December
Cinayi, December 1
Wokayikila ali ngati funde lapanyanja lotengeka ndi mphepo ndi lowindukawinduka.—Yak. 1:6.
Nthawi zina cingakhale covuta kumvetsetsa mfundo ina yake m’Mawu a Mulungu. Kapena mwina Yehova sangayankhe mapemphelo athu mmene tinali kuyembekezela. Izi zingatipangitse kuyamba kukaikila. Ngati siticitapo kanthu pa zimene timakaikila, cikhulupililo cathu cingafooke ndipo ubale wathu na Yehova ungawonongeke. (Yak. 1:7, 8) Ndipo kukaikila kungatitaitse ngakhale ciyembekezo cathu ca zakutsogolo. Mtumwi Paulo anayelekezela ciyembekezo cathu ca zakutsogolo na nangula. (Aheb. 6:19) Nangula amathandiza kuti sitima yapamadzi ikhazikike panthawi yacimphepo, kutinso isatengeke n’kukagunda miyala. Komanso nangulayo angakhale wopanda thandizo ngati cheni yake yomangilila ku sitimayo ni yosalimba. Ndipo nguwe nayonso imapangitsa cheni kukhala yofooka. Nakonso kukaikila kumafooketsa cikhulupililo cathu. Munthu wokaikila akayesedwa mwa kutsutsidwa, angataye cikhulupililo cake cakuti Yehova adzakwanilitsa malonjezo ake. Tikataya cikhulupililo cathu, timatayanso ciyembekezo cathu. Munthu wotelo angakhale alibiletu cimwemwe ngakhale pang’ono! w21.02 30 ¶14-15
Cisanu, December 2
Abulahamu anakhulupilila mwa Yehova.—Yak. 2:23.
Abulahamu ayenela kuti anali na zaka zoposa 70 pamene anacoka mumzinda wa Uri pamodzi na banja lake. (Gen. 11:31–12:4) Ndipo kwa zaka pafupi-fupi 100, anali kukhala m’matenti m’madela osiyana-siyana a dziko la Kanani. Abulahamu anamwalila ali na zaka 175. (Gen. 25:7) Koma iye sanaone kukwanilitsidwa kwa lonjezo la Yehova lakuti adzapeleka dziko limene anayendamo kwa mbadwa zake. Ndipo anafa asanaone mzinda kapena kuti Ufumu umene Mulungu anakhazikitsa. Ngakhale n’conco, Malemba amati Abulahamu anamwalila ali “wokalamba, . . . ndi wokhutila.” (Gen. 25:8) Ngakhale kuti iye anakumana na mavuto ambili, anakhalabe na cikhulupililo colimba ndiponso anayembekezela Yehova mwacimwemwe. Kodi anakwanitsa bwanji kupilila? Anakwanitsa cifukwa pa umoyo wake wonse, Yehova anali kumuteteza na kumusamalila monga bwenzi lake. (Gen. 15:1; Yes. 41:8; Yak. 2:22) Mofanana na Abulahamu, nafenso tikuyembekezela mzinda wokhala na maziko eni-eni. (Aheb. 11:10) Komabe, sitikuyembekezela kumangidwa kwa mzindawo cifukwa Ufumu wa Mulungu unakhazikitsidwa kale mu 1914, ndipo pano tikamba ukulamulila kumwamba. (Chiv. 12:7-10) Cimene tikuyembekezela n’cakuti uyambe kulamulila pano padziko lapansi. w20.08 4-5 ¶11-12
Ciŵelu, December 3
Maganizo a mumtima mwa munthu ali ngati madzi akuya, koma munthu wozindikila ndi amene amawatunga.—Miy. 20:5.
Kuti timvetsele mwachelu kwa ena, tifunika kukhala odzicepetsa komanso oleza mtima. Kucita zimenezi n’kofunika pa zifukwa zitatu. Coyamba, tidzapewa kuweluza ena molakwika. Caciŵili, tidzakwanitsa kudziŵa mmene m’bale wathu akumvelela komanso zolinga zake, ndipo izi zidzatilimbikitsa kucita naye zinthu mwacifundo kwambili. Cacitatu, tikapatsa mpata m’bale wathu kuti afotokoze za mumtima mwake, tingamuthandize kudzidziŵa bwino. Zili conco cifukwa nthawi zina anthufe sitidziŵa cimene cikutivutitsa mumtima mpaka titafotokozelako ena mmene tikumvelela. Abale na alongo athu ena zimawavuta kufotokoza mmene akumvelela cifukwa ca mmene anakulila, cikhalidwe cawo, kapena cifukwa ca cibadwa cawo. Pangatenge nthawi yaitali kuti ayambe kutidalila moti n’kukamba nafe momasuka. Koma akamasuka, m’pamene tingadziŵe bwino mmene akumvelela. Ngati tikhala oleza mtima monga Yehova, iwo angayambe kutidalila. Ndipo akafuna kutifotokozela za mumtima mwawo, tiyenela kumvetsela mwachelu. w20.04 15-16 ¶6-7
Sondo, December 4
Uzisodza anthu amoyo. —Luka 5:10.
Nsomba zimakhala pa malo amene pali madzi amene zimakonda, komanso pamene zimapeza cakudya cambili. Msodzi afunikanso kuganizila nthawi yoyenela yopita kukapha nsomba. Ponena za nthawi yabwino yopha nsomba, onani zimene m’bale wina ku cisumbu ca Pacific anauza mmishonale atapangana naye kuti akaphe nsomba pamodzi. Mmishonaleyo anati: “Tikakumana maŵa m’maŵa pa 9 awazi.” M’baleyo anayankha kuti: “Aa! 9 awazi, mungokamba cifukwa cosadziŵa. Tifunika kupita kukapha nsomba pa nthawi imene tingazipeze, osati cabe pa nthawi yotikomela.” Mofananamo, asodzi a anthu m’nthawi ya atumwi anali kupita kumalo kumene akanapeza anthu komanso panthawi imene anthuwo akanapezeka. Mwacitsanzo, otsatila a Yesu anali kulalikila ku kacisi na m’masunagoge, kunyumba ndi nyumba, komanso kumisika. (Mac. 5:42; 17:17; 18:4) Nafenso tifunika kudziŵa nthawi yabwino imene tingapeze anthu panyumba, kapena kumalo ena m’gawo lathu. Tifunika kukhala okonzeka kusintha ndandanda yathu kuti tipite kukalalikila panthawi yoyenela komanso kumalo kumene tingapeze anthu.—1 Akor. 9:19-23. w20.09 4 ¶8-9
Mande, December 5
Polankhula zoona, tiyeni tikule m’zinthu zonse, kudzela m’cikondi, pansi pa iye amene ndi mutu, Khristu.—Aef. 4:15.
Njila imodzi imene tingalimbitsile ubwenzi wathu na Yesu, ni kucilikiza makonzedwe a gulu la Yehova. Timalimbitsa ubwenzi wathu na Yesu, mutu wa mpingo, mwa kucita zinthu mogwilizana na amuna amene anaikidwa kuti azititsogolela mwacikondi. (Aef. 4:16) Mwacitsanzo, tsopano tikucita zonse zotheka kuti Nyumba za Ufumu zonse zizigwilitsidwa nchito mokwanila. Pa cifukwa ici, mipingo ina anaiphatikiza pamodzi. Izi zathandiza kupulumutsa ndalama zambili za gulu. Koma zacititsanso kuti ofalitsa ena asamukile ku mipingo ina. N’kutheka kuti ofalitsa okhulupilika amenewa anatumikila mu mpingo wawo kwa zaka zambili, ndipo anapanga ubwenzi wathithithi na abale na alongo mu mpingowo. Koma tsopano auzidwa kuti asamukile ku mpingo wina. Kukamba zoona, Yesu amakondwela kwambili akaona Akhristu okhulupilikawa akugonjela makonzedwe amenewa. w20.04 24 ¶14
Ciŵili, December 6
Mfumu ya kum’mwela idzayamba kukankhana nayo.—Dan. 11:40.
Mfumu ya kumpoto na mfumu ya kum’mwela akhala akulimbilana ulamulilo wa dziko lonse. Mwacitsanzo, ganizilani zimene zinacitika Nkhondo Yaciŵili ya Padziko Lonse itatha. Pambuyo pa nkhondoyo, Boma la Soviet Union linayamba kulamulila madela ambili ku Europe. Izi zinakakamiza mfumu ya kum’mwela kupanga mgwilizano wa zankhondo na maiko ena. Mgwilizano umenewo umachedwa NATO (North Atlantic Treaty Organization). Mfumu ya kumpoto na mfumu ya kum’mwela akhala akupikisana pofuna kupanga gulu lankhondo lamphamvu kwambili padziko lonse. Iwo amawononga ndalama zambili pocita zimenezi. Kuwonjezela apo, mfumu ya kumpoto inalimbana na mfumu ya kum’mwela mwa kuthandiza maiko kapena magulu odana na mfumu ya kum’mwelayo mu Africa, ku Asia, na ku Latin America. M’zaka zaposacedwa, Russia na maiko ogwilizana naye akhala amphamvu kwambili padzikoli. Iwo amalimbana na mfumu ya kum’mwela poseŵenzetsa makompyuta. Mfumu ya kumpoto na mfumu ya kum’mwela amaimbana milandu yakuti akuwonongelana mapulogilamu a pa kompyuta, pofuna kusokoneza cuma ca mfumu inzake kapena kugwetsa boma. Ndiponso monga mmene Danieli anakambila, mfumu ya kumpoto ikupitiliza kuzunza anthu a Mulungu.—Dan. 11:41. w20.05 13 ¶5-6
Citatu, December 7
Inetu ndidzafunafuna nkhosa zanga ndi kuzisamalila.—Ezek. 34:11.
“Kodi mayi angaiŵale mwana wake woyamwa”? Yehova anafunsa funso limeneli m’masiku a mneneli Yesaya. Mulungu anauza anthu ake kuti, “Ngakhale amayi amenewa akhoza kuiwala, koma ine sindidzakuiwala.” (Yes. 49:15) Si kaŵili-kaŵili Yehova kudziyelekezela na mayi. Koma izi n’zimene anacita panthawiyo. Mulungu anayelekezela cikondi camphamvu cimene cimakhalapo pakati pa mayi na mwana wake pofotokoza cikondi camphamvu cimene iye ali naco pa atumiki ake. Amayi ambili angavomeleze zimene mlongo wina dzina lake Jasmin anakamba. Iye anati: “Ukamayamwitsa mwana, cikondi pakati iwe na mwanayo cimakula kwambili moti cimakhalapo kwa moyo wonse.” Yehova amadziŵa ngakhale pamene mmodzi cabe wa ana ake waleka kulalikila na kusonkhana. Ambili mwa abale na alongo athu ozilala amenewa m’kupita kwa nthawi amabwelelanso mu mpingo, ndipo timawalandila na manja aŵili. Yehova amafuna kuti iwo abwelele. Ifenso n’zimene timafuna.—1 Pet. 2:25. w20.06 18 ¶1-3
Cinayi, December 8
[Ikani maso anu] pa zinthu zosaoneka, . . . Pakuti zooneka n’zakanthawi, koma zosaoneka n’zamuyaya.—2 Akor. 4:18.
Pali cuma cina cimene sicioneka. Ndipo cuma cosaoneka ndico camtengo wapatali kwambili. Pa ulaliki wake wa pa phili, Yesu anakamba za cuma ca kumwamba cimene n’camtengo wapatali kwambili kuposa cuma cakuthupi. Kenako anakamba kuti: “Kumene kuli cuma cako, mtima wako umakhalanso komweko.” (Mat. 6:19-21) Anthufe timafuna-funa cinthu cimene timaona kuti n’cofunika kwambili kapena camtengo wapatali. Timaunjika ‘cuma cathu kumwamba’ mwa kuyesetsa kukhala na mbili yabwino kwa Mulungu, kapena kuti kukhala naye pa ubwenzi. Yesu anakamba kuti cuma cimeneci sicingawonongeke kapena kubedwa. Mtumwi Paulo anatilimbikitsa kuti tiyenela ‘kuika maso athu pa zinthu zosaoneka.’ (2 Akor 4:17, 18) Zinthu zosaoneka zimenezo ni cuma cimene cimaphatikizapo madalitso amene tidzalandila m’dziko latsopano la Mulungu. Kodi timayamikila cuma cosaoneka cimeneci? w20.05 26 ¶1-2
Cisanu, December 9
Malangizo anga adzagwa ngati mvula.—Deut. 32:2.
Zimene Mose anaphunzitsa Aisiraeli zinalimbitsa cikhulupililo cawo, ndiponso zinawatsitsimula monga mmene mvula yowaza imatsitsimulila zomela. Nanga ife tingacite ciani kuti kaphunzitsidwe kathu kazikhala kolimbikitsa komanso kotsitsimula? Polalikila ku nyumba na nyumba kapena pocita ulaliki wapoyela, tiyenela kuonetsa anthu dzina la Mulungu lakuti Yehova poseŵenzetsa Baibo. Ndiponso tingawagaŵile mabuku, mavidiyo, na zinthu zina za pa webusaiti yathu zimene n’zolemekeza Yehova. Tikakhala kunchito, kusukulu, kapena paulendo, tingapeze mpata wouzako ena za Mulungu wathu wacikondi kuti amudziŵe. Tikamauzako ena za colinga ca Yehova kwa anthu komanso dziko lapansi, timawathandiza kuzindikila kuti iye amatikonda kwambili. Timathandizanso kuyeletsa dzina la Mulungu mwa kuuzako ena coonadi ponena za Atate wathu wacikondi. Tikatelo, timawathandiza kuti aleke kukhulupilila mabodza amene anthu ena anawaphunzitsa ponena za Yehova. Coonadi ca m’Baibo cimene timaphunzitsa anthu cimawatsitsimula kwambili.—Yes. 65:13, 14. w20.06 10 ¶8-9
Ciŵelu, December 10
Bwelelani kwa ine ndipo ine ndibwelela kwa inu.—Mal. 3:7.
Kodi ni makhalidwe ati amene tiyenela kukhala nawo kuti tikwanitse kuthandiza anthu amene afuna kubwelela kwa Yehova? Onani mfundo zimene tingaphunzilepo pa fanizo la Yesu la mwana woloŵelela. (Luka 15:17-24) Mwanayo anazindikila kuti anacita zinthu mopanda nzelu, ndipo anaganiza zobwelela kunyumba. Atate wake atamuona, anamuthamangila na kumukumbatila pofuna kum’tsimikizila kuti amam’konda. Mwanayo anali kuvutitsidwa na cikumbumtima, komanso anali kudziona wosayenelela kuchedwa mwana wawo. Atate wake anamumvela cifundo mwanayo pamene anali kuwafotokozela mocokela pansi pa mtima mmene anali kumvelela. Ndiyeno, atate wake anacita zinthu zina zimene zinathandiza mwanayo kuona kuti amulandila na manja aŵili, monga mwana wawo wokondedwa. Pofuna kuonetsa kuti amamukondadi mwana wolapayo, anamukonzela phwando na kum’patsa zovala zabwino. Yehova ali ngati tate wa m’fanizo limeneli. Amawakonda abale na alongo athu ozilala ndipo amafuna kuti abwelele kwa iye. Mwa kutengela citsanzo ca Yehova, tingawathandize ozilala kubwelela kwa iye. Kuti tikwanitse kucita zimenezi, tifunika kukhala oleza mtima, acifundo, komanso acikondi. w20.06 25-26 ¶8-9
Sondo, December 11
Mukamasunga mawu anga nthawi zonse, ndiye kuti ndinudi ophunzila anga. Mudzadziŵa coonadi, ndipo coonadi cidzakumasulani. —Yoh. 8:31, 32.
Yesu anakamba kuti ena amalandila coonadi “mwacimwemwe,” koma akakumana na mavuto cikhulupililo cawo cimafooka. (Mat. 13:3-6, 20, 21) Mwina iwo amafooka cifukwa cakuti poyamba sanazindikile kuti ngati munthu wasankha kutsatila Yesu, akhoza kukumana na mavuto. (Mat. 16:24) Mwinanso anali kuganiza kuti munthu akakhala Mkhristu ndiye kuti basi sazikumana na mavuto alionse, azingolandila madalitso okha-okha. Koma popeza tikukhala m’dziko loipali, tidzakumanabe na mavuto. Nthawi iliyonse zinthu zingasinthe mu umoyo, ndipo cimwemwe cathu cingacepe. (Sal. 6:6; Mlal. 9:11) Abale na alongo ambili amaonetsa kuti amakhulupililadi kuti anapeza coonadi. N’cifukwa ciani takamba conco? Cifukwa safooka m’cikhulupililo ngakhale pamene wokhulupilila mnzawo wawakhumudwitsa kapena pamene wacita chimo. (Sal. 119:165) M’malomwake, iwo akakumana na ciyeso, cikhulupililo cawo cimalimbilako, osati kucepa. (Yak. 1:2-4) Tifunika kukhala na cikhulupililo colimba ngati cimeneco. w20.07 8 ¶1; 9 ¶4-5
Mande, December 12
Ngati wina akusoŵa nzelu, azipempha kwa Mulungu.—Yak. 1:5.
Musanayambe kuŵelenga Baibo, pemphani Yehova kuti akuthandizeni kuona mmene mungapindulile na zimene mudzaŵelenga. Mwacitsanzo, ngati mufuna malangizo a zimene mungacite kuti mulimbane na vuto lina lake, pemphani Yehova kuti akuthandizeni kupeza mfundo m’Mawu ake zimene zingakutsogoleleni. (Afil. 4:6, 7) Yehova anatipatsa luso lapadela lotha kuyelekeza zinthu m’maganizo. Kuti nkhani ya m’Baibo imene mukuŵelenga ikhale yeni-yeni kwa inu, yesani kuyelekeza nkhaniyo m’maganizo ndipo muzidziona kuti munthu amene mukuŵelengayo ndinu. Yesani kuona zinthu zimene munthuyo anali kuona, na kuyesa kumvela mmene anamvelela. Cotsatila sinkha-sinkhani. Kusinkha-sinkha kumatanthauza kuganizila mosamala zimene mukuŵelenga, komanso mmene nkhaniyo ikukhudzilani. Kumathandiza munthu kugwilizanitsa mfundo na kumvetsetsa mozama nkhaniyo. Kuŵelenga Baibo popanda kusinkha-sinkha kuli monga kungoyang’ana nchelwa cabe, osazitenga kuti umange nyumba. Kusinkha-sinkha kudzakuthandizani kuti mukhale na cithunzi conse. w21.03 15 ¶3-5
Ciŵili, December 13
Ndikuyamika Mulungu, . . . sindiiŵala za iwe m’mapembedzelo anga, usana ndi usiku. —2 Tim. 1:3.
Zikanatheka Paulo kusumika maganizo ake pa zakumbuyo, na kuganiza kuti ngati sakanasankha kukhala Mkhristu wokangalika motelo, mwina sakanamangidwa. Iye akanakwiyila amuna a m’cigawo ca Asia amene anamusiya, ndipo akanaleka kudalila mabwenzi ake ena. Koma Paulo sanacite zimenezo. Ngakhale kuti Paulo anali kudziŵa kuti posacedwa adzaphedwa, iye anasumikabe maganizo pa nkhani yaikulu, imene ni kubweletsa ulemelelo kwa Yehova. Ndipo anapitiliza kuganizila mmene angalimbikitsile ena. Iye anadalila Yehova mwa kupemphela nthawi zonse. M’malo mosumika maganizo ake pa aja amene anamusiya, anayamikila mocokela pansi pamtima thandizo limene anzake okhulupilika anam’patsa. Kuwonjezela apo, Paulo anapitilizabe kuŵelenga Mawu a Mulungu. (2 Tim. 3:16, 17; 4:13) Ndipo koposa zonse, iye anali na cidalilo conse kuti Yehova na Yesu amamukonda. w21.03 18 ¶17-18
Citatu, December 14
Monga momwe amasonkhanitsila namsongole ndi kumutentha pamoto, zidzakhalanso conco pa mapeto a nthawi ino.—Mat. 13:40.
Panthawi inayake m’zaka za m’ma 100 C.E., Akhristu ambili onyenga analoŵa mumpingo wacikhristu. Iwo anayamba kuphunzitsa ziphunzitso zabodza na kuphimba coonadi ca m’Mawu a Mulungu. Kucokela nthawiyo mpaka kufika mu 1870, padziko lapansi panalibe gulu la atumiki a Mulungu. Akhristu onyenga anaculuka mumpingo wacikhristu monga namsongole, moti zinali zovuta kwambili kudziŵa Akhristu oona. (Mat. 13:36-43) N’cifukwa ciani kudziŵa zimenezi n’kofunika? Cifukwa zionetsa kuti mafumu kapena maboma amene analamulila kuyambila m’caka ca 100 C.E. mpaka mu 1870, amene taŵelenga mu Danieli caputa 11, sangakhale mfumu ya kumpoto kapena mfumu ya kum’mwela. Zili conco cifukwa panthawiyi panalibe gulu la anthu a Mulungu limene akanaliukila. Koma pambuyo pa caka ca 1870, mafumu aŵili amenewa, ya kumpoto na ya kum’mwela, anaonekelanso. w20.05 3 ¶5
Cinayi, December 15
Pali mtundu umene waloŵa m’dziko langa.—Yow. 1:6.
Yoweli anakambilatu kuti mlili wa dzombe udzawononga dziko la Isiraeli ndipo lidzadya comela ciliconse m’dzikolo! (Yow. 1:4) Kwa zaka zambili, takhala tikukhulupilila kuti ulosiwu ni wophiphilitsila, ndipo umakamba za atumiki a Yehova amene akupitiliza kugwila nchito yolalikila monga gulu la dzombe limene palibe angaliletse. Tinali kukhulupilila kuti nchitoyi imasautsa ‘dziko,’ kapena kuti anthu amene amatsogoleledwa na atsogoleli a zipembedzo. Koma tikaŵelenga mosamala mbali zonse za ulosiwu, tiona kuti m’poyenela kusintha kamvedwe kathu. Onani zimene Yehova analonjeza ponena za mlili wa dzombe. Iye anati: “Ndidzakucotselani mdani wa kumpoto [dzombe] kuti akhale kutali ndi inu.” (Yow. 2:20) Ngati dzombe liimila Mboni za Yehova zimene zimagwila nchito yolalikila na kupanga ophunzila pomvela lamulo la Yesu, n’cifukwa ciani Yehova analonjeza kuti adzalicotsa? (Ezek. 33:7-9; Mat. 28:19, 20) Izi zionetselatu kuti dzombe limene Yehova akulicotsa siliimila atumiki ake okhulupilika. Koma liimila cinacake kapena winawake amene amazunza anthu ake. w20.04 3 ¶3-5
Cisanu, December 16
Ngati wina akusoŵa nzelu, azipempha kwa Mulungu.—Yak. 1:5.
Kodi tiyenela kucita ciani tikaona kuti Yehova sanayankhe pemphelo lathu mwamsanga? Yakobo anakamba kuti tiyenela kupitilizabe kum’pempha Mulungu. Yehova sakalipa ngati tipitilizabe kum’pempha nzelu. Iye sadzatitonza. Atate wathu wakumwamba “amapeleka mowolowa manja” tikamupempha nzelu zotithandiza kupilila mayeso. (Sal. 25:12, 13) Iye amaona mavuto athu, ni wacifundo, ndipo ni wofunitsitsa kutithandiza. Kudziŵa zimenezi, kumatibweletsela cimwemwe! Koma kodi Yehova amatipatsa bwanji nzelu? Kupitila m’Mawu ake. (Miy. 2:6) Kuti tipeze nzelu zimenezo, timafunika kuŵelenga Mawu a Mulungu na zofalitsa zozikidwa pa Baibo. Koma palinso zina zimene tiyenela kucita. Tifunika kuseŵenzetsa nzelu za Mulungu mu umoyo wathu mwa kucita zimene iye amatiuza. Yakobo analemba kuti: “Muzicita zimene mawu amanena, osati kungomva cabe.” (Yak. 1:22) Tikamasewenzetsa malangizo a Mulungu, timakhala anthu obweletsa mtendele, ololela, komanso acifundo. (Yak. 3:17) Makhalidwe amenewa amatithandiza kupilila mayeso alionse popanda kutaya cimwemwe cathu. w21.02 29 ¶10-11
Ciŵelu, December 17
Thupi lonselo limakula . . . malinga ndi nchito yoyenelela ya ciwalo ciliconse.—Aef. 4:16.
Wophunzila Baibo amapitabe patsogolo mpaka kukabatizika akamalandila thandizo locokela kwa ena mumpingo. Wofalitsa aliyense angathandize kuti mpingo ukule. Mlongo wina mpainiya anakamba kuti: “Pali mawu akuti kulela mwana n’kwatonse. Niona kuti n’zofanana na nchito yopanga ophunzila. Nthawi zambili zimadalila thandizo la mpingo wonse kuti munthu abwele m’coonadi.” A m’banja, mabwenzi, na aziphunzitsi a kusukulu onse amacita mbali yawo pothandiza mwana kuti akule bwino. Amacita zimenezi mwa kulimbikitsa mwanayo na kum’phunzitsa zinthu zofunika. Mofananamo, ofalitsa angapeleke malangizo, cilimbikitso, na kukhala zitsanzo zabwino kwa maphunzilo a Baibo powathandiza kupita patsogolo kuti akabatizike. (Miy. 15:22) N’cifukwa ciani wofalitsa amene amatsogoza phunzilo la Baibo ayenela kuvomela thandizo limene ofalitsa ena angapeleke kwa wophunzila wake? Cifukwa ambili angathandizile kuti wophunzila apite patsogolo mwauzimu. w21.03 8 ¶1-3
Sondo, December 18
Tikanena kuti: “Tilibe ucimo,” ndiye kuti tikudzinamiza.—1 Yoh. 1:8.
Akhristu tonse, kaya ndife acinyamata kapena acikulile, tifunika kuyesetsa kupewa kukhala na umoyo wapaŵili. Mtumwi Yohane anaonetsa kuti n’zosatheka kuyenda m’coonadi, pa nthawi imodzi-modziyo n’kumacita makhalidwe oipa. (1 Yoh. 1:6) Ngati tifuna kuti Yehova azikondwela nafe, nthawi zonse tiyenela kucita zinthu monga kuti aliyense akutiona. Ndipo kukamba zoona, kulibe chimo lobisika, cifukwa Yehova amaona zonse zimene timacita. (Aheb. 4:13) Tiyenela kupewa kuona chimo mmene anthu a m’dzikoli amalionela. M’nthawi ya Yohane, anthu ampatuko anali kukamba kuti n’zotheka munthu kukhalabe pa ubale na Mulungu olo kuti amacita chimo mwadala. Masiku ano, anthu m’dzikoli alinso na maganizo aconco. Ambili amakamba kuti amakhulupilila Mulungu. Koma saona chimo mmene Yehova amalionela, maka-maka pa nkhani ya kugonana. Zimene Yehova amaziona kuti ni chimo, iwo amati ni cosankha ca munthu kapena ni ufulu wake. w20.07 22 ¶7-8
Mande, December 19
[Tizikondana] ndi mawu . . . ndi . . . m’zocita zathu.—1 Yoh. 3:18.
Kodi mumawakambilako alongo anu auzimu pakakhala pofunikila? Mwacitsanzo, ganizilani cocitika ici congoyelekezela. Tinene kuti ofalitsa ena amaona kuti mlongo wina amene mwamuna wake si Mboni, amakonda kufika mocedwa pamisonkhano, ndiponso amacoka mwamsanga misonkhano ikatha. Komanso amaona kuti nthawi zambili satenga ana ake pobwela ku misonkhano. Conco, iwo akumunena kuti sayesetsa kupempha mwamuna wake kuti azimulola kutenga ana pobwela ku misonkhano. Koma zoona zake n’zakuti mlongoyo akucita zonse zimene angathe. Iye alibe ufulu wokwanila wosankha nthawi yocita zinthu. Ndiponso alibe mphamvu yolamula zimene ana afunika kucita. Mungacite bwino kumuyamikila mlongoyo na kufotokozela ofalitsa enawo zimene iye amacita bwino. Mukatelo, mungathandize kuti ofalitsa enawo aleke kumukambila zoipa. Akulu amadziŵa kuti Yehova amafuna kuti alongo azisamalidwa bwino. (Yak. 1:27) Conco, amacita zinthu mokoma mtima monga Yesu, ndipo saika malamulo pamene sipafunikila malamulo. (Mat. 15:22-28) Ngati akulu ayesetsa kuthandiza alongo, alongowo amaona kuti Yehova na gulu lake amawakonda. w20.09 24-25 ¶17-19
Ciŵili, December 20
[Mulungu] wakudziŵitsani, inu Mfumu Nebukadinezara, zimene zidzacitike.—Dan. 2:28.
Kwa moyo wake wonse, mneneli Danieli anali wodzicepetsa ndipo nthawi zonse anali kupempha Yehova kuti amutsogolele. Mwacitsanzo, pamene Yehova anamuseŵezetsa pomasulila maloto a Nebukadinezara, Danieli sanadzitame kuti anakwanitsa kucita zimenezo mwa nzelu zake. M’malomwake, anapeleka ulemelelo wonse kwa Yehova. (Dan. 2:26-28) Kodi tiphunzilapo ciani pamenepa? Ngati abale amatiyamikila cifukwa ca mmene timakambila nkhani kapena ngati zinthu zimatiyendela bwino mu ulaliki, tifunika kupeleka ulemelelo wonse kwa Yehova. Tifunika kuzindikila kuti popanda thandizo lake sitingakwanitse kucita zimenezi. (Afil. 4:13) Tikatelo, ndiye kuti tikutengela citsanzo cabwino ca Yesu. Yesu anali kudalila Yehova. (Yoh. 5:19, 30) Iye sanayese kulanda ulamulilo Atate wake wakumwamba. Afilipi 2:6 imakamba za Yesu kuti: “Kukhala wolingana ndi Mulungu sanakuganizilepo ngati cinthu coti angalande.” Pokhala mwana wogonjela, Yesu anali kudziŵa kuti panali zinthu zina zimene sakanakwanitsa kucita, ndipo anali kulemekeza ulamulilo wa Atate wake. w20.08 11 ¶12-13
Citatu, December 21
Thamangani m’njila yoti mukalandile mphotoyo.—1 Akor. 9:24.
Pali vuto lina limene anthu ena othamanga pa njila yopita ku moyo amakumana nalo. Amalimbana na zovuta zimene anthu ena sangazione kapena kuzimvetsetsa. Ngati muona kuti anthu ena samvetsetsa vuto limene muli nalo, mungalimbikitsidwe na citsanzo ca Mefiboseti. (2 Sam. 4:4) Iye anali wolemala, ndiponso Mfumu Davide anamukayikila moti anamucitila zinthu mopanda cilungamo. Ngakhale n’conco, iye sanakhumudwe na zimenezi. Koma anayamikila zabwino zimene zinamucitikila pa umoyo. Anayamikilanso zabwino zimene Davide anamucitila kumbuyoko. (2 Sam. 9:6-10) Conco, pamene Davide anamuweluza mopanda cilungamo, Mefiboseti sanasumike maganizo ake pa zinthu zopanda cilungamo zimenezo. Sanalole zinthu zimenezo kum’khumudwitsa. Komanso sanaimbe mlandu Yehova cifukwa ca zimene Davide anacita. Koma anaganizila kwambili zimene akanacita pocilikiza Davide, mfumu yoikidwa na Yehova. (2 Sam. 16:1-4; 19:24-30) Yehova anaonetsetsa kuti citsanzo cabwino ca Mefiboseti calembedwa m’Baibo kuti ife tiphunzilepo kanthu.—Aroma 15:4. w20.04 26 ¶3; 30 ¶18-19
Cinayi, December 22
Ndife anchito anzake a Mulungu.—1 Akor. 3:9.
Ena mu mpingo angaikidwe kukhala amishonale, apainiya apadela, kapena apainiya a nthawi zonse. Abale na alongo ambili atenga kulalikila na kupanga ophunzila kukhala nchito yawo. Ngakhale kuti alengezi a nthawi zonse amenewa amakhala na zocepa kuthupi, iwo alandila madalitso ambili ocokela kwa Yehova mu umoyo wawo. (Maliko 10:29, 30) Timawakonda kwambili abale na alongo amenewa, ndipo ndife okondwa kuti ni ziwalo za mpingo! Kodi abale apaudindo na atumiki a nthawi zonse, ndiwo okha ali na malo mu mpingo? Kutali-tali! Wofalitsa uthenga wabwino aliyense ni wofunika kwa Mulungu komanso ku mpingo. (Aroma 10:15; 1 Akor. 3:6-8) Ndipo cimodzi mwa zolinga zazikulu za mpingo ni kupanga ophunzila a Ambuye wathu Yesu Khristu. (Mat. 28:19, 20; 1 Tim. 2:4) Ofalitsa onse mu mpingo, obatizika na osabatizika, amaika patsogolo nchitoyi mu umoyo wawo.—Mat. 24:14. w20.08 21 ¶7-8
Cisanu, December 23
Ndipo dziŵani kuti ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse mpaka m’nyengo ya mapeto a nthawi ino.—Mat. 28:20.
Monga mmene lemba la tsiku la lelo lionetsela, tikakumana na mavuto Yesu adzaticilikiza. Mawu a Yesu amenewa amatilimbikitsa kwambili. Tikutelo cifukwa ciani? Cifukwa masiku ena amakhala ovuta kucita nawo. Mwacitsanzo, tikataikilidwa wokondedwa wathu, timakhala acisoni osati kwa masiku ocepa ayi, koma mwina kwa zaka zambili. Ndipo cimatiŵaŵa kwambili. Ena amalimbana na masiku ovuta a ukalamba. Ndipo palinso ena amene amakhala okhwethemuka masiku ena cifukwa ca kupsinjika maganizo. Ngakhale n’telo, timapeza mphamvu zokwanitsa kupilila cifukwa tidziŵa kuti Yesu ali nafe “masiku onse,” ngakhale zinthu zitavuta bwanji pa umoyo wathu. (Mat. 11:28-30) Mawu a Mulungu amatitsimikizila kuti Yehova adzatithandiza kupitila mwa angelo ake. (Aheb. 1:7, 14) Mwacitsanzo, angelo amaticilikiza na kutitsogolela tikamalalikila ‘uthenga wabwino wa Ufumu,’ kwa anthu “kudziko lililonse, fuko lililonse, [komanso] cinenelo ciliconse.”—Mat. 24:13, 14; Chiv. 14:6. w20.11 13-14 ¶6-7
Ciŵelu, December 24
Maganizo a mumtima mwa munthu ali ngati madzi akuya, koma munthu wozindikila ndi amene amawatunga.—Miy. 20:5.
Timafuna kuti ophunzila athu azimvetsa mfundo yakuti zimene akuphunzilazo n’zocokela m’Mawu a Mulungu ouzilidwa. (1 Ates. 2:13) Tingacite bwanji zimenezo? Limbikitsani wophunzila wanu kuti azifotokozapo pa zimene akuphunzila. M’malo mofotokozela wophunzila wanu mfundo za coonadi nthawi zonse, m’pempheni kuti akufokozelenkoni zina mwa izo. Thandizani wophunzila wanu kuona mmene angaseŵenzetsele mfundo za m’Mawu a Mulungu. M’funseni mafunso otsogolela ku yankho, komanso mafunso ofuna kudziŵa maganizo ake pa malemba amene akuŵelenga. (Luka 10:25-28) Mwacitsanzo, mungam’funse kuti: “Kodi lembali lakuthandizani kuona khalidwe liti la Yehova?” “Kodi mfundo iyi ya m’Baibo ingakuthandizeni bwanji?” “Kodi mungatipo bwanji pa zimene taphunzilazi?” Cofunika kwambili, si kuculuka kwa zimene munthu waphunzila, koma kuzikonda na kuzigwilitsila nchito. Lolelani Baibo kuphunzitsa lokha. Kuti munole luso lanu la kuphunzitsa, mufunika kukhala wodzicepetsa. w20.10 15 ¶5-6
Sondo, December 25
Bzala mbewu zako m’mawa, ndipo dzanja lako lisapume mpaka madzulo.—Mlal. 11:6.
Sitikayika konse kuti nchito yolalikila idzatha panthawi yake. Ganizilani zimene zinacitika m’nthawi ya Nowa. M’nthawiyo, Yehova anaonetsa kuti nthawi zonse iye amasunga nthawi. Kukali zaka 120, iye anaikilatu nthawi yobweletsa Cigumula. Patapita zaka zambili, Yehova anauza Nowa kuti amange cingalawa. Mwina kwa zaka 40 kapena 50 Cigumula cisanayambe, Nowa anapitilizabe kugwila nchitoyo mwakhama. Ngakhale kuti anthu sanali kulabadila uthenga wake, Nowa anapitiliza kulalikila uthenga wocenjeza anthu mpaka pamene Yehova anamuuza kuti nthawi yafika yakuti aloŵetse vinyama m’cingalawa. Ndiyeno, nthawi itakwana, “Yehova anatseka citseko.” (Gen. 6:3; 7:1, 2, 16) Posacedwa, Yehova adzatiuza kuti nchito yolalikila yatha. Kenako adzawononga dziko la Satanali, na kubweletsa dziko latsopano limene mudzakhala cilungamo. Conco pamene tikuyembekezela nthawiyo, tiyeni titengele citsanzo ca Nowa na ena amene sanalole dzanja lawo kupuma. Tiyeni tipitilize kuika maganizo athu pa nchito yolalikila, kukhala oleza mtima, komanso kukhulupilila kwambili Yehova na malonjezo ake. w20.09 13 ¶18-19
Mande, December 26
Zinthu zonse zizicitika moyenela ndi mwadongosolo.—1 Akor. 14:40.
Popanda dongosolo la umutu, m’banja la Yehova mukanakhala msokonezo komanso mopanda cimwemwe. Mwacitsanzo, palibe akanadziŵa kuti pothela pake ndani ayenela kupanga zigamulo, komanso amene ayenela kukhala patsogolo polabadila zigamulo zimenezo. Koma ngati makonzedwe a Mulungu a umutu ni abwino motelo, nanga n’cifukwa ciani akazi ambili masiku ano amaona kuti amuna awo amawapondeleza? Cifukwa amuna ambili amanyalanyaza miyezo ya Yehova yokhudza banja, ndipo amasankha kutsatila cikhalidwe kapena miyambo yawo. Nthawi zina amacitila nkhanza akazi awo cifukwa ca dyela longofuna kukhutulitsa zimene mtima wawo ufuna. Mwacitsanzo, mwamuna angapondeleze mkazi wake pofuna kuti azimulemekeza kwambili kapena kuonetsa anthu kuti iye ni “mwamuna weni-weni.” Iye angaganize kuti sangakakamize mkazi wake kuti azimukonda, koma angacite zinthu zomupangitsa kuti azimuwopa. Angaganize kuti mkaziyo akakhala na mantha adzakwanitsa kumulamulila. N’zoonekelatu kuti kaganizidwe kameneka, komanso kucita zinthu mwanjila imeneyi kumalanda akazi ulemu umene ayenela kupatsidwa. Ndipo izi n’zosiyana kwambili na zimene Yehova amafuna.—Aef. 5:25, 28. w21.02 3 ¶6-7
Ciŵili, December 27
[Mutulileni] nkhawa zanu zonse, pakuti amakudelani nkhawa.—1 Pet. 5:7.
Akhristu amene ali na nkhawa angapeze thandizo mwa kupemphela kwa Yehova mocokela pansi pamtima. Yehova poyankha mapemphelo anu, adzakupatsani ‘mtendele wake umene umaposa kuganiza mozama kulikonse’ kwa anthu. (Afil. 4:6, 7) Yehova amatithandiza kucepetsa nkhawa tikakumana na mavuto, kupitila mwa mzimu wake woyela wamphamvu. (Agal. 5:22) Pamene mukamba na Yehova m’pemphelo, muuzeni nkhawa zanu zonse. Chulani zinthu mwacindunji. Muuzeni vuto lanu, ndipo m’fotokozeleni mmene mukumvelela. Ngati n’zotheka kuthetsa vutolo, m’pempheni kuti akupatseni nzelu zokuthandizani kudziŵa zimene mungacite na kuti akupatseni mphamvu zocitila zimenezo. Ngati palibe zimene mungacite pothetsa vutolo, pemphani Yehova kuti akuthandizeni kusadela nkhawa kwambili za vutolo. Ngati muchula mwacindunji mavuto anu m’pemphelo, n’kupita kwa nthawi mudzaona mosavuta mmene Yehova akuyankhila mapemphelo amenewo. Ngati mwakhala mukupemphela ndipo pemphelo lanu silinayankhidwe mwamsanga, musagwe mphwayi. Kuwonjezela pa kuchula zinthu mwacindunji m’pemphelo, Yehova amafunanso kuti muzipemphela mosalekeza.—Luka 11:8-10. w21.01 3 ¶6-7
Citatu, December 28
[Yesu] anawauza kuti: “Si onse amene angathe kucita zimenezi, koma okhawo amene ali ndi mphatso.”—Mat. 19:11.
Mpingo umakhala na mabanja amene ali na ŵana komanso amene alibe ŵana. Komanso muli abale na alongo amene sali pabanja. Kodi iwo tiyenela kuŵaona motani? Onani mmene Yesu anali kuonela umbeta. Pa utumiki wake padziko lapansi, Yesu sanakwatilepo. Anakhala wosakwatila cakuti anaseŵenzetsa nthawi yake na mphamvu zake pocita utumiki wake. Yesu sanakhazikitse lamulo lakuti munthu afunika kukhala pabanja kapena kukhala mbeta. Komabe, iye anakamba kuti Akhristu ena angasankhe kukhala mbeta. (Onani mfundo younikila pa Mateyu 19:12.) Yesu anali kulemekeza anthu amene sanali pabanja. Sanaone kuti anthuwo ni otsikilapo kapena osoŵekela mbali ina yake mu umoyo wawo. Mofanana ndi Yesu, mtumwi Paulo anacita utumiki wake ali mbeta. Paulo sanaphunzitsepo kuti Mkhristu akakwatila ndiye kuti walakwa. Iye anadziŵa kuti imeneyi ni nkhani yaumwini. w20.08 28 ¶7-8
Cinayi, December 29
Mulungu ndiye cikondi. —1 Yoh. 4:16.
Mtumwi Yohane anakhala moyo wautali komanso wokhala na zocitika zambili zokondweletsa. Iye anakumana na mavuto ambili amene akanafooketsa cikhulupililo cake. Koma nthawi zonse anali kuyesetsa kusunga malamulo a Yesu, kuphatikizapo lamulo la kukonda abale na alongo ake. Cotulukapo cake n’cakuti, Yohane anali wotsimikiza kuti Yehova na Yesu anali kum’konda, na kuti adzam’patsa mphamvu zom’thandiza kupilila vuto lililonse. (Yoh. 14:15-17; 15:10) Palibe ciliconse cimene Satana na dongosolo lake anacita, cimene cinalepheletsa Yohane kuonetsa cikondi kwa abale na alongo ake mwa zokamba na zocita zake. Mofanana na Yohane, tikukhala m’dziko lolamulidwa na Satana, amene ni Mulungu wa dongosolo lino wopanda cikondi. (1 Yoh. 3:1, 10) Ngakhale kuti iye amafuna kuti tileke kukonda abale na alongo athu, sangatilepheletse kucita zimenezo kokha ngati tamulola ndife. Tiyeni titsimikize mtima kukonda abale na alongo athu mwa kuwaonetsa cikondico mwa zokamba na zocita zathu. Ndipo tikatelo, tidzakondwela kukhala m’banja la Yehova na kukhala na umoyo wopindulitsa kwambili.—1 Yoh. 4:7. w21.01 13 ¶18-19
Cisanu, December 30
Mulungu . . . amatipatsa mphamvu kuti tithe kupilila.—Aroma 15:5.
Umoyo m’dziko lolamulidwa na Satanali, ungakhale wovuta kucita nawo ndipo nthawi zina tingasoŵe cocita. (2 Tim. 3:1) Koma tisade nkhawa kapena kucita mantha. Yehova adziŵa mavuto amene tipitamo. Tikagwa, iye analonjeza kuti adzatigwila mwamphamvu na dzanja lake lamanja. (Yes. 41:10, 13) Tili na cidalilo conse cakuti adzaticilikiza, tingapeze mphamvu m’Malemba na kupilila vuto lililonse limene tingakumane nalo. Mavidiyo athu na maseŵelo ongomvetsela komanso nkhani zakuti, “Tsanzilani Cikhulupililo Cawo,” zimathandiza kumvetsetsa zocitika za m’Baibo. Musanayambe kutamba, kumvetsela, kapena kuŵelenga nkhani zofufuzidwa bwino zimenezi, pemphani Yehova kuti akuthandizeni kupeza mfundo zimene mungaseŵenzetse. Yelekezani kuti munthu amene mukuŵelenga m’nkhaniyo ndinu. Sinkha-sinkhani zimene atumiki a Yehova amenewo anacita, na kuona mmene iye anawathandizila kugonjetsa mavuto amenewa. Ndiyeno seŵenzetsani zimene mwaphunzilazo pocita na vuto limene mwakumana nalo. Yamikilani Yehova pa thandizo limene wapeleka kale. Ndipo onetsani kuti mwayamikila thandizo limenelo mwa kupeza mipata yolimbikitsila ena na kuwacilikiza. w21.03 19 ¶22-23
Ciŵelu, December 31
Ana ndi colowa cocokela kwa Yehova.—Sal. 127:3.
Ngati ndimwe okwatilana, ndipo mufuna kukhala ndi ana, dzifunseni kuti: ‘Kodi ndife odzicepetsa, komanso okonda zinthu zauzimu cakuti Yehova angatisankhe kusamalila mwana wakhanda?’ (Sal. 127:4) Ngati ndimwe kholo, dzifunseni kuti: ‘Kodi nimaphunzitsa ana anga za kufunika kolimbikila nchito?’ (Mlal. 3:12, 13) ‘Kodi nimayesetsa kuteteza ana anga ku zinthu zoipa?’ (Miy. 22:3) Simungathe kuchingiliza ana anu ku mavuto onse. Koma mungawakonzekeletse mmene angacitile nawo mavuto pa umoyo, mwa kupitilizabe kuwaphunzitsa mwacikondi kudalila Mawu a Mulungu. (Miy. 2:1-6) Mwacitsanzo, ngati wacibululu wanu waleka kutumikila Yehova, thandizani ana anu kucokela m’Mawu a Mulungu, kuona kufunika kokhalabe okhulupilika kwa Yehova. (Sal. 31:23) Kapena ngati munthu amene mumam’konda wamwalila, onetsani ana anu mmene angaseŵenzetsele Mawu a Mulungu kuti apeze citonthozo na mtendele wa maganizo.—2 Akor. 1:3, 4; 2 Tim. 3:16. w20.10 27 ¶7