LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • es23 masa. 88-97
  • September

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • September
  • Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2023
  • Tumitu
  • Cisanu, September 1
  • Ciŵelu, September 2
  • Sondo, September 3
  • Mande, September 4
  • Ciŵili, September 5
  • Citatu, September 6
  • Cinayi, September 7
  • Cisanu, September 8
  • Ciŵelu, September 9
  • Sondo, September 10
  • Mande, September 11
  • Ciŵili, September 12
  • Citatu, September 13
  • Cinayi, September 14
  • Cisanu, September 15
  • Ciŵelu, September 16
  • Sondo, September 17
  • Mande, September 18
  • Ciŵili, September 19
  • Citatu, September 20
  • Cinayi, September 21
  • Cisanu, September 22
  • Ciŵelu, September 23
  • Sondo, September 24
  • Mande, September 25
  • Ciŵili, September 26
  • Citatu, September 27
  • Cinayi, September 28
  • Cisanu, September 29
  • Ciŵelu, September 30
Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2023
es23 masa. 88-97

September

Cisanu, September 1

Anam’pempha kuti awaonetse cizindikilo cocokela kumwamba.—Mat. 16:1.

Anthu ena m’nthawi ya Yesu sanakhutile na ziphunzitso zake zocititsa cidwi. Iwo anali kufuna zowonjezeleka. Koma pamene iye anakana kuwapatsa cizindikilo cimene anali kufuna, anthuwo anapunthwa. (Mat. 16:4) Kodi Malemba amati ciani? Ponena za Mesiya, mneneli Yesaya analemba kuti: “Iye sadzafuula kapena kukweza mawu ake, ndipo mawu ake sadzamvedwa mumsewu.” (Yes. 42:1, 2) Yesu anali kucita utumiki wake modzicepetsa osati modzionetsela. Iye sanamange akacisi odzionetsela ndipo sanavale zovala zapamwamba zacipembedzo kapena kulamula kuti anthu azimuchula na maina audindo a cipembedzo. Pamene Yesu anali kuzengedwa mlandu kuti aphedwe, iye anakana kukondweletsa Mfumu Herode mwa kumuonetsa cizindikilo. (Luka 23:8-11) Yesu anali kucita zozizwitsa. Koma colinga cake cacikulu cinali kulalikila uthenga wabwino. Iye anauza ophunzila ake kuti: “[Ici] ndico colinga cimene ndinabwelela.”—Maliko 1:38. w21.05 4 ¶9-10

Ciŵelu, September 2

Pakuti moyo wosatha adzaupeza akamaphunzila ndi kudziŵa za inu, Mulungu yekhayo amene ali woona, ndi za Yesu Khristu, amene inu munamutuma.—Yoh. 17:3.

Timafuna-funa awo ‘amene anali ndi maganizo abwino amene angawathandize kukapeza moyo wosatha.’ (Mac. 13:48) Kuti tithandize anthu amenewo kukhala ophunzila a Yesu, tiyenela kuŵathandiza (1) kumvetsa, (2) kuvomeleza, komanso (3) kuseŵenzetsa zimene akuphunzila m’Baibo. (Akol. 2:6, 7; 1 Ates. 2:13) Onse mu mpingo angathandize ophunzila Baibo atsopano amenewa mwa kuwaonetsa cikondi, komanso kuwalandila mwacimwemwe akabwela ku misonkhano. (Yoh. 13:35) Mphunzitsi wa Baibo angafunikenso kuthela nthawi yoculuka komanso kucita khama pothandiza wophunzila kusiya zikhulupililo kapena miyambo ‘yozikika molimba.’ (2 Akor. 10:4, 5) Zingatenga miyezi yambili kuti muthandize munthu kupanga masinthidwe amenewo kuti akakwanilitse colinga cake ca kubatizika. Ndipo m’pake kupanga masinthidwe amenewa. w21.07 3 ¶6

Sondo, September 3

Tsimikizilani zinthu zonse. Gwilani mwamphamvu cimene cili cabwino.—1 Ates. 5:21.

Kodi timakhulupililadi mu mtima mwathu kuti ife a Mboni za Yehova timaphunzitsa coonadi, komanso kuti timalambila Yehova m’njila imene iye amavomeleza? Mtumwi Paulo anali kukhulupilila kuti anali na coonadi. (1 Ates. 1:5) Koma sanakhulupilile zimenezi cabe cifukwa cokondwela na coonadi. Paulo anali kuphunzila mawu a Mulungu mwakhama. Anali kukhulupilila kuti “Malemba onse anauzilidwa ndi Mulungu.” (2 Tim. 3:16) Kodi anaphunzila zotani? Paulo anapeza umboni wosatsutsika m’Malemba wakuti Yesu anali Mesiya wolonjezedwa, umboni umene atsogoleli acipembedzo aciyuda anaukana. Atsogoleli amenewo anali kunena kuti amaphunzitsa coonadi ponena za Mulungu, koma anali kumukana mwa zocita zawo. (Tito 1:16) Mosiyana na iwo, Paulo sanasankhe zinthu zimene ayenela kukhulupilila m’Mawu a Mulungu. Iye anali wokonzeka kuphunzitsa na kucita “cifunilo conse ca Mulungu.”—Mac. 20:27. w21.10 18 ¶1-2

Mande, September 4

Palibe munthu angabwele kwa ine akapanda kukokedwa ndi Atate amene anandituma ine.—Yoh. 6:44.

Pamene tibyala na kuthilila, tiyenela kukumbukila kuti Mulungu ndiye amakulitsa. (1 Akor. 3:6, 7) Yehova amaona kuti moyo wa anthu onse ni wamtengo wapatali. Iye watipatsa mwayi woseŵenzela pamodzi na Mwana wake, posonkhanitsa anthu a mitundu yonse mapeto a dongosolo lino asanafike. (Hag. 2:7) Nchito yathu yolalikila tingaiyelekezele na nchito yopulumutsa anthu. Ndipo zili monga kuti ife tili m’gulu limene latumidwa kukapulumutsa anthu amene atsekeledwa pamgodi. Ngakhale kuti ni anthu ocepa cabe ogwila nchito za pamgodi amene angapezeke amoyo, nchito yopulumutsa anthu imene onsewo agwila ni yofunika kwambili. N’cimodzimodzinso na nchito yathu yolalikila. Sitidziŵa kuti ni anthu angati amene adzapulumutsidwa ku dongosolo la Satana. Koma Yehova angaseŵenzetse aliyense wa ife powathandiza. M’bale Andreas wa ku Bolivia ananena kuti, “Nikaona kuti munthu waphunzila coonadi ca m’Baibo ndipo wabatizika, nimadziŵa kuti siinali nchito ya munthu mmodzi.” Tiyeni tipitilize kukhala na maganizo amenewa pa utumiki wathu. Tikacita zimenezi, Yehova adzatidalitsa, ndipo utumiki wathu udzakhala gwelo la cimwemwe ceni-ceni. w21.05 19 ¶19-20

Ciŵili, September 5

[Wonjokani] mumsampha wa Mdyerekezi.—2 Tim. 2:26.

Colinga ca nkhumbalume kapena kuti wosaka nyama cimakhala cimodzi, cimene ni kugwila kapena kupha nyama. Iye angaseŵenzetse misampha yosiyana-siyana, ngakhale imene anafotokoza mmodzi wa anzake acinyengo a Yobu. (Yobu 18:8-10) Kodi nkhumbalume angaipusitse bwanji nyama kuti aikole mu msampha wake? Coyamba, amafuna kuidziŵa bwino nyamayo. Kodi imakonda kupita kuti? Imakonda ciani? Nanga ni msampha uti umene ungaigwile mosazindikila? Satana ali ngati nkhumbalume wotelo. Coyamba amafuna atidziŵe bwino. Amaona kumene timakonda kupita ndiponso zokonda zathu. Ndiyeno amachela msampha umene amaona kuti ungatikole mosazindikila. Ngakhale n’telo, Baibo imatitsimikizila kuti ngakhale titagwidwa mu msampha wake tingathe kuwonjoka. Imatiphunzitsanso mmene tingapewele misampha imeneyi. Misampha iŵili yamphamvu kwambili ya Satana, ni kunyada, komanso dyela. Kwa zaka masauzande, Satana wakhala akuseŵenzetsa makhalidwe oipa amenewa monga misampha yabwino kwambili. Ali monga wosaka mbalame amene amakopela mbalame mu msampha wake, kapena mu ukonde. (Sal. 91:3) Koma sitiyenela kugwidwa na Satana. Cifukwa ciani? Cifukwa Yehova wativumbulila macenjela amene Satana amaseŵenzetsa.—2 Akor. 2:11. w21.06 14 ¶1-2

Citatu, September 6

Imvi ndizo cisoti cacifumu ca ulemelelo zikapezeka m’njila yachilungamo.—Miy. 16:31.

Okalamba okhulupilika, ni cuma camtengo wapatali. Mawu a Mulungu amayelekezela imvi za okalamba amenewa na cisoti cacifumu. (Miy. 20:29) Komabe, tingayambe kuona okalamba kukhala osafunika. Acicepele amene amaona okalamba kuti ni ofunika, amapeza cinthu camtengo wapatali kuposa cuma cakuthupi. Okalamba okhulupilika ni amtengo wapatali kwa Yehova Mulungu. Iye amaona umunthu wawo wamkati, ndipo amayamikila makhalidwe awo abwino. Amayamikilanso ngati iwo agaŵilako acicepele cidziŵitso cimene akhala naco, pa zaka zonse zimene akhala akutumikila Mulungu mokhulupilika. (Yobu 12:12; Miy. 1:1-4) Yehova amayamikilanso kupilila kwawo. (Mal. 3:16) Olo kuti akhala akukumana na mavuto, cikhulupililo cawo mwa Yehova sicinagwedezeke. Ciyembekezo cawo ca zakutsogolo calimbilako kuposa mmene cinalili atangophunzila coonadi. Ndipo Yehova amawakonda cifukwa copitiliza kulengeza za dzina lake ngakhale pa ukalamba wawo.—Sal. 92:12-15. w21.09 2 ¶2-3

Cinayi, September 7

Aliyense payekha ayese nchito yake, kuti aone kuti ndi yotani. Akatelo adzakhala ndi cifukwa cosangalalila ndi nchito yake.—Agal. 6:4.

Nthawi na nthawi, ni bwino kumapenda zolinga zathu. Tingadzifunse kuti: ‘Kodi nimadziona kuti nimaposa ena? Kodi nimagwila nchito molimbika mu mpingo cifukwa cofuna kukhala woposa ena? Kapena nimagwila nchito molimbika cifukwa cofuna kupatsa Yehova zabwino koposa?’ Baibo imatiuza kuti sitiyenela kudziyelekezela na ena. Cifukwa ciani? Cifukwa ngati timaona kuti ndife oposa abale athu tingakhale onyada. Ndipo ngati timakonda kudziyelekezela na ena, tingalefuke. (Aroma 12:3) Tizikumbukila kuti Yehova anatikokela kwa iye, osati cifukwa cakuti ndife okongola, odziŵa kulankhula bwino, kapena cifukwa cokondedwa na anthu ambili, koma cifukwa timam’konda komanso kumvela Mwana wake.—Yoh. 6:44; 1 Akor. 1:26-31. w21.07 14-15 ¶3-4

Cisanu, September 8

Munaphunzitsidwa kuti mukhale atsopano mu mphamvu yoyendetsa maganizo anu.—Aef. 4:23.

Kuti tikhale atsopano mu mphamvu yoyendetsa maganizo athu, tiyenela kupemphela, kuŵelenga Mawu a Mulungu, na kusinkhasinkha. Conco pitilizani kucita zimenezi, ndipo muzipempha Yehova kuti akupatseni nyonga. Mzimu wake woyela udzakuthandizani kuthetsa cizolowezi canu codzilinganiza na ŵena. Yehova adzakuthandizani kuzindikila ngati mwayamba mzimu wa kaduka na kudzikuza. Adzakuthandizaninso kuwazula mwamsanga makhalidwe oipa amenewa. (2 Mbiri 6:29, 30) Yehova amadziŵa za mu mtima mwathu. Amadziŵanso kuti timalimbana na mzimu wa dziko komanso zophophonya zathu. Iye akamationa tikuyesetsa kugwebana na zoipa ngati zimenezi, cikondi cake pa ife cimakulilako. Yehova potionetsa kuti amatikonda kwambili, amagwilitsa nchito citsanzo ca mmene mayi amakondela mwana wake. (Yes. 49:15) N’zolimbikitsa cotani nanga kudziŵa kuti Yehova amatikonda kwambili akationa tikulimbana na zoipa kuti tim’tumikile na mtima wonse! w21.07 24-25 ¶17-19

Ciŵelu, September 9

Sangalalani ndi anthu amene akusangalala.—Aroma 12:15.

Tingawonjezele cimwemwe cathu ngati tiikilapo mtima pa nchito iliyonse imene tingapatsidwe m’gulu la Yehova. Muzikhala ‘otanganidwa kwambili’ na nchito yolalikila, komanso kutengako mbali mokwanila pa zocitika za pa mpingo. (Mac. 18:5; Aheb. 10:24, 25) Muzikonzekelanso bwino misonkhano kuti mukapelekepo ndemanga zolimbikitsa. Musamaione mopepuka mbali ya wophunzila imene angakupatseni pa misonkhano ya mkati mwa mlungu. Akakupemphani kugwila nchito inayake mu mpingo, osazengeleza ndipo khalani wodalilika. Musamatenge mopepuka nchito iliyonse imene mungapatsidwe, moti n’kungoicita mwa mwambo cabe. Muziyesetsa kukulitsa maluso anu. (Miy. 22:29) Mukamaikilapo mtima pa zinthu zauzimu komanso pa nchito zina, mudzapita patsogolo mofulumila, ndipo mudzakhala na cimwemwe cowilikiza. (Agal. 6:4) Cina, cidzakhala copepuka kukondwela na ena amene alandila utumiki umene inu munali kuufuna.—Agal. 5:26. w21.08 22 ¶11

Sondo, September 10

Nzelu yocokela kumwamba, coyamba, ndi yoyela, kenako yamtendele, yololela, yokonzeka kumvela, yodzaza ndi cifundo ndi zipatso zabwino, yopanda tsankho, ndiponso yopanda cinyengo.—Yak. 3:17.

Tipewe kunyada, ndipo tizikhala ophunzitsika. Monga mmene matenda angalimbitsile mitsempha ya ku mtima wathu na kuulepheletsa kugunda bwino, kunyada nakonso kungalimbitse mtima wathu wophiphilitsa, na kutilepheletsa kumvela malangizo a Yehova. Afarisi anaumitsa mitima yawo moti anakana kuona umboni wosatsutsika wovumbulidwa na mzimu woyela wa Mulungu. (Yoh. 12:37-40) Iyi ni khalidwe loipa kwambili cifukwa linawatsekela mwayi wokalandila moyo wosatha. (Mat. 23:13, 33) Conco, n’kofunika kwambili kupitiliza kulola Mawu a Mulungu na mzimu wake kuumba umunthu wathu, komanso kusonkhezela maganizo athu na zocita zathu. Cifukwa Yakobo anali wodzicepetsa, analola Yehova kuti amuphunzitse. Ndipo kudzicepetsa kwake kunam’thandiza kukhala mphunzitsi waluso. w22.01 10 ¶7

Mande, September 11

Pemphanibe. —Mat. 7:7.

Pamene ‘tilimbikila kupemphela,’ tingakhale na cidalilo cakuti Atate wathu wakumwamba adzamvetsela. (Akol. 4:2) Olo kuti pangatenge nthawi kuti mapemphelo athu ayankhidwe, Yehova analonjeza kuti adzatiyankha “pa nthawi imene tikufunika thandizo.” (Aheb. 4:16) Ndiye cifukwa cake, sitiyenela kuimba Yehova mlandu ngati zimene tinali kuyembekezela, sizinacitike mwamsanga mmene tinali kuganizila. Mwacitsanzo, kwa zaka zambili anthu oculuka akhala akupemphela kuti Ufumu wa Mulungu uwononge dongosolo loipali. Ndipo izi n’zimene Yesu anatiuza kucita. (Mat. 6:10) Koma kungakhale kupusa munthu kutaya cikhulupililo cake mwa Mulungu, cabe cifukwa mapeto sanafike pa nthawi imene anthu anali kuganizila. (Hab. 2:3; Mat. 24:44) Conco, n’canzelu kupitiliza kuyembekezela pa Yehova, komanso kupemphela kwa iye mwa cikhulupililo. Mapeto adzafika pa nthawi yake yoikidwilatu, cifukwa Yehova anasankha kale ‘tsiku na ola’ pamene mapeto adzafika. Ndipo tsikulo lidzakhala nthawi yoyenelela kwa anthu onse.—Mat. 24:36; 2 Pet. 3:15. w21.08 10 ¶10-11

Ciŵili, September 12

Modzicepetsa, [muziona] ena kukhala okuposani.—Afil. 2:3.

Okalamba odzicepetsa amadziŵa kuti malinga na msinkhu wawo, sangakwanitse kucita zambili mmene anali kucitila kale. Mwacitsanzo, ganizilani za oyang’anila madela. Akafika zaka 70, amapemphedwa kukacita utumiki wina. Koma izi zimakhala zovuta, cifukwa amakonda kwambili kutumikila abale awo. Komabe, iwo amadziŵa kuti cingakhale bwino kuti abale acinyamata agwile nchito imeneyi. Akatelo, amaonetsa mzimu umene Alevi anali nawo m’nthawi ya Aisiraeli. Aleviwo akafika zaka 50, anali kutula pansi udindo wawo wotumikila pa cihema. Utumiki umene Alevi acikulilewo anali kucita si ndiwo anali maziko a cimwemwe cawo. Iwo anali kucita utumiki uliwonse umene apatsidwa mokangalika, komanso kucita zimene angathe pophunzitsa acinyamata nchito. (Num. 8:25, 26) Mofananamo, abale amene kale anali oyang’anila madela, olo kuti lomba sacezela mipingo, ni dalitso ku mipingo yawo. w21.09 8-9 ¶3-4

Citatu, September 13

Bambo, ndacimwila kumwamba komanso ndacimwila inu. Sindilinso woyenela kuchedwa mwana wanu.—Luka 15:21.

Yesu anafotokoza fanizo logwila mtima la mwana woloŵelela, lopezeka pa Luka 15:11-32. Mwanayo anapandukila atate ake na kucoka pa nyumba, ndipo anapita “kudziko lina lakutali.” Kumeneko, iye anayamba makhalidwe oipa. Koma pamene zinthu zinayamba kumuthina, anazindikila kuti anapanga cisankho colakwika. Anazindikilanso kuti ku nyumba kwa atate ake anali kukhala umoyo wabwino kwambili. Yesu anati mwanayo “nzelu zitam’bwelela,” anaganiza zobwelela ku nyumba na kukapempha cikhululukilo kwa atate ake. Mwanayo anacita bwino ngako kuzindikila kuti anapanga cisankho coipa. Iye anayenela kucitapo kanthu! Mwana woloŵelela anaonetsa kuti analapadi mocokela pansi pamtima pa zimene anacita. Fanizoli si nthano cabe yogwila mtima. Koma lingathandize akulu mu mpingo kudziŵa ngati m’bale kapena mlongo amene anacita chimo lalikulu walapadi zenizeni. w21.10 5 ¶14-15

Cinayi, September 14

Ndigwedeza mitundu yonse ya anthu.—Hag. 2:7.

N’ciani cimene sicidzagwedezeka kapena kucotsedwa? Mtumwi Paulo analemba kuti: “Poona kuti tidzalandila Ufumu umene sungagwedezeke, tiyeni tipitilize . . . [kucitila] Mulungu utumiki wopatulika m’njila yovomelezeka, ndipo tiucite moopa Mulungu komanso mwaulemu waukulu.” (Aheb. 12:28) Kugwedeza kotsiliza kukadzatha, ni Ufumu wa Mulungu wokha umene udzakhalapo. (Sal. 110:5, 6; Dan. 2:44) Ino si nthawi yocita zengelezu! Anthu ayenela asankhe, kaya kupitiliza na moyo umene dzikoli limalimbikitsa, wopita ku ciwonongeko, kapena kutumikila Yehova na makhalidwe awo kuti akapeze moyo wamuyaya. (Aheb. 12:25) Mwa nchito yathu yolalikila, tingathandize anthu kupanga cisankho pa nkhani yofunika kwambili imeneyi. Ndipo nthawi zonse tizikumbukila mawu a Ambuye Yesu akuti: “Uthenga wabwino uwu wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika.”—Mat. 24:14. w21.09 19 ¶19-20

Cisanu, September 15

Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono.—Aheb. 13:5.

Imwe akulu, ni udindo wanu kutonthoza alambili anzanu amene wokondedwa wawo wasiya Yehova. (1 Ates. 5:14) Muziwalimbikitsa misonkhano isanayambe komanso ikatha. Muziwayendelako na kupemphela nawo pamodzi. Cina, muzilalikila nawo, komanso kuwaitanilako pa kulambila kwanu kwa pabanja. Abusa auzimu ayenela kuonetsa cifundo na cikondi ku nkhosa ya Yehova imene ili na cisoni. (1 Ates. 2:7, 8) Yehova “safuna kuti wina aliyense adzawonongedwe, koma amafuna kuti anthu onse alape.” (2 Pet. 3:9) Ngakhale munthu acite chimo lalikulu bwanji, moyo wake umakhalabe wamtengo wapatali kwa Mulungu. Kumbukilani kuti Yehova analipila mtengo wapamwamba kwambili, umene ni nsembe ya dipo la Mwana wake wokondeka, kaamba ka miyoyo ya anthu ocimwa. Mwacifundo, Yehova amayesa kuthandiza anthu amene amusiya kubwelela kwa iye. Iye amayembekezela kuti anthuwo adzabwelela kwa iye, monga mmene fanizo la Yesu la mwana wolowelela limaonetsela.—Luka 15:11-32. w21.09 30-31 ¶17-19

Ciŵelu, September 16

Mwaloŵa kukapindula ndi nchito imene iwo anaigwila mwamphamvu.—Yoh. 4:38.

Bwanji ngati simukwanitsa kutengako mbali mokwanila pa nchito yolalikila na kupanga ophunzila, cifukwa ca matenda kapena thanzi lofooka? Mungakhalebe acimwemwe pa zimene mumakwanitsa kucita pa nchito yokolola. Ganizilani za Mfumu Davide. Pa nthawi ina, iye pamodzi na asilikali ake anapulumutsa mabanja awo na katundu wawo kwa Aamaleki. Koma asilikali ena 200 sanapite nawo ku nkhondo cifukwa anali olema kwambili. Conco, iwo anatsala kuti azilonda katundu. Atapambana nkhondoyo, Davide analamula kuti zinthu zimene anafunkha zigaŵidwe mofanana kwa aliyense. (1 Sam. 30:21-25) Izi n’zofanana na nchito yathu yopanga ophunzila ya padziko lonse. Conco, aliyense akacita zonse zotheka pa nchitoyi, tonse tidzakhala na cimwemwe cofanana pothandiza munthu kudziŵa Yehova, na kuyamba kuyenda pa njila ya ku moyo. Yehova amaona kuyesetsa kwathu na zolinga zathu zabwino, ndipo amatidalitsa. Amatiphunzitsanso mmene tingapezele cimwemwe pa nchito yaikulu yokolola. (Yoh. 14:12) Conco, tingakhale otsimikiza kuti Yehova amakondwela nafe malinga ngati sitifooka. w21.10 28 ¶15-17

Sondo, September 17

Kukongola kwa anyamata ndiko mphamvu zawo.—Miy. 20:29.

Pamene tipita tikalamba, tingayambe kuona kuti Yehova sangatiseŵenzetse poyelekezela na mmene zinalili tikali acinyamata. N’zoona kuti mphamvu n’zocepekela, koma tingagwilitsile nchito nzelu na cidziŵitso cimene tili naco, pothandiza acinyamata kufikapo mwauzimu kuti asamalile maudindo ena. Okalamba ayenela kukhala odzicepetsa pothandiza acinyamata. Munthu wodzicepetsa amaona ena kukhala omuposa. (Afil. 2:3, 4) Okalamba odzicepetsa amadziŵa kuti pali njila zambili za mogwilila nchito, zimene zimagwilizana na Malemba. Paja amati pali njila zambili zophela khoswe. Conco, okalamba sayembekezela kuti aliyense azicita zinthu mmene iwo anali kucitila kale. (Mlal. 7:10) Olo kuti ali na cidziŵitso cokulilapo cimene angagaŵileko acinyamata, iwo amadziŵa kuti “zocitika za padzikoli zikusintha,” komanso kuti angafunike kuphunzila njila zatsopano za mocitila zinthu.—1 Akor. 7:31. w21.09 8 ¶1, 3

Mande, September 18

Ndi mulungu wina uti amene angafanane nanu, inu Yehova? Ndinu woyela kopambana, ndani angafanane ndi inu?—Eks. 15:11.

Yehova salola alambili ake kucita ciliconse codetsa. Iye ni gwelo la ciyelo. Izi zinaonekela bwino pa mawu amene analembedwa pa kacitsulo kagolide pa nduwila ya mkulu wa ansembe. Pa kacitsuloko panali polemba kuti, “Ciyelo n’ca Yehova.” (Eks. 28:36-38) Uthenga wolembedwa pa kacitsuloko, unatsimikizila aliyense kuti Yehova alidi woyela. Nanga bwanji za Mwisiraeli amene sakanakwanitsa kuona kacitsuloko, cifukwa analibe mwayi woyandikila mkulu wa ansembe? Kodi akanauphonya uthenga wofunika umenewo? Ayi! Mwisiraeli aliyense anamvela uthengawo pamene Cilamulo cinali kuŵelengedwa kwa amuna, akazi, na ŵana. (Deut. 31:9-12) Mukanakhalako panthawiyo, mukanamvela mawu aya akuti: “Ine ndine Yehova Mulungu wanu . . . Muzikhala oyela, cifukwa ine ndine woyela.” “Mukhale oyela kwa ine, cifukwa ine Yehova ndine woyela.”—Lev. 11:44, 45; 20:7, 26. w21.12 3 ¶6-7

Ciŵili, September 19

Siyani kuvutika mumtima. —Luka 12:29.

Ena amadela nkhawa zofunikila zakuthupi cifukwa angamakhale m’dziko limene muli mavuto azacuma. Conco, cingakhale covuta kwa iwo kupeza ndalama zokwanila zosamalila banja lawo. Kapena wosamalila banjalo angamwalile, n’kusiya banja lonse pamavuto popanda wolisamalila. M’malo modela nkhawa za mavuto athu, tiyenela kudalila Yehova. Kumbukilani kuti Yehova, analonjeza kuti adzatisamalila pa zakuthupi tikaika zauzimu patsogolo. (Mat. 6:32, 33) Iye nthawi zonse amakwanilitsa lonjezo lake limeneli. (Deut. 8:4, 15, 16; Sal. 37:25) Ngati Yehova amasamalila mbalame na maluŵa, palibe cifukwa codela nkhawa za cakudya kapena zovala. (Mat. 6:26-30; Afil. 4:6, 7) Monga mmene cikondi cimasonkhezela makolo kupezela ana awo zofunikila zakuthupi, nayenso Atate wathu wakumwamba cikondi cimam’sonkhezela kusamalila anthu ake mwakuthupi. w21.12 17 ¶4-5; 18 ¶8

Citatu, September 20

Yehova anapitilizabe kukhala ndi Yosefe ndi kumusonyeza kukoma mtima kosatha. —Gen. 39:21.

Kodi munthu wina, kapena Mkhristu mnzanu anakucitilamponi colakwa coŵaŵa kwambili? Ganizilani za Yosefe amene anacitilidwa zopanda cilungamo na abale ake enieni. Iye anasumika maganizo pa utumiki wake kwa Yehova, amene anamudalitsa kwambili cifukwa ca kupilila moleza mtima. M’kupita kwanthawi, Yosefe anakhululukila amene anamulakwila, ndipo Yehova anamudalitsa kwambili. (Gen. 45:5) Mofanana na Yosefe, nafenso tingatonthozedwe ngati tayandikila Yehova, na kuyembekezela kuti adzathetsa zopanda cilungamo zimene ena angaticitile. (Sal. 7:17; 73:28) Ngati mukupilila zopanda cilungamo kapena zinthu zina, dziŵani kuti Yehova ali pafupi na “anthu a mtima wosweka.” (Sal. 34:18) Amakukondani cifukwa ca kuleza mtima kwanu, komanso pomutulila nkhawa zanu. (Sal. 55:22) Iye ni woweluza wa dziko lonse lapansi. Amaona zonse zimene zikucitika. (1 Pet. 3:12) Ngati mukumana na mavuto amene simungawathetse, kodi mudzayembekezela Yehova moleza mtima? w21.08 11 ¶14; 12 ¶16

Cinayi, September 21

Pitilizani kuzindikila cifunilo ca Yehova.—Aef. 5:17.

N’canzelu kuseŵenzetsa umoyo wathu m’njila imene idzapangitsa kuti Yehova atiyanje. Tiyenela kuika zofunika patsogolo. Nthawi zina, kugwilitsa nchito bwino nthawi yathu kumafuna kusankha pakati pa zinthu ziŵili zimene pa izo zokha zilibe vuto. Nkhani yodziŵika bwino yokamba za Yesu atapita ku nyumba ya Mariya na Marita, imaonetsa bwino mfundo imeneyi. Marita anakondwela ngako kulandila Yesu monga mlendo wake, ndipo anayamba kuphika zakudya zambili. Koma Mariya m’bale wake anakhala pafupi na Mbuye wake, kuti amvetsela pamene anali kuphunzitsa. Kuphika kumene Marita anacita kunalibe vuto ayi, koma Yesu anati Mariya “wasankha cinthu cabwino kwambili.” (Luka 10:38-42) Patapita nthawi, n’kutheka kuti Mariya anaiŵala zakudya zimene zinaphikidwa pa nthawiyo, koma tingakhale otsimikiza kuti sanaiŵale zimene anaphunzila kwa Yesu. Mariya anaona nthawi imene anali na Yesu kukhala yamtengo wapatali. Nafenso timaona nthawi imene timathela na Yehova kukhala yamtengo wapatali. w22.01 27 ¶5-6

Cisanu, September 22

Kodi waona mmene Ahabu wadzicepetsela pamaso panga? —1 Maf. 21:29.

Ngakhale kuti Ahabu anadzicepetsa pamaso pa Yehova, zimene anacita pambuyo pake zinaonetsa kuti sanalape kwenikweni. Iye sanathetse kulambila Baala mu ufumu wake. Komanso sanalimbikitse anthu kulambila Yehova. Ahabu atafa, Yehova anaonetsa mmene anali kuonela munthuyu. Mneneli wa Mulungu Yehu, anati Ahabu anali munthu ‘woipa.’ (2 Mbiri 19:1, 2) Ganizilani izi: Ngati Ahabu anali atalapadi na mtima wonse, mneneliyo sakanamuchula kukhala munthu woipa wodana na Yehova. N’zoonekelatu kuti ngakhale kuti Ahabu anamva kuipa na zocita zake, iye sanalape mocokela pansi pa mtima. Tiphunzilapo ciani pa nkhani ya Ahabu? Poyamba, Ahabu anadzicepetsa pamene anamva uthenga wa Eliya wokamba za cilango cimene banja lake lidzalandila. Ici cinali ciyambi cabwino. Koma zimene anacita pambuyo pake zinaonetsa kuti iye sanalape mocokela pansi pamtima. Conco, kulapa kwenikweni si kungomvela cisoni pa zimene unacita. w21.10 3 ¶4-5, 7-8

Ciŵelu, September 23

Uthenga wabwino uwu wa Ufumu udzalalikidwa. —Mat. 24:14.

Yesaya anali mneneli, ndipo n’kutheka kuti nayenso mkazi wake anali kugwila nchito ya uneneli, cifukwa amachulidwa kuti “mneneli wamkazi.” (Yes. 8:1-4) Monga banja, Yesaya na mkazi wake anasumika maganizo awo pa kulambila Yehova. Masiku anonso, anthu okwatilana angacite zonse zotheka kuti aike mtima wawo pa kutumikila Yehova. Iwo angalimbitse cikhulupililo cawo mwa Yehova, ngati aphunzila maulosi a m’Baibo capamodzi, na kuona mmene amakwanilitsidwila nthawi zonse. (Tito 1:2) Angaganizileko zimene angacite pothandiza kukwanilitsa maulosi ena a m’Baibo. Mwacitsanzo, iwo angatengepo gawo pokwanilitsa ulosi wa Yesu wakuti uthenga wabwino udzalalikidwa padziko lonse lapansi mapeto asanafike. Anthu ali pa banja akatsimikiza kuti maulosi a m’Baibo amakwanilitsikadi, adzakulitsa cifuno cawo cocita zambili mu utumiki wa Yehova mmene angathele. w21.11 16 ¶9-10

Sondo, September 24

Anauza wophunzilayo kuti: “Kuyambila lelo awa akhala mayi ako!”—Yoh. 19:27.

Yesu anali kudela nkhawa amayi ake amene ayenela kuti anali amasiye panthawiyi. Yesu anali kum’konda kwambili mayi wake Mariya, ndipo anaonetsetsa kuti adzasamalidwa bwino. Conco anamuikiza m’manja mwa Yohane, podziŵa kuti adzam’samalila bwino kuuzimu. Kuyambila tsiku limenelo, Yohane anakhala monga mwana wa Mariya, ndipo Yohane anasamalila Mariya monga mayi ake omubala. Ndithudi, Yesu anaonetsa cikondi cacikulu kwa mayi wabwino kwambili ameneyo, amene anamusamalila atangobadwa komanso amene anaimilila pafupi na iye pa nthawi ya imfa yake. Kodi tingaphunzile ciani pa mawu a Yesu? Ubale wathu na abale na alongo athu acikhristu ungakhale wolimba kwambili kuposa ubale wathu na acibale akuthupi. Acibale athu angatitsutse kapena kutisiya. Koma Yesu analonjeza kuti tikamamatilabe Yehova na gulu lake, ‘tidzapeza zoculuka kuwilikiza maulendo 100’ kuposa zimene tingataye. Ambili adzakhala ana athu okondedwa, amayi kapena atate. (Maliko 10:29, 30) Kodi mumamvela bwanji kukhala m’banja lauzimu limene ni logwilizana mwa cikhulupililo na cikondi—inde cikondi pa Yehova komanso pa wina na mnzake?—Akol. 3:14; 1 Pet. 2:17. w21.04 9-11 ¶7-8

Mande, September 25

Musaiŵale kucita zabwino ndi kugaŵana zinthu ndi ena. —Aheb. 13:16.

Kuonetsa cikondi cosasintha kumafuna kudzimana. Masiku ano, abale na alongo ambili amaonetsa cikondi cosasintha kwa alambili anzawo, ngakhale kwa anthu amene sawadziŵa n’komwe. Mwacitsanzo, akamvela kuti kwacitika ngozi yacilengedwe, mwamsanga amapeleka thandizo lofunikila. Komanso, akaona kuti wina mu mpingo wakumana na mavuto, iwo amayesetsa kupeleka thandizo lofunikila. Mofanana na Akhristu a ku Makedoniya, iwo amadzimana kwambili. Amaseŵenzetsa nthawi yawo na cuma cawo, “ngakhale zoposa pamenepo,” kuti athandize abale awo amene ali pa mavuto. (2 Akor. 8:3) Akulu achelu masiku ano naonso amayamikila thandizo limene abale na alongo acikondi amapeleka kwa ena. Mawu olimbikitsa komanso a pa nthawi yake amenewo, adzapatsa mphamvu abale na alongo kuti apitilize kupeleka thandizo.—Yes. 32:1, 2. w21.11 11 ¶14; 12 ¶21

Ciŵili, September 26

Chela khutu lako ndi kumva mawu a anthu anzelu.—Miy. 22:17.

Tonsefe timafunikila uphungu nthawi na nthawi. Ndipo nthawi zina, tingafunike kuyamba ndife kufunsila uphungu kwa munthu amene timamudalila. Nthawi zinanso, m’bale amene amatikonda angatifikile na kutiuza kuti tayamba “kuloŵela njila yolakwika,” imene pambuyo pake ingatigwilitse fuwa la moto. (Agal. 6:1) Mwinanso, tingapatsidwe uphungu mwa kuongoleledwa tikacita colakwa cacikulu. Kaya uphunguwo taulandila pa zifukwa zotani, tiyenela kuumvela. Kucita zimenezi n’kopindulitsa kwa ife, ndipo kungapulumutse moyo wathu. (Miy. 6:23) Lemba la tsiku lalelo litilimbikitsa ‘kumvela mawu a anthu anzelu.’ Palibe munthu adziŵa zonse, ndipo nthawi zambili pamakhala munthu amene amatiposa m’cidziŵitso, komanso maluso. (Miy. 12:15) Conco, kumvela uphungu n’cizindikilo cakuti ndife odzicepetsa. Kumaonetsa kuti timadziŵa bwino zopeleŵela zathu, komanso kuti timafunikila thandizo kuti tikwanilitse zolinga zathu. Mfumu yanzelu Solomo inalemba kuti: “Aphungu akaculuka [zolingalila] zimakwanilitsidwa.”—Miy. 15:22. w22.02 8 ¶1-2

Citatu, September 27

Wobisa macimo ake zinthu sizidzamuyendela bwino, koma woulula n’kuwasiya adzacitilidwa cifundo.—Miy. 28:13.

Kulapa kwa zoona sikumangolekezela pa kudzimvela cisoni pa chimo lalikulu limene tinacita. Koma kumafuna kuti munthu asinthe kaganizidwe kake, na mmene aonela zinthu. Izi ziphatikizapo kuleka khalidwe lake loipa, na kutembenuka n’kuyambanso kuyenda m’njila ya Yehova. (Ezek. 33:14-16) Wocimwayo ayenela kudziŵa kuti colinga cake cacikulu ni kukonza ubale wake na Yehova. Kodi tiyenela kucita ciyani ngati mnzathu wapamtima wacita chimo lalikulu? Tingapweteketse mnzathu ngati tiyesa kubisa chimo lake. Kucita izi n’kosathandiza cifukwa Yehova amaona. (Miy. 5:21, 22) Muuzeni mnzanuyo kuti akulu afuna kum’thandiza. Ngati iye wakana kukaonana na akulu, inu pitani mukaŵauze akulu za chimolo. Makatelo, mudzaonetsa kuti mufuna kumuthandizadi mnzanuyo. w21.10 7 ¶19-21

Cinayi, September 28

Musamaganizile zofuna zanu zokha, koma muziganizilanso zofuna za ena.—Afil. 2:4.

Tonsefe, tiyenela kutengela mzimu wodzimana wa Yesu. Baibo imati iye ‘anakhala ngati kapolo.’ (Afil. 2:7) Kapolo wabwino, kapena mtumiki wabwino, amafuna-funa mipata yokondweletsela mbuye wake. Popeza ndife akapolo a Yehova komanso atumiki kwa abale athu, mosakayikila timafuna kutumikila Yehova ndiponso abale athu mokwanila. Dzifunseni kuti: ‘Kodi ndine wokonzeka kudzimana zinthu zina kuti nithandize ena? Kodi nimadzipeleka mwamsanga pakafunika anchito oyeletsa malo ocitilapo msonkhano kapena Nyumba ya Ufumu?’ Tiyelekeze kuti mwazindikila mbali yofunika kuwongolela, koma cikukuvutani kupanga masinthidwe ofunikila. Zikakhala conco, pemphelani kwa Yehova mocokela pansi pa mtima. Muuzeni Yehova mmene mumvelela, na kumupempha kuti ‘alimbitse zolakalaka zanu’ kuti mucite zinthu zonse zimene iye amakonda.—Afil. 2:13. w22.02 22-23 ¶9-11

Cisanu, September 29

Ndidzakutsitsimutsani. —Mat. 11:28.

Yesu anaonetsa kukoma mtima mwa kukhala wololela, komanso wodekha ngakhale m’mikhalidwe yovuta. (Mat. 11:29, 30) Mwacitsanzo, pamene mayi wa ku Foinike anam’pempha kuti amucilitsile mwana wake, poyamba Yesu anakana pempho lake. Koma mayiyo ataonetsa cikhulupililo cacikulu, iye mokoma mtima anamucilitsila mwana wake. (Mat. 15:22-28) Ngakhale kuti Yesu anali wokoma mtima, sanaleke kupeleka uphungu pakafunika kutelo. Nthawi zina, anali kuonetsa kukoma mtima mwa kuwongolela anthu amene anali kuwakonda. Mwacitsanzo, Petulo atayesa kumulefula kuti asacite cifunilo ca Yehova, Yesu anamudzudzula pamaso pa atumwi ake ena. (Maliko 8:32, 33) Iye anacita izi, osati kuti acititse Petulo manyazi, koma kuti amuphunzitse na kumucenjeza pamodzi na atumwi ena kupewa kudzikuza. N’kutheka kuti Petulo anacita manyazi, koma anapindula na uphunguwo. Kuti tionetse kukoma mtima kwa anthu amene timawakonda, nthawi zina tingafunike kukamba nawo mosapita m’mbali. Mukafuna kucita zimenezo, tengelani citsanzo ca Yesu mwa kuzika uphungu wanu pa mfundo za m’Mawu a Mulungu. w22.03 11 ¶12-13

Ciŵelu, September 30

Tiyeni nthawi zonse tizitamanda Mulungu. Tizichita zimenezi monga nsembe imene tikupeleka kwa Mulungu, yomwe ndi cipatso ca milomo yathu. Timagwilitsa nchito milomo imeneyi polengeza dzina lake kwa anthu ena.—Aheb. 13:15.

Timalambila Yehova tikamam’tamanda. (Sal. 34:1) Timatamanda Yehova tikamauzako ena za makhalidwe ake abwino komanso nchito zake. Citamando cathu cimacokela mu mtima. Conco, tikamapatula nthawi yosinkhasinkha ubwino wa Yehova, kutanthauza zonse zimene waticitila, tidzakhala na zifukwa zambili zomutamandila. Nchito yolalikila imatipatsa mpata wabwino ‘wotamanda Mulungu monga nsembe imene tikupeleka kwa [iye], yomwe ni cipatso ca milomo yathu.’ Monga mmene timasankhila bwino mawu tisanapemphele kwa Yehova, tiyenela kucitanso cimodzimodzi pa zimene tidzakamba kwa anthu amene timawalalikila. Tifuna kuti nsembe yathu yacitamando ikhale yabwino koposa. Ndiye cifukwa cake, timauzako ena coonadi mocokela mu mtima. w22.03 21 ¶8

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani