May
Mande, May 1
Ganizilani mozama za munthu amene anapilila.—Aheb. 12:3.
Pofuna kutithandiza kum’dziŵa bwino Mwana wake, Yehova anaikamonso mabuku a Uthenga Wabwino anayi m’Mawu ake. Mabuku anayi amenewo, amafotokoza umoyo wa Yesu na utumiki wake. Mabukuwo amatiuza zimene Yesu anakamba, kutionetsa zimene anacita komanso mmene anali kumvelela. Amatithandizanso ‘kuganizila mozama’ citsanzo ca Yesu. Conco, tingati m’mabuku amenewa muli mapazi amene Yesu anasiya kumbuyo. Conco, mwa kuphunzila Mauthenga Abwino amenewa, tingapitilizebe kum’dziŵa bwino Yesu. Cotulukapo cake n’cakuti tingatsatile mapazi ake mosamala kwambili. Kuti tipindule mokwanila na Mauthenga Abwino amenewa sitiyenela kumangoyaŵelenga cabe ayi. Tifunika kupatula nthawi yowaphunzila mosamala komanso kuwasinkha-sinkha mozama. (Yelekezelani na Yoswa 1:8.) Muzitha kuona m’maganizo mwanu zocitika za m’mabuku a Uthenga Wabwino ngati kuti zikucitika lelo. Yelekezani m’maganizo kuti mukuona, kumvela, na kukhudzika na zimene zinali kucitika. Kuti muthe kucita zimenezi, fufuzani m’zofalitsa za gulu la Yehova. w21.04 4-5 ¶11-13
Ciŵili, May 2
Ife timalalikila za Khristu amene anapacikidwa. Kwa Ayuda, cimeneci ndi cinthu cokhumudwitsa.—1 Akor. 1:23.
Kukali zaka mahandiledi kuti Yesu abwele padziko lapansi, Yehova anaonetsa m’Mawu ake kuti Mesiya adzapelekedwa na ndalama 30 zasiliva. (Zek. 11:12, 13) Wom’pelekayo anali kudzakhala mmodzi wa mabwenzi apamtima a Yesu. (Sal. 41:9) Nayenso mneneli Zekariya analemba kuti: “Ipha m’busa ndipo nkhosa zake zibalalike.” (Zek. 13:7) M’malo mopunthwa na zocitika zimenezi, anthu oona mtima anayenela kulimbikitsidwa cifukwa coona kuti maulosi amenewa akukwanilitsidwa pa Yesu. Kodi timaona kuti masiku anonso anthu ali na vuto limenelo? Inde. M’masiku athu ano, Mboni zina zocepa zodziŵika bwino zasiya coonadi, n’kukhala anthu ampatuko. Ndipo zayesa kupatutsa ena pa coonadi. Iwo amafalitsa nkhani zoipa, kupotoza coonadi, na kufalitsa mabodza okhudza Mboni za Yehova kupitila m’manyuzipepala, pa wailesi, pa TV, komanso pa Intaneti. Koma anthu oona mtima sapunthwa. M’malomwake, iwo amadziŵa kuti Baibo inakambilatu kuti zotelezi zidzacitika.—Mat. 24:24; 2 Pet. 2:18-22. w21.05 11 ¶12; 12-13 ¶18-19
Citatu, May 3
Njila ya olungama ili ngati kuwala kwamphamvu kumene kumamka kuwonjezeleka mpaka tsiku litakhazikika.—Miy. 4:18.
Baibo imaonetsa kuti cidziŵitso colondola cimawonjezeleka m’kupita kwa nthawi. (Akol. 1:9, 10) Yehova amavumbula coonadi mwapang’ono-pang’ono, ndipo tiyenela kuyembekezela moleza mtima kufikila kuwala kwa coonadi kutaunikilidwa bwino-bwino. Bungwe Lolamulila likaona kuti kamvedwe kathu kafunika kusinthadwa pa mfundo ina yake ya coonadi, silizengeleza kupanga masinthidwe ofunikila. Machalichi ambili amasintha ziphunzitso zawo kuti akondweletse anthu awo, kapena kuti dziko liwakonde. Koma gulu la Yehova posintha kamvedwe kawo ka coonadi, colinga cathu cimakhala kuti timuyandikile kwambili Mulungu wathu, komanso kuti tim’lambile m’njila imene Yesu anakhazikitsa. (Yak. 4:4) Timapanga masinthidwe amenewa cifukwa comvetsa bwino Malemba, osati cifukwa cotengela umoyo wamakono, kapena zimene anthu ambili amafuna. Kunena zoona, ife coonadi timacikonda ngako!—1 Ates. 2:3, 4. w21.10 22 ¶12
Cinayi, May 4
[Mutulileni] nkhawa zanu zonse.—1 Pet. 5:7.
Kodi mungacite ciyani mukamva kuti muli nokha-nokha? Ganizilani mmene Yehova akukucilikizilani. (Sal. 55:22) Izi zidzakuthandizani kukhala na kapenyedwe koyenela pa vuto lanu. Ganizilaninso mmene Yehova akuthandizila alambili anzanu amene amasungulumwa. (1 Pet. 5:9, 10) M’bale Hiroshi, amene kwa zaka zambili wakhala yekha Mboni ya Yehova m’banja lawo, anati: “Kudziŵa kuti tonse tikucita zimene tingathe potumikila Yehova, kungalimbikitse ena a ife amene tili tekha m’coonadi m’banja lathu.” Cina, khalani na pulogilamu yabwino yocita zauzimu. Izi ziphatikizapo kuuza Yehova momasuka mmene mumvelela. Ni cinthu cofunika kwambili kuŵelenga Mawu a Mulungu nthawi zonse, na kusinkha-sinkha pa nkhani zoonetsa kuti Yehova amakukondani. Akhristu ena amaloŵeza pa mtima Malemba otonthoza monga Salimo 27:10 na Yesaya 41:10. Ena amaona kuti kumvetsela nkhani zojambulidwa zimene zidzaphunzilidwa, kumawathandiza kusakhala osungulumwa pokonzekela misonkhano, kapena poŵelenga Baibo. w21.06 9-10 ¶5-8
Cisanu, May 5
Sudzaopa zoopsa zilizonse zadzidzidzi.—Miy. 3:25.
Kodi muli na cisoni cifukwa cofeledwa munthu amene mumam’konda? Muzipatula nthawi kuti mulimbitse cikhulupililo canu cakuti akufa adzauka, mwa kuŵelenga nkhani za m’Baibo zokamba za anthu amene anaukitsidwa. Kodi muli na cisoni cifukwa wa m’banja mwanu anacotsedwa mu mpingo? Ŵelengani na kufufuza kuti mutsimikize zakuti cilango ca Yehova n’copindulitsa nthawi zonse. Kaya mukumane na vuto lotani, seŵenzetsani mpata umenewo kuti mulimbitse cikhulupililo canu. Khuthulani za mu mtima mwanu kwa Yehova. Musamadzipatule, koma gwilizanani kwambili na abale na alongo anu. (Miy. 18:1) Muzicita zinthu zimene zingakuthandizeni kupilila, olo kuti mungamalile pamene mukucita zimenezo. (Sal. 126:5, 6) Musaleke kupezeka ku misonkhano, kulalikila, na kuŵelenga Baibo. Cina, sumikani maganizo anu pa madalitso amene Yehova wakusungilani. Mukamaona mmene Yehova akukuthandizilani, cikhulupililo canu mwa iye cidzalimbila-limbilako. w21.11 23 ¶11; 24 ¶17
Ciŵelu, May 6
Mofanana ndi zimenezi, Atate wanga wakumwamba sakufuna kuti mmodzi wa tianati akawonongeke.—Mat. 18:14.
Kodi ophunzila a Yesu ali ngati “tiana” m’njila ina iti? Kodi dziko limaona kuti anthu ofunika ni ati? Aja olemela, ochuka, komanso aulamulilo. Koma ophunzila a Yesu amaoneka ngati “tiana” tosafunika, ndiponso topanda pake. (1 Akor. 1:26-29) Koma Yehova sawaona mwa njila imeneyi. N’ciani cinapangitsa Yesu kukamba za “tianati”? Ophunzila ake anam’funsa funso lakuti: “Ndani kwenikweni amene adzakhala wamkulu kwambili mu Ufumu wakumwamba?” (Mat. 18:1) Pa nthawiyo, Ayuda ambili anali kuona kuti kukhala na udindo n’kofunika kwambili. Katswili wina anati: “Kupatsidwa ulemu na kukhala wochuka zinali zofunika kwambili mu moyo wawo.” Yesu anali kudziŵa kuti ophunzila ake anayenela kucita khama kuti acotse m’mitima yawo mzimu wa mpikisano, umene unali wozika mizu m’cikhalidwe ca Ayuda. w21.06 20 ¶2; 21 ¶6, 8; 22 ¶9
Sondo, May 7
Mafuta ndi zofukiza zonunkhila n’zimene zimasangalatsa mtima, cimodzimodzinso kukoma kwa mnzako cifukwa ca malangizo ake ocokela pansi pa mtima, kumasangalatsa mtima.—Miy. 27:9.
Pokhala mkulu, mtumwi Paulo anapeleka citsanzo cabwino. Mwacitsanzo, pamene abale na alongo ku Tesalonika anafunikila uphungu, Paulo sanazengeleze kuupeleka. M’makalata ake, coyamba iye anawayamikila pa nchito zawo za cikhulupililo, za cikondi, komanso kupilila kwawo. Anaganizilanso mmene zinthu zinalili pa umoyo wawo, ndipo anawauza kuti iye anali kudziŵa mavuto anali kupitamo, komanso mazunzo amene iwo anali kupilila. (1 Ates. 1:3; 2 Ates. 1:4) Anafika ngakhale pouza abalewo kuti anali citsanzo kwa Akhristu ena. (1 Ates. 1:8, 9) Iwo anakondwela kwambili Paulo atawayamikila mwa njila imeneyi. Sitikayikila kuti Paulo anali kuwakonda ngako Akhristu amenewo. Ndiye cifukwa cake, iye anakwanitsa kuwapatsa uphungu wothandiza m’makalata ake aŵili amene analembela Atesalonika.—1 Ates. 4:1, 3-5, 11; 2 Ates. 3:11, 12. w22.02 15 ¶6
Mande, May 8
Adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso.—Chiv. 21:4.
Satana amaseŵenzetsa atsogoleli a zipembedzo zonyenga kukamba kuti Yehova ni wankhanza, ndipo ndiye amacititsa anthu kuvutika. Ena amafika pokamba kuti ana akamwalila, ndiye kuti Mulungu waatenga kuti akakhale angelo kumwamba. Uku ndiye kumunyoza Mulungu! Koma ife sititelo ayi. Tikadwala matenda aakulu, kapena munthu amene timam’konda akamwalila, sitiimba Mulungu mlandu. Mosiyana na anthu ena, timakhulupilila kuti tsiku lina iye adzakonza zinthu zonse. Timauza aliyense amene angatimvetsele kuti Yehova ni Mulungu wacikondi. Izi zimamuthandiza kuyankha amene akumutonza. (Miy. 27:11) Yehova ni Mulungu wacikondi. Iye cimamuŵaŵa akaona tikulila cifukwa ca mavuto amene tikupilila monga cizunzo, matenda, kapena zophophonya zathu. (Sal. 22:23, 24) Yehova amakhudzidwa kwambili tikamavutika. Ni wofunitsitsa kuthetsa mavuto, ndipo adzawathetsadi.—Yelekezelani na Ekisodo 3:7, 8; Yesaya 63:9. w21.07 9-10 ¶9-10
Ciŵili, May 9
Munamuveka ulemelelo ndi ulemu monga cisoti cacifumu.—Sal. 8:5.
Posacedwa, anthu omvela adzasangalala na dalitso lalikulu, limene ni mwayi wokonda Yehova na kum’tumikila kwamuyaya! Yesu adzathetsa mavuto onse amene Adamu na Hava anabweletsa cifukwa cosankha kucoka m’banja la Mulungu. Cina, Yehova adzaukitsa anthu mamiliyoni, na kuwapatsa thanzi labwino, komanso moyo wosatha m’dziko lapansi limene adzalisandutse kukhala paradaiso. (Luka 23:42, 43) Pamene banja la Yehova la padziko lapansi lidzakhala langwilo, onse adzakhala na “ulemelelo ndi ulemu,” zimene Davide anakamba. Ngati ndinu a “khamu lalikulu,” muli na ciyembekezo cabwino zedi. (Chiv. 7:9) Mulungu amakukondani, ndipo afuna kuti mukhale ciwalo ca banja lake. Conco, citani zonse zotheka kuti mum’kondweletse. Tsiku lililonse, muzikumbukila malonjezo a Mulungu mu mtima mwanu. Muziyamikila mwayi umene muli nawo wolambila Atate wathu wakumwamba. Komanso, muziyamikila mwayi wanu wom’tamanda mpaka muyaya! w21.08 7 ¶18-19
Citatu, May 10
Tidzakolola tikapanda kutopa.—Agal. 6:9.
Mneneli Yeremiya analalikila anthu opanda cidwi komanso otsutsa kwa zaka zambili. Iye analefuka kwambili cifukwa ‘conyozedwa na kutonzedwa’ na anthu otsutsa, moti anaganiza zongoleka utumiki wake. (Yer. 20:8, 9) Koma Yeremiya sanafooke! N’ciani cinam’thandiza kuthetsa maganizo olefula, na kukhalanso wacimwemwe mu utumiki wake? Iye anasumika maganizo pa mfundo ziŵili izi zofunika. Yoyamba, uthenga wa Mulungu umene Yeremiya anauza anthu unali kukamba za “tsogolo labwino.” (Yer. 29:11) Yaciŵili, Yeremiya anali kudziŵika na dzina Mulungu. (Yer. 15:16) Mofananamo, ifenso timalalikila uthenga wopatsa ciyembekezo, komanso timadziŵika na dzina la Mulungu pokhala Mboni zake. Tikamasumika maganizo pa mfundo zimenezi, tidzakhala acimwemwe kaya anthu amvetsele kapena ayi. Conco, musalefuke kapena kutaya mtima ngati wophunzila Baibo wanu sakupita patsogolo mmene imwe mufunila. Kupanga ophunzila kumafuna kuleza mtima.—Yak. 5:7, 8. w21.10 27 ¶12-13
Cinayi, May 11
Tiyeninso tivule colemela ciliconse ndi chimo limene limatikola mosavuta lija.—Aheb. 12:1.
Kaya tatumikila Yehova kwa nthawi yaitali motani, tiyenela kupitiliza kulimbitsa cikhulupililo cathu mwa iye. Cifukwa ciani? Cifukwa ngati sitingasamale, cikhulupililo cathu cingayambe kucepa. Monga taphunzilila, cikhulupililo cimaphatikizapo umboni weniweni wa zinthu zosaoneka. Zinthu zimene sitingathe kuziona, tingaziiŵale mosavuta. Ndiye cifukwa cake, Paulo anati kupanda cikhulupililo ni “chimo limene limatikola mosavuta.” Ndiye tingacite ciani kuti tipewe msampha umenewu? (2 Ates. 1:3) Coyamba, muzipempha mzimu woyela wa Yehova nthawi zonse. Cifukwa ciani? Cifukwa cikhulupililo ni khalidwe limene mzimu woyela umabala. (Agal. 5:22, 23) Sitingalimbitse cikhulupililo cathu mwa Mlengi wathu popanda thandizo la mzimu wake woyela. Ngati tipitiliza kupempha Yehova mzimu wake, iye adzatipatsa. (Luka 11:13) Ndipo tingam’pemphe mwacindunji kuti: “Tiwonjezeleni cikhulupililo.” (Luka 17:5) Cinanso, muziŵelenga Mawu a Mulungu nthawi zonse.—Sal. 1:2, 3. w21.08 18-19 ¶16-18
Cisanu, May 12
Imvi ndizo cisoti cacifumu ca ulemelelo.—Miy. 16:31.
Okalamba amathandiza m’njila zambili. Olo kuti tsopano alibe mphamvu poyelekezela na kale, iwo ali na cidziŵitso cokulilapo. Yehova angapitilize kuwagwilitsila nchito. Mwacitsanzo, Baibo imatiuza za anthu okhulupilika amene anatumikila Yehova mokangalika mpaka pa ukalamba wawo. Mwacitsanzo, Mose anali na zaka pafupifupi 80 pamene anakhala mneneli wa Yehova, komanso mtsogoleli wa Aisiraeli. Pamene Danieli anali na zaka mwina zoposa 90, Yehova anapitiliza kumugwilitsila nchito monga mneneli. Nayenso mtumwi Yohane ayenela kuti anali za zaka m’ma 90 pamene anauzilidwa kulemba buku la Chivumbulutso. Simiyoni munthu “wolungama ndi woopa Mulungu,” amachulidwa mwacidule m’Baibo, koma Yehova anali kum’dziŵa bwino kuti iye anali ndani. Ndipo anam’patsa mwayi woona Yesu ali khanda, komanso kulosela zokhudza Yesu ameneyo na mayi ake.—Luka 2:22, 25-35. w21.09 3-4 ¶5-7
Ciŵelu, May 13
Inu Yehova, mtima wanga sunadzikweze, . . . sindinafune zinthu zapamwamba kwambili.—Sal. 131:1.
Makolo ayenela kusamala kuti asamayelekezele mwana wina na wina, kapena kufuna kuti ana azicita zimene sangakwanitse. Ngati makolo amacita zimenezi, angalefule ana awo. (Aef. 6:4) Mlongo wina dzina lake Sachiko anati: “Amayi anali kufuna kuti nizikhoza zonse pa mayeso, zimene zinali zosatheka kwa ine. Ngakhale kuti papita zaka zingapo ndithu kucokela pamene n’natsiliza sukulu, nthawi zina nimakayikilabe ngati zimene nimacita kwa Yehova n’zokwanila.” Mfumu Davide anakamba kuti ‘sanafune zinthu zapamwamba kwambili,’ kapena zinthu zimene sakanakwanitsa kucita. Cifukwa cakuti anali wodzicepetsa, anakhala wokhutila komanso ‘anakhazika mtima wake pansi.’ (Sal. 131:2) Kodi makolo akuphunzilapo ciani pa mawu a Davide? Makolo angaonetse kuti ni odzicepetsa ngati sayembekezela kucita zinthu zimene sangathe, kapena zimene ana awo sangakwanitse. Iwo angathandize ana awo kuona kuti ni ofunika mwa kuzindikila zimene anawo angathe kucita na zimene sangathe. Akatelo, anawo adzadziikila zolinga zimene angakwanilitse. w21.07 21-22 ¶5-6
Sondo, May 14
Aliyense ayenela kunyamula katundu wake.—Agal. 6:5.
Tizikumbukila kuti Yehova anapatsa aliyense ufulu wodzisankhila zocita. Izi zitanthauza kuti tingasankhe kumumvela kapena kusamumvela. Ana ena makolo awo si citsanzo cabwino, koma anawo asankha kutumikila Yehova na kukhalabe okhulupilika kwa iye. Ndipo ana ena amene makolo awo anayesetsa kuwaphunzitsa coonadi, analeka kutumikila Yehova atakula. Conco, ni ufulu wake munthu kusankha kaya kupitiliza kutumikila Yehova kapena ayi. (Yos. 24:15) Motelo, inu makolo, musamadziimbe mlandu mwana wanu akaleka kutumikila Yehova. Nthawi zina, kholo lingasiye coonadi, ngakhalenso kusiya banja lake. (Sal. 27:10) Ndipo cimakhala covuta kwa ana amene anali kuona kholo limenelo kukhala citsanzo cabwino. Imwe ŵana, ngati mmodzi wa makolo anu anacotsedwa mu mpingo, dziŵani kuti Yehova amvetsa mmene mumvelela. Iye amakukondani, ndipo amayamikila kukhulupilika kwanu. Dziŵaninso kuti si mlandu wanu ngati kholo lanu lapanga cisankho colakwika. w21.09 27 ¶5-7
Mande, May 15
Yehova amalanga aliyense amene iye amamukonda.—Aheb. 12:6.
Mkhristu amene wacotsedwa mu mpingo tingamuone ngati nkhosa yodwala imene ingayambukize nkhosa zina. Iye ni wodwala mwauzimu. (Yak. 5:14) Mofanana na matenda akuthupi, kudwala mwauzimu kumayambukila ena. Conco, nthawi zina munthu wodwala mwauzimu angafunikile kucotsedwa mu mpingo. Cilango cimeneci cimaonetsa cikondi ca Yehova pa nkhosa zake zokhulupilika, ndipo cingathandize wocimwayo kuvomeleza kuti analakwadi, komanso kuti alape. Wocotsedwayo ayenela kumapezeka ku misonkhano, kumene angalandile malangizo omuthandiza kukhalanso wolimba mwauzimu. Iye alinso na ufulu wotenga zofalitsa kuti aziŵelenga, na kutamba JW Broadcasting®. Ndipo akulu akaona kuti akupita patsogolo, angamam’patse uphungu na malangizo mwa apa na apo, omuthandiza kucila mwauzimu kuti abwezedwe mu mpingo. w21.10 10 ¶9, 11
Ciŵili, May 16
Sikuti aliyense wonena kwa ine kuti, “Ambuye, Ambuye,” adzaloŵa Ufumu wakumwamba ayi.—Mat. 7:21.
Masiku ano, timatsatila dongosolo la kulambila la Akhristu oyambilila. Mwacitsanzo, m’gulu lathu tili na oyang’anila madela, akulu, komanso atumiki othandiza, potengela Akhristu a m’zaka za zana loyamba. (Afil. 1:1; Tito 1:5) Cina, timatengela citsanzo ca Akhristu amenewo pa nkhani yokhudza kugonana, ukwati, kupatulika kwa magazi, komanso kuteteza mpingo kwa anthu ocita zoipa osalapa. (Mac. 15:28, 29; 1 Akor. 5:11-13; 6:9, 10; Aheb. 13:4) Baibo imatiuza momveka bwino kuti pali “cikhulupililo cimodzi” covomelezeka kwa Mulungu. (Aef. 4:4-6) Ha, ni mwayi waukulu cotani nanga kukhala pakati pa anthu a Yehova, komanso kudziŵa coonadi conena za Yehova na colinga cake! Motelo, tiyeni tigwilebe coonadi mwamphamvu komanso motsimikiza. w21.10 22-23 ¶15-17
Citatu, May 17
Khalani m’malo anu, imani cilili ndi kuona Yehova akukupulumutsani.—2 Mbiri 20:17.
Mfumu Yehosafati anakumana na vuto lalikulu. Gulu la asilikali la Aamoni, Amowabu, komanso amuna a kudela la mapili la Seiri, anawopseza iye, banja lake, na anthu ake. (2 Mbiri 20:1, 2) Kodi Yehosafati anacita ciani? Iye anayang’ana kwa Yehova kuti amuthandize na kum’patsa mphamvu. Pemphelo la Yehosafati la pa 2 Mbiri 20:5-12, linaonetsa kuti iye anali kudalila kwambili Atate wake wacikondi wakumwamba. Yehova anakamba na Yehosafati kupitilila mwa Mlevi wina dzina lake Yahazieli. Anamuuza mawu a lemba la tsiku lalelo. Yehosafati anacita zonse zimene anauzidwa cifukwa anali kukhulupilila kwambili Mulungu wake. Iye na anthu ake atapita kuti akacite nkhondo na adani awo, Yehosafati anaika kutsogolo gulu la oimba m’malo motsogoza asilikali odziŵa kumenya nkhondo. Yehova anayankha pemphelo la Yehosafati mwa kugonjetsa gulu la asilikali la adani ake.—2 Mbiri 20:18-23. w21.11 15-16 ¶6-7
Cinayi, May 18
Cifukwa ca kukoma mtima kosatha kwa Yehova, ife sitinafafanizidwe, ndipo cifundo cake sicidzatha. —Maliro 3:22.
Tikakumana na mayeso, tingakhale na cidalilo cakuti Yehova adzaticilikiza mwa kutipatsa thandizo lofunikila kuti tisunge umphumphu wathu. (2 Akor. 4:7-9) Tili na cidalilo cakuti Yehova adzapitiliza kutionetsa cikondi cosasintha, cifukwa wamasalimo anatitsimikizila kuti: “Diso la Yehova lili pa anthu amene amamuopa, amene amayembekezela kukoma mtima kwake kosatha.” (Sal. 33:18-22) Tisanayambe kutumikila Yehova, iye anationetsa cikondi cimene amaonetsa anthu onse. Koma popeza tsopano ndife alambili ake, timapindulanso na cikondi cake cosasintha. Mosonkhezeledwa na khalidwe limeneli, Yehova amatifungatila na manja ake kuti atiteteze. Iye adzakhala nafe pafupi nthawi zonse, na kukwanilitsa colinga cake ponena za ife. Ndipo amafuna kuti tikhale mabwenzi ake mpaka muyaya. (Sal. 46:1, 2, 7) Conco, kaya tikumane na mayeso otani, Yehova adzatipatsa mphamvu zofunikila kuti tisunge umphumphu wathu. w21.11 7 ¶17-18
Cisanu, May 19
Pitilizani kulolelana ndi kukhululukilana ndi mtima wonse. —Akol. 3:13.
Ambili a ife timadziŵako anthu amene anasungila cakukhosi mnzawo wa kunchito, kusukulu, wacibale, kapena wa m’banja mwawo, mwina kwa zaka. Kumbukilani kuti abale ake 10 a Yosefe anamusungila cakukhosi. Ndipo izi zinawafikitsa pa kum’citila coipa. (Gen. 37:2-8, 25-28) Koma Yosefe anacita zinthu mosiyana na iwo. Ataikidwa pa udindo, sanabwezele coipa kwa abale ake, koma anawacitila cifundo. Iye sanasunge cakukhosi. M’malo mwake, anacita zinthu mogwilizana na lamulo limene linadzalembedwa pa Levitiko 19:18. (Gen. 50:19-21) Citsanzo ca Yosefe ca kukhululuka m’malo mosunga cakukhosi kapena kubwezela, n’cothandiza kwambili kwa Akhristu amene afuna kukondweletsa Mulungu. Yesu anakamba kuti tizikhululukila amene atilakwila. (Mat. 6:9, 12) Mofananamo, mtumwi Paulo analimbikitsa Akhristu anzake kuti: “Okondedwa, musabwezele coipa.”—Aroma 12:19. w21.12 11 ¶13-14
Ciŵelu, May 20
Anthu amene amamuopa adzawacitila zokhumba zawo, adzamva kufuula kwawo kopempha thandizo ndipo adzawapulumutsa.—Sal. 145:19.
Usiku wa pa Nisani 14, mu 33 C.E., Yesu anapita ku munda wa Getsemane. Kumeneko, iye anakhuthula za mu mtima mwake kwa Yehova. (Luka 22:39-44) Pa nthawi yovuta imeneyi, “anapeleka mapemphelo opembedzela . . . mofuula komanso akugwetsa misozi.” (Aheb. 5:7) Kodi Yesu anapemphelela ciani usiku wotsilizawo asanaphedwe? Iye anapempha mphamvu kuti akhalebe wokhulupilika kwa Yehova, na kucita cifunilo ca Mulungu. Yehova anamva pemphelo locondelela la Mwana wake wopsinjika maganizo, ndipo anatuma mngelo kuti akam’limbikitse. Yesu anadziŵa kuti ali na udindo waukulu wokweza dzina la Atate wake. Yehova anamvetsela mapemphelo a Yesu ocokela pansi pa mtima. Cifukwa ciani? Cifukwa cofunika kwambili kwa Yesu cinali kukhalabe wokhulupilika kwa Atate wake, na kukweza dzina la Mulungu. Ngati nafenso cofunika kwambili ni kukhalabe wokhulupilika kwa Yehova, iye adzayankha mapemphelo athu.—Sal. 145:18. w22.01 18 ¶15-17
Sondo, May 21
Pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzila anga. Muziwabatiza . . . ndi kuwaphunzitsa.—Mat. 28:19, 20.
Ambili masiku ano amakhumudwa nafe cifukwa cakuti sititengako mbali m’zandale. Iwo amafuna kuti tizivotako pa masankho. Komabe, timadziŵa kuti tikasankha mtsogoleli waumunthu kuti azitilamulila, ndiye kuti tikukana Yehova. (1 Sam. 8:4-7) Anthu amaona kuti tiyenela kumanga masukulu, zipatala, komanso kucita zinthu zina zothandiza anthu. Iwo amakana uthenga wathu cifukwa timasumika maganizo athu pa nchito yolalikila, osati pa kuthetsa mavuto amene ali padzikoli. Tingacite ciani kuti tisapunthwe? (Mat. 7:21-23) Colinga cathu cacikulu ciyenela kukhala pa kugwila nchito imene Yesu anatilamula. Tisatengeke na zandale kapena kutangwanika pofuna kuyesa kuthetsa mavuto a m’dzikoli. Timakonda anthu, ndipo timasamala za mavuto awo. Koma tidziŵa kuti njila yabwino yothandizila anansi athu, ni mwa kuwaphunzitsa za Ufumu wa Mulungu ndiponso mwa kuwathandiza kukhala pa ubwenzi wabwino na Yehova. w21.05 7 ¶19-20
Mande, May 22
Masiku otsiliza adzakhala nthawi yapadela komanso yovuta. —2 Tim. 3:1.
Ngakhale kuti olamulila a dzikoli amati amatumikila Mulungu, iwo safuna kutula pansi udindo wawo. Conco, monga anacitila olamulila m’nthawi ya Yesu, olamulila masiku ano amatsutsa Wodzozedwa wa Yehova mwa kuzunza otsatila ake okhulupilika. (Mac. 4:25-28) Kodi Yehova amacita ciani? Salimo 2:10-12 imati: “Tsopano inu mafumu, sonyezani kuzindikila, lolani kuti maganizo anu akonzedwe, inu oweluza a dziko lapansi. Tumikilani Yehova mwamantha. Kondwelani ndipo nthunthumilani. Psompsonani mwanayo kuopela kuti Mulungu angakwiye, ndipo mungawonongeke ndi kucotsedwa panjilayo. Pakuti mkwiyo wake umatha kuyaka mofulumila. Odala ndi onse amene akuthawila kwa iye.” Yehova mokoma mtima wapatsa otsutsa amenewa mwayi wakuti apange cisankho canzelu. Iwo angasinthe maganizo awo na kusankha Ufumu wa Yehova. Komabe, nthawi yotsalayi ni yocepa. (Yes. 61:2) Kuposa kale lonse, ino ndiye nthawi yakuti anthu aphunzile coonadi, na kusankha kutumikila Mulungu. w21.09 15-16 ¶8-9
Ciŵili, May 23
Pokhala ndi cakudya, zovala ndi pogona, tikhale okhutila ndi zinthu zimenezi.—1 Tim. 6:8.
Paulo anali kukamba kuti tiyenela kukhutila na zinthu zakuthupi zimene tili nazo. (Afil. 4:12) Cinthu camtengo wapatali kwa ife ni ubale wathu na Mulungu, osati zinthu zakuthupi zimene tili nazo. (Hab. 3:17, 18) Ganizilani zimene Mose anauza Aisiraeli atakhala zaka 40 m’cipululu. Iye anati: “Yehova Mulungu wanu wakudalitsani pa ciliconse cimene dzanja lanu likucita. . . . Yehova Mulungu wanu wakhala nanu zaka 40 zimenezi, ndipo simunasoŵe kanthu.” (Deut. 2:7) Pa zaka 40 zonsezo, Yehova anapatsa Aisiraeli mana monga cakudya. Zovala zawo zimene anacoka nazo ku Iguputo sizinathe. (Deut. 8:3, 4) Yehova amakondwela kwambili tikakhala okhutila, ngakhale pa zocepa zimene angatipatse. Tiziona zinthuzo kuti ni mphatso, ndipo tiziyamikila. w22.01 5 ¶10-11
Citatu, May 24
Khulupilila Yehova ndi mtima wako wonse, ndipo usadalile luso lako lomvetsa zinthu.—Miy. 3:5.
Inu amuna okwatila, muli na udindo woyang’anila banja lanu. N’cifukwa cake mumagwila nchito molimbika kuti muteteze na kusamalila banja lanu. Mukakumana na mavuto, mwina mungaone kuti mungakwanitse kuwathetsa pamwekha. Pewani mzimu wodzidalila. M’malo mwake, pemphani Yehova panokha kuti akuthandizeni. Cinanso, muzipemphela na mkazi wanu mocokela pansi pa mtima. Funsilani malangizo kwa Yehova mwa kuŵelenga Baibo na zofalitsa zimene gulu la Mulungu limapeleka, ndipo muziseŵenzetsa malangizo ake. Ena sangagwilizane na zisankho zanu zozikidwa pa Baibo. Iwo angakuuzeni kuti ndalama na katundu ndizo zingateteze bwino banja lanu. Koma kumbukilani citsanzo ca Mfumu Yehosafati. (2 Mbiri 20:1-30) Iye anadalila Yehova, ndipo anaonetsa zimenezo mwa zocita zake. Yehova sanamusiye munthu wokhulupilika ameneyu, ndipo inunso sadzakusiyani.—Sal. 37:28; Aheb. 13:5. w21.11 15 ¶6; 16 ¶8
Cinayi, May 25
Mulungu . . . cosalungama. —Deut. 32:4.
Popeza Mulungu anatilenga m’cifanizilo cake, timafuna kuti anthu azicitilidwa zinthu mwacilungamo. (Gen. 1:26) Koma cifukwa copanda ungwilo, tingaone zinthu molakwika cifukwa coganiza kuti tikudziŵa zonse pa nkhaniyo. Mwacitsanzo, Yona sanakondwele pamene Yehova anasankha kucitila cifundo anthu a ku Nineve. (Yona 3:10–4:1) Koma onani zinacitika. Cifukwa cowacitila cifundo, Anineve olapa oposa 120,000 anapulumuka. Potsilizila pake, tiona kuti Yona ndiye anaweluza molakwika anthuwo, osati Yehova. Yehova safunika kucita kufotokozela anthu zifukwa zimene wapangila zisankho. N’zoona kuti kumbuyoko analola atumiki ake kufotokoza mmene iwo anamvelela pa zigamulo zimene iye anapanga, kapena zimene anali kufuna kupanga. (Gen. 18:25; Yona 4:2, 3) Ndipo nthawi zina, anali kufotokoza zifukwa zimene anapangila cigamulo cina cake. (Yona 4:10, 11) Komabe, Yehova safunika civomelezo cathu asanacite cina cake, kapena pambuyo pocita cinthuco.—Yes. 40:13, 14; 55:9. w22.02 3-4 ¶5-6
Cisanu, May 26
Amene ali wamkulu kwambili pa nonsenu akhale ngati wamng’ono kwambili pa nonsenu, ndipo amene ali mtsogoleli akhale wotumikila.—Luka 22:26.
Timakhala ngati “wamng’ono kwambili” pamene ‘tiona ena kukhala otiposa.’ (Afil. 2:3) Tikakulitsa kwambili khalidwe limeneli, tidzapewa kukhumudwitsa ena. Abale na alongo athu onse amatiposa m’njila zina. N’cosavuta kuona zimenezi ngati timasumika maganizo athu pa makhalidwe awo abwino. Tiyenela kukumbukila uphungu umene mtumwi Paulo anapeleka kwa Akorinto. Anati: “Kodi akukupangitsa kukhala wosiyana ndi ena ndani? Inde, uli ndi ciani cimene sunacite kulandila? Ndiye ngati unacita kulandila zinthu zimenezo, n’cifukwa ciani ukudzitama ngati kuti sunacite kulandila?” (1 Akor. 4:7) Tiyenela kusamala kwambili kuti tisagwele m’mayeselo odziona kuti ndife apamwamba, kapena kuganiza kuti ndife ofunika kwambili kuposa ena. Ngati m’bale amakamba nkhani zotentha, kapena ngati mlongo ali na mphatso yoyambitsa maphunzilo a Baibo, iwo sayenela kuzengeleza kupeleka citamando kwa Yehova. w21.06 22 ¶9-10
Ciŵelu, May 27
Bzala mbewu zako . . . ndipo dzanja lako lisapume.—Mlal. 11:6.
Kwa Mboni za Yehova zambili, vuto la kusapeza anthu panyumba likukulila-kulila. Ofalitsa ena amakhala m’madela amene nyumba zambili zili m’mipanda kapena zili na citetezo cokhwima. Pangakhale mlonda amene amaletsa aliyense kulowa popanda cilolezo cocokela kwa amene akhala mkati. Ofalitsa ena amapeza anthu ocepa m’makomo, kapena amalalikila m’madela akutali kumene kumakhala anthu ocepa. Ofalitsa ena angafunike kuyenda misenga yaitali, kuti akalalikile cabe munthu mmodzi amenenso mwina sangapezeke panyumba. Tikakumana na zopinga zotele, sitiyenela kufooka. Yesani kufikila anthu panthawi zosiyana-siyana. Tidzapeza anthu ambili ngati tilalikila pa nthawi imene iwo angapezeke panyumba. Paja munthu aliyense ali na nthawi imene amapezeka panyumba! Abale na alongo ambili, amaona kuti cimakhala cothandiza kulalikila masana kapena madzulo cifukwa m’pamene amapeza anthu ambili. Kuwonjezela apo, anthu angakhale kuti akupumula, ndipo amakhala okonzeka kukambilana nawo pa nthawi ngati zimenezo. w21.05 15 ¶5, 7
Sondo, May 28
Amandipembedza pacabe, cifukwa amaphunzitsa malamulo a anthu ngati ziphunzitso za Mulungu. —Maliko 7:7.
Kodi timaona kuti masiku anonso anthu ali na vuto limenelo? Inde. Ambili amakwiya cifukwa cakuti Mboni za Yehova sizicita nawo miyambo yosagwilizana na Malemba, monga kukondwelela masiku akubadwa, na Khrisimasi. Ena amakalipa akaona kuti Mboni za Yehova sizicitako zikondwelelo za dziko lawo, kapena cifukwa sizitsatila miyambo ya malilo yosemphana na Mawu a Mulungu. Aja amene amakhumudwa pa zifukwa zimenezi, amakhulupilila na mtima wonse kuti amalambila Mulungu movomelezeka. Koma sangamukondweletse ngati amakonda kwambili miyambo ya dziko kuposa ziphunzitso zomveka bwino za m’Baibo. (Maliko 7:8, 9.) Tingacite ciani kuti tisapunthwe? Tiyenela kukonda kwambili malamulo a Yehova na mfundo zake. (Sal. 119:97, 113, 163-165) Ngati timam’konda Yehova, tidzakana miyambo iliyonse yosam’kondweletsa. Sitidzalola ciliconse kusokoneza cikondi cathu pa Yehova. w21.05 6 ¶15-16
Mande, May 29
Ukhalebe woganiza bwino pa zinthu zonse, imva zoŵaŵa, gwila nchito ya mlaliki.—2 Tim. 4:5.
Kodi tingauseŵenzetsa bwanji uphungu wa mtumwi Paulo umenewu? Tifunika kupitiliza kulimbitsa cikhulupililo cathu mwa kuphunzila mawu a Mulungu nthawi zonse, kupitiliza kupemphela, ndiponso kucita zambili m’nchito imene Yehova watipatsa. (2 Tim. 4:4) Tikakhala na cikhulupililo, sitidzakhala na nkhawa tikamvela nkhani zoipa zokhudza Mboni za Yehova. (Yes. 28:16) Cikondi cathu pa Yehova, pa Mawu ake, ndiponso pa abale athu cidzatithandiza kupewa kupunthwa cifukwa ca aja amene aleka coonadi. M’zaka za zana loyamba, ambili anapunthwa, ndipo anam’kana Yesu. Koma ena ambili anamulandila. Ena mwa iwo anali mmodzi wa oweluza m’Khoti Yapamwamba ya Ayuda, komanso ngakhale “ansembe ambilimbili.” (Mac. 6:7; Mat. 27:57-60; Maliko 15:43) Mofananamo, masiku ano anthu ofika mamiliyoni sanapunthwe. Cifukwa ciani? Cifukwa amadziŵa na kukonda mfundo za coonadi zopezeka m’Malemba. Mawu a Mulungu amakamba kuti: “Okonda cilamulo canu amapeza mtendele woculuka, ndipo palibe cowakhumudwitsa.”—Sal. 119:165. w21.05 13 ¶20-21
Ciŵili, May 30
Mphamvu yanga imakhala yokwanila iweyo ukakhala wofooka.—2 Akor. 12:9.
Mtumwi Paulo anazindikila kuti zonse zimene anacita potumikila Yehova zinatheka cifukwa ca mphamvu za Mulungu osati zake. IKupitila mwa mzimu wake woyela, Yehova anapatsa Paulo mphamvu zomuthandiza kukwanilitsa mbali zonse za utumiki wake, mosasamala kanthu za cizunzo, kuponyedwa m’ndende, komanso mavuto ena amene anakumana nawo. Timoteyo, mnzake wacicepele wa Paulo, nayenso anayenela kudalila mphamvu za Mulungu kuti akwanitse kucita utumiki wake. Iye anali kuyenda na Paulo pa maulendo atali-atali aumishonale. Kuwonjezela apo, Paulo analinso kutuma Timoteyo kukacezela mipingo na kuilimbikitsa. (1 Akor. 4:17) N’kutheka kuti Timoteyo anali kudzidelela. Mwina ndiye cifukwa cake Paulo anamulimbikitsa kuti: “Usalole kuti munthu aliyense akudelele poona kuti ndiwe wamng’ono.” (1 Tim. 4:12) Ndipo panthawiyo, Timoteyo anali na munga wake m’thupi—“kudwaladwala.” (1 Tim. 5:23) Koma iye anadziŵa kuti mzimu wamphamvu woyela wa Yehova, udzamupatsa mphamvu zofunikila kuti alalikile uthenga wabwino komanso kuti atumikile abale ake.—2 Tim. 1:7. w21.05 21 ¶6-7
Citatu, May 31
Ika mtima wako pa magulu a ziweto zako.—Miy. 27:23.
Mfundo ya pa Yakobo 1:19, imagwila nchito kwa awo amene amapeleka uphungu. Yakobo analemba kuti: “Munthu aliyense akhale wofulumila kumva, wodekha polankhula, wosafulumila kukwiya.” Mwina mkulu angaganize kuti akudziŵa mikhalidwe yonse ya munthu amene akufuna kupatsa uphungu, koma kodi iye adziŵadi zonse? Miyambo 18:13 imatikumbutsa kuti: “Munthu aliyense woyankhila nkhani asanaimvetsetse n’ngopusa, ndipo amacita manyazi.” Conco, ni bwino kufunsa mwiniwake kuti afotokoze zoona zake. Izi ziphatikizapo kumvetsela coyamba musanalankhule. Mkulu angafunse kuti: “Kodi zinthu zili motani pa umoyo wanu?” “Kodi pali mbali imene tingathandizilepo?” Akulu akamamvetsela coyamba kwa abale na alongo awo kuti adziŵe zimene akupitamo, adzipeleka thandizo lofunikila komanso cilimbikitso. Kupeleka uphungu wothandiza sikungoŵelenga cabe malemba angapo kapena kupelekapo malingalilo ayi. Abale na alongo athu ayenela kuona kuti timawadela nkhawa, timawamvetsetsa, komanso tifuna kuwathandiza. w22.02 17 ¶14-15