aheb. 11:10.

Abulahamu analolela kusiya umoyo wofewa umene anali nawo mu mzinda wa Uri. Cifukwa ciani? Cifukwa anali kuyembekezela “mzinda wokhala ndi maziko enieni.” (Aheb. 11:8-10, 16) Mzinda umene Abulahamu anali kuyembekezela ni Ufumu wa Mulungu. Amene adzalamulila mu Ufumu umenewo ni Yesu Khristu komanso Akhristu odzozedwa okwana 144,000. Paulo anakamba kuti Ufumu umenewo ni “mzinda wa Mulungu wamoyo, Yerusalemu wakumwamba.” (Aheb. 12:22; Chiv. 5:8-10; 14:1) Yesu anaphunzitsa ophunzila ake kuti azipemphela kuti Ufumu umenewo ubwele, n’colinga cakuti cifunilo ca Mulungu cicitike pano padziko lapansi, monga mmene zilili kumwamba. (Mat. 6:10) Kodi Abulahamu anali kudziŵa mmene Ufumu wa Mulungu udzakhalila? Iyai. Kwa zaka mahandiledi ambili, nkhani imeneyi inali “cinsinsi copatulika.” (Aef. 1:8-10; Akol. 1:26, 27) Koma Abulahamu anali kudziŵa kuti ena mwa mbadwa zake adzakhala mafumu. N’zimene Yehova anamulonjeza.—Gen. 17:1, 2, 6. w20.08 2-3 ¶2-4

Citatu, October 5

Pitilizani kukula pamene mukumuona iye monga maziko anu, ndi kukhazikika m’cikhulupililo. —Akol. 2:6, 7.

Tifunika kupewa ziphunzitso za anthu ampatuko. Kungocokela pamene mpingo wacikhristu unayamba, Mdyelekezi wakhala akuseŵenzetsa aphunzitsi onyenga pocititsa atumiki a Mulungu okhulupilika kuyamba kukayikila zimene amaphunzila. Pa cifukwa cimeneci, tifunika kuphunzila kusiyanitsa pakati pa zoona na mabodza. Adani athu angaseŵenzetse mawebusaiti kapena malo ocezela pa intaneti pofuna kufooketsa cikhulupililo cathu mwa Yehova, kapena pofuna kutipangitsa kuti tisamakondane na Akhristu anzathu. Koma musakhulupilile mabodza awo. Kumbukilani kuti ni ocokela kwa Satana. (1 Yoh. 4:1, 6; Chiv. 12:9) Kuti Satana asatigonjetse, tifunika kukhulupilila kwambili Yesu na udindo umene Mulungu anam’patsa pokwanilitsa colinga cake. Tiyenelanso kukhulupilila cabe kapolo wokhulupilika ndi wanzelu amene Yehova akumugwilitsila nchito potsogolela gulu lake masiku ano. (Mat. 24:45-47) Timalimbitsa cikhulupililo cathu mwa kuŵelenga Mawu a Mulungu nthawi zonse. Tikatelo, cikhulupililo cathu cidzakhala ngati mtengo umene uli na mizu yopita patali. Paulo anakamba mfundo yofanana na imeneyi polembela mawu a mu lemba la lelo. w20.07 23-24 ¶11-12

Cinayi, October 6

Munthu amaona zooneka ndi maso, koma Yehova amaona mmene mtima ulili.—1 Sam. 16:7.

Pokhala anthu opanda ungwilo, tonsefe tili na cizoloŵezi coweluza ena potengela maonekedwe awo. (Yoh. 7:24) Koma vuto n’lakuti sitingadziŵe zambili za munthu poona cabe maonekedwe ake. Mwacitsanzo, ngakhale dokotala wanzelu kwambili komanso wodziŵa bwino nchito yake sangadziŵe zambili poona cabe mmene wodwala akuonekela. Amafunika kumvetsela mwachelu kuti adziŵe matenda amene munthuyo anadwalapo, mmene vuto lake likum’khudzila, kapena mmene akumvelela pa nthawiyo. Dokotalayo angafunenso kuti wodwalayo akamutenge ekiselo (X-ray) kuti adziŵe mmene m’thupi mwake mulili. Popanda kucita izi, angamupatse mankhwala olakwika. Nafenso n’cimodzi-modzi. Sitingawadziŵe bwino abale na alongo athu poona cabe maonekedwe awo. Tifunika kuyesetsa kudziŵa bwino umunthu wawo wamkati. N’zoona kuti sitingadziŵe zamumtima, koma tingacite zonse zotheka potengela citsanzo ca Yehova. Iye amamvetsela olambila ake. Amaganizila mmene zinthu zilili mu umoyo wawo, komanso zimene anakumana nazo m’mbuyomu. Kuwonjezela apo, amawaonetsa cifundo. w20.04 14-15 ¶1-3

Cisanu, October 7

Aliyense aziganiza m’njila yakuti akhale munthu woganiza bwino.—Aroma 12:3.

Tifunika kukulitsa khalidwe la kudzicepetsa cifukwa cakuti anthu odzikuza sakhala ‘oganiza bwino.’ Anthu odzikuza amakonda kukangana na ena, ndiponso amadziona kuti ni apamwamba kwambili kuposa ena. Zimene amaganiza na kucita, nthawi zambili zimabweletsa mavuto kwa iwo komanso kwa anthu ena. Ngati sangasinthe, Satana angapotoze na kucititsa khungu maganizo awo. (2 Akor. 4:4; 11:3) Koma munthu wodzicepetsa amakhala woganiza bwino. Iye amadziona moyenela, ndipo amazindikila kuti ena amamuposa m’njila zambili. (Afil. 2:3) Komanso amadziŵa kuti “Mulungu amatsutsa odzikweza, koma odzicepetsa amawasonyeza kukoma mtima kwake kwakukulu.” (1 Pet. 5:5) Anthu oganiza bwino amapewa kudzikweza cifukwa safuna kuti Yehova aziwatsutsa kapena kuti akhale mdani wawo. Kuti tikhalebe odzicepetsa, tifunika kutsatila malangizo a m’Baibo akuti tivule “umunthu wakale pamodzi ndi nchito zake, ndipo [tivale] umunthu watsopano.” Tifunika kuphunzila za Yesu na kuyesetsa kutengela citsanzo cake mosamala kwambili.—Akol. 3:9, 10; 1 Pet. 2:21. w20.07 7 ¶16-17

Ciŵelu, October 8

Thupi lomwe ndi limodzi koma lili ndi ziwalo zambili. —1 Akor. 12:12.

Ni mwayi waukulu cotani nanga kukhala ciwalo ca mpingo wa Yehova! Tili m’paradaiso wauzimu wa anthu amtendele komanso acimwemwe. Kodi muli na malo otani mu mpingo? Mtumwi Paulo anayelekezela mpingo na thupi la munthu. Anayelekezelanso ofalitsa mu mpingo na ziwalo za thupi. (Aroma 12:4-8; 1 Akor. 12:12-27; Aef. 4:16) Phunzilo loyamba limene tingatengepo pa fanizo la Paulo, n’lakuti aliyense wa ife amacita mbali yofunika m’banja la Yehova. Paulo anayamba fanizo lake pokamba kuti: “Monga tilili ndi ziwalo zambili m’thupi limodzi, koma ziwalozo sizigwila nchito yofanana, momwemonso ifeyo, ngakhale kuti ndife ambili, tili thupi limodzi mwa Khristu, ndipo aliyense payekha ndi ciwalo ca mnzake.” (Aroma 12:4, 5) Kodi mfundo ya Paulo inali iti? Inali yakuti aliyense wa ife ali na mbali yake mu mpingo, ndipo aliyense ni wofunika. w20.08 20 ¶1-2; 21 ¶4

Sondo, October 9

Yehova anamufunsa kuti, “Ukam’pusitsa motani?”—1 Maf. 22:21.

Makolo, kodi mungatengele bwanji citsanzo ca Yehova ca kudzicepetsa? Ngati m’poyenela, mungafunse ana anu kuti mudziŵe maganizo awo ponena za nchito inayake imene mufuna kugwila. Ngati malingalilo awo ali bwino, mungawagwilitsile nchito. Yehova amapelekanso citsanzo cabwino pankhani yokhala woleza mtima ngakhale pamene atumiki ake akayikila zosankha zake. Yehova atatsala pang’ono kuwononga mizinda ya Sodomu na Gomora, Abulahamu anadela nkhawa ndipo Yehova anamvetsela nkhawa zake. (Gen. 18:22-33) Komanso kumbukilani mmene Yehova anacitila zinthu na Sara, mkazi wa Abulahamu. Iye sanakhumudwe kapena kukwiya pamene Sara anaseka atamva lonjezo lake lakuti adzakhala na mwana mu ukalamba wake. (Gen. 18:10-14) Koma anakamba naye mwaulemu. Kodi imwe makolo na akulu mumpingo, mungaphunzilepo ciani pa citsanzo ca Yehova cimeneci? Kodi mumacita bwanji ngati anthu amene mumawayang’anila sanagwilizane na zosankha zanu? Kodi mumathamangila kuwadzudzula kapena mumayesetsa kumvetsetsa maganizo awo? Kukamba zoona, m’mipingo na m’mabanja zinthu zimayenda bwino kwambili komanso mumakhala cimwemwe ngati anthu amene ali na udindo amatengela citsanzo ca Yehova. w20.08 10 ¶7-9

Mande, October 10

Mphamvu yanga imakhala yokwanila iweyo ukakhala wofooka.—2 Akor. 12:9.

Pamene tinayamba kugwilizana ndi anthu a Yehova, mwina tinali ofunitsitsa kulandila thandizo kucokela kwa ena, pozindikila kuti mwauzimu, tinali ngati tuŵana tosadziŵa zambili. (1 Akor. 3:1, 2) Koma bwanji panopa? Ngati takhala tikutumikila Yehova kwa zaka zoculuka ndipo tsopano timadziŵa zambili, mwina cingakhale covuta kulandila thandizo kwa Akhristu amene akhala zaka zocepa m’coonadi. Komabe, kumbukilani kuti nthawi zambili, Yehova amaseŵenzetsa abale na alongo potilimbikitsa. (Aroma 1:11, 12) Conco ngati tifuna kuti Yehova atipatse mphamvu, tifunika kukhala okonzeka kulandila thandizo kwa abale na alongo athu. Kukhala wopambana, sikudalila mphamvu, maphunzilo, cuma, kapena kumene amakhala. Cofunika ni kudzicepetsa na kudalila Yehova. Tiyeni tonse tiyesetse mwa (1) kudalila Yehova, (2) kuphunzila pa zitsanzo za atumiki a Mulungu ochulidwa m’Baibo, ndi (3) kuvomela thandizo la Akhristu anzathu. Tikatelo, ndiye kuti olo timadziona ngati ofooka kwambili, Yehova adzatithandiza kukhala amphamvu. w20.07 14 ¶2; 19 ¶18-19

Ciŵili, October 11

Aliyense wa inu apitilize kuonetsa khama limene anali nalo poyamba. . . musakhale aulesi, koma mukhale otsanzila anthu amene, mwa cikhulupililo ndi kuleza mtima, akulandila zinthu zimene Mulungu analonjeza monga colowa cawo.—Aheb. 6:11, 12.

Nthawi zina cingakhale covuta kukhala oleza mtima pamene tikulalikila acibululu amene si Mboni. Koma mfundo ya pa Mlaliki 3:2, 7 ingatithandize. Imati: “Pali . . . nthawi yokhala cete ndi nthawi yolankhula.” Khalidwe lathu labwino lingathandize abululu athu kufuna kumvetsela uthenga wathu. Pa nthawi imodzi-modziyo, timakhala chelu kusakila mipata yowauzako za Yehova. (1 Pet. 3:1, 2) Timafunika kulalikila na kuphunzitsa mwakhama. Koma nthawi zonse timafunika kukhala oleza mtima na munthu aliyense, kuphatikizapo a m’banja lathu. Tingaphunzile kuleza mtima mwa kuona zitsanzo za anthu okhulupilika akale ochulidwa m’Baibo komanso a masiku ano. Mwacitsanzo, Habakuku analakalaka kuti zinthu zoipa zithe. Koma anaonetsa kuti anali woleza mtima pamene anati: “Ine ndidzaimabe pamalo a mlonda.” (Hab. 2:1) Mtumwi Paulo anakamba kuti anali kungofuna ‘kumaliza’ utumiki wake. Komabe, moleza mtima iye anapitiliza “kucitila umboni mokwanila za uthenga wabwino.”—Mac. 20:24. w20.09 11-12 ¶12-14

Citatu, October 12

Kukhala wolingana ndi Mulungu [Yesu] sanakuganizilepo ngati cinthu coti angalande. —Afil. 2:6.

Yesu sadziona kuti ni wapamwamba kwambili olo kuti ni Yehova yekha amene amamuposa mphamvu. Potengela citsanzo ca Yesu, atumiki odzicepetsa a Yehova amathandiza kuti m’gulu la Mulungu mukhale cikondi, cimene ni cizindikilo ca anthu a Mulungu. (Luka 9:48; Yoh. 13:35) Nanga bwanji ngati muona kuti mumpingo muli nkhani inayake imene akulu sakuisamalila bwino? M’malo moyamba kudandaula, mungaonetse kudzicepetsa mwa kucilikiza amene amatsogolela mumpingo. (Aheb. 13:17) Kuti mudziŵe mmene mungacitile zimenezi, dzifunseni kuti: ‘Kodi nkhaniyi ni yaikuludi moti ingafunike cisamalilo? Kodi ino ingakhale nthawi yabwino yofunika kuisamalila? Kodi ni udindo wanga kuisamalila? Kodi colinga canga n’cofunadi kulimbikitsa mgwilizano mumpingo, kapena nifuna cabe kudzichukitsa?’ Kwa Yehova, cofunika kwambili ni kukhala wodzicepetsa kuposa kukhala na maluso. Iye amaonanso kuti kukhala ogwilizana n’kofunika kwambili kuposa cangu pa nchito. Conco, citani zonse zotheka kuti muzitumikila Yehova modzicepetsa. Mukamacita zimenezo, mudzathandiza mpingo kukhala wogwilizana.—Aef. 4:2, 3. w20.07 4-5 ¶9-11

Cinayi, October 13

Yesu anawauza kuti: “Musaope! Pitani, kauzeni abale anga.” —Mat. 28:10.

Yesu anayamikila thandizo la akazi oopa Mulungu amene anali kumutumikila “pogwilitsa nchito cuma cawo.” (Luka 8:1-3) Iye anali kuwauza mfundo zozama za coonadi. Mwacitsanzo, pa nthawi ina anawauza kuti iye adzafa kenako adzaukitsidwa. (Luka 24:5-8) Komanso monga mmene anacitila na atumwi ake, iye anakonzekeletsa akazi amenewo kaamba ka mayeselo amene anali kudzakumana nawo kutsogolo. (Maliko 9:30-32; 10:32-34) N’zocititsa cidwi kuti ngakhale kuti atumwi anamuthaŵa Yesu pa nthawi imene anagwidwa, akazi ena amene anali kumutumikila anali naye pafupi pamene iye anali kufa pa mtengo wozunzikilapo. (Mat. 26:56; Maliko 15:40, 41) Akazi oopa Mulungu ndiwo anali oyamba kudziŵa kuti Yesu waukitsidwa. Ndipo iye anawatuma kuti akauze atumwi kuti iye waukitsidwa kwa akufa. (Mat. 28:5, 9, 10) Komanso, akazi ayenela kuti analipo pa Pentekosite wa mu 33 C.E., pamene ophunzila a Khristu anadzozedwa na mzimu woyela, analandilako mphamvu yozizwitsa yokamba zinenelo zosiyana-siyana, ndipo anali kuuzako ena “zinthu zazikulu za Mulungu.”—Mac. 1:14; 2:2-4, 11. w20.09 23 ¶11-12

Cisanu, October 14

Nthawi zonse uzisamala ndi zimene umacita komanso zimene umaphunzitsa.—1 Tim. 4:16.

Nchito yopanga ophunzila ni yopulumutsa miyoyo. Tidziŵa bwanji? Yesu atapeleka lamulo lopezeka pa Mateyu 28:19, 20 anati: “Pitani mukaphunzitse anthu . . . kuti akhale ophunzila . . . Muziwabatiza.” Kodi ubatizo ni wofunika motani? Ni ciyenelezo kwa onse ofuna cipulumutso. Munthu amene afuna kubatizika, ayenela kukhulupilila kuti cipulumutso n’cotheka kokha cifukwa Yesu anapeleka moyo wake monga nsembe na kuukitsidwa. Ndiye cifukwa cake mtumwi Petulo anauza Akhristu anzake kuti: ‘Ubatizo, ukukupulumutsani mwa kuukitsidwa kwa Yesu Khristu.’ (1 Pet. 3:21) Conco wophunzila watsopano akabatizika, amakhala na ciyembekezo ca moyo wosatha. Kuti tipange ophunzila, tifunika kukulitsa “luso la kuphunzitsa.” (2 Tim. 4:1, 2) Cifukwa ciani? Cifukwa Yesu anatilamula kuti: “Pitani [mukapange] . . . ophunzila. . . , ndi kuwaphunzitsa.” Mtumwi Paulo anati “pitiliza kucita” nchitoyi, “cifukwa ukatelo udzadzipulumutsa wekha komanso anthu okumvela.” w20.10 14 ¶1-2

Ciŵelu, October 15

Kuyambila lelo uzisodza anthu amoyo.—Luka 5:10.

Mtumwi Petulo anaphunzila kukonda nchito yosodza anthu. Ndipo mothandizidwa na Yehova, Petulo anakhala waluso kwambili pa nchitoyo. (Mac. 2:14, 41) Timalalikila cifukwa cakuti timakonda Yehova. Ici ndiye cifukwa cacikulu cimene timagwilila nchitoyi. Kukonda Yehova kumatithandiza kuthetsa mantha alionse amene tingakhale nawo. Yesu ataitana Petulo kuti akhale msodzi wa anthu, anamuuza kuti: “Usacite mantha.” (Luka 5:8-11) Sikuti Petulo anali kuyopa zimene zikanamucitikila ngati wakhala wotsatila wa Khristu. Koma anayopa poona kuculuka kwa nsomba zimene Yesu anawathandiza kugwila mozizwitsa, moti anadziona kuti anali wosayenelela kugwila nchito pamodzi na Yesu. Mofanana na Petulo, na imwe mungakhale na mantha. Mwina mumacita mantha mukaganizila zimene mudzafunika kucita mukadzakhala wophunzila wa Khristu. Ngati n’conco, yesetsani kukulitsa cikondi canu pa Yehova, Yesu, komanso pa anansi anu. Mukatelo, mudzakhala wokonzeka kulabadila ciitano ca Yesu cakuti mukhale msodzi wa anthu.—Mat. 22:37, 39; Yoh. 14:15. w20.09 3 ¶4-5

Sondo, October 16

Pitani mukaphunzitse anthu . . . kuti akhale ophunzila. —Mat. 28:19, 20.

Timakondwela kwambili kuseŵenzetsa nthawi yathu, mphamvu zathu, na cuma cathu kuti tipeze anthu amene ‘ali ndi maganizo abwino amene angawathandize kukapeza moyo wosatha.’ (Mac. 13:48) Pocita zimenezi, timatengela citsanzo ca Yesu. Iye anati: “Cakudya canga ndico kucita cifunilo ca amene anandituma ndi kutsiliza nchito yake.” (Yoh. 4:34; 17:4) Nafenso ndiye cokhumba ca mtima wathu. Timafuna tikatsilize nchito imene tinapatsidwa. (Yoh. 20:21) Timafunanso kuti ena, kuphatikizapo ozilala, agwile nafe nchitoyi mopilila. (Mat. 24:13) Kukamba zoona, nchito imene Yesu anatipatsa si yopepuka. Koma si ili pamapewa pathu tokha. Yesu analonjeza kuti adzakhala nafe. Timagwila nchitoyi ya kupanga ophunzila monga “anchito anzake a Mulungu,” komanso pamodzi na “Khristu.” (1 Akor. 3:9; 2 Akor. 2:17) Conco, tingakwanitse kuitsiliza nchitoyi. Ni mwayi wokondweletsa kugwila nchito imeneyi na kuthandiza ena kucitanso cimodzi-modzi.—Afil. 4:13. w20.11 7 ¶19-20

Mande, October 17

Yesu anali kukulabe m’nzelu ndi mu msinkhu. Ndipo Mulungu ndi anthu anapitiliza kukondwela naye. —Luka 2:52.

Nnthawi zambili, zosankha za makolo zimakhudza ana awo kwa nthawi yaitali. Ngati makolo sapanga zosankha zabwino, angabweletsele ana awo mavuto. Koma ngati amapanga zosankha mwanzelu, amathandiza ana awo kukhala na umoyo wacimwemwe, komanso wokhutilitsa. Koma nawonso ana afunika kupanga zosankha zabwino. Cosankha copambana cimene aliyense angapange, ni kutumikila Atate wathu wacikondi, Yehova. (Sal. 73:28) Mtima wa Yosefe na Mariya unali pa kuthandiza ana awo kutumikila Yehova. Ndipo zosankha zawo monga makolo zinaonetsa kuti ndico cinali colinga cawo cacikulu. (Luka 2:40, 41, 52) Yesu nayenso anapanga zosankha zanzelu zimene zinam’thandiza kucita mbali yake pa colinga ca Yehova. (Mat. 4:1-10) Yesu anakula n’kukhala munthu wokoma mtima, wokhulupilika, komanso wolimba mtima. Inde, anakula monga mwana amene kholo lililonse loopa Mulungu lingam’nyadile na kukondwela naye. w20.10 26 ¶1-2

Ciŵili, October 18

Maso ako aziyang’ana patsogolo.—Miy. 4:25.

Ganizilani zitsanzo izi: Mlongo wokalamba akuganizila za masiku osangalatsa a kale lake. Ngakhale kuti akukumana na mavuto palipano, akucitabe zonse zimene angathe potumikila Yehova. (1 Akor. 15:58) Tsiku lililonse amayelekeza kuti ali m’dziko latsopano, pamodzi na anthu amene amawakonda. Mlongo wina, akukumbukila kuti Mkhristu mnzake anamukhumudwitsa kumbuyoku, koma waganiza zongoiiŵala nkhaniyo. (Akol. 3:13) M’bale wina wakumbukila zolakwa zimene anacitapo kumbuyoku, koma akusumika maganizo ake pa kukhalabe wokhulupilika tsopano. (Sal. 51:10) Kodi Akhristu atatuwa akufanana pa ciani? Onse akukumbukila zimene zinacitika mu umoyo wawo wakumbuyo, koma sakhalila kungoganizila zimenezo. M’malomwake, ‘akuyang’ana kutsogolo.’ N’cifukwa ciani kucita zimenezo n’kofunika? Munthu sangathe kuyenda bwino-bwino mu msewu ngati akungoyang’ana-yang’ana kumbuyo. Mofananamo, sitingapite patsogolo mu utumiki wathu kwa Yehova ngati nthawi zonse timangoganizila zakumbuyo.—Luka 9:62. w20.11 24 ¶1-3

Citatu, October 19

Anayamba kumudelela. —1 Sam. 17:42.

Goliyati, amene anali msilikali wamphamvu, anali kuona kuti Davide ni wofooka. Goliyati anali cimunthu cacikulu, ndipo ananyamula zida zankhondo zoopsa, komanso anali wophunzitsidwa bwino kumenya nkhondo. Koma Davide anadalila mphamvu za Yehova, moti anakwanitsa kugonjetsa mdani wake, Goliyati. (1 Sam. 17:41-45, 50) Davide analimbananso na vuto lina limene likanamupangitsa kudziona ngati wofooka komanso wopanda mphamvu. Iye anali kutumikila mokhulupilika mfumu ya Isiraeli imene Yehova anasankha, dzina lake Sauli. Poyamba, Mfumu Sauli anali kumulemekeza Davide. Koma m’kupita kwa nthawi, kunyada kunapangitsa Sauli kuyamba kucitila nsanje Davide. Iye anayamba kucitila Davide zinthu zoipa, cakuti anafika mpaka pofuna kumupha. (1 Sam. 18:6-9, 29; 19:9-11) Davide anapitiliza kulemekeza Sauli monga mfumu yosankhidwa na Yehova, olo kuti Sauliyo anali kumucitila zinthu zopanda cilungamo. (1 Sam. 24:6) Davide anadalila Yehova kuti amupatse mphamvu zomuthandiza kupilila mavuto amene anali kukumana nawo.—Sal. 18:1, tumawu twa pamwamba. w20.07 17 ¶11-13

Cinayi, October 20

M’nthawi ya mapeto mfumu ya kum’mwela idzayamba kukankhana nayo [mfumu ya kumpoto]. —Dan. 11:40.

Mbali yaikulu ya ulosi wa mfumu ya kumpoto komanso mfumu ya kum’mwela inakwanilitsidwa kale. Conco, sitikayikila kuti mbali yotsala nayonso idzakwanilitsidwa. Kuti timvetsetse ulosi wa pa Danieli caputa 11, tifunika kukumbukila kuti ulosiwu umakamba za olamulila na maboma okhawo amene zocita zawo zinakhudza anthu a Mulungu mwacindunji. Atumiki a Mulungu ni ocepa kwambili poyelekezela ndi anthu onse padzikoli. Nanga n’cifukwa ciani maboma amakonda kuwazunza? Cifukwa colinga cacikulu ca Satana na onse amene ali kumbali yake ni kuwononga anthu amene amatumikila Yehova na Yesu. (Gen. 3:15; Chiv. 11:7; 12:17) Kuti timvetsetse ulosi wa m’buku la Danieli, tifunikanso kuonetsetsa kuti ukugwilizana na maulosi ena a m’Mawu a Mulungu. Ndipo popanda kuyelekezela ulosi wa Danieli na mavesi ena a m’Baibo, sitingathe kuumvetsetsa. w20.05 2 ¶1-2

Cisanu, October 21

Kodi akufa adzaukitsidwa motani? Inde, kodi iwo adzauka ndi thupi lotani?—1 Akor. 15:35.

Anthu ambili masiku ano ali na maganizo osiyana-siyana pankhani ya zimene zimacitika munthu akamwalila. Koma kodi Baibo imaphunzitsa ciani? Munthu akamwalila thupi lake limawola. Koma amene analenga cilengedwe angaukitse munthuyo na kum’patsa thupi loyenelela. (Gen. 1:1; 2:7) Mtumwi Paulo anaseŵenzetsa fanizo loonetsa kuti Mulungu sadzaukitsa munthu na thupi limene anali nalo asanamwalile. Ganizilani za “mbewu.” Mbewu ikabyalidwa m’nthaka, imamela kenako n’kukhala comela catsopano. Comelaco cimakhala cosiyana na kambewu. Paulo anaseŵenzetsa fanizo limeneli poonetsa kuti Mlengi wathu angapeleke ‘thupi monga mwakufuna kwake.’ Paulo anakambanso kuti, “palinso matupi akumwamba, ndi matupi apadziko lapansi.” Motani? Padzikoli pali matupi anyama, koma kumwamba kuli matupi amzimu, monga amene angelo ali nawo.—1 Akor. 15:36-41. w20.12 9-10 ¶7-9

Ciŵelu, October 22

Kodi ndidzalimbana ndi masautso anga kufikila liti?Kodi masiku a moyo wanga adzakhala odzaza ndi cisoni kufikila liti?—Sal. 13:2.

Tonsefe, timafuna kukhala na mtendele wa mumtima. Palibe amene amafuna kukhala na nkhawa. Koma nthawi zina nkhawa zimaticulukila ndipo timakhala na mafunso monga amene Mfumu Davide anafunsa mu lemba la tsiku la lelo Pali zinthu zambili zimene zingatibweletsele nkhawa. Ndipo nthawi zina, palibe zimene tingacite kuti zimenezo zisacitike. Mwacitsanzo, sitingaletse kuti anthu asakweze mitengo ya zakudya, zovala, kapena ya nyumba za lendi. Komanso, sitingapeweletu kuyesedwa na anzathu a kunchito kapena a kusukulu kuti ticite zinthu zosakhulupilika, kapena za ciwelewele. Ndipo palibe zimene tingacite kuti tiletse anthu kucita zaupandu m’dela lathu. Timakumana na mavuto amenewa cifukwa tikukhala m’dziko limene maganizo a anthu ambili si ogwilizana na mfundo za m’Baibo. Satana, mulungu wa dzikoli, adziŵa kuti anthu ena adzalola “nkhawa za moyo wa m’nthawi ino” kuwalepheletsa kutumikila Yehova. (Mat. 13:22; 1 Yoh. 5:19) Ndiye cifukwa cake dzikoli ni lodzala na zinthu zobweletsa nkhawa! w21.01 2 ¶1, 3

Sondo, October 23

Aliyense amene amadana ndi m’bale wake ndi wopha munthu, ndipo mukudziŵa kuti aliyense wopha munthu sadzalandila moyo wosatha.—1 Yoh. 3:15.

Yohane anatilimbikitsanso kupewa kuzonda abale kapena alongo athu. Ngati tilephela kumvela uphungu umenewu, Satana angamatiseŵenzetse. (1 Yoh. 2:11) Izi n’zimene zinacitika cakumapeto kwa nthawi ya Akhristu oyambilila. Satana anali kucita zonse zotheka kulimbikitsa cidani na magaŵano pakati pa anthu a Mulungu. Panthawi imene Yohane analemba makalata ake, anthu amene anali kuonetsa mzimu monga wa Satana anali ataloŵa mu mpingo. Mwacitsanzo, Diotirefe anayambitsa magaŵano aakulu mu mpingo wina. (3 Yoh. 9, 10) Iye sanali kulemekeza akulu oyendela, oimila bungwe lolamulila. Iye anafika ngakhale pocotsa ena mu mpingo amene anali kuceleza anthu amene iye sanali kuwakonda. Ati kudzikuza kwake ati! Ngakhale masiku ano, Satana akali kuyesa-yesabe kugaŵanitsa na kugonjetsa anthu a Mulungu. Conco, tisalole cidani kutigaŵanitsa. w21.01 11 ¶14

Mande, October 24

Zikamaliza kucitila umboni wawo, cilombo . . . cidzacita nazo nkhondo, ndipo cidzazigonjetsa ndi kuzipha.—Chiv. 11:7.

Pankhondo yoyamba ya padziko lonse, maboma a Germany na Britain anazunza atumiki a Mulungu amene anakana kumenya nawo nkhondo. Boma la America linaponya m’ndende abale amene anali kutsogolela pa nchito yolalikila. Cizunzo cimeneci cinakwanilitsa ulosi wa pa Chivumbulutso 11:7-10. M’zaka za m’ma 1930 komanso maka-maka pankhondo yaciŵili ya padziko lonse, mfumu ya kumpoto inazunza anthu a Mulungu mwankhanza kwambili. Hitler na otsatila ake analetsa nchito ya anthu a Mulungu. Anthu otsutsawo anapha atumiki a Yehova pafupi-fupi 1,500, ndipo ena ofika m’masauzande anawatsekela m’ndende zacibalo. Mfumu ya kumpoto inaika ziletso pa atumiki a Mulungu kuti asakhale na ufulu wotamanda dzina la Yehova poyela. Mwa kucita izi, ‘inaipitsa malo opatulika’ ndiponso ‘inacotsa nsembe zoyenela kupelekedwa nthawi zonse.’ (Dan. 11:30b, 31a) Mtsogoleli wa dzikolo, dzina lake Hitler, anacita kulumbila kuti adzafafanizilatu Mboni za Yehova mu Germany. w20.05 6 ¶12-13

Ciŵili, October 25

Pokonda abale, khalani ndi cikondi ceniceni pakati panu. Posonyezana ulemu, khalani patsogolo.—Aroma 12:10.

Tikamaonetsana cikondi ceni-ceni, tidzateteza mpingo ku mzimu wa mpikisano. Kumbukilani kuti Yonatani sanayese kupikisana na Davide. Sanamuone monga wopikisana naye pa mpando wacifumu. (1 Sam. 20:42) Tonsefe tingatengele citsanzo ca Yonatani. Musaone anchito anzanu kukhala opikisana nawo cifukwa ca maluso awo, ‘koma modzicepetsa onani ena kukhala okuposani.’ (Afil. 2:3) Kumbukilani kuti aliyense pali zimene angacite pothandiza mpingo. Tikakhalabe odzicepetsa, tidzaona zabwino mwa abale na alongo athu, na kupindula na citsanzo ca kukhulupilika kwawo. (1 Akor. 12:21-25) Tikamaonetsana cikondi ceni-ceni, timalimbitsa mgwilizano pakati pa anthu a Mulungu. Timaonetsanso kuti ndifedi ophunzila a Yesu, ndipo zimakopa anthu a maganizo abwino kuti ayambe kutumikila Yehova. Koposa zonse, timapeleka ulemelelo kwa “Tate wacifundo cacikulu ndi Mulungu amene amatitonthoza m’njila iliyonse,” Yehova.—2 Akor. 1:3. w21.01 24 ¶14; 25 ¶16

Citatu, October 26

Popeza simuli mbali ya dzikoli . . . dziko likudana nanu.—Yoh. 15:19.

Masiku ano, nthawi zina anthu satilemekeza ife Mboni za Yehova, ndipo amatiseka na kutiona monga anthu osaphunzila komanso ofooka. Cifukwa ciani? Cifukwa khalidwe lathu n’losiyana ndi la anthu a m’dzikoli. Ife timayesetsa kukhala odzicepetsa, ofatsa, komanso omvela. Koma anthu masiku ano amakonda kutamanda anthu onyada, odzikuza, komanso opanduka. Cina, popeza kuti sititengako mbali m’zandale ndipo sitiloŵa usilikali, ndife osiyana ndi anthu a m’dzikoli moti amationa ngati otsika. (Aroma 12:2) Ngakhale kuti anthu m’dzikoli amationa monga ofooka, Yehova akutigwilitsila nchito kucita zinthu zazikulu. Iye akutithandiza kugwila nchito yaikulu yolalikila imene sinacitikepo m’mbili yonse ya anthu. Masiku ano, ife atumiki ake timamasulila na kufalitsa magazini m’vitundu vambili padziko lapansi. Komanso timaseŵenzetsa Baibo pothandiza anthu mamiliyoni ambili kukhala na umoyo wabwino. Pa zonsezi, Yehova ndiye ayenela kutamandidwa. w20.07 15 ¶5-6

Cinayi, October 27

Ndicita monga momwe Atate wandilamulila. —Yoh. 14:31.

Yesu amagonjela kwa Yehova, koma osati cifukwa cakuti alibe nzelu kapena maluso. Palibe munthu aliyense wanzelu amene anaphunzitsa momveka bwino, komanso mosavuta monga Yesu. (Yoh. 7:45, 46) Yehova anadziŵa kuti Yesu ni waluso kwambili cakuti anamulola kuseŵenza naye polenga zinthu m’cilengedwe. (Miy. 8:30; Aheb. 1:2-4) Ndipo kungocokela pamene Yesu anaukitsidwa, Yehova anam’patsa ‘ulamulilo wonse kumwamba ndi padziko lapansi.’ (Mat. 28:18) Ngakhale kuti Yesu ni waluso kwambili, amayang’anabe kwa Yehova kaamba ka citsogozo. Cifukwa ciani? Cifukwa amawakonda Atate wake. Amuna afunika kudziŵa kuti Yehova analinganiza zakuti mkazi azigonjela mwamuna wake osati cifukwa coona kuti akazi ni otsika kwa amuna ayi. Yehova anaonetsa zimenezi mwa kusankha akazi komanso amuna kuti akalamulile pamodzi na Yesu. (Agal. 3:26-29) Yehova anaonetsa kuti amadalila Mwana wake mwa kum’patsa ulamulilo. Mofananamo, mwamuna wanzelu amapatsako mkazi wake ulamulilo pamlingo woyenela. w21.02 11 ¶13-14

Cisanu, October 28

Anthu amene anapilila timawacha odala.—Yak. 5:11.

Mawu a Mulungu ali ngati galasi lodziyang’anapo. Amatithandiza kudziŵa mbali zimene tifunika kuwongolela. (Yak. 1:23-25) Mwacitsanzo, pambuyo poŵelenga Mawu a Mulungu, tingazindikile kuti tiyenela kulamulila mkwiyo wathu. Na thandizo la Yehova, timadziŵa mmene tingacitile zinthu modekha na anthu amene atikhumudwitsa kapena tikakumana na mavuto. Timakhala oganiza bwino ndipo timapanga zosankha zabwino. (Yak. 3:13) Conco, m’pofunika kwambili kuidziŵa bwino Baibo! Nthawi zina timaphunzila zofunika kupewa pambuyo pakuti talakwitsa zinthu. Njila yabwino yopezela nzelu ni kuphunzila pa zimene ena anacita bwino, komanso pa zimene ena analakwitsa. Ndiye cifukwa cake Yakobo akutilimbikitsa kuphunzila ku zitsanzo za anthu ochulidwa m’Baibo monga Abulahamu, Yobu, Rahabi, komanso Eliya. (Yak. 2:21-26; 5:10, 11, 17, 18) Atumiki a Yehova okhulupilika amenewo, anakwanitsa kupilila mayeso amene akanawalanda cimwemwe. Citsanzo cawo ca kupilila cionetsa kuti na thandizo la Yehova nafenso tingakwanitse kupilila. w21.02 29-30 ¶12-13

Ciŵelu, October 29

Zolinga zimakhazikika anthu akakambilana, ndipo uzitsatila malangizo anzelu pomenya nkhondo yako.—Miy. 20:18.

Pa phunzilo la Baibo, mphunzitsi ndiye amakhala na udindo waukulu wothandiza wophunzilayo kumvetsa Mawu a Mulungu. Ngati mphunzitsiyo wakupemphani kuti mupite naye ku phunzilo, muzidziona kuti ndimwe wothandiza wake. Udindo wanu ni kum’cilikiza. (Mlal. 4:9, 10) Kodi mungacite ciani maka-maka kuti mukhale wothandiza wabwino pa phunzilo la Baibo? Konzekelani phunzilo la Baibo. Coyamba, pemphani mphunzitsi kuti akuuzenkoni zina zokhudza wophunzilayo. Mudziŵako zotani zokhudza wophunzilayo? Kodi mudzaphunzila naye mutu ciani? Mudzafuna kugogomeza mfundo yanji pa mutu umenewu? Kodi pali zina zimene niyenela kucita kapena kusacita kapenanso kusakamba pamene tikuphunzila naye? Ningacite ciani kuti nilimbikitse wophunzilayo kupita patsogolo? Mwacionekele, mphunzitsi sangakuuzeni zacinsinsi zokhudza wophunzilayo. Koma zina zimene angakuuzenkoni zingakuthandizeni. Mmishonale wina dzina lake Joy ananena kuti: “Kukambilana zimenezi kumathandiza amene napita naye ku phunzilo kuonetsa cidwi kwa wophunzila na kudziŵa zimene angakambe pa phunzilolo.” w21.03 9 ¶5-6

Sondo, October 30

Ngati dziko likudana nanu, mukudziŵa kuti linadana ndi ine lisanadane ndi inu.—Yoh. 15:18.

Timazondedwa cifukwa cakuti timayendela mfundo zolungama za Mulungu. Miyezo imeneyi ni yosiyana kwambili na dzikoli pa nkhani ya makhalidwe abwino. Mwacitsanzo, anthu ambili amavomeleza poyela kugonana koipitsitsa kofanana na kumene Mulungu anawonongela nako anthu a ku Sodomu na Gomora. (Yuda 7) Cifukwa cakuti timamamatila miyezo ya m’Baibo ponena za makhalidwe otelo, anthu ambili amatinyoza na kutinena kuti ndife okhwimitsa zinthu! (1 Pet. 4:3, 4) N’ciani cingatithandize kupilila anthu akamatizonda na kutinyoza? Tiyenela kukhala na cikhulupililo colimba kuti Yehova adzatithandiza. Mofanana na cishango, cikhulupililo cathu cingathe ‘kuzimitsa mivi yonse yoyaka moto ya woipayo.’ (Aef. 6:16) Koma kuwonjezela pa cikhulupililo, palinso cina. Tifunikanso cikondi. Cifukwa ciani? Cifukwa cikondi “sicikwiya.” Cimakwilila komanso kupilila zonse zokhumudwitsa. (1 Akor. 13:4-7, 13) Cikondi pa Yehova, pa alambili anzathu, komanso ngakhale pa adani athu cimatithandizila kupilila cidani. w21.03 20-21 ¶3-4

Mande, October 31

Usamafulumile kukwiya mumtima mwako, pakuti anthu opusa ndi amene sacedwa kupsa mtima.—Mlal. 7:9.

Nthawi zina, timaonetsa cikondi cathu pa abale na alongo athu mwa zimene timapewa kucita. Mwacitsanzo, timapewa kukwiya msanga na zimene angakambe. Ganizilani zimene zinacitika cakumapeto kwa umoyo wa Yesu padziko lapansi. Yesu anauza ophunzila ake kuti ngati afuna kukapeza moyo, anayenela kudya mnofu wake na kumwa magazi ake. (Yoh. 6:53-57) Zimene iye anakamba zinali zodabwitsa kwambili, cakuti ophunzila ake ambili anamusiya—koma osati mabwenzi ake eni-eni. Iwo anamamatila kwa iye mokhulupilika. Sanamvetse zimene Yesu anakamba, ndipo n’kutheka kuti nawonso anali odabwa. Komabe, mabwenzi okhulupilika a Yesu sanaganize kuti zimene anakamba zinali zolakwika na kukhumudwa nazo. M’malomwake, anamukhulupilila, podziŵa kuti amakamba zoona. (Yoh. 6:60, 66-69) Conco, m’pofunika kwambili kupewa kukhumudwa msanga na zimene anzathu angakambe. Koma timawalola kufotokoza zimene akutanthauza.—Miy. 18:13. w21.01 11 ¶13

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani