LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • es22 masa. 108-118
  • November

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • November
  • Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2022
  • Tumitu
  • Ciŵili, November 1
  • Citatu, November 2
  • Cinayi, November 3
  • Cisanu, November 4
  • Ciŵelu, November 5
  • Sondo, November 6
  • Mande, November 7
  • Ciŵili, November 8
  • Citatu, November 9
  • Cinayi, November 10
  • Cisanu, November 11
  • Ciŵelu, November 12
  • Sondo, November 13
  • Mande, November 14
  • Ciŵili, November 15
  • Citatu, November 16
  • Cinayi, November 17
  • Cisanu, November 18
  • Ciŵelu, November 19
  • Sondo, November 20
  • Mande, November 21
  • Ciŵili, November 22
  • Citatu, November 23
  • Cinayi, November 24
  • Cisanu, November 25
  • Ciŵelu, November 26
  • Sondo, November 27
  • Mande, November 28
  • Ciŵili, November 29
  • Citatu, November 30
Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2022
es22 masa. 108-118

November

Ciŵili, November 1

Munthu aliyense woyankhila nkhani asanaimvetsetse n’ngopusa, ndipo amacita manyazi.—Miy. 18:13.

M’kaonedwe kathu kaumunthu, tingaganize kuti Yona anali munthu wosadalilika, kapenanso wosakhulupilika. Yehova anamupatsa lamulo lacindunji lakuti akalengeze uthenga waciweluzo ku Nineve. M’malo momvela lamulo limenelo, Yona anakwela combo copita ku dziko lina, “kuthawa Yehova.” (Yona 1:1-3) Kodi mukanakhala imwe sembe munam’patsanso mwayi wina womvela lamulo limeneli? Mwina ayi. Koma Yehova anaona kuti Yona anafunika kum’patsanso mwayi wina. (Yona 3:1, 2) Pemphelo limene Yona anapeleka limaonetsa bwino kuti anali munthu wotani. (Yona 2:1, 2, 9) Mosakayikila, Yona anapemphela kambili-mbili kwa Yehova. Koma pemphelo limene anapeleka ali m’mimba mwa cinsomba, limatithandiza kudziŵa kuti m’ceni-ceni iye anali munthu wabwino, olo kuti anathaŵa utumiki wake. Mawu amene anakamba m’pemphelolo aonetsa kuti anali wodzicepetsa, woyamikila, komanso wofunitsitsa kumvela Yehova. Mpake kuti Yehova sanayang’ane kwambili pa zolakwa zake, koma anayankha pemphelo lake na kupitiliza kum’seŵenzetsa monga mneneli. N’kofunika kwambili kuti akulu ‘azimvetsetsa’ mmene zinthu zilili asanapeleke uphungu. w20.04 15-16 ¶6-7

Citatu, November 2

[Paulo] anakambilana nawo mfundo za m’Malemba. Iye anali kufotokoza ndi kusonyeza umboni wolembedwa powatsimikizila. —Mac. 17:2, 3.

Ophunzila a m’nthawi ya Atumwi anakhulupilila ziphunzitso zacikhristu, ndipo anadalila mzimu woyela kuti uwathandize kumvetsetsa Mawu a Mulungu. Anafufuza kuti atsimikizile ngati ziphunzitso zimenezo zinalidi zozikidwa pa Malemba. (Mac. 17:11, 12; Aheb. 5:14) Cikhulupililo cawo sicinali cozikidwa cabe pa mmene anali kuonela Yehova ndi anthu ake. Komanso sanali kutumikila Yehova cabe cifukwa cokonda kuyanjana na Akhristu anzawo. M’malomwake, cikhulupililo cawo cinazikidwa pa “kumudziŵa Mulungu molondola.” (Akol. 1:9, 10) Coonadi ca m’Baibo sicisintha. (Sal. 119:160) Mwacitsanzo, coonadi ca m’Baibo sicisintha ngati wokhulupilila mnzathu watikhumudwitsa kapena ngati wacita chimo lalikulu. Komanso sicisintha ngakhale pamene takumana na mavuto. Motelo, tiyenela kuzidziŵa bwino ziphunzitso za m’Baibo ndiponso kukhutila kuti ziphunzitso zimenezo n’zoona. Monga mmene nangula amatetezela boti ku cimphepo camkuntho, cikhulupililo cathu colimba cozikidwa pa coonadi ca m’Baibo cidzatithandiza kuti tisafooke pamene takumana na mayeselo. w20.07 9 ¶6-7

Cinayi, November 3

Anatilamula kuti tilalikile kwa anthu ndi kupeleka umboni wokwanila.—Mac. 10:42.

Yesu amaona kuti tikamacitila zabwino abale ake odzozedwa, ndiye kuti tikucitila iyeyo. (Mat. 25:34-40) Njila imodzi yaikulu imene timathandizila odzozedwa ni mwa kutengako mbali mokwanila pa nchito yopanga ophunzila, imene Yesu analamula otsatila ake kuti azicita. (Mat. 28:19, 20) Popanda thandizo la Akhristu a “nkhosa zina,” abale a Khristu sangakwanitse kugwila nchito yaikulu yolalikila imene ikucitika padziko lonse masiku ano. (Yoh. 10:16) Motelo, ngati ndimwe wa nkhosa zina, dziŵani kuti nthawi iliyonse imene mugwila nchitoyi, mumaonetsa kuti mumakonda odzozedwa komanso Yesu. Cina cimene tingacite kuti tikhale mabwenzi a Yehova na Yesu ni kupanga zopeleka zocilikizila nchito imene iwo akuitsogolela. (Luka 16:9) Mwacitsanzo, tingapange zopeleka zocilikizila nchito ya padziko lonse. Zopelekazi zimathandiza pa nchito monga kupeleka thandizo kwa anthu okhudzidwa pakacitika ngozi zacilengedwe kapena matsoka ena. Tingapangenso zopeleka zothandizila pa mpingo wathu. Komanso, tingathandize anthu amene tidziŵa kuti ni osoŵa.—Miy. 19:17. w20.04 24 ¶12-13

Cisanu, November 4

Iyo sidzaganizila Mulungu wa makolo ake. . . . Ndipo idzapeleka ulemu kwa mulungu wa m’malo okhala ndi mipanda yolimba kwambili.—Dan. 11:37, 38.

Pokwanilitsa ulosi wa pa lembali, mfumu ya kumpoto inacita zinthu ‘mosaganizila Mulungu wa makolo ake.’ Kodi inacita bwanji zimenezi? Pofuna kuthetsa zipembedzo, boma la Soviet Union linapanga pulani inayake yomwe colinga cake cinali kulanda mphamvu zipembedzo. Kuyambila mu 1918, bomalo linakhazikitsa lamulo limene linapangitsa kuti m’kupita kwa nthawi, kumasukulu ana aziphunzitsidwa zakuti kulibe Mulungu. Nanga kodi mfumu ya kumpoto inapeleka bwanji “ulemu kwa mulungu wa m’malo okhala ndi mipanda yolimba kwambili”? Boma la Soviet Union linawononga ndalama zambili-mbili popanga gulu la nkhondo lalikulu ndi la mphamvu kwambili, komanso popanga zida za nyukiliya masauzande oculuka kuti ulamulilo wake ukhale wamphamvu. M’kupita kwa nthawi, mfumu ya kumpoto na mfumu ya kum’mwela, onse anakwanitsa kupanga zida zankhondo zambili zamphamvu zotha kupha anthu mabiliyoni! Mfumu ya kumpoto inacilikiza mfumu ya kum’mwela m’njila inayake yapadela. Iwo ‘anaika pamalowo cinthu conyansa cobweletsa ciwonongeko’ cimene ni bungwe la United Nations.—Dan. 11:31. w20.05 6-7 ¶16-17

Ciŵelu, November 5

M’bale wakoyu . . . anali wotayika koma tsopano wapezeka. —Luka 15:32.

Kodi ndani angathandize pa nchito yosakila ozilala? Tonsefe, kaya ndife akulu, apainiya, acibululu a munthu wozilala, kapena ofalitsa mumpingo, tingathandize posakila ozilala. Kodi muli na mnzanu kapena wacibululu amene analeka kusonkhana na kulalikila? Kodi munakumanapo na munthu wozilala pamene munali mu ulaliki wa kunyumba na nyumba kapena pamene munali kucita ulaliki wa poyela? Ngati munthuyo angalole kucezeledwa, mupempheni kuti akupatseni namba yake ya foni kapena adresi, na kumuuza kuti mungakonde kukaipeleka kwa akulu a mumpingo. Mkulu wina dzina lake Thomas kuti: “Coyamba, nimafunsa abale na alongo ngati adziŵako kumene ozilala a mumpingo mwathu amakhala. Nthawi zina nimapempha ofalitsa kuti anifotokozele ngati akumbukilako aliyense amene analeka kusonkhana. Nikapita kukacezela abale na alongo ozilalawo, nimawafunsa za umoyo wa ana awo komanso wa acibululu awo. Anthu ena ozilala amakhala kuti anali kusonkhana pamodzi ndi ana awo, ndipo panthawiyo anawo anapita patsogolo mpaka kufika pokhala ofalitsa. Nawonso anawo tingawathandize kubwelela kwa Yehova.” w20.06 24 ¶1; 25 ¶6-7

Sondo, November 6

Ndidzakumbukila zocita za Ya, ndithu ndidzakumbukila nchito yanu yodabwitsa yakale. —Sal. 77:11.

Pa zolengedwa zonse padzikoli, ni anthu cabe amene amakwanitsa kuphunzila makhalidwe mwa kukumbukila zimene zinawacitikila na kuganizilapo. Mwa kucita izi, timakwanitsa kuphunzila mfundo za makhalidwe abwino na kusintha kaganizidwe kathu komanso umoyo wathu. (1 Akor. 6:9-11; Akol. 3:9, 10) Timakwanitsa ngakhale kuphunzitsa cikumbumtima cathu kusiyanitsa coyenela na cosayenela. (Aheb. 5:14) Timaphunzilanso kukhala acikondi ndi acifundo. Timakwanitsanso kutengela khalidwe la Yehova la cilungamo. Njila imodzi imene tingaonetsele kuti timayamikila mphatso yotha kukumbukila zinthu, ni mwa kuyesetsa kukumbukila zonse zimene Yehova anaticitila potithandiza na kutitonthoza m’mbuyomo. Kucita zimenezi kudzatithandiza kukhala na cidalilo cakuti adzatithandizanso kutsogolo. (Sal. 77:12; 78:4, 7) Njila ina, ni mwa kukumbukila zinthu zabwino zimene ena amaticitila na kuwayamikila. Akatswili anapeza kuti anthu oyamikila, nthawi zambili amakhala acimwemwe. w20.05 23 ¶12-13

Mande, November 7

Uziopa dzina laulemelelo ndi locititsa manthali, dzina lakuti Yehova, amene ndi Mulungu wako.—Deut. 28:58.

Ganizilani mmene Mose anamvelela pamene anali m’phanga n’kuona ulemelelo wa Yehova ukudutsa. Buku la Insight on the Scriptures limakamba kuti zimene Mose anaona “zinali zocititsa mantha kwambili. Ndipo palibe munthu amene anali ataonapo masomphenya aconco Yesu Khristu asanabwele padziko lapansi.” Mose anamva mawu amene ayenela kuti anakambidwa na mngelo. Mawuwo anali akuti: “Yehova, Yehova, Mulungu wacifundo ndi wacisomo, wosakwiya msanga ndiponso wodzaza ndi kukoma mtima kosatha ndi coonadi. Wosungila mibadwo masauzande kukoma mtima kosatha, wokhululukila zolakwa ndi macimo.” (Eks. 33:17-23; 34:5-7) Mosakayikila, Mose anali kukumbukila masomphenyawo akachula dzina la Yehova. Conco n’zosadabwitsa kuti pambuyo pake, iye anauza anthu a Mulungu Aisiraeli mawu a mu lemba la tsiku lalelo. Poganizila za dzina la Yehova, tingacitenso bwino kusinkha-sinkha za makhalidwe ake. Tiyenela kusinkha-sinkha za makhalidwe ake monga mphamvu, nzelu, cilungamo, na cikondi cake. Kuganizila makhalidwe amenewa na ena kungatithandize kuti tizimuopa kwambili Mulungu.—Sal. 77:11-15. w20.06 8-9 ¶3-4

Ciŵili, November 8

Pitiliza kutsatila zimene unaphunzila ndi zimene unakhulupilila pambuyo pokhutila nazo. —2 Tim. 3:14.

Yesu anakamba kuti ophunzila ake adzadziŵika cifukwa ca cikondi cimene amaonetsana. (Yoh. 13:34, 35) Koma pali zina zimene tifunika kucita kuti tikhale na cikhulupililo colimba. Cikhulupililo cathu sicifunika kuzikidwa cabe pa cikondi cimene anthu a Mulungu ali naco. Cifukwa ciani? Cifukwa ngati cikhulupililo cathu n’cozikidwa cabe pa cikondi cimeneco, cingakhale cosavuta kutaya cikhulupililoco. Mwacitsanzo, tingaleke kutumikila Yehova ngati m’bale kapena mlongo, mwina ngakhale mkulu kapena mpainiya wacita chimo lalikulu. Tingalekenso kutumikila Yehova ngati m’bale kapena mlongo watikhumudwitsa, kapena ngati wakhala wampatuko n’kumakamba kuti zimene timakhulupilila n’zabodza. Conco, kuti tikhale na cikhulupililo colimba, tifunika kukhala pa ubale wolimba na Yehova. Ngati cikhulupililo canu mwa Mulungu n’cozikidwa cabe pa zimene anthu ena amacita osati pa ubale wanu na iye, ndiye kuti n’cosalimba. Mmene mumaonela Yehova komanso anthu ake, zingakuthandizeni kukulitsa cikhulupililo canu pa mlingo winawake. Koma cina cofunika kwambili ni kuphunzila Baibo mozama, kumvetsetsa zimene mukuphunzilazo, ndiponso kufufuza n’colinga cakuti mukhutile kuti zimene mumaphunzila ni coonadi conena za Yehova. Mufunika kudzipezela maumboni inu eni oonetsa kuti Baibo imaphunzitsa coonadi ponena za Yehova.—Aroma 12:2. w20.07 8 ¶2-3

Citatu, November 9

Muthandize ofookawo.—Mac 20:35.

Pali zambili zimene zakhala zikucitika zoonetsa kuti angelo amaseŵenzela nafe pamodzi pothandiza ozilala amene ni ofunitsitsa kubwelela kwa Yehova. (Chiv. 14:6) Mwacitsanzo, Silvio wa ku Ecuador, anapemphela kwa Yehova na mtima wonse kuti amuthandize kubwelela mu mpingo. Pamene anali kupemphela, akulu aŵili anafika kunyumba kwake kudzam’cezela. Panthawiyo, akuluwo anakondwela kuyamba kupeleka thandizo lofunikila kwa iye kuti abwelele kwa Yehova. Tidzapeza cimwemwe coculuka ngati tithandiza ozilala kubwelela kwa Yehova. Mpainiya wina dzina lake Salvador, amene amayesetsa kuthandiza ozilala, anati: “Nikaganizila za ozilala amene abwelela kwa Yehova, nthawi zina, nimagwetsa misozi ya cisangalalo. Nimakondwela ngako kuona kuti Yehova wapulumutsa imodzi mwa nkhosa zake zokondedwa kucoka m’dziko la Satana, ndiponso kuti n’nali na mwayi wogwila naye nchito yopulumutsayo.” Ngati ndimwe ozilala, musakayikile kuti Yehova akali kukukondani, ndipo amafuna kuti mubwelele kwa iye. Yehova akukuyembekezelani mwacidwi kuti mubwelele, ndipo adzakulandilani na manja aŵili. w20.06 29 ¶16-18

Cinayi, November 10

[udzayamba] kuona Mlangizi wako Wamkulu.—Yes. 30:20.

Monga ‘Mlangizi wathu Wamkulu,’ Yehova anatipatsa zitsanzo za m’Baibo n’colinga cakuti tiphunzilepo kanthu. (Yes. 30:21) Timaphunzila zambili mwa kusinkha-sinkha nkhani za m’Baibo za anthu amene anaonetsa makhalidwe abwino. Timaphunzila zambili tikaŵelenga zitsanzo za anthu amene analephela kuonetsa makhalidwe abwino monga kudzicepetsa. (Sal. 37:37; 1 Akor. 10:11) Ganizilani zimene zinacitikila Mfumu Sauli. Poyamba iye anali mnyamata wodzicepetsa. Iye anadziŵa kuti panali zinthu zina zimene sakanakwanitsa kucita, ndipo anayopa kulandila udindo wokhala mfumu. (1 Sam. 9:21; 10:20-22) Koma m’kupita kwa nthawi, Sauli anayamba kudzikuza. Khalidwe la kudzikuza limeneli linaonekela atangokhala mfumu. Mwacitsanzo, pa nthawi ina iye analephela kuugwila mtima pamene anali kuyembekezela mneneli Samueli ndipo anapeleka nsembe yopseleza olo kuti sunali udindo wake kucita zimenezo. Zotulukapo zake zinali zakuti Yehova analeka kumuyanja Sauli, ndipo m’kupita kwa nthawi anam’kana kuti asakhale mfumu. (1 Sam. 13:8-14) Tingacite bwino kuphunzilapo kanthu pa citsanzo coticenjeza cimeneci mwa kupewa kucita zinthu modzikuza. w20.08 10 ¶10-11

Cisanu, November 11

Muzilemekeza anthu amene. . . amakutsogolelani mwa Ambuye.—1 Ates. 5:12.

N’zoona kuti mwa Khristu, Yehova wapeleka “mphatso za amuna” mu mpingo wake. (Aef. 4:8) “Mphatso za amuna” zimenezi ziphatikizapo a m’Bungwe Lolamulila, abale othandizila Bungwe Lolamulila, a m’Komiti ya Nthambi, oyang’anila madela, alangizi a masukulu, akulu mu mpingo, komanso atumiki othandiza. Abale onsewa amaikidwa na mzimu woyela kuti asamalile nkhosa za Yehova zamtengo wapatali, na kulimbikitsa mpingo. (1 Pet. 5:2, 3) Abale amaikidwa na mzimu woyela kuti asamalile maudindo osiyana-siyana. Ziwalo za thupi monga manja na miyendo, zimagwila nchito kuti thupi lonse lipindule. Mofananamo, nawonso abale oikidwa paudindo na mzimu woyela amagwila nchito mwakhama kuti apindulitse mpingo wonse. Iwo sadzifunila ulemelelo. M’malomwake, amayesetsa kulimbikitsa abale na alongo awo. (1 Ates. 2:6-8) Timayamikila Yehova potipatsa amuna amenewa oyenelela mwauzimu, komanso osadzikonda. w20.08 21 ¶5-6

Ciŵelu, November 12

Pitani mukaphunzitse anthu. —Mat. 28:19.

Cimodzi mwa zifukwa zimene zimatilimbikitsa kulalikila n’cakuti anthu ni “onyukanyuka ndi otayika,” ndipo ali na njala yaikulu yofuna kuphunzila coonadi ca Ufumu. (Mat. 9:36) Yehova amafuna kuti anthu a mtundu uliwonse adziŵe coonadi molondola kuti akapulumuke. (1 Tim. 2:4) Kudziŵa kuti nchito yolalikila imathandiza anthu kuti akapulumuke, kumatisonkhezela kuyamba kuigwila. Timagwila nchito yopulumutsa miyoyo ya anthu. (Aroma 10:13-15; 1 Tim. 4:16) Conco nafenso tiyenela kukhala na zida zoyenelela zogwilila nchito yathu yolalikila. Tiyenelanso kudziŵa bwino moseŵenzetsela zida zimenezo. Yesu anapeleka malangizo omveka bwino kwa ophunzila ake a mmene akanagwilila nchito yosodza anthu. Anawauza zofunika kunyamula, malo kumene anafunika kukalalikila, ndiponso zimene anafunika kukamba. (Mat. 10:5-7; Luka 10:1-11) Masiku ano, Gulu la Yehova latipatsa Thuboksi imene ili na zida zothandiza kwambili polalikila. Ndipo timaphunzitsidwa mmene tingaseŵenzetsele zida zimenezo. Zimene timaphunzilazo zimatithandiza kusacita mantha polalikila komanso kukulitsa luso pa nchitoyi.—2 Tim. 2:15. w20.09 4 ¶6-7, 10

Sondo, November 13

Palibe cimene cimandisangalatsa kwambili kuposa kumva kuti ana anga akuyendabe m’coonadi.—3 Yoh. 4.

Tangoganizilani cimwemwe cimene mtumwi Yohane anali naco, pamene anamvela kuti anthu amene anawaphunzitsa coonadi akutumikilabe Yehova mokhulupilika. Akhristu okhulupilika amenewo anali kukumana na mavuto ambili. Ndipo Yohane anayesetsa kuwathandiza kulimbitsa cikhulupililo cawo monga ana ake auzimu. Mofanana na Yohane, nafenso timakondwela ngati ana athu kapena anthu amene timaphunzila nawo Baibo adzipatulila kwa Yehova, ndipo akupitiliza kum’tumikila. (3 Yoh. 3) Ca mu 98 C.E., mzimu woyela wa Yehova unamutsogolela Yohane kulemba makalata ake atatu. Iye analemba makalatawo pofuna kulimbikitsa Akhristu okhulupilika kuti apitilize kukhulupilila Yesu na kuyendabe m’coonadi. Yohane anali na nkhawa cifukwa ca zimene aphunzitsi onyenga anali kucita mumpingo wacikhristu. (1 Yoh. 2:18, 19, 26) Anthu ampatuko amenewo anali kukamba kuti amam’dziŵa Mulungu, koma sanali kumvela malamulo ake. w20.07 20 ¶1-3?

Mande, November 14

Khulupililani Mulungu, khulupililaninso ine.—Yoh. 14:1.

Popeza kuti uthenga umene timalalikila timaukhulupilila, timakhala ofunitsitsa kuuzako ena uthenga umenewu mmene tingathele. Timakhulupilila malonjezo opezeka m’Mawu a Mulungu. (Sal. 119:42; Yes. 40:8) Masiku ano, taona maulosi a m’Baibo akukwanilitsidwa. Taona anthu akusintha umoyo wawo pamene ayamba kutsatila malangizo a m’Baibo. Zimenezi zimalimbitsa cikhulupililo cathu cakuti uthenga wabwino wa Ufumu ni uthenga umene munthu aliyense afunika kuumva. Timakhulupililanso Yesu amene Mulungu anamusankha kukhala Mfumu ya Ufumu wake. Conco, olo tikumane na mavuto otani, tidziŵa kuti Yehova nthawi zonse adzakhala pothaŵila pathu na mphamvu yathu. (Sal. 46:1-3) Kuwonjezela apo, sitikayikila kuti Yesu kucokela kumwamba, akutsogolela pa nchito yolalikila pogwilitsila nchito mphamvu na ulamulilo zimene Yehova anamupatsa. (Mat. 28:18-20) Cikhulupililo cimatithandiza kukhala otsimikiza kuti Yehova adzadalitsa khama lathu. w20.09 12 ¶15-17

Ciŵili, November 15

Wandicitila zinthu zabwino. . . . Mayiyu wacita zimene angathe.—Maliko 14:6, 8.

Nthawi zina, alongo angafunikile munthu wina wowaikilako kumbuyo kapena kuti kuwakambilako pa zovuta zimene angakumane nazo. (Yes. 1:17) Mwacitsanzo, mlongo wamasiye kapena amene anasudzulidwa na mwamuna wake, angafunikile wina kumuthandiza pa nchito zina zimene mwamuna wake anali kucita. Komanso mlongo wacikulile angafunikile munthu wina womuthandiza pokamba na madokotala. Nthawi zinanso, mlongo mpainiya amene amagwila nchito zina za m’gulu angafunikile wina womuikilako kumbuyo ngati ena akumunena kuti sacita zambili mu ulaliki monga mmene apainiya ena amacitila. Tiyeni tikambilane citsanzo ca Yesu. Yesu anali kuwaikila kumbuyo mwamsanga alongo ake auzimu ngati anthu ena akuwakambila zoipa. Mwacitsanzo, anaikila kumbuyo Mariya pamene Marita anamuimba mlandu. (Luka 10:38-42) Panthawi inanso, Yesu anaikila kumbuyo Mariya pamene ena anali kumudzudzula poganiza kuti zimene anacita zinali zolakwika. (Maliko 14:3-9) Yesu anadziŵa cimene cinasonkhezela Mariya kucita zimenezo, ndipo anamuyamikila. Iye anafika ngakhale polosela kuti zimene anacitazo zidzalengezedwa “kulikonse kumene uthenga wabwino udzalalikidwe m’dziko lonse.” w20.09 24 ¶15-16

Citatu, November 16

Wetani gulu la nkhosa za Mulungu lomwe analisiya m’manja mwanu, osati mokakamizika, koma mofunitsitsa.—1 Pet. 5:2.

M’busa wabwino anali kudziŵa kuti nthawi zina nkhosa zingasocele. Ngati nkhosa yasocela, m’busa sanali kucita nayo zinthu mwankhanza. Ganizilani citsanzo cimene Yehova anapeleka pothandiza atumiki ake amene anayamba kufooka pom’tumikila. Panthawi ina, mneneli Yona anathaŵa utumiki umene Yehova anamupatsa. Olo zinali conco, Yehova sanamusiye Yona. Monga m’busa wabwino, Yehova anapulumutsa Yona na kum’thandiza kupeza mphamvu zofunikila kuti akwanilitse utumiki wake. (Yona 2:7; 3:1, 2) Pambuyo pake, Mulungu anagwilitsila nchito comela ca mtundu wa mphonda pomuthandiza kuona kuti moyo wa munthu aliyense ni wofunika kwambili. (Yona 4:10, 11) Kodi tiphunzilapo ciani? Akulu afunika kupitilizabe kuthandiza Akhristu amene anazilala. Iwo ayenela kuyesetsa kumvetsetsa cimene cinapangitsa nkhosa kusocela. Ndipo nkhosayo ikabwelela kwa Yehova, akulu ayenela kupitiliza kuonetsa kuti amaikonda na kuidela nkhawa. w20.06 20-21 ¶10-12

Cinayi, November 17

Adzathandizidwa ndi thandizo locepa.—Dan. 11:34.

Ulamulilo wa Soviet Union utatha mu 1991, anthu a Mulungu m’maiko amene anali kulamulidwa na bomalo analandila “thandizo locepa,” kutanthauza kuti anakhala na ufulu kwa kanthawi. Pa cifukwa cimeneci, iwo anayamba kulalikila mwaufulu, ndipo posapita nthawi anthu masauzande ambili m’maikowo anakhala Mboni. M’kupita kwa nthawi, Russia na maiko ogwilizana naye anakhala mfumu ya kumpoto. Boma limakhala mfumu ya kumpoto kapena ya kum’mwela ngati: (1) zocita zake zimakhudza mwacindunji anthu a Mulungu, (2) limacita zinthu zoonetsa kuti limazonda Yehova ndi anthu ake, komanso (3) limalimbana na mfumu inzake yamphamvu. Zocita za Russia na maiko ogwilizana naye zakhudza mwacindunji anthu a Mulungu. Analetsa nchito yolalikila, ndiponso azunza abale na alongo athu masauzande ambili. Zimene acitazi zaonetsa kuti amazonda Yehova komanso anthu ake. Ndipo maiko amenewa akhala akulimbana na mfumu ya kum’mwela, imene ni Ulamulilo Wamphamvu Padziko Lonse wa Britain na America. w20.05 12-13 ¶3-4

Cisanu, November 18

Uzisamala ndi. . . zimene umaphunzitsa.—1 Tim. 4:16.

Popeza nchito yopanga ophunzila imaphatikizapo kuphunzitsa, kaphunzitsidwe kathu kayenela kukhala kaluso. Timaphunzitsa anthu mamiliyoni mfundo za coonadi ca m’Baibo. Timakonda zimene timaphunzitsa kucokela m’Mawu a Mulungu. Mwa ici, tingamafune kumakambapo kwambili pa zimene tikuphunzitsa. Komabe, kaya ni potsogoza Nsanja ya Mlonda, Phunzilo la Baibo la Mpingo, kapena phunzilo la Baibo lapanyumba, wotsogoza sayenela kukambapo kwambili. Ayenela kulola Baibo kuti ndiyo iziphunzitsa. Kuti mphunzitsi acite zimenezi, ayenela kukhala wodziletsa kuti apewe kumafotokoza zonse zimene akudziŵa pa lemba kapena nkhani iliyonse. (Yoh. 16:12) Linganizani cidziŵitso ca m’Baibo cimene munali naco pamene munabatizika, na cimene muli naco lelo. Mwacidziŵikile, panthawiyo munali kungodziŵa ziphunzitso zoyambilila za m’Baibo basi. (Aheb. 6:1) Koma lomba muli na cidziŵitso coculuka, ndipo zakutengelani zaka kuti mukhale naco. Conco, musayese kukhutulila wophunzila wanu watsopano zonse panthawi imodzi. w20.10 14-15 ¶2-4

Ciŵelu, November 19

Iyeyu si mmisili wamatabwa, mwana wa Mariya.—Maliko 6:3.

Yehova anasankhila Yesu makolo abwino koposa. (Mat. 1:18-23; Luka 1:26-38) Mawu a Mariya okhudza mtima opezeka m’Baibo, amaonetsa kukula kwa cikondi cake pa Yehova, na Mawu ake. (Luka 1:46-55) Ndiponso mmene Yosefe anacitila zinthu atapatsidwa malangizo a Yehova, zimaonetsa kuti nayenso anali kuwopa Mulungu, komanso anali kufuna kum’kondweletsa. (Mat. 1:24) Onani kuti Yehova sanasankhile Yesu makolo olemela ayi. Nsembe imene Yosefe na Mariya anapeleka Yesu atabadwa, ionetsa kuti iwo anali osaukila. (Luka 2:24) Iwo ayenela kuti anali kukhala umoyo wosalila zambili, maka-maka banja lawo litakula n’kukhala na ana 7 kapena kuposelapo. (Mat. 13:55, 56) Yehova anateteza Yesu ku mavuto ena, koma sanachingilize Mwana wakeyo ku mavuto onse. (Mat. 2:13-15) Mwacitsanzo, Yesu anali na acibale amene poyamba sanakhulupilile kuti iye anali Mesiya. (Maliko 3:21; Yoh. 7:5) Zionekanso kuti imfa ya Yosefe, tate wake womulela, inam’khudza kwambili. w20.10 26-27 ¶4-6

Sondo, November 20

Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono. —Aheb. 13:5.

Kodi munayamba mwamvelapo kuti muli nokha-nokha, wopanda wina aliyense wokuthandizani kulimbana na vuto limene munakumana nalo? Ambili anamvelapo conco, kuphatikizapo atumiki a Yehova okhulupilika. (1 Maf. 19:14) Ngati zimenezi zingakucitikileni, kumbukilani lonjezo la Yehova lakuti: “Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono.” Conco tingakambe motsimikiza kuti: “Yehova ndiye mthandizi wanga. Sindidzaopa.” (Aheb. 13:5, 6) Mtumwi Paulo analemba mawu amenewa kwa Akhristu anzake a ku Yudeya ca m’ma 61 C.E. Mawu akewo atikumbutsa zolembedwa pa Salimo 118:5-7. Mwa zocitika pa umoyo wake, Paulo mofanana na wamasalimo anadziŵa kuti Yehova ndiye Mthandizi wake. Mwacitsanzo, zaka zoposa ziŵili kumbuyoko asanalembe kalata yake kwa Aheberi, Paulo ananyamuka ulendo woopsa wa panyanja yowinduka na cimphepo camkuntho. (Mac. 27:4, 15, 20) Asanyamuke ulendowo komanso mkati mwa ulendowo, Yehova anaonetsa m’njila zambili kuti analidi Mthandizi wa Paulo. w20.11 12 ¶1-2

Mande, November 21

Usanene kuti: “N’cifukwa ciani kale zinthu zinali bwino kuposa masiku ano?”—Mlal. 7:10.

N’cifukwa ciani si kwanzelu kumangoniza zakuti umoyo wathu unali bwino kale kuposa masiku ano? Kulakalaka umoyo wakale kungatipangitse kumangokumbukila cabe zinthu zabwino zakale. Mwacitsanzo, ganizilani za Aisiraeli akale. Atatuluka mu Iguputo, iwo mwamsanga anaiŵala kuti umoyo wawo unali wa mavuto m’dzikolo. M’malomwake, anangosumika maganizo awo pa zakudya zabwino zimene anali kukonda ku Iguputo. Iwo anati: “Tikukumbukila nsomba zaulele zimene tinali kudya ku Iguputo, nkhaka, mavwende, adyo komanso anyezi wamitundumitundu!” (Num. 11:5) Kodi n’zoona kuti zakudyazo zinali “zaulele”? Ayi. Aisiraeli anali kupeleka malipilo oŵaŵa. Panthawiyo, iwo anali kukhala umoyo wopondelezedwa mwankhanza monga akapolo ku Iguputo. (Eks. 1:13, 14; 3:6-9) Ngakhale n’telo, anaiŵalilatu za mavuto onsewo, n’kuyamba kulakalaka umoyo wakale. Anasankha kusumika maganizo pa zinthu zabwino zakale, m’malo moika maganizo awo pa zabwino zimene Yehova anali atangowacitila. Khalidwe limenelo linaputa mkwiyo wa Yehova.—Num. 11:10. w20.11 25 ¶5-6

Ciŵili, November 22

Yehova ali pafupi ndi anthu a mtima wosweka. Ndipo odzimvela cisoni mumtima mwawo amawapulumutsa.—Sal. 34:18.

Nthawi zina, timaganizila za mfundo yosatsutsika yakuti moyo ni waufupi, komanso ni “wodzaza ndi masautso.” (Yobu 14:1) Conco, m’pomveka kuti nthawi zina timalefuka. Atumiki a Yehova ambili m’nthawi zakale anamvelapo cimodzi-modzi. Ena anali kufuna kuti afe cabe. (1 Maf. 19:2-4; Yobu 3:1-3, 11; 7:15, 16) Koma mobweleza-bweleza, Yehova, Mulungu amene iwo anali kum’dalila anali kuwatonthoza na kuwalimbikitsa. Zocitika za mu umoyo wawo zinalembedwa kuti zititonthoze na kutiphunzitsa. (Aroma 15:4) Ganizilani za Yosefe mwana wa Yakobo, m’kanthawi kocepa, Yosefe anacoka pakukhala mwana wokondedwa wa atate ake, n’kukakhala kapolo wamba wa nduna yacikunja ya ku Iguputo. (Gen. 37:3, 4, 21-28; 39:1) Ndiyeno Mkazi wa Potifara ananamizila Yosefe kuti anali kufuna kum’gwilila. Ndipo popanda kufufuza nkhani yonseyo, Potifara anaponya Yosefe m’ndende na kum’manga m’maunyolo. (Gen. 39:14-20; Sal. 105:17, 18) Conco m’pomveka kuti Yosefe analefuka mtima. w20.12 16-17 ¶1-4

Citatu, November 23

Dzina lanu liyeletsedwe.—Mat. 6:9.

??Yesu anati: “Dzina lanu liyeletsedwe.” Ici n’cimodzi mwa zinthu zofunika kwambili zimene iye anakamba kuti tiyenela kupemphelela. Koma kodi mawu amene Yesu anakamba akuti “dzina lanu liyeletsedwe” atanthauza ciani? Kuyeletsa cinthu kumatanthauza kucipangitsa kukhala cosadetsedwa kapena kuti caukhondo. Ena angafunse kuti, ‘Popeza kuti dzina la Mulungu n’loyela kale, n’cifukwa ciani lifunika kuyeletsedwa?’ Kuti tiyankhe funsoli, coyamba tiyenela kudziŵa kuti dzina n’ciani maka-maka. Dzina silitanthauza cabe mawu oitanila munthu kapena zilembo zongolembedwa pa pepala. Onani zimene Baibo imakamba. Imati: “Ndi bwino kusankha dzina labwino kusiyana ndi cuma coculuka.” (Miy. 22:1; Mlal. 7:1) Kodi n’cifukwa ciani dzina n’lofunika kwambili? Cifukwa cakuti limaphatikizapo mbili ya munthu, kutanthauza mmene anthu ena amamuonela mwini dzinalo. Conco cofunika kwambili si mmene dzina limalembedwela kapena mmene limachulidwila ayi, koma mmene anthu amaganizila akamvela dzinalo kapena akaliona. Anthu akamakamba mabodza ponena za Yehova, ndiye kuti akuipitsa mbili yake. Ndipo akaipitsa mbili yake, ndiye kutinso akudetsa dzina lake. w20.06 3 ¶5-7

Cinayi, November 24

Moyo wanga wasokonezeka kwambili. Kodi inu Yehova, mudzadikila kufikila liti?—Sal. 6:3.

Tingakhale na nkhawa kwambili mpaka kulephela kuganizila zinthu zina. Mwacitsanzo, tingade nkhawa kuti sitidzakhala na ndalama zokwanila zogulila zofunikila, kapena kuti tidzalephela kugwila nchito tikadwala, kapena kucotsedwa nchito kumene. Mwina tingakhalenso na nkhawa kuti sitidzakhala okhulupilika tikayesedwa kuti tiphwanye malamulo a Mulungu. Posacedwa, Satana adzapangitsa anthu amene amawalamulila kuukila anthu a Mulungu. Conco, tingakhale na nkhawa kuti tidzacita ciani panthawiyo. Koma mwina tingadzifunse kuti: ‘Kodi n’kulakwa kuda nkhawa pa zinthu zimenezi?’ Tidziŵa kuti Yesu anauza otsatila ake kuti: “Lekani kudela nkhawa.” (Mat. 6:25) Kodi izi zitanthauza kuti iye amatiyembekezela kukhala opanda nkhawa iliyonse? Kutalitali! Ndi iko komwe, atumiki a Yehova ena akale okhulupilika anavutikapo na nkhawa, koma Yehova sanaleke kuwakonda. (1 Maf. 19:4) Conco, pokamba mawu amenewa, Yesu anali kutilimbikitsa kuti tisamade nkhawa kwambili posakila zofunikila mu umoyo cakuti n’kulephela kutumikila bwino Mulungu. w21.01 3 ¶4-5

Cisanu, November 25

Mutu wa mkazi ndi mwamuna.—1 Akor. 11:3.

Mwamuna adzayankha mlandu kwa Yehova na Yesu pa mmene amacitila zinthu na banja lake. (1 Pet. 3:7) Monga Mutu wa banja lake lonse m’cilengedwe, Yehova ali na mphamvu zopanga malamulo a mmene ana ake ayenela kukhalila, na kuonetsetsa kuti malamulowo akutsatilidwa. (Yes. 33:22) Yesu nayenso monga mutu wa mpingo wacikhristu ali na ufulu wopanga malamulo na kuonetsetsa kuti akutsatilidwa. (Agal. 6:2; Akol. 1:18-20) Potengela Yehova na Yesu, mutu wa banja lacikhristu ali na mphamvu zopangila banja lake zosankha. (Aroma 7:2; Aef. 6:4) Komabe, mphamvu zake zili na malile. Mwacitsanzo, malamulo ake ayenela kuzikidwa pa mfundo za m’Mawu a Mulungu. (Miy. 3:5, 6) Ndipo mutu wa banja alibe mphamvu zopangila malamulo anthu ena amene si a m’banja lake. (Aroma 14:4) Cina, ana ake akakula n’kucoka pakhomo amapitiliza kumulemekeza, koma sakhalanso pansi pa umutu wake.—Mat. 19:5. w21.02 2-3 ¶3-5

Ciŵelu, November 26

[Samalila] anthu amene ndi udindo [wako] kuwasamalila. —1 Tim. 5:8.

Imodzi mwa njila yofunika imene mutu wa banja ungaonetsele kuti umakonda banja lake, ni mwa kulipezela zofunikila zakuthupi. Komabe, ayenela kukumbukila kuti zinthu zakuthupi sizingakhutilitse banja lake kuuzimu. (Mat. 5:3) Pamene Yesu anali kufa pamtengo wozunzikilapo anayesesa kuti Mariya ali na womusamalila. Ngakhale kuti anali kumva ululu kwambili, Yesu anakonza zakuti Yohane azisamalila Mariya. (Yoh. 19:26, 27) M’bale amene ni mutu wa banja mwina angakhale na maudindo ambili ofunika. Angafunike kugwila nchito yake yakuthupi molimbika kuti khalidwe lake licititse kuti Yehova alemekezeke. (Aef. 6:5, 6; Tito 2:9, 10) Ndipo mwina angakhale na nchito zina mu mpingo, monga kucita ubusa na kutsogolela pa nchito yolalikila. Panthawi imodzi-modzi, m’pofunika kwambili kuti aziphunzila Baibo na mkazi wake komanso ana ake nthawi zonse. Iwo adzayamikila kwambili zoyesa-yesa zake powathandiza kukhala athanzi kuthupi, acimwemwe, komanso olimba kuuzimu.—Aef. 5:28, 29; 6:4. w21.01 12 ¶15, 17

Sondo, November 27

[Mkazi wabwino] amayang’anila zocitika za pabanja pake.—Miy. 31:27.

Pofotokoza za mkazi wabwino, Mawu a Mulungu amanena kuti amayang’anila nyumba yake, amagula na kusamalila malo, ndiponso amacita malonda. (Miy. 31:15, 16, 18) Iye si kapolo amene alibe ufulu wofotokoza maganizo ake. M’malomwake, mwamuna wake amam’dalila mwa kumvetsela malingalilo ake. (Miy. 31:11, 26) Ngati mwamuna alemekeza mkazi wake mwa njila imeneyi, mkaziyo adzamugonjela mokondwela. Ngakhale kuti Yesu anacita zinthu zazikulu, saona kuti kugonjela Yehova n’kudzipeputsa. (1 Akor. 15:28; Afil. 2:5, 6) Mofananamo, mkazi wabwino amene amatengela citsanzo ca Yesu saona kuti kugonjela mwamuna wake n’kudzipeputsa. Iye amacilikiza mwamuna wake osati cabe cifukwa comukonda, koma kweni-kweni cifukwa cokonda Yehova na kum’lemekeza. Mkazi wacikhristu wogonjela, sangacilikize mwamuna wake ngati wam’pempha kucita zinthu zophwanya malamulo a m’Baibo kapena mfundo zake. w21.02 11 ¶14-15; 12 ¶19

Mande, November 28

Cisautso cimabala cipililo. —Aroma 5:3.

Cikondi pa Mulungu cimathandiza atumiki a Yehova nthawi zonse kupilila mazunzo. Mwacitsanzo, atumwi atalamulidwa na khoti lamphamvu komanso lapamwamba la Ayuda kuti aleke kulalikila, cikondi pa Mulungu cinawalimbikitsa “kumvela Mulungu monga wolamulila, osati anthu.” (Mac. 5:29; 1 Yoh. 5:3) Cikondi cacikulu cotelo cimalimbitsanso abale athu masiku ano, amene ambili a iwo amaima zolimba pa cikhulupililo pamene akuzunzidwa na maboma oipa komanso amphamvu. M’malo molefuka, timauona kukhala mwayi kupilila cidani ca dzikoli. (Mac. 5:41; Aroma 5:4, 5) Ciyeso cikacokela kwa a m’banja lathu, cimakhala cimodzi mwa mayeso ovuta kwambili kuwapilila. Tikayamba kuonetsa cidwi na coonadi, ena mwa a m’banja lathu angaganize kuti tasoceletsedwa. Ena angaganize kuti tacita misala. (Yelekezelani na Maliko 3:21) Angafike ngakhale potitsutsa kwambili. Koma sitiyenela kudabwa na citsutso cimeneci. Yesu anati: “Adani a munthu adzakhala a m’banja lake lenileni.”—Mat. 10:36 . w21.03 21 ¶6-7

Ciŵili, November 29

Munthu aliyense akhale wofulumila kumva, wodekha polankhula.—Yak. 1:19.

Ngati mwapita na wofalitsa kuphunzilo yake ya Baibo, mvetselani mwachelu pamene mphunzitsi na wophunzila akukambilana. Mukacita zimenezi mudzakhala wokonzeka kupeleka thandizo pakafunikila kutelo. Komabe, mufunika kukhala wozindikila. Mwacitsanzo, simungafunike kukambapo kwambili, kudula mawu mphunzitsi, kapena kubweletsapo nkhani ina. Koma na ndemanga yacidule, fanizo, kapena funso, mungathandize kumveketsa mfundo imene ikuphunzitsidwa. Nthawi zina mungaone kuti mulibe zambili zokambapo pankhaniyo. Koma ngati mumuyamikila wophunzilayo na kumuonetsa cidwi, mudzam’thandiza kwambili kupita patsogolo. Ngati m’poyenela, fotokozelani wophunzilayo mmene munaphunzilila coonadi, mmene munagonjetsela copinga cina cake kapena mmene Yehova wakuthandizilani mu umoyo wanu. (Sal. 78:4, 7) Mwina izi n’zimene wophunzilayo angafunikile kumva. Zimenezi zingalimbitse cikhulupililo cake, kapena kum’limbikitsa kupita patsogolo mpaka kukabatizika. w21.03 10 ¶9-10

Citatu, November 30

Mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzila anga.—Mat. 28:19.

Kodi ndani kwenikweni amene amacititsa kuti zinthu zitiyendele bwino mu ulaliki? Paulo anayankha funso limeneli polembela kalata Akhristu a mu mpingo wa ku Korinto. Iye anati: “Ineyo ndinabzala, Apolo anathilila, koma Mulungu ndiye anakulitsa. Cotelo wobzala kapena wothilila sali kanthu, koma Mulungu amene amakulitsa.” (1 Akor. 3:6, 7) Tiyenela kutengela citsanzo ca Paulo mwa kutamanda Yehova nthawi zonse ngati ulaliki ukutiyendela bwino. Tingaonetse bwanji kuti timayamikila mwayi ‘wogwila nchito limodzi’ na Yehova, Yesu, ndiponso angelo? (2 Akor. 6:1) Tingatelo mwa kuyesetsa kusakila mipata youzako ena uthenga wabwino. Tikafesa mbewu za coonadi, tiyenelanso kumazithilila. Ngati munthu waonetsa cidwi, tiyenela kuyesetsa kucita ulendo wobwelelako n’colinga coyambitsa phunzilo la Baibo. Pamene wophunzila akupita patsogolo, timakondwela kuona Yehova akumuthandiza kusintha maganizo na mtima wake. w20.05 30 ¶14, 16-18

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani