LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • es23 masa. 77-87
  • August

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • August
  • Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2023
  • Tumitu
  • Ciŵili, August 1
  • Citatu, August 2
  • Cinayi, August 3
  • Cisanu, August 4
  • Ciŵelu, August 5
  • Sondo, August 6
  • Mande, August 7
  • Ciŵili, August 8
  • Citatu, August 9
  • Cinayi, August 10
  • Cisanu, August 11
  • Ciŵelu, August 12
  • Sondo, August 13
  • Mande, August 14
  • Ciŵili, August 15
  • Citatu, August 16
  • Cinayi, August 17
  • Cisanu, August 18
  • Ciŵelu, August 19
  • Sondo, August 20
  • Mande, August 21
  • Ciŵili, August 22
  • Citatu, August 23
  • Cinayi, August 24
  • Cisanu, August 25
  • Ciŵelu, August 26
  • Sondo, August 27
  • Mande, August 28
  • Ciŵili, August 29
  • Citatu, August 30
  • Cinayi, August 31
Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2023
es23 masa. 77-87

August

Ciŵili, August 1

Atate, akhululukileni. —Luka 23:34.

Zioneka kuti Yesu anali kukamba asilikali aciroma amene anamukhomelela misomali m’manja mwake na m’mapazi ake. Yesu sanalole kuti zopanda cilungamo zimene anacitilidwa, zimupangitse kukalipa na kusunga mkwiyo. (1 Pet. 2:23) Mofanana na Yesu, tiyenela kukhala okonzeka kukhululukila ena. (Akol. 3:13) Anthu ena kuphatikizapo acibale athu, angatitsutse cifukwa samvetsetsa zimene timakhulupila komanso mmene timacitila zinthu mu umoyo wathu. Angatinenele mabodza, kuticitsa manyazi pamaso pa ena, kutiwonongela zofalitsa, kapena kutiopseza kuti adzativulaza. M’malo mosunga cakukhosi, tingapemphe Yehova kuti atsegule maso a anthu otitsutsawo, kuti tsiku lina akaphunzile coonadi. (Mat. 5:44, 45) Nthawi zina, kukhululuka kungakhale kovuta maka-maka ngati tinacitilidwa zinthu zoipa kwambili. Koma ngati tilola mkwiyo na kusunga cakukhosi kuzika mizu mu mtima mwathu, timadzivulaza tekha. (Sal. 37:8) Tikasankha kukhululuka, timapewa kukhalabe okwinyilila cifukwa ca zoipa zimene zinaticitikila.—Aef. 4:31, 32. w21.04 8-9 ¶3-4

Citatu, August 2

Iwo anali . . . kumukhumudwitsa kaŵili-kaŵili.—Sal. 78:40.

Kodi pali wa m’banja mwanu amene anacotsedwa mu mpingo? Izi zimakhala zomvetsa cisoni kwambili! Ganizilani cabe mmene cinamuŵaŵila Yehova, pamene angelo ena m’banja lake anam’pandukila. (Yuda 6) Ndipo ganizilaninso mmene cinamuŵaŵila kuona anthu ake okondeka, Aisiraeli, akum’pandukila mobweleza-bweleza. (Sal. 78:41) Dziŵani kuti Atate wathu wakumwamba, cimamupweteka wa m’banja lanu akaleka kum’tumikila. Iye amamvetsa cisoni cimene mumakhala naco. Ndipo mwacikondi adzakulimbikitsani na kukuthandizani. Mwana akacotsedwa mu mpingo, makolo amakonda kuganizila zina zimene akanacita, pothandiza mwanayo kukhalabe m’coonadi. M’bale wina anati: “N’nadziimba mlandu, ndipo n’nali kulota maloto oipa.” Mlongo wina amene nayenso anakumanapo na vutoli, anali kudzifunsa kuti: “Pokhala kholo, kodi n’nalakwitsa ciani? N’naona kuti n’nalephela kukhomeleza coonadi mwa mwana wanga.” w21.09 26 ¶1-2, 4

Cinayi, August 3

[Anazindikila] kuti anali anthu osaphunzila ndiponso anthu wamba.—Mac. 4:13.

Anthu ambili amaona kuti anthu a Mulungu sangaphunzitse Baibo cifukwa sanapite ku masukulu ochuka ophunzitsa za umulungu. Koma ayenela kupenda mosamala kuti adziŵe zoona zeni-zeni. Izi n’zimene wolemba Uthenga Wabwino Luka anatsimikiza kucita. Iye anayesetsa kufufuza “zinthu zonse mosamala kwambili kucokela pa ciyambi.” Anafuna kuti oŵelenga ‘adziŵe bwino-bwino kuti zinthu zimene’ anamvela zokhudza Yesu n’zodalilika. (Luka 1:1-4) Ayuda okhala mu mzinda wakale wa Bereya anali monga Luka. Iwo atamva uthenga wabwino wokhudza Yesu kwa nthawi yoyamba, anafufuza m’Malemba a Ciheberi kuti atsimikizile ngati zimene anali kuuzidwa zinalidi zoona. (Mac. 17:11) Mofananamo, anthu masiku ano ayenelanso kupenda mosamala kuti adziŵe zoona zeni-zeni. Ayenela kulinganiza zimene amaphunzitsidwa na anthu a Mulungu na zimene Malemba amakamba. Ayenelanso kuidziŵa bwino mbili yamakono ya anthu a Yehova. Akacita zimenezi, sadzalola tsankho kapena zokamba za anthu kuwacititsa khungu. w21.05 3 ¶7-8

Cisanu, August 4

Futukulani mtima wanu. —2 Akor. 6:13.

Kodi mu mpingo mwanu muli wina wake amene mungamuceleze? Akhristu anzathu angayamikile kwambili kuceza nawo maka-maka pa nthawi zina. Ena cingaŵavute kukhala na acibale awo osakhulupilila pa maholide azikondwelelo. Enanso angakhale acisoni kwambili maka-maka pa masiku ena monga, pa tsiku limene mnzawo wa m’cikwati anamwalila. Tikadzipeleka kuceza na abale na alongo amene ali na zopinga ngati zimenezi, timawaonetsa kuti ‘timasamaladi za iwo.’ (Afil. 2:20) Pali zifukwa zambili zimene zingapangitse Mkhristu kusungulumwa nthawi zina. Komabe, tisaiŵale kuti Yehova amadziŵa bwino mmene timamvelela tikasungulumwa. Nthawi zambili amatipatsa zimene timafunikila kupitila mwa Akhristu anzathu. (Mat. 12:48-50) Nafenso timaonetsa ciyamikilo cathu kwa Yehova pa makonzedwe ake acikondi, mwa kucita zonse zotheka pa kucilikiza banja lathu lauzimu. Mosasamala kanthu za mmene timamvelela nthawi zina, sitili tekha, cifukwa Yehova nthawi zonse ali nafe! w21.06 13 ¶18-20

Ciŵelu, August 5

Khalani ndi khalidwe labwino pakati pa anthu a m’dzikoli, kuti pamene akukunenelani monga anthu ocita zoipa, pa mapeto pake iwo pokhala mboni zimene zikuona ndi maso zocita zanu zabwino, adzatamande Mulungu.—1 Pet. 2:12.

Yesu anakhalabe na maganizo oyenela na kupitiliza kulalikila, ngakhale kuti ena anali kukana uthenga wake. Cifukwa ciani? Iye anali kudziŵa kuti anthu anafunikila kudziŵa coonadi, ndipo anafuna kupeleka mpata kwa anthu ambili kuti alandile uthenga wa Ufumu. Anadziŵanso kuti anthu amene poyamba anakana uthengawo, m’kupita kwa nthawi adzaulandila. Ganizilani zimene zinacitika m’banja lake leni-leni. Panthawi yonse imene Yesu anacita utumiki wake kwa zaka zitatu na hafu, palibe aliyense wa m’banja lake amene anakhala wophunzila wake. (Yoh. 7:5) Ngakhale n’telo, pambuyo pa kuukitsidwa kwake, iwo anakhala Akhristu. (Mac. 1:14) Sitidziŵa kuti ndani amene m’kupita kwa nthawi adzaphunzila coonadi ca m’Baibo cimene timaphunzitsa. Anthu ena, amatenga nthawi kusiyana na ena kuti alandile uthenga wathu. Ngakhale aja amene amasankha kusatimvetsela, amaona khalidwe lathu labwino, ndipo m’kupita kwa nthawi angayambe ‘kutamanda Mulungu.’ w21.05 18 ¶17-18

Sondo, August 6

Pitani ndi kulalikila kuti, “Ufumu wakumwamba wayandikila.” —Mat. 10:7.

Yesu ali padziko lapansi, anapatsa otsatila ake nchito ya mbali ziŵili. Anawauza kulalikila uthenga wabwino wa Ufumu, ndipo anawaonetsa mocitila mwake. (Luka 8:1) Mwacitsanzo, Yesu anauza ophunzila ake zimene anayenela kucita kaya anthu alandile uthenga wa Ufumu, kapena kuukana. (Luka 9:2-5) Iye anafotokozela otsatila ake za kukula kwa nchito yawo yolalikila, powauka kuti adzacitila “umboni ku mitundu yonse.” (Mat. 24:14; Mac. 1:8) Kuwonjezela apo, anauza otsatila ake kuti aphunzitse anthu oyenelela kusunga zinthu zonse zimene iye anawalamula. Yesu anaonetsa kuti nchito yofunika imeneyi inali kudzapitilizabe “mpaka m’nyengo ya mapeto a nthawi ino.” (Mat. 28:18-20) Ndipo m’masomphenya amene anaonetsa Yohane, Yesu anaonetsa bwino kuti ophunzila ake onse ayenela kuthandiza ena kuphunzila za Yehova.—Chiv. 22:17. w21.07 2-3 ¶3-4

Mande, August 7

Tisakhale odzikuza, oyambitsa mpikisano pakati pathu, ndi ocitilana kaduka.—Agal. 5:26.

Masiku ano, anthu ambili amacita zinthu mosonkhezeledwa na mzimu wampikisano. Mwacitsanzo, munthu wamalonda angacite zilizonse zowononga malonda a anzake kuti zake ziyende. Wocita maseŵela angavulaze mnzake mwadala pofuna kuti iye apambane maseŵelawo. Mwana wa sukulu angabele mayeso n’colinga cakuti apite ku yunivesiti. Pokhala Akhristu, timadziŵa kuti khalidwe limeneli n’loipa; lili m’gulu la “nchito za thupi.” (Agal. 5:19-21) Komabe, kodi zingatheke atumiki ena a Yehova kuyambitsa mzimu wampikisano mu mpingo mosazindikila? Limeneli ni funso lofunika kwambili cifukwa mzimu wampikisano ungasokoneze mgwilizano wa mpingo. Ndiye tingacite bwino kuganizila zitsanzo za amuna na akazi okhulupilika a nthawi za m’Baibo amene anapewa mzimu wampikisano. w21.07 14 ¶1-2

Ciŵili, August 8

Wodala ndi munthu amene amacita zinthu moganizila munthu wonyozeka. Pa tsiku la tsoka, Yehova adzamupulumutsa.—Sal. 41:1.

Cikondi cosasintha cimatilimbikitsa kuthandiza opsinjika maganizo. Abale na alongo okoma mtima, modzipeleka amathandiza ena mu mpingo amene ni opsinjika maganizo. Iwo amawakonda ngako abale na alongo awo, ndipo amacita zonse zotheka kuti awathandize. (Miy. 12:25; 24:10) Izi n’zimene mtumwi Paulo anatilimbikitsa kucita pamene anati: “Lankhulani molimbikitsa kwa amtima wacisoni, thandizani ofooka, khalani oleza mtima kwa onse.” (1 Ates. 5:14) Nthawi zambili, njila yabwino imene tingathandizile m’bale kapena mlongo wolefuka, ni kumumvetsela mwachelu, komanso kumutsimikizila kuti timam’konda. Yehova amaona zabwino zimene tingacitile nkhosa zake za mtengo wapatali. Miyambo 19:17 imati: “Wokomela mtima munthu wonyozeka akukongoza Yehova, ndipo adzam’bwezela zimene anacitazo.” w21.11 10 ¶11-12

Citatu, August 9

Talaŵani ndipo muone kuti Yehova ndi wabwino. Wodala ndi munthu wamphamvu amene amathaŵila kwa iye.—Sal. 34:8.

Tingacite ciani pali pano pokonzekela zam’tsogolo? Tizikhala okhutila komanso acimwemwe cifukwa cokhala pa ubale na Yehova. Tikafika pom’dziŵa bwino Mulungu wathu, m’pamenenso tidzakulitsa cidalilo cathu cakuti iye adzatiteteza pamene Gogi wa Magogi adzatiukila. Mawu a lemba la tsiku lalelo, amaonetsa cifukwa cake Davide anali kudalila thandizo la Yehova. Iye anali kudalila Yehova nthawi zonse, ndipo Mulungu wake sanamgwilitse mwala. Ali wacinyamata, Davide anayang’anizana na Goliyati, ciphona coopsa cacifilisiti, na kuciuza kuti: “Lelo Yehova akupeleka m’manja mwanga.” (1 Sam. 17:46) Pambuyo pake, Davide anayamba kutumikila mfumu Sauli, imene kangapo konse inafuna kumupha. Koma “Yehova anali ndi” Davide. (1 Sam. 18:12) Cifukwa coona mmene Yehova anam’thandizila m’mbuyomu, Davide anadziŵa kuti Mulungu adzam’thandizanso pa mayeso amene anali kukumana nawo. w22.01 6 ¶14-15

Cinayi, August 10

Ana onse a Mulungu anayamba kufuula ndi cisangalalo.—Yobu 38:7.

Pa zonse zimene amacita, Yehova moleza mtima amakhala na nthawi yokwanila kuti atsilize nchito yake. Amacita zimenezi kuti dzina lake lilemekezedwe, komanso kuti apindulitse anthu. Mwacitsanzo, ganizilani mmene Yehova mwapang’ono-pang’ono analengela dziko lapansi kuti anthu azikhalamo. Pofotokoza za dziko lapansi, Baibo imakamba kuti iye “anaika miyezo yake, “maziko ake,” komanso “mwala wake wapakona.” (Yobu 38:5, 6) Iye anatenganso nthawi yoyang’ana zinthu zimene analenga. (Gen. 1:10, 12) Ganizilani mmene angelo anamvelela atayamba kuona zinthu zimene Yehova anali kulenga. Iwo ayenela kuti anakondwela ngako na zimenezi! Ndipo pa nthawi ina, iwo “anayamba kufuula ndi cisangalalo.” Kodi tiphunzilaponji pamenepa? Tiphunzilapo kuti Yehova anatenga zaka masauzande kuti atsilize kulenga zinthu zonse. Ndipo atayang’ana zonse zimene analenga mwaluso, iye anaona kuti “zinali zabwino kwambili.”—Gen. 1:31. w21.08 9 ¶6-7

Cisanu, August 11

Wacita bwino kwambili, kapolo wabwino ndi wokhulupilika iwe!—Mat. 25:23.

M’fanizo la Yesu la matalente, munthu wina anafuna kupita pa ulendo. Asananyamuke, iye anaitana akapolo ake na kuwapatsa matalente kuti acitile malonda. Podziŵa zimene akapolo akewo angakwanitse kucita, iye anapatsa kapolo woyamba matalente asanu, waciŵili anam’patsa aŵili, ndipo wacitatu anam’patsa imodzi. Akapolo aŵili anagwila nchito molimbika kuti aculukitse ndalama za mbuye wawo. Koma kapolo wacitatu sanacite nayo ciliconse ndalama imene anapatsidwa, ndipo mbuye wake anam’cotsa nchito. Kapolo woyamba komanso waciŵili, anaona nchito imene anapatsidwa kukhala yofunika ngako, ndipo anaigwila molimbika kuti apindulitse mbuye wake. Zotulukapo n’zakuti iye anapindula matalente enanso aŵili a mbuye wake. Kapolo ameneyo anafupidwa cifukwa cogwila nchito molimbika. Mbuye wake anakondwela kwambili cakuti anam’patsa maudindo owonjezeleka. w21.08 21 ¶7; 22 ¶9-10

Ciŵelu, August 12

Ndigwedezanso kumwamba, [na] dziko lapansi.—Hag. 2:6.

Yehova waonetsa kuleza mtima kwakukulu masiku ano otsiliza. Iye safuna kuti wina aliyense akawonongedwe. (2 Pet. 3:9) Wapatsa anthu onse nthawi yakuti alape. Koma kuleza mtima kwake kuli na polekezela. Amene amakana mwayi umenewu mapeto awo adzafanana monga a Farao m’nthawi ya Mose. Yehova anauza Farao kuti: “Pofika pano ndikanatambasula kale dzanja langa ndi kukupha ndi mlili, iweyo ndi anthu ako, kukufafanizani padziko lapansi. Koma ndakusiya ndi moyo kuti ndikusonyeze mphamvu zanga, ndi kuti dzina langa lilengezedwe padziko lonse lapansi.” (Eks. 9:15, 16) Mitundu yonse nayonso idzadziŵa kuti Yehova ndiye Mulungu yekha woona. (Ezek. 38:23) Kugwedeza kochulidwa mu lemba la tsiku lalelo, kukutanthauza ciwonongeko camuyaya kwa aja amene, mofanana na Farao, amakana kuvomeleza kuti Yehova ndiye woyenela kulamulila. w21.09 18-19 ¶17-18

Sondo, August 13

Sangalalani ndi anthu amene akusangalala. Lilani ndi anthu amene akulila.—Aroma 12:15.

Kodi cimakupwetekani mtima ngati munthu amene mumakonda anacotsedwa mu mpingo? Nanga bwanji ngati ena mu mpingo akamba zinthu zongowonjezela cisoni canu? Kukamba zoona, si onse angakambe zinthu zolimbikitsa. (Yak. 3:2) Tonsefe ndife opanda ungwilo. Conco, musadabwe ngati wina wasoŵa conena, kapena mosadziŵa wakamba zinthu zimene zakukwiyitsani. Kumbukilani malangizo a mtumwi Paulo akuti: “Pitilizani kulolelana ndi kukhululukilana ndi mtima wonse, ngati wina ali ndi cifukwa codandaulila.” (Akol. 3:13) Pitilizani kuthandiza okhulupilika m’banjalo. Iwo afunikila cikondi na cilimbikitso canu kuposa kale lonse. (Aheb. 10:24, 25) Nthawi zina, zacitikapo kuti a m’banja la munthu wocotsedwa amasalidwa monga kuti nawonso ni ocotsedwa. Koma tisalole zimenezi kucitika. Ana amene makolo awo anasiya coonadi, ndiwo afunikila kwambili kuwalimbikitsa na kuwayamikila. w21.09 29 ¶13-14; 30 ¶16

Mande, August 14

Munthu wanzelu amamvetsela ndi kuphunzila malangizo owonjezeleka.—Miy. 1:5.

Okalamba akamaceza na acicepele, onse amapindula. (Aroma 1:12) Acicepele adzakulitsa ciyamiko cawo pa Yehova poona mmene amasamalila atumiki ake okhulupilika, ndipo okalamba adzaona kuti amakondewa. Iwo adzakondwela kwambili kukusimbilankoni mmene Yehova waadalitsila. Kukongola kwa kuthupi kumatha munthu akamakula, koma anthu okhulupilika kwa Yehova, amakongolelako m’kupita kwa zaka. (1 Ates. 1:2, 3) N’cifukwa ciani zili conco? Cifukwa kwa zaka, iwo alola mzimu wa Mulungu kuwaumba, na kuŵathandiza kukulitsa makhalidwe abwino. Tikafika powadziŵa bwino okalamba athu okondedwa, kuwalemekeza, na kuphunzila kwa iwo, m’pamenenso tiziŵaona kuti ni cuma camtengo wapatali. Mpingo umalimbilako ngati nawonso okalamba amaona acicepele kuti ni ofunika. w21.09 7 ¶15-18

Ciŵili, August 15

Lekani kuweluza ena kuti inunso musaweluzidwe, pakuti ciweluzo cimene mukuweluza naco ena inunso mudzaweluzidwa naco.—Mat. 7:1, 2.

Tizipewa kucita zinthu mouma mtima, tiziyesetsa kukhala ‘acifundo cacikulu,’ potengela citsanzo ca Mulungu wathu. (Aef. 2:4) Cifundo si mmene munthu amamvelela cabe mumtima. Munthu wacifundo amathandiza ena. Conco, tonsefe tizikhala chelu kuti tione anthu amene tingathandize, kaya ni m’banja mwathu, mu mpingo, kapena m’dela lathu. Kukamba zoona, pali njila zambili za mmene tingaonetsele cifundo. Kodi pali amene akufunikila thandizo? Mungamuthandize mwina mwa kum’patsa cakudya kapena kum’citila cinthu cina cabwino. Kodi Mkhristu amene anabwezedwa mu mpingo akufunikila anzake abwino omulimbikitsa? Kodi tingauzeko ena uthenga wabwino wotonthoza? (Yobu 29:12, 13; Aroma 10:14, 15; Yak. 1:27) Tikamakhala chelu kuti tione amene akufunikila thandizo, tidzaona kuti pali mipata yambili yowaonetsela cifundo. Tikamacitila anthu cifundo, timakondweletsa Atate wathu wakumwamba, amene ni Mulungu “wacifundo cacikulu.” w21.10 13 ¶20-22

Citatu, August 16

Yehova ndi M’busa wanga. Sindidzasoŵa kanthu.—Sal. 23:1.

Mu Salimo 23, Davide anachula zinthu zokhalitsa, zimene ni madalitso oculuka auzimu amene analandila cifukwa colola Yehova kukhala M’busa wake. Yehova anam’tsogolela “m’tinjila tacilungamo,” ndipo iye anacilikiza Davide mokhulupilika pa nthawi zabwino komanso zovuta. Davide anadziŵa kuti umoyo wake “m’mabusa a msipu wambili” a Yehova udzakhala na mavuto. Nthawi zina, iye anali kulefulidwa, monga kuti akuyenda “m’cigwa ca mdima wandiweyani,” komanso kuti adzakhala na adani. Koma cifukwa Yehova anali M’busa wake, Davide ‘sanaope kanthu.’ Kodi Davide ‘sanasoŵe ciliconse’ m’lingalilo lotani? Mwauzimu tingakambe kuti, iye anali na zonse zofunikila. Cimwemwe cake sicinadalile zinthu zakuthupi. Davide anakhutila na zimene Yehova anam’patsa. Cinali cofunika ngako kwa iye cinali madalitso na citetezo ca Mulungu wake. Malinga na mawu a Davide, tiona kuti n’kofunika kwambili kukhala na maganizo oyenela pa zinthu zakuthupi. w22.01 3-4 ¶5-7

Cinayi, August 17

Aliyense payekha adzalandila mphoto yake mogwilizana ndi nchito yake.—1 Akor. 3:8.

Atumiki a Yehova akale naonso anali kulalikila anthu amene sanali kufuna kumvetsela. Mwacitsanzo, Nowa anali “mlaliki wa cilungamo,” ndipo ayenela kuti analalikila kwa zaka zambili. (2 Pet. 2:5) Mosakaika konse, iye anali na cikhulupililo cakuti ena adzamvetsela uthenga wake. Koma Yehova sanamuuze zilizonse zoonetsa kuti anthu adzamvetsela kapena ayi. M’malo mwake, pouza Nowa kuti akhome cingalawa, Mulungu anati: “Udzaloŵe m’cingalawaco limodzi ndi ana ako, mkazi wako, ndi akazi a ana ako.” (Gen. 6:18) Poona kuti ni anthu ocepa cabe angakwane m’cingalawa cimene Mulungu anamuuza kukhoma, Nowa ayenela kuti anazindikila kuti si onse adzamvetsela. (Gen. 6:15) Ndipo monga tidziŵila, palibe ngakhale mmodzi m’dziko loipalo amene anamvetsela uthenga wa Nowa. (Gen. 7:7) Kodi Yehova anaona Nowa kukhala wolephela? Kutalitali! Mulungu anaona Nowa kukhala mlaliki wopambana, cifukwa anacita mokhulupilika zonse zimene Yehova anamuuza.—Gen. 6:22. w21.10 26 ¶10-11

Cisanu, August 18

Ndinali ndi zonse pocoka kuno, koma Yehova wandibweza wopanda kanthu.—Rute 1:21.

Tangoganizilani mmene Rute anamvelela, atamvela mawu amenewa! Rute anacita zonse zotheka kuti athandize Naomi. Anali kulila naye, kumutonthoza, ndipo anakhala naye kwa nthawi yaitali. Ngakhale zinali conco, Naomi anati: “Yehova wandibweza wopanda kanthu.” Zimene Naomi anakamba zinaonetsa monga kuti sanayamikile thandizo la Rute, amene anaima pafupi naye. Mawu amenewa ayenela kuti anamupweteka mtima Rute. Ngakhale n’telo, iye anamamatilabe kwa Naomi. (Rute 1:3-18) Mlongo wopsinjika maganizo mwina angakambe zinthu zimene zingatikhumudwitse, ngakhale titacita zonse zotheka kuti tim’thandize. Koma ife tisakhumudwe. Tisamusiye mlongo wathuyo amene akufunikila thandizo, ndipo tipemphe Yehova kuti atithandize kupeza njila imene tingamutonthozele. (Miy. 17:17) Mlongo amene akufunikila thandizo, poyamba angakane thandizo lathu. Komabe, cifukwa comuonetsa cikondi cosasintha, tidzamamatilabe kwa iye.—Agal. 6:2. w21.11 11 ¶17-19

Ciŵelu, August 19

Khalani oyela m’makhalidwe anu onse.—1 Pet. 1:15.

M’Baibo, mawu akuti “ciyelo” amatanthauza kukhala na makhalidwe oyela aumulungu kapena kukhala wopatulika. Mawuwa angatanthauzenso kudzipatulila kuti utumikile Mulungu. M’mawu ena tingati, timakhala oyela ngati tili na makhalidwe abwino, timalambila Yehova m’njila yovomelezeka, komanso ngati tili pa ubale wabwino na Mulungu. Timacita cidwi kwambili tikaona kuti Yehova, amene ni woyela koposa, amafuna kuti tikhalebe mabwenzi ake, olo kuti ndife opanda ungwilo. Yehova ni woyela m’njila zake zonse. Timadziŵa zimenezi tikaona zimene aserafi, amene ni angelo okhala pafupi na mpando wacifumu wa Mulungu anakamba. Ena a iwo analengeza kuti: “Woyela, woyela, woyela ndiye Yehova wa makamu.” (Yes. 6:3) Komabe, kuti angelo akhale pa ubale wolimba na Mulungu, ayenela kukhala oyela, ndipo ni mmene alili. w21.12 3 ¶4-5

Sondo, August 20

Samalani kwambili kuti mmene mukuyendela si monga anthu opanda nzelu, koma ngati anzelu. Muzigwilitsa nchito bwino nthawi yanu.—Aef. 5:15, 16.

Kambili, acinyamata amadela nkhawa mmene angaseŵenzetsele umoyo wawo m’njila yabwino koposa. Aphunzitsi awo kusukulu komanso acibale awo amene si Mboni, angawalimbikitse kucita maphunzilo a pamwamba kuti akapeze nchito yabwino. Kucita maphunzilowo kungawadyele nthawi yawo yoculuka. Kumbali ina, makolo komanso abale na alongo mu mpingo, angalimbikitse acinyamata kuseŵenzetsa umoyo wawo mu utumiki wa Yehova. N’ciani cingathandize wacinyamata amene amakonda Yehova kupanga cisankho cabwino koposa? Iye angapindule kwambili akaŵelenga Aefeso 5:15-17 na kuisinkhasinkha. Pambuyo poŵelenga mavesiwa, wacinyamata angadzifunse kuti: ‘Kodi “cifunilo ca Yehova” n’ciani? N’cisankho cotani cingamusangalatse? N’cisankho citi cidzanithandiza kuseŵenzetsa bwino nthawi yanga?’ Kumbukilani kuti “masikuwa ndi oipa,” ndipo dzikoli lolamulidwa na Satana lidzatha posacedwa. w22.01 27 ¶5

Mande, August 21

Abale akewo sanali kumukhulupilila.—Yoh. 7:5.

Kodi Yakobo anakhala liti wotsatila wa Yesu wokhulupilika? Yesu ataukitsidwa, “anaonekela kwa Yakobo, kenakonso kwa atumwi onse.” (1 Akor. 15:7) Ataonana na Yesu, m’pamene Yakobo anasinthila umoyo wake. Iye analipo pamene atumwi anali kuyembekezela kulandila mzimu woyela m’cipinda cam’mwamba ku Yerusalemu. (Mac. 1:13, 14) Patapita nthawi, Yakobo anayamba kutumikila m’bungwe lolamulila la m’zaka za zana loyamba. (Mac. 15:6, 13-22; Agal. 2:9) Ndipo cisanafike caka ca 62 C.E., iye anauzilidwa kulemba kalata kwa Akhristu odzozedwa. Kalatayo imatipindulila nafenso masiku ano, kaya ciyembekezo cathu n’cakumwamba kapena padziko lapansi. (Yak. 1:1) Malinga n’zimene wolemba mbili yakale, dzina lake Josephus anakamba, Yakobo anaphedwa mocita kulamulidwa na Mkulu wa Ansembe dzina lake Hananiya. Yakobo anakhalabe wokhulupilika kwa Yehova mpaka mapeto a moyo wake padziko lapansi. w22.01 8 ¶3; 9 ¶5

Ciŵili, August 22

Mulungu wanga, Mulungu wanga, mwandisiyilanji ine? —Mat. 27:46.

Phunzilo limodzi limene tingatengemo m’lemba la tsiku lalelo n’lakuti tisamayembekezele kuti Yehova azitichinga ku mavuto oyesa cikhulupililo cathu. Monga mmene Yesu anayesedwela mpaka imfa, nafenso tifunika kukhala okonzeka kufela cikhulupililo cathu, ngati pangafunike kutelo. (Mat. 16:24, 25) Komabe, tili na cidalilo cakuti Mulungu sangalole kuti tiyesedwe mpaka kufika pamene sitingathe kupilila. (1 Akor. 10:13) Phunzilo lina n’lakuti, mofanana na Yesu, nafenso tingavutike ngakhale kuti sitinalakwe ciliconse. (1 Pet. 2:19, 20) Anthu amene amatitsutsa amacita zimenezo osati cifukwa cakuti talakwitsa zina zake, koma cifukwa cakuti sitili mbali ya dziko ndipo timacitila umboni za coonadi. (Yoh. 17:14; 1 Pet. 4:15, 16) Yesu anali kudziŵa cifukwa cake Yehova analola kuti iye avutike. Atumiki a Yehova nthawi zina samvetsa cifukwa cake Yehova walola kuti iwo akumane na mayeso ena ake. (Hab. 1:3) Mulungu wathu woleza mtima ndiponso wacifundo, amadziŵa kuti anthu otelo sikuti alibe cikhulupililo. Iwo amafunika citonthozo cimene iye angapeleke.—2 Akor. 1:3, 4. w21.04 11 ¶9-10

Citatu, August 23

Pemphelo langa likhale lokonzedwa ngati zofukiza pamaso panu. —Sal. 141:2.

Yehova adzavomeleza kulambila kwawo malinga ngati n’kogwilizana na colinga cake, komanso ngati kukucitika cifukwa comukonda na kumulemekeza. Tidziŵa kuti iye ni woyenela kum’lambila, komanso timafuna kuti tizimulambila m’njila yabwino koposa. Imodzi mwa njila zimene timalambilila Yehova, ni pamene tipemphela kwa iye. Malemba amayelekezela mapemphelo athu na nsembe zofukiza zimene zinali kupelekedwa pa cihema, komanso patapita nthawi, pa kacisi. Zofukiza zimenezo zinali kukondweletsa mtima wa Mulungu. Mofananamo, mapemphelo athu ocokela pansi pa mtima ‘amamusangalatsa’ Mulungu, ngakhale pamene taseŵenzetsa mawu wamba osavuta. (Miy. 15:8; Deut. 33:10) Yehova amakondwela kumva mawu athu oonetsa kuti timam’konda na kumuyamikila. Iye amafuna kuti tizimuuza nkhawa zathu, komanso zimene timafuna. Musanayambe kupemphela kwa Yehova, bwanji osaganizila mofatsa zimene mudzakamba m’pemphelo? Mukatelo, mudzapeleka ‘nsembe yofukiza’ yabwino koposa kwa Atate wanu wakumwamba. w22.03 20 ¶2; 21 ¶7

Cinayi, August 24

Pa nthawi imene Ambuye Yesu adzaonekele kucokela kumwamba limodzi ndi angelo ake amphamvu m’moto walawilawi, inuyo amene panopo mukuvutika mudzapeza mpumulo pamodzi nafe.—2 Ates. 1:7.

Pa Aramagedo, sudzakhala udindo wathu kusankha amene ayenela kucitilidwa cifundo na Yehova kapena kuwonongedwa. (Mat. 25:34, 41, 46) Nthawiyo ikadzafika, kodi tidzalemekeza ciweluzo ca Yehova, kapena kodi tidzaleka kum’tumikila cifukwa cosagwilizana na ciweluzo cake? Kunena zoona, ino ndiyo nthawi yolimbitsa cikhulupililo cathu mwa Yehova, kuti m’tsogolomu tikam’khulupilile kwathunthu. Ganizilani mmene tidzamvelela kukhala m’dziko latsopano la Mulungu. Cipembedzo conyenga, mabungwe a zamalonda adyela, komanso maboma andale amene amapondeleza anthu na kubweletsa mavuto ambili, sizidzakhalakonso. Matenda, ukalamba, na imfa, zidzacotsedwapo. Ndipo Satana na ziŵanda zake adzamangidwa zaka 1,000. Mavuto onse amene iwo abweletsa cifukwa ca kupanduka kwawo adzathetsedwa. (Chiv. 20:2, 3) Tidzakondwela ngako kuti tinakhulupilila mmene Yehova amacitila zinthu! w22.02 6-7 ¶16-17

Cisanu, August 25

Odala ndi anthu amene amabweletsa mtendele.—Mat. 5:9.

Yesu anali kuyamba ndiye kukhazikitsa mtendele, ndipo anali kulimbikitsa ena kuthetsa kusamvana pakati pawo. Anaphunzitsa anthu kuti ayenela kukhazikitsa mtendele na m’bale wawo, ngati afuna kuti Yehova alandile kulambila kwawo. (Mat. 5:23, 24) Ndipo mobweleza-bweleza, anathandiza atumwi kuthetsa mkangano pa nkhani yakuti ndani anali wamkulu pakati pawo. (Luka 9:46-48; 22:24-27) Kuti tikhale munthu wobweletsa mtendele, pali cina cimene tiyenela kucita kuposa cabe kungopewa kuyambitsa mikangano. Tiyenela kuyamba ndife kukhazikitsa mtendele, komanso kulimbikitsa abale na alongo athu kuthetsa kusamvana pakati pawo. (Afil. 4:2, 3; Yak. 3:17, 18) Tingadzifunse kuti: ‘Kodi ndine wokonzeka kudzimana zinthu zina kuti nikhazikitse mtendele na ena? M’bale kapena mlongo akanikhumudwitsa, kodi nimasunga cakukhosi? Kodi nimayembekezela kuti wina abwele kudzakhazikitsa mtendele, kapena nimayamba ndine kucita zimenezo, olo pamene iye akuoneka kuti ndiye wolakwa? w22.03 10 ¶10-11

Ciŵelu, August 26

Kupatsa kumabweletsa cimwemwe coculuka kuposa kulandila. —Mac. 20:35.

Kale kwambili, Baibo inakambilatu kuti anthu a Mulungu “adzadzipeleka mofunitsitsa” kuti atumikile Yehova motsogoleledwa na Mwana wake. (Sal. 110:3) Ulosi umenewo ukukwanilitsika masiku ano. Caka ciliconse, atumiki a Yehova okangalika amataila maola mamiliyoni ambili-mbili pa nchito yolalikila. Amacita zimenezi mwa kufuna kwawo, ndipo salipilidwa kalikonse. Iwo amapatulanso nthawi yothandiza Akhristu anzawo kuthupi, kuuzimu, komanso kuwalimbikitsa. Abale a paudindo amathela maola osaŵelengeka pokonzekela nkhani zokakamba ku mpingo, komanso pocita maulendo aubusa kwa abale na alongo. N’ciani cimawalimbikitsa kugwila nchito zonsezi? Cikondi. Inde, cikondi pa Yehova komanso pa anthu anzawo. (Mat. 22:37-39) Yesu anapeleka citsanzo cabwino koposa pa nkhani yoika zofunikila za ena patsogolo pa zofunikila zake. Timayesetsa mmene tingathele kutsatila mapazi ake. (Aroma 15:1-3) Amene amatengela citsanzo cake adzapindula kwambili. w22.02 20 ¶1-2

Sondo, August 27

Malipilo a munthu waganyu asagone m’nyumba mwako kufikila m’mawa.—Lev. 19:13.

Mu Isiraeli, munthu wogwila nchito yaganyu m’munda anali kupatsidwa malipilo ake pakutha kwa tsiku. Kusamulipila wanchito wotelo, kukanapangitsa kuti asoŵe ndalama zosamalila banja lake pa tsikulo. Yehova anati: “Iye ndi wovutika. [Ndipo] akuyembekezela malipilo akewo mwacidwi.” (Deut. 24:14, 15; Mat. 20:8) Masiku ano, anchito ambili amalandila malipilo awo kamodzi kapena kaŵili pa mwezi, osati tsiku lililonse. Komabe, mfundo ya pa Levitiko 19:13 ikali kugwilabe nchito. Mabwana ena amadyela masuku pa mutu anchito awo mwa kuwalandilitsa ndalama yocepa yosayendelana na nchito imene amagwila. Iwo amadziŵa kuti anchito awo kulibe kumene angapite, koma azigwilabe nchitoyo ngakhale alandile malipilo ocepa. M’mawu ena tingati, mabwana otelo ‘akugoneka malipilo a anchito awo.’ Mkhristu amene amalemba anthu nchito ayenela kukumbukila mfundo imeneyi. w21.12 10 ¶9-10

Mande, August 28

Ndikumva ludzu.—Yoh. 19:28.

Yesu ayenela kuti anali na ludzu kwambili cifukwa ca mavuto onse amene anapitamo. Anafunika thandizo kuti athetse ludzu lake. Yesu sanaganize kuti akafotokoza mmene anali kumvelela adzaoneka kuti ni wofooka. Nafenso sitiyenela kuganiza conco. Nthawi zambili, sitikonda kuuza ena zosoŵa zathu. Koma ngati taona kuti tikufunikila thandizo la wina, tisazengeleze kupempha ena kuti atithandize. Mwacitsanzo, ngati ndimwe wokalamba kapena wolemala, mungapemphe mnzanu kukupelekankoni ku sitolo kapena ku cipatala. Ngati tapsinjika maganizo kapena kulefuka, tingafunike kupempha mkulu kapena mnzathu wokhwima kuuzimu kuti atimvetsele kapena kutiuzako “mawu abwino” amene angatisangalatse. (Miy. 12:25) Tisaiŵale kuti abale na alongo athu amatikonda, ndipo amafuna kutithandiza “pakagwa mavuto.” (Miy. 17:17) Koma iwo sangadziŵe zimene tiganiza. Conco sangadziŵe kuti tifunikila thandizo ngati sitinawauze. w21.04 11-12 ¶11-12

Ciŵili, August 29

Ukafooka pa tsiku la masautso, mphamvu zako zidzakhala zocepa.—Miy. 24:10.

Zinthu zikasintha pa umoyo wathu, cimakhala covuta kwa ambili a ife kucilandila. Ena amene akhala mu utumiki wanthawi zonse wapadela, utumiki wawo wasintha. Cifukwa ca ukalamba, enanso asiya utumiki umene amaukonda. N’cibadwa kusakondwela ngati masinthidwe a conco nafenso atikhudza. Kuona zinthu mmene Yehova amazionela kungatithandize kuzolowela kusintha kumeneko. Iye akucita zinthu zazikulu masiku ano, ndipo tili na mwayi wapadela wokhala anchito anzake. (1 Akor. 3:9) Cikondi ca Yehova pa ife sicisintha. Conco, ngati masinthidwe a m’gulu akukhudzani inuyo panokha, pewani kumangokhalila kuganizila zifukwa zimene anapangila masinthidwewo. M’malo moyewa masiku ‘akale,’ mwapemphelo onani zabwino pa masinthidwewo. (Mlal. 7:10) Khalani na maganizo oyenela. Tikatelo, tidzakhalabe acimwemwe komanso okhulupilika, ngakhale pamene zinthu zasintha. w22.03 17 ¶11-12

Citatu, August 30

Yehova, Yehova, Mulungu . . . wosungila mibadwo masauzande kukoma mtima kosatha.—Eks. 34:6, 7.

Kodi Yehova amaonetsa ndani cikondi cosasintha? Baibo imakamba kuti tingakonde zinthu zambili monga “ulimi,” “vinyo na mafuta,” “cidzudzulo,” “cidziŵitso,” “nzelu”—kungochulako zocepa cabe. (2 Mbiri 26:10; Miy. 12:1; 21:17; 29:3) Komabe, cikondi cosasintha sitingacionetse ku zinthu, koma kwa anthu okha basi. Yehova saonetsa cikondi cosasintha kwa aliyense, koma amacionetsa kwa anthu amene ali naye pa ubale wolimba. Mulungu wathu ni wokhulupilika kwa mabwenzi ake. Iye ali nawo na colinga cabwino, ndipo sadzaleka kuwakonda. Yehova anaonetsa cikondi kwa anthu onse. Yesu anauza Nikodemo kuti: “Mulungu anakonda kwambili dziko [kutanthauza mtundu wa anthu] mwakuti anapeleka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupilila iye asawonongeke, koma akhale ndi moyo wosatha.”—Yoh. 3:1, 16; Mat. 5:44, 45. w21.11 2 ¶3; 3 ¶6-7

Cinayi, August 31

Ngati inu mudzapilile, mudzapeza moyo.—Luka 21:19.

Umoyo m’dzikoli ni wovuta kwambili, ndipo mwina m’tsogolomu tidzakumana na mavuto aakulu kwambili. (Mat. 24:21) Tiyembekezela mwacidwi nthawi pamene zinthu zonsezi zidzakhala zakale—sitidzazikumbukilanso ndipo sizidzacitikanso! (Yes. 65:16, 17) N’zoonekelatu kuti tiyenela kupitiliza kupilila. Cifukwa ciani? Cifukwa Yesu anati: “Ngati inu mudzapilile, mudzapeza moyo.” (Luka 21:19) Tikaganizila za ena amene amatha kupilila mayeso ngati athu, ifenso tidzakwanitsa kupilila. Kodi ndani ali citsanzo cabwino koposa pa nkhani ya kupilila? Yehova Mulungu. Kodi yankho ili mwadabwa nalo? N’kutheka. Koma mukaliganizila bwino mungamvetse cifukwa cake. Dzikoli likulamulidwa na Mdyelekezi, ndipo ni lodzala na mavuto. Yehova ngati afuna angaliwononge dzikoli mosavuta, koma akuyembekezela nthawi yoikika kutsogolo kuti akacite zimenezi. (Aroma 9:22) Pali pano, Mulungu wathu akupitilizabe kupilila mpaka pamene nthawi yoikidwilatu idzafike. w21.07 8 ¶2-4

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani