LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • es23 masa. 37-46
  • April

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • April
  • Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2023
  • Tumitu
  • Ciŵelu, April 1
  • Sondo, April 2
  • Mande, April 3
  • TSIKU LA CIKUMBUTSO
    Dzuŵa Likaloŵa
    Ciŵili, April 4
  • Citatu, April 5
  • Cinayi, April 6
  • Cisanu, April 7
  • Ciŵelu, April 8
  • Sondo, April 9
  • Mande, April 10
  • Ciŵili, April 11
  • Citatu, April 12
  • Cinayi, April 13
  • Cisanu, April 14
  • Ciŵelu, April 15
  • Sondo, April 16
  • Mande, April 17
  • Ciŵili, April 18
  • Citatu, April 19
  • Cinayi, April 20
  • Cisanu, April 21
  • Ciŵelu, April 22
  • Sondo, April 23
  • Mande, April 24
  • Ciŵili, April 25
  • Citatu, April 26
  • Cinayi, April 27
  • Cisanu, April 28
  • Ciŵelu, April 29
  • Sondo, April 30
Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2023
es23 masa. 37-46

April

Ciŵelu, April 1

Pakuti Mulungu anakonda kwambili dziko mwakuti anapeleka Mwana wake wobadwa yekha.—Yoh. 3:16.

Yesu anaonetsa kuti amatikonda kwambili mwa kupeleka moyo wake kaamba ka ife. (Yoh. 15:13) Palibe cimene tingabwezele Yehova na Yesu pa cikondi cimene iwo anationetsa. Koma tingaonetse kuyamikila mwa zimene timacita pa umoyo wathu. (Akol. 3:15) Odzozedwa amayamikila kwambili dipo, cifukwa inapangitsa kuti zikhale zotheka kukhala na ciyembekezo cakumwamba. (Mat. 20:28) Cifukwa cokhulupilila nsembe ya Khristu, Yehova amawacha olungama, ndipo waatenga kukhala ana ake. (Aroma 5:1; 8:15-17, 23) Naonso a nkhosa zina amayamikila dipo. Pa maziko a cikhulupililo cawo m’magazi amene Khristu anakhetsa, iwo ali na kaimidwe kabwino pamaso pa Mulungu, ndipo ali na ciyembekezo ‘codzatuluka m’cisautso cacikulu.’ (Chiv. 7:13-15) Magulu aŵili amenewa amaonetsela kuti amayamikila dipo, mwa kupezeka pa Cikumbutso caka ciliconse. w22.01 23 ¶14-15

Kuŵelenga Baibo kwa Cikumbutso: (Zocitika usana: Nisani 10) Mateyu 21:18, 19; 21:12, 13; Yohane 12:20-50

Sondo, April 2

Khristu anatigula.—Agal. 3:13.

Yesu anavutika maganizo kwambili na mlandu umene anam’patsa monga cifukwa comuphela. Anamusemela mlandu wabodza wakuti anali wonyoza Mulungu—munthu wosalemekeza Mulungu kapena dzina la Mulungu. (Mat. 26:64-66) Mlandu umenewu unam’vutitsa maganizo kwambili Yesu, cakuti anapempha Atate wake kuti zocititsa manyazi zimenezi zisam’citikile. (Mat. 26:38, 39, 42) Yesu anayenela kupacikidwa pamtengo kuti amasule Ayuda ku tembelelo. (Agal. 3:10) Iwo analonjeza kuti adzasunga Cilamulo ca Mulungu koma analephela kutalitali! Mwa ici, tembelelo limeneli linangowonjezela pa limene anali nalo kale monga ana ocimwa a Adamu. (Aroma 5:12) Cilamulo ca Mulungu cinakamba kuti munthu akacita chimo loyenela imfa ayenela kuphedwa. Pambuyo pake, mtembo wake ungapacikidwe pamtengo. (Deut. 21:22, 23; 27:26) Conco Yesu popacikidwa pa mtengo, anapangitsa kuti mtundu umene unam’kanawo upindule na nsembe yake. w21.04 16 ¶5-6

Kuŵelenga Baibo kwa Cikumbutso: (Zocitika usana: Nisani 11) Mateyu 21:33-41; 22:15-22; 23:1-12; 24:1-3

Mande, April 3

Ndikupeleka moyo wanga. —Yoh. 10:17.

Ganizilani zimene zinacitikila Yesu patsiku lothela la moyo wake padziko lapansi. Asilikali aciroma anamumenya mopanda cifundo. (Mat. 26:52-54; Yoh. 18:3; 19:1) Pom’kwapula, anaseŵenzetsa shamboko imene inali kunyotsola minofu pathupi pake. Kenako, anam’nyamulitsa cimtengo colema pamsana pake, apo magazi ali cu cu cu! Ndiyeno Yesu akuyamba kuguza cimtengoco kupita kumene anali kukamuphela. Posapita nthawi, asilikali aciroma analamula munthu wina kum’nyamulila mtengowo. (Mat. 27:32) Pamene Yesu anafika pamalo om’phelapo, asilikaliwo anam’khomelela misomali kumanja na kumapazi. Ndipo kulemela kwa thupi lake kunang’ambilako zilonda za misomali zija. Mabwenzi ake anagwidwa na cisoni cacikulu, ndipo amayi ake anali kungolila, pamene atsogoleli aciyuda anali kum’nyodola. (Luka 23:32-38; Yoh. 19:25) Ola lililonse linali losautsa kosaneneka. Mtima wake unapsinjika, m’cifuwa munathina, cakuti kupuma kunayamba kuvuta. Pamene anali kutsilizika, anapeleka pemphelo lothela lacipambano. Kenako anagwetsa mutu, na kupeleka moyo wake. (Maliko 15:37; Luka 23:46; Yoh. 10:18; 19:30) Kunena zoona, Yesu anafa imfa yoŵaŵa yapang’ono-pang’ono, ndiponso yonyazitsa! w21.04 16 ¶4

Kuŵelenga Baibo kwa Cikumbutso: (Zocitika usana: Nisani 12) Mateyu 26:1-5, 14-16; Luka 22:1-6

TSIKU LA CIKUMBUTSO
Dzuŵa Likaloŵa
Ciŵili, April 4

Muzicita zimenezi pondikumbukila.—Luka 22:19.

Yesu anawauza ophunzila ake 11 okhulupilika za mapangano aŵili—pangano latsopano komanso pangano la Ufumu. (Luka 22:20, 28-30) Mapangano amenewa anatsegula njila kuti atumwiwo komanso anthu ena oŵelengeka akakhale mafumu ndiponso ansembe kumwamba. (Chiv. 5:10; 14:1) Otsalila odzozedwa okha, amene ali m’mapangano aŵiliwa, ndiwo amadya mkate na kumwa vinyo pa Cikumbutso. Yehova waapatsa ciyembekezo cabwino ngako—moyo wosafa komanso wosawonongeka kumwamba. Iwo adzalamulila pamodzi na Yesu Khristu waulemelelo, komanso odzozedwa onse a 144,000. Ndipo koposa zonse, iwo adzaima pamaso pa Yehova Mulungu. (1 Akor. 15:51-53; 1 Yoh. 3:2) Odzozedwa amadziŵa kuti ayenela kukhalabe okhulupilika mpaka imfa.—2 Tim. 4:7, 8. w22.01 21 ¶4-5

Kuŵelenga Baibo kwa Cikumbutso: (Zocitika usana: Nisani 13) Mateyu 26:17-19; Luka 22:7-13 (Zocitika dzuŵa litaloŵa: Nisani 14) Mateyu 26:20-56

Citatu, April 5

Iwe udzakhala ndi ine m’Paradaiso.—Luka 23:43.

Apandu aŵili anapacikidwa pamodzi na Yesu. (Luka 23:40, 41) Mmodzi wa apanduwo anatembenukila kwa Yesu n’kumuuza kuti: “Yesu, mukandikumbukile mukakaloŵa mu Ufumu wanu.” (Luka 23:42) Podziŵa kuti Atate wake ni wacifundo, Yesu anakamba mawu opatsa ciyembekezo mpanduyo amene anali pafupi kufa. (Sal. 103:8; Aheb. 1:3) Yehova ni wokonzeka kutikhululukila na kutionetsa cifundo ngati tilapadi pa zoipa zimene tinacita, ndiponso ngati tikhulupilila kuti tingakhululukidwe macimo athu cifukwa ca magazi okhetsedwa a Yesu Khristu. (1 Yoh. 1:7) Kwa ena, cimakhala covuta kukhulupilila kuti Yehova anawakhululukiladi. Ngati umu ni mmene mumamvelela nthawi zina, ganizilani izi: Yesu ali pafupi kufa, anakamba mawu oonetsa cifundo kwa mpandu uja amene anali atangoyamba kumene kuonetsa cikhulupililo mwa iye. Nanga kuli bwanji Yehova kwa olambila ake okhulupilika!—Sal. 51:1; 1 Yoh. 2:1, 2. w21.04 9 ¶5-6

Kuŵelenga Baibo kwa Cikumbutso: (Zocitika usana: Nisani 14) Mateyu 27:1, 2, 27-37

Cinayi, April 6

Yesu anati: “Ndakwanilitsa cifunilo canu!”—Yoh. 19:30.

Mwa kusungabe umphumphu wake mpaka imfa, Yesu anakwanilitsa zinthu zambili. Coyamba, anaonetsa kuti Satana ni wabodza. Yesu anaonetsa kuti munthu wangwilo angakwanitse kusunga umphumphu wake mwangwilo mosasamala kanthu zonse zimene Satana angacite. Caciŵili, Yesu anapeleka moyo wake monga dipo. Cifukwa cakuti anapeleka moyo wake monga nsembe, zinatheka anthu opanda ungwilo kukhala pa ubale na Mulungu, na kuwapatsa ciyembekezo cokakhala na moyo kwamuyaya. Cacitatu, Yesu anaonetsa kuti Yehova ni wolamulila wolungama, ndipo anacotsa citonzo pa dzina la Atate wake. Tiziona tsiku lililonse kukhala monga lothela pa kusunga umphumphu wathu. Tikatelo, olo tiyang’anizane na imfa, tidzatha kukamba kuti, “Yehova, nacita zonse zimene nikanatha posunga umphumphu wanga, kuonetsa kuti Satana ni wabodza komanso nacotsa citonzo pa dzina lanu na kuonetsa kuti inu ndinu woyenela kulamulila!” w21.04 12 ¶13-14

Kuŵelenga Baibo kwa Cikumbutso: (Zocitika usana: Nisani 15) Mateyu 27:62-66 (Zocitika dzuŵa litaloŵa: Nisani 16) Mateyu 28:2-4

Cisanu, April 7

Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, amene ndikukondwela naye, muzimumvela.—Mat. 17:5.

Yesu atanamilizilidwa na kuweluzidwa pa mlandu womusemela, akunyodoledwa, kuzunzidwa mwankhanza, na kukhomeleledwa pamtengo wozunzikilapo. Pamene akumukhomelela, misomali ikuloŵa m’manja mwake na m’mapazi ake. Kupuma kulikonse n’kopweteka, kukamba mawu alionse n’koŵaŵa. Koma afunika alankhulebe, cifukwa ali na mawu ofunika kwambili. Kukamba zoona, tingatengepo maphunzilo ofunika kwambili pa mawu othela a Yesu. Tiphunzilapo kuti tiyenela kukhululukila ena na kukhulupilila kuti Yehova adzatikhululukila. Tili na mwayi kukhala na banja labwino lauzimu la abale na alongo amene ni okonzeka kutithandiza. Koma tikafunikila thandizo, tiyenela kuwapempha kuti atithandize. Tidziŵa kuti Yehova adzatithandiza kupilila ciyeso ciliconse cimene tingakumane naco. Ndipo taona kufunika koona tsiku lililonse monga tsiku lothela loonetsela kuti tasunga umphumphu wathu tili na cidalilo conse kuti moyo wathu ni wotetezeka m’manja mwa Yehova. w21.04 8 ¶1; 13 ¶17

Kuŵelenga Baibo kwa Cikumbutso: (Zocitika usana: Nisani 16) Mateyu 28:1, 5-15

Ciŵelu, April 8

Pakuti moyo wosatha adzaupeza akamaphunzila ndi kudziŵa za inu, Mulungu yekhayo amene ali woona, ndi za Yesu Khristu, amene inu munamutuma. —Yoh. 17:3.

Kutsatila mapazi a Yesu kumatsogolela ku moyo wosatha. Pamene mnyamata wina wacuma anafunsa Yesu zimene anafunika kucita kuti akapeze moyo wamuyaya, Yesu anamuyankha kuti: ‘Bwela ukhale wotsatila wanga.’ (Mat. 19:16-21) Kwa Ayuda ena amene sanakhulupilile kuti iye ni Khristu, Yesu anati: “Nkhosa zanga . . . zimanditsatila. Ndidzazipatsa moyo wosatha.” (Yoh. 10:24-29) Timaonetsa cikhulupililo cathu mwa Yesu, mwa kucita zimene iye anaphunzitsa kupitila m’mawu na zocita zake. Ngati ticita zimenezo, tidzapitilizabe kuyenda panjila ya kumoyo wosatha. (Mat. 7:14) Tisanayambe kutsatila mapazi a Yesu mosamala, tifunika kumudziŵa. “Kudziŵa” Yesu si cocitika ca kamodzi cabe ayi, kumafuna kupitiliza. Tifunika kupitiliza kum’dziŵa bwino—kuphunzila makhalidwe ake, kaganizidwe kake, komanso mfundo zake. Kaya takhala m’coonadi kwa nthawi yaitali bwanji, tiyenela kupitilizabe “kudziŵa” Yehova na Mwana wake. w21.04 4 ¶9-10

Sondo, April 9

Kale ndinali wonyoza Mulungu, [komanso] wozunza anthu ake.—1 Tim. 1:13.

N’kutheka kuti nthawi zina mtumwi Paulo anali kudziimba mlandu cifukwa ca zolakwa zimene anacita kumbuyoko. Ndipo n’zosadabwitsa kuti iye anakamba kuti anali munthu “wocimwa kwambili.” (1 Tim. 1:15) Akalibe kuphunzila coonadi, Paulo anali kuzunza Akhristu mu mzinda na mzinda, ndipo ena anali kuwaponya m’ndende na kuvomeleza kuti aphedwe. (Mac. 26:10, 11) Ganizilani cabe mmene Paulo akanamvelela kukumana na Mkhristu wacinyamata amene makolo ake anaphedwa cifukwa cakuti iye anavomeleza kuti iwo aphedwe. Paulo anadziimba mlandu pa zolakwa zake, koma anadziŵa kuti sakanatha kusintha zakumbuyo. Iye anavomeleza kuti Khristu anamufela, ndipo mwacidalilo analemba kuti: “Mwa kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu, ndili monga ndililimu.” (1 Akor. 15:3, 10) Kodi tiphunzilapo ciani? Vomelezani kuti Khristu anakufelani na kukukonzelani njila kuti mukhale pa ubwenzi wolimba na Yehova. (Mac. 3:19) Cofunika kwa Yehova ni zimene timacita palipano, komanso zimene tidzacita kutsogolo, osati zolakwa zimene tinacita kumbuyoku.—Yes. 1:18. w21.04 23 ¶11

Mande, April 10

Muziyesa mawu ouzilidwawo kuti muone ngati ali ocokeladi kwa Mulungu, cifukwa aneneli onyenga ambili aloŵa m’dziko.—1 Yoh. 4:1.

Ngakhale kuti Ayuda ambili m’nthawi ya Yesu sanali kuyembekezela kuti Mesiya adzafunika kufa, onani zimene zinaloseledwa m’Malemba: “Anakhuthula moyo wake mu imfa ndipo anaonedwa monga mmodzi wa ocimwa. Iye ananyamula chimo la anthu ambili ndipo analowelelapo kuti athandize olakwa.” (Yes. 53:12). Conco, Ayudawo analibe cifukwa cokanila Yesu pamene anaphedwa monga kuti anali wocimwa. Masiku ano, tingapewe kupunthwa mwa kuphunzila zoona zake. Pa ulaliki wake wa pa Phili, Yesu anacenjeza ophunzila ake kuti ena ‘adzakunamizilani zoipa zilizonse.’ (Mat. 5:11) Satana ndiye gwelo la mabodza amenewa. Iye amasonkhezela otsutsa kufalitsa mabodza okhudza anthu okonda coonadi. (Chiv. 12:9, 10) Tiyenela kukaniza mabodza amene anthu otitsutsa amakamba. Tisalole kuti mabodza otelo atiwopseze kapena kufooketsa cikhulupililo cathu. w21.05 11 ¶14; 12 ¶16

Ciŵili, April 11

Musacite mantha: ndinu ofunika kwambili kuposa mpheta zoculuka.—Mat. 10:31.

Thandizani wophunzila wanu kudalila Yehova. Yesu anatsimikizila ophunzila ake kuti Yehova adzawathandiza cifukwa amawakonda. (Mat. 10:19, 20, 29, 30) Mukumbutseni wophunzila wanu kuti iyenso Yehova adzam’thandiza. Mungam’thandize kudalila Yehova mwa kupemphela naye limodzi pa zolinga zake. M’bale Franciszek wa ku Poland ananena kuti: “Nthawi zambili mphunzitsi wanga anali kuchula zolinga zanga m’mapemphelo ake. Pamene n’nali kuona mmene Yehova anali kuyankhila mapemphelo ake, inenso mwamsanga n’nayamba kupemphela. N’tayamba nchito yatsopano n’naona thandizo la Yehova n’tapempha kuti masiku ena nisamagwile nchito kuti nizipita ku misonkhano ya mpingo komanso ku msonkhano wacigawo.” Yehova amasamala kwambili za maphunzilo athu a Baibo. Iye amawayamikila aphunzitsi acikhristu amene amagwila nchito molimbika pothandiza anthu kuyandikila kwa iye, ndipo amawakonda cifukwa ca kulimbika kwawo kumeneku. (Yes. 52:7) Ngati palipano simutsogoza phunzilo la Baibo, mungathandizebe maphunzilo a Baibo kupita patsogolo mpaka kukabatizika, mwa kumapita na ofalitsa ena ku maphunzilo awo. w21.06 7 ¶17-18

Citatu, April 12

Amakondwela ndi cilamulo ca Yehova, ndipo amaŵelenga ndi kusinkhasinkha cilamulo cake usana ndi usiku.—Sal. 1:2.

Tingaonetse kuti timayamikila mphatso ya Mawu a Mulungu mwa kuwaŵelenga nthawi zonse. Tizikhala na pulogilamu yocita phunzilo laumwini. Tisamangocita phunzilo laumwini pamene tapezela mpata. Tikamatsatila pulogilamu yathu yocita phunzilo laumwini, cikhulupililo cathu cidzapitiliza kukhala colimba. Mosiyana na “anthu anzelu ndi ozindikila” a m’dzikoli, ife tili na cikhulupililo colimba cozikidwa pa Mawu a Mulungu. (Mat. 11:25, 26) Cifukwa coŵelenga buku lopatulika limeneli, ife tidziŵa cifukwa cake zinthu zikuipilaipila padzikoli, komanso zimene Yehova adzacita posacedwa. Conco, tiyeni tiyesetse kulimbitsa cikhulupililo cathu, komanso kuthandiza anthu ambili kuti akhale na cikhulupililo mwa Mlengi wathu. (1 Tim. 2:3, 4) Ndipo tiyeni tipitilize kuyang’ana kutsogolo panthawi imene onse padziko lapansi adzatamanda Yehova mwa kukamba mawu apa Chivumbulutso 4:11 akuti: “Ndinu woyenela, inu Yehova Mulungu wathu wamphamvu, kulandila ulemelelo . . . cifukwa munalenga zinthu zonse.” w21.08 19 ¶18-20

Cinayi, April 13

Pokonda abale, khalani ndi cikondi ceniceni pakati panu. —Aroma 12:10.

Pokhala abusa, akulu ali na udindo wopeleka uphungu pakafunika kutelo. Ayenela kuyesetsa kupeleka uphungu wothandiza komanso wolimbikitsa, umene ‘umasangalatsa mtima.’ (Miy. 27:9) Akulu amakonda abale na alongo awo. Nthawi zina, amaonetsa cikondi cimeneco mwa kuwongolela munthu amene akuloŵela njila yolakwika. (Agal. 6:1) Mkulu asanapeleke uphungu, coyamba ayenela kuganizila zimene mtumwi Paulo anakamba zokhudza cikondi. Iye anati: “Cikondi n’coleza mtima ndiponso n’cokoma mtima. . . . Cimakwilila zinthu zonse, cimakhulupilila zinthu zonse, cimayembekezela zinthu zonse, cimapilila zinthu zonse.” (1 Akor. 13:4, 7) Kusinkhasinkha mfundo ya palembali, kudzathandiza mkulu kupenda colinga cake copelekela uphungu, ndipo adzatha kupeleka uphunguwo mwacikondi. Ngati wolandila uphungu aona kuti mkuluyo amam’dela nkhawa, iye angalandile uphunguwo mosavuta. w22.02 14 ¶3; 15 ¶5

Cisanu, April 14

Iwo anapanduka ndi kukhumudwitsa mzimu wake woyela. —Yes. 63:10.

Yehova analenga ana ake auzimu komanso aumunthu angwilo. Koma mngelo wopandukayo, Satana (kutanthauza “Wotsutsa”), anapangitsanso anthu angwilo, Adamu na Hava, kupandukila Yehova. Komanso angelo ena, kuphatikizapo anthu ena, nawonso anapanduka. (Yuda 6) Izi zinam’khumudwitsa kwambili Yehova. Ngakhale n’telo, iye anapilila ndipo adzapitilizabe kupilila mpaka pa nthawi imene adzawononga onse om’pandukila. Izi zidzabweletsa madalitso kwa atumiki ake okhulupilika, amene akupilila naye limodzi zinthu zoipa m’dongosolo lino la zinthu. Satana anati Yobu, komanso atumiki onse okhulupilika a Yehova amam’tumikila pa zifukwa zadyela. (Yobu 1:8-11; 2:3-5) Mpaka pano Mdyelekezi akali kukambabe zimenezi. (Chiv. 12:10) Tingaonetse kuti zonse zimene Satana amakamba n’zabodza, mwa kupilila mayeso athu na kukhalabe okhulupilika kwa Yehova cifukwa comukonda. w21.07 9 ¶7-8

Ciŵelu, April 15

Cotsani zocita zanu zoipa pamaso panga. Lekani kucita zoipa.—Yes. 1:16.

Mtumwi Paulo, anafotokoza citsanzo cogwila mtima cotithandiza kuona kufunika kopanga masinthidwe ofunikila pa umoyo wathu. Iye analemba kuti tiyenela kupacika umunthu wathu wakale “pamtengo.” (Aroma 6:6) M’mawu ena, tingati tiyenela kutengela citsanzo ca Khristu. Izi zitanthauza kuti tiyenela kupha maganizo osayenela na makhalidwe oipa amene Yehova amadana nawo. Tikatelo, m’pamene tidzakhala na cikumbumtima coyela, ndiponso ciyembekezo codzakhala na moyo kwamuyaya. (Yoh. 17:3; 1 Pet. 3:21) Yehova sadzasintha miyezo yake kuti igwilizane na khalidwe lathu. M’malo mwake, ndife tiyenela kusintha na kutsatila miyezo yake. (Yes. 1:17, 18; 55:9) Ngakhale pambuyo pa ubatizo, mudzafunika kupitiliza kukaniza zilakolako zoipa. Pemphani Yehova kuti akuthandizeni, ndipo dalilani mzimu wake osati mphamvu zanu. (Agal. 5:22; Afil. 4:6) Tiyenela kucita khama kuti tivule umunthu wakale na kusauvalanso. w22.03 6 ¶15-17

Sondo, April 16

[Yehova] adzakucilikiza. —Sal. 55:22.

Yehova anatilonjeza kuti adzatipatsa cakudya, zovala, komanso pogona, ngati tifuna-funa ufumu coyamba na kutsatila miyezo yake yolungama. (Mat. 6:33) Tikakhulupilila lonjezo limeneli, tidzapewa kuganiza kuti zinthu zakuthupi za m’dzikoli, n’zimene zingatibweletsele citetezo ceniceni na cimwemwe cosatha. Timadziŵa kuti tidzakhala na mtendele weniweni wa maganizo, kokha ngati ticita cifunilo ca Yehova. (Afil. 4:6, 7) Ngakhale tingakwanitse kugula zinthu zambili, tizionanso ngati nthawi tili nayo yozisamalila. Kodi n’kutheka kuti timakonda kwambili zinthu zimene tili nazo? Kumbukilani kuti Mulungu anatipatsa zocita m’banja lake. Mwa ici, tisamalole zinthu zina kutitangwanitsa. Sitifuna olo pang’ono kukhala monga munthu uja amene anataya mwayi wotumikila Yehova, komanso mwayi wotengedwa kukhala mmodzi wa ana ake, cabe cifukwa cokondetsetsa zinthu zocepa zakuthupi zimene anali nazo.—Maliko 10:17-22. w21.08 6 ¶17

Mande, April 17

[Yankhani] aliyense amene wakufunsani.—1 Pet. 3:15.

Mukamaŵelenga Baibo, mudzaona kuti makhalidwe amene Yehova ali nawo, ni amenenso amaonekela bwino m’zinthu zimene analenga. Makhalidwe ake amenewo amatithandiza kukhulupilila kuti iye alikodi. (Eks. 34:6, 7; Sal. 145:8, 9) Mukafika pom’dziŵa bwino Yehova, cikhulupililo canu mwa iye cidzalimba, cikondi canu pa iye cidzakulilako, komanso ubale wanu na iye udzalimbilako. Muziuzako ena za cikhulupililo canu mwa Mulungu. Koma kodi mungacite ciani ngati munthu amene mwam’lalikila, wakufunsani funso lokhudza kukhalapo kwa Mulungu, ndipo simudziŵa mmene mungamuyankhile? Yesani kupeza yankho la m’Malemba lofotokozedwa m’zofalitsa zathu, ndiyeno kambilanani naye yankholo. Mungapemphenso wofalitsa wa cidziŵitso cokulilapo kuti akuthandizeni. Kaya munthuyo avomeleze mayankho a m’Baibo kapena ayi, mudzakhala mutapindulabe na kufufuza kwanu. Ndipo cikhulupililo canu cidzalimbilako. w21.08 18 ¶14-15

Ciŵili, April 18

Sindinakubisileni ciliconse. —Mac. 20:20.

Sitiyenela kucita kudzimana zinthu zonse kuti tikondweletse Yehova. (Mlal. 5:19, 20) Komabe, ngati tizengeleza kucita zambili potumikila Mulungu cabe cifukwa cosafuna kudzimana zinthu zina, tingacite zinthu mofanana na munthu wa m’fanizo la Yesu amene anadziunjikila cuma cambili koma n’kunyalanyaza Mulungu. (Luka 12:16-21) Tikakumana na mavuto, mwapemphelo timayesetsa kuseŵenzetsa luso lathu la kuzindikila kuti tidziŵe mmene tingathanile nawo mavutowo. (Miy. 3:21) Yehova amatidalitsa m’njila zambili. Tingaonetse kuti timayamikila madalitso amenewa ngati ticita zonse zotheka kuti tim’tamande. (Aheb. 13:15) Izi ziphatikizapo kuwonjezela utumiki wathu, ndipo izi zingatibweletsela madalitso owonjezeleka. Tsiku lililonse, tiyeni tizifuna-funa njila kuti timulaŵe Yehova na kuona kuti ni wabwino. (Sal. 34:8) Tikatelo, tidzakhala ngati Yesu amene anati: “Cakudya canga ndico kucita cifunilo ca amene anandituma ndi kutsiliza nchito yake.”—Yoh. 4:34. w21.08 30-31 ¶16-19

Citatu, April 19

Kunyada kumafikitsa munthu ku ciwonongeko, ndipo mtima wodzikuza umacititsa munthu kupunthwa.—Miy. 16:18.

Satana amafuna kuti tikhale onyada. Iye amadziŵa kuti tikalola kunyada kutilamulila tidzakhala ngati iye, ndipo tidzataya mwayi wokhala na moyo wosatha. Conco, mtumwi Paulo anacenjeza kuti munthu “angakhale wotukumuka cifukwa ca kunyada, n’kulandila ciweluzo cofanana ndi cimene Mdyelekezi analandila.” (1 Tim. 3:6, 7) Izi zingacitikile aliyense wa ife, kaya ndife atsopano m’coonadi kapena tatumikila Yehova kwa zaka zambili. Anthu onyada amakhala odzikonda. Satana amafuna kuti tikhale odzikonda, tiziganizila kwambili za ife eni kuposa Yehova, makamaka tikakumana na vuto. Mwacitsanzo, kodi wina anakunamizilamponi? Kapena munacitilidwapo zinthu zopanda cilungamo? Satana amafuna kuti muziimba mlandu Yehova kapena abale anu. Ndipo zimenezi zikacitika, Mdyelekezi amafuna muziganiza kuti cinthu cokha cothandiza nikucita zinthu mmene inuyo mufunila, m’malo motsatila citsogozo ca Yehova cimene amapeleka m’Mawu ake.—Mlal. 7: 16, 20. w21.06 15 ¶4-5

Cinayi, April 20

“Limbani mtima anthu nonse a m’dzikoli ndipo gwilani nchito,” watelo Yehova. “Pakuti ine ndili ndi inu,” watelo Yehova wa makamu.—Hag. 2:4.

Yehova anapatsa mneneli Hagai nchito yofunika kwambili. Hagai ayenela kuti anali pagulu la Ayuda amene anabwelela ku Yerusalemu, atamasulidwa ku ukapolo ku Babulo mu 537 B.C.E. Atangofika kumeneko, alambili okhulupilika amenewo anayala maziko a nyumba ya Yehova, kapena kuti kacisi. (Ezara 3:8, 10) Koma pasanapite nthawi, panabuka vuto linalake. Iwo analefulidwa na kuleka kugwila nchitoyo cifukwa ca anthu owatsutsa. (Ezara 4:4; Hag. 1:1, 2) Conco, mu 520 B.C.E., Yehova anauza Hagai kuti akadzutsenso cangu ca Ayuda amenewo, na kuwalimbikitsa kuti amalize nchito yomanga kacisi. (Ezara 6:14, 15) Uthenga wa Hagai cinali kulimbitsa cikhulupililo ca Ayuda mwa Yehova. Mawu akuti “Yehova wa makamu,” ayenela kuti anawalimbikitsa kwambili. Yehova ali na ulamulilo pa makamu a angelo amphamvu. Conco, Ayuda anayenela kum’dalila kuti apambane. w21.09 15 ¶4-5

Cisanu, April 21

Mwakutelo, onse adzadziŵa kuti ndinu ophunzila anga, ngati mukukondana.—Yoh. 13:35.

Masiku ano, Mboni za Yehova padziko lonse zimakondana kwambili na kugwilizana. Mosiyana na zipembedzo zina, ubale wathu wacikondi suyang’ana dziko, mtundu, cikhalidwe, maphunzilo, na zina zotelo. Timaona umboni wa cikondi ceniceni pa misonkhano yathu ya mpingo, yadela, komanso yacigawo. Izi zimatithandiza kukhulupilila kwambili kuti timalambila Yehova m’njila imene iye amavomeleza. (Yoh. 13:34) Malemba amatilimbikitsa kuti ‘tizikondana kwambili.’ (1 Pet. 4:8) Ndipo timaonetsa kuti timakondana ngati tikhululukilana, na kulolelana pa zophophonya zathu. Timafunanso kukhala opatsa komanso oceleza kwa onse mu mpingo, ngakhale kwa aja amene anatilakwila. (Akol. 3:12-14) Cikondi coteloco ndiye cizindikilo cacikulu cotidziŵila kuti ndife Akhristu oona. w21.10 22 ¶13-14

Ciŵelu, April 22

Womukonda [mwana wake] ndi amene amamuyang’anila kuti amulangize.—Miy. 13:24.

Kodi kucotsa munthu wocimwa wosalapa kungam’thandize kusintha khalidwe lake? Inde. Ambili amene anacitapo macimo aakulu anakamba kuti anayeneladi kucotsedwa mu mpingo, cifukwa kunawagunduza kuti azindikile kulakwa kwawo. Kunawathandizanso kusintha khalidwe lawo, na kubwelelanso m’manja mwa Yehova. (Aheb. 12:5, 6) Ganizilani citsanzo ici. M’busa waona kuti nkhosa yake ina ni yodwala. Iye akudziŵa kuti, kuti athandize nkhosa yodwalayo kucila, ayenela kuicotsa pa zinzake. Monga timadziŵila, nkhosa zimayenda gulu, ndipo zimakhwinyilila ngati azipatula. M’busa akacotsa nkhosa yodwalayo pa zinzake, kodi zitanthauza kuti ni wankhanza kapena woipa mtima? Ayi. Iye amadziŵa kuti ngati angalekelele nkhosayo kukhala pamodzi na zinzake, nkhosa zinazo zingayambukilidwe. Koma akapatula nkhosa yodwalayo, amateteza gulu lonse la nkhosa. w21.10 10 ¶9-10

Sondo, April 23

Onetsani kuwala kwanu pamaso pa anthu, kuti aone nchito zanu zabwino ndi kuti alemekeze Atate wanu wakumwamba.—Mat. 5:16.

Ni mwayi wapadela kukhala m’banja lokondana la padziko lonse. Tifuna kuti anthu ambili agwilizane nafe pa kulambila Mulungu wathu. Pa cifukwa cimeneci, tiyenela kukhala osamala kuti tisabweletse citonzo pa anthu a Yehova, kapena kwa Atate wathu wakumwamba. Tiziyesetsa kukhala na khalidwe limene lingakope anthu kuti amvetsele uthenga wabwino. Nthawi zina, anthu ena angatitonze kapena kutizunza cabe cifukwa timamvela Atate wathu wakumwamba. Koma bwanji ngati timacita mantha kuuzako ena za cikhulupililo cathu? Tingakhale otsimikiza kuti Yehova na Mwana wake adzatithandiza. Yesu anauza ophunzila ake kuti sayenela kuda nkhawa na zimene adzakamba. Cifukwa ciani? Cifukwa Yesu anakamba kuti: “Mudzapatsidwa nthawi yomweyo zoti mulankhule, pakuti wolankhula simudzakhala inu panokha, koma mzimu wa Atate wanu udzalankhula kudzela mwa inu.”—Mat. 10:19, 20. w21.09 24 ¶17-18

Mande, April 24

Ndidzauza Yehova kuti: “Inu ndinu pothaŵilapo panga ndi malo anga acitetezo.”—Sal. 91:2.

Mose anaseŵenzetsa mawu ofanizila ofanana na amenewa. (Sal. 90:1) Kuwonjezela apo, kumapeto kwa moyo wake, Mose anakamba mfundo yolimbikitsa yakuti: “Mulungu wakale lomwe ndiwo malo ako obisalamo, ndipo iwe uli m’manja amene adzakhalapo mpaka kalekale.” (Deut. 33:27) Kodi mawu akuti “uli m’manja amene adzakhalapo mpaka kalekale,” atiuza ciani ponena za Yehova? Yehova akakhala Pothaŵilapo pathu, timamva kukhala otetezeka. Ngakhale n’telo, nthawi zina tingalefuke cakuti tingayambe kuona kuti sitilinso otetezeka. Pa nthawi zotelo, kodi Yehova adzacitanji kwa ife? (Sal. 136:23) Iye mwacikondi adzatinyamula na manja ake, na kutithandiza kuti tisakhalenso olefuka. (Sal. 28:9; 94:18) Kudziŵa kuti Mulungu adzaticilikiza, kumatithandiza kukumbukila kuti ndife odalitsika m’njila ziŵili izi: Yoyamba, tili na malo othaŵilapo acitetezo, mosasamala kanthu za kumene tikhala. Yaciŵili, Atate wathu wacikondi wakumwamba amasamala kwambili za ife. w21.11 6 ¶15-16

Ciŵili, April 25

Mayeselo osiyana-siyana . . . akukucititsani cisoni.—1 Pet. 1:6.

Yesu anadziŵa kuti zopanda cilungamo zidzayesa cikhulupililo ca ophunzila ake. Kuti awathandize kupilila, iye anawauza fanizo lopezeka m’buku la Luka. Yesu anasimba nkhani ya mkazi wamasiye amene sanaleke kupempha kuti woweluza wopanda cilungamo am’citile cilungamo. Mkaziyo anali na cidalilo cakuti akalimbikila kupempha, adzayankhidwa. Potsilizila pake, woweluza anamvetsela pempho lake. Kodi tiphunzilapo ciani? Yehova si wopanda cilungamo. Ndiye cifukwa cake Yesu anati: “Ndithu, ngakhale kuti Mulungu amalezela mtima osankhidwa ake, kodi sadzaonetsetsa kuti cilungamo cacitika kwa iwo, amene amafuulila kwa iye usana ndi usiku?” (Luka 18:1-8) Kenako, Yesu anakambanso kuti: “Mwana wa munthu akadzafika, kodi adzapezadi cikhulupililo [cotelo] padziko lapansi?” Tikacitilidwa zopanda cilungamo, tiyenela kuonetsa kuti tili na cikhulupililo colimba cofanana na ca mkazi wamasiye, mwa kukhala oleza mtima komanso kupilila. Cikhulupililo cotelo, cidzatithandiza kukhala na cidalilo cakuti posacedwa Yehova adzacitapo kanthu. Cina, tiyenela kukhulupilila mphamvu ya pemphelo. w21.11 23 ¶12; 24 ¶14

Citatu, April 26

Kodi wacinyamata angakhale bwanji woyela pa moyo wake? Mwa kudziyang’anila ndi kucita zinthu mogwilizana ndi mawu anu. —Sal. 119:9.

Imwe acicepele, kodi nthawi zina mumaona kuti miyezo ya Yehova ni yopanikiza kwambili? Satana amafuna kuti muziona conco. Iye amafuna kuti muziona kuti amene akuyenda pa msewu wotakasuka, ndiwo amasangalala na umoyo. Angaseŵenzetse zocita za anzanu ku sukulu, kapena zimene mumaona pa Intaneti, kuti akupangitseni kuona kuti mukumanidwa zabwino. Satana amafuna muziona kuti miyezo ya Yehova imakuphelani ufulu wosangalala na moyo. Koma kumbukilani kuti: Satana safuna kuti anthu amene akuyenda pa njila yake adziŵe kumene njilayo ikuwatsogolela. (Mat. 7:13, 14) Koma Yehova, wakuonetsani bwino-bwino zimene wasungila awo amene amayendabe pa njila yopita ku moyo.—Sal. 37:29; Yes. 35:5, 6; 65:21-23. w21.12 23 ¶6-7

Cinayi, April 27

[Khululukila] m’bale [wako] ndi mtima wonse.—Mat. 18:35.

Timadziŵa kuti tiyenela kukhululukila ena. Ndipo ndiye cinthu coyenela kucita. Koma tingamavutike kucita zimenezi. Nthawi zina mtumwi Petulo ayenela kuti anali kumvela mwa njila imeneyi. (Mat. 18:21, 22) Ndiye n’ciani cingatithandize? Coyamba, tiyenela kusinkha-sinkha za kuculuka kwa zimene Yehova watikhululukila. (Mat. 18:32, 33) Si ndife oyenela cikhululukilo cake, koma amatikhululukila na mtima wonse. (Sal. 103:8-10) Pa nthawi imodzimodzi “ifenso tiyenela kukondana.” Conco, kukhululuka si nkhani yocita kusankha kuti tikhululuke kapena ayi. Tiyenela kuwakhululukila abale na alongo athu. (1 Yoh. 4:11) Caciŵili, tiyenela kuganizila zotulukapo zabwino zimene zingakhalepo tikakhululuka. Tingathandize munthu amene watilakwila, kugwilizanitsa mpingo, kuteteza ubale wathu na Yehova, ndiponso kumva kukhala omasuka. (2 Akor. 2:7; Akol. 3:14) Cothela, tiyenela kupemphela kwa amene amafuna kuti tizikhululuka. Tisalole kuti Satana asokoneze mtendele umene tili nawo na alambili anzathu. (Aef. 4:26, 27) Timafunikila thandizo la Yehova kuti tipewe kugwela mu msampha wa Satana. w21.06 22 ¶11; 23 ¶14

Cisanu, April 28

Iwe ukhaladi mfumu ya Isiraeli.—1 Sam. 23:17.

Davide anali kuthaŵa-thaŵa kuti apulumutse moyo wake. Sauli, mfumu yamphamvu ya Isiraeli, anali kufunitsitsa kumupha. Pamene Davide anali kufuna zakudya, anafika mu mzinda wa Nobu, mmene anapempha mitanda isanu ya mkate. (1 Sam. 21:1, 3) Patapita nthawi, iye na asilikali ake anabisala m’phanga kuti atetezeke. (1 Sam. 22:1) Kodi Davide anapezeka bwanji mu mkhalidwe wovuta umenewu? Sauli anali kucitila nsanje kwambili Davide cifukwa anachuka, komanso cifukwa anapambana nkhondo zambili. Sauli anadziŵa kuti kusamvela kwake n’kumene kunapangitsa Yehova kumukana kuti asakhale mfumu ya Isiraeli, komanso kuti Yehova anali atasankha Davide kukhala mfumu ya m’tsogolo. (1 Sam. 23:16, 17) Pokhalabe mfumu ya Isiraeli, Sauli anali na asilikali ambili, na ŵanthu ambili om’cilikiza. N’cifukwa cake, Davide anathaŵa kuti apulumutse moyo wake. Kodi n’kutheka kuti Sauli anali kuona kuti angakwanitse kulepheletsa colinga ca Mulungu pa Davide? (Yes. 55:11) Baibo siikamba, koma cimene tidziŵa n’cakuti: Sauli anaika moyo wake pa ciwopsezo. Anthu otsutsana na Mulungu sapambana konse! w22.01 2 ¶1-2

Ciŵelu, April 29

Nikodemo . . . anabwela kwa Yesu usiku.—Yoh. 3:1, 2.

Yesu anali kugwila nchito yolalikila molimbika. Iye anaonetsa kuti amakonda anthu mwa kulalikila pa mpata uliwonse wapezeka. (Luka 19:47, 48) N’ciani cinamusonkhezela kucita zimenezi? Yesu anali kuwamvelela cifundo. Pa nthawi ina, anthu ambili anali kufuna kumva mawu ake moti iye na ophunzila ake, “sanathe n’komwe kudya cakudya.” (Maliko 3:20) Iye analinso wokonzeka kuphunzitsa anthu usiku—nthawi imene munthu wina anaona kuti ili bwino kwa iye kukamvetsela kwa Yesu. Ambili amene poyamba anamvetsela kwa iye sanakhale ophunzila ake, ngakhale kuti anawacitila umboni mokwanila. Nafenso tiyenela kupatsa aliyense mwayi womvetsela uthenga wabwino. (Mac. 10:42) Kuti ticite zimenezi, tingafunike kusintha mmene timacitila ulaliki. M’malo mongotsatila ndandanda yathu, tiyeni tikhale okonzeka kusintha kuti tizilalikila pa nthawi imene tingapeze anthu ambili. Tikatelo, dziŵani kuti Yehova adzakondwela kwambili. w22.01 17 ¶13-14

Sondo, April 30

Munthu wapweteka munthu mnzake pomulamulila.—Mlal. 8:9.

Masiku ano, anthu ambili cimawavuta kukhulupilila anthu audindo. Izi zili conco cifukwa aona kuti a zamalamulo komanso maboma amakondela anthu olemela komanso amphamvu, ndipo amapondeleza osauka. Kuwonjezela apo, atsogoleli ena acipembedzo amacita zoipa. Izi zapangitsa kuti anthu ena aleke kukhulupilila Mulungu. Conco, munthu akavomela kuphunzila nafe Baibo, timakhala na nchito yom’thandiza kukhulupilila Yehova, komanso kudalila anthu omuimilako padziko lapansi. Anthu amene timaphunzila nawo Baibo, si ndiwo okha ayenela kuphunzila kukhulupilila Yehova na gulu lake. Ngakhale ife amkhalakale m’coonadi, tiyenela kupitiliza kukhulupilila kuti njila ya Yehova yocitila zinthu imakhala yabwino koposa nthawi zonse. Nthawi zina, kukhulupilila kwathu Mulungu kungayesedwe pa nkhaniyi. w22.02 2 ¶1-2

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani