LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • es23 masa. 67-77
  • July

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • July
  • Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2023
  • Tumitu
  • Ciŵelu, July 1
  • Sondo, July 2
  • Mande, July 3
  • Ciŵili, July 4
  • Citatu, July 5
  • Cinayi, July 6
  • Cisanu, July 7
  • Ciŵelu, July 8
  • Sondo, July 9
  • Mande, July 10
  • Ciŵili, July 11
  • Citatu, July 12
  • Cinayi, July 13
  • Cisanu, July 14
  • Ciŵelu, July 15
  • Sondo, July 16
  • Mande, July 17
  • Ciŵili, July 18
  • Citatu, July 19
  • Cinayi, July 20
  • Cisanu, July 21
  • Ciŵelu, July 22
  • Sondo, July 23
  • Mande, July 24
  • Ciŵili, July 25
  • Citatu, July 26
  • Cinayi, July 27
  • Cisanu, July 28
  • Ciŵelu, July 29
  • Sondo, July 30
  • Mande, July 31
Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2023
es23 masa. 67-77

July

Ciŵelu, July 1

Pambuyo pake, kwa anthu amene aphunzilapo kanthu pa cilangoco, cimabala cipatso camtendele, comwe ndi cilungamo.—Aheb. 12:11.

Kucotsa munthu mu mpingo ni makonzedwe a Yehova. Aliyense amapindula, kuphatikizapo wolakwayo. Ena mu mpingo angayambe kukamba kuti sanagamule bwino kuti uje acotsedwe mu mpingo. Koma dziŵani kuti kambili anthu otelo samachula zoipa zimene wolakwayo anacita. Timakhala kuti sitidziŵa zoona zake pa nkhaniyo. Ndiye n’canzelu kukhulupilila kuti akulu amene anaweluza nkhaniyo, anayesetsa kutsatila mfundo za m’Malemba, podziŵa kuti ‘akuweluzila Yehova.’ (2 Mbiri 19:6) Mukagwilizana na cigamulo ca akulu ca kucotsa wacibale wanu mu mpingo, ndiye kuti mukumuthandiza kubwelela kwa Yehova. Mlongo Elizabeth anati: “Cinali covuta kwambili kuleka kukamba na mwana wathu wamkulu. Koma atabwelela kwa Yehova, anavomeleza kuti anayeneladi kucotsedwa mu mpingo. Pambuyo pake, iye anati anaphunzilapo kanthu pa zimene zinamucitikilazo.” w21.09 28-29 ¶11-12

Sondo, July 2

Anaona mkazi wina wamasiye wosauka akuponya timakobidi tiŵili tating’ono mmenemo. —Luka 21:2.

Ganizilani za mkazi wamasiye uja. Mosakayikila, iye anali kulaka-laka kupeleka zambili kwa Yehova. Komabe anacita zimene akanakwanitsa. Anapatsa Yehova zonse zimene akanatha kupeleka. Ndipo Yesu anadziŵa kuti copeleka ca mkazi wamasiyeyo cinali ca mtengo wapatali m’maso mwa Atate wake. Apa pali phunzilo lofunika kwambili kwa ife. Yehova amakondwela tikam’patsa zonse zimene tingathe, kutanthauza kum’tumikila na mtima wathu wonse komanso moyo wathu wonse. (Mat. 22:37; Akol. 3:23) Yehova amakondwela akamaona kuti tikucita zonse zimene tingathe! Mfundo imeneyi igwila nchito pa kuculuka kwa nthawi na mphamvu zimene timaseŵenzetsa pa kulambila kwathu, kuphatikizapo pankhani ya ulaliki na misonkhano. Kodi mungaseŵenzetse bwanji phunzilo limene mwatengapo pankhani ya mkazi wamasiye? Yesani kuganizila anthu amene angalimbikitsidwe mukawatsimikizila kuti Yehova amakondwela na kuyesetsa kwawo pom’tumikila. Mwina mlongo wacikulile amavutika maganizo, kapena kudziona kuti ni wakutha nchito, cifukwa cakuti thanzi lake silimulola kucita zimene anali kukwanitsa kale mu utumiki. w21.04 6 ¶17, 19-20

Mande, July 3

Wodala ndi munthu wopilila mayeselo, cifukwa akadzavomelezedwa, adzalandila mphoto ya moyo. —Yak. 1:12.

Yehova akudziŵa nthawi yoyenelela yodzawononga dziko loipali. Cifukwa ca kuleza mtima kwake, anthu ambili afika pom’dziŵa, ndipo khamu la anthu ofika m’mamiliyoni akumulambila na kum’tamanda. Onsewo amayamikila kuti Yehova wapilila kwanthawi yaitali mpaka iwo kubadwa, kuphunzila kum’konda, komanso kudzipatulila kwa iye. Yehova akadzawafupa anthu mamiliyoni amene adzapilila mpaka mapeto, zidzaonetselatu kuti cisankho cake ca kupilila cinali canzelu! Olo kuti Satana wacititsa zinthu zowawitsa mtima komanso mavuto, Yehova wakhalabe “Mulungu wacimwemwe.” (1 Tim. 1:11) Ifenso tingakhalebe acimwemwe poyembekezela moleza mtima kuti Yehova akayeletse dzina lake, kuthetsa nkhani ya ulamulilo, makhalidwe onse oipa, komanso mavuto onse amene tikukumana nawo pali pano. Tiyeni tikhale otsimikiza mtima kupilila komanso kulimbikitsidwa podziŵa kuti Atate wathu wakumwamba nayenso akupilila. w21.07 13 ¶18-19

Ciŵili, July 4

Kodi mu Nazareti mungatuluke kanthu kabwino? —Yoh. 1:46.

Anthu ambili m’zaka za zana loyamba sanam’khulupilile Yesu. Kwa iwo, iye anali cabe mwana wa kalipentala wosauka. Ndipo anali wocokela ku Nazareti, mzinda umene unali kuonedwa kuti ni wotsika. Ngakhale Natanayeli amene anakhala wophunzila wa Yesu, poyamba anati: “Kodi mu Nazareti mungatuluke kanthu kabwino?” N’kutheka kuti anali kuganizila za ulosi wa pa Mika 5:2, umene unakambilatu kuti Mesiya adzabadwila ku Betelehemu, osati ku Nazareti. Mneneli Yesaya analosela kuti adani a Yesu adzalephela kuganizila “tsatanetsatane wa mibadwo ya makolo” a Mesiya. (Yes. 53:8) Anthu amenewo akanapenda zonse zokhudza Yesu, akanadziŵa kuti iye anabadwila ku Betelehemu, komanso kuti anali mbadwa ya Mfumu Davide. (Luka 2:4-7) Conco, malo amene Yesu anabadwilako anali ogwilizana na ulosi wa pa Mika 5:2. Nanga kodi vuto linali ciani? Anthu anafulumila kumuweluza Yesu m’maganizo awo asanadziŵe zonse zokhudza iye. Kaamba ka ici, iwo anapunthwa. w21.05 2-3 ¶4-6

Citatu, July 5

Wolungama . . . akandidzudzula ndiye kuti wandidzoza mafuta pamutu panga.—Sal. 141:5.

M’Baibo muli zitsanzo zabwino za anthu amene anadalitsidwa cifukwa comvela uphungu. Ganizilani za Yobu. Olo kuti anali munthu woopa Mulungu, iye sanali wangwilo. Cifukwa ca cipsinjo cake cacikulu, anakamba zinthu mosalingalila bwino. Izi zinapangitsa kuti Elihu, komanso Yehova am’patse uphungu mosapita m’mbali. Kodi Yobu anacita ciyani? Iye anati: “Ndinalankhula, koma sindinali kuzindikila . . . ndikubweza mawu anga, ndipo ndikulapa m’fumbi ndi m’phulusa.” (Yobu 42:3-6, 12-17) Kudzicepetsa kwake kunaonekela pamene analandila uphungu kwa Elihu, ngakhale kuti Elihu anali wocepelepo kwa iye. (Yobu 32:6, 7) Mofananamo, kudzicepetsa kudzatithandiza nafenso kuseŵenzetsa uphungu ngakhale pamene taona kuti sitinafunikile kupatsidwa uphunguwo, kapena ngati amene watipatsa uphunguwo ni wocepelapo kwa ife. Ndani wa ife safuna kupita patsogolo pokulitsa zipatso zimene mzimu woyela umabala, komanso pocita utumiki wathu wacikhristu? w22.02 11 ¶8; 12 ¶12

Cinayi, July 6

Mwakutelo, onse adzadziŵa kuti ndinu ophunzila anga, ngati mukukondana.—Yoh. 13:35.

Onse mu mpingo ali na udindo wothandiza kuti mu mpingomo mukhale cikondi na mtendele, kuti pasapezeke aliyense woona kuti ali yekha-yekha. Zimene timakamba na kucita zingakhale zothandiza zedi! Kodi mungacite ciani kuti muthandize aja amene m’banja mwawo iwo okha ndiwo Mboni, kuti nawonso azimvela kuti ni ziwalo za mpingo? Khalani patsogolo kupanga ena kukhala mabwenzi anu. Tingayambe mwa kulandila mwansangala anthu amene asamukila mu mpingo mwathu. (Aroma 15:7) Komabe, siziyenela kuthela cabe pa kuwapatsa moni mwaubwenzi. M’malo mwake, tiyenela kukhala nawo pa ubwenzi wolimba m’kupita kwa nthawi. Conco, muzikhala na cidwi ceni-ceni kwa amene asamukila mu mpingo mwanu. Mosaloŵelela nkhani zawo zaumwini, yesani kumvetsa mavuto amene akupitamo. Ena zimaŵavuta kufotokoza mmene akumvelela. Conco samalani kuti musawakakamize kukamba. Koma mokoma mtima afunseni mafunso mosamala kuti afotokoze za mu mtima mwawo. Ndipo amvetseleni moleza mtima akamayankha. Mwacitsanzo, mungaŵafunse mmene anaphunzilila coonadi. w21.06 11 ¶13-14

Cisanu, July 7

Zidzamva mawu anga, ndipo zidzakhala gulu limodzi ndi m’busa mmodzi.—Yoh. 10:16.

Timayamikila mwayi umene tili nawo wotumikila Yehova mogwilizana monga “gulu limodzi” pansi pa “m’busa mmodzi”! Buku lakuti Gulu Lokhazikitsidwa Kucita Cifunilo ca Yehova, tsamba 165 limati: “Popindula na umodzi umenewo, tilinso na udindo wa kuulimbitsa.” Conco, tiyenela ‘kuzolowela kuona abale na alongo athu mmene Yehova amawaonela.’ Kwa Yehova, tonse ndife “tiana” ta mtengo wapatali. Kodi umu ni mmene mumaonela abale na alongo anu? Yehova amaona ndipo amayamikila zonse zimene mumacita powathandiza na kuwasamalila. (Mat. 10:42) Timawakonda alambili anzathu. Conco, ndife ‘otsimikiza mtima kusaikila m’bale wathu cokhumudwitsa kapena copunthwitsa.’ (Aroma 14:13) Timaona abale na alongo athu kukhala otiposa, ndipo timafuna kuwakhululukila mocokela pansi pa mtima. Tisalole kuti ena atipunthwitse. M’malo mwake, “tiyeni titsatile zinthu zobweletsa mtendele ndiponso zolimbikitsana.”—Aroma 14:19. w21.06 24 ¶16-17

Ciŵelu, July 8

Mulungu . . . amakulitsa. —1 Akor. 3:7.

Tiyenela kuŵelenga Mawu a Mulungu mwakhama na kuseŵenzetsa malangizo ake, komanso ocokela ku gulu lake. Tikatelo, pang’ono-m’pang’ono tidzayamba kukulitsa makhalidwe amene Khristu anali nawo. Kuwonjezela apo, cidziŵitso cathu ponena za Mulungu cidzawonjezeleka. Yesu anafotokoza fanizo la kanjele kakang’ono, poonetsa mmene uthenga wa Ufumu umene timalalikila umakulila m’mitima ya anthu a maganizo abwino. Iye anati: “Mbewuzo zimamela ndi kukula. Koma mmene zimenezi zimacitikila, mwiniwakeyo [wobyala] sadziwa ayi. Pang’onopang’ono, payokha nthaka ija imabala zipatso. Coyamba mmela umabiliwila, kenako umatulutsa ngala, pamapeto pake maso okhwima a tiligu amaonekela m’ngalamo.” (Maliko 4:27, 28) Yesu anali kufotokoza kuti monga mmene mbewu imakulila pang’ono-pang’ono, nayenso munthu amene walandila uthenga wa Ufumu amakula kuuzimu mwapang’ono-pang’ono. Mwacitsanzo, maphunzilo athu a Baibo akamayandikila Yehova, timatha kuona kuti iwo akupanga masinthidwe mu umoyo wawo. (Aef. 4:22-24) Koma tizikumbukila kuti Yehova ndiye amacititsa kanjele kakang’onoko kukula. w21.08 8-9 ¶4-5

Sondo, July 9

Kuona ndi maso kuli bwino kuposa kulakalaka ndi mtima. —Mlal. 6:9.

Tingapeze cimwemwe ngati ticifuna-funa m’njila yoyenela. Munthu amene amakondwela na ‘zimene maso aona,’ amakhutila na zimene ali nazo, kuphatikizapo zimene angakwanitse kucita pali pano. Koma munthu amene amangolakalaka mu mtima, amafunitsitsa zinthu zimene kwa iye n’zosatheka kukhala nazo. Kodi pali phunzilo lotani pamenepa? Kuti tikhale acimwemwe, tiyenela kusumika maganizo athu pa zimene tili nazo, komanso pa zolinga zimene n’zotheka kuzikwanilitsa. Kodi n’zothekadi kukhala okhutila na zimene tili nazo? Inde, n’zotheka ndithu. Koma anthu ambili amaona kuti n’zosatheka, cifukwa mwacibadwa ife anthu timafuna kukhala na zinthu zatsopano. Komabe, n’zothekadi kukhala okondwela na zimene tili nazo. Kodi izi zingatheke bwanji? Kuti tiyankhe funsoli, ganizilani fanizo la Yesu la matalente lopezeka pa Mateyu 25:14-30. Fanizoli limatiphunzitsa mmene tingakhalile acimwemwe, komanso mmene tingawonjezele cimwemwe cathu pa mautumiki amene tikucita pali pano. w21.08 21 ¶5-6

Mande, July 10

Ine ndimakhala kumwamba pamalo oyela. Ndimakhalanso ndi munthu wopsinjika ndi wa mtima wodzicepetsa.—Yes. 57:15.

Yehova amasamala za anthu ‘opsinjika ndi a mtima wodzicepetsa.’ Tonsefe, osati akulu okha, tingawalimbikitse abale na alongo athu okondedwa amenewa. Njila imodzi imene tingawalimbikitsile ni kuwaonetsa cidwi ceniceni. Yehova amafuna tizionetsa cikondi cake ku nkhosa zake za mtengo wapatali. (Miy. 19:17) Tingathandizenso abale na alongo athu mwa kukhala odzicepetsa. Sitifuna kudzipezela ulemelelo cifukwa ca maluso athu, zimene zingapangitse ena kuyamba kuticitila kaduka. M’malo mwake, tiyenela kuseŵenzetsa maluso na cidziŵitso cathu kuti tilimbikitsane. (1 Pet. 4:10, 11) Tingaphunzile zambili za mokhalila na ŵena poona mmene Yesu anacitila zinthu na otsatila ake. Anali munthu wamkulu woposa onse amene anakhalako. Ngakhale n’conco, iye anali “wofatsa ndi wodzicepetsa.” (Mat. 11:28-30) Pophunzitsa, anali kuseŵenzetsa mawu osavuta kumva na mafanizo ogwila mtima kuti afike pa mtima anthu odzicepetsa.—Luka 10:21. w21.07 23 ¶11-12

Ciŵili, July 11

Funsa . . . amuna acikulile pakati panu, ndipo akufotokozela. —Deut. 32:7.

Muzipeza nthawi yoceza na okalamba. N’zoona kuti kuyang’ana kumawavuta, kuyenda nako n’kovutikila, ndipo cimakhala covuta kulankhula bwino-bwino. Koma iwo amafunabe kukhala okangalika, ndipo adzipangila “mbili yabwino” kwa Yehova. (Mlal. 7:1) Muzikumbukila kuti Yehova amawaona kuti ni ofunika ngako. Motelo, pitilizani kuwalemekeza. Khalani monga Elisa. Iye anafunitsitsa kukhalabe na Eliya pa tsiku lawo lothela kukhala pamodzi. Katatu konse Elisa anauza Eliya kuti: “Sindikusiyani.” (2 Maf. 2:2, 4, 6) Muziwaonetsa cidwi ceniceni okalamba mwa kuwafunsa mafunso mokoma mtima. (Miy. 1:5; 20:5; 1 Tim. 5:1, 2) Afunseni mafunso monga akuti: “Pamene munali wacicepele, n’ciani cinakupangitsani kutsimikiza kuti mwapeza coonadi?” “Kodi zocitika mu umoyo wanu zakuthandizani bwanji kuyandikila kwambili Yehova?” “N’ciani cakuthandizani kupitiliza kukhala acimwemwe potumikila Yehova?” (1 Tim. 6:6-8) Ndiyeno mvetselani pamene akufotokoza. w21.09 5 ¶14; 7 ¶15

Citatu, July 12

Mulungu amacita zinthu m’njila imene imamusangalatsa. Iye amalimbitsa zolakalaka zanu kuti mucite zinthu zonse zimene iye amakonda.—Afil. 2:13.

Pamene mucita zonse zotheka pomvela lamulo la kulalikila na kupanga ophunzila, mumaonetsa cikondi canu pa Mulungu. (1 Yoh. 5:3) Ganizilani izi: Cikondi canu pa Yehova cinakusonkhezelani kuyamba kulalikila nyumba na nyumba. Kodi lamulo limeneli linali lopepuka kulitsatila? Osati kwenikweni. Mutafika pa khomo la munthu kwa ulendo woyamba kuti mulalikile, kodi munacita mantha? Mosakayikila munacitadi mantha! Koma podziŵa kuti iyi ni nchito imene Yesu afuna kuti muigwile, munamvelabe lamulo limeneli. Mwacionekele, m’kupita kwa nthawi, cinakhala copepuka kwa imwe kugwila nchito yolalikila. Nanga bwanji zotsogoza phunzilo la Baibo? Kodi mumacita mantha mukaiganizila nkhani imeneyi? Mwina. Komabe, mukapempha Yehova kuti akuthandizeni kugonjetsa mantha, kenako na kulimba mtima kuti muyambe kutsogoza phunzilo la Baibo, Yehova adzakuthandizani kukulitsa cikhumbo canu ca kupanga ophunzila. w21.07 3 ¶7

Cinayi, July 13

Apatsidwe cizindikilo padzanja lawo lamanja kapena pamphumi pawo.—Chiv. 13:16.

M’nthawi zakale, akapolo anali kudindiwa cizindikilo copseleza coonetsa umwini wa mbuye wawo. Mofananamo, onse masiku ano akuyembekeledwa kukhala na cizindikilo pa dzanja kapena pa mphumi pawo. Mabomawo adzafuna kuti aliyense aonetse mwa maganizo ake, komanso zocita zake kuti akucilikiza ndale m’dzikoli. Kodi ife tidzalandila cizindikilo cophiphilitsa cimeneco na kucilikiza maboma a ndale? Awo amene adzakana, adzakumana na mavuto aakulu. Buku la Chivumbulutso limati: “Aliyense asathe kugula kapena kugulitsa, kupatulapo ngati ali ndi cizindikiloco.” (Chiv. 13:17) Koma anthu a Mulungu adziŵa zimene Mulungu adzacita kwa anthu amene ali na cizindikilo cochulidwa pa Chivumbulutso 14:9, 10. M’malo mokhala na cizindikilo cimeneco, zidzakhala ngati iwo alemba pa dzanja lawo kuti, “Wa Yehova.” (Yes. 44:5) Ino ndiye nthawi yolimbitsa cikhulupililo cathu mwa Yehova. Cikhulupililo cathu cikalimba, Yehova adzakhala wonyadila kukamba kuti ndife ake-ake! w21.09 18 ¶15-16

Cisanu, July 14

Citsulo cimanola citsulo cinzake. Momwemonso munthu amanola munthu mnzake.—Miy. 27:17.

Kuti tikwanilitse utumiki wathu, tiyenela kulandila thandizo la ena. Mtumwi Paulo anaphunzitsa Timoteyo njila zoyenela kuseŵenzetsa polalikila na kuphunzitsa. Ndipo anam’limbikitsa kuthandizakonso ena kuseŵenzetsa njila zimenezo. (1 Akor. 4:17) Mofanana na Timoteyo, nafenso tingaphunzile zambili kwa aja amene ni aciyambakale mumpingo. Cina, pemphani Yehova kuti akuthandizeni. Pemphani Yehova kuti akutsogoleleni nthawi zonse mukapita mu ulaliki. Popanda mphamvu yake ya mzimu woyela, palibe aliyense wa ife angathe kucita ciliconse. (Sal. 127:1; Luka 11:13) Popempha Yehova kuti akuthandizeni, chulani zinthu mwacindunji. Mwacitsanzo, mungam’pemphe kuti akutsogoleleni kwa aliyense amene ali na maganizo oyenelela, komanso amene ni wokonzeka kumvetsela. Kuwonjezela apo, pangani nthawi yocita phunzilo laumwini. Mawu a Mulungu amanena kuti: ‘Zindikilani cimene cili cifunilo ca Mulungu, cabwino, covomelezeka ndi cangwilo.’ (Aroma 12:2) Tikakhala otsimikiza kuti timadziŵadi coonadi cokhudza Mulungu, m’pamene timalankhula mwacidalilo pokambilana na ena mu ulaliki. w21.05 18 ¶14-16

Ciŵelu, July 15

Zonse zimene mukucita mu nchito ya Ambuye sizidzapita pacabe.—1 Akor. 15:58.

Bwanji ngati mwayesetsa kuphunzila Baibo na munthu ndiponso kumupemphelela, koma iye sapita patsogolo, ndipo mwaganiza zoleka kuphunzila naye? Kapena bwanji ngati mukalibe kuthandizapo munthu mpaka kufika pobatizika? Kodi muyenela kudziimba mlandu, mwina kuganiza kuti Yehova sasangalala na utumiki wanu? Onani cimene Yehova amayang’ana pofuna kuona ngati ndife opambana pa nchito yolalikila. Iye amayang’ana kwambili pa kuyesetsa kwathu na kupilila kwathu. Iye amaona kuti nchito yathu yolalikila ikuyenda bwino, tikamaigwila mwakhama cifukwa com’konda, kaya anthu amvetsele kapena ayi. Paulo anati: “Mulungu si wosalungama woti angaiŵale nchito yanu ndi cikondi cimene munacisonyeza pa dzina lake, mwa kutumikila oyela ndipo mukupitiliza kuwatumikila.” (Aheb. 6:10) Yehova amayamikila khama lathu na cikondi cathu, olo kuti sipangakhale zotulukapo zabwino pa nchito yathu yolalikila. Conco, mawu amene Paulo anakamba omwe ni lemba la tsiku lalelo, ni olimbikitsa kwa inu. w21.10 25 ¶4-6

Sondo, July 16

Ciliconse cimene Atate adzandipatse cidzabwela kwa ine, ndipo wobwela kwa ine sindidzamukana.—Yoh. 6:37.

Kukoma mtima kwa Yesu na cikondi cake, zinaonekela bwino na mmene anali kucitila zinthu kwa ophunzila ake. Anadziŵa kuti maluso na mikhalidwe yawo pa umoyo zinali zosiyana. Iwo sanali na maudindo ofanana, komanso sakanacita zofanana mu ulaliki. Komabe, Yesu anali kuyamikila aliyense cifukwa cocita zimene akanatha. Fanizo la matalente lionetsa bwino khalidwe la Yesu limeneli. M’fanizo limenelo, mbuye anagaŵila kapolo aliyense nchito “malinga ndi luso lake.” Mmodzi wa akapolo aŵili akhama anapindula zambili kuposa mnzake. Koma mbuye wawo anayamikila onse aŵili na mawu ofanana akuti: “Wacita bwino kwambili, kapolo wabwino ndi wokhulupilika iwe!” (Mat. 25:14-23) Yesu amacita nafe zinthu mwacikondi komanso mokoma mtima. Amadziŵa kuti maluso na mikhalidwe ya anthu pa umoyo imasiyana, ndipo amayamikila tikacita zimene tingakwanitse. Tiyenela kutengela citsanzo ca Yesu pocita zinthu na ŵena. w21.07 23 ¶12-14

Mande, July 17

Sindingatambasule dzanja langa ndi kuukila mbuyanga. —1 Sam. 24:10.

Mfumu Davide anali kucitila ena cifundo. Mwacitsanzo, pamene Nabala munthu woipa mtima anakamba monyoza kwa asilikali a Davide, na kukana kuwapatsa zakudya, Davide anakalipa kwambili ndipo anaganiza zakuti akaphe Nabala, na onse a m’nyumba yake. Koma Abigayeli, mkazi wa Nabala, anali woleza mtima, ndipo anacitapo kanthu mwamsanga. Izi zinathandiza Davide kupewa kupalamula mlandu wa magazi. (1 Sam. 25:9-22, 32-35) Onani kuti cifukwa cokwiya, Davide anaganiza zakuti akaphe Nabala na a m’nyumba yake onse. Ndipo patapita nthawi, Davide anaweluza munthu wa m’fanizo la Natani kuti ayenela kuphedwa pa zimene anacita. Pa cocitika caciŵilici, tingadabwe kuti n’cifukwa ciani Davide anaweluza wakubayo mouma mtima conco. Ganizilani mmene anali kumvelela. Pa nthawiyo, Davide anali na cikumbumtima comuimba mlandu. Munthu akaweluza ena mopanda cifundo, zimaonetsa kuti sali pa ubale wabwino na Yehova. w21.10 12 ¶17-18; 13 ¶20

Ciŵili, July 18

Mukhale oyela, cifukwa ine ndine woyela.—1 Pet. 1:16.

Mawu a lemba la tsiku lalelo, aonetsa kuti n’zotheka kutengela Yehova, amene ni citsanzo cabwino koposa pa nkhani ya ciyelo. Conco, tifunika kukhala oyela m’makhalidwe athu onse. Koma izi zingaoneke zosatheka cifukwa ndife opanda ungwilo. Ngakhale mtumwi Petulo iye mwini analakwitsapo zinthu zina, koma citsanzo cake cionetsa kuti tingathe kukhala oyela. Anthu ambili amaganiza kuti munthu woyela, ni uja amene sasangalala konse, wovala zovala zacipembedzo, komanso nkhope yake yooneka yacifundo-cifundo. Koma zimenezi si zoona. Yehova, amene ni woyela, amafotokozedwa kuti ni “Mulungu wacimwemwe.” (1 Tim. 1:11) Anthu amene amamulambila amachedwa “odala.” (Sal. 144:15) Yesu anadzudzula anthu ovala zovala zapadela, komanso odzionetsela kuti ni olungama pamaso pa anthu. (Mat. 6:1; Maliko 12:38) Pokhala Akhristu, timadziŵa zimene kukhala woyela kumatanthauza cifukwa ca zimene timaphunzila m’Baibo. Timadziŵanso kuti Mulungu wathu wacikondi, sangatiuze kucita zinthu zimene sitingakwanitse. w21.12 2 ¶1, 3

Citatu, July 19

Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse.—Maliko 12:30.

Pa mphatso zonse zimene Mulungu anatipatsa mwa cisomo cake, mphatso imene imaposa zonsezo, mwina ni mphatso ya kumulambila. Timaonetsa kuti timamukonda Yehova ngati ‘tisunga malamulo ake.’ (1 Yoh. 5:3) Moimilako Atate wake, Yesu anatilamula kupanga ophunzila na kuŵabatiza. (Mat. 28:19) Iye anatilamulanso kuti tizikondana. (Yoh. 13:35) Anthu omvela, Yehova amawalandila m’banja la alambili ake a padziko lonse. (Sal. 15:1, 2 ) Onetsani cikondi kwa ena. Cikondi ndiye khalidwe lalikulu la Yehova. (1 Yoh. 4:8) Iye anationetsa cikondi tisanamudziŵe n’komwe. (1 Yoh. 4:9, 10) Timatengela citsanzo cake ngati tikonda ena. (Aef. 5:1) Njila yabwino koposa imene tingaonetsele kuti timakonda ena, ni kuwaphunzitsa za Yehova mapeto asanafike. (Mat. 9:36-38) Tikatelo, timawapatsa ciyembekezo codzakhala m’banja la Mulungu. w21.08 5-6 ¶13-14

Cinayi, July 20

Palibe amene ali ndi cikondi cacikulu kuposa [ici].—Yoh. 15:13.

Cikondi cacikulu cimene Yesu ali naco pa Yehova, cinamusonkhezela kutumikila Atate wake komanso ife. (Yoh. 14:31) Mmene iye anali kucitila zinthu na ŵanthu, zinaonetsa kukula kwa cikondi cake pa iwo. Tsiku lililonse, anali kuonetsa cikondi na cifundo, ngakhale pamene anthu anali kumutsutsa. Ndipo njila yaikulu imene anaonetsela cikondi cake pa anthu, ni kuwaphunzitsa za Ufumu wa Mulungu. (Luka 4:43, 44) Yesu anaonetsanso cikondi codzimana pa Mulungu komanso anthu, mwa kudzipeleka kuti akavutike komanso kuphedwa na anthu ocimwa. Mwa kutelo, iye anatsegula njila yakuti tonse tikapeze moyo wosatha. Tinadzipatulila na kubatizika cifukwa cokonda Atate wathu wakumwamba Yehova. Conco, mofanana na Yesu, tiyenela kuonetsa kuti timakonda Yehova mwa kukonda anthu anzathu. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Amene sakonda m’bale wake amene amamuona, sangakonde Mulungu amene sanamuonepo.”—1 Yoh. 4:20. w22.03 10 ¶8-9

Cisanu, July 21

Samalani kwambili kuti mmene mukuyendela si monga anthu opanda nzelu, koma ngati anzelu. Muzigwilitsa nchito bwino nthawi yanu.—Aef. 5:15, 16.

Ngakhale kuti timakondwela kuthela nthawi na Yehova, timakumana na zopinga. Timakhala umoyo wotangwanika, moti cimativuta kupeza nthawi yocita zauzimu. Nchito ya kuthupi, maudindo a m’banja, na zinthu zina, zingatidyele nthawi yathu cakuti tingamaone kuti tilibenso nthawi yopemphela, yoŵelenga, komanso yosinkhasinkha. Palinso cina cingatidyele nthawi yathu ife osadziŵa. Ngati sitingasamale, tingamacite zinthu zina zimene mwa izo zokha si zoipa. Koma zinthuzo zingatidyele nthawi yathu imene tikanaiseŵenzetsa kuyandikila kwambili Yehova. Mwacitsanzo, zosangalatsa. Tonsefe timapindula tikamapatula nthawi yosangulukako. Koma ngakhale zosangalatsa zoyenela zingatenge nthawi yathu yambili, cakuti n’kutsala na nthawi yocepa yocita zinthu zauzimu. Conco, tiziika zosangalatsa pa malo ake.—Miy. 25:27; 1 Tim. 4:8. w22.01 26 ¶2-3

Ciŵelu, July 22

Mlendo wokhala pakati panu muzimuona ngati mbadwa. Muzim’konda mmene mumadzikondela nokha.—Lev. 19:34.

Pamene Yehova anauza Aisiraeli kuti ayenela kukonda anzawo, sanatanthauze kuti azikonda cabe anthu a mtundu wawo okha. Iye anawauzanso kuti azikonda alendo okhala pakati pawo. Malangizo omveka bwino amenewa apezeka pa Levitiko 19:33, 34. Mlendo anayenela kuonedwa “ngati mbadwa,” ndipo Aisiraeli anayenela ‘kum’konda’ mmene anali kudzikondela okha. Mwacitsanzo, Aisiraeli anayenela kulola alendo komanso osauka kupindula na makonzedwe a kukunkha. (Lev. 19:9, 10) Mfundo yokamba za kukonda alendo igwilanso nchito kwa Akhristu masiku ano. (Luka 10:30-37) Motani? Pali anthu mamiliyoni amene anasamukila ku maiko ena, ndipo mwina ena a iwo amakhala kufupi na kwanu. N’kofunika kwambili kucita nawo zinthu mwaulemu anthu amenewo. w21.12 12 ¶16

Sondo, July 23

Ofuna-funa Yehova sadzasoŵa ciliconse cabwino.—Sal. 34:10.

Tikamadalila kwambili citsogozo ca Yehova pali pano, m’pamenenso tidzakulitsa cidalilo cathu cakuti iye adzatipulumutsa m’tsogolomu. Zimafuna cikhulupililo komanso kukhala okonzeka kudalila Yehova, kuti tipemphe abwana athu masiku akuti tikacite msonkhano wadela kapena wacigawo. Kapenanso kuwapempha kuti tiziweluka mwamsanga, n’colinga cakuti tikapezeke ku misonkhano yampingo na mu ulaliki. Bwanji ngati abwana akana pempho lathu, ndipo aticotsa nchito. Kodi timakhala na cikhulupililo kuti Yehova sadzatisiya kapena kutitaya, komanso kuti nthawi zonse adzatipatsa zofunikila pa umoyo? (Aheb. 13:5) Ambili amene ali mu utumiki wa nthawi zonse, angafotokozeko zocitika zoonetsa mmene Yehova anawathandizila pa nthawi zovuta kwambili. Kukamba zoona, iye ni wokhulupilika. Popeza Yehova ali kumbali yathu, palibe cifukwa coopela za kutsogolo. Mulungu wathu sadzatisiya m’pang’ono pomwe, malinga ngati tiika cifunilo cake patsogolo. w22.01 7 ¶16-17

Mande, July 24

Simukuweluzila munthu koma mukuweluzila Yehova.—2 Mbiri 19:6.

Kodi kukhulupilila kwathu akulu kungayesedwe motani? Tinene kuti munthu amene wacotsedwa ni bwenzi lathu la pamtima. Mwina tingaganize kuti akulu sanapende mfundo zonse zokhudza mlanduwo, kapena tingaone kuti iwo sanauweluze bwino kusiyana na mmene Yehova akanaweluzila. N’ciani cingatithandize kulemekeza cigamulo cimeneco? Tizikumbukila kuti kucotsa munthu mu mpingo ni makonzedwe a Yehova, ndipo amapindulitsa mpingo, ngakhale wolakwayo. Ngati munthu wosalapa aloledwa kukhalabe mu mpingo, khalidwe lake loipalo lingayambukile ena. (Agal. 5:9) Kuwonjezela apo, sangaone kukula kwa chimo lake. Ndiponso, sadzakhala na comulimbikitsa kuti awongolele maganizo ake na zocita zake kuti Yehova amuyanjenso. (Mlal. 8:11) Tisakaikile konse mfundo yakuti akulu satenga udindo wawo mopepuka akamapenda zakuti munthu ayenela kucotsedwa kapena ayi. w22.02 5-6 ¶13-14

Ciŵili, July 25

Bango lophwanyika sadzalisansantha ndipo nyale yofuka sadzaizimitsa.—Mat. 12:20.

Kuleza mtima ndiponso cifundo, n’zofunika kwambili maka-maka ngati wina poyamba akukana uphungu wozikika m’Baibo. Mkulu sayenela kukwiya kapena kukhumudwa ngati amene wapatsa uphungu sanaugwilitsile nchito. Popemphela payekha, mkulu angapemphe Yehova kuti athandize wopatsidwa uphungu kumvetsa cifukwa cake wapatsidwa uphunguwo, komanso kuti auseŵenzetse. Munthu amene wapatsidwa uphunguwo angafunikile nthawi kuti asinkhesinkhe zimene anauzidwa. Ngati mkulu apeleka uphungu modekha komanso mokoma mtima, cidzakhala cosavuta munthu kuulandila. Ndipo nthawi zonse uphungu uyenela kucokela m’Mawu a Mulungu. Tifuna kuti uphungu wathu ukhale wothandiza, komanso ‘wosangalatsa mtima.’—Miy. 27:9. w22.02 18 ¶17; 19 ¶19

Citatu, July 26

Cinthu cimene unali kuyembekeza cikalepheleka, cimadwalitsa mtima.—Miy. 13:12.

Tikapempha mphamvu zotithandiza kulimbana na ciyeso cina cake, kapena kugonjetsa cifooko cina cake, tingaone monga Yehova akutenga nthawi kuyankha pemphelo lathu. N’cifukwa ciani Yehova sayankha mapemphelo athu onse nthawi yomweyo? Iye amaona mapemphelo athu ocokela pansi pamtima monga umboni wakuti tili na cikhulupililo. (Aheb. 11:6) Yehova ali na cidwi coona ngati zocita zathu zigwilizana na mapemphelo athu, komanso ngati tikucita cifunilo cake. (1 Yoh. 3:22) Conco, tingafunike kukhala oleza mtima, na kucita zinthu mogwilizana na mapemphelo athu pamene tiyesetsa kuthetsa zizoloŵezi zoipa. Yesu anati mapemphelo athu ena sangayankhidwe mwamsanga. Iye anatilimbikitsa kuti: “Pemphanibe, ndipo adzakupatsani. Pitilizani kufunafuna, ndipo mudzapeza. Gogodanibe, ndipo adzakutsegulilani. Pakuti aliyense wopempha amalandila, aliyense wofunafuna amapeza, ndipo aliyense wogogoda adzamutsegulila.”—Mat. 7:7, 8. w21.08 8 ¶1; 10 ¶9-10

Cinayi, July 27

Ndimakonda kwambili cilamulo canu! Ndimasinkhasinkha cilamuloco tsiku lonse.—Sal. 119:97.

Kuti mulimbitse cikhulupililo canu mwa Mlengi, muyenela kupitiliza kuphunzila Mawu a Mulungu. (Yos. 1:8) Onani mmene maulosi a m’Baibo anakwanilitsidwila, komanso mmene mfundo za m’Baibo zimagwilizanila. Kucita zimenezi, kudzalimbitsa cikhulupililo canu cakuti Mlengi wathu wacikondi komanso wanzelu ndiye anatilenga, ndiponso kuti ndiye anauzila Baibo. (2 Tim. 3:14; 2 Pet. 1:21) Pamene muŵelenga Mawu a Mulungu, muziona mmene uphungu wake ungakuthandizileni. Mwacitsanzo, kale kwambili Baibo inaticenjeza kuti kukonda ndalama n’koipa, ndipo kumabweletsa “zopweteka zambili.” (1 Tim. 6:9, 10; Miy. 28:20; Mat. 6:24) Ndiye cifukwa cake, n’kothandiza ngako kumvela cenjezo la m’Baibo lakuti tipewe kukonda ndalama. Kodi mungaganizileko mfundo zina za m’Baibo zimene zakhala zothandiza? Tikaona mmene mfundo za m’Baibo zilili zothandiza, m’pamenenso tidzayamba kudalila kwambili malangizo anzelu a Mlengi wathu wacikondi. (Yak. 1:5) Zotulukapo n’zakuti, tidzakhala na umoyo wacimwemwe.—Yes. 48:17, 18. w21.08 17-18 ¶12-13

Cisanu, July 28

Pakuti Mulungu si wosalungama woti angaiŵale nchito yanu ndi cikondi cimene munacisonyeza pa dzina lake.—Aheb. 6:10.

Ngati mupita mukalamba, dziŵani kuti Yehova amakumbukila zonse zimene munam’citila m’mbuyomu. Mwakhala mukucilikiza nchito yolalikila mokangalika. Mwakhala mukupilila mayeso osiyana-siyana, kutsatila miyezo ya m’Baibo, kusamalila maudindo aakulu, komanso kuphunzitsa ena. Mwakhala mukuyendela pamodzi na gulu la Yehova limene lili pa liŵilo. Ndipo mwalimbikitsa amene ali mu utumiki wanthawi zonse. Yehova Mulungu amakukondani ngako cifukwa cokhala okhulupilika. Iye analonjeza kuti “sadzasiya anthu ake okhulupilika.” (Sal. 37:28) Analonjezanso kuti: “Munthu wa imvi ndimamunyamula nthawi zonse.” (Yes. 46:4) Conco, musadzione kukhala osafunika m’gulu la Yehova poona kuti lomba mwakalamba. Ndinu ofunikadi kwambili! w21.09 3 ¶4

Ciŵelu, July 29

Yehova wasonyezanso cifundo kwa onse omuopa.—Sal. 103:13.

Yehova amaonetsa cifundo cifukwa ni wanzelu zakuya. Baibo imati “nzelu yocokela kumwamba,” ni “yodzaza ndi cifundo ndi zipatso zabwino.” (Yak. 3:17) Monga kholo lacikondi, Yehova amadziŵa kuti cifundo cake cimapindulitsa ana ake. (Yes. 49:15) Cifundo ca Mulungu cimatipatsa ciyembekezo ca zakutsogolo olo kuti ndife opanda ungwilo. Conco, popeza Yehova ali na nzelu zakuya, amaticitila cifundo pakakhala cifukwa cocitila zimenezo. Pa nthawi imodzimodzi, iye amadziŵa pamene sangafunike kuonetsa cifundo. Pokhala wanzelu, saonetsa cifundo akaona kuti kucita zimenezo kungakhale kulekelela khalidwe loipa. Bwanji ngati mtumiki wa Mulungu mwadala wasankha kuyamba makhalidwe oipa. Tingacite ciani? Paulo mouzilidwa analemba kuti: ‘Lekani kuyanjana’ naye. (1 Akor. 5:11) Anthu ocita zoipa osalapa amacotsedwa mu mpingo. Kucita izi n’kofunikila kuti abale na alongo athu okhulupilika atetezedwe, komanso kumaonetsa kuti njila za Yehova n’zoyela. w21.10 9-10 ¶7-8

Sondo, July 30

Mulungu amakonda munthu wopeleka mokondwela. —2 Akor. 9:7.

Timalambila Yehova tikamacilikiza nchito ya Ufumu mwa zopeleka zathu. Aisiraeli sanaloledwe kukaonekela kwa Yehova cimanja-manja. (Deut. 16:16) Anayenela kupeleka mphatso malinga na mmene zinthu zinalili kwa iwo. Mwa kutelo, iwo anaonetsa ciyamikilo cawo pa makonzedwe amene anakhazikitsidwa kuti awapindulitse mwauzimu. Kodi tingaonetse bwanji kuti timam’konda Yehova, komanso kuti timayamikila zinthu zauzimu zimene timalandila? Njila imodzi ni kupanga copeleka cocilikiza mpingo wathu, komanso nchito ya padziko lonse mmene tingakwanitsile. Mtumwi Paulo anakamba kuti: “Mphatso yocokela pansi pa mtima ndi imene Mulungu amakondwela nayo, cifukwa Mulungu amafuna kuti munthu apeleke zimene angathe, osati zimene sangathe.” (2 Akor. 8:4, 12) Yehova amayamikila copeleka ciliconse cimene tingapange mocokela pansi pa mtima, kaya cikhale cocepa motani.—Maliko 12:42-44. w22.03 24 ¶13

Mande, July 31

Lankhulani molimbikitsa kwa amtima wacisoni, thandizani ofooka, khalani oleza mtima kwa onse.—1 Ates. 5:14.

Akulu, sangathetse mavuto onse amene anthu a Yehova amakumana nawo. Koma ngakhale n’telo, Yehova amafuna kuti akulu acite zimene angathe polimbikitsa nkhosa zake na kuziteteza. Kodi akulu otangwanika angapatule bwanji nthawi kuti athandize abale na alongo? Mwa kutengela citsanzo ca Paulo. Iye anali kufuna-funa mipata yoyamikila abale ake na kuwalimbikitsa. Akulu ayenela kutengela citsanzo cake mwa kuwaonetsa cikondi anthu a Yehova. (1 Ates. 2:7) Paulo anauza alambili anzake kuti iye komanso Yehova amawakonda. (2 Akor. 2:4; Aef. 2:4, 5) Iye anali kuwaona kuti ni mabwenzi ake, ndipo anali kuceza nawo. Anaonetsa kuti amawakhulupilila mwa kuwauza moona mtima nkhawa zake ndiponso zifooko zake. (2 Akor. 7:5; 1 Tim. 1:15) Komabe, sanali kungoganizila za mavuto ake. M’malo mwake, anali kufuna kuthandiza abale ake. w22.03 28 ¶9-10

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani