LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • es23 masa. 98-108
  • October

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • October
  • Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2023
  • Tumitu
  • Sondo, October 1
  • Mande, October 2
  • Ciŵili, October 3
  • Citatu, October 4
  • Cinayi, October 5
  • Cisanu, October 6
  • Ciŵelu, October 7
  • Sondo, October 8
  • Mande, October 9
  • Ciŵili, October 10
  • Citatu, October 11
  • Cinayi, October 12
  • Cisanu, October 13
  • Ciŵelu, October 14
  • Sondo, October 15
  • Mande, October 16
  • Ciŵili, October 17
  • Citatu, October 18
  • Cinayi, October 19
  • Cisanu, October 20
  • Ciŵelu, October 21
  • Sondo, October 22
  • Mande, October 23
  • Ciŵili, October 24
  • Citatu, October 25
  • Cinayi, October 26
  • Cisanu, October 27
  • Ciŵelu, October 28
  • Sondo, October 29
  • Mande, October 30
  • Ciŵili, October 31
Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2023
es23 masa. 98-108

October

Sondo, October 1

Wodala amene sapeza cokhumudwitsa mwa ine.—Mat. 11:6.

Mawu a Mulungu ndiwo maziko a zimene timaphunzitsa na kukhulupilila. Ngakhale n’telo, ambili masiku ano amakhumudwa cifukwa amaganiza kuti kalambilidwe kathu n’kocititsa ulesi. Ndipo zimene timaphunzitsa zimasiyana na zimene iwo amafuna kumva. Tingacite ciani kuti tisapunthwe? Mtumwi Paulo anauza Akhristu a ku Roma kuti: “Munthu amakhala ndi cikhulupililo cifukwa ca zimene wamva. Ndipo zimene wamvazo zimacokela m’mawu onena za Khristu.” (Aroma 10:17) Conco timalimbitsa cikhulupililo cathu mwa kuŵelenga Malemba, osati mwa kucitako miyambo yacipembedzo yosagwilizana na malemba, olo kuti ioneke yokondweletsa kwambili m’maso mwathu. Tifunika kukhala na cikhulupililo colimba cozikidwa pa cidziŵitso colongosoka cifukwa “popanda cikhulupililo n’zosatheka kukondweletsa Mulungu.” (Aheb. 11:1, 6) Conco, sitifunika kucita kuona cizindikilo capadela cocokela kumwamba kuti tikhulupilile kuti tapeza coonadi. Kupenda mosamala ziphunzitso za m’Baibo zolimbitsa cikhulupililo n’kokwanila kuti tikhutile na kucotsa zikayikilo zilizonse zimene tingakhale nazo. w21.05 4-5 ¶11-12

Mande, October 2

Zondicitikila zija, zathandiza kupititsa patsogolo uthenga wabwino m’malo moulepheletsa.—Afil. 1:12.

Mtumwi Paulo anakumana na mavuto ambili. Iye anafunikila mphamvu maka-maka pamene anali kumenyedwa, kuponyedwa miyala, na kuikidwa m’ndende. (2 Akor. 11:23-25) Paulo anafotokoza poyela kuti nthawi zina anali kuvutika na maganizo olefula. (Aroma 7:18, 19, 24) Anapililanso vuto lina lokhudza thanzi limene linali monga “munga m’thupi,” ndipo anali wofunitsitsa kuti Mulungu amucotsele mungawo. (2 Akor. 12:7, 8) Yehova anam’patsa mphamvu Paulo kuti apitilize kucita utumiki wake mosasamala kanthu za mavuto amene anakumana nawo. Ganizilani zimene Paulo anakwanitsa kucita. Mwacitsanzo, pamene anali m’ndende ya panyumba ku Roma, iye analalikila uthenga wabwino mokangalika kwa atsogoleli aciyuda komanso mwina kwa akulu-akulu a boma. (Mac. 28:17; Afil. 4:21, 22) Analalikilanso asilikali oteteza mfumu, na kucitila umboni kwa onse amene anali kubwela kudzamuona. (Mac. 28:30, 31; Afil. 1:13) Panthawi imodzimodziyo, Paulo analemba makalata ouzilidwa amene amapindulitsa Akhristu oona masiku ano. w21.05 21 ¶4-5

Ciŵili, October 3

“Musapitilile zinthu zolembedwa,” kuti aliyense wa inu asadzitukumule.—1 Akor. 4:6.

Kunyada kunapangitsa Mfumu Uziya ya Yuda kukana uphungu na kucita zinthu modzikuza. Uziya anakwanitsa kucita zinthu zambili. Anapambana nkhondo zambili, anamanga zimango zambili, ndipo anali wocita bwino pankhani ya zaulimi. “Mulungu woonayo anacititsa kuti zinthu zizimuyendela bwino.” (2 Mbiri 26:3-7, 10) Baibo imati: “Koma atangokhala wamphamvu, mtima wake unadzikuza mpaka kufika pom’pweteketsa.” Yehova anali atalamula kuti ansembe okha ndiwo anayenela kupeleka zofukiza m’kacisi. Koma modzikuza, Mfumu Uziya anapita m’kacisi kukapeleka zofukiza. Yehova sanakondwele nazo zimenezo, moti anakantha munthu wodzikuzayo na khate. (2 Mbiri 26:16-21) Kodi nafenso zingatheke kugwidwa mu msampha wa kunyada monga zinacitikila kwa Uziya? Inde zingatheke, ngati timadziona kuti ndife apamwamba. Conco tizikumbukila kuti maluso aliwonse amene tili nawo, komanso mwayi uliwonse wa utumiki umene tingalandile mu mpingo, Yehova ndiye amatipatsa. (1 Akor. 4:7) Ngati ndife onyada, Yehova sadzatigwilitsila nchito. w21.06 16 ¶7-8

Citatu, October 4

Musakondwele ndi zimenezi, kuti mizimu yakugonjelani, koma kondwelani cifukwa maina anu alembedwa kumwamba.—Luka 10:20.

Yesu anadziŵa kuti si nthawi zonse pamene ophunzila ake azikhala na zocitika zokondweletsa conco mu ulaliki. Ndi iko komwe, sitidziŵa kuti ni angati amene anamvetsela kwa ophunzilawo na kukhala Akhristu. Ophunzilawo anayenela kukondwela, osati cabe cifukwa ulaliki unawayendela bwino, koma cacikulu, cifukwa codziŵa kuti Yehova anayamikila khama lawo. Tikamapilila mu utumiki wathu, tidzapeza moyo wosatha. Tikamayesetsa kubyala mbewu za coonadi za Ufumu na kuzithilila, timakhalanso kuti ‘tikutsatila mzimu wa Mulungu,’ mwa kulola mzimuwo kugwila nchito pa ife. Ngati ‘sitilema’ kapena kulefuka, Yehova adzatipatsa moyo wosatha, kaya tathandiza wophunzila watsopano kudzipatulila kwa Mulungu kapena ayi.—Gal. 6:7-9. w21.10 26 ¶8-9

Cinayi, October 5

Anawamvela cifundo . . . Conco anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambili.—Maliko 6:34.

Panthawi ina, Yesu na ophunzila ake anali wolema kwambili pambuyo pogwila nchito yolalikila. Iwo anali kufuna malo kuti apumuleko, koma cikhamu ca anthu cinawatsatila. Atawamvela cifundo, Yesu anayamba kuwaphunzitsa “zinthu zambili.” Yesu anali kudziŵa mmene anthu a m’khamulo anali kumvelela. Iye anaona mmene iwo anali kuvutikila. Anali kufunikila ciyembekezo, ndipo iye anali kufuna kuwathandiza. Ni mmenenso anthu alili masiku ano. Musatengele maonekedwe awo a kunja. Ali monga nkhosa zopanda m’busa wozitsogolela. Mtumwi Paulo anafotokoza kuti anthu otelo sadziŵa Mulungu ndipo alibe ciyembekezo. (Aef. 2:12) Tikaganizila mmene umoyo wauzimu wa anthu ulili m’gawo lathu, cikondi na cifundo zimatilimbikitsa kuwathandiza. Ndipo njila yabwino yowathandizila ni kuwapempha kuti tiziphunzila nawo Baibo. w21.07 5 ¶8

Cisanu, October 6

Tisakhale odzikuza, . . . ocitilana kaduka.—Agal. 5:26.

Munthu wodzikuza amakhala wonyada komanso wodzikonda. Munthu wakaduka samangolakalaka zinthu zimene wina ali nazo, koma amafunanso kuti zimene munthuyo ali nazo zikhale zake. Kukamba zoona, kaduka ni khalidwe loipa kwambili. Kudzikuza komanso kaduka tingaziyelekezele na ciswe cimene cimadya mtengo pang’ono-pang’ono. Ngakhale mtengowo ungaoneke wolimba, m’kupita kwa nthawi umagwa. Mofananamo, munthu angatumikile Yehova kwa nthawi yaitali. Koma ngati amam’tumikila mosonkhezeledwa na mzimu wonyada komanso kaduka sangapite patali. (Miy. 16:18) Iye adzaleka kutumikila Yehova ndipo angadzipweteke na kupweteketsa ena. Tingapewe kudzikuza mwa kutsatila uphungu wa mtumwi Paulo wakuti: “Musacite ciliconse ndi mtima wokonda mikangano kapena wodzikuza, koma modzicepetsa, ndi kuona ena kukhala okuposani.”—Afil. 2:3. w21.07 15-16 ¶6-8

Ciŵelu, October 7

Pamene tinali kulalikila uthenga wabwino kwa inu, sitinali kungolankhula basi, koma uthengawo unakukhudzani kwambili, komanso unabwela limodzi ndi mphamvu ya mzimu woyela, ndipo unacititsa kuti mukhale otsimikiza mtima kwambili.—1 Ates. 1:5.

Ena amaganiza kuti cipembedzo coona ciyenela kuyankha mafunso onse, ngakhale aja amene mayankho ake sapezeka m’Baibo. Koma kodi zimenezi n’zotheka? Ganizilani citsanzo ca mtumwi Paulo. Iye analimbikitsa Akhristu anzake ‘kutsimikizila zinthu zonse,’ koma anavomeleza kuti pali zambili zimene sanali kudziŵa. (1 Ates. 5:21) Iye anakamba kuti: “Tikudziŵa mopeleŵela, pakuti pa nthawi ino sitikuona bwino-bwino cifukwa tikugwilitsa nchito galasi losaoneka bwino-bwino.” (1 Akor. 13:9, 12) Paulo sanali kudziŵa zonse. N’cimodzimodzi na ife. Koma iye anali kudziŵa zambili zokhudza Yehova. Zimene anali kudziŵazo, zinali zokwanila kuti atsimikize kuti analidi na coonadi. Imodzi mwa njila zimene tingalimbitsile cikhulupililo cathu cakuti tili na coonadi, ni kuona ngati zimene Mboni za Yehova zimacita masiku ano, zigwilizana na dongosolo la kulambila limene Yesu anakhazikitsa. w21.10 18-19 ¶2-4

Sondo, October 8

Akakwanitsa zaka 50 atuluke m’gululo.—Num. 8:25.

Inu okalamba, kaya muli mu utumiki wanthawi zonse kapena ayi, mungacite zambili pothandiza ena. Motani? Muyenela kuzoloŵela mikhalidwe yatsopano, kudziikila zolinga zatsopano, na kusumika maganizo anu pa zimene mungakwanitse kucita, osati pa zimene simungakwanitse. Mfumu Davide anali kufunitsitsa na mtima wake wonse kumanga nyumba ya Yehova. Koma Yehova atauza Davide kuti adzamange nyumbayo ni wacinyamata Solomo, Davide anagwilizana na cisankho ca Yehova, ndipo anacilikiza nchitoyo na mtima wonse. (1 Mbiri 17:4; 22:5) Davide sanaganize kuti ndiye anali woyenelela kumanga nyumbayo poona kuti Solomo anali “wamng’ono ndi wosakhwima.” (1 Mbiri 29:1) Iye anadziŵa kuti, kuti nchito yomangayo itheke, zinadalila pa dalitso la Yehova osati pa msinkhu kapena cidziŵitso ca otsogolela. Mofanana na Davide, okalamba masiku ano amakhalabe okangalika olo kuti utumiki wawo wasintha. Ndipo amadziŵa kuti Yehova adzadalitsa acinyamata amene amagwila nchito imene iwo anali kucita. w21.09 9 ¶4; 10 ¶5, 8

Mande, October 9

Adzacititsa ofatsa kutsatila zigamulo zake, ndipo adzaphunzitsa ofatsa kuyenda m’njila yake.—Sal. 25:9.

Zolinga zathu zauzimu zimapangitsa umoyo wathu kukhala waphindu. Komabe, cinsinsi cake cagona pa kudziikila zolinga potengela maluso athu na mikhalidwe yathu, osati zolinga za ŵena. Kudziikila zolinga zimene sitingakwanitse kungatigwilitse mwala ndipo tingalefuke. (Luka 14:28) Mtumiki aliyense wa Yehova ni wosiyana, koma ni wofunika kwambili m’banja lake. Yehova sanakukokeleni kwa iye cifukwa munali kucita bwino kuposa ena. Anakukokelani kwa iye cifukwa anayang’ana mu mtima wanu na kuona kuti ndimwe wofatsa, komanso wofunitsitsa kuphunzila kwa iye kuti musinthe. Dziŵani kuti iye amayamikila mukamacita zonse zotheka kuti mum’tumikile. Kupilila na kukhulupilika kwanu ni umboni wakuti muli na “mtima woona komanso wabwino.” (Luka 8:15) Conco, pitilizani kupatsa Yehova zabwino koposa. Mukatelo, mudzakhala na cifukwa cosangalalila na ‘nchito [yanu].’—Agal. 6:4. w21.07 24 ¶15; 25 ¶20

Ciŵili, October 10

Amene wabweza wocimwa panjila yake yoipa, adzapulumutsa moyo wa wocimwayo.—Yak. 5:20.

Tingafunike kuyembekezela moleza mtima kuti cilungamo cicitike. Mwacitsanzo, akulu akadziŵa kuti wina wacita colakwa cacikulu mu mpingo, amapempha “nzelu yocokela kumwamba” kuti athe kuona nkhaniyo mmene Yehova akuionela. (Yak. 3:17) Colinga cawo ni kufuna ‘kubweza wocimwa panjila yake yoipa,’ ngati n’kotheka. (Yak. 5:19, 20) Cina, iwo amayesetsa kucita zonse zotheka kuti ateteze mpingo na kutonthoza okhudzidwawo. (2 Akor. 1:3, 4) Ndipo asanayambe kuweluza mlandu wa colakwa cacikulu, coyamba akulu amaifufuza nkhaniyo, ndipo izi zimatenga nthawi. Ndiyeno mwa pemphelo komanso mosamala, iwo amapeleka uphungu wa m’Malemba kwa wolakwayo “pa mlingo woyenela.” (Yer. 30:11) Akulu sapanga zigamulo mopupuluma. Iwo akamatsatila malangizo a Yehova poweluza mlandu, mpingo umapindula kwambili. w21.08 11 ¶12-13

Citatu, October 11

Kumene inu mupite inenso ndipita komweko . . . Anthu a mtundu wanu adzakhala anthu a mtundu wanga, ndipo Mulungu wanu adzakhala Mulungu wanga.—Rute 1:16.

Cifukwa cakuti mu Isiraeli munagwa njala, Naomi, mwamuna wake, komanso ana awo aŵili, anasamukila ku Mowabu. Kumeneko, mwamuna wa Naomi anamwalila. Ana ake aŵili anakwatila, koma n’zacisoni kuti naonso anamwalila. (Rute 1:3-5) Naomi anafika potaya mtima cifukwa ca mavuto amenewa. Iye anapsinjika maganizo kwambili cifukwa ca cisoni, moti anaganiza kuti Yehova wamuukila. Ponena za Mulungu, iye anati: “Dzanja la Yehova landiukila.” “Wamphamvuyonse wacititsa moyo wanga kukhala woŵaŵa kwambili.” Anakambanso kuti: “Ndi Yehova amene wandicititsa kukhala wonyozeka, ndipo ndi Wamphamvuyonseyo amene wandigwetsela tsokali.” (Rute 1:13, 20, 21) Yehova amadziŵa kuti “kupondelezedwa kumapangitsa munthu wanzelu kucita zinthu zopanda nzelu.” (Mlal. 7:7) Iye anakhudza mtima wa Rute kuti athandize Naomi, na kumuonetsa cikondi cosasintha. Modzipeleka komanso mwacikondi, Rute anathandiza apongozi ake kupezanso mphamvu mwauzimu. w21.11 9 ¶9; 10 ¶10, 13

Cinayi, October 12

Azipempha kwa Mulungu.—Yak. 1:5.

Kodi kusumika maganizo athu pa mautumiki amene tikucita pali pano, kutanthauza kuti tileke kufunafuna njila zina zowonjezela utumiki wathu kwa Yehova? Ayi! Tiyenela kudziikila zolinga zauzimu zimene zingatithandize kukhala aluso mu utumiki, komanso othandiza kwa abale na alongo athu. Tidzakwanilitsa zolinga zathu ngati modzicepetsa timasumika maganizo athu pa kutumikila ena m’malo mofuna kutumikilidwa. (Miy. 11:2; Mac. 20:35) Kodi mungadziikile zolinga zotani? Pemphani Yehova kuti akuthandizeni kudziŵa zolinga zimene n’zotheka kwa inu kuzikwanilitsa. (Miy. 16:3) Kodi mungadziikile colinga cocitako upainiya wothandiza, wanthawi zonse, kukatumikila pa Beteli, kapena kugwilako nchito zamamangidwe m’gulu la Mulungu? Ngati n’kotheka kwa inu, mungaphunzile cinenelo cina n’colinga cakuti muzilalikila anthu a cineneloco m’gawo lanu, kapena kusamukila ku dela la cineneloco. w21.08 23 ¶14-15

Cisanu, October 13

Kukoma mtima kosatha [cikondi cosasintha ca Yehova] kudzakhalapobe mpaka kale-kale.—Sal. 136:1.

Yehova amakondwela kuonetsa cikondi cosasintha. (Hos. 6:6) Koma coyamba, tiyenela kudziŵa kuti cikondi cosasintha n’ciani. Kodi cikondi cosasintha n’ciani? Malinga na mbali yakuti “Matanthauzo a Mawu Ena” mu Baibo la Dziko Latsopano la Cizungu, mawuwa amatanthauza “kukonda munthu mokhulupilika, modzipeleka, na kumamatila kwa iye zivute zitani. Nthawi zambili, amagwilitsidwa nchito pokamba za cikondi cimene Mulungu amaonetsa anthu, komanso cimene anthu amaonetsana pakati pawo.” Yehova n’citsanzo cabwino koposa pa kuonetsa cikondi cosasintha. Ndiye cifukwa cake, Mfumu Davide anati: “Inu Yehova, kukoma mtima kwanu kosatha [cikondi cosasintha] kuli kumwamba . . . Inu Mulungu, kukoma mtima kwanu kosatha ndi kwamtengo wapatali! (Sal. 36:5, 7) Mofanana na Davide, kodi timayamikila kwambili cikondi cosasintha ca Mulungu? w21.11 2 ¶1-2; 3 ¶4

Ciŵelu, October 14

Koma inu muzipemphela motele: “Atate wathu wakumwamba.” —Mat. 6:9.

Banja la alambili a Yehova liphatikizapo Yesu, amene ni “woyamba kubadwa wa cilengedwe conse,” na angelo miyanda-miyanda. (Akol. 1:15; Sal. 103:20) Ali padziko lapansi, Yesu anaonetsa kuti n’zotheka anthu okhulupilika kuchula Yehova kuti Atate wawo. Pokamba na ophunzila ake, iye anachula Yehova kuti “Atate wanga ndi Atate wanu.” (Yoh. 20:17) Tikadzipatulila na kubatizika, timakhala m’banja la abale na alongo. (Maliko 10:29, 30) Yehova ni Tate wacikondi. Yesu amafuna kuti tiziona Yehova mmene iye amamuonela—inde monga kholo lacikondi lofikilika, osati lokhwimitsa zinthu. M’pemphelo lake lacitsanzo, iye anayamba na mawu akuti: “Atate wathu.” Yesu akanafuna sembe anatiuza kuchula Yehova kuti “Wamphamvuyonse,” “Mlengi,” kapena “Mfumu yamuyaya,” amene ni maina audindo oyenelela a m’Malemba. (Gen. 49:25; Yes. 40:28; 1 Tim. 1:17) Komabe, Yesu anatiuza kuchula Yehova kuti “Atate.” w21.09 20 ¶1, 3

Sondo, October 15

Manase anadziŵa kuti Yehova ndiye Mulungu woona. —2 Mbiri 33:13.

Mfumu Manase mouma khosi, sanalabadile macenjezo a Yehova amene anapeleka kupitila mwa aneneli ake. Potsilizila pake, “Yehova anawabweletsela akulu-akulu a asilikali a mfumu ya Asuri. Iwo anagwila Manase akubisala m’dzenje. Atatelo anam’manga ndi zomangila ziŵili zamkuwa n’kupita naye ku Babulo.” Ali m’ndende ku dziko lacilendo, Manase ayenela kuti anaganizilapo mozama pa zimene anacita. Iye “anadzicepetsa kwambili pamaso pa Mulungu wa makolo ake.” Kuwonjezela apo, anapitiliza kucondelela Yehova Mulungu wake kuti amukhululukile. (2 Mbiri 33:10-12) M’kupita kwa nthawi, Yehova anayankha mapemphelo a Manase. Mapemphelo ake anaonetsa kuti iye anasinthadi, ndipo Yehova anaona zimenezo. Conco, iye anamubwezanso pa ufumu. Manase anacita zonse zotheka poonetsa kuti analapadi. w21.10 4 ¶10-11

Mande, October 16

Aŵili amaposa mmodzi, cifukwa amapeza mphoto yabwino pa nchito yawo imene amaigwila mwakhama.—Mlal. 4:9.

Akula na Purisikila anafunika kucoka ku malo amene anazoloŵela, kupeza nyumba yatsopano, na kuyambanso bizinesi yawo yosoka matenti ku malo atsopano. Atafika ku Korinto ku malo awo atsopano, Akula na Purisikila anagwilizana na mpingo wa kumeneko, komanso anayamba kutumikila pamodzi na mtumwi Paulo kuti alimbikitse abale. Patapita nthawi, iwo anasamukila m’matauni ena kumene alengezi a Ufumu anali ocepa kwambili. (Mac. 18:18-21; Aroma 16:3-5) Iwo ayenela kuti anasangalala kwambili na umoyo wopindulitsa umenewo! Anthu amene ali pa banja angatengele citsanzo ca Purisikila na Akula, akaika zinthu za Ufumu patsogolo. Nthawi yabwino imene angakambilane zolinga zawo zauzimu, m’pamene ali pa cibwenzi. Anthu ali pa banja akamapanga zisankho pamodzi, komanso kuyesetsa kukwanilitsa zolinga zina zauzimu, adzakhala na mipata yambili yoona mmene Yehova akuwathandizila.—Mlal. 4:12. w21.11 17 ¶11-12

Ciŵili, October 17

Aliyense wa inu aziopa mayi ndi bambo ake . . . Ine ndine Yehova Mulungu wanu.—Lev. 19:3.

N’zoonekelatu kuti tiyenela kumvela lamulo la Yehova lakuti tizilemekeza makolo athu. Dziŵani kuti lamulo la pa Levitiko 19:3, lakuti tizilemekeza atate na amayi athu, libwela pambuyo pa langizo lakuti, “Mukhale oyela, cifukwa ine Yehova Mulungu wanu ndine woyela.” (Lev. 19:2) Mogwilizana na lamulo la Yehova lakuti tizilemekeza makolo athu, tingadzifunse kuti, ‘Kodi ine nimacita motani pa mbali imeneyi?’ Ngati muona kuti simunacite zambili polemekeza makolo anu m’mbuyomu, mungafunike kuwongolela mbali zina. Simungasinthe zakumbuyo, koma mungacite zotheka pali pano kuti mucite zambili pothandiza makolo anu. Mwina mungakonze zakuti muzikhala na nthawi yambili yoceza nawo. Kapena kupeleka thandizo lokwanila kuthupi, kuuzimu, komanso kuwalimbikitsa. Mukatelo, ndiye kuti mwacita mogwilizana na Levitiko 19:3. w21.12 4-5 ¶10-12

Citatu, October 18

Lekani kuweluza ena.—Mat. 7:1.

Mfumu Davide anacita macimo aakulu. Mwacitsanzo, iye anacita cigololo na Batiseba, ndipo anafika ngakhale pa kuphetsa mwamuna wake. (2 Sam. 11:2-4, 14, 15, 24) Cotulukapo cake, zimene Davide anacita sizinavutitse iye yekha cabe, koma zinavutitsanso banja lake, kuphatikizapo akazi ake ena. (2 Sam. 12:10, 11) Pa nthawi ina, Davide analephela kudalila Yehova na mtima wonse pamene analamula atumiki ake kuti aŵelenge khamu la Aisiraeli popanda cilolezo. Kodi panakhala zotulukapo zotani? Aisiraeli pafupifupi 70,000 anafa na mlili! (2 Sam. 24:1-4, 10-15) Kodi mukanamuweluza Davide kuti sayenela cifundo ca Yehova? Umu si mmene Yehova anamuonela. Iye anayang’ana kwambili pa mbili ya Davide ya kukhulupilika, komanso kulapa kwake mocokela pansi pa mtima. Pa cifukwa cimeneci, Yehova anam’khululukila Davide pa macimo ake aakuluwo. Iye anali kudziŵa kuti Davide anali kum’konda kwambili, ndipo anali kufuna kucita zoyenela. Kodi simuyamikila kuti Yehova amaona zabwino mwa ife?—1 Maf. 9:4; 1 Mbiri 29:10, 17. w21.12 19 ¶11-13

Cinayi, October 19

Nthawi yomweyo anayamba kuona, ndipo anayamba kumutsatila akulemekeza Mulungu.—Luka 18:43.

Yesu anali kucitila cifundo anthu olemala. Kumbukilani uthenga umene iye anatumiza kwa Yohane M’batizi. Anati: “Akhungu akuona, olumala akuyenda, akhate akuyeletsedwa, ogontha akumva, [ndipo] akufa akuukitsidwa.” Poona zozizwitsa za Yesu, ‘anthu onse anatamanda Mulungu.’ (Luka 7:20-22) Akhristu amatengela citsanzo ca Yesu mwa kucitila cifundo anthu olemala. Conco, timakhala okoma mtima, oganizila ena, komanso oleza mtima kwa anthu otelo. N’zoona kuti Yehova sanatipatse mphamvu yocita zozizwitsa. Koma tili na mwayi wouzako anthu ali na khungu lakuthupi kapena lauzimu uthenga wabwino wokamba za paradaiso, mmene anthu adzakhala na thanzi labwino kuthupi komanso kuuzimu. (Luka 4:18) Uthenga wabwino umenewu wathandiza anthu ambili kutamanda Mulungu. w21.12 9 ¶5

Cisanu, October 20

Munamva za kupilila kwa Yobu ndipo mwaona zimene Yehova anamupatsa.—Yak. 5:11.

Onani kuti zimene Yakobo anaphunzitsa zinazikidwa pa Malemba. Iye anaseŵenzetsa Mawu a Mulungu pothandiza omvela ake kuona kuti Yehova nthawi zonse amafupa awo amene mofanana na Yobu, ni okhulupilika kwa iye. Yakobo anaphunzitsa mfundo imeneyi na mawu osavuta kumva. Mwakutelo, anthu anatamanda Yehova osati iye. Zimene tiphunzilapo: Uthenga wanu uzikhala wosavuta kumva, ndipo phunzitsani kucokela m’Mawu a Mulungu. Colinga cathu si kufuna kuonetsa ena kuculuka kwa zimene tidziŵa, koma ni kuwathandiza kuona kuculuka kwa nzelu za Yehova, komanso kuti amasamala kwambili za ife. (Aroma 11:33) Tingakwanilitse colingaci ngati nthawi zonse zokamba zathu zimazikidwa pa Malemba. Mwacitsanzo, m’malo mouza maphunzilo athu a Baibo zimene ife tikanacita tikanakhala iwo, tiziwathandiza kuganizila zitsanzo za m’Baibo kuti amvetse mmene Yehova amaonela zinthu. Tikatelo, iwo adzakhala ofunitsitsa kukondweletsa Yehova osati ife. w22.01 11 ¶9-10

Ciŵelu, October 21

Uzikonda mnzako mmene umadzikondela wekha.—Lev. 19:18.

Mulungu samangofuna kuti tizipewa kucita zinthu zopweteka ena. Kukonda anzathu mmene timadzikondela, n’kofunika kwambili kwa Mkhristu amene afuna kukondweletsa Mulungu. Onani mmene Yesu anagogomezela kufunika kwa lamulo la pa Levitiko 19:18. Mfarisi wina anafunsa Yesu kuti: “Kodi lamulo lalikulu kwambili m’Cilamulo ndi liti?” Yesu anamuyankha kuti “lamulo lalikulu kwambili komanso loyamba,” ni kukonda Yehova Mulungu na mtima wathu wonse, moyo wathu wonse, komanso maganizo athu onse. Ndiyeno Yesu anagwila mawu Levitiko 19:18, imene imati: “Laciŵili lofanana nalo ndi ili, ‘Uzikonda mnzako mmene umadzikondela wekha.’” (Mat. 22:35-40) Pali njila zambili zoonetsela cikondi kwa anzathu. Njila ina ni kuseŵenzetsa langizo la pa Levitiko 19:18 lakuti: ‘Usabwezele coipa kapena kusunga cakukhosi.’ w21.12 10-11 ¶11-13

Sondo, October 22

Ataona mphepo yamkuntho, anacita mantha, ndipo atayamba kumila anafuula kuti: “Ambuye, ndipulumutseni!”—Mat. 14:30.

Yesu anatambasula dzanja lake na kumupulumutsa. Petulo akanapitiliza kuyang’ana Yesu, akanakwanitsa kuyenda pamadzi amphamvu amenewo. Koma cifukwa coyang’ana cimphepoco, iye anacita mantha ndipo anakayikila. Kenako, anayamba kumila. (Mat. 14:24-31) Tingapindule na citsanzo ca Petulo. Iye atatsika m’boti na kuyenda pamadzi, sanadziŵe kuti zinthu zina zidzamuceutsa n’kuyamba kumila. Anali kufuna kupitiliza kuyenda pamadzipo mpaka atafika kwa Mbuye wake. Koma analephela kulunjikitsa maganizo ake pa colinga cakeco. N’zoona kuti sitingayende pamadzi, koma timakumana na mavuto oika cikhulupililo cathu pamayeso. Tikalephela kusumika maganizo athu pa Yehova na malonjezo ake, tidzayamba kumila mwauzimu. Kaya tikumane na mphepo yophiphilitsa yotani, tiyenela kupitiliza kusumika maganizo athu pa Yehova, komanso thandizo lake. w21.12 17-18 ¶6-7

Mande, October 23

Ine ndidzaloŵa m’nyumba yanu cifukwa ca kuculuka kwa kukoma mtima kwanu kosatha.—Sal. 5:7.

Pemphelo, kuŵelenga Baibo, na kusinkha-sinkha, ni mbali ya kulambila Yehova. Tikapemphela, timakhala kuti tikukambilana na Atate wathu wakumwamba amene amatikonda ngako. Tikamaŵelenga Baibo, timafika ‘pomudziŵadi Mulungu,’ amene ni gwelo la nzelu. (Miy. 2:1-5) Tikamasinkha-sinkha, timakhala kuti tikuganizila makhalidwe abwino a Yehova, komanso colinga cake cokondweletsa cokhudza mtundu wonse wa anthu. Iyi ni njila yabwino koposa imene tingaseŵenzetsele bwino nthawi yathu. Koma kodi n’ciani cingatithandize kupindula kwambili tikamacita zimenezi? Ngati n’zotheka, khalani pamalo a zii. Ganizilani citsanzo ca Yesu. Asanayambe utumiki wake padziko lapansi, iye anakhala masiku 40 m’cipululu. (Luka 4:1, 2) Kumalo a zii amenewo, Yesu anali kupemphela kwa Yehova, na kusinkha-sinkha zimene Atate wake anali kufuna kuti iye acite. Mosakayikila, kucita zimenezo kunamuthandiza kukonzekela mayeso amene anali kudzakumana nawo. w22.01 27-28 ¶7-8

Ciŵili, October 24

Aphungu akaculuka [zolingalila] zimakwanilitsidwa.—Miy. 15:22.

Mkulu kapena m’bale wina wofikapo kuuzimu, angatichulile mbali inayake imene tiyenela kuwongolela. Ngati munthu amene amatikonda watipatsa uphungu wozikika m’Baibo, tiyenela kuuseŵenzetsa. Kukamba zoona, cingativute kulandila uphungu umene wapelekedwa mwacindunji. Tingafike ngakhale pokhumudwa. Cifukwa ciani? Olo kuti timavomeleza kuti ndife opanda ungwilo, cingativute kulandila uphungu munthu akatichulila mbali ina yake imene tinalakwitsa. (Mlal. 7:9) Tingayambe kupeleka zifukwa zodzilungamitsa. Komanso tingakaikile zolinga za wopeleka uphunguyo, kapena tingakhumudwe na mmene waupelekela. Tingafike ngakhale pa kumupeza zifukwa, n’kumadziuza kuti: ‘Ameneyu sanganipatse uphungu, nayenso ali n’zolakwa zake.’ Ndipo ngati tiona kuti uphungu umene tapatsidwa si wotiyenelela, tingaunyalanyaze, kapena tingafunsile kwa ena amene tikudziŵa kuti adzatipatsa uphungu umene tingakonde. w22.02 8-9 ¶2-4

Citatu, October 25

Mudzakhala amphamvu mukakhala osatekeseka ndi acikhulupililo.—Yes. 30:15.

Kodi n’kutheka kuti umoyo m’dziko latsopano, ungadzabweletse zovuta zina zimene zingadzayese cikhulupililo cathu pa njila imene Yehova amacitila zinthu? Mwacitsanzo, ganizilani zinacitika Aisiraeli atangomasulidwa mu ukapolo ku Iguputo. Ena anayamba kudandaula cifukwa coyewa zakudya zabwino zimene anasiya ku Iguputo, ndipo anafika ngakhale ponyoza mana amene Yehova anali kuwapatsa. (Num. 11:4-6; 21:5) Kodi nafenso tingadzakhale na mzimu wodandaula pambuyo pa cisautso cacikulu? Sitidziŵa kuti padzakhala nchito yoculuka motani yoyeletsa dziko lapansi, kuti pang’ono-m’pang’ono likhale paladaiso. N’zoonekelatu kuti padzakhala nchito zambili zofunika kugwila, ndipo zina mwa izo zidzakhala zovuta poyamba. Kodi tidzadandaula na zimene Yehova adzatipatse pa nthawiyo? Mfundo pano ni yakuti: Ngati pali pano timayamikila zimene Yehova amatipatsa, tidzayamikila koposa zimene iye adzatipatse panthawiyo. w22.02 7 ¶18-19

Cinayi, October 26

Adzagwila covala ca munthu amene ndi Myuda ndi kunena kuti: “Anthu inu tipita nanu limodzi.”—Zek. 8:23.

Mu ulosi wa pa Zekariya 8:23, mawu akuti “Myuda” komanso “anthu inu” amaimila gulu limodzi-modzi la anthu, limene ni otsalila odzozedwa. (Aroma 2:28, 29) “Amuna 10 ocokela m’zilankhulo zonse za anthu a mitundu ina,” amaimila a nkhosa zina. Iwo ‘amagwila [mwamphamvu]’ odzozedwa—kutanthauza kuwamamatila mokhulupilika, na kugwilizana nawo pa kulambila koyela. Mofananamo, pokwanilitsa ulosi wa pa Ezekieli 37:15-19, 24, 25, Yehova wagwilizanitsa kwambili odzozedwa na a nkhosa zina. Ulosiwu umakamba za ndodo ziŵili. Awo amene ali na ciyembekezo cakumwamba ali ngati ndodo “ya Yuda” (mtundu umene mafumu a Isiraeli anali kusankhidwa). Ndipo aja amene ali na ciyembekezo ca padziko lapansi ali ngati ndodo “ya Efuraimu.” Yehova anali kudzagwilizanitsa magulu aŵili kuti akhale “ndodo imodzi.” Izi zitanthauza kuti iwo amatumikila pamodzi mogwilizana pansi pa Mfumu yawo, Khristu Yesu.—Yoh. 10:16. w22.01 22 ¶9-10

Cisanu, October 27

Samalani kuti musamacite cilungamo canu pamaso pa anthu ndi colinga cakuti akuoneni.—Mat. 6:1.

Yesu anakamba za anthu amene anali kuthandiza osauka modzionetsela kuti anthu awaone n’kuwatamanda. Ngakhale kuti zimene anacitazo zinali zabwino, Yehova sanakondwele nawo. (Mat. 6:2-4) Tingaonetse khalidwe la ubwino, kokha ngati timacita zabwinozo osati na zolinga zadyela. Conco, dzifunseni kuti: ‘Kodi nimadziŵa zabwino zimene niyenela kucita na kuyesetsa kuzicita? Kodi colinga canga pocita zabwinozo n’ciyani?’ Yehova amaseŵenzetsa mzimu wake kuti agwile nchito zosiyana-siyana. (Gen. 1:2) Conco, khalidwe lililonse limene mzimu umabala liyenela kutipangitsa kuonetsa nchito yake. Mwacitsanzo, wophunzila Yakobo analemba kuti: “Cikhulupililo copanda nchito zake ndi cakufa.” (Yak. 2:26) N’cimodzimodzinso na makhalidwe ena amene mzimu wa Mulungu umabala. Nthawi iliyonse tikaonetsa khalidwe limenelo, timapeleka umboni wakuti mzimu wa Mulungu ukugwila nchito mwa ife. w22.03 11-12 ¶14-16

Ciŵelu, October 28

Khalani motsanzila Woyela amene anakuitanani. Inunso khalani oyela m’makhalidwe anu onse.—1 Pet. 1:15.

Tingakhale kuti timacita zinthu zonse zauzimu, komanso kucitila ena zabwino. Koma Petulo anatilimbikitsa kucita cinthu cina cofunika kwambili. Iye asanatilimbikitse kukhala oyela m’makhalidwe athu onse, anati: “Konzekeletsani maganizo anu kuti mugwile nchito mwamphamvu.” (1 Pet. 1:13) Kodi nchito imeneyi ni iti? Petulo anati abale a Khristu odzozedwa anali ‘kudzalengeza makhalidwe abwino kwambili’ a uyo amene anawaitana.’ (1 Pet. 2:9) Akhristu onse lelo lino, ali na mwayi wogwila nchito yofunika kwambili imeneyi, imene imathandiza anthu kwambili. Monga anthu oyela, ulidi mwayi wapadela kutengako mbali mokangalika pa nchito yolalikila na kuphunzitsa. (Maliko 13:10) Tikamayesetsa kucita zimenezi, timaonetsa kuti timakonda Mulungu komanso anzathu. Timaonetsanso kuti timafuna ‘kukhala oyela’ m’makhalidwe athu onse. w21.12 13 ¶18

Sondo, October 29

Ciliconse cimene mwakhululukila munthu ndi mtima wonse, inenso ndimukhululukila cimodzimodzi.—2 Akor. 2:10.

Mtumwi Paulo anali kuona abale na alongo ake moyenelela. Iye anali kudziŵa kusiyana pakati pa khalidwe loipa na ŵanthu oipa. Anali kuwakonda abale ake, ndipo anali kuona zabwino mwa iwo. Iwo akamavutika kucita zoyenela, iye sanali kukaikila zolinga zawo, koma anali kuona kuti iwo angofunikila thandizo basi. Ganizilani mmene Paulo anathandizila alongo aŵili mu mpingo wa ku Filipi. (Afil. 4:1-3) Zioneka kuti Eodiya na Suntuke anasemphana maganizo, ndipo izi zinapangitsa kuti asakhalenso mabwenzi. Paulo sanacite nawo zinthu mwaukali kapena kuwaweluza, koma anasumika maganizo ake pa makhalidwe awo abwino. Iwo anali alongo okhulupilika amene anali na mbili yabwino. Paulo anadziŵa kuti Yehova anali kuwakonda. Kuona alongowa moyenelela, kunamusonkhezela kuwalimbikitsa kuti athetse kusamvana pakati pawo. Kunam’thandizanso kukhalabe wacimwemwe, ndiponso kukhala pa ubale wolimba na ena mu mpingo. w22.03 30 ¶16-18

Mande, October 30

Yehova ali pafupi ndi anthu a mtima wosweka. Ndipo odzimvela cisoni mumtima mwawo amawapulumutsa.—Sal. 34:18.

Mtendele umene Yehova amapeleka umatikhazika mtima pansi, na kutithandiza kukhala oganiza bwino. Izi n’zimene zinacitikila mlongo wina dzina lake Luz. Iye anati: “Nimalimbana na vuto la kusungulumwa. Nthawi zina, vuto limeneli limanipangitsa kuona kuti Yehova sanikonda. Izi zikacitika, nthawi yomweyo nimauza Yehova mmene nikumvelela. Pemphelo limanithandiza kumvelako bwino.” Citsanzo ca mlongoyu, cionetsa kuti pemphelo limatithandiza kukhala na mtendele wa maganizo. (Afil. 4:6, 7) Tidziŵa kuti Yehova na Yesu kuti adzaticilikiza wokondedwa wathu akamwalila. Talimbikitsidwa kuti tizionetsa cifundo pamene tikulalikila na kuphunzitsa, cifukwa Yehova Mulungu na Yesu Khristu ni acifundo. Ndipo n’zolimbikitsa kuti Yehova na Mwana wake wokondeka, amadziŵa zifooko zathu, ndipo amafuna kutithandiza kupilila. Tiyembekezela mwacidwi tsiku limene Yehova “adzapukuta misozi yonse m’maso [mwathu].”—Chiv. 21:4. w22.01 15 ¶7; 19 ¶19-20

Ciŵili, October 31

Loŵani pacipata copapatiza. Pakuti msewu waukulu ndi wotakasuka ukupita kuciwonongeko, ndipo anthu ambili akuyenda mmenemo. —Mat. 7:13.

Yesu anachula zipata ziŵili zosiyana zotsogolela ku misewu iŵili yosiyana—msewu “wotakasuka,” komanso msewu “wopanikiza.” (Mat. 7:14) Palibe msewu wacitatu. Tifunika kusankha tokha msewu umene tidzayendamo. Ici ndiye cisankho cofunika kopambana cimene tiyenela kupanga, cifukwa moyo wosatha umadalila cisankho cimeneci. Msewu “wotakasuka” ni wodziŵika cifukwa ni wosavuta kuyendamo. N’zacisoni kuti anthu oculuka asankha kuyendabe mu msewu umenewu potsatila unyinji umene ukuyendamo. Iwo sadziŵa kuti Satana Mdyelekezi, ndiye akupangitsa anthu kuyenda mu msewu umenewu wopita ku ciwonongeko. (1 Akor. 6:9, 10; 1 Yoh. 5:19) Mosiyana na msewu “wotakasuka,” msewu winawo ni “wopanikiza,” ndipo Yesu anati ni anthu oŵelengeka amene akuupeza. Cifukwa ciani? Onani kuti pa vesi yotsatila, Yesu anacenjeza otsatila ake za aneneli onyenga.—Mat. 7:15. w21.12 22-23 ¶3-5

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani