LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • es23 masa. 118-128
  • December

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • December
  • Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2023
  • Tumitu
  • Cisanu, December 1
  • Ciŵelu, December 2
  • Sondo, December 3
  • Mande, December 4
  • Ciŵili, December 5
  • Citatu, December 6
  • Cinayi, December 7
  • Cisanu, December 8
  • Ciŵelu, December 9
  • Sondo, December 10
  • Mande, December 11
  • Ciŵili, December 12
  • Citatu, December 13
  • Cinayi, December 14
  • Cisanu, December 15
  • Ciŵelu, December 16
  • Sondo, December 17
  • Mande, December 18
  • Ciŵili, December 19
  • Citatu, December 20
  • Cinayi, December 21
  • Cisanu, December 22
  • Ciŵelu, December 23
  • Sondo, December 24
  • Mande, December 25
  • Ciŵili, December 26
  • Citatu, December 27
  • Cinayi, December 28
  • Cisanu, December 29
  • Ciŵelu, December 30
  • Sondo, December 31
Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2023
es23 masa. 118-128

December

Cisanu, December 1

Zidzamva mawu anga.—Yoh. 10:16.

Yesu anayelekezela ubale wake ndi otsatila ake, na mgwilizano umene umakhalapo pakati pa m’busa na nkhosa zake. (Yoh. 10:14) Mpake kuyelekezela mwa njila imeneyo, cifukwa nkhosa zimadziŵa m’busa wawo, komanso kumvetsela mawu ake. Munthu wina wa paulendo anadzionela yekha zimenezi. Iye anati: “Tinali kufuna kujambula nkhosa. Conco, tinayamba kuziitana kuti zibwele pafupi nafe. Koma nkhosazo sizinabwele pafupi cifukwa sizinali kudziŵa mawu athu. Kenako, panafika m’busa wacicepele. Iye ataziitana, nkhosazo zinayamba kumutsatila.” Cocitika ca munthu wa paulendoyo citikumbutsa mawu a Yesu onena za nkhosa zake, kutanthauza ophunzila ake. Iye anati: “Zidzamva mawu anga.” Popeza Yesu ali kumwamba, kodi tingamvele bwanji mawu ake? Njila yaikulu imene timaonetsela kuti timamvela mawu a Mbuye wathu, ni kucita zimene iye anatiphunzitsa.—Mat. 7:24, 25. w21.12 16 ¶1-2

Ciŵelu, December 2

Onse ndi ocimwa ndipo ndi opelewela pa ulemelelo wa Mulungu.—Aroma 3:23.

Mtumwi Paulo anali wokangalika pozunza Akhristu. Koma pambuyo pake, anavomeleza zolakwa zake, ndipo anali wofunitsitsa kusintha khalidwe lake. (1 Tim. 1:12-16) Na thandizo la Yehova, Paulo anakhala m’busa wacikondi, wacifundo, komanso wodzicepetsa. Anakhulupilila kuti Yehova anam’khululukila, ndipo sanaike maganizo ake pa zophophonya zake. (Aroma 7:21-25) Sanayembekezele kukhala wangwilo. Koma anayesetsa kukulitsa makhalidwe acikhristu, ndipo modzicepetsa anadalila thandizo la Yehova kuti akwanilitse utumiki wake. (1 Akor. 9:27; Afil. 4:13) Akulu ni anthu opanda ungwilo. Ndipo Yehova amafuna kuti iwo azivomeleza zophophonya zawo, komanso kukulitsa makhalidwe acikhristu. (Aef. 4:23, 24) Mkulu ayenela kudzisanthula poseŵenzetsa Mawu a Mulungu, na kupanga masinthidwe ofunikila. Akatelo, Yehova adzam’thandiza kukhala wacimwemwe komanso mkulu wabwino.—Yak. 1:25. w22.03 29-30 ¶13-15

Sondo, December 3

Lekani kuweluza ena. —Mat. 7:1.

Kodi tingacite ciani tikazindikila kuti taweluza Mkhristu mnzathu? Tizikumbukila kuti tiyenela kukonda abale athu. (Yak. 2:8) Tiyenelanso kucondelela Yehova kuti atithandize kuleka kuweluza ena. Tingacite zinthu mogwilizana na mapemphelo athu, mwa kupatula nthawi yoceza na munthu amene tinali kumuweluza. Tingam’pemphe kuti tikaseŵenze naye mu ulaliki, kapena kukadya naye cakudya kwathu. Tikafika pomudziŵa bwino m’bale wathu, tidzayamba kuona zabwino mwa iye potengela citsanzo ca Yehova na Yesu. Tikatelo, tidzaonetsa kuti tikumvela lamulo la m’busa wathu wabwino lakuti tileke kuweluza ena. Monga mmene nkhosa zimamvela mawu a m’busa wawo, nawonso otsatila a Yesu amamvela mawu ake. Kaya ndife a “kagulu ka nkhosa” kapena a “nkhosa zina,” tiyeni tipitilize kumvela mawu a m’busa wabwino.—Luka 12:32; Yoh. 10:11, 14, 16. w21.12 19 ¶11; 21 ¶17-18

Mande, December 4

Iye sanamvele malangizo ocokela kwa akulu. —1 Maf. 12:8.

Rehobowamu atakhala mfumu ya Isiraeli, anthu anabwela kwa iye na kum’pempha kuti awafeŵetseleko goli imene atate wake Solomo anawasenzetsa. Rehobowamu anacita bwino kufunsila nzelu kwa akulu-akulu Aisiraeli kuti adziŵe zimene angayankhe anthuwo. Akuluwo anauza mfumuyo kuti ngati adzacita zinthu zimene anthuwo amupempha, ndiye kuti anthuwo adzam’tumikila nthawi zonse. (1 Maf. 12:3-7) Komabe, Rehobowamu sanakhutile na malangizo amene anapatsidwa. Conco, anapita kukafunsila kwa anthu a msinkhu wake amene anakula naye limodzi. Anamuuza kuti aonjezele goli la anthuwo. (1 Maf. 12:9-11) Rehobowamu akanacita bwino kufunsila kwa Yehova kuti amuthandize kudziŵa malangizo amene ayenela kutsatila. Koma iye anamvela anthu a msinkhu wake. Izi zinabweletsa mavuto aakulu kwa Rehobowamu komanso kwa Aisiraeli. Mofananamo, si nthawi zonse pamene tingakonde malangizo amene tingapatsidwe. Ngakhale n’conco, ngati malangizowo azikika pa mawu a Mulungu, tiyenela kuwatsatila. w22.02 9 ¶6

Ciŵili, December 5

Kukongola kwa anyamata ndiko mphamvu zawo. —Miy. 20:29.

Munthu wodzicepetsa sasumika maganizo ake pa zimene acinyamata sakwanitsa kucita, koma pa mphamvu zawo. Iye sawaona kukhala opikisana nawo, koma monga anchito anzake. Okalamba amaona acinyamata kukhala mphatso yocokela kwa Yehova. Pamene mphamvu zawo zicepela-cepela, iwo amayamikila kuti pali acinyamata amphamvu amene mofunitsitsa amasamalila maudindo mu mpingo. Citsanzo cabwino ngako ca m’Baibo ca wokalamba amene anayamikila thandizo la wacitsikana, ni Naomi. Poyamba, Naomi anauza Rute mpongozi wake wamasiye kubwelela kwawo. Komabe, Rute ataumilila kupita naye Naomi ku Betelehemu, Naomi anayamikila cicilikizo ca Rute ca mtima wonse. (Rute 1:7, 8, 18) Linali dalitso cotani nanga kwa akazi onse aŵiliwa! (Rute 4:13-16) Kudzicepetsa kudzathandiza okalamba kutengela citsanzo ca Naomi. w21.09 10-11 ¶9-11

Citatu, December 6

Mulungu si wosalungama woti angaiŵale nchito yanu ndi cikondi cimene munacisonyeza.—Aheb. 6:10.

Atate wathu wakumwamba amadziŵa zimene aliyense wa ife angathe kucita. Mwina inu mungacite zambili kupambana anzanu. Kapena simungathe kucita zambili mofanana na ena, mwina cifukwa ca ukalamba, matenda, kapena maudindo anu m’banja. Koma musalefuke. (Agal. 6:4) Yehova sadzaiŵala nchito yanu. Iye adzakondwela ngati mukumupatsa zimene mungathe na colinga cabwino. Yehova amaona ngakhale zolinga za mtima wanu. Amafuna kuti mukhale acimwemwe komanso okhutila na zimene mumatha kucita pom’lambila. Tili na mtendele wamaganizo cifukwa timadziŵa kuti Yehova amathandiza alambili ake akakumana na mavuto. (Yes. 41:9, 10) Ndipo tili na zifukwa zabwino zokhalila acimwemwe polambila Atate wathu wacikondi, amene ni woyenela kulandila “ulemelelo ndi ulemu” kucokela ku zolengedwa zake zonse.—Chiv. 4:11. w22.03 24 ¶16; 25 ¶18

Cinayi, December 7

Ndinafulumila ndipo sindinazengeleze kusunga malamulo anu. —Sal. 119:60.

Timafuna kutengela citsanzo ca Yesu. Koma tisalefuke tikalephela kutengela citsanzo cake ndendende. (Yak. 3:2) Kumbukilani kuti wophunzila saposa mphunzitsi wake. Ngakhale n’telo, pamene wophunzilayo akuphunzila zinthu kwa mphunzitsi wake, n’kutheka kuti azilakwitsa zinthu zina. Koma ngati iye aphunzilapo kanthu pa zimene akulakwitsa na kuyesetsa kutengela citsanzo ca mphunzitsi wake, adzakhala akupitabe patsogolo. Mofananamo, tikamaseŵenzetsa zimene timaphunzila m’Baibo, na kuyesetsa kuwongolela mbali zimene timalakwitsa, tidzakwanitsa kutengela citsanzo ca Yesu. (Sal. 119:59) Tikukhala m’dziko lodzala na ŵanthu odzikonda. Koma anthu a Yehova ni osiyana kwambili na iwo. Talimbikitsidwa kuona mzimu wodzimana wa Yesu, ndipo ndife ofunitsitsa kutengela citsanzo cake. (1 Pet. 2:21) Tikamayesetsa kutengela mzimu wodzimana wa Yesu, tidzakhala acimwemwe podziŵa kuti tikukondweletsa Yehova. w22.02 24 ¶16; 25 ¶18

Cisanu, December 8

M’makalata akewo muli zinthu zina zovuta kuzimvetsa.—2 Pet. 3:16.

Njila imodzi imene Yehova amapelekela malangizo kwa anthu ake masiku ano, ni kupitila m’Mawu ake Baibo. Tikamapatula nthawi yosinkhasinkha zimene Yehova amatiphunzitsa, tidzakwanitsa kutsatila malangizo ake, na kukwanilitsa nchito yathu yolalikila. (1 Tim. 4:15, 16) Yehova amapelekanso malangizo kupitila mwa “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu.” (Mat. 24:45) Nthawi zina, kapoloyo angapeleke malangizo amene sitingawamvetsetse. Mwacitsanzo, mwina tingapatsidwe malangizo acindunji otithandiza kukapulumuka ngozi yacilengedwe, imene tingaone kuti singacitike kudela lathu. Kodi tingacite ciyani tikaona kuti malangizo amene tapatsidwa ni osathandiza? Tiyenela kuganizila nkhani za m’Baibo zimene timaŵelenga. Nthawi zina, anthu a Mulungu amalandila malangizo amene mkaonedwe kathu ka umunthu angaoneke osathandiza. Koma pambuyo pake, amakhala opulumutsa moyo.—Ower. 7:7; 8:10. w22.03 18-19 ¶15-16

Ciŵelu, December 9

Atate, ndikuikiza mzimu wanga m’manja mwanu.—Luka 23:46.

Na cidalilo conse, Yesu anakamba mawu a lemba la tsiku lalelo. Iye anadziŵa kuti tsogolo lake linadalila pa Yehova, ndipo anali wotsimikiza kuti Atate wake adzamukumbukila. Kodi tingaphunzile ciani pa mawu a Yesu? Khalani wokonzeka kuika moyo wanu m’manja mwa Yehova. Kuti mucite zimenezo muyenela “kukhulupilila Yehova ndi mtima wanu wonse.” (Miy. 3:5) Ganizilani citsanzo ca mnyamata wina wa Mboni wa zaka 15, dzina lake Joshua, amene anali kudwala matenda akupha. Iye anakana njila zocizila matenda zophwanya lamulo la Mulungu. Atatsala pang’ono kufa, anauza amayi ake kuti: “Amama, nili m’manja mwa Yehova. . . . Cimene ningakuuzeni motsimikiza amama ni ici: Mosakayika konse, Yehova adzaniukitsa ndithu kwa akufa. Iye adziŵa zili mumtima mwanga ndipo nimam’konda kwambili.” Aliyense wa ife angacite bwino kudzifunsa kuti, ‘Ngati cikhulupililo canga cingayesedwe cifukwa cakuti moyo wanga uli paciopsezo, kodi nidzaika moyo wanga m’manja mwa Yehova na kukhulupilila kuti iye adzanikumbukila?’ w21.04 12-13 ¶15-16

Sondo, December 10

Wothilila ena mosaumila nayenso adzathililidwa mosaumila.—Miy. 11:25.

Anthu a Yehova amalimbikitsidwa na ulaliki. Tikamauzako ena mfundo za coonadi ca m’Baibo, timatsitsimulidwa na kupezanso mphamvu kaya anthu amvele uthenga wathu kapena ayi. Cifukwa ca mmene zinthu zilili pa umoyo wawo, ena angaone kuti sangakwanitse kucita zambili mu ulaliki. Ngati umu ni mmene mumamvelela, musaiŵale kuti Yehova amakondwela na zimene mumakwanitsa kucita. Yehova amaona, ndipo amayamikila cikhumbo cathu cofuna kugwila nchito yolalikila, ngakhale pamene sitikutha kucoka panyumba. Iye angatitsegulile mipata yolalikila kwa obwela kudzatisamalila, madokotala, kapena manesi. Ngati tiyelekezela zimene timacita palipano na zimene tinali kucita kale, tingalefuke. Koma ngati tiona mmene Yehova akutithandizila palipano, tidzapeza mphamvu zotithandiza kupilila mayeso alionse mwacimwemwe. Pa mbewu za coonadi zimene timabyala, sitidziŵa kuti n’ziti zimene zingamele na kukula.—Mlal. 11:6. w21.05 24-25 ¶14-17

Mande, December 11

N’cifukwa ciyani unanyoza mawu a Yehova mwa kucita cinthu coipa pamaso pake?—2 Sam. 12:9.

Dyela linapangitsa Mfumu Davide kuiŵala zimene Yehova anam’patsa, kuphatikizapo cuma, kuchuka, na kugonjetsa adani ake ambili pankhondo. Davide moyamikila anavomeleza kuti mphatso za Mulungu ‘zinali zoculuka kwambili moti sakanatha kuzifotokoza.’ (Sal. 40:5) Koma pa nthawi ina Davide anaiŵala zimene Yehova anam’patsa. Olo kuti Davide anali na akazi ambili, analola cilako-lako cosayenela cokhumbila mkazi wa mwini kukula mu mtima mwake. Mkaziyo dzina lake anali Batiseba, ndipo mwamuna wake anali Uriya Mhiti. Modzikonda Davide anagona na Batiseba, ndipo anakhala na pathupi. Zimene anacita Davide zinali zoipa kwambili, koma anacita zoposa pamenepo. Anakonza zakuti Uriya aphedwe! (2 Sam. 11:2-15) Kodi Davide anali kuganiza ciani? Kodi anali kuganiza kuti Yehova sangaone? Mtumiki wa Yehova ameneyo yemwe poyamba anali wokhulupilika, anagwela mu msampha wa dyela ndipo anakumana na mavuto aakulu. Koma condweletsa n’cakuti pambuyo pake, Davide anavomeleza colakwa cake ndipo analapa. Iye anayamikila kwambili kuti wayanjidwanso na Yehova!—2 Sam. 12:7-13. w21.06 17 ¶10

Ciŵili, December 12

Sitinganene kuti ndife oyenela kugwila nchito imeneyi . . . , koma ndife oyenela kugwila nchito imeneyi cifukwa ca Mulungu. —2 Akor. 3:5.

Tingamaone kuti tilibe luso lotsogoza phunzilo la Baibo. Mwina timaona kuti tifunika kukhala na cidziŵitso cacikulu kapena kukhala mphunzitsi waluso tisanayambe kutsogoza phunzilo. Ngati umu ni mmene mumamvelela, onani zinthu zitatu izi zimene zingakuthandizeni kukulitsa cidalilo canu. Coyamba, Yehova amakuona kukhala woyenelela kuphunzitsa ena. Caciŵili, Yesu, amene ali na ‘ulamulilo wonse kumwamba ndi padziko lapansi,’ wakulamulani kuti muziphunzitsa. (Mat. 28:18) Ndipo cacitatu, mungadalile ena kukuthandizani. Yesu anali kudalila zimene Atate wake anam’phunzitsa kukamba, ndipo nanunso mungacite zimenezo. (Yoh. 8:28; 12:49) Kuwonjezela apo, mungapemphe woyang’anila kagulu kanu ka ulaliki, mpainiya wocita bwino, kapena wofalitsa waluso kuti akuthandizeni kuyambitsa phunzilo la Baibo na kulitsogoza. Njila imodzi imene mungakulitsile cidalilo canu, ni kupezekapo pamene ofalitsa amenewa akutsogoza maphunzilo awo a Baibo. w21.07 6 ¶12

Citatu, December 13

Munthu wokhulupilika pa cinthu cacing’ono alinso wokhulupilika pa cinthu cacikulu, ndipo munthu wosalungama pa cinthu cacing’ono alinso wosalungama pa cinthu cacikulu.—Luka 16:10.

Pamene mapeto a dzikoli akuyandikila, tizikhulupilila kwambili mmene Yehova amacitila zinthu kuposa kale lonse. Cifukwa ciani? Cifukwa pa cisautso cacikulu, mwina tingadzalandile malangizo ooneka acilendo, osathandiza, kapena ovuta kuwatsatila. Yehova sadzacita kukamba nafe iye mwini. Mwacionekele, iye adzapeleka malangizowo kupitila mwa anthu osankhidwa omuimilako. Imeneyo sidzakhala nthawi yoyamba kukaikila malangizowo n’kumadzifunsa kuti, ‘Kodi malangizo aya acokeladi kwa Yehova, kapena abale amene akutsogolela angowapanga pa iwo okha?’ Kodi mudzakhulupilila Yehova na gulu lake panthawi yovuta imeneyo? Ngati pali pano timakhulupilila malangizo amene timalandila na kuwatsatila na mtima wonse, tidzakacitanso cimodzi-modzi pa cisautso cacikulu. w22.02 6 ¶15

Cinayi, December 14

Kodi ine ndacita ciyani poyelekeza ndi inu?—Ower. 8:2.

Yehova anathandiza Gidiyoni na asilikali ake 300 kupambana nkhondo. Ndipo izi zikanapangitsa iwo kukhala onyada. Amuna a fuko la Efuraimu anapita kwa Gidiyoni, osati kuti akamuyamikile, koma kuti akakangane naye cifukwa sanawapemphe kuti am’thandize pa nkhondoyo. (Ower. 8:1) Ndiyeno Gidiyoni anawakumbutsa mmene Yehova anawathandizila kumbuyoku. Amunawo atamvela zimenezi, “mkwiyo wawo unaphwa.” (Ower. 8:3) Gidiyoni anadzicepetsa kuti asungitse mtendele pakati pa anthu a Mulungu. Pa citsanzo ca a Efuraimu, tiphunzilapo kuti tiyenela kupewa kudzifunila ulemelelo m’malo molemekeza Yehova. Mitu ya mabanja komanso akulu, tingatengepo phunzilo pa citsanzo ca Gidiyoni. Ngati wina wakhumudwa cifukwa ca zimene tacita, tiyenela kudziŵa cifukwa cake munthuyo wakhumudwa. Cina, tingamuyamikile pa zimene wacita bwino. Koma kuti ticite zimenezi, tiyenela kukhala odzicepetsa. Kukhazikitsa mtendele kuli bwino kuposa kufuna kuonetsa ena kuti ni olakwa. w21.07 16-17 ¶10-12

Cisanu, December 15

Tiyeni tipange munthu m’cifanizilo cathu.—Gen. 1:26.

Yehova anatilemekeza potilenga m’cifanizilo cake. Cifukwa cakuti tinalengedwa m’cifanizilo ca Mulungu, tingathe kukulitsa na kuonetsa makhalidwe abwino, monga cikondi, cifundo, kukhulupilika, komanso cilungamo. (Sal. 86:15; 145:17) Pamene tikulitsa makhalidwe amenewa, timalemekeza Yehova na kuonetsa kuti timamuyamikila. (1 Pet. 1:14-16) Tikamacita zinthu zokondweletsa Atate wathu wakumwamba, timakhala acimwemwe komanso okhutila. Popeza tili na makhalidwe amene Yehova ali nawo, tingathe kukhala mtundu wa anthu amene iye afuna m’banja lake. Yehova anatikonzela malo abwino okhalamo. Kale kwambili, Yehova asanalenge munthu woyamba, anapanga dziko lapansi kuti anthu azikhalamo. (Yobu 38:4-6; Yer. 10:12) Popeza Yehova ni woganizila ena komanso woolowa manja, anakonza zinthu zabwino zambili kuti tizikondwela nazo. (Sal. 104:14, 15, 24) Atayang’ana zinthu zimene anali kulenga, “anaona kuti zili bwino.”—Gen. 1:10, 12, 31. w21.08 3 ¶5-6

Ciŵelu, December 16

Makhalidwe amene mzimu woyela umatulutsa ndiwo cikondi, cimwemwe, mtendele, kuleza mtima, kukoma mtima, ubwino, cikhulupililo, kufatsa ndi kudziletsa. —Agal. 5:22, 23.

Tonsefe tinapatsidwa nchito yolalikila na kupanga ophunzila. (Mat. 28:19, 20; Aroma 10:14) Kodi mungakonde kunola maluso anu pa nchito yofunika ngako imeneyi? Muziŵelenga malangizo a m’bulosha yakuti Kuphunzitsa, ndipo dziikileni zolinga zokuthandizani kuseŵenzetsa zimene mwaphunzila. Pamene mudziikila zolinga zanu, musanyalanyaze cinthu cofunika kwambili—kukulitsa makhalidwe acikhristu. (Akol. 3: 12; 2 Pet. 1:5-8) Mosakayikila, tonsefe timafunitsitsa kucita zambili potumikila Yehova kuposa zimene tikucita pali pano. M’dziko latsopano la Mulungu, tonse tidzam’tumikila mokwanila. Koma pali pano, ngati tiyesetsa kucita zimene tingathe pom’tumikila, tidzawonjezela cimwemwe cathu na kucepetsako maganizo olefula. Ndipo cofunika kwambili, tidzapeleka ulemu na citamando kwa Yehova, “Mulungu [wathu] wacimwemwe.” (1 Tim. 1:11) Conco, tiyeni tizikondwela na mwayi wa utumiki umene tili nawo. w21.08 25 ¶18-20

Sondo, December 17

Aliyense wofika kwa Mulungu ayenela kukhulupilila kuti iye alikodi.—Aheb. 11:6.

Ngati munakulila m’banja la Mboni za Yehova, ndiye kuti mwina munaphunzila za Yehova muli wamng’ono. Munaphunzila kuti iye ni Mlengi, ali na makhalidwe abwino, komanso kuti ali na colinga cabwino kwa anthu. (Gen. 1:1; Mac. 17:24-27) Anthu ambili sakhulupilila kuti Mulungu aliko, kapena kuti iye ndiye Mlengi. M’malo mwake, iwo amakhulupilila kuti moyo unangoyambika wokha. Kenako pang’ono-m’pang’ono, zamoyo zinayamba kusandulika kukhala zamoyo zamitundu yosiyana-siyana. Ndipo ena mwa anthu amenewo amakhala ophunzila kwambili. Iwo amati sayansi yatsimikizila kuti zimene Baibo imakamba si zoona, komanso kuti anthu amene amakhulupilila mwa Mlengi ni mbuli, opanda nzelu, komanso otengeka mosavuta. Kaya takhala Mboni ya Yehova kwa nthawi yaitali bwanji, tonsefe tiyenela kupitiliza kulimbitsa cikhulupililo cathu. Tikatelo, sitidzasoceletsedwa na “nzelu za anthu ndi cinyengo copanda pake,” zimene anthu otsutsa Mawu a Mulungu amaphunzitsa.—Akol. 2:8. w21.08 14 ¶1-3

Mande, December 18

Ndinu woyenela, inu Yehova Mulungu wathu wamphamvu, kulandila ulemelelo ndi ulemu.—Chiv. 4:11.

Abele, Nowa, Abulahamu, komanso Yakobo, anaonetsa ulemu na cikondi kwa Yehova mwa kumumvela, kuika cikhulupililo cawo mwa iye, na kupeleka nsembe. Iwo anacita zimene akanatha kuti alemekeze Yehova, ndipo iye anavomeleza kulambila kwawo. Iye anapatsa mbadwa za Abulahamu Cilamulo ca Mose. Malamulowo anali na malangizo okhudza kulambila Yehova m’njila imene iye amavomeleza. Yesu atafa na kuukitsidwa, Yehova sanafunenso kuti anthu azimulambila motsatila Cilamulo ca Mose. (Aroma 10:4) Akhristu anayenela kutsatila cilamulo catsopano, kutanthauza “cilamulo ca Khristu.” (Agal. 6:2) Iwo anayenela kumvela “cilamulo” cimeneci, osati mwa kutsatila mndandanda wa zoyenela kucita komanso zosayenela, koma mwa kutengela citsanzo ca Yesu na kucita zimene iye anaphunzitsa. Masiku anonso, Akhristu amacita zimene angathe potsatila Khristu kuti akondweletse Yehova, komanso kuti ‘atsitsimulidwe.’—Mat. 11:29. w22.03 20-21 ¶4-5

Ciŵili, December 19

Iye anakhalabe kwayekha m’cipululu ndi kupitiliza kupemphela.—Luka 5:16.

Yehova amamvetsela kwa ana ake. Iye anamvetsela mapemphelo ambili amene Mwana wake woyamba kubadwa anapeleka ali padziko lapansi. Iye anamvetsela pamene Yesu anali kupemphela popanga zisankho zazikulu, monga posankha atumwi ake 12. (Luka 6:12, 13) Yehova anamvetselanso Yesu pamene anali kupemphela ali wopsinjika maganizo. Atatsala pang’ono kupelekedwa, Yesu anapemphela mocokela pansi pamtima kwa Atate wake za mayeso ovuta amene anali kudzakumana nawo. Yehova sanangomvetsela pemphelo la Yesu limenelo, koma anatumanso mngelo kuti akalimbikitse Mwana wake wokondeka. (Luka 22:41-44) Masiku ano, Yehova amapitilizabe kumvetsela mapemphelo a atumiki ake, ndipo amawayankha panthawi yoyenela, komanso m’njila yabwino koposa. (Sal. 116:1, 2) Onani mmene Yehova anayankhila mapemphelo a mlongo wina ku India. Iye anali na vuto la kupsinjika maganizo kwa nthawi yaitali, ndipo anali kupemphela kwa Yehova mocokela pansi pamtima za vutolo. Iye anati: “Pulogilamu ya Broadcasting® ya May 2019, inanilimbikitsa ngako cifukwa inali kukamba za mmene tingagonjetsele nkhawa zathu. Ndipo izi n’zimene n’nali kufunikila pa nthawiyo. Linali yankho la pemphelo langa.” w21.09 21-22 ¶6-7

Citatu, December 20

[Thaŵilani] kumapili.—Luka 21:21.

Tangoganizilani mmene zinalili zovuta kwa Akhristu oyambilila amenewo kusiya pafupifupi zonse anali nazo, na kukayamba umoyo watsopano kumalo acilendo. Zinafuna kuti iwo akhale na cikhulupililo mwa Yehova kuti iye adzawapatsa zofunikila zakuthupi. Onani cinawathandiza. Kukali zaka zisanu kuti Aroma azungulile Yerusalemu, mtumwi Paulo anapeleka malangizo ofunika kwa Akhristu aciheberi akuti: “Moyo wanu ukhale wosakonda ndalama, koma mukhale okhutila ndi zimene muli nazo pa nthawiyo. Pakuti Mulungu anati: ‘Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono.’ Moti tikhale olimba mtima ndithu ndipo tinene kuti: ‘Yehova ndiye mthandizi wanga. Sindidzaopa. Munthu angandicite ciani?’” (Aheb. 13:5, 6) Mosakayikila, aja amene anatsatila malangizo a Paulo Aroma asanaukile mzindawo, cinakhala cosavuta kwa iwo kuzoloŵela umoyo wosalila zambili kumalo awo atsopano. Iwo anali na cidalilo cakuti Yehova adzawasamalila kuthupi. w22.01 4 ¶7, 9

Cinayi, December 21

Nchito zake zonse [za Yehova] amazicitila cifundo.—Sal. 145:9.

Tikaganizila za munthu wacifundo, mwina zimabwela m’maganizo mwathu ni munthu wokoma mtima, komanso wopatsa. Tingaganizilenso za Msamariya wacifundo wa m’fanizo la Yesu. Munthu wa mtundu wina ameneyu, ‘anacitila cifundo’ Myuda amene anagwa m’manja mwa acifwamba. Msamariya ameneyo “anagwidwa cifundo” poona Myuda wovulazidwa, ndipo anam’samalila mwacikondi. (Luka 10:29-37) Fanizoli litiphunzitsa khalidwe la Mulungu wathu—cifundo. Mulungu amaticitila cifundo cifukwa amatikonda, ndipo amacita zimenezi tsiku lililonse. Pali njila inanso imene munthu angaonetsele cifundo. Njila imeneyo, ni kuleka kupatsa cilango munthu amene ayenela kulangidwa. N’zimene Yehova amacita. Iye wakhala akuticitila cifundo. Wamasalimo anati: “Sanaticitile mogwilizana ndi macimo athu.” (Sal. 103:10) Koma nthawi zina, Yehova amapeleka cilango cokhwima kwa munthu amene wacita chimo. w21.10 8 ¶1-2

Cisanu, December 22

Kukoma mtima kwanga kosatha sikudzacotsedwa kwa iwe. —Yes. 54:10.

Yehova amaonetsa cikondi cosasintha kwa okhawo amene ali pa ubale wabwino na iye—atumiki ake. Mfundo imeneyi ni yoona, tikaona zimene Mfumu Davide komanso mneneli Danieli anakamba. Mwacitsanzo, Davide anati: “Pitilizani kusonyeza kukoma mtima kwanu kosatha [cikondi cosasintha] kwa anthu okudziŵani.” “Yehova adzapitiliza kusonyeza kukoma mtima kwake kosatha [cikondi cosasintha] mpaka kalekale, kwa anthu amene amamuopa.” Ndipo Danieli anakamba kuti: “Inu Yehova Mulungu woona, anthu amene amakukondani ndi kusunga malamulo anu mumawasonyeza kukoma mtima kosatha.” (Sal. 36:10; 103:17; Dan. 9:4) Malinga na mawu ouzilidwa amenewa, Yehova amaonetsa cikondi cosasintha kwa atumiki ake cifukwa amam’dziŵa, amamuopa, amam’konda, komanso amasunga malamulo ake. Zoonadi, Yehova amasungila alambili ake oona cikondi cosasintha. Tisanayambe kutumikila Yehova, iye anationetsa cikondi cimene amaonetsa anthu onse. (Sal. 104:14) Koma popeza tsopano ndife alambili ake, timapindulanso na cikondi cake cosasintha. w21.11 4 ¶8-9

Ciŵelu, December 23

Yehova Mulungu wako ndi amene uyenela kumulambila.—Mat. 4:10.

Olo munthu atikakamize bwanji, timamvelabe mawu a Yesu ali pamwambapa. Masiku ano, anthu ambili amakonda kumvetsela kwa atsogoleli acipembedzo ochuka. Iwo amakopeka na atsogoleliwo, moti amacita ngati n’kuwalambila. Ambili amakhamukila ku machalichi awo, kugula mabuku awo, na kupeleka ndalama zambili kwa iwo. Ndipo ena amakhulupilila zonse zimene atsogoleli amenewo amakamba. Ngati anthuwo amacita zimenezi kwa atsogoleli acipembedzo, ndiye kuti ngati angaone Yesu angacite zoposa pamenepa. Koma mosiyana na zipembedzo zina, alambili oona a Yehova alibe ochedwa atsogoleli pakati pawo. Ngakhale kuti timalemekeza amene amatitsogolela, timatsatila kwambili mawu a Yesu akuti: “Nonsenu ndinu abale.” (Mat. 23:8-10) Sititsatila munthu, kaya akhale mtsogoleli wacipembedzo kapena wandale. Siticilikiza zolinga zawo, ndipo sititengela mbali iliyonse mu za dziko. Pa mbali zimenezi, timasiyana kwambili na zipembedzo zimene zimati n’zacikhristu.—Yoh. 18:36. w21.10 20 ¶6-7

Sondo, December 24

Ine ndine Yehova Mulungu wako . . . Usakhale ndi milungu ina iliyonse kupatulapo ine.—Eks. 20:2, 3.

Mkhristu amene afuna kukhala woyela, sayenela kuona cinthu ciliconse kapena munthu aliyense kukhala wofunika kwambili kuposa ubale wake na Mulungu. Ndipo cifukwa timadziŵika kuti Mboni za Yehova, timayesetsa kupewa kucita zinthu zimene zinganyozetse kapena kuipitsa dzina lake loyela. (Lev. 19:12; Yes. 57:15) Aisiraeli anayenela kusunga malamulo poonetsa kuti Yehova ni Mulungu wawo. Levitiko 18:4 imati: “Muzisunga zigamulo zanga ndi kutsatila mfundo zanga. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.” Caputala 19, cimachula zina mwa mfundozo. Mwacitsanzo, mavesi 5-8, 21, 22 amakamba za kupeleka nsembe za nyama. Nsembezo zinayenela kupelekedwa m’njila yakuti ‘zisaipitse cinthu copatulika ca Yehova.’ Kuŵelenga mavesi amenewa kuyenela kutilimbikitsa kukokondweletsa Yehova, komanso kupeleka nsembe zacitamando zovomelezeka, monga mmene Aheberi 13:15 imatilimbikitsila. w21.12 5-6 ¶14-15

Mande, December 25

Usangalale ndi mkazi wapaunyamata wako.—Miy. 5:18.

Mabanja acinyamata angapindule na zitsanzo za anthu ena amene anaphunzila kudalila Yehova. Mabanja ena akhala mu utumiki wanthawi zonse kwa zaka zambili. Bwanji osafunsila malangizo kwa iwo ngati mukuganizila zodziikila zolinga. Iyi ni njila imene mungaonetsele kuti mumadalila Yehova. (Miy. 22:17, 19) Kumbukilani kuti ukwati ni mphatso yocokela kwa Yehova. (Mat. 19:5, 6) Iye amafuna kuti okwatilana azikondwela na mphatso imeneyi. Inu mabanja acinyamata, bwanji osapenda mmene mukuseŵenzetsela umoyo wanu. Kodi mukucita zonse zotheka kuti muonetse Yehova kuti mukuyamikila mphatso imene anakupatsani? Kambilanani na Yehova m’pemphelo. Fufuzani mfundo zothandiza m’Mawu ake zogwilizana na mmene zinthu zilili kwa imwe. Kenaka, tsatilani malangizo amene Yehova amakupatsani. Dziŵani kuti mudzakhala na umoyo wacimwemwe komanso wopindulitsa, mukaika mtima wanu pa kutumikila Yehova. w21.11 19 ¶16, 18

Ciŵili, December 26

Tonsefe timapunthwa nthawi zambili.—Yak. 3:2.

Yakobo anali kudziona moyenela. Iye sanadzione kukhala wofunika kwambili, kapena woposa Akhristu anzake cifukwa cokhala m’bale wake wa Yesu, kapena cifukwa ca mautumiki ake. Iye anacha alambili anzake kuti “abale anga okondedwa.” (Yak. 1:16, 19; 2:5) Yakobo sanapangitse ena kuona kuti ndiye amacita bwino koposa. Zimene tiphunzilapo: Tizikumbukila kuti tonsefe ndife ocimwa. Sitiyenela kudziona kuti timaposa anthu amene timaphunzila nawo Baibo. Cifukwa ciani? Ngati tipangitsa wophunzila wathu kuona kuti sitilakwitsa zinthu, iye angamaganize kuti sangakwanitse kutsatila zimene Mulungu amafuna. Koma tikavomeleza moona mtima kuti nafenso cimativuta nthawi zina kutsatila mfundo za m’Malemba, komanso tikamufotokozela mmene Yehova watithandizila kusintha umoyo wathu, tidzathandiza wophunzilayo kuona kuti nayenso angakwanitse kutumikila Yehova. w22.01 11-12 ¶13-14

Citatu, December 27

Khalani ndi maganizo amenewa, amenenso Khristu Yesu anali nawo.—Afil. 2:5.

Tikamaganiza kwambili ngati Yesu, m’pamenenso tidzacita zinthu monga iye, komanso tidzatha kuonetsa bwino makhalidwe ake. (Aheb. 1:3) Mwina tingaganize kuti: ‘Yesu ni wangwilo. Siningakwanitse kucita zinthu ndendende mmene anali kucitila.’ Mukakhala na maganizo amenewa, muzikumbukila mfundo izi. Yoyamba, munalengedwa m’njila yakuti muzitha kutengela Yehova na Yesu. Conco, mukasankha kutengela citsanzo cawo mudzakwanitsa kufika pamlingo wina wake. (Gen. 1:26) Yaciŵili, mzimu woyela wa Mulungu ni wamphamvu kwambili m’cilengedwe conse. Ungakuthandizeni kucita zimene simungakwanitse pa inu nokha. Yacitatu, Yehova pali pano, sayembekezela kuti muzionetsa cipatso ca mzimu mwangwilo. Ndiye cifukwa cake, pokhala Tate wathu wacikondi iye anaika zaka 1,000, kuti anthu amene ali na ciyembekezo ca padziko lapansi akafike pokhala angwilo kwathunthu. (Chiv. 20:1-3) Cimene Yehova amafuna kwa ife pali pano, n’cakuti tiyesetse kudalila thandizo lake. w22.03 9 ¶5-6

Cinayi, December 28

Ndisananene kanthu, Inu Yehova mumakhala mutadziŵa kale zonse.—Sal. 139:4.

Pemphelo si njila yokhayo imene tingalimbitsile ubale wathu na Yehova. Kuŵelenga Mawu a Mulungu na kupezeka pa misonkhano yacikhristu, nakonso kungatithandize kumuyandikila kwambili Mulungu. Kodi pali cimene mungacite kuti muziseŵenzetsa bwino nthawi yoŵelenga, komanso yopezeka pa misonkhano ya mpingo? Dzifunseni kuti: ‘N’ciani cimanisokoneza nikakhala pa misonkhano kapena nikamaŵelenga?’ Kodi ni foni kapena mauthenga amene wina angakutumileni pa cipangizo canu? Mukazindikila kuti maganizo anu akuyenda-yenda pamene muŵelenga, kapena muli pa misonkhano ya mpingo, pemphani Yehova kuti akuthandizeni. Cingakhale covuta kuiŵala nkhawazo kuti musumike maganizo anu pa zauzimu. Zikakhala conco, pemphani mtendele umene udzateteza mtima wanu, komanso “maganizo anu.”—Afil. 4:6, 7. w22.01 29-30 ¶12-14

Cisanu, December 29

Chela khutu lako ndi kumva mawu a anthu anzelu.—Miy. 22:17.

Mfumu Uziya anakana uphungu. Iye analoŵa m’malo ena ake m’kacisi wa Yehova, kumene ansembe okha ndiwo anali kuloledwa kuloŵako, ndipo anafuna kupeleka nsembe yofukiza. Ansembe a Yehova anamuuza kuti: “Mfumu Uziya si nchito yanu kufukiza kwa Yehova, koma nchito yofukizayi ni ya ansembe.” Kodi Uziya anacita ciani? Sembe iye modzicepetsa anamvela uphunguwo na kucoka m’kacisi nthawi yomweyo, mwina Yehova akanam’khululukila. Koma “Uziya anakwiya kwambili.” N’cifukwa ciani iye anakana uphungu? Popeza anali mfumu, n’kutheka kuti anaona kuti ali na mphamvu zocita ciliconse cimene afuna. Koma Yehova sanakondwele na zimene anacita. Cifukwa ca kudzikuza kwake, Uziya anakanthidwa na khate, ndipo ‘anakhalabe wakhate mpaka tsiku limene anamwalila.’ (2 Mbiri 26:16-21) Citsanzo ca Uziya citiphunzitsa kuti kaya ndife munthu wotani, tikakana uphungu wozikika m’Baibo timataya ciyanjo ca Yehova. w22.02 9 ¶7

Ciŵelu, December 30

Cotelo lapani ndi kutembenuka kuti macimo anu afafanizidwe, ndiponso kuti nyengo zotsitsimutsa zibwele kucokela kwa Yehova.—Mac. 3:19.

Munthu amene ali na “umunthu wakale,” kaganizidwe kake, komanso kacitidwe kake ka zinthu, kamakhala m’njila ya ucimo. (Akol. 3:9) Iye angakhale wodzikonda, wa mtima wapacala, wosayamika, komanso wonyada. Angamakonde kupenyelela zamalisece, komanso mafilimu oipa. N’zoona kuti iye angakhale na makhalidwe abwino, ndipo angamadziimbe mlandu pa zoipa zimene amacita kapena kukamba. Koma alibe mtima uja wofunitsitsa kusintha kaganizidwe kake na khalidwe lake. (Agal. 5:19-21; 2 Tim. 3:2-5) Popeza ndife opanda ungwilo, sitingathetseletu maganizo onse osayenela, komanso zilakolako zoipa mumtima mwathu. Nthawi zina, tidzakamba mawu kapena kucita zinthu zimene tingadziimbe mlandu pambuyo pake. (Yer. 17:9; Yak. 3:2) Koma tikavula umunthu wakale, sitimalolanso makhalidwe akuthupi kutilamulila. Timasintha n’kukhala munthu wa khalidwe labwino.—Yes. 55:7. w22.03 3 ¶4-5

Sondo, December 31

Modzicepetsa, [muziona] ena kukhala okuposani.—Afil. 2:3.

Inu akulu, muziyang’ana pa makhalidwe abwino amene abale na alongo ali nawo. Aliyense ni wopanda ungwilo, koma ali na makhalidwe osililika. N’zoona kuti nthawi na nthawi, akulu angafunike kuwongolela maganizo a m’bale kapena mlongo. Koma monga mtumwi Paulo, akulu ayenela kuyesetsa kupewa kusumika maganizo pa zokhumudwitsa zimene munthu angakambe kapena kucita. M’malo mwake, angacite bwino kuika maganizo pa cikondi cimene munthuyo ali naco pa Yehova, kupilila kwake potumikila Mulungu, komanso zabwino zimene amatha kucita. Akulu amene amaona zabwino mwa ena, amathandiza kuti mu mpingo mukhale cikondi. Kumbukilani kuti Yehova safuna kuti mukhale angwilo, koma afuna kuti mukhale okhulupilika. (1 Akor. 4:2) Khalani otsimikiza kuti Mulungu amayamikila zimene mumacita pom’tumikila. Iye ‘sadzaiŵala nchito yanu na cikondi cimene munacisonyeza pa dzina lake, mwa kutumikila oyela ndipo mukupitiliza kuwatumikila.’—Aheb. 6:10. w22.03 31 ¶19, 21

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani