LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • es23 masa. 108-118
  • November

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • November
  • Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2023
  • Tumitu
  • Citatu, November 1
  • Cinayi, November 2
  • Cisanu, November 3
  • Ciŵelu, November 4
  • Sondo, November 5
  • Mande, November 6
  • Ciŵili, November 7
  • Citatu, November 8
  • Cinayi, November 9
  • Cisanu, November 10
  • Ciŵelu, November 11
  • Sondo, November 12
  • Mande, November 13
  • Ciŵili, November 14
  • Citatu, November 15
  • Cinayi, November 16
  • Cisanu, November 17
  • Ciŵelu, November 18
  • Sondo, November 19
  • Mande, November 20
  • Ciŵili, November 21
  • Citatu, November 22
  • Cinayi, November 23
  • Cisanu, November 24
  • Ciŵelu, November 25
  • Sondo, November 26
  • Mande, November 27
  • Ciŵili, November 28
  • Citatu, November 29
  • Cinayi, November 30
Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2023
es23 masa. 108-118

November

Citatu, November 1

Onse adzaphunzitsidwa ndi Yehova.—Yoh. 6:45.

Yehova amatithandiza m’njila zambili. Iye angakuthandizeni kukhala wodekha mukakumana na munthu wotsutsa mu ulaliki. Angakuthandizeninso kukumbukila lemba loyenelela pamene munthu wina waonetsa cidwi. Cina, amakuthandizani kupitiliza kulalikila olo kuti gawo lanu n’louma. (Yer. 20:7-9) Yehova wationetsanso ubwino wake mwa kutiphunzitsa mogwilila nchito yolalikila. Pa misonkhano ya mkati mwa mlungu, timamvetsela maulaliki acitsanzo ogwila mtima, ndipo timalimbikitsidwa kuseŵenzetsa malangizo ake mu ulaliki. Poyamba, tingadodome kuseŵenzetsa malangizo atsopano mu ulaliki. Koma tikawaseŵenzetsa tidzaona kuti ni othandiza kwambili m’gawo lathu. Pa misonkhano ya mpingo komanso ya cigawo, timalimbikitsidwanso kuseŵenzetsa njila zina zolalikila zimene sitinaziseŵenzetsepo. Kucita zimenezi kumafuna kudzimanako zinthu zina. Koma tikatelo, Yehova amatidalitsa. w21.08 27 ¶5-6

Cinayi, November 2

Muzigwilitsa nchito bwino nthawi yanu cifukwa masikuwa ndi oipa.—Aef. 5:16.

Mtumwi Paulo anapeleka uphungu wamphamvu m’kalata yake yopita kwa Akorinto. Atalemba kalatayo, anawatumizila Tito. Iye anakondwela kwambili kudziŵa kuti iwo analabadila uphunguwo. (2 Akor. 7:6, 7) Akulu angatengele citsanzo ca Paulo mwa kupatula nthawi yoceza na alambili anzawo. Njila imodzi imene angacitile zimenezi, ni kufika mofulumila ku misonkhano ya mpingo, kuti akhale na maceza olimbikitsa na ena. Zimangotenga mphindi zocepa kuti mupeleke cilimbikitso kwa m’bale kapena mlongo. (Aroma 1:12) Cina, mkulu amene amatengela citsanzo ca Paulo, amalimbitsa cikhulupililo ca alambili anzake poseŵenzetsa Mawu a Mulungu, na kuwatsimikizila kuti Mulungu amawakonda. Amafuna-funa mipata kuti awayamikile. Ndipo mkuluyo akafuna kupeleka uphungu, amazika uphunguwo m’Mawu a Mulungu. Amakamba mosapita m’mbali koma mokoma mtima, cifukwa amafuna kuti opatsidwa uphunguwo aulandile na kuuseŵenzetsa.—Agal. 6:1. w22.03 28-29 ¶11-12

Cisanu, November 3

Tili ndi cuma cimeneci m’zonyamulila zoumbidwa ndi dothi, kuti mphamvu yoposa yacibadwa icokele kwa Mulungu, osati kwa ife.—2 Akor. 4:7.

Masiku ano, Yehova amapatsa anthu ake “mphamvu yoposa yacibadwa” kuti apitilize kum’tumikila mokhulupilika. Njila imodzi imene amatilimbikitsila, ni kupitila m’pemphelo. Malinga na Aefeso 6:18, mtumwi Paulo akutilangiza kuti tizipemphela kwa Mulungu “pa cocitika ciliconse.” Ndipo Mulungu adzatilimbikitsadi. Nthawi zina tingaone kuti mavuto atikulila msinkhu kapena sitingadziŵe zofunikila kuchula m’pemphelo. Koma Yehova amatipempha kuti tizipemphela kwa iye ngakhale pamene zativuta kufotokoza bwino-bwino mmene tikumvelela. (Aroma 8:26, 27) Iye amatilimbikitsanso kupitila m’Baibo. Paulo anali kudalila pa Malemba kuti amupatse mphamvu na citonthozo. Nafenso tingawadalile. (Aroma 15:4) Pamene tiŵelenga Mawu a Mulungu na kuwasinkha-sinkha, Yehova mwa mzimu wake, angatithandize kumvetsa bwino mmene Malemba angatithandizile.—Aheb. 4:12. w21.05 22 ¶8-10

Ciŵelu, November 4

Mulungu . . . amalimbitsa zolakalaka zanu kuti mucite zinthu zonse zimene iye amakonda.—Afil. 2:13.

Sitiona mopepuka nchito yathu yophunzitsa, ngakhale kuti timakumana na zopinga zimene zingatilepheletse kutengako mbali mmene tifunila m’nchito yopanga ophunzila. Mwina timaona kuti sitingakwanitse kucita zambili cifukwa ca mmene zinthu zilili kwa ife. Mwacitsanzo, ofalitsa ena ni okalamba kapena ali na thanzi lofooka. Kodi ndiye mmene zinthu zilili kwa inu? Ngati n’telo, taphunzila kuti tingatsogoze maphunzilo a Baibo kupitila pa zipangizo zamakono! Conco mungayambitse phunzilo la Baibo na kulitsogoza muli m’nyumba mwanu. Koma palinso phindu lina pamenepa. Ena amafuna kuphunzila Baibo, koma sapezeka pa nyumba pa nthawi imene abale athu anapatula kuti azilalikila. Komabe, ena amapezeka pa nyumba m’mawa kwambili kapena m’madzulo kwambili. Kodi mungakonze zakuti muziphunzila Baibo na munthu wina pa nthawi ngati zimenezi? Yesu anaphunzitsa Nikodemo usiku, nthawi imene Nikodemo anaona kuti inali bwino kwa iye.—Yoh. 3:1, 2. w21.07 5 ¶10-11

Sondo, November 5

Popeza anthu awa ayandikila kwa ine ndi pakamwa pawo pokha, ndipo andilemekeza ndi milomo yawo yokha koma mtima wawo auika kutali ndi ine.—Yes. 29:13.

Ophunzila a Yohane M’batizi anadabwa cifukwa ophunzila a Yesu sanali kusala kudya. Yesu anafotokoza kuti panalibe cifukwa cosalila kudya cifukwa iye anali akali na moyo. (Mat. 9:14-17) Ngakhale n’telo, Afarisi na otsutsa ena anamuimba mlandu Yesu cifukwa sanali kutsatila miyambo yawo. Iwo anakwiya pamene Yesu anasankha kucilitsa odwala pa Sabata. (Maliko 3:1-6; Yoh. 9:16) Anali kukamba kuti amalemekeza Sabata, koma anali kuona kuti palibe vuto kucita malonda m’kacisi. Iwo anakwiya kwambili Yesu atawadzudzula kaamba ka zimenezo. (Mat. 21:12, 13, 15) Ndipo pamene Yesu anali kulalikila anthu m’sunagoge ku Nazareti, anthuwo anakwiya kwambili iye atapeleka zitsanzo zokhudza mbili ya Aisiraeli, zimene zinavumbula kuti iwo anali anthu odzikonda komanso opanda cikhulupililo. (Luka 4:16, 25-30) Anthu ambili anapunthwa cifukwa Yesu sanacite zimene iwo anali kuyembekezela.—Mat. 11:16-19. w21.05 5-6 ¶13-14

Mande, November 6

Tikudziŵa bwino ziwembu zake.—2 Akor. 2:11.

Imodzi mwa njila zimene Yehova amaticenjezela za kunyada komanso dyela, ni mwa kutilimbikitsa kuphunzila ku zimene zinacitikila ena. Tikaganizila za dyela, mwina mwamsanga Satana Mdyelekezi ndiye amabwela m’maganizo. Pokhala mmodzi wa angelo a Yehova, Satana ayenela kuti anali na maudindo ambili abwino. Koma anali kufunanso zina. Anali kufuna kuti nayenso azilambilidwa, pamene ni Yehova yekha woyenela kulambilidwa. Satana amafuna tikhale monga iye. Conco, amayesa kutipangitsa kukhala osakhutila na zimene tili nazo. Ulendo woyamba pamene anayesa kucita zimenezi, m’pamene anakamba na Hava. Yehova mwacikondi anapatsa Hava na mwamuna wake zakudya za mwana alilenji zokhutilitsa—‘zipatso za mtengo uliwonse wa m’mundamo’ kupatulapo cabe mtengo umodzi. (Gen. 2:16) Ngakhale n’telo, Satana anapusitsa Hava mwa kum’pangitsa kuganiza kuti anafunikiladi kudya cipatso ca mu mtengo umodziwo woletsedwa. Hava analephela kuyamikila zimene anali nazo, anali kufunanso zina. Tidziŵa zotsatila zimene zinacitika. Hava anacimwa ndipo pothela pake anamwalila.—Gen. 3:6, 19. w21.06 14 ¶2-3; 17 ¶9

Ciŵili, November 7

Mubelekane, muculuke, mudzaze dziko lapansi, ndipo muliyang’anile.—Gen. 1:28.

Adamu na Hava anafunikila kukhala na ŵana, komanso kusamalila malo awo okhala. Ngati iwo akanacita zinthu mogwilizana na colinga ca Yehova, iwo pamodzi na mbadwa zawo akanakhalabe m’banja la Mulungu kwamuyaya. Adamu na Hava anali na malo olemekezeka m’banja la Yehova. Ponena za mmene Yehova analengela munthu, pa Salimo 8:5 komanso mawu amunsi, Davide anati: “Munamucepetsa pang’ono poyelekeza ndi angelo, kenako munamuveka ulemelelo ndi ulemu monga cisoti cacifumu.” N’zoona kuti anthu sanapatsidwe mphamvu, nzelu, komanso maluso, olingana na angelo. (Sal. 103:20) Ngakhale n’telo, anthu ni ‘ocepako pang’ono’ powayelekezela na angelo amphamvu. Koma n’zacisoni kuti Adamu na Hava, anataya malo awo m’banja la Yehova. Izi zinabweletsa mavuto aakulu kwa mbadwa zake. Koma colinga ca Yehova sicinasinthe. Iye afuna kuti anthu omvela akakhale ana ake kwamuyaya. w21.08 2-3 ¶2-4

Citatu, November 8

“Sipakufunika gulu lankhondo, kapena mphamvu, koma mzimu wanga,” watelo Yehova.—Zek. 4:6.

Masiku ano, atumiki a Yehova ambili amatsutsidwa. Mwacitsanzo, ena amakhala ku maiko amene nchito yathu ni yoletsedwa, ndipo iwo angamangidwe na ‘kuwatengela kwa abwanamkubwa na mafumu,’ kuti ukhale umboni kwa iwo. (Mat. 10:17, 18) Mboni zina zimakumana na citsutso cosiyanako. Zimatsutsidwa na a m’banja mwawo amene akuyesetsa kuwaletsa kutumikila Mulungu, ngakhale kuti m’dziko limene akukhala muli ufulu wolambila Yehova. (Mat. 10:32-36) Nthawi zambili, otsutsawo amaleka kutsutsa abale awo akaona kuti alephela kuwaletsa kutumikila Mulungu wawo. Ndipo nthawi zina, aja amene anali otsutsa kwambili afika pokhala Mboni zokangalika. Motelo, mukakumana na citsutso, musafooke. Khalani wolimba mtima, cifukwa Yehova na mzimu wake woyela wamphamvu ali ku mbali yanu. Conco, palibe cifukwa coopela. w22.03 16 ¶8

Cinayi, November 9

Inu okonda Yehova danani naco coipa.—Sal. 97:10.

Baibo imati Yehova amadana na “maso odzikweza, lilime lonama, [komanso] manja okhetsa magazi a anthu osalakwa.” (Miy. 6:16, 17) Iye amadananso na “munthu wacinyengo.” (Sal. 5:6) Yehova amadana nawo kwambili makhalidwe amenewa moti m’nthawi ya Nowa, anaseselatu anthu oipa cifukwa anali atadzadza dziko lonse na ciwawa. (Gen. 6:13) Cina, kupitila mwa mneneli Malaki, Yehova anakamba kuti amadana na anthu amene amasemela akazi awo mlandu wabodza n’colinga cakuti asudzulane. Mulungu salandila kulambila kwawo, ndipo adzawaweluza pa khalidwe lawo loipalo. (Mal. 2:13-16; Aheb. 13:4) Yehova amafuna kuti ‘tizinyansidwa na coipa.’ (Aroma 12:9) Mawu akuti ‘kunyansidwa’ naco cinthu, amatanthauza kudana naco kwambili, ngakhalenso kucita naco mselu. Conco, tiyenela kunyansidwa na maganizo ofuna kucita cimene Yehova amati n’coipa. w22.03 4-5 ¶11-12

Cisanu, November 10

Odala ndi anthu onse amene amamuyembekezela.—Yes. 30:18.

Posacedwa, Atate wathu wa kumwamba adzatidalitsa kudzela mu Ufumu wake. Onse oyembekezela pa Yehova, adzalandila madalitso pali pano komanso m’dziko latsopano limene likubwela. Anthu a Mulungu akakaloŵa m’dziko latsopano, sadzakhalanso na nkhawa, kapena mavuto amene amakumana nawo masiku ano. Zopanda cilungamo zidzatha, ndipo zopweteka sizidzakhalaponso. (Chiv. 21:4) Sitidzakhalanso na nkhawa ya kusapeza zimene tifunikila, cifukwa zidzakhalapo zoculuka. (Sal. 72:16; Yes. 54:13) Zidzakhala zokondweletsa zedi! Koma pali pano, Yehova akutikonzekeletsa umoyo watsopano pansi pa ulamulilo wake, potithandiza kugonjetsa zizoloŵezi zoipa na kukulitsa makhalidwe aumulungu. Musataye mtima, ndipo musalefuke. Umoyo wabwino uli patsogolo. Pamene tikuyembekezela tsogolo labwino, tiyeni tipitilize kuyembekezela Yehova moleza mtima pamene iye akutsiliza nchito yake! w21.08 13 ¶17-19

Ciŵelu, November 11

Musaiŵale kucita zabwino ndi kugaŵana zinthu ndi ena, pakuti nsembe zotelo Mulungu amakondwela nazo.—Aheb. 13:16.

Pasanapite nthawi yaitali kucokela pamene analandila kalata ya mtumwi Paulo, Akhristu ku Yudeya anafunika kusiya nyumba zawo, mabizinesi awo, na acibale awo osakhulupilila na kuyamba ‘kuthaŵila kumapili.’ (Mat. 24:16) Pa nthawiyo, kunali kofunikila kwambili kuti iwo azithandizana. Ngati iwo anali kutsatila malangizo a Paulo asanayambe kuthaŵila ku mapili, cinali cosavuta kwa iwo kukhala na umoyo wosalila zambili. Si nthawi zonse pamene abale na alongo athu angatiuze za zosoŵa zawo zakuthupi. Conco, khalani wofikilika. Mosakayikila, mudziŵako abale na alongo mu mpingo mwanu amene nthawi zonse ni okonzeka kuthandiza ena. Iwo satipangitsa kuona kuti ndife mtolo kwa iwo. Timadziŵa kuti iwo ni ofunitsitsa kutithandiza pa nthawi ya mavuto, ndipo timafuna kutengela citsanzo cawo. w22.02 23-24 ¶13-15

Sondo, November 12

[Sungani] umodzi wathu mwa mzimuwo, ndi mwamtendele monga comangila cotigwilizanitsa. —Aef. 4:3.

M’zaka zaposacedwa, mipingo yambili aiphatikiza pamodzi, ndipo izi zapangitsa kuti mipingo ina iloŵe m’dela lina. Akatipempha kusamukila ku mpingo watsopano, cingativute kusiya mabwenzi athu na acibale. Kodi akulu amalandila malangizo mwacindunji kucokela kwa Mulungu owauza mpingo kumene wofalitsa aliyense ayenela kupitako? Ayi. Pa cifukwa cimeneci, cingakhale covuta kutsatila malangizo amene tapatsidwa. Koma Yehova amawakhulupilila akuluwo kuti adzapanga zigamulo zoyenela. Nafenso tiziwakhulupilila. N’cifukwa ciani tiyenela kugwilizana na akulu, na kucilikiza zigamulo zawo ngakhale kuti sitinazikonde? Cifukwa kucita zimenezo, kumathandiza kusungitsa mtendele pakati pa anthu a Mulungu. Mpingo umapita bwino patsogolo, ngati onse modzicepetsa amacilikiza zigamulo za bungwe la akulu. (Aheb. 13:17) Coposa zonse, timaonetsa Yehova kuti timam’khulupilila tikamagwilizana na aja amene iye wasankha kuti atiyang’anile.—Mac. 20:28. w22.02 4-5 ¶9-10

Mande, November 13

Pitiliza kukhala wodzipeleka poŵelenga pamaso pa anthu, powadandaulila, ndi powaphunzitsa.—1 Tim. 4:13.

Ngati ndinu m’bale wobatizika, mungadziikile colinga cokhala mphunzitsi waluso. Cifukwa ciani? Cifukwa ngati ‘mudzipeleka’ pa kuŵelenga na kuphunzitsa, mudzakhala dalitso kwa omvela anu. (1 Tim. 4:15) Dziikileni colinga coŵelenga na kuseŵenzetsa phunzilo lililonse m’bulosha lakuti, Citani Khama pa Kuŵelenga na Kuphunzitsa. Ŵelengani phunzilo limodzi palokha, kuliyeseza mofikapo pamene muli kunyumba, komanso kuwaseŵenzetsa malangizowo pokamba nkhani. Funsilankoni malingalilo kwa mlangizi wothandiza, kapena kwa akulu ena “amene amacita khama kulankhula ndi kuphunzitsa.” (1 Tim. 5:17) Musamangofuna kudziŵa cabe malangizo a m’buloshayo, komanso muziyesetsa kuthandiza omvela anu kulimbitsa cikhulupililo cawo, komanso kuwalimbikitsa kugwilitsila nchito zimene aphunzila. Mwa kutelo, mudzawonjezela cimwemwe canu komanso cawo. w21.08 24 ¶17

Ciŵili, November 14

Modzicepetsa, [muziona] ena kukhala okuposani. —Afil. 2:3.

Ngati timaona ena kukhala otiposa, tidzapewa kupikisana na abale athu amene ali na maluso kuposa ife. M’malo mopikisana nawo, tidzasangalalila nawo limodzi, maka-maka ngati akuseŵenzetsa maluso awo potumikila Yehova. Tikatelo, tonsefe tidzalimbikitsa mtendele na mgwilizano mu mpingo. Ngati tikhala odzicepetsa mwa kuzindikila kuti pali zina zimene sitingakwanitse kucita, tidzakwanitsa kuthetsa kaduka. Ngati ndife odzicepetsa, sitidzadziona kuti timacita bwino kuposa ena. M’malo mwake, tidzayesetsa kuphunzilako kwa ena amene acita bwino kuposa ife. Mwacitsanzo, tinene kuti m’bale mu mpingo amapeleka nkhani zotentha za anthu onse. Tingam’funse mmene amakonzekelela nkhani zake. Ngati mlongo amadziŵa kuphika bwino, tingam’funse kuti atiuzeko mophikila bwino. w21.07 16 ¶8-9

Citatu, November 15

[Yehova] sacita cosalungama.—Deut. 32:4.

M’buku la Numeri, timaŵelenga kuti Yehova anaweluza kuti Mwisiraeli wina aphedwe cifukwa cotola nkhuni pa Sabata. Koma patapita zaka, m’buku la Samueli waciŵili timaphunzila kuti Yehova anakhululukila Mfumu Davide atacita cigololo, komanso kupha munthu. (Num. 15:32, 35; 2 Sam. 12:9, 13) Mwina tingafunse kuti, ‘N’cifukwa ciani Yehova anakhululukila Davide atacita cigololo komanso kupha munthu, koma anaweluza kuti munthu aphedwe pa chimo looneka laling’ono?’ Si nthawi zonse pamene Baibo imafotokoza zonse zokhudza nkhani. Mwacitsanzo, tidziŵa kuti Davide analapa macimo ake mocokela pansi pa mtima. (Sal. 51:2-4) Koma bwanji za munthu amene anaphwanya lamulo la Sabata? Kodi iye anali munthu wotani? Kodi anamva cisoni pa zimene anacita? Kodi anaphwanyapo malamulo a Yehova kumbuyoko? Kodi ananyalanyazapo macenjezo, ngakhale kuwakana? Baibo sikamba. Komabe, tidziŵa kuti Mulungu wathu “ndi wolungama m’njila zake zonse.”—Sal. 145:17. w22.02 2-3 ¶3-4

Cinayi, November 16

Nzelu zimakhala ndi anthu odzicepetsa.—Miy. 11:2.

Munthu wodzicepetsa sayembekezela kucita zimene sangakwanitse. Izi zimam’thandiza kukhala wacimwemwe komanso wokangalika. Munthu wodzicepetsa tingamuyelekezele na dalaivala amene akuyendetsa motoka pa makata. Dalaivala amabwezako magiya kuti apitilize kuyenda mpaka atafika ku msondo. N’zoona kuti adzayendetsa motokayo pang’ono-pang’ono, koma adzapitilizabe ulendo wake. Mofananamo, munthu wodzicepetsa amadziŵa nthawi yoyenela “kubweza magiya,” n’colinga cakuti apitilize kutumikila Yehova na kuthandiza ena. (Afil. 4:5) Ganizilani citsanzo ca Barizilai. Iye anali na zaka 80 pamene Mfumu Davide anam’pempha kuti akakhale naye ku nyumba ya mfumu. Cifukwa ca kudzicepetsa, Barizilai anakana pempho la mfumu limeneli. Podziŵa zimene sangakwanitse kucita, Barizilai anapempha kuti wacinyamata Chimamu apite m’malo mwa iye. (2 Sam. 19:35-37) Mofanana na Barizilai, okalamba amakondwela kupatsa mwayi acinyamata wakuti atumikile. w21.09 10 ¶6-7

Cisanu, November 17

Palibe amene akum’dziŵa bwino Mwana koma Atate okha. Komanso Atatewo palibe amene akuwadziŵa bwino koma Mwana yekha ndiponso amene Mwanayo wakonda kuwaululila za Atatewo.—Luka 10:22.

Kodi cimakuvutani kuona Yehova kuti ni Tate wacikondi? Ni mmene zilili kwa ena a ife. Cimakhaladi covuta makamaka ngati atate athu akuthupi anali kuticitila nkhanza. Koma n’zolimbikitsa kudziŵa kuti Yehova amamvetsa mmene timvelela. Iye amafuna kukhala nafe pafupi. Ndiye cifukwa cake Baibo imatilimbikitsa kuti: “Yandikilani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikilani.” (Yak. 4:8) Yehova amatikonda, ndipo amatiuza kuti adzakhala Atate wathu wabwino koposa. Yesu angatithandize kuyandikila Yehova. Iye amam’dziŵa bwino Yehova, ndipo anatengela ndendende makhalidwe a Atate wake cakuti anati: “Amene waona ine waonanso Atate.” (Yoh. 14:9) Pokhala woyamba kubadwa, Yesu amatiphunzitsa mmene tingalemekezele Atate wathu na kuwamvela, mmene tingapewele kuwakhumudwitsa, komanso zimene tingacite kuti atiyanje. Koma umoyo wa Yesu padziko lapansi maka-maka, unaonetsa kuti Yehova ni wacikondi komanso wokoma mtima. w21.09 21 ¶4-5

Ciŵelu, November 18

Wetani gulu la nkhosa za Mulungu lomwe analisiya m’manja mwanu.—1 Pet. 5:2.

Anthu a Yehova ni ogwilizana pa kulambila Mulungu yekha woona. Yehova anapatsa akulu udindo waukulu kwambili wosunga mpingo kukhala woyela. Ngati Mkhristu wacita chimo lalikulu, Yehova amafuna kuti akulu aipende mosamala nkhaniyo, na kuona ngati munthuyo angakhalebe mu mpingo. Mwa zina, ayenela kuona ngati munthuyo ni wolapadi zenizeni pa zimene anacita. Iye angakambe kuti ni wolapa, koma kodi amadanadi na zimene anacitazo? Kodi watsimikiza mtima kuti sadzabwelezanso chimolo? Koma ngati kuyanjana na anthu osayenela ndiko kunam’pangitsa kuti agwele m’chimolo, kodi ni wokonzeka kudula mayanjano ake na anthu amenewo? Akulu amapemphela kwa Yehova, amaganizila zimene Baibo imakamba pa nkhaniyo, ndipo amaona mmene wolakwayo akumvelela pa zimene anacita. Ndiyeno, amagamula ngati iye angakhalebe mu mpingo. Nthawi zina, wolakwayo angafunike kucotsedwa mu mpingo.—1 Akor. 5:11-13. w22.02 5 ¶11-12

Sondo, November 19

Muvale umunthu watsopano. —Akol. 3:10.

Kaya tinabatizika caposacedwa kapena kwa zaka zambili, tonsefe tiyenela kukhala na umunthu umene Yehova amakonda. Kuti tikhale nawo, tiyenela kulamulila kaganizidwe kathu. Cifukwa ciyani? Cifukwa kambili, maganizo athu ndiwo amaumba umunthu wathu. Ngati nthawi zonse timaganizila mmene tingakhutilitsile zolakalaka zathu za kuthupi, tingakambe na kucita zinthu zoipa. (Aef. 4:17-19) Koma ngati tidzaza maganizo athu na zinthu zabwino, tidzakamba na kucita zinthu m’njila imene imakondweletsa Atate wathu, Yehova. (Agal. 5:16) Komabe, sitingaletseletu maganizo onse oipa kuloŵa mumtima mwathu. Koma tingasankhe kusacita zimene tikuganizazo. Tisanabatizike, tiyenela kuleka kukamba zinthu zimene Yehova amadana nazo, komanso kusazicita. Iyi ndiye sitepu yoyamba ndiponso yofunika kwambili kuti tivule umunthu wakale. Komabe, kuti tim’kondweletse kwambili Yehova, tiyenelanso kuvala umunthu watsopano. w22.03 8 ¶1-2

Mande, November 20

Mwanjila ina iliyonse, munasonyeza kuti ndinu oyela pa nkhani imeneyi.—2 Akor. 7:11.

Si copepuka kwa akulu kudziŵa ngati munthu amene anacita chimo lalikulu, analapadi mocokela pansi pamtima. Cifukwa ciani? Cifukwa akulu sangakwanitse kudziŵa za mu mtima mwa munthu. Conco, iwo amadalila zimene aona na maso kuti adziŵe ngati m’bale kapena mlongo ni wolapadi. Iwo adzafuna kuona umboni woonetsa kuti wocimwayo anasintha zenizeni kaganizidwe kake, mmene amaonela zinthu, na khalidwe lake. Pangafunike nthawi yokwanila kuti munthuyo apange masinthidwe ofunikila. Kuti munthu wocotsedwa aonetse kuti walapa zenizeni, ayenela kupezeka ku misonkhano nthawi zonse, komanso kucita zimene akulu anamulangiza kuti azipemphela nthawi zonse na kuŵelenga Baibo. Ayenelanso kucita khama kuti apewe zinthu zimene zinam’tsogolela ku chimolo. Ngati wayesetsa kukonza ubale wake na Yehova, iye ayenela kutsimikiza kuti Yehova adzamukhululukila, ndipo akulu adzamubwezeletsa mu mpingo. w21.10 6 ¶16-18

Ciŵili, November 21

Usadzipangile fano kapena cifanizilo ca cinthu ciliconse cakumwamba, kapena capadziko lapansi . . . Usaziwelamile.—Eks. 20:4, 5.

Cifukwa cokonda kwambili Mulungu, Yesu anali kulambila Yehova yekha basi, ali kumwamba komanso atabwela padziko lapansi. (Luka 4:8) Anauzanso ophunzila ake kuti azilambila Yehova yekha. Yesu komanso ophunzila ake, sanali kugwilitsila nchito zifanizilo polambila. Popeza Mulungu ni mzimu, palibe cimene munthu angapange cimene cingafanane naye m’maonekedwe. (Yes. 46:5) Nanga bwanji za kupanga zifanizilo za anthu amene amati ni oyela mtima, na kuyamba kupemphela ku zifanizilo zimenezo? Lamulo laciŵili pa Malamulo Khumi, Yehova anakamba mawu a mu lemba la tsiku lalelo. Anthu ofuna kukondweletsa Mulungu, amadziŵa kuti iye safuna kuti tizilambila mafano. Olemba mbili yakale anati Akhristu oyambilila anali kulambila Mulungu yekha basi. Masiku ano, Mboni za Yehova zimatsatila mmene Akhristu a m’zaka za zana loyamba anali kulambilila. w21.10 19-20 ¶5-6

Citatu, November 22

Munthu amene ali padenga la nyumba asadzatsike kukatenga katundu m’nyumba mwake.—Mat. 24:17.

Yesu anacenjeza Akhristu oyambilila a ku Yudeya kuti nthawi ikadzafika, ‘magulu ankhondo azazungulila’ mzinda wa Yerusalemu. (Luka 21:20-24) Izi zikadzacitika, iwo anayenela ‘kuthaŵila kumapili.’ Kuthaŵa kumeneko kukanapulumutsa miyoyo yawo, koma anafunika kusiya zinthu zawo zambili. Zaka zambili kumbuyoko, Nsanja ya Mlonda ina inati: “Iwo anasiya minda, nyumba, osatenga ngakhale katundu wawo m’nyumba zawo. Pokhala na cidalilo cakuti Yehova adzawateteza na kuwathandiza, iwo anaika kulambila Mulungu patsogolo pa cina ciliconse cooneka ngati cofunika kwambili.” Nsanjayo inatinso: “M’tsogolomu tingadzakumane na mayeso okhudza mmene timaonela zinthu zakuthupi. Kodi zinthuzo ndiye zofunika kwambili, kapena kodi cipulumutso ndiye cofunika koposa cifukwa cakuti tili ku mbali ya Mulungu? Inde, mapeto akadzafika, tingafunike kukapilila mavuto na kukhala odzimana. Tidzayenela kukhala okonzeka kucita zonse zotheka.” w22.01 4 ¶7-8

Cinayi, November 23

Inu Mulungu, kukoma mtima kwanu kosatha ndi kwamtengo wapatali!—Sal. 36:7.

Pasanapite nthawi yaitali Aisiraeli atacoka ku Iguputo, Yehova anadzidziŵikitsa kwa Mose mwa kuchula dzina lake na makhalidwe ake. Iye anati: “Yehova, Yehova, Mulungu wacifundo ndi wacisomo, wosakwiya msanga ndiponso wodzaza ndi kukoma mtima kosatha [“cikondi cosasintha,” NW-E] ndi coonadi. Wosungila mibadwo masauzande kukoma mtima kosatha, wokhululukila zolakwa ndi macimo.” (Eks. 34:6, 7) Pokamba mawu amenewa oonetsa makhalidwe ake, Yehova anauza Mose mbali yapadela yokhudza cikondi cake cosasintha. Ni mbali iti imeneyo? Yehova podzifotokoza, sanangonena kuti ali na cikondi cosasintha [kapena kuti “kukoma mtima kosatha”], koma anati ni “wodzaza ndi kukoma mtima kosatha.” Kafotokozedwe kameneka kamapezekanso nthawi zisanu m’Baibo. (Num. 14:18; Sal. 86:15; 103:8; Yow. 2:13; Yona 4:2) Pa nthawi zonsezi, mawu amenewa amakamba za Yehova yekha basi osati anthu. Kodi izi si zocititsa cidwi kuti Yehova amaligogomeza kwambili khalidwe lake limeneli? w21.11 2-3 ¶3-4

Cisanu, November 24

Lekani kudela nkhawa moyo wanu.—Mat. 6:25.

Amene anali pa banja angatenge phunzilo pa citsanzo ca mtumwi Petulo na mkazi wake. Patapita miyezi pafupi-fupi 6 pambuyo poonana na Yesu koyamba, mtumwi Petulo anafunika kupanga cisankho cacikulu. Petulo anali kugwila nchito ya usodzi kuti azisamalila banja lake. Koma Yesu atamuitana kuti azimutsatila nthawi zonse, iye anafunika kuganizila mkazi wake asanapange cisankho cimeneci. (Luka 5:1-11) Petulo anasankha kugwila nchito yolalikila pamodzi na Yesu. Ndipo sitikayikila kuti mkazi wake anagwilizana na cisankho cimeneci. Baibo imaonetsa kuti pambuyo pakuti Yesu waukitsidwa, Petulo anapita na mkazi wake maulendo angapo kukalalikila. (1 Akor. 9:5) Mosakayikila, citsanzo cake monga mkazi wacikhristu cinathandiza Petulo kukhala na ufulu wa kulankhula pamene anapeleka malangizo kwa amuna na akazi acikhristu. (1 Pet. 3:1-7) Mwacionekele, Petulo na mkazi wake anali kukhulupilila lonjezo la Yehova lakuti adzawasamalila ngati aika Ufumu wake patsogolo.—Mat. 6:31-34. w21.11 18 ¶14

Ciŵelu, November 25

Muzitsanzila ine.—1 Akor. 11:1.

Mtumwi Paulo anali kuwakonda abale ake. Iye anagwila nchito molimbika kuti awathandize. (Mac. 20:31) Pa cifukwa cimeneci, nawonso alambili anzake anali kum’konda ngako. Pa nthawi ina, akulu a ku Efeso “analila kwambili” atadziŵa kuti sadzamuonanso Paulo. (Mac. 20:37) Nawonso akulu odzipeleka amawakonda kwambili abale na alongo awo, ndipo amayesetsa kuwathandiza. (Afil. 2:16, 17) Koma nthawi zina, akulu amakumana na zovuta. N’ciyani cingawathandize kugonjetsa zovutazo? Akulu ogwila nchito molimbika amenewa, angacite bwino kuganizila citsanzo ca Paulo. Iye sanali monga angelo, koma anali munthu wopanda ungwilo amene nthawi zina anali kuvutika kucita zoyenela. (Aroma 7:18-20) Pamwamba pa izi, anali kulimbana na mavuto ena. Koma Paulo sanalefuke kapena kutaya cimwemwe. Potengela citsanzo cake, akulu angagonjetse zovuta zimene amakumana nazo, na kukhalabe acimwemwe potumikila Yehova. w22.03 26 ¶1-2

Sondo, November 26

Muzisunga masabata anga. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.—Lev. 19:3.

Levitiko 19:3, imakamba za kusunga Sabata. Ife Akhristu sitili pansi pa Cilamulo. N’cifukwa cake sitisunga Sabata mlungu uliwonse. Ngakhale n’telo, tingaphunzile zambili poona mmene Aisiraeli anali kusungila Sabata, ndiponso mmene anali kupindulila akacita zimenezo. Sabata inali nthawi yopumula ku nchito za kuthupi, kuti munthu asumike maganizo ake pa zauzimu. Ndiye cifukwa cake, pa tsikuli Yesu anali kupita ku sunagoge m’tauni ya kwawo kukaŵelenga Mawu a Mulungu. (Eks. 31:12-15; Luka 4:16-18) Lamulo la Mulungu la pa Levitiko 19:3 la ‘kusunga masabata,’ liyenela kutipangitsa kupatula nthawi ku zocita zathu za tsiku na tsiku, kuti tikhale na nthawi yoculuka yocita zauzimu. Kodi muona kuti muyenela kuwongolela pa mbali imeneyi? Nthawi zonse mukamapatula nthawi yocita zauzimu, mudzakhala pa ubale wolimba na Yehova, umene ni wofunika ngako kuti mukhale woyela. w21.12 5 ¶13

Mande, November 27

Ine sindinabwele kudzaitana anthu olungama, koma ocimwa kuti alape.—Luka 5:32.

Ali padziko lapansi, Yesu anali kuyanjana na anthu a zikhalidwe zonse. Iye anali kudya pamodzi na anthu olemela ndiponso aulamulilo. Koma analinso kuceza kwambili na anthu osauka, komanso opondelezedwa. Kuwonjezela apo, iye anali kucitila cifundo anthu amene anali kuonedwa ngati “ocimwa.” Anthu ena odzilungamitsa anakhumudwa na zimene Yesu anacita. Iwo anafunsa ophunzila ake kuti: “N’cifukwa ciani inu mumadya ndi kumwa limodzi ndi okhometsa msonkho ndi anthu ocimwa?” Poyankha funso limeneli Yesu anawauza mawu a lemba la tsiku lalelo. (Luka 5:29-31) Kukali zaka Mesiya asanabwele, mneneli Yesaya anafotokoza kuti iye adzakanidwa na anthu a m’dziko. Ulosiwo unati: “Iye ananyozedwa ndipo anthu anali kumupewa . . . Ife tinali kuyang’ana kumbali kuti tisaone nkhope yake. Ananyozedwa ndipo tinamuona ngati wopanda pake.” (Yes. 53:3) Mesiya anali kudzakanidwa na “anthu.” Conco Ayuda a m’nthawi ya atumwi anafunika kuyembekezela kuti Yesu adzakanidwa. w21.05 8-9 ¶3-4

Ciŵili, November 28

Yehova adzamulimbitsa.—Yak. 5:15.

Akhristu ena oyambilila anali kucedwa kumvela uphungu. (Yak. 1:22) Ena anali kukondela anthu olemela. (Yak. 2:1-3) Ndipo enanso cinali kuwavuta kulamulila lilime lawo. (Yak. 3:8-10) Akhristu amenewo anali na mavuto aakulu, koma Yakobo sanatope nawo. Iye anapeleka uphungu mokoma mtima koma mosapita m’mbali, ndipo analimbikitsa odwala mwauzimu kupempha thandizo kwa akulu. (Yak. 5:13, 14) Zimene tiphunzilapo: Athandizeni mosapita m’mbali, koma muziwaonabe moyenelela. Ambili amene timaphunzila nawo Baibo angamavutike kucita zimene amaphunzila. (Yak. 4:1-4) Pangatenge nthawi kuti azule makhalidwe oipa, na kukulitsa makhalidwe acikhristu. Tiyenela kulimba mtima kuti tiwauze mbali zimene ayenela kuwongolela. Tiyenelanso kukhalabe na maganizo oyenela pa iwo, pokhulupilila kuti Yehova adzakokela anthu odzicepetsa kwa iye, na kuwathandiza kusintha umoyo wawo.—Yak. 4:10. w22.01 11 ¶11-12

Citatu, November 29

Aliyense wotseka khutu lake kuti asamve kudandaula kwa munthu wonyozeka, nayenso adzaitana koma sadzayankhidwa.—Miy. 21:13.

Akhristu onse ayenela kukhala acifundo potengela citsanzo ca Yehova. Cifukwa ciani? Cifukwa cimodzi n’cakuti iye sadzamvetsela mapemphelo a anthu amene sacitila ena cifundo. Palibe angafune kuti Yehova asayankhe mapemphelo ake. Conco, timayesetsa kupewa kukhala opanda cifundo. M’malo motseka makutu kuti tisamve kulila kwa Mkhristu mnzathu, nthawi zonse tiyenela kukhala okonzeka kumva “kudandaula kwa munthu wonyozeka.” Tiziyesetsa kutsatila uphungu wouzilidwa wakuti: “Wosacita cifundo adzaweluzidwa mopanda cifundo.” (Yak. 2:13) Kukumbukila kuti nafenso timafuna kucitilidwa cifundo, kudzatilimbikitsa kuonetsa ena cifundo. Conco, tizicitila cifundo maka-maka wocimwa wolapa akabwelela mu mpingo. Zitsanzo za anthu ochulidwa m’Baibo amene anali okoma mtima komanso acifundo, zingatithandize kukhala acifundo na kupewa kukhala ouma mtima. w21.10 12 ¶16-17

Cinayi, November 30

Khalani pansi pompano, ine ndikupita uko kukapemphela. —Mat. 26:36.

Usiku wothela wa moyo wake padziko lapansi, Yesu anapita ku malo a zii kumene anatha kusinkha-sinkha na kupemphela. Iye anapeza malowo m’munda wa Getsemane. Pa nthawiyo, Yesu anapatsa ophunzila ake malangizo a panthawi yake okamba za pemphelo. Iwo anafika m’munda wa Getsemane usiku kwambili, mwina kudutsa pakati pa usiku. Yesu anauza atumwi ake ‘kukhalabe maso,’ ndipo iye anapita kukapemphela. (Mat. 26:37-39) Koma pamene anali kupemphela, iwo anagona. Atawapeza ali cigonele, Yesu anawauzanso kuti: “Khalani maso ndipo pemphelani kosalekeza.” (Mat. 26:40, 41) Iye anadziŵa kuti ophunzila ake anali opsinjika maganizo kwambili, komanso olema. Yesu anamvetsa kuti “thupi ndi lofooka.” Iye anapitanso maulendo ena aŵili kukapemphela, koma atabwelako anapeza ophunzila ake ali gone m’malo mopemphela.—Mat. 26:42-45. w22.01 28 ¶10-11

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani