LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • es24 masa. 98-108
  • October

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • October
  • Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2024
  • Tumitu
  • Ciŵili, October 1
  • Citatu, October 2
  • Cinayi, October 3
  • Cisanu, October 4
  • Ciŵelu, October 5
  • Sondo, October 6
  • Mande, October 7
  • Ciŵili, October 8
  • Citatu, October 9
  • Cinayi, October 10
  • Cisanu, October 11
  • Ciŵelu, October 12
  • Sondo, October 13
  • Mande, October 14
  • Ciŵili, October 15
  • Citatu, October 16
  • Cinayi, October 17
  • Cisanu, October 18
  • Ciŵelu, October 19
  • Sondo, October 20
  • Mande, October 21
  • Ciŵili, October 22
  • Citatu, October 23
  • Cinayi, October 24
  • Cisanu, October 25
  • Ciŵelu, October 26
  • Sondo, October 27
  • Mande, October 28
  • Ciŵili, October 29
  • Citatu, October 30
  • Cinayi, October 31
Kusanthula Malemba Tsiku na Tsiku—2024
es24 masa. 98-108

October

Ciŵili, October 1

Ndidzakutamandani pakati pa mpingo.​—Sal. 22:22.

Tonsefe tingatengeko mbali pa misonkhano ya mpingo tikamaimba, na kupeleka ndemanga zokonzekela bwino. Ena cimawavuta kuimba nyimbo kapena kupeleka ndemanga pagulu. Kodi na imwe cimakuvutani? Ngati n’conco, onani zimene ena acita kuti athetse mantha amenewo. Pa nkhani ya kuimba nyimbo, ena apeza kuti n’cothandiza kuimba mocokela pansi pamtima. Tikamaimba nyimbo za Ufumu, colinga cathu cacikulu ni kutamanda Yehova. Conco, muzikonzekela nyimbozo muli ku nyumba, monga mmene mungakonzekele mbali zina za msonkhano. Ndipo yesani kuona mmene mawu a nyimbozo akugwilizanila na mfundo zimene mudzaphunzila ku msonkhano. Cina, sumikani maganizo anu pa mawu, osati mmene mukuimbila. Kuyankhapo pa misonkhano kumakhala kovuta kwa ena. N’ciyani cingakuthandizeni? Muziyankhapo kaŵili-kaŵili. Muzikumbukila kuti yankho loyamba liyenela kukhala lalifupi, losavuta kumva, ndiponso loyankha funso mwacindunji. Yehova amayamikila kwambili kufunitsitsa kwathu kum’tamanda pa misonkhano. w22.04 7-8 ¶12-15

Citatu, October 2

Yehova ndiye mthandizi wanga. Sindidzaopa.​—Aheb. 13:6.

Liwu lakuti “mthandizi” limakamba za munthu amene akuthamanga kuti akathandize munthu amene akukuwa kupempha thandizo. Yelekezani kuti mukumuona Yehova akuthamanga kuti akapulumutse munthu wosautsika. Mosakayikila, mungavomeleze kuti mafotokozedwe amenewa amaonetsa kuti Yehova ni wofunitsitsa kutithandiza. Inde, amalakalaka kuti akhale mthandizi wathu. Popeza kuti Yehova ali kumbali yathu, tingathe kupilila mavuto alionse mwacimwemwe. Ni zinthu ziti zimene Yehova amacita potithandiza kupilila mavuto mwacimwemwe? Kuti tiyankhe funso limeneli, tiyeni tikambilane buku la Yesaya. Cifukwa ciyani? Cifukwa maulosi ambili amene Yesaya anauzilidwa kulemba, amakhudza atumiki a Mulungu masiku ano. Yesaya pofotokoza mmene Yehova amacitila zinthu, anaseŵenzetsa mawu osavuta kumva pokamba za Yehova. Citsanzo ca zimenezi ticipeza m’caputala 30 ca Yesaya. M’caputala cimeneci, Yesaya anafotokoza momveka bwino mmene Yehova amathandizila anthu ake. Iye analemba kuti Yehova amatithandiza (1) mwa kumvetsela mapemphelo athu mwachelu na kuwayankha, (2) mwa kutitsogolela, komanso (3) mwa kutidalitsa pali pano, na kutilonjeza madalitso ena m’tsogolo. w22.11 8 ¶2-3

Cinayi, October 3

Usacite mantha ndi mavuto amene ukumane nawo . . . Sonyeza kukhulupilika kwako mpaka imfa, ndipo ndidzakupatsa mphoto ya moyo.​—Chiv. 2:10.

M‘mauthenga a Yesu opita ku mpingo wa Simuna na Filadefiya, iye anauza Akhristu akumeneko kuti sayenela kuopa cizunzo cifukwa Yehova adzawadalitsa kaamba ka kukhulupilika kwawo. (Chiv. 3:10) Tiyenela kudziŵa kuti tidzazunzidwa, ndipo tizikhala okonzeka kupilila. (Mat. 24:9, 13; 2 Akor. 12:10) Buku la Chivumbulutso limatiuza kuti anthu a Mulungu adzazunzidwa “m’tsiku la Ambuye.” (Chiv. 1:10) Chivumbulutso caputala 12 imaonetsa kuti kumwamba kunabuka nkhondo Ufumu wa Mulungu utangobadwa. Mikayeli amene ni Yesu Khristu waulemelelo, pamodzi na angelo anamenya nkhondo na Satana komanso ziŵanda zake. (Chiv. 12:7, 8) Zotulukapo, adani a Mulungu amenewo anagonjetsedwa na kuponyedwa padziko lapansi, zimene zinapangitsa kuti padziko lapansi pakhale mavuto aakulu.​—Chiv. 12:9, 12. w22.05 5 ¶12-13

Cisanu, October 4

Yehova Mulungu wathu si wopanda cilungamo.​—2 Mbiri 19:7.

Ziweluzo za Yehova nthawi zonse zimakhala zacilungamo. Iye alibe tsankho. Kukhululuka kwake sikudalila maonekedwe a munthu, cuma, kudziŵika, kapena maluso ake. (1 Sam. 16:7; Yak. 2:1-4) Palibe angakakamize Yehova kucita zina zake kapena kum’patsa ciphuphu. Iye sapeleka zigamulo cifukwa cothedwa nzelu, kapena kukondela. (Eks. 34:7) Mosakaika konse, Yehova ni woweluza wabwino koposa cifukwa amamvetsetsa kwambili, komanso ni wozindikila. (Deut. 32:4) Olemba Malemba Acihebeli anazindikila kuti Yehova amakhululuka mwapadela kwambili. Nthawi zina polemba, iwo anali kuseŵenzetsa mawu amene buku lina linati mawuwo, “amakambidwa maka-maka pofuna kufotokoza mmene Mulungu amakhululukila munthu wocimwa. Ndipo mawuwo sakambidwa pofuna kuonetsa kukhululukilana kumene kumacitika pakati pa anthu.” Ni Yehova yekha amene ali na mphamvu zokhululukila mokwanila munthu wocimwa wolapa. w22.06 4 ¶10-11

Ciŵelu, October 5

Phunzitsa mwana m’njila yomuyenelela. Ngakhale akadzakalamba sadzapatukamo.​—Miy. 22:6.

Ngati mukulela nokha ana kapena ngati mnzanu wa m’cikwati si Mboni, dziŵani kuti citsanzo canu ca cikhulupililo cimalimbikitsa ena. Bwanji ngati mwaona kuti ana anu sakulabadila zimene mukuwaphunzitsa? Kumbukilani kuti kuphunzitsa mwana kumatenga nthawi. Tikabyala mbewu, nthawi zina tingakaikile ngati mbewuyo idzakula na kubala zipatso. Ngakhale sitingadziŵiletu motsimikiza kuti mtengo udzabaladi zipatso, timapitiliza kuuthilila kuti ukule bwino. (Maliko 4:26-29) Mofananamo, pokhala nakubala, nthawi zina mungakaikile ngati mukuwafika pa mtima ana anu. Simungadziŵiletu zisankho zimene ana anu adzapanga. Koma mukapitiliza kucita zotheka kuti muwaphunzitse, mudzawapatsa mpata wabwino kwambili wakuti akule kuuzimu. w22.04 19-20 ¶16-17

Sondo, October 6

Kunyada kumafikitsa munthu ku ciwonongeko, ndipo mtima wodzikuza umacititsa munthu kupunthwa.​—Miy. 16:18.

Pamene Solomo anali mlambili wa Yehova wokhulupilika, iye anali kudziona moyenela. Ali wacinyamata, modzicepetsa anazindikila zimene sakanakwanitsa kucita, ndipo anapempha citsogozo ca Yehova. (1 Maf. 3:7-9) Cina, kuciyambi kwa ulamulilo wake, Solomo anali kudziŵa za kuwopsa kokhala wonyada. N’zomvetsa cisoni kuti pambuyo pake Solomo analephela kutsatila uphungu wa iye mwini. Pa nthawi ina mu ulamulilo wake, iye anayamba kunyalanyaza malamulo a Mulungu. Mwacitsanzo, limodzi mwa malamulowo linali lakuti mfumu yaciheberi siyenela ‘kudziculukitsila akazi kuti mtima wake ungapatuke.’ (Deut. 17:17) Koma Solomo ananyalanyaza lamulo limeneli, ndipo anadzitengela akazi 700 komanso ena apambali 300. (1 Maf. 11:1-3) Mwina iye anaganiza kuti kucita zimenezo kunalibe vuto. M’kupita kwa nthawi, Solomo anakumana na mavuto obwela cifukwa cosiya Yehova.​—1 Maf. 11:9-13. w22.05 23 ¶12

Mande, October 7

“Wolungama wanga adzakhala ndi moyo mwa cikhulupililo cake,” ndipo “ngati wabwelela m’mbuyo, ine sindikondwela naye.”​—Aheb. 10:38.

Anthu ayenela kupanga cisankho cofunika kwambili: Aliyense ayenela kusankha, kaya kukhala kumbali ya Yehova Mulungu wolamulila wa cilengedwe conse, kapena kukhala pansi pa ulamulilo wa mdani wankhanza, Satana Mdyelekezi. Palibe zokamba kuti ine sin’dzakhala kumbali iliyonse. Cisankho cimene adzapanga cidzakhudza tsogolo lawo. (Mat. 25:31-33, 46) Pa “cisautso cacikulu,” iwo adzaikidwa cizindikilo ca cipulumutso kapena ca ciwonongeko. (Chiv. 7:14; 14:9-11; Ezek. 9:4, 6) Ngati munasankha kucilikiza ulamulilo wa Yehova, munapanga cisankho canzelu. Ndipo mufunitsitsa kuthandiza ena kusankha mwanzelu. Anthu amene amacilikiza mokhulupilika ulamulilo wa Mulungu adzapeza madalitso. Tingacite bwino kumaŵelenga mfundo za coonadi zofunika kwambili zimenezi. Kucita izi kudzatithandiza kupitilizabe kutumikila Yehova. Kuwonjezela apo, tingaseŵenzetse zimene taphunzilazo pothandiza ena kupanga cisankho canzelu, na kumamatila ku zimene asankhazo. w22.05 15 ¶1-2

Ciŵili, October 8

Ndinu odala pamene anthu . . . akukunamizilani zoipa zilizonse cifukwa ca ine.​—Mat. 5:11.

Tizimvetsela kwa Yehova osati adani athu. Yobu anamvetsela mwachelu pamene Yehova anali kukamba naye. Mulungu polankhula kwa Yobu, zinali monga akumuuza kuti: ‘Nidziŵa zonse zimene zakucitikila. Kodi uganiza siningakwanitse kukusamalila?’ Yobu anayankha modzicepetsa komanso moyamikila kwambili pa ubwino wa Yehova. Iye anati: “Ndinkangomva za inu, koma tsopano diso langa lakuonani.” (Yobu 42:5) N’kutheka kuti Yobu pokamba mawu amenewa anali paphulusa, thupi lake lili zilonda zokha-zokha. Ngakhale zinali conco, Yehova anam’tsimikizila Yobu kuti amam’konda komanso kuti akumuyanjabe. (Yobu 42:7, 8) Masiku anonso, anthu angatinyoze na kutiyesa opanda pake. Iwo angatisemele cinyau aliyense payekha kapena monga gulu. Nkhani ya Yobu, itiphunzitsa kuti Yehova ali na cidalilo mwa ife cakuti tidzakhalabe okhulupilika pokumana na mayeso. w22.06 24 ¶15-16

Citatu, October 9

Ukwati wa Mwanawankhosa wafika.​—Chiv. 19:7.

Babulo Wamkulu akadzawonongedwa, kumwamba kudzakhala mfuu yaikulu yacisangalalo. Koma palinso cina cidzabweletsa cimwemwe cacikulu. (Chiv. 19:1-3) Ni “ukwati wa Mwanawankhosa,” umene ni cocitika cokondweletsa kwambili cothela cochulidwa m’buku la Chivumbulutso. Nkhondo ya Aramagedo isanayambe, onse a 144,000 adzakhala kumwamba. Komabe, imeneyo sidzakhala nthawi ya ukwati wa Mwanawankhosa. (Chiv. 21:1, 2) Ukwati wa Mwanawankhosa udzacitika pambuyo pa nkhondo ya Aramagedo, adani onse a Mulungu akadzawonongedwa. (Sal. 45:3, 4, 13-17) Kodi ukwati wa Mwanawankhosa utanthauza ciyani kwa oloŵetsedwamo? Monga mmene ukwati umagwilizanitsila mwamuna na mkazi, ukwati wophiphilitsa umenewo udzagwilizanitsa Yesu Khristu Mfumu, na a 144,000 amene ni “mkwatibwi” wake. Cocitika capadela cimeneco cidzakhazikitsa boma latsopano limene lidzalamulila dziko lapansi zaka 1,000.​—Chiv. 20:6. w22.05 17 ¶11-13

Cinayi, October 10

Kapolo ameneyu adzakhala wodala ngati mbuye wake . . . adzam’peza akucita zimenezo!​—Mat. 24:46.

Yesu analosela kuti m’nthawi ya mapeto, adzaika “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu” kuti azipeleka cakudya cauzimu. (Mat. 24:45) Ndipo izi n’zimenedi iye akucita. Wotiyang’anila ameneyu, akugwilitsa nchito kagulu kocepa ka abale odzozedwa popeleka “cakudya [cauzimu] pa nthawi yoyenela” kwa anthu a Mulungu, komanso acidwi. Amuna amenewa sadziona kuti ni olamulila cikhulupililo ca ena. (2 Akor. 1:24) M’malo mwake, iwo amadziŵa kuti Yesu Khristu ndiye “mtsogoleli ndi wolamulila” anthu ake. (Yes. 55:4) Kungoyambila mu 1919, kapolo wokhulupilika ameneyu wakhala akukonza zofalitsa zosiyana-siyana zimene zathandiza anthu acidwi kuphunzila coonadi ca m’Mawu a Mulungu. Mu 1921, kapoloyu anatulutsa buku lakuti Zeze wa Mulungu, pofuna kuthandiza anthu acidwi kuphunzila Baibo. M’kupita kwa nthawi, panatulutsidwanso mabuku ena. Ni buku liti linakuthandizani kudziŵa Atate wathu wakumwamba na kuyamba kum’konda? w22.07 10 ¶9-10

Cisanu, October 11

Mudzandiika pamaso panu mpaka kale-kale.​—Sal. 41:12.

Yehova ni woolowa manja kwambili. Kaya mum’patse zoculuka motani, nthawi zonse iye adzakubwezelani mowilikiza. (Maliko 10:29, 30) Ngakhale m’dziko loipali iye adzakupatsani umoyo wabwino, wokondweletsa, komanso wokhutilitsa. Ndipo ico n’ciyambi cabe. Mungapitilize kutumikila Atate wanu wokondeka kwamuyaya. Cikondi pakati pa inu na Atate wanu cidzapitilizabe kukula. Ndipo popeza Yehova adzakhalako kosatha, inunso mudzakhala kosatha. Mukadzipatulila na kubatizika, mumakhala na mwayi wopatsa Atate wanu cinthu camtengo wapatali kwambili. Ciliconse cabwino cimene munakhalapo naco, kuphatikizapo cimwemwe, ni Yehova anakupatsani. Poonetsa kuyamikila, pali cinacake cimene mungam’patse Mwini kumwamba na dziko lapansi comwe alibe​—ndico utumiki wanu wokhulupilika. (Yobu 1:8; 41:11; Miy. 27:11) Iyi ni njila yabwino zedi yoseŵenzetsela moyo wanu. w23.03 6 ¶16-17

Ciŵelu, October 12

Kodi wacinyamata angakhale bwanji woyela pa moyo wake? Mwa kudziyang’anila ndi kucita zinthu mogwilizana ndi mawu anu.​—Sal. 119:9.

Pa nthawi ya unyamata, cilakolako ca kugonana cingakhale camphamvu kwambili, moti mungamalakelake kucita ciwelewele. Satana amafuna kuti mugonje ku zilakolako zanu. Ndiye n’ciyani cingakuthandizeni kusungabe khalidwe loyela? (1 Ates. 4:3, 4) Mukamapemphela kwa Yehova panokha, muuzeni mmene mukumvela, ndipo m’pempheni kuti akulimbitseni. (Mat. 6:13) Kumbukilani kuti iye amafuna kukuthandizani, osati kukupezani zifukwa. (Sal. 103:13, 14) Musamayese kuthetsa nokha mavuto amene mumakumana nawo. Auzenkoni makolo anu. N’zoona kuti simungamasuke kukambilana nkhani zacinsinsi na makolo anu. Koma mufunikabe kutelo. Mwa kuŵelenga Baibo na kusinkhasinkha mfundo zake, simudzavutika kupanga zisankho zokondweletsa Yehova. Mudzaona kuti simucita kufunika lamulo pa ciliconse, cifukwa mudzakhala mutadziŵa mmene Yehova amaonela zinthu pa nkhani zosiyana-siyana. w22.08 5 ¶10-12

Sondo, October 13

Ngati munthu sasamalila anthu amene ndi udindo wake kuwasamalila, . . . wakana cikhulupililo.​—1 Tim. 5:8.

Mkhristu amene ni mutu wa banja sautenga mopepuka udindo wosamalila banja lake kuthupi. Ngati ndinu mutu wa banja, munada nkhawa kuti mwina simudzakwanitsa kupeza cakudya ca banja lanu na malo okhala. N’kutheka kuti mulinso na nkhawa yakuti ngati nchito yanu ingathe, simudzapezanso ina. Mwinanso mumadodoma kusinthako zinthu zina kuti mukhale na umoyo wosalila zambili. Satana wapambana pa nchito yake yolepheletsa anthu ambili kutumikila Yehova cifukwa iwo amakhala na mantha otelowo. Satana amafuna tizikhulupilila kuti Yehova sasamala za munthu aliyense payekha, komanso kuti sangatithandize kupeza zosoŵa za banja lathu. Mwa ici, tingayambe kuyesetsa kucita zonse zotheka kuti tisunge nchito yathu, ngakhale kuti kucita zimenezo kungafune kuti tinyalanyaze mfundo za m’Malemba. w22.06 15 ¶5-6

Mande, October 14

Ciyembekezo cimene tili nacoci cili ngati nangula wa miyoyo yathu ndipo n’cotsimikizika ndiponso cokhazikika.​—Aheb. 6:19.

Tinafika podziŵa kuti Mulungu ni “wacifundo ndi wacisomo, wosakwiya msanga ndiponso wodzaza ndi kukoma mtima kosatha ndi coonadi.” (Eks. 34:6) Yehova amakonda cilungamo. (Yes. 61:8) Ndiye cifukwa cake cimamuŵaŵa akamationa tikuvutika. Conco, iye ni wokonzeka kudzacotsapo mavuto onse panthawi yake yoikika. Inde, ni wofunitsitsa kudzatelo. (Yer. 29:11) N’zocititsa cidwi kwambili! M’pake kuti Yehova timam’konda kwambili. N’cifukwa cina citi cimene timakondela coonadi? Coonadi cimatipindulila m’njila zambili. Ganizilani citsanzo ici. Coonadi ca m’Baibo cimaphatikizapo ciyembekezo cathu ca zam’tsogolo. Monga mmene nangula amathandizila boti kuti isamatengeke-tengeke na mafunde, naconso ciyembekezo cathu cozikika pa Baibo cimatithandiza kusasunthika tikakumana na mayeso. Pa lemba la tsiku lalelo, mtumwi Paulo anali kufotokoza za ciyembekezo copita kumwamba ca Akhristu odzozedwa. Koma mawuwa amagwilanso nchito kwa Akhristu amene ali na ciyembekezo codzakhala na moyo kwamuyaya m’paradaiso padziko lapansi. (Yoh. 3:16) Kukamba zoona, kuphunzila za ciyembekezo ca moyo wosatha kwapangitsa umoyo wathu kukhala waphindu. w22.08 14-15 ¶3-5

Ciŵili, October 15

Dzuŵa lisaloŵe muli cikwiyile.​—Aef. 4:26.

Cikondi ndiwo maziko a kudalilana wina na mnzake. 1 Akorinto caputala 13, imafotokoza mmene cikondi cimatithandizila kudalila abale athu, kapena kuyambilanso kuwadalila. (1 Akor. 13:4-8) Mwacitsanzo, vesi 4 imati “cikondi n’coleza mtima ndiponso n’cokoma mtima.” Yehova amaleza nafe mtima ngakhale pamene tam’cimwila. Mofananamo, tiyenela kuwalezela mtima abale athu akatikhumudwitsa m’mawu kapena m’zocita. Vesi 5 imati: “[Cikondi] sicikwiya. Sicisunga zifukwa.” Conco, tizipewa kusunga zolakwa za abale athu mumtima, na colinga cakuti akakalakwitsanso, tikawakumbutse. Ndipo Mlaliki 7:9 imati ‘tisamafulumile kukwiya mumtima mwathu.’ Muziyesetsa kuona abale na alongo athu mmene Yehova amawaonela. Iye amawakonda, ndipo sawasungila zifukwa akalakwa. Ifenso tiyenela kucita cimodzimodzi. (Sal. 130:3) M’malo moyang’ana pa zophophonya zawo, tiziyang’ana pa makhalidwe awo abwino.​—Mat. 7:1-5. w22.09 3-4 ¶6-7

Citatu, October 16

Padzafika nthawi ya masautso.​—Dan. 12:1.

Buku la Danieli limafotokoza ndondomeko ya zocitika zokondweletsa zimene zidzacitika m’nthawi yamapeto. Mwacitsanzo, Danieli 12:1 imakamba kuti Mikayeli, amene ni Yesu Khristu, “waimilila [kutanthauza kuti ali ciimilile] kuti athandize anthu a [Mulungu].” Kuimilila kophiphilitsa kumeneku kunayamba mu 1914 pamene Yesu anaikidwa kukhala Mfumu ya Ufumu wa Mulungu kumwamba. Komabe, Danieli anauzidwanso kuti Yesu “adzaimilila” pa “nthawi ya masautso imene sinakhalepo kuyambila pamene mtundu woyambilila wa anthu unakhalapo kufikila nthawi imeneyo.” “Nthawi ya masautso” imeneyi ni “cisautso cacikulu” cochulidwa pa Mateyu 24:21. Yesu adzaimilila, kapena kuti adzacitapo kanthu kuti ateteze anthu a Mulungu kumapeto kwa nthawi ya masautso imeneyi, kutanthauza pa Aramagedo. Buku la Chivumbulutso limachula anthu a Mulungu amenewa kuti a “khamu lalikulu amene atuluka m’cisautso cacikulu.”​—Chiv. 7:9, 14. w22.09 21 ¶4-5

Cinayi, October 17

Amene wandicimwilayo ndi amene ndim’fafanize m’buku langa.​—Eks. 32:33.

Maina amene palipano alimo m’buku la moyo akhoza kufafanizidwa, kapena kuti kucotsedwamo. Zili ngati kuti Yehova poyamba analemba mainawo na pensulo. (Chiv. 3:5) Tiyenela kuyesetsa kuti dzina lathu likhalebe m’buku la moyo limenelo mpaka pamene lidzalembedwe mwacikhalile na colembela ca inki, titelo kunena kwake. Gulu limodzi la anthu amene maina awo analembedwa m’buku la moyo, ni aja amene anasankhidwa kuti akalamulile pamodzi na Yesu kumwamba. Malinga na mawu a mtumwi Paulo kwa ‘anchito anzake’ ku Filipi, maina a odzozedwa, amene anaitanidwa kuti akalamulile na Yesu alimo m’buku la moyo. (Afil. 4:3) Koma kuti maina awo akhalemobe m’buku lophiphilitsa limeneli, ayenela kukhalabe okhulupilika. Iwo akadzalandila cidindo cothela, kaya asanamwalile kapena cisautso cacikulu cisanayambe, maina awo adzalembedwa mwacikhalile m’buku limeneli.​—Chiv. 7:3. w22.09 14 ¶3; 15 ¶5-6

Cisanu, October 18

Odala ndi amene akumva mawu a Mulungu ndi kuwasunga!​—Luka 11:28.

Tiyelekezele motele: Wina wake waphika cakudya cimene mumacikonda kwambili. Koma cifukwa cakuti ndinu wofulumila komanso wotangwanika, mukudya cakudyaco mothamanga moti mukulephela kumva kukoma kwake. Ndipo pamene mwatsiliza kudya, mwaona kuti cakudyaco mwacidya mothamanga kwambili moti simunamve kukoma kwake. Mofananamo, kodi munayamba mwaŵelengapo Baibo mothamanga cakuti simunamve kukoma kwa uthenga wake? Inde, musamathamange poŵelenga Mawu a Mulungu. Koma muziona m’maganizo mwanu zocitikazo. Muziyelekezela mawu a anthu amene akukamba, komanso muzisinkhasinkha zimene mwaŵelengazo. Mukamaŵelenga mwa njila imeneyi mudzakhala acimwemwe. Yesu anaika “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu” kuti azikonza cakudya cauzimu pa nthawi yoyenela. Ndipo timadyetsedwa bwino mwauzimu. (Mat. 24:45) Cinthu cacikulu cimene kapolo wokhulupilika amagwilitsa nchito pokonza cakudya cauzimu, ni Malemba ouzilidwa.​—1 Ates. 2:13. w22.10 7-8 ¶6-8

Ciŵelu, October 19

Akukhala mosatekeseka.​—Sal. 123:4.

Baibo inakambilatu kuti m’masiku otsiliza, anthu adzakhala onyoza. (2 Pet. 3:3, 4) Iwo amacita zimenezi cifukwa cotsatila “zilakolako zawo pa zinthu zonyoza Mulungu.” (Yuda 7, 17, 18) Kodi tingadziteteze motani kuti tisatengele khalidwe la anthu onyoza amenewo? Njila imodzi ni kusagwilizana nawo anthu amene amakonda kudandaula pa ciliconse. (Sal. 1:1) Izi zitanthauza kuti sitiyenela kumvetsela kapena kuŵelenga nkhani za ampatuko. Timadziŵa kuti tikapanda kusamala, tingakhale na mzimu wotsutsa, na kuyamba kukayikila Yehova komanso citsogozo cimene timalandila kupitila m’gulu lake. Kuti tipewe khalidwe limeneli, tingadzifunse kuti: ‘Kodi nthawi zambili nimakonda kudandaula tikalandila malangizo atsopano, kapena pakakhala kusintha kwa kamvedwe kathu? Kodi nimakonda kupeza zifukwa abale amene akutsogolela?’ Ngati tingathetse khalidwe limeneli mwamsanga, Yehova adzakondwela nafe.​—Miy. 3:34, 35. w22.10 20 ¶9-10

Sondo, October 20

A nyumba ya Isiraeli sakafuna kukumvela.​—Ezek. 3:7.

Mzimu wa Mulungu unalimbikitsa Ezekieli pa nchito yolalikila anthu “amakani ndi osamva.” Yehova anauza Ezekieli kuti: “Ndacititsa nkhope yako kuti ikhale yolimba mofanana ndi nkhope zawo, ndiponso cipumi cako kuti cikhale colimba mofanana ndi zipumi zawo. Ndacititsa cipumi cako kukhala ngati mwala wa dayamondi, colimba kuposa mwala wa nsangalabwi. Usawaope, ndipo usacite mantha ndi nkhope zawo.” (Ezek. 3:8, 9) Zinali monga Yehova akuuza Ezekieli kuti: ‘Usalole kuti ankhutukumve amenewa akulefule. Nikulimbitsa.’ Pambuyo pa izi, mzimu wa Mulungu unatengela Ezekieli ku gawo lake lolalikila. Ezekieli analemba kuti: “Dzanja la Yehova linandigwila mwamphamvu.” Zinamutengela mlungu wathunthu kuti mneneli ameneyu amvetsetse uthenga wa Mulungu kotelo kuti akaulengeze mwacidalilo. (Ezek. 3:14, 15) Kenako, Yehova anamulamula kuti apite ku cigwa kumene “mzimu unaloŵa mwa [iye].” (Ezek. 3:23, 24) Apa tsopano Ezekieli anali wokonzeka kuyamba utumiki wake. w22.11 4-5 ¶8-9

Mande, October 21

Inu Yehova, kodi ndidzalilila thandizo koma inu osandimva kufikila liti? . . . N’cifukwa ciyani mukupitiliza kuyang’ana khalidwe loipa?​—Hab. 1:2, 3.

Mneneli Habakuku anakumana na mavuto ambili. Pa nthawi ina, iye anakayikila ngati Yehova amasamala za iye. Conco, anauza Yehova m’pemphelo mmene anali kumvela. Yehova anayankha pemphelo locokela pansi pamtima la mtumiki wake wokhulupilika ameneyu. (Hab. 2:2, 3) Habakuku ataganizila nchito zopulumutsa za Yehova, anakhalanso wacimwemwe. Iye anakhala wotsimikiza kuti Yehova amasamaladi za iye, komanso kuti adzam’thandiza kupilila mavuto. (Hab. 3:17-19) Kodi tiphunzilapo ciyani pamenepa? Tikakumana na mavuto, tizipemphela kwa Yehova na kumuuza mmene tikumvela. Kenako, tiziyang’ana kwa iye kuti atithandize. Tikatelo, tidzakhala na cidalilo conse kuti Yehova adzatipatsa mphamvu zofunikila kuti tipilile. Ndipo tikaona mmene watithandizila, cikhulupilila cathu mwa iye cidzalimbilako. Inde, ngati mupitiliza kucita zauzimu, inunso simudzalola mavuto kapena zikayiko kukukanganulani kwa Yehova.​—1 Tim. 6:6-8. w22.11 15 ¶6-7

Ciŵili, October 22

Ndithu ndikukuuza lelo, iwe udzakhala ndi ine m’Paradaiso.​—Luka 23:43.

Yesu na amuna aŵili ocita zoipa amene anapacikidwa naye anazunzika ali pafupi kufa. (Luka 23:32, 3) Amunawo anali kunyoza Yesu. (Mat. 27:44; Maliko 15:32) Koma mmodzi anasintha maganizo ake. Iye anati: “Yesu, mukandikumbukile mukakaloŵa mu Ufumu wanu.” Poyankha Yesu anamuuza mawu a lemba la tsiku la lelo. (Luka 23:39-42) Zimene Yesu anauza wocita zoipayo ziyenela kutilimbikitsa kuganizila mmene umoyo udzakhalile m’Paradaiso. Ndipo pali zimene tingaphunzilepo zokhudza Paradaiso kucokela ku ulamulilo wamtendele wa Mfumu Solomo. Yesu pokhala Solomo wamkulu, adzagwila nchito pamodzi na olamulila anzake kuti adzasandutse dziko lapansi kukhala paradaiso. (Mat. 12:42) Conco, a “nkhosa zina” ayenela kuonetsetsa kuti akucita zinthu zowayeneleza kukakhala na moyo kwamuyaya m’Paradaiso.​—Yoh. 10:16. w22.12 8 ¶1; 9 ¶4

Citatu, October 23

Mosakayikila, iye adzakukomela mtima akadzamva kulila kwako.​—Yes. 30:19.

Yesaya akutitsimikizila kuti Yehova amamvetsela mwachelu tikamapempha thandizo kwa iye. Ndipo iye adzayankha mapemphelo athu mosazengeleza. Yesaya anati: “Akadzangomva kulila kwakoko, iye adzakuyankha.” Mawu olimbikitsa amenewa amatikumbutsa kuti Atate wathu ni wofunitsitsa, inde amalakalaka kuthandiza anthu amene amam’pempha thandizo. Ndipo kudziŵa izi kumatithandiza kupilila mwacimwemwe. Yehova amamvetsela mwachelu pemphelo la aliyense wa ife. Cifukwa ciyani tikutelo? M’cinenelo coyambilila, liwu lakuti “inu” m’mavesi oyambilila a Yesaya caputala 30, analigwilitsa nchito poonetsa kuti Yehova anali kukamba na gulu la anthu. Koma pa vesi 19, anagwilitsa nchito mawu oonetsa kuti uthengawo unali kupita kwa munthu mmodzi payekha. Mwacitsanzo, Yesaya analemba kuti: “Iwe sudzalilanso,” “iye adzakukomela mtima,” “iye adzakuyankha.” Pokhala Tate wacikondi, Yehova amamvetsela mwachelu mapemphelo athu.​—Sal. 116:1; Yes. 57:15. w22.11 9 ¶5-6

Cinayi, October 24

Khalani ocenjela ngati njoka koma oona mtima ngati nkhunda.​—Mat. 10:16.

Kulalikila na kuphunzitsa ngakhale kuti tikuzunzidwa kumatibweletsela cimwemwe na mtendele. M’zaka za zana loyamba, pamene olamulila aciyuda analamula atumwi kuti aleke kulalikila, amuna okhulupilila amenewo anasankha kumvela Mulungu. Iwo sanaleke kulalikila, ndipo nchitoyo inawabweletsela cimwemwe. (Mac. 5:27-29, 41, 42) N’zoona kuti nchito yathu ikaikilidwa ziletso, tiyenela kulalikila mocenjela. Koma ngati ticita zonse zotheka, tidzakhala na mtendele umene umabwela cifukwa cokondweletsa Yehova, komanso cifukwa couzako ena uthenga wopulumutsa moyo. Khalani na cidalilo kuti ngakhale panthawi zovuta kwambili, n’zotheka kukhala na mtendele wa mumtima. Pa nthawi zimenezo, tizikumbukila kuti mtendele umene timafunikila ni mtendele umene ni Yehova yekha angatipatse. Conco, mudalileni pamene kwabuka matenda, kwacitika matsoka a zacilengedwe, kapena pamene mukuzunzidwa. Mamatilani gulu lake. Ndipo pitilizani kuyembekezela mwacidwi tsogolo labwino limene wakusungilani. Mukatelo, “Mulungu wamtendele adzakhala nanu.”​—Afil. 4:9. w22.12 21 ¶17-18

Cisanu, October 25

[Valani] umunthu watsopano.​—Aef. 4:24.

Kuti izi zitheke tiyenela kulimbikila. Mwa zina, tiyenela kuyesetsa kucotsa makhalidwe oipa mwa ife, monga kuwawidwa mtima kwanjilu, kupsa mtima, na mkwiyo. (Aef. 4:31, 32) N’cifukwa ciyani kucita izi kungakhale kovuta. Cifukwa makhalidwe ena oipa anazika mizu kwambili. Mwacitsanzo, Baibo imakamba kuti anthu ena ‘amakonda kukwiya,’ komanso ‘amakonda kupsa mtima. (Miy. 29:22) Munthu wa makhalidwe ozika mizu ngati amenewa, angafunike kupitiliza kulimbikila kuti asinthe ngakhale pambuyo pa ubatizo. (Aroma 7:21-23) Pemphelani kwa Yehova za khalidwe limene mukulimbana nalo, muli na cidalilo cakuti adzakumvelani na kukuthandizani. (1 Yoh. 5:14, 15) Ngakhale kuti Yehova sadzathetsa khalidwelo mozizwitsa, angakupatseni mphamvu kuti musafooke. (1 Pet. 5:10) Citani zinthu mogwilizana na mapemphelo anu, popewa kucita zinthu zimene zingapangitse umunthu wanu wakale kubwelanso. Ndipo musalole maganizo anu kukhazikika pa zilakolako zoipa.​—Afil. 4:8; Akol. 3:2. w23.01 10 ¶7, 9-10

Ciŵelu, October 26

Munthu amene amakonda Mulungu azikondanso m’bale wake.​—1 Yoh. 4:21.

Imodzi mwa njila zimene tingaonetsele cikondi cathu ni kukangalika pa nchito yolalikila. Timalalikila aliyense amene takumana naye. Polalikila siticita tsankho. Timakamba na aliyense mosayang’ana khungu, mtundu, cuma, kapena maphunzilo. Mwa ici, timacita zinthu mogwilizana na cifunilo ca Yehova “cakuti anthu, kaya akhale a mtundu wotani, apulumuke ndi kukhala odziŵa coonadi molondola.” (1 Tim. 2:4) Timaonetsanso cikondi cathu pa Mulungu na Khristu mwa kukonda abale na alongo athu. Timasamala kwambili za iwo, ndipo timawathandiza akakumana na mavuto. Cina, timawatonthoza munthu amene amam’konda akamwalila, kupita kukawaona akadwala, komanso kuyesetsa kuwalimbikitsa akalefuka. (2 Akor. 1:3-7; 1 Ates. 5:11, 14) Ndiponso timapitiliza kuwapemphelela, podziŵa kuti “pembedzelo la munthu wolungama limagwila nchito mwamphamvu kwambili.”​—Yak. 5:16. w23.01 28-29 ¶7-8

Sondo, October 27

Pitilizani kutonthozana ndi kulimbikitsana.​—1  Ates. 5:11.

Monga mmene wogwila nchito ya mamangidwe amakulitsila maluso ake m’kupita kwa nthawi, nafenso tinganole maluso athu kuti tizilimbikitsa ena mogwila mtima. Tingawathandize kupeza mphamvu zotha kupilila mayeso mwa kuwauzako zitsanzo za anthu akale amene anapilila. (Aheb. 11:32-35; 12:1) Tingalimbikitsenso mtendele mu mpingo mwa kuchula zabwino zimene ena amacita, kusungitsa mtendele pakabuka nkhani imene ingausokoneze, komanso kubwezeletsa mtendele tikasemphana maganizo na ena. (Aef. 4:3) Cina, tingalimbitsebe cikhulupililo ca abale na alongo athu powauzako mfundo zofunika za coonadi ca m’Baibo, kuwathandiza pa zosoŵa zawo, ndiponso polimbikitsa aliyense amene wafooka mwauzimu. Nafenso timakhala acimwemwe komanso okhutila tikamalimbitsa cikhulupililo ca abale na alongo athu. Mosiyana na zimango zenizeni zimene zimawonongeka m’kupita kwa nthawi, zotulukapo za utumiki wathu wolimbikitsa ena zimakhala zabwino mpaka kale-kale. w22.08 22 ¶6; 25 ¶17-18

Mande, October 28

Yehova amapeleka nzelu. Kudziŵa zinthu ndi kuzindikila kumatuluka m’kamwa mwake.​—Miy. 2:6.

Yesu anaonetsa khalidwe lofunika kwambili limene lingatithandize kumvetsetsa zimene timaŵelenga m’Mawu a Mulungu. Khalidwelo ni kuzindikila. (Mat. 24:15) Kodi kuzindikila n’ciyani? Ni luso lotithandiza kuona mmene mfundo imodzi imagwilizanila na mfundo ina, ndiponso mmene imasiyanilana na mfundo ina, komanso lotithandiza kudziŵa mfundo zobisika. Kuwonjezela apo, Yesu anaonetsa kuti tiyenela kukhala ozindikila kuti timvetse zocitika zimene zimakwanilitsa maulosi a m’Baibo. Timafunikilanso khalidwe la kuzindikila kuti tipindule kwenikweni na zimene timaŵelenga m’Baibo. Yehova amapatsa atumiki ake luso la kuzindikila. Conco, mufikileni m’pemphelo na kum’pempha kuti akuthandizeni kukhala na khalidwe limeneli. Kodi mungacite bwanji zinthu mogwilizana na pemphelo lanu? Iunikeni bwino nkhani imene mukuŵelenga, ndipo onani mmene ikugwilizanila na mfundo zina zimene mumadziŵa kale. Pezani tanthauzo la zimene mukuŵelenga m’Baibo, komanso kuona mmene mungaziseŵenzetsele mu umoyo wanu. (Aheb. 5:14) Mwa kugwilitsa nchito kuzindikila poŵelenga, kamvedwe kanu ka Malemba kadzakula. w23.02 10 ¶7-8

Ciŵili, October 29

Cifukwa ca iye tili ndi moyo, timayenda ndipo tilipo.​—Mac. 17:28.

Yelekezani kuti mnzanu wakupatsani nyumba. Koma mbali zina za nyumbayo penti yake inatha, ndipo mtenje wake umadontha. Ngakhale kuti mbali zina n’zowonongeka, nyumbayo ni mphatso ya mtengo wapatali kwambili. Mosakaikila, mungayamikile mphatso ya nyumbayo ndipo mungamaisamalile bwino. Mofananamo, Yehova anatipatsa moyo umene ni mphatso ya mtengo wapatali. Ndipo Yehova anaonetsa kuti amaona moyo wathu kukhala wofunika mwa kupeleka mwana wake monga dipo. (Yoh. 3:16) Yehova ndiye Gwelo la moyo. (Sal. 36:9) Povomeleza mfundo ya coonadi imeneyi, mtumwi Paulo anati: “Cifukwa ca iye tili ndi moyo, timayenda ndipo tilipo.” (Mac. 17:25, 28) Conco, mpake kunena kuti moyo umene tili nawo ni mphatso yocokela kwa Mulungu. Iye mwacikondi amatipatsa zimene tifunikila kuti tikhale na moyo. (Mac. 14:15-17) Koma Yehova sateteza miyoyo yathu mozizwitsa. M’malo mwake, iye amayembekezela kuti tizidzisamalila bwino kuthupi komanso kuuzimu.​—2 Akor. 7:1. w23.02 20 ¶1-2

Citatu, October 30

Lemba m’buku mawu onse amene ndidzalankhula nawe.​—Yer. 30:2.

Ndife oyamikila cotani nanga kwa Yehova Mulungu potipatsa Baibo! Kupitila m’Baibo, iye amatipatsa uphungu wanzelu umene ungatithandize kulimbana na mavuto amene timakumana nawo masiku ano. Watipatsanso ciyembekezo ca tsogolo labwino. Ndipo coposa zonse, Yehova anavumbula makhalidwe ake ambili kupyolela m’Baibo. Tikamasinkhasinkha makhalidwe ake abwino, mitima yathu imakopeka kuti tikhale pa ubwenzi wabwino na Mulungu wathu mwa kumuyandikila. (Sal. 25:14) Yehova amafuna kuti anthu amudziŵe. M’masiku akale, anali kuuza anthu zokhudza iye kupitila m’maloto, m’masomphenya, ngakhalenso mwa angelo. (Num. 12:6; Mac. 10:3, 4) Koma kodi zikanatheka bwanji kuti maloto, masomphenya, kapena mauthenga ocokela kwa angelo amenewa tiwaphunzile ngati sakanalembedwa? Ndiye cifukwa cake Yehova anauza amuna ‘kulemba m’buku’ zimene iye anafuna kuti tidziŵe. Popeza “njila ya Mulungu woona ndi yangwilo,” ndife otsimikiza kuti njila yolankhula nafe imeneyi ni yabwino koposa komanso yopindulitsa.​—Sal. 18:30. w23.02 2 ¶1-2

Cinayi, October 31

Kupatsa kumabweletsa cimwemwe coculuka kuposa kulandila.​—Mac. 20:35.

Dziikileni zolinga zokupindulilani. Sankhani zolinga zimene zingalimbitse cikhulupililo canu, na kukuthandizani kuti mukhale Mkhristu wokhwima. (Aef. 3:16) Mwacitsanzo, mungadziikile colinga cocita phunzilo la inu mwini na kuŵelenga Baibo mokhazikika. (Sal. 1:2, 3) Kapena mungadziikile colinga comapemphela kaŵili-kaŵili komanso mocokela pansi pa mtima. Mwinanso mungaone kuti muyenela kusamala kwambili posankha zosangalatsa, ndiponso mmene mumagwilitsila nchito nthawi yanu. (Aef. 5:15, 16) Mudzakhala Mkhristu wokhwima ngati muthandiza anthu ena. Mwacitsanzo, mungadziikile colinga cakuti muzithandiza okalamba komanso odwala mu mpingo mwanu. Mwina mungadzipeleke kupita kukawagulilako zinthu, kapena kuwathandiza mmene angaseŵenzetsele zipangizo zamakono. Mumaonetsanso kuti mumakonda anthu mwa kuwauzako uthenga wabwino wa Ufumu. (Mat. 9:36, 37) Ngati n’kotheka, mungadziikile colinga cokacitako utumiki wanthawi zonse. w22.08 6 ¶16-17

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani